John


1

Joh 1:1 PACHIYAMBI panali Mawu, ndipo Mawu adali ndi Mulungu, ndipo Mawu adali Mulungu.

Joh 1:2 Awa adali pachiyambi ndi Mulungu.

Joh 1:3 Zinthu zonse zidalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikadalengedwa kanthu kena kali konse kolengedwa.

Joh 1:4 Mwa Iye mudali moyo; ndi moyowu udali kuwunika kwa anthu.

Joh 1:5 Ndipo kuwunikaku kudawala mumdima; ndi mdimawu sudakuzindikira.

Joh 1:6 Kudali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane.

Joh 1:7 Iyeyu adadza mwa umboni, kudzachita umboni za kuwunikaku, kuti anthu onse kudzera mwa iye akakhulupirire.

Joh 1:8 Iye sindiye kuwunikaku, koma adatumidwa kukachita umboni wa kuwunikaku.

Joh 1:9 Uku ndiko kuwunika kwenikweni kumene kuwunikira anthu onse akulowa m’dziko lapansi.

Joh 1:10 Adali m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye, koma dziko lapansi silidamzindikira Iye.

Joh 1:11 Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sadamlandira Iye.

Joh 1:12 Koma onse amene adamlandira Iye, kwa iwo adapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;

Joh 1:13 Amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.

Joh 1:14 Ndipo Mawu adasandulika thupi nakhazikika pakati pa ife, ( ndipo tidawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate), wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.

Joh 1:15 Yohane achita umboni za Iye, nafuwula nati, Uyu ndiye amene ndidanena za Iye, wakudzayo pambuyo panga adalipo ndisanabadwe ine; chifukwa adakhala woyamba wa ine.

Joh 1:16 Chifukwa mwa kudzala kwake tilandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo.

Joh 1:17 Chifukwa chilamulo chidapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi chowonadi zinadza mwa Yesu Khristu.

Joh 1:18 Kulibe munthu adawona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pachifuwa cha Atate, Iyeyu adafotokozera.

Joh 1:19 Ndipo uwu ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda adatuma ansembe ndi alembi aku Yerusalemu ankamfunse iye, Ndiye yani?

Joh 1:20 Ndipo adabvomera, wosakana; nalola kuti, sindine Khristu.

Joh 1:21 Ndipo adamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, sindine. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha Iyayi.

Joh 1:22 Chifukwa chake adati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mawu kwa iwo adatituma ife unena chiyani za iwe wekha?

Joh 1:23 Iye adati, ndine mawu a wofuwula m’chipululu, Lungamitsani njira ya Ambuye, monga adati Yesaya m’neneriyo.

Joh 1:24 Ndipo wotumidwawo adali a kwa Afarisi.

Joh 1:25 Ndipo adamfunsa iye, nati kwa iye, nanga ukubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?

Joh 1:26 Yohane adawayankha, nati, Ine ndikubatiza ndi madzi, koma pakati pa inu payimilira amene simumdziwa.

Joh 1:27 Ndiye wakudza pambuyo panga, amene adalipo ndisanabadwe ine sindiyenera kumasula lamba wa nsapato yake.

Joh 1:28 Zinthu izi zidachitika mu Betaniya tsidya lija la Yordano, komwe adalikubatiza Yohane.

Joh 1:29 M’mawa mwake Yohane adawona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!

Joh 1:30 Ndiye amene ndidati za Iye, pambuyo panga palinkudza munthu amene adalipo ndisanabadwe ine; pakuti adali woyamba wa ine.

Joh 1:31 Ndipo sindidamdziwa Iye; koma kuti awonetsedwe kwa Israyeli, chifukwa cha ichi ndidadza ine kudzabatiza ndi madzi.

Joh 1:32 Ndipo Yohane adachita umboni, nati, Ndidawona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhala pa Iye.

Joh 1:33 Ndipo sindidamdziwa Iye, koma Iye Wonditumayo kudzabatiza ndi madzi. Iyeyu adanena ndi ine, Amene udzawona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.

Joh 1:34 Ndipo ine ndidawona, ndikuchita umboni kuti uyu ndiye Mwana wa Mulungu.

Joh 1:35 M’mawa mwake Yohane adayimiliransondi ophunzira ake awiri;

Joh 1:36 Ndipo poyang’ana Yesu alikuyenda, adati, Onani Mwana wankhosa wa Mulungu!

Joh 1:37 Ndipo wophunzira awiri adamva iye alimkuyankhula, natsata Yesu.

Joh 1:38 Koma Yesu adachewuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nawo, Mufuna chiyani? Ndipo adati kwa Iye, Rabi (ndiko kutanthauza, Mphunzitsi), mumakhala kuti?

Joh 1:39 Ndipo adati kwa iwo, Tiyeni, mukawone. Pamenepo anadza nawona kumene amakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; popeza kuti linali Ola la khumi.

Joh 1:40 M’modzi wa awiriwo amene adamva Yohane akuyankhula, namtsata Iye adali Andreya m’bale wake wa Simoni Petro.

Joh 1:41 Iye adayamba kupeza m’bale wake yekha Simoni, nanena naye, tapeza ife Mesiya ndiko kutanthauza Khristu.

Joh 1:42 Anadza naye kwa Yesu. M’mene adamuyang’ana iye, adati, Ndiwe Simoni mwana wa Yona; udzatchedwa Khefa ndiko kutanthauza Thanthwe.

Joh 1:43 M’mawa mwake adafuna kutuluka kupita ku Galileya, nampeza Filipo. Ndipo Yesu adanena naye, Tsata Ine.

Joh 1:44 Tsopano Filipo adali wa ku Betisayida, mzinda wa Andreya ndi Petro.

Joh 1:45 Filipo adapeza Natanayeli, nanena naye, Iye amene Mose adalembera za Iye m’chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu wa ku Nazareti, mwana wa Yosefe.

Joh 1:46 Natanayeli adati kwa iye, ku Nazarete mkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo adanena naye, Tiye ukawone.

Joh 1:47 Yesu adawona Natanayeli alimkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, mu Israyeli ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!

Joh 1:48 Natanayeli adanena naye, Mudandidziwira kuti? Yesu adayankha nati kwa iye, Asadakuyitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mtengo wa mkuyu paja, ndidakuwona iwe.

Joh 1:49 Natanayeli adayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israyeli:

Joh 1:50 Yesu adayankha nati kwa iye, chifukwa ndidati kwa iwe kuti ndidakuwona pansi pa mtengo wa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzawona zinthu zoposa izi.

Joh 1:51 Ndipo adanena naye, Indetu indetu, ndinena ndi inu, Mudzawona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa munthu.



2

Joh 2:1 Ndipo tsiku lachitatu padali ukwati mu Kana wa Galileya; ndipo amake a Yesu adali komweko.

Joh 2:2 Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake adayitanidwa ku ukwatiwo.

Joh 2:3 Ndipo pamene adafuna vinyo, amake a Yesu adanena ndi Iye, Alibe vinyo.

Joh 2:4 Yesu adanena naye, mkazi, ndiri ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga sidafike.

Joh 2:5 Amake adanena kwa atumiki, chiri chonse chimene akanena kwa inu, chitani.

Joh 2:6 Ndipo padali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoyikidwako monga mwa mayeretsedwe wa Ayuda, yonse ya myeso iwiri kapena itatu.

Joh 2:7 Yesu adanena nawo, Dzadzani mitsukoyo ndi madzi. Ndipo adayidzadza nde, nde, nde.

Joh 2:8 Ndipo adanena nawo, Tungani tsopano, mupite nawo kwa mkulu wa phwando. Ndipo adapita nawo.

Joh 2:9 Koma pamene mkuluyo adalawa madzi osandulika vinyowo, ndipo sadadziwa kumene adachokera; (koma atumiki amene adatunga madzi adadziwa), mkuluyo adayitana mkwati.

Joh 2:10 Nanena naye, Munthu ali yense amayamba kuyika vinyo wokoma; ndipo anthu amwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.

Joh 2:11 Chiyambi ichi cha zozizwitsa zake Yesu adazichita mu Kana wa Galileya, adawonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake adakhulupilira Iye.

Joh 2:12 Zitapita izi adatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka.

Joh 2:13 Ndipo Paskha wa Ayuda adayandikira, ndipo Yesu adakwera kupita ku Yerusalemu.

Joh 2:14 Ndipo adapeza m’kachisi iwo akugulitsa ng’ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama ali kukhala pansi.

Joh 2:15 Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, adatulutsa onse mu kachisimo, ndi nkhosa ndi ng’ombe, nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagudubuza magome;

Joh 2:16 Nati kwa iwo akugulitsa nkhunda; chotsani izi muno, musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.

Joh 2:17 Ndipo ophunzira ake adakumbukira kuti kudalembedwa, changu cha pa nyumba yanu chandidya ine.

Joh 2:18 Ndipo Ayuda adayankha nati kwa Iye, Mutiwonetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?

Joh 2:19 Yesu adawayankha, nati, Pasulani kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuwutsa.

Joh 2:20 Pamenepo Ayuda adati, zaka makumi anayi kudza zisanu ndi chimodzi adali mkumanga kachisiyu, kodi inu mudzamuwutsa masiku atatu?

Joh 2:21 Koma Iye adali kunena za kachisi wa thupi lake.

Joh 2:22 Chifukwa chake atawuka kwa akufa, ophunzira ake adakumbukira kuti adanena ichi; ndipo adakhulupirira cholemba, ndi mawu amene Yesu adanena.

Joh 2:23 Tsopano pamene Iye adali mu Yerusalemu pa Paskha paphwando, ambiri adakhulupirira dzina lake, pakuwona zozizwitsa zake zimene adachitazi.

Joh 2:24 Koma Yesu sadzipereka mwini yekha kwa iwo; chifukwa Iye adadziwa anthu onse.

Joh 2:25 Ndipo sadasowa wina achite umboni za munthu; pakuti adadziwa Iye yekha chimene chidali mwa munthu.



3

Joh 3:1 Padali munthu wa afarisi dzina lake Nikodemo, wolamulira Ayuda;

Joh 3:2 Iyeyu adadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zozizwitsa izi zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.

Joh 3:3 Yesu adayankha nati kwa iye, Indetu, indetu ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuwona Ufumu wa Mulungu.

Joh 3:4 Nikodemo adanena kwa Iye, munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso kachiwiri m’mimba ya amake ndi kubadwa?

Joh 3:5 Yesu adayankha, Indetu, indetu ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa Ufumu wa Mulungu.

Joh 3:6 Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu.

Joh 3:7 Usadabwe chifukwa ndidati kwa iwe, uyenera kubadwa mwatsopano.

Joh 3:8 Mphepo iwomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mawu ake, koma sudziwa kumene yichokera, ndi kumene yipita; chotero ali yense wobadwa mwa mzimu.

Joh 3:9 Nikodemo adayankha nati kwa iye, izi zingatheke bwanji?

Joh 3:10 Yesu adayankha nati kwa iye, kodi uli mphunzitsi wa Israyeli, ndipo sudziwa izi?

Joh 3:11 Indetu, indetu ndinena kwa iwe, Tiyankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiwona; ndipo umboni wathu simuwulandira.

Joh 3:12 Ngati ndakuwuzani za pansi pano, ndipo simukhulupirira, mudzakhulupirira bwanji, ngati ndikuwuzani za kumwamba?

Joh 3:13 Ndipo kulibe munthu adakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala m’Mwambayo.

Joh 3:14 Ndipo monga Mose adakweza njoka m’chipululu, chotero Mwana wa Munthu ayenera kukwezekedwa;

Joh 3:15 Kuti yense wakukhulupirira mwa Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.

Joh 3:16 Pakuti Mulungu adakonda dziko lapansi, kotero kuti adapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wokhulupirira mwa Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.

Joh 3:17 Pakuti Mulungu sadatume Mwana wake ku dziko lapansi; kuti akatsutse dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe kupyolera mwa Iye.

Joh 3:18 Wokhulupirira pa Iye satsutsidwa: wosakhulupirira watsutsidwa ngakhale tsopano, chifukwa sadakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.

Joh 3:19 Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuwunika kudadza ku dziko lapansi, ndipo anthu adakonda mdima koposa kuwunika; pakuti ntchito zawo zidali zoipa.

Joh 3:20 Pakuti yense wochita zoipa adana ndi kuwunika, ndipo sabwera kwa kuwunika, kuti ntchito zake zingatsutsidwe.

Joh 3:21 Koma wochita chowonadi abwera kukuwunika, kuti ntchito zake ziwonekere kuti zidachitidwa mwa Mulungu.

Joh 3:22 Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake ku dziko la Yudeya; ndipo pamenepo adaswela nawo pamodzi, ndipo anabatizidwa.

Joh 3:23 Ndipo Yohane adalinkubatiza mu Ayinoni pafupi pa Salemu, chifukwa padali madzi ambiri pamenepo; ndipo adafika nabatizidwa.

Joh 3:24 Pakuti Yohane adali asadayikidwe m’ndende pamenepo.

Joh 3:25 Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ake a Yohane ndi a Yuda zokhudza mayeretsedwe.

Joh 3:26 Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene adali ndi inu tsidya lija la Yordano, amene mudachitira umboni, taonani yemweyu akubatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.

Joh 3:27 Yohane adayankha nati, Munthu sakhoza kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba.

Joh 3:28 Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndidati, Sindine Khristu, koma kuti ndiri wotumidwa m’tsogolo mwake mwa Iye.

Joh 3:29 Iye amene ali naye mkwatibwi ali ndi mkwati, koma mzake wa mkwatiyo, wakuyimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mawu a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe change chimene chikwaniritsidwa.

Joh 3:30 Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe.

Joh 3:31 Iye wochokera kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse.

Joh 3:32 Chimene adachiwona nachimva, achita umboni wa ichi chomwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wake.

Joh 3:33 Iye amene alandira umboni wake adayikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali woona.

Joh 3:34 Pakuti Iye amene Mulungu adamtuma alankhula mawu a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu kwa Iye ndi muyeso.

Joh 3:35 Atate akonda Mwana,ndipo wapatsa zinthu zonse m’dzanja lake.

Joh 3:36 Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzawona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.



4

Joh 4:1 Chifukwa chake pamene Ambuye adadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu adapanga ndipo adabatiza ophunzira ambiri koposa Yohane.

Joh 4:2 (Angakhale Yesu sanabatiza mwiniyo koma ophunzira ake.)

Joh 4:3 Iye adachoka ku Yudeya, ndipo adapitanso ku Galileya.

Joh 4:4 Ndipo adayenera kudutsa pakati pa Samariya.

Joh 4:5 Chifukwa chake adadza ku mudzi wa Samariya, dzina lake Sukari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe.

Joh 4:6 Ndipo pamenepo padali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu popeza adatopa ndi ulendo wake motero adakhala pachitsime: kunali ngati ola lachisanu ndi chimodzi.

Joh 4:7 Kunadza mkazi wa ku Samariya kudzatunga madzi; Yesu adanena naye, Undipatse Ine ndimwe.

Joh 4:8 (Pakuti ophunzira ake adachoka kupita kumzinda kuti akagule chakudya.)

Joh 4:9 Pamenepo mkazi wa ku Samariyayo adanena ndi Iye, Bwanji Inu, muli m’Yuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? Pakuti Ayuda sayenderana nawo a Samariya.

Joh 4:10 Yesu adayankha nati kwa iye. Ukadadziwa mphatso ya Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.

Joh 4:11 Mkaziyo adanena ndi Iye, Ambuye, mulibe chotungira madzi, ndi chitsime chiri chakuya; ndipo mwatenga kuti madzi a moyo?

Joh 4:12 Kodi muli wamkulu kuposa atate wathu Yakobo amene adatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake ndi ng’ombe zake?

Joh 4:13 Yesu adayankha nati kwa iye, yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu.

Joh 4:14 Koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira m’moyo wosatha.

Joh 4:15 Mkaziyo adanena kwa Iye, Ambuye , ndipatseni madzi amenewo, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisabwere kuno kudzatunga.

Joh 4:16 Yesu adanena kwa iye, pita, kamuyitane mwamuna wako, nubwere kuno.

Joh 4:17 Mkaziyo adayankha nati kwa Iye, ndiribe mwamuna. Yesu adanena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe;

Joh 4:18 Pakuti wakhala nawo amuna asanu; ndipo iye amene ukukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zowona.

Joh 4:19 Mkazi adanena ndi Iye, Ambuye ndazindikira kuti ndinu Mneneri.

Joh 4:20 Makolo athu ankalambira m’phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.

Joh 4:21 Yesu adanena naye mkazi, khulupirira Ine, ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri ili, kapena mu Yerusalemu.

Joh 4:22 Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso cha kwa Ayuda.

Joh 4:23 Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo imene olambira wowona adzalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.

Joh 4:24 Mulungu ndi Mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.

Joh 4:25 Mkazi adanena ndi Iye, ndidziwa kuti Mesiya abwera wotchedwa Khristu: akadzabwera Iyeyu, adzatiwuza zinthu zonse.

Joh 4:26 Yesu adanena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene.

Joh 4:27 Ndipo pamenepo adabwera ophunzira ake nazizwa kuti adalimkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina adati, Mukufuna chiyani? Kapena, mukulankhula naye chiyani?

Joh 4:28 Pamenepo mkazi adasiya mtsuko wake wa madzi napita kumzinda, nanena ndi anthu,

Joh 4:29 Idzani mudzawone munthu amene adandiwuza zinthu ziri zonse ndidazichita: kodi uyu sindiye Khristu?

Joh 4:30 Ndipo iwo adatuluka mumzinda nabwera kwa Iye.

Joh 4:31 Pa mphindikati iyi ophunzira ake adampempha Iye, ndi kunena, Rabi, idyani.

Joh 4:32 Koma Iye adati kwa iwo, Ine ndiri nacho chakudya chimene inu simuchidziwa.

Joh 4:33 Chifukwa chake ophunzira adanena wina ndi mzake, kodi pali wina adamtengera Iye kanthu kakudya?

Joh 4:34 Yesu adanena nawo, chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene adandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.

Joh 4:35 Kodi simunena inu, kuti, yatsala miyezi inayi, ndipo kudza kukolola? Onani ndinena kwa inu, kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kuti mukololedwe.

Joh 4:36 Wakukolola alandira kulipira, nasonkhanitsira zipatso ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi wokololayo.

Joh 4:37 Pakuti m’menemo chonenacho chiri chowona, wofesa ndi wina, womweta ndi winanso

Joh 4:38 Ine ndidatuma inu kukamweta chimene simudagwirirapo ntchito: ena adagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yawo kukakolola.

Joh 4:39 Ndipo mumzinda muja Asamariya ambiri adamkhulupirira Iye, chifukwa cha mawu a mkazi wochita umboniyo kuti, adandiwuza ine zinthu ziri zonse ndidazichita.

Joh 4:40 Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, adamfunsa akhale nawo; ndipo adakhala komweko masiku awiri.

Joh 4:41 Ndipo ambiri oposa adakhulupirira chifukwa cha mawu ake;

Joh 4:42 Ndipo adanena kwa mkazi, kuti, tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kuyankhula kwako; pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti uyu ndithu ndi Khristu, Mpulumutsi wadziko lapansi.

Joh 4:43 Tsopano atapita masiku awiriwo adachoka komweko kupita ku Galileya.

Joh 4:44 Pakuti Yesu mwini adachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m’dziko la kwawo.

Joh 4:45 Ndipo pamene adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira Iye, atakawona zonse zimene adazichita mu Yerusalemu pamphwando; pakuti iwonso adapita kuphwando.

Joh 4:46 Choncho Yesu adabweranso ku Kana wa ku Galileya, kumene adasandutsa madzi vinyo. Ndipo kudali nduna yina ya mfumu mwana wake adadwala mu Kapernao.

Joh 4:47 Iyeyu pamene adamva kuti Yesu wachoka ku Yudeya nafika ku Galileya, adapita kwa Iye nampempha kuti atsike kukachiritsa mwana wake; pakuti adali pafupi imfa.

Joh 4:48 Pamenepo Yesu adati kwa iye, ngati simuwona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.

Joh 4:49 Nduna ya mfumuyo idanena kwa Iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga.

Joh 4:50 Yesu adanena naye, Pita, mwana wako ali ndi moyo. Munthuyo adakhulupirira mawu amene Yesu adanena naye, napita.

Joh 4:51 Ndipo m’mene tsopano iye adalikutsika, atumiki ake adakomana naye, nanena, kuti mwana wanu ali ndi moyo.

Joh 4:52 Ndipo adawafunsa ola lake limene adayamba kuchilalo, pamenepo adati kwa iye, kuti, Dzulo, ola la chisanu ndi chiwiri malungo adamsiya.

Joh 4:53 Choncho atateyo adadziwa kuti ndi ola lomwelo limene Yesu adati kwa iye, mwana wako ali ndi moyo; ndipo adakhulupirira iye yekha ndi a pabanja lake onse.

Joh 4:54 Ichi ndi chozizwa chachiwiri Yesu adachita, atachokera ku Yudeya, ndi kulowa mu Galileya.



5

Joh 5:1 Zitapita izi padali phwando la Ayuda; ndipo Yesu adakwera kupita ku Yerusalemu.

Joh 5:2 Koma padali thamanda mu Yerusalemu pa chipata cha nkhosa, lotchedwa mu Chihebri lilime Betsaida, liri ndi makumbi asanu.

Joh 5:3 M’menemo mumagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, wosayenda, opuwala, kudikira madzi kuti avundulidwe.

Joh 5:4 Ndipo m’ngelo amatsika nyengo yina mu thamandalo, nabvundula madzi; aliyense amene amayambirira kulowamo m’madzi atabvundulidwa amakhala wokonzedwa kumatenda ali wonse adali nawo.

Joh 5:5 Ndipo padali munthu wina apo, wodwala kwa zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.

Joh 5:6 Pamene Yesu adamuwona iye atagona pamenepo, adadziwa kuti adatero kwa nthawi yayitali, adanena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi?

Joh 5:7 Wodwalayo adayankha Iye, Ambuye, ndiribe munthu wondibviyika ine muthamanda, pakuti panthawi imene madzi abvundulidwa; wina amakhala atatsika kale, ine ndisadatsike.

Joh 5:8 Yesu adanena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende.

Joh 5:9 Ndipo pomwepo munthuyo adachira, nayalula mphasa yake, nayenda; ndipo tsiku lomwelo lidali la sabata.

Joh 5:10 Chifukwa chake Ayuda adanena kwa wochiritsidwayo, Ndi sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako.

Joh 5:11 Koma iyeyu adayankha iwo, Iye amene adandichiritsa, yemweyu adati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende.

Joh 5:12 Ndipo iwo adamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe. Yalula mphasa yako nuyende.

Joh 5:13 Koma wochiritsidwayo sanadziwa ngati ndani, pakuti Yesu adachoka kachetechete, popeza padali khamu pa malo paja.

Joh 5:14 Zitapita izi Yesu adampeza iye m’kachisi, nati kwa iye, Tawona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.

Joh 5:15 Munthuyo adachoka, nawuza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa.

Joh 5:16 Ndipo chifukwa cha ichi, Ayuda adalondalonda Yesu, nafuna kumupha chifukwa adachita zinthu izi padzuwa la sabata.

Joh 5:17 Koma Yesu adayankha iwo, atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.

Joh 5:18 Chifukwa cha ichi Ayuda adawonjeza kufuna kumupha, sichifukwa cha kuswa tsiku la sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.

Joh 5:19 Pamenepo Yesu adayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza mwana kuchita kanthu pa yekha koma chimene awona Atate achichita ndicho pakuti zinthu zimene Iye azichita zomwezonso mwananso azichita momwemo.

Joh 5:20 Pakuti Atate akonda namuwonetsa Iye zinthu zimene zonse azichita yekha; ndipo adzamuwonetsa Iye ntchito za zikulu zoposa izi, kuti mukazizwe.

Joh 5:21 Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.

Joh 5:22 Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma adapereka kuweruza konse kwa Mwana.

Joh 5:23 Kuti anthu onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene adamtuma Iye.

Joh 5:24 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mawu anga, ndi kukhulupirira Iye amene adandituma Ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo iye satsutsidwa, koma wachokera ku imfa, kulowa m’moyo.

Joh 5:25 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.

Joh 5:26 Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso adapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha.

Joh 5:27 Ndipo adampatsa Iye ulamuliro wakuzenga milandunso, pakuti Iye ali Mwana wa munthu.

Joh 5:28 Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake.

Joh 5:29 Ndipo adzatuluka; amene adachita zabwino, kukuwuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuwuka kwa chiwonongeko.

Joh 5:30 Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali wolungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Atate wondituma Ine.

Joh 5:31 Ngati ndichita umboni mwa Ine ndekha, umboni wanga suli wowona.

Joh 5:32 Pali wina wochita umboni wa Ine; ndipo ndidziwa kuti umboni umene Iye andichitira Ine uli wowona.

Joh 5:33 Inu mudatuma kwa Yohane, ndipo iye adachitira umboni chowonadi.

Joh 5:34 Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu; koma ndinena zinthu izi, kuti inu mukapulumutsidwe.

Joh 5:35 Iyeyo adali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu mudafuna kukondwera m’kuwunika kwake kanthawi.

Joh 5:36 Koma Ine ndiri nawo umboni wa ukulu woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate adandipatsa Ine ndizitsirize ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate adandituma Ine.

Joh 5:37 Ndipo Atate mwini yekha wonditumayo, Iyeyu wandichitira Ine umboni. Simudamva mawu ake nthawi iri yonse kapena kuwona mawonekedwe ake.

Joh 5:38 Ndipo mulibe mawu ake wokhala mwa inu; chifukwa kuti amene Iyeyu adamtuma, inu simumkhulupirira.

Joh 5:39 Musanthula m’malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nawo moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;

Joh 5:40 Ndipo simufuna kubwera kwa Ine, kuti mukhale ndi moyo.

Joh 5:41 Ine sindilandira ulemu kwa anthu.

Joh 5:42 Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha.

Joh 5:43 Ndabwera Ine m’dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; koma akabwera wina m’dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamulandira.

Joh 5:44 Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mzake ndipo ulemu wochokera kwa Mulungu yekha simuwufuna?

Joh 5:45 Musaganize kuti Ine ndidzakutsutsani inu kwa Atate; pali m`modzi wakukutsutsani, ndiye Mose amene inu mumkhulupirira

Joh 5:46 Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; pakuti iyeyu adalembera za Ine.

Joh 5:47 Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mawu anga?



6

Joh 6:1 Zitapita zinthu izi adachoka Yesu kupita kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiya.

Joh 6:2 Ndipo khamu lalikulu lidamtsata Iye, chifukwa adawona zozizwitsa zimene adachita pa wodwala.

Joh 6:3 Koma Yesu adakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi wophunzira ake.

Joh 6:4 Ndipo Paskha, phwando la Ayuda, adayandikira.

Joh 6:5 Pamenepo Yesu pokweza maso ake ndi kuwona kuti khamu lalikulu lirimkudza kwa Iye, adanena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?

Joh 6:6 Koma adanena ichi kuti amuyese; pakuti adadziwa yekha chimene adzachita.

Joh 6:7 Filipo adayankha Iye, mikate ya mazana awiri siyikwanira iwo, kuti yense atenge pang’ono.

Joh 6:8 M’modzi wa wophunzira ake Andreya, m’bale wake wa Simoni Petro, adanena ndi Iye.

Joh 6:9 Pali m’nyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabalere, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere?

Joh 6:10 Ndipo Yesu adati, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo padali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo adakhala pansi, chiwerengero chawo chinali zikwi zisanu.

Joh 6:11 Pomwepo Yesu adatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, adagawira kwa ophunzira ake: ndipo ophunzira kwa iwo akukhala pansi momwemonso ndi tinsomba monga iwo adafuna.

Joh 6:12 Ndipo pamene adakhuta, Iye adanena kwa wophunzira ake, sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.

Joh 6:13 Pomwepo adasonkhanitsa, nadzadza mitanga khumi ndi iwiri ndi makombo a mikate isanuyo yabalere, imene idatsalira amadyawo.

Joh 6:14 Chifukwa chake anthu, powona chozizwa chimene Yesu adachita, adanena, ichi ndiye chowonadi kuti m’neneri ndithu wadza ku m’dziko lapansi.

Joh 6:15 Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kubwera kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, adachokanso kupita ku phiri pa yekha.

Joh 6:16 Koma pofika madzulo, wophunzira ake adatsikira kunyanja;

Joh 6:17 Ndipo adalowa muchombo, nawoloka nyanja kupita ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu adali asanadze kwa iwo.

Joh 6:18 Ndipo nyanja idawuka chifukwa cha mphepo yayikulu idawomba.

Joh 6:19 Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, adawona Yesu akuyenda pamwamba panyanja, ndi kuyandikira chombo; ndipo adachita mantha.

Joh 6:20 Koma Iye adati kwa iwo, Ndine; musawope.

Joh 6:21 Pamenepo adalola kumlandira m’chombo; ndipo pomwepo chombo chidafika kumtunda kumene adalikunkako.

Joh 6:22 M’mawa mwake pamene anthu adayima tsidya lija la nyanja adawona kuti padalibe chombo china koma chimodzi chimne ophunzira ake adalowa ndi kuti Yesu sadalowa pamodzi ndi wophunzira m`chombomo, koma wophunzira ake adachoka pa wokha;

Joh 6:23 ( Koma zombo zina zidachoka ku Tiberiya, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate pamene Yesu adayamika;)

Joh 6:24 Chifukwa chake pamene anthu adawona kuti padalibe Yesu, ndi wophunzira akenso padalibe, iwo wokha adalowa m`zombozo nadza ku Kapernao, alikumfuna Yesu.

Joh 6:25 Ndipo pamene adampeza Iye tsidya lina la nyanja, adati kwa Iye, Rabi, munadza kuno liti?

Joh 6:26 Yesu adayankha iwo nati, indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa mudawona zozizwitsa, koma chifukwa mudadya mkate, ndipo mudakhuta.

Joh 6:27 Gwirani ntchito sichifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chatsalira ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.

Joh 6:28 Pamenepo adati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?

Joh 6:29 Yesu adayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo adamtuma.

Joh 6:30 Chifukwa chake adati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tiwone ndi kukhulupirira Inu?

Joh 6:31 Atate athu adadya mana m’chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera kumwamba adawapatsa iwo kudya.

Joh 6:32 Chifukwa chake Yesu adati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, si Mose amene adakupatsani inu mkate wakumwamba; koma Atate wanga anakupatsani inu mkate wowona wa Kumwamba.

Joh 6:33 Pakuti mkate wa Mulungu ndiye Iye wotsika pansi kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo ku dziko lapansi.

Joh 6:34 Pamenepo adati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umenewu nthawi zonse.

Joh 6:35 Yesu adati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala ndi iye wokhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.

Joh 6:36 Koma ndidati kwa inu, Kuti ngakhale mwandiwona, simukhulupirira.

Joh 6:37 Onse amene andipatsa Ine Atate adzadza kwa Ine; ndipo iye wakudza kwa Ine sindidzamtaya konse kunja.

Joh 6:38 Pakuti ndidatsika Kumwamba, sikuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene adandituma Ine.

Joh 6:39 Ndipo ichi ndicho chifuniro cha Atate amene adandituma Ine, kuti za ichi chonse Iye adandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma kuti ndichiwukitse ichi tsiku lomaliza.

Joh 6:40 Ichi ndicho chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, kuti yense woyang’ana Mwana, ndi kukhulupirira pa Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomaliza.

Joh 6:41 Ndipo Ayuda adang’ung’udza za Iye, chifukwa adati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba.

Joh 6:42 Ndipo iwo adanena, Si Yesu uyu mwana wa Yosefe, atate wake ndi amayi wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndidatsika Kumwamba?

Joh 6:43 Yesu adayankha nati kwa iwo, Musang’ung’udze mwa inu nokha.

Joh 6:44 Palibe munthu angathe kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomaliza.

Joh 6:45 Zalembedwa mwa aneneri, ndipo iwo onse adzakhala wophunzitsidwa za Mulungu. Chifukwa chake munthu ali yense amene adamva ndipo waphunzira za Atate adza kwa Ine.

Joh 6:46 Sikuti munthu wina wawona Atate, koma kupatula Iye amene ali wchokera kwa Mulungu, ameneyo wawona Atate.

Joh 6:47 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira pa Ine ali nawo moyo wosatha.

Joh 6:48 Ine ndine mkate wa moyo.

Joh 6:49 Makolo anu adadya mana m’chipululu, ndipo adamwalira.

Joh 6:50 Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira.

Joh 6:51 Mkate wamoyo wotsika Kumwamba, Ndine amene. Ngati munthu aliyense akadyako mkate umenewu, adzakhala ndi moyo kosatha, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine. Ndiwo thupi langa limene ndidzapereka, likhale moyo wa dziko lapansi.

Joh 6:52 Pamenepo Ayuda adatetana wina ndi mzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?

Joh 6:53 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.

Joh 6:54 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuwukitsa iye tsiku lomaliza.

Joh 6:55 Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu.

Joh 6:56 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.

Joh 6:57 Monga Atate wamoyo adandituma Ine, ndipo Inenso ndiri ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.

Joh 6:58 Uwu ndiwo mkate wotsika Kumwamba: si monga makolo anu, adadya mana namwalira; iye wakudya mkate umenewu adzakhala ndi moyo nthawi zonse.

Joh 6:59 Zinthu izi adanena musunagoge, Iye pophunzitsa mu Kapernao.

Joh 6:60 Pamenepo ambiri akuphunzira ake pakumva izi, adati, Mawu awa ndi wosautsa; akhoza kumva awa ndani?

Joh 6:61 Koma Yesu podziwa mwa Iye yekha kuti wophunzira ake alikung’ung’udza chifukwa cha ichi, adati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?

Joh 6:62 Nanga bwanji mukadzawona Mwana wa Munthu alikukwera kumene adali kale lomwe?

Joh 6:63 Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mawu amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.

Joh 6:64 Koma pali ena mwa inu amene sakhulupilira. Pakuti Yesu adadziwiratu poyamba amene ali wosakhulupirira, ndi amene adzampereka Iye.

Joh 6:65 Ndipo adanena chifukwa cha ichi ndidati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate wanga.

Joh 6:66 Pa ichi ambiri wophunzira ake adabwerera m’mbuyo, ndipo sadayendayendanso ndi Iye.

Joh 6:67 Chifukwa chake Yesu adati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka?

Joh 6:68 Simoni Petro adamuyankha Iye, Ambuye, tidzapita kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.

Joh 6:69 Ndipo ife tikukhulupirira, ndipo tatsimikiza kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wa moyo.

Joh 6:70 Yesu adawayankha iwo, Kodi sindidakusankhani khumi ndi awiri, ndipo wa inu m’modzi ali m`dierekezi?

Joh 6:71 Koma adanena za Yudasi Isikariyote, mwana wa Simoni, pakuti iye ndiye amene adzampereka Iye, wokhala m’modzi wakhumi ndi awiri.



7

Joh 7:1 Ndipo zitapita izi Yesu, adayendayenda mu Galileya; pakuti sadafuna kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda adafuna kumupha Iye.

Joh 7:2 Koma phwando la Ayuda la misasa, lidayandikira.

Joh 7:3 Choncho abale ake adati kwa Iye, chokani pano, mupite ku Yudeya, kuti wophunzira anunso akapenye ntchito zanu zimene mukuchita.

Joh 7:4 Pakuti palibe munthu amachita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera. Ngati mukuchita izi, dziwonetsereni eni nokha ku dziko lapansi.

Joh 7:5 Pakuti angakhale abale ake sadakhulupirira Iye.

Joh 7:6 Chifukwa chake Yesu adanena nawo, nthawi yanga siyidafike; koma nthawi yanu yakonzeka kale.

Joh 7:7 Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake ziri zoyipa.

Joh 7:8 Kwerani inu kupita kuphwando; sindikwera Ine ku phwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siyidakwanire.

Joh 7:9 Ndipo pamene adanena nawo mawu awa adakhalabe mu Galileya.

Joh 7:10 Koma pamene abale ake adakwera kupita kuphwando, pomwepo Iyenso adakwera, si mowonekera koma monga mobisika.

Joh 7:11 Pomwepo Ayuda adalikumfuna Iye paphwando, nanena, Ali kuti uja?

Joh 7:12 Ndipo kudali kung’ung’udza kwambiri za Iye pakati pa anthu; popeza kuti ena adanena, kuti Ali wabwino; koma ena adanena, Iyayi, koma asocheretsa anthu.

Joh 7:13 Ngakhale adatero padalibe munthu adalankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuwopa Ayuda.

Joh 7:14 Koma pamene padafika pakati pa phwando Yesu adakwera nalowa m’kachisi, naphunzitsa.

Joh 7:15 Chifukwa chake Ayuda adazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, koma wosaphunzira.

Joh 7:16 Yesu adayankha iwo, nati, chiphunzitso changa sichiri changa, koma cha Iye amene adandituma Ine.

Joh 7:17 Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa ine ndekha.

Joh 7:18 Iye wolankhula zochokera kwa Iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wofuna ulemu wa Iye amene adamtuma, yemweyu ali wowona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.

Joh 7:19 Si Mose kodi adakupatsani chilamulo, ndipo palibe m’modzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha Ine chifukwa chiyani?

Joh 7:20 Anthu adayankha nati, Muli ndi chiwanda: ndani afuna kukuphani Inu?

Joh 7:21 Yesu adayankha nati kwa iwo, Ndachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa nonse.

Joh 7:22 Chifukwa cha ichi Mose adakupatsani inu mdulidwe (sikuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo) ndipo mudula munthu tsiku la sabata.

Joh 7:23 Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku lasabata?

Joh 7:24 Musaweruze monga mwamawonekedwe, koma weruzani chiweruzo cholungama.

Joh 7:25 Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu adanena, kodi suyu amene afuna kumupha?

Joh 7:26 Ndipo tawona amayankhula molimba mtima, ndipo sadanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi aulamuliro akudziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo?

Joh 7:27 Koma ameneyo tidziwa kumene akuchokera koma pamene Khristu adzabwera palibe munthu: m’modzi adzadziwa kumene adzachoka.

Joh 7:28 Pamenepo Yesu adafuwula m’kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, mundidziwa Ine, ndiponso mukudziwa Ine kumene ndichokera; ndipo sindidadza kwa Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali wowona.

Joh 7:29 Ine ndimdziwa Iye; chifukwa ndiri wochokera kwa Iye, nandituma Ine Iyeyu.

Joh 7:30 Pamenepo adafuna kumgwira Iye; koma padalibe wina adamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake idali isadafike.

Joh 7:31 Koma ambiri anthu adakhulupirira Iye; ndipo adanena, pamene Khristu akabwera, kodi adzachita zozizwa zambiri zoposa zimene munthu uyu akuzichita?

Joh 7:32 Afarisi adamva anthu ali kung’ung’udza za Iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi adatuma asilikari kuti akamgwire Iye.

Joh 7:33 Pamenepo Yesu adati kwa iwo, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine.

Joh 7:34 Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo komwe ndiri Ine, inu simungathe kudzako.

Joh 7:35 Chifukwa chake Ayuda adati mwa iwo wokha, Adzapita kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzapita kwa Amitundu wobalalikawo, ndi kuphunzitsa Amitunduwo?

Joh 7:36 Mawu awa amene adanena ndi wotani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine; ndipo komwe ndiri Ine, inu simungathe kudzako?

Joh 7:37 Koma tsiku lomaliza, lalikululo laphwando, Yesu adayimilira nafuwula ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, abwere kwa Ine, namwe.

Joh 7:38 Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chidati, mitsinje ya madzi a moyo idzayenda, kutuluka m’kati mwake.

Joh 7:39 (Koma ichi adati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye adati adzalandire; pakuti Mzimu padalibe pamenepo, chifukwa Yesu sadalemekezedwa panthawi pomwepo).

Joh 7:40 Pamenepo ambiri mwa anthu pakumva mawu awa, adanena, M’neneriyo ndi uyu ndithu.

Joh 7:41 Ena adanena, Uyu ndi Khristu. Koma ena adanena, kodi Khristu abwera kutuluka mu Galileya?

Joh 7:42 Kodi sichidati chilembo kuti Khristu adzabwera kutuluka mwa mbewu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kudali Davide?

Joh 7:43 Tsono kudakhala kusiyana pakati pawo chifukwa cha Iye.

Joh 7:44 Koma ena mwa iwo adafuna kumgwira Iye; koma padalibe munthu adamgwira kumanja.

Joh 7:45 Pamenepo asilikariwo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo iwowa adati kwa iwo, simudamtenga Iye bwanji?

Joh 7:46 Asilikariwo adayankha, chiyambire padalibe munthu adayankhula chotero.

Joh 7:47 Pamenepo Afarisi adayankha iwo, kodi mwanyengedwanso inunso?

Joh 7:48 Kodi wina wa olamulira kapena wa Afarisi adakhulupirira Iye.?

Joh 7:49 Koma anthu awa osadziwa chilamulo, akhala wotembereredwa.

Joh 7:50 Nikodemo adanena kwa iwo, ( iye uja adadza kwa Yesu ndi usiku wokhala m’modzi wa iwo,)

Joh 7:51 Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene akuchita?

Joh 7:52 Adayankha nati kwa iye, kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuwone kuti m’Galileya sadawuka m’neneri.

Joh 7:53 Ndipo munthu aliyense adapita ku nyumba yake.



8

Joh 8:1 Yesu adapita ku phiri la Azitona.

Joh 8:2 Ndipo m’mawa adabweranso kukachisi, ndipo anthu adadza kwa Iye; ndipo m’mene anthu onse adakhala pansi adawaphunzitsa.

Joh 8:3 Ndipo alembi ndi Afarisi adabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m’chigololo, ndipo pamene adamuyimika iye pakati,

Joh 8:4 Iwo adanena kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa ali mkati mochita chigololo.

Joh 8:5 Koma m’chilamulo Mose adatilamulira, tiwaponye miyala otere. Nanga Inu munena chiyani za iye?

Joh 8:6 Koma ichi adanena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomtsutsa Iye. Koma Yesu, m’mene adawerama pansi adalemba pansi ndi chala chake ngati kuti Iye sakuwamva iwo.

Joh 8:7 Koma pamene adakhalakhala alikufunsabe Iye, adaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.

Joh 8:8 Ndipo m’mene adaweramanso adalemba ndi chala chake pansi.

Joh 8:9 Ndipo iwo amene adamva ichi, adatsutsika m’chikumbumtima chawo, natulukamo m’modzi m’modzi, kuyambira akulu, kufikira wotsiriza; ndipo Yesu adatsala yekha ndi mkazi alichiyimile pakati.

Joh 8:10 Koma pamene Yesu adaweramuka, adati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti aja adakutsutsa? Palibe munthu adakutsutsa kodi?

Joh 8:11 Iye adati, Palibe Ambuye. Ndipo Yesu adati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usakachimwenso.

Joh 8:12 Pamenepo Yesu adalankhulanso nawo, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuwunika kwa moyo.

Joh 8:13 Chifukwa chake Afarisi adati kwa Iye, muchita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli wowona.

Joh 8:14 Yesu adayankha nati kwa iwo, Ngakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli wowona; chifukwa ndidziwa kumene ndidachokera ndi kumene ndimukako koma inu simudziwa kumene ndichokera ndi kumene ndipita.

Joh 8:15 Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu.

Joh 8:16 Ndipo ngati ndiweruza Ine, chiweruzo changa chiri chowona; pakuti sindiri ndekha, koma Ine ndi Atate amene adandituma Ine.

Joh 8:17 Zidalembedwanso m’chilamulo chanu kuti umboni wa anthu awiri uli wowona.

Joh 8:18 Ine ndine wochita umboni wa ine ndekha, ndipo Atate amene adandituma Ine achita umboni wa Ine.

Joh 8:19 Chifukwa chake adanena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu adayankha, simudziwa, kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga.

Joh 8:20 Mawu awa adalankhula Yesu ali m’nyumba ya chuma cha Mulungu pophunzitsa m’kachisi; ndipo padalibe munthu adagwira Iye, pakuti nthawi yake siyidafike.

Joh 8:21 Pamenepo adatinso kwa iwo; ndipita Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo mutchimo lanu mudzafa; kumene ndipita Ine, simungathe kufikako.

Joh 8:22 Ndipo Ayuda adanena, kodi adzadzipha yekha? Pakuti akunena, kumene ndipita Ine, simungathe kufikako.

Joh 8:23 Ndipo Iye adanena nawo, Inu ndinu wochokera pansi; ine ndine wochokera kumwamba; inu ndinu adziko lino lapansi; sindiri Ine wadziko lino lapansi.

Joh 8:24 Chifukwa chake ndidati kwa inu, kuti mudzafa m’machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m’machimo anu.

Joh 8:25 Pamenepo adanena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu adati kwa iwo, chimene ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pa chiyambi.

Joh 8:26 Ndiri nazo zambiri zolankhula ndi zoweruza za inu; koma wondituma Ine ali wowona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.

Joh 8:27 Iwo sadazindikira kuti adalikunena nawo za Atate.

Joh 8:28 Chifukwa chake Yesu adati, pamene mudzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga adandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.

Joh 8:29 Ndipo Iye wondituma Ine ali ndi Ine; Atate sadandisiye Ine ndekha; chifukwa ndichita Ine zinthu zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.

Joh 8:30 Pamene Iye adalankhula mawu awa, ambiri adakhulupirira pa Iye.

Joh 8:31 Pamenepo Yesu adanena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli wophunzira anga ndithu;

Joh 8:32 Ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.

Joh 8:33 Adamuyankha Iye, tiri mbewu ya Abrahamu, ndipo sitidakhala akapolo a munthu nthawi ili yonse; munena bwanji, Mudzayesedwa a ufulu?

Joh 8:34 Yesu adayankha iwo, nati, indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wochita tchimo ali kapolo wa tchimolo.

Joh 8:35 Koma kapolo sakhala m’nyumba nthawi yonse koma; mwana ndiye amakhala nthawi yonse.

Joh 8:36 Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu.

Joh 8:37 Ndikudziwa kuti muli mbewu ya Abrahamu; koma mukufuna kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu.

Joh 8:38 Ine ndilankhula zimene ndidawona kwa Atate, ndipo inunso muchita chimene mudawona kwa Atate wanu.

Joh 8:39 Adamuyankha nati kwa Iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu adanena nawo, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu.

Joh 8:40 Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndidalankhula ndi inu chowonadi, chimene ndidamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sadachita.

Joh 8:41 Inu muchita ntchito za atate wanu. Adati kwa Iye, sitinabadwe ife m’chiwerewere; tiri naye Atate m’modzi ndiye Mulungu.

Joh 8:42 Yesu adati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukakonda Ine; pakuti Ine ndidatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindidadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu adandituma Ine.

Joh 8:43 Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa chiyani? Chifukwa simungathe kumva mawu anga.

Joh 8:44 Inu muli wochokera mwa atate wanu m’dierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu adali wakupha kuyambira pachiyambi, ndipo sadayima m’chowonadi, pakuti mwa iye mulibe chowonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake, pakuti ali wabodza, ndi atate wake wabodza.

Joh 8:45 Ndipo chifukwa ndinena ndi inu chowonadi, simukhulupirira Ine.

Joh 8:46 Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ndipo ngati Ine ndinena chowonadi, simukhulupirira Ine chifukwa chiyani?

Joh 8:47 Iye wochokera kwa Mulungu akumva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.

Joh 8:48 Ayuda adamuyankha nati kwa Iye, kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?

Joh 8:49 Yesu adayankha, Ndiribe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.

Joh 8:50 Koma Ine sinditsata ulemerero wanga; ndipo alipo m` modzi woutsata ndi woweruza.

Joh 8:51 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, munthu akasunga mawu anga, sadzawona imfa nthawi yonse.

Joh 8:52 Ayuda adati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu adamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, munthu akasunga mawu anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.

Joh 8:53 Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene adamwalira? Ndi aneneri adamwalira: mudziyesera nokha muli yani?

Joh 8:54 Yesu adayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu;

Joh 8:55 Ndipo inu simudamdziwa Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye; ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mawu ake.

Joh 8:56 Atate wanu Abrahamu adakondwera kuwona tsiku langa; ndipo adawona, nasangalala.

Joh 8:57 Ayuda pamenepo adati kwa Iye, Inu simudafikire zaka makumi asanu, ndipo inu mudawona Abrahamu kodi?

Joh 8:58 Yesu adati kwa iwo, indetu, indetu, ndinena kwa inu, asadakhale Abrahamu, Ine ndilipo.

Joh 8:59 Pamenepo adatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka m’kachisi, nawadutsa iwo pakati pawo, napita.



9

Joh 9:1 Ndipo pamene Yesu amadutsa, adawona munthu wosawona chibadwire.

Joh 9:2 Ndipo wophunizra ake adamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, adachimwa ndani mwini wake, makolo ake, kuti adabadwa wosawona?

Joh 9:3 Yesu adayankha, Sadachimwa ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikawonetsedwe mwa iye.

Joh 9:4 Ndiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, akadali masana; ukadza usiku palibe munthu angathe kugwira nchito.

Joh 9:5 Pakukhala Ine m’dziko lapansi, ndiri kuwunika kwa dziko lapansi.

Joh 9:6 Pamene adanena izi, adalabvulira pansi, nakanda thope ndi malobvuwo, napaka thopelo m’maso mwa munthu wosawonayo.

Joh 9:7 Ndipo adati kwa iye, Pita, ukasambe muthamanda la Siloamu (ndilo losandulika, wotumidwa) pamenepo adapita nakasamba, nabwera akuyang’ana.

Joh 9:8 Ndipo amzake ndi iwo adamuwona kale, kuti adali wopemphapempha, adanena, Kodi si uyu uja adakhala ndi wosaona?

Joh 9:9 Ena adanena, kuti, Ndiyeyu; ena adanena, Iyayi, koma afanana naye. Iyeyu adati, Ndine amene.

Joh 9:10 Pamenepo adanena ndi iye, Nanga maso ako adatseguka bwanji?

Joh 9:11 Iyeyu adayankha, nati, Munthu wotchedwa Yesu adakanda thope, napaka m’maso mwanga, nati kwa ine, pita ku thamanda la Silowamu ukasambe, ndipo ndidapita ndikukasamba, ndipo ndinapenya.

Joh 9:12 Ndipo adati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Adati, sindikudziwa ine.

Joh 9:13 Adapita naye kwa Afarisi iye amene adali wosawona kale.

Joh 9:14 Ndipo lidali tsiku la sabata limene Yesu adakanda thope, namtsegulira iye maso ake.

Joh 9:15 Ndipo Afarisi adamfunsanso, m’mene adapenyera. Ndipo adati kwa iwo, adapaka thope m’maso mwanga, ndidasamba, ndipo ndidapenya.

Joh 9:16 Choncho ena mwa Afarisi adanena, Munthu uyu sadachokere kwa Mulungu, chifukwa sasunga tsiku la sabata. Koma ena adanena, Ngati munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zozizwitsa zotere? Ndipo padali kugawanikana pakati pa iwo.

Joh 9:17 Ndipo adanenanso kwa wosawonayo, Iwe unenanji za Iye? Pakuti adakutsegulira maso ako. Iye adati, Ali m`neneri.

Joh 9:18 Koma Ayuda sadakhulupirira za iye kuti adali wosawona, napenya, kufikira pamene adayitana atate wake ndi amake a iye amene adapenya.

Joh 9:19 Ndipo adawafunsa iwo, nanena kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosawona? Ndipo apenya bwanji tsopano?

Joh 9:20 Makolo ake adayankha nati, Tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosawona.

Joh 9:21 Koma sitidziwa umo wapenyera tsopano; kapena sitimdziwa amene adamtsegula maso ake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha.

Joh 9:22 Mawu awa adanena makolo ake chifukwa adawopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzabvomereza Iye kuti ndiye Khristu, adzachotsedwa m’sunagoge.

Joh 9:23 Chifukwa cha ichi makolo ake adati, mufunseni; ali wamsinkhu.

Joh 9:24 Pamenepo adamuyitananso munthu adali wosawonayo, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.

Joh 9:25 Iye adayankha nati, kaya iye ndi wochimwa kapena ayi, sindikudziwa: chinthu chimodzi ndichidziwa, ndi ichi kuti ndidali wosawona, tsopano ndipenya.

Joh 9:26 Pamemnepo adati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Adatsegula motani iye maso ako?

Joh 9:27 Iye adayankha iwo, Ndidakuwuzani kale, ndipo simudamva; mufuna kumvanso bwanji? Kodi inunso mufuna kukhala wophunzira ake?

Joh 9:28 Ndipo adamulalatira iye, nati, Iwe ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife wophunzira a Mose.

Joh 9:29 Ife tikudziwa kuti Mulungu adalankhula ndi Mose; koma za ameneyo, sitikudziwa kumene akuchokera.

Joh 9:30 Munthuyo adayankha nati kwa iwo, chifukwa chiyani mwa Iye muli chozizwitsa ndi kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo kuti Iye adanditsegulira maso anga.

Joh 9:31 Tsopano tidziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake amvera ameneyo.

Joh 9:32 Kuyambira pachiyambi cha dziko lapansi sikudamveka kuti munthu wina adatsegulira maso munthu wosawona chibadwire.

Joh 9:33 Ngati munthuyu sadachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.

Joh 9:34 Adayankha nati kwa iye, Wobadwa iwe konse m`zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo adamponya kunja.

Joh 9:35 Yesu atamva kuti adamponya kunja; ndipo atampeza iye, adati kwa iye, Kodi ukhulupirira Mwana wa Mulungu?

Joh 9:36 Iyeyu adayankha nati, Ndani Iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire Iye?

Joh 9:37 Yesu adati kwa iye, Wamuwona Iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iye amene.

Joh 9:38 Ndipo iye adati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo adampembedza Iye.

Joh 9:39 Ndipo Yesu adati, Kudzaweruza ndadza Ine ku dziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo openya akhale osawona.

Joh 9:40 Ndipo Afarisi ena akukhala ndi Iye atamva izi, adati kwa Iye, Kodi ifenso ndife osawona?

Joh 9:41 Yesu adati kwa iwo, Mukadakhala osawona simukadakhala ndi tchimo; koma tsopano munena, kuti, tikupenya: choncho tchimo lanu likhala chikhalire.



10

Joh 10:1 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowera pakhomo mkhola la nkhosa koma akwerera pena iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.

Joh 10:2 Koma iye wolowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa.

Joh 10:3 Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndipo nkhosa zimva mawu ake; ndipo ayitana nkhosa za iye yekha mayina awo, nazitsogolera kunja.

Joh 10:4 Pamene atulutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mawu ake.

Joh 10:5 Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; chifukwa sizidziwa mawu a alendo.

Joh 10:6 Fanizo ili Yesu adanena kwa iwo; koma sadazindikira zinthu zimene Yesu adalikuyankhula nawo.

Joh 10:7 Pamenepo Yesu adanenanso nawo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ine ndine khomo lankhosa.

Joh 10:8 Onse amene adadza m’tsogolo mwa ine ali akuba, ndi wolanda; ndipo nkhosa sizidamva iwo.

Joh 10:9 Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza msipu.

Joh 10:10 Siyikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuwononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.

Joh 10:11 Ine ndine mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.

Joh 10:12 Koma iye amene ali mbusa wolipidwa, nkhosa sizikhala zake za iye, akawona m’mbulu ulimkudza, amasiya nkhosazo, nathawa; ndipo m’mbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;

Joh 10:13 Wolipidwa amathawa, chifukwa iye ndi wolipidwa, ndipo sasamalira nkhosa.

Joh 10:14 Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira nkhosa zanga, ndi zanga zindizindikira Ine.

Joh 10:15 Monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.

Joh 10:16 Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala khola limodzi, ndi mbusa m’modzi.

Joh 10:17 Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikawutengenso.

Joh 10:18 Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiwutaya Ine ndekha. Ndiri nayo mphamvu yakuwutaya ndiponso ndiri nayo mphamvu yakuwutenganso; lamulo ili ndidalandira kwa Atate wanga.

Joh 10:19 Padakhalanso kugawanika pakati pa Ayuda chifukwa cha mawu awa.

Joh 10:20 Ndipo ambiri mwa iwo adanena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumvera Iye bwanji?

Joh 10:21 Ena adanena, Mawu awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosawona?

Joh 10:22 Ndipo kudali ku Yerusalemu, paphwando la kudzipereka; idali nyengo yozizira.

Joh 10:23 Ndpo Yesu adalimkuyendayenda m’kachisi m’khumbi la Solomo.

Joh 10:24 Pamenepo Ayuda anadza namzungulira Iye, nanena ndi Iye, kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiwuzeni momveka.

Joh 10:25 Yesu adayankha iwo, Ndakuwuzani, ndipo simukhulupirira. Ntchitozi ndizichita Ine m’dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni.

Joh 10:26 Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa Nkhosa zanga monga ndidanenera kwa inu.

Joh 10:27 Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo Ine ndizizindikira izo, ndipo zinditsata Ine.

Joh 10:28 Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzawonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa.

Joh 10:29 Atate wanga, amene adandipatsa izo ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m’dzanja la Atate wanga.

Joh 10:30 Ine ndi Atate ndife amodzi.

Joh 10:31 Pamenepo Ayuda adatolanso miyala kuti amponye Iye.

Joh 10:32 Yesu adayankha iwo, Ndakuwonetsani ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala Ine?

Joh 10:33 Ayuda adamuyankha Iye, chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.

Joh 10:34 Yesu adayankha iwo, Kodi sikudalembedwa m’chilamulo chanu, ndidati Ine, Muli milungu?

Joh 10:35 Ngati adawatcha milungu iwo, amene mawu a Mulungu adawadzera ndipo malembo sangathe kuthyoledwa;

Joh 10:36 Kodi inu munena za Iye, amene Atate adampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndidati, ndiri Mwana wa Mulungu?

Joh 10:37 Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine.

Joh 10:38 Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.

Joh 10:39 Choncho adafunanso kumgwira Iye; koma adapulumuka m’dzanja lawo.

Joh 10:40 Ndipo adachoka napitanso tsidya lija la Yordano, kumalo kumene kudali Yohane adalikubatiza poyamba paja; ndipo adakhala komweko.

Joh 10:41 Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, sadachita chozizwa Yohane; koma zinthu ziri zonse Yohane adanena za Iye zidali zowona.

Joh 10:42 Ndipo ambiri adakhulupirira pa Iye komweko.



11

Joh 11:1 Tsopano munthu wina adadwala dzina lake Lazaro wa ku Betaniya, wa’mudzi wa Mariya ndi mbale wake Marita.

Joh 11:2 (Adali Mariya uja adadzoza Ambuye ndi mafuta wonunkhila bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake amene mlongo wake Lazaro adadwala.)

Joh 11:3 Choncho alongo ake adatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, wonani, amene mumkonda wadwala.

Joh 11:4 Koma Yesu pamene adamva, adati, kudwala kumeneku sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.

Joh 11:5 Tsopano Yesu adakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro.

Joh 11:6 Pamene adamva kuti Iye akudwala, adakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri.

Joh 11:7 Ndipo pambuyo pake adanena kwa wophunzira ake, Tiyeni tipitenso ku Yudeya.

Joh 11:8 Wophunzira ake adanena kwa Iye, Ambuye, Ayuda adalikufuna kukuponyani miyala, tsopano apa; ndipo mupitanso komweko kodi?

Joh 11:9 Yesu adayankha, kodi sikuli maola khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuwunika kwa dziko lino lapansi.

Joh 11:10 Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuwunika mwa iye.

Joh 11:11 Zinthu izi Iye adati, ndipo zitatha izi adanena nawo, Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndipita kukamuwukitsa iye m’tulo take.

Joh 11:12 Chifukwa chake wophunzira ake adati kwa Iye Ambuye, ngati ali m’tulo adzakhala bwino.

Joh 11:13 Koma Yesu adanena za imfa yake: koma iwowa adayesa kuti adanena za mpumulo wa tulo.

Joh 11:14 Pamenepo Yesu adati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.

Joh 11:15 Ndipo ndikondwera chifukwa cha Inu kuti kudalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye.

Joh 11:16 Pamenepo Tomasi wotchedwa Didimo, adati kwa wophunizra anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi.

Joh 11:17 Ndipo pamene Yesu adadza, adapeza kuti pamenepo atakhala kale m’manda masiku anayi.

Joh 11:18 Ndipo Betaniya adali pafupi pa Yerusalemu, kutalika kwake ngati mitunda khumi ndi isanu.

Joh 11:19 Koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wawo.

Joh 11:20 Pamenepo Marita, pakumva mwamsanga kuti Yesu alinkudza, adapita kukakomana ndi Iye; koma Mariya adakhalabe m’nyumba.

Joh 11:21 Ndipo Marita adati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala Inu kuno mlongo wanga sakadafa.

Joh 11:22 Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu.

Joh 11:23 Yesu adanena naye, Mlongo wako adzawukanso.

Joh 11:24 Marita adanena kwa Iye, Ndidziwa kuti adzawuka mkuwukitsidwa kwa tsiku lomaliza.

Joh 11:25 Yesu adati kwa iye, Ine ndine kuwuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;

Joh 11:26 Ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira Ichi?

Joh 11:27 Adanena kwa Iye, inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, wakudza m’dziko lapansi.

Joh 11:28 Ndipo m’mene adati ichi adachoka nayitana Mariya m’bale wake m’seri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuyitana iwe.

Joh 11:29 Koma iyeyo, pakumva, adanyamuka nsanga, nabwera kwa Iye.

Joh 11:30 Tsopano Yesu adali asadafike kumudzi, koma adali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye.

Joh 11:31 Pamenepo Ayuda wokhala naye m’nyumba ndi kumtonthoza iye, pakuwona Mariya adanyamuka msanga, natuluka, namtsata iye nanena kuti apita ku manda kukalira komweko.

Joh 11:32 Pamene Mariya adafika pamene padali Yesu, m’mene adamuwona Iye, adagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.

Joh 11:33 Pamenepo Yesu, pakumuwona iye alikulira, adadzuma mumzimu, nabvutika mwini.

Joh 11:34 Adati, Mwamuyika kuti iye? Adanena ndi Iye, Ambuye, tiyeni, mukawone.

Joh 11:35 Yesu adalira.

Joh 11:36 Ndipo Ayuda adanena, Tawonani momwe, adamkondera!

Joh 11:37 Koma ena mwa iwo adati, Uyu wotsegulira maso wosawona uja, sakadakhoza kodi kuchita kuti sakadafa ameneyunso?

Joh 11:38 Pamenepo Yesu adadzumanso mwa Iye yekha nafika kumanda. Koma padali phanga, ndipo mwala udayikidwa pamenepo.

Joh 11:39 Yesu adanena, chotsani mwala. Marita, mlongo, wake wa womwalirayo adanena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anayi.

Joh 11:40 Yesu adanena naye, Kodi sindinati kwa iwe kuti ngati, ukhulupirira, udzawona ulemerero wa Mulungu.

Joh 11:41 Ndipo adachotsa mwala, kuchokera pa malo pamene adayikapo womwalirayo. Ndipo Yesu adakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti mudamva Ine.

Joh 11:42 Ndipo ndidadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuyimilira pozungulira ndidanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu mudandituma Ine.

Joh 11:43 Ndipo m’mene adanena izi, adafuwula ndi mawu akulu, Lazaro, tuluka.

Joh 11:44 Ndipo womwalirayo adatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake idazingidwa ndi kamsalu. Yesu adati kwa iwo, M’masuleni iye, ndipo mlekeni apite.

Joh 11:45 Ndipo ambiri a mwa Ayuda amene adadza kwa Mariya, m’mene adawona zinthu zimene Yesu adachita adakhulupirira Iye.

Joh 11:46 Koma ena a mwa iwo adapita kwa Afarisi, nawauza zinthu zimene Yesu adazichita.

Joh 11:47 Pamenepo ansembe akulu, ndi Afarisi adasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu akuchita zozizwitsa zambiri!

Joh 11:48 Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzabwera Aroma nadzamtenga malo athu ndi mtundu wathu.

Joh 11:49 Koma wina wa m’modzi wa iwo, dzina lake Kayafa, wokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho adati kwa iwo, simudziwa kanthu konse inu.

Joh 11:50 Kapena simuganiza kuti mkokoma kwa inu kuti munthu m’modzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usawonongeke.

Joh 11:51 Koma ichi sadanena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho adanenera kuti Yesu adzafera mtunduwo;

Joh 11:52 Ndipo sichifukwa cha mtunduwo wokha ayi; koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu wobalalitsidwawo.

Joh 11:53 Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo adapangana kuti amuphe Iye.

Joh 11:54 Chifukwa chake Yesu sadayendayendanso mowonekera mwa Ayuda, koma adachokapo kupita kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efraimu; nakhala komweko pamodzi ndi wophunzira ake.

Joh 11:55 Koma Paskha wa Ayuda adali pafupi; ndipo ambiri adakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku milaga, usanafike Paskha kukadziyeretsa iwo wokha.

Joh 11:56 Pamenepo adali kumfuna Yesu, nanena wina ndi mzake poyimilira iwo m’kachisi, Muyesa bwanji inu, sadzabwera kuphwando kodi?

Joh 11:57 Koma ansembe akulu ndi afarisi adalamulira, kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, awulule, kuti akamgwire Iye.



12

Joh 12:1 Pomwepo atatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paskha, Yesu adabwera ku Betaniya kumene Lazaro adaukitsidwa kwa akufa.

Joh 12:2 Kumeneko iwo adamkozera Iye chakudya; ndipo Marita adatumikira; koma Lazaro adali m’modzi wa iwo akukhala pachakudya pamodzi ndi Iye.

Joh 12:3 Pamenepo Mariya m’mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta wonunkhira bwino a nardo a mtengo wake wapatali, adadzodza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake ndipo nyumba idadzazidwa ndi m’nunkho wake wa mafutawo.

Joh 12:4 Koma Yudase Isikariyote, mwana wa Simon m’modzi wa wophunzira ake, amene adzampereka Iye, adanena,

Joh 12:5 Bwanji mafuta wonunkhirawa sadagulitsidwe ndi makobiri mazana atatu, ndi kuwapatsa wosauka?

Joh 12:6 Koma adanena ichi sichifukwa adalikusamalira wosauka, koma chifukwa adali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoyikidwamo.

Joh 12:7 Pamenepo Yesu adati, Mlekeni iye, pakuti adachisungira ichi tsiku la kuyikidwa kwanga.

Joh 12:8 Pakuti wosauka muli nawo pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi ine nthawi zonse.

Joh 12:9 Pamenepo ambiri amwa Ayuda adadziwa Iye kuti adali pomwepo; ndipo adabwera, sichifukwa cha Yesu yekha, koma kuti akawonenso Lazaro, amene Iye adamuwukitsa kwa akufa.

Joh 12:10 Koma ansembe akulu adapangana kuti akaphe Lazaronso.

Joh 12:11 Pakuti ambiri a Ayuda adachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu

Joh 12:12 Tsiku limzake anthu ambiri adabwera kuphwando, atamva kuti Yesu alikubwera ku Yerusalemu.

Joh 12:13 Adatenga nthambi za mitengo ya kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuwula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m’dzina la Ambuye, ndiye Mfumu ya Israyeli.

Joh 12:14 Ndipo Yesu, m’mene adapeza kabulu adakhala pamenepo; monga kwalembedwa;

Joh 12:15 Usawope, mwana wamkazi wa Ziyoni; tawona Mfumu yako idza wokhala pa mwana wa bulu.

Joh 12:16 Zinthu izi sadazidziwa wophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu adalemekezedwa, pamenepo adakumbukira kuti izi zidalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi

Joh 12:17 Pamenepo anthu amene adali pamodzi ndi Iye, m’mene adayitana Lazaro kutuluka m’manda, namuwukitsa kwa akufa, adachitira umboni.

Joh 12:18 Chifukwa cha ichinso anthu adabweranso kudzakomana ndi Iye, chifukwa adamva kuti Iye adachita chozozwitsa ichi.

Joh 12:19 Chifukwa chake Afarisi adanena wina ndi mzake, Muwona kuti simupindula kanthu konse; wonani dziko litsata pambuyo pa Iye.

Joh 12:20 Ndipo padali Ahelene ena mwa iwo akukwera kupita kukalambira paphwando.

Joh 12:21 Ndipo iwo adabwera kwa Filipo wa ku Betsaida wa m’Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuwona Yesu.

Joh 12:22 Filipo adabwera nanena kwa Andreya; nabwera Andreya ndi Filipo, nanena ndi Yesu.

Joh 12:23 Ndipo Yesu adayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.

Joh 12:24 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbewu ya tirigu siyigwa m’nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.

Joh 12:25 Iye wokonda moyo wake adzawutaya; ndipo wodana ndi moyo wake m’dziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha.

Joh 12:26 Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.

Joh 12:27 Moyo wanga wabvutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndidadzera nthawi iyi.

Joh 12:28 Atate, Lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mawu wochokera kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.

Joh 12:29 Choncho anthu amene adayimilira ndi kumva mawu adanena kuti kwagunda. Ena adanena, m’ngelo wayankhula ndi Iye.

Joh 12:30 Yesu adayankha nati, Mawu awa sadafike chifukwa cha Ine, koma cha inu.

Joh 12:31 Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.

Joh 12:32 Ndipo Ine, m’mene ndikwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha.

Joh 12:33 Adanena ichi kuzindikiritsa kuti imfa yanji adzafa nayo.

Joh 12:34 Anthu adayankha Iye, Tidamva ife m’chilamulo kuti Khristu akhalakunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu ameneyu ndani?

Joh 12:35 Pamenepo Yesu adati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang’ono ndipo kuwunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuwunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene apita.

Joh 12:36 Pokhala muli nako kuwunika, khulupirirani kuwunikako, kuti mukakhale ana a kuwunikako. Zinthu izi Yesu adalankhula, nachoka nabisala mwini yekha kwa iwo.

Joh 12:37 Koma angakhale adachita zozizwitsa zambiri zotere pamaso pawo iwo sadakhulupirira Iye.

Joh 12:38 Kuti mawu a Yesaya m’neneri akakwaniritsidwe, amene adati, Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu? Ndipo mkono wa Ambuye wabvumbulukira kwa yani?

Joh 12:39 Chifukwa cha ichi sadathe kukhulupirira, pakuti Yesaya adatinso,

Joh 12:40 Wadetsa maso awo, nawumitsa mtima wawo; kuti angawone ndi maso, angazindikire ndi mtima, Nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.

Joh 12:41 Zinthu izi adanena Yesaya chifukwa adawona ulemerero wake; wayankhula za Iye.

Joh 12:42 Ngakhale kudali tero,akulu olamulira ambiri adakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sadabvomereza, kuti angaletsedwe m’sunagoge.

Joh 12:43 Pakuti adakonda ulemerero wa anthu koposa ulemu wa Mulungu.

Joh 12:44 Koma Yesu adafuwula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine.

Joh 12:45 Ndipo wondiwona Ine awona amene adandituma Ine.

Joh 12:46 Ndadza Ine kuwunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.

Joh 12:47 Ndipo ngati wina akumva mawu anga, ndi kusawakhulupirira, Ine sindimuweruza; pakuti sindinabwera kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.

Joh 12:48 Iye amene andikana Ine, ndikusalandira mawu anga, ali naye womuweruza iye; mawu amene ndayankhula, iwowa adzamuweruza iye tsiku lomaliza.

Joh 12:49 Pakuti sindinayankhula mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu adandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikayankhule.

Joh 12:50 Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake liri moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndiyankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndiyankhula.



13

Joh 13:1 Tsopano pasadafike phwando la Paskha Yesu, podziwa kuti nthawi yake idafika yochoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kupita kwa Atate, m’mene adakonda ake a Iye yekha a m’dziko lapansi, adawakonda kufikira chimariziro.

Joh 13:2 Ndipo utangotha mgonera, mdierekezi adatha kuyika mu mtima wake wa Yudase Isikariyote, mwana wamwamuna wa Simoni, kuti ankampereke Iye.

Joh 13:3 Yesu podziwa kuti Atate adampatsa Iye zinthu zonse m’manja mwake, ndi kuti adachokera kwa Mulungu, napita kwa Mulungu,

Joh 13:4 Iye adanyamuka pa mgonero, nabvula malaya ake; ndipo m’mene adatenga chopukutira adadzimanga m’chiwuno.

Joh 13:5 Pomwepo adathira madzi mu chosambira, nayamba kusambitsa mapazi a wophunzira ake ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene adadzimanga nacho.

Joh 13:6 Adadza pomwepo kwa Simoni Petro; Ndipo Petro adanena ndi Iye, Ambuye, Kodi Inu mundisambitsa ine mapazi?

Joh 13:7 Yesu adayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine, suchidziwa tsopano; koma udzadziwa mtsogolo mwake.

Joh 13:8 Petro adanena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga ku nthawi yonse. Yesu adamuyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe gawo pamodzi ndi Ine

Joh 13:9 Simoni Petro adanena ndi Iye, Ambuye, Simapazi anga wokha ayi, komanso manja anga ndi mutu wanga.

Joh 13:10 Yesu adanena naye, Amene adatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse; ndipo inu ndinu woyera, koma si nonse ayi.

Joh 13:11 Pakuti adadziwa amene adzampereka Iye; chifukwa cha ichi adati, simuli woyera nonse.

Joh 13:12 Pamenepo atatha Iye kusambitsa mapazi awo, ndi kubvala malaya ake, adakhalanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi?

Joh 13:13 Inu munditcha Ine Mphunzitsi ndi Ambuye; ndipo munena bwino; pakuti ndine amene.

Joh 13:14 Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mzake.

Joh 13:15 Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.

Joh 13:16 Indetu, indetu ndinena ndi inu, Mtumiki sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye.

Joh 13:17 Ngati mudziwa zinthu izi, wodala inu ngati muzichita izo.

Joh 13:18 Sindinena za inu nonse; ndikudziwa ndawasankha; koma kuti cholemba chikwaniritsidwe, Iye wakudya mkate adatsamilitsa chidendene chake molimbana ndi Ine.

Joh 13:19 Tsopano ndinena kwa inu, Chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.

Joh 13:20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene aliyense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.

Joh 13:21 Yesu m’mene adanena izi, adabvutika mumzimu, nachitira umboni, nati, Indetu, Indetu, ndinena ndi inu, kuti m’modzi wa inu adzandipereka Ine.

Joh 13:22 Wophunzira adalimkupenyana wina ndi mzake ndi kusinkhasinkha kuti adanena za yani.

Joh 13:23 Ndipo m’modzi wa wophunzira ake, amene Yesu adamkonda, adatsamira pa chifuwa cha Yesu.

Joh 13:24 Pamenepo Simoni Petro adamkodola nanena naye, Utiwuze ndiye yani amene anena za iye.

Joh 13:25 Iyeyu potsamira pomwepo, pa chifuwa cha Yesu, adanena ndi Iye, Ambuye, ndiye yani?

Joh 13:26 Ndipo Yesu adayankha, Ndi iyeyu amene Ine ndidzamsunzira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo m’mene adasunsa nthongo adayitenga nampatsa Yudase Isikariyote mwana wa Simoni.

Joh 13:27 Ndipo pambuyo pa nthongoyo, Satana adalowa mwa Iyeyu. Pamenepo Yesu adanena naye, Chimene uchita, chita msanga.

Joh 13:28 Koma padalibe m’modzi wa iwo akukhalapo adadziwa chimene adafuna, poti adatere naye.

Joh 13:29 Pakuti popeza Yudase adali nalo thumba, ena adalikuyesa kuti Yesu adanena kwa iye, gula zimene zitisowa paphwando; kapena kuti apatse kanthu kwa awumphawi;

Joh 13:30 Iye pamene adalandira nthongo, adatuluka pomwepo. Koma udali usiku.

Joh 13:31 Choncho pamene adatuluka Yesu adanena, Tsopano Mwana wa munthu alemekezedwa, ndipo Mulungu alemekezedwa mwa Iye;

Joh 13:32 Ndipo ngati Mulungu adzalemekeza Iye.Mulungu adzamlemekeza Iye mwa Iye yekha,ndipo adzalemekeza Iye tsopano apa.

Joh 13:33 Tiyana, katsala kanthawi ndi khala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndidanena kwa Ayuda, kuti kumene ndimkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.

Joh 13:34 Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mzake.

Joh 13:35 Mwa ichi anthu onse adzazindikira kuti muli wophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mzake.

Joh 13:36 Simoni Petro adanena ndi Iye,Ambuye mupita kuti? Yesu adayankha, Kumene ndipita sungathe kunditsata Ine tsopano; koma udzanditsata pambuyo pake.

Joh 13:37 Petro adanena ndi Iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano chifukwa ninji? Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu.

Joh 13:38 Yesu adayankha, Moyo wako kodi udzawutaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asadalire tambala udzandikana Ine katatu.



14

Joh 14:1 Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.

Joh 14:2 M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuwuzani inu; pakuti ndipita kukakukonzerani inu malo.

Joh 14:3 Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.

Joh 14:4 Ndipo kumene ndipita Ine, mukukudziwa, ndipo njira yake mukuyidziwa.

Joh 14:5 Tomasi adanena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene mukupita; tidziwa njira bwanji?

Joh 14:6 Yesu adanena naye, Ine ndine njira, ndi chowonadi ndi moyo. Palibe munthu abwera kwa Atate, koma mwa Ine.

Joh 14:7 Ngati mukadazindikira Ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira Iye, ndipo mwamuwona Iye.

Joh 14:8 Filipo adanena ndi Iye, Ambuye, tiwonetseni ife Atate, ndipo chitikwanira.

Joh 14:9 Yesu adanena naye, kodi ndiri ndi inu nthawi yayikulu yotere, ndipo sudandizindikira, Filipo? Iye amene wandiona Ine wawona Atate; unena iwe bwanji, Mutiwonetsere Atate?

Joh 14:10 Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mawu amene ndinena Ine kwa inu sindiyankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake.

Joh 14:11 Khulupirirani Ine, kuti Ine ndiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati sichomwecho, khulupirirani Ine chifukwa cha ntchito zomwe.

Joh 14:12 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupurira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.

Joh 14:13 Ndipo chiri chonse mukafunse m’dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.

Joh 14:14 Ngati mudzapempha kanthu m’dzina langa, ndidzachita.

Joh 14:15 Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.

Joh 14:16 Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse.

Joh 14:17 Ndiye Mzimu wa chowonadi, amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuwona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye, chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.

Joh 14:18 Sindidzakusiyani inu mukhale amasiye; ndibwera kwa inu.

Joh 14:19 Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindiwonanso Ine; koma inu mundiwona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.

Joh 14:20 Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.

Joh 14:21 Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadziwonetsa ndekha kwa iye.

Joh 14:22 Yudasi, amene sindiye Isikariyote, adanena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudziwonetsa nokha kwa ife, koma sikwa dziko lapansi?

Joh 14:23 Yesu adayankha nati kwa iye, Ngati munthu akonda Ine, adzasunga mawu anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzabwera kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.

Joh 14:24 Wosandikonda Ine sasunga mawu anga; ndipo mawu amene mumva sali mawu anga, koma a Atate wondituma Ine.

Joh 14:25 Zinthu izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu.

Joh 14:26 Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zinthu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndidanena kwa inu.

Joh 14:27 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usabvutike, kapena usachite mantha.

Joh 14:28 Mwamva kuti Ine ndidanena kwa inu, ndipita, ndipo ndibwera kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu koposa Ine.

Joh 14:29 Ndipo tsopano ndakuwuzani chisadachitike kuti pamene chitachitika mukakhulupirire.

Joh 14:30 Sindidzayankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wadziko lapansi adza; ndipo alibe gawo pa Ine;

Joh 14:31 Koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate anga adandipatsa ine lamulo, chotero ndichita.



15

Joh 15:1 Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye mlimi.

Joh 15:2 Nthambi ili yonse ya mwa Ine yosabala chipatso Iye ayichotsa; ndi ili yonse yobala chipatso,Iye ayisadza, kuti yikabale chipatso chochuluka.

Joh 15:3 Tsopano mwayeretsedwa inu chifukwa cha mawu amene ndayankhula ndi inu.

Joh 15:4 Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siyingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siyikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.

Joh 15:5 Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake; wokhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Joh 15:6 Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo anthu azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.

Joh 15:7 Ngati mukhala mwa Ine, ndi mawu anga akhala mwa inu,mudzapempha chimene chiri chonse muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.

Joh 15:8 Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala wophunzira anga.

Joh 15:9 Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalanibe m’chikondi changa.

Joh 15:10 Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake.

Joh 15:11 Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhalebe mwa inu, ndikuti chimwemwe chanu chikhale chodzadza.

Joh 15:12 Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mzake, monga ndakonda inu.

Joh 15:13 Palibe munthu ali nacho chikondi chachikulu choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Joh 15:14 Inu muli abwenzi anga, ngati muzichita ziri zonse zimene ndikulamulirani inu.

Joh 15:15 Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi, chifukwa zinthu zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.

Joh 15:16 Inu simudandisankha Ine, koma Ine ndidakusankhani inu, ndipo ndidakuyikani, kuti mukapite inu ndikubala chipatso; ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chiri chonse mukapempha Atate m’dzina langa akakupatseni inu.

Joh 15:17 Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mzake.

Joh 15:18 Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti linada Ine lisadayambe kuda inu.

Joh 15:19 Mukadakhala adziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndidakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.

Joh 15:20 Kumbukirani mawu amene Ine ndidanena kwa inu, kapolo sali wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati adandisautsa Ine, adzakusautsani inunso; ngati adasunga mawu anga, adzasunga anunso.

Joh 15:21 Koma zinthu izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa; chifukwa sadziwa wondituma Ine.

Joh 15:22 Ngati sindikadadza ndi kulankhula nawo sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chobisala pa machimo awo.

Joh 15:23 Iye wondida Ine, adanso Atate wanga.

Joh 15:24 Ngati sindikadachita pakati pa iwo ntchito zimene palibe munthu wina adazichita,iwo sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano iwo pamodzi adawowona, ndipo adandida Ine pamodzi ndi Atate wanga.

Joh 15:25 Koma kutero, kuti mawu wolembedwa m’chilamulo chawo akwaniritsidwe, kuti, Adandida Ine kopanda chifukwa.

Joh 15:26 Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa chowonadi amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.

Joh 15:27 Ndipo inunso mudzachitira umboni, chifukwa mudali ndi Ine kuyambira pachiyambi.



16

Joh 16:1 Zinthu izi ndayankhula kwa inu kuti musakhumudwitsidwe.

Joh 16:2 Adzakutulutsani m’masunagoge; koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.

Joh 16:3 Ndipo zinthu izi adzachita, chifukwa sadadziwa Atate, kapena Ine.

Joh 16:4 Koma zinthu izi ndayankhula ndi Inu kuti pamene ikudza nthawi , mukakumbukire kuti ndidakuwuzani. Koma izi sindidanena kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndidali pamodzi ndi inu.

Joh 16:5 Koma tsopano ndipita kwa Iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Mupita kuti?

Joh 16:6 Koma chifukwa ndayankhula izi ndi inu chisoni chadzadza mumtima mwanu.

Joh 16:7 Koma ndinena Ine chowonadi ndi inu; kuti kuli phindu kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzabwera kwa inu; koma ngati ndichoka ndidzamtuma Iye kwa inu.

Joh 16:8 Ndipo akadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro;

Joh 16:9 Za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine;

Joh 16:10 Za chilungamo chifukwa ndipita kwa Atate, ndipo simundiwonanso Ine;

Joh 16:11 Za chiweruzo chifukwa mfumu ya dziko lino lapansi yaweruzidwa.

Joh 16:12 Ndiri nazo zambirinso zonena kwa inu, koma simungathe kuzidziwa tsopano lino.

Joh 16:13 Koma akabwera Iyeyo, Mzimu wa chowonadi, adzakutsogolerani inu m’chowonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu ziri zones adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilimkudza adzakuwonetserani.

Joh 16:14 Iyeyo adzalemekeza Ine; chifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzawonetsa kwa inu izo.

Joh 16:15 Zinthu ziri zonse Atate ali nazo ndi zanga; chifukwa chake ndidati, kuti adzatenga za mwa Ine, nadzaziwonetsa izo kwa inu.

Joh 16:16 Katsala kanthawi, ndipo simundiwonanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiwona Ine, chifukwa ndipita kwa Atate.

Joh 16:17 Pamenepo wophunzira ake tsono adati mwa iwo wokha, Ichi chiyani chimene anena kwa ife, kanthawi ndipo simundiwona; ndipo kanthawi mudzandiwona chifukwa ndipita kwa Atate?

Joh 16:18 Chifukwa chake adanena, Ichi n’chiyani chimene anena, kanthawi? Sitidziwa chimene ayankhula.

Joh 16:19 Yesu adazindikira kuti adalikufuna kumfunsa Iye, ndipo adati kwa iwo, Kodi muli kufunsana wina ndi mzake za ichi, kuti ndidati, kanthawi ndipo simundiwona Ine, ndiponso kanthawi mudzandiwona Ine?

Joh 16:20 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.

Joh 16:21 Mkazi pamene ali mu zowawa ali ndi chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wangobala mwana, sakumbukiranso chisawutso, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu ku dziko lapansi.

Joh 16:22 Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuwonaninso, ndipo mtima wanu, udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.

Joh 16:23 Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa Ine kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa.

Joh 16:24 Kufikira tsopano simudapempha kanthu m’dzina langa, pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniritsidwe.

Joh 16:25 Zinthu izi ndiyankhula ndi inu m’miyambi; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m’miyambi, koma ndidzakuwonetsani inu momveka bwino za Atate.

Joh 16:26 Tsiku limenelo mudzapempha m’dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzapemphera inu kwa Atate;

Joh 16:27 Pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndidatuluka kwa Mulungu.

Joh 16:28 Ndidatuluka kuchokera kwa Atate, ndipo ndabwera kudziko lapansi; ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.

Joh 16:29 Wophunzira ake adanena, Onani, tsopano muyankhula zomveka, ndipo mulibe kunena miyambi.

Joh 16:30 Tsopano tidziwa kuti mudziwa zinthu zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ichi tikhulupirira kuti mudatuluka kuchokera kwa Mulungu.

Joh 16:31 Yesu adayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano?

Joh 16:32 Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense kuzake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine.

Joh 16:33 Zinthu izi ndayankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chisautso, koma kondwerani chifukwa; ndalilaka dziko lapansi Ine.



17

Joh 17:1 Mawu awa adayankhula Yesu; ndipo adakweza maso ake kumwamba, ndipo adati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;

Joh 17:2 Monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi liri lonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.

Joh 17:3 Ndipo moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Khristu, amene Inu mudamtuma.

Joh 17:4 Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m’mene ndidatsiriza ntchito imene mudandipatsa kuti ndichite.

Joh 17:5 Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndidali nawo ndi Inu lisadakhale dziko lapansi.

Joh 17:6 Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m’dziko lapansi; adali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mawu anu.

Joh 17:7 Azindikira tsopano kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine ndi zanu;

Joh 17:8 Pakuti ndawapatsa iwo mawu amene mudandipatsa Ine; ndipo adalandira, nazindikira kowona kuti ndidatuluka kwa Inu, ndipo adakhulupirira kuti Inu mudandituma Ine.

Joh 17:9 Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine pakuti iwo alia nu.

Joh 17:10 Ndipo zanga zonse ziri zanu, ndi zanu ziri zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo.

Joh 17:11 Sindikhalanso m’dziko lapansi, koma iwo ali m’dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m’dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale m’modzi, monga ife.

Joh 17:12 Pamene ndidakhala nawo, Ine m`dziko la pansi ndidalikuwasunga iwo m’dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndidawasunga, ndipo sadatayika m’modzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniritsidwe.

Joh 17:13 Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo zinthu izi ndiyankhula m’dziko lapansi; kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo wokha.

Joh 17:14 Ine ndawapatsa iwo mawu anu; ndipo dziko lapansi, linadana nawo, chifukwa sali adziko lapansi, monga Ine sindiri wadziko lapansi.

Joh 17:15 Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woyipayo.

Joh 17:16 Pakuti siali a dziko lapansi monga Ine sindiri wadziko lapansi.

Joh 17:17 Patulani iwo m’chowonadi; mawu anu ndi chowonadi.

Joh 17:18 Monga momwe mwandituma Ine kudziko lapansi Inenso ndituma iwo kudziko lapansi.

Joh 17:19 Ndipo chifukwa cha iwo, Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale wopatulidwa m’chowonadi.

Joh 17:20 Koma sindipempherera iwo wokha, komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mawu awo;

Joh 17:21 Kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa ife; kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu mudandituma Ine.

Joh 17:22 Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale m`modzi, monga ife tiri m’modzi.

Joh 17:23 Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa m’modzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu mudandituma Ine, nimudawakonda iwo, monga momwe mudakonda Ine.

Joh 17:24 Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndiri Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang’anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti mudandikonda Ine lisadakhazikike dziko lapansi.

Joh 17:25 Atate wolungama, dziko lapansi silidadziwa Inu, koma Ine ndidadziwa Inu; ndipo awa azindikira kuti Inu mudandituma Ine;

Joh 17:26 Ndipo ndidazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene mudandikonda nacho Ine chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.



18

Joh 18:1 Pamene Yesu adanena mawu awa, adatuluka ndi wophunzira ake, kupita tsidya lija la mtsinje wa Kedroni, kumene kudali munda, umene adalowamo Iye ndi wophunzira ake.

Joh 18:2 Ndipo Yudase amene adampereka Iye, adadziwa malowa; chifukwa Yesu ankapitako kawirikawiri ndi wophunzira ake.

Joh 18:3 Pamenepo Yudase, m’mene adalandira gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe akulu ndi Afarisi, adafika komweko ndi nyali ndi miwuni ndi zida.

Joh 18:4 Pamenepo Yesu, podziwa zinthu zonse ziri nkudza pa Iye, adatuluka nati kwa iwo, Mufuna yani?

Joh 18:5 Iwo adamyankha Iye, Yesu Mnazarete. Yesu adanena nawo, Ndine. Ndipo Yudase yemwe wompereka Iye, adayima nawo pamodzi.

Joh 18:6 Ndipo nthawi yomweyo adanena ndi iwo, Ndine, adabwerera m’mbuyo, nagwa pansi.

Joh 18:7 Pamenepo adawafunsanso, Mufuna yani? Ndipo iwo adati, Yesu Mnazarete.

Joh 18:8 Yesu adayankha, Ndati Ndine, chifukwa chake ngati mufuna Ine, lekani awa apite;

Joh 18:9 Kuti akwaniritsidwe mawu amene adayankhula kuti, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindidataya ndi m’modzi.

Joh 18:10 Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, adalisolola nakantha kapolo wa mkulu wa nsembe, namdula khutu lake lamanja. Dzina la kapoloyo lidali Malikasi.

Joh 18:11 Pamenepo Yesu adati kwa Petro, Longa lupanga m’chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindiyenera kumwera ichi kodi?

Joh 18:12 Ndipo gululo ndi kapitawo ndi asilikari a Ayuda adagwira Yesu nam’manga Iye;

Joh 18:13 Nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti adali mpongozi wa Kayafa, amene adali mkulu wa ansembe chaka chomwecho.

Joh 18:14 Tsopano Kayafa ndiye uja adalangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu m’modzi afere anthu.

Joh 18:15 Ndipo Simoni Petro ndi wophunzira wina adatsatira Yesu, koma wophunzira ameneyo adali wodziwika kwa mkulu wa nsembe, nalowa pamodzi ndi Yesu m’bwalo la mkulu wa ansembe;

Joh 18:16 Koma Petro adayima pakhomo kunja, chifukwa chake wophunzira winayo amene adadziwika kwa akulu a nsembe, adatuluka nayankhula ndi wapakhomo nalowetsa Petro.

Joh 18:17 Pamenepo buthu lapakhomolo lidanena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa wophunzira a munthu uyu? Iyeyu adanena, Sindine.

Joh 18:18 Koma atumiki ndi asilikari adalikuyimirirako ; adasonkha moto wamakala; pakuti kudali kuzizila; ndipo adalikuwotha moto; koma Petronso adali nawo alikuyimilira ndi kuwotha moto.

Joh 18:19 Ndipo mkulu wa ansembe adafunsa Yesu za wophunzira ake, ndi chiphunzitso chake.

Joh 18:20 Yesu adayankha iye, Ine ndayankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndidaphunzitsa Ine nthawi zonse m’sunagoge ndi m’kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindidayankhula kanthu.

Joh 18:21 Undifunsiranji Ine? Funsa iwo amene adamva chimene ndidayankhula nawo, tawona, amenewo adziwa chimene ndidanena Ine.

Joh 18:22 Koma m’mene Iye adanena izi, m’modzi wa asilikari akuyimilirako adapanda Yesu khofi, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa nsembe chomwecho?

Joh 18:23 Yesu adayankha iye, Ngati ndayankhula choyipa, chitira umboni wa choyipacho, koma ngati bwino, undipandiranji?

Joh 18:24 Tsopano Anasi adamtumiza Iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa nsembe.

Joh 18:25 Ndipo Simoni Petro adalikuyimilira ndi kuwotha moto. Pomwepo adati kwa iye, Suli iwenso wa wophunzira ake kodi? Iyeyu adakana nati, Sindine.

Joh 18:26 M’modzi wa atumiki a mkulu wansembe ndiye m’bale wake wa uja amene Petro adamdula khutu, adanena, Ine sindidakuwona iwe kodi m’munda pamodzi ndi iye?

Joh 18:27 Pamenepo Petro adakananso; ndipo pomwepo adalira tambala.

Joh 18:28 Pamenepo adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku nyumba ya chiweruzo; koma kudali mamawa; ndipo iwo sadalowa ku nyumba ya chiweruzo, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paskha.

Joh 18:29 Ndipo Pilato adatulukira kunja kwa iwo, nati, chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu?

Joh 18:30 Iwo adayankha nati kwa iye, Akadakhala wosachita zoyipa uyu sitikadampereka Iye kwa inu.

Joh 18:31 Ndipo Pilato adati kwa iwo, Mutengeni Iye inu, ndi kumuweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda adati kwa iye, Tiribe ulamuliro wakupha munthu aliyense.

Joh 18:32 Kuti mawu a Yesu akwaniritsidwe, amene adanena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo.

Joh 18:33 Chifukwa chake Pilato adalowanso m’nyumba ya chiweruzo, nayitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda kodi?

Joh 18:34 Yesu adayankha, Kodi munena ichi mwa inu nokha kapena ena adakuwuzani za Ine?

Joh 18:35 Pilato adayankha, Ndiri Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe akulu adakupereka kwa ine; wachita chiyani?

Joh 18:36 Yesu adayankha, Ufumu wanga suli wapadziko lino lapansi; Ufumu wanga ukadakhala wa dziko lapansi, atumiki anga akadamenya nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera komkuno.

Joh 18:37 Pomwepo Pilato adati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu adayankha, munena kuti ndine Mfumu. Ndidabadwira ichi Ine, ndipo ndidadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni za chowonadi. Yense wakukhala mwa chowonadi amva mawu anga.

Joh 18:38 Pilato adanena kwa Iye, chowonadi ndi chiyani? Ndipo pamene adanena ichi, adatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nawo, Ine sindikupeza chifukwa chiri chonse mwa Iye.

Joh 18:39 Koma muli nawo machitidwe akuti ndimamasulira inu m’modzi pa Paskha; Kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu Mfumu ya Ayuda?

Joh 18:40 Pomwepo iwo adafuwulanso, nanena, Si munthu uyu, koma Baraba. Koma Baraba adali wachifwamba.



19

Joh 19:1 Pamenepo tsono Pilato adamtenga Yesu, namkwapula.

Joh 19:2 Ndipo asilikali adaluka chisoti chaminga nabveka pa mutu pake, namfunda Iye mwinjiro wa papu;

Joh 19:3 Nadza kwa Iye, nati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda! Ndipo adampanda Iye khofi ndi manja awo.

Joh 19:4 Ndipo Pilato adatulukanso kunja, nanena nawo, Tawonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chiri chonse.

Joh 19:5 Pamenepo Yesu adatuluka kunja, atabvala chisoti cha minga, ndi mwinjiro wa papu. Ndipo Pilato adanena nawo, Tawonani munthuyu!

Joh 19:6 Ndipo pamene ansembe akulu ndi asilikari adamuwona Iye, adafuwula nanena, Mpachikeni, Iye, mpachikeni Iye. Pilato adanena nawo, Mtengeni inu Iye, nimumpachike; pakuti ine sindikupeza chifukwa mwa Iye.

Joh 19:7 Ayuda adayankha iye, Tiri nacho chilamulo ife, ndipo monga mwachilamulocho ayenera kufa, chifukwa adadziyesera yekha Mwana wa Mulungu.

Joh 19:8 Ndipo pamene Pilato adamva mawu awa, adachita mantha kwambiri.

Joh 19:9 Ndipo adalowanso ku nyumba ya chiweruzo, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sadamyankha kanthu.

Joh 19:10 Ndipo Pilato adanena kwa Iye, Simulankhula kwa ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndiri nawo wakukumasulani, ndipo ndiri nawo ulamuliro wakukupachikani?

Joh 19:11 Yesu adamyankha iye, Simukadakhala nawo ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa Kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo lalikulu.

Joh 19:12 Kuchokera pa ichi Pilato adafuna kum’masula Iye; koma Ayuda adafuwula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara.

Joh 19:13 Pamene Pilato adamva kunena kotero, adatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira; kumalo amene amatchedwa bealo la miyala, koma m’chihebri, Gabata.

Joh 19:14 Ndipo lidali tsiku lokonzekera Paskha; padali monga ola lachisanu ndi chimodzi. Ndipo adanena kwa Ayuda, Tawonani, mfumu yanu!

Joh 19:15 Pamenepo adafuwula iwowa, Chotsani, chotsani, mpachikeni Iye! Pilato adanena nawo, Ndipachike Mfumu yanu kodi? Ansembe akulu adayankha, tiribe mfumu koma Kayisala.

Joh 19:16 Ndipo pamenepo adampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Ndipo adamtenga Yesu, namutsogoza m’njira.

Joh 19:17 Ndipo Iye adasenza mtanda wake, natuluka kupita ku malo wotchedwa Malo a Chigaza, amene atchedwa m’Chihebri, Gologota;

Joh 19:18 Kumene adampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, mbali yina ndi yina, koma Yesu pakati.

Joh 19:19 Ndipo Pilato adalemba dzina naliyika pamtanda. Ndipo padalembedwa kuti YESU MNAZARETE, MFUMU YA AYUDA.

Joh 19:20 Ndipo lembo ilo adaliwerenga ambiri wa Ayuda; chifukwa malo amene Yesu adapachikidwapo adali pafupi pa mzindawo; ndipo lidalembedwa m’Chihebri, m’Chigriki, ndi m’Chilatini.

Joh 19:21 Pamenepo ansembe akulu a Ayuda, adanena kwa Pilato, Musalembe Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu adati, Ndiri Mfumu ya Ayuda.

Joh 19:22 Pilato adayankha, Chimene ndalemba, ndalemba.

Joh 19:23 Pamenepo asilikali, atampachika Yesu, adatenga zobvala zake nazigawa panayi, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malayawo adawombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, adalibe msoko.

Joh 19:24 Iwo adati wina kwa mzake, Tisang’ambe awa, koma tichite mayere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniritsidwe limene linena, Adagawana zobvala zanga mwa iwo wokha, ndi pa malaya anga adachitira mayere. Ndipo asilikari adachita izi.

Joh 19:25 Koma pa mtanda wa Yesu adayimilira amake ndi m’bale wa amake, Mariya, mkazi wa Klewopa, ndi Mariya wa Magadala.

Joh 19:26 Pamenepo Yesu pakuwona amake ndi wophunzira amene adamkonda, alikuyimilirako, adanena kwa amake, Mayi, wonani, mwana wanu!

Joh 19:27 Pamene adanena kwa wophunzirayo, Tawona, amayi ako! Ndipo kuyambira ola lomweli wophunzirayo adapita nawo kwawo.

Joh 19:28 Chitapita ichi, Yesu podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniritsidwe, adanena, Ndimva ludzu.

Joh 19:29 Tsopano adatenga chotengera chodzala ndi vinyo wosasa ndipo adazenenga chinkhupule chodzadza ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake.

Joh 19:30 Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo adati, kwatha; ndipo adaweramitsa mutu wake napereka mzimu.

Joh 19:31 Pomwepo Ayuda popeza padali tsiku lokonzekera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la sabata, pakuti tsiku lomwelo la sabata lidali lalikulu, adapempha Pilato kuti miyendo yawo ithyoledwe, ndipo achotsedwe.

Joh 19:32 Ndipo adabwera asilikari nathyola miyendo ya woyambayo, ndi winayo wopachikidwa pamodzi ndi Iye;

Joh 19:33 Koma pofika kwa Yesu, m’mene adamuwona Iye, kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake;

Joh 19:34 Koma m’modzi wa asilikali adamgwaza ndi nthungo m’nthiti yake, ndipo padatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.

Joh 19:35 Ndipo iye amene adawona, wachita umboni, ndi umboni wake uli wowona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zowona, kuti inunso mukakhulupirire.

Joh 19:36 Pakuti izi zidachitika kuti lembo likwaniritsidwe, fupa la Iye silidzathyoledwa.

Joh 19:37 Ndipo linenanso lembo lina, Adzayang’ana pa Iye amene adampyoza.

Joh 19:38 Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimateya, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuwopa Ayuda, adapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato adalola. Chifukwa chake adadza, nachotsa mtembo wake.

Joh 19:39 Koma adadzanso Nikodemo, amene adabwera kwa iye usiku poyamba paja, adatenga chisanganizo cha mule ndi aloye, monga miyeso zana

Joh 19:40 Pamenepo adatenga mtenbo wa Yesu, nawukulunga ndi nsalu za bafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa mayikidwe a maliro a Ayuda.

Joh 19:41 Tsopano pamene Iye adapachikidwapo padali munda; ndi m’mundamo mudali manda atsopano m’mene sadayikidwamo munthu aliyense nthawi zonse.

Joh 19:42 Pomwepo ndipo adayika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzekera la Ayuda, pakuti mandawo adali pafupi.



20

Joh 20:1 Tsiku loyamba la sabata adadza Mariya wa Magadalena m’mamawa, kusadayambe kucha pamanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.

Joh 20:2 Pomwepo adathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu adamkonda, nanena nawo. Adamchotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene adamuyika Iye.

Joh 20:3 Choncho Petro adapita ndi wophunzira winayo, nafika kumanda.

Joh 20:4 Choncho adathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo adathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;

Joh 20:5 Ndipo m’mene adawerama chosuzumira adawona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sadalowamo;

Joh 20:6 Pamenepo adadzanso Simoni Petro alinkutsata iye, nalowa m’manda; ndipo adawona nsalu zabafuta zitakhala.

Joh 20:7 Ndipo kansalu kamene kadali pamutu pake, kosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma kopindika padera pamalo pena.

Joh 20:8 Pamenepo tsono adalowanso wophunzira winayo, amene adayamba kufika kumanda, ndipo adawona, nakhulupirira.

Joh 20:9 Pakuti kufikira pomwepo sadadziwa malembo akuti ayenera Iye kuwuka kwa akufa.

Joh 20:10 Pamenepo wophunzirawo adachokanso, kupita kwawo.

Joh 20:11 Koma Mariya adalikuyimilira kumanda kuja, alikulira. Ndipo m’mene adali kulira adawerama nasuzumira m’manda;

Joh 20:12 Ndipo adawona angelo awiri atabvala zoyera alikukhala m’modzi kumutu, ndi wina kumiyendo, pamene mtembo wa Yesu udagona.

Joh 20:13 Ndipo iwowa adanena kwa iye, Mkazi, uliranji? Adanena nawo, chifukwa adachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene adamuyika Iye.

Joh 20:14 Ndipo m’mene adanena izi, adachewuka m’mbuyo, nawona Yesu ali chiliri, ndipo sadadziwa kuti ndiye Yesu.

Joh 20:15 Yesu adanena naye, Mkazi, Uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumanda adanena ndi Iye, Mbuye ngati mwamunyamula Iye, ndiwuzeni kumene mwamuyika Iye, ndipo ndidzamchotsa.

Joh 20:16 Yesu adanena naye, Mariya. Iyeyu m’mene adacheuka, adanena ndi Iye m’Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi.

Joh 20:17 Yesu adanena naye, Usandikhudza, pakuti sindidathe kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, ndikwera kupita kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.

Joh 20:18 Mariya Magadalene adapita, nawuza wophunzirawo, kuti, Ndawona Ambuye; ndi kuti adanena zinthu izi kwa iye.

Joh 20:19 Pamenepo pokhala madzulo, tsiku lomwelo loyamba la sabata, makomo ali hitsekere, kumene adakhala wophunzira, chifukwa cha kuwopa Ayuda, Yesu adadza nayimilira pakati pawo, nanena nawo, Mtendere ukhale ndi inu.

Joh 20:20 Ndipo pamene adanena ichi, adawonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo wophunzira adakondwera pakuwona Ambuye.

Joh 20:21 Chifukwa chake Yesu adatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.

Joh 20:22 Ndipo pamene adanena ichi, adawapumira, nanena nawo, Landirani Mzimu Woyera.

Joh 20:23 Zochimwa za aliyense muzikhululukira, zidzakhululukidwa kwa iwo; ndipo za aliyense muzigwiritsa, zidzagwiridwa.

Joh 20:24 Koma Tomasi, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sadakhala nawo pamodzi, pamene Yesu adadza.

Joh 20:25 Choncho wophunzira ena adanena naye, Tamuwona Ambuye. Koma iye adati kwa iwo, Ndikapanda kuwona m’manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuyika chala changa m’chizindikiro cha misomaliyo, kuyika dzanja langa ku nthiti yake; sindidzakhulupirira.

Joh 20:26 Ndipo patapita masiku asanu ndi atatu, wophunzira ake adalinso m’nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nawo. Yesu adadza, makomo ali chitsekere, nayimilira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.

Joh 20:27 Pomwepo adanena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuwone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliyike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira.

Joh 20:28 Tomasi adayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.

Joh 20:29 Yesu adanena kwa iye, Chifukwa wandiwona Ine, wakhulupirira; Wodala iwo akukhulupirira angakhale sadawona

Joh 20:30 Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu adazichita pamaso pa wophunzira ake zimene sizidalembedwa m’buku ili.

Joh 20:31 Koma zidalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nawo moyo kupyolera m’dzina lake.



21

Joh 21:1 Zitapita izi Yesu adadziwonetseranso kwa wophunzira ake ku nyanja ya Tiberiya. Koma adadziwonetsera mwini yekha chotere.

Joh 21:2 Adali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanayeli wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedayo, ndi awiri ena a wophunzira ake.

Joh 21:3 Simoni Petro adanena nawo, ndinka kukasodza. Adanena naye, ifenso tipita nawe. Adatuluka, nalowa m’chombo; ndipo mu usiku uja sadagwira kanthu.

Joh 21:4 Koma pakuyamba kucha, Yesu adayimilira pambali pa nyanja, komatu wophunzira sadadziwa kuti ndiye Yesu.

Joh 21:5 Yesu adanena nawo, Ananu muli nako kanthu kakudya kodi? Adamyankha Iye, Ayi.

Joh 21:6 Ndipo Iye adati kwa iwo, ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja la chombo, ndipo mudzapeza. Pamenepo adaponya, ndipo adalibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba.

Joh 21:7 Pamenepo wophunzira uja amene Yesu adamkonda adanena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, adadzibveka malaya a pathupi, pakuti adali wamaliseche, nadziponya yekha m’nyanja.

Joh 21:8 Ndipo wophunzira ena adabwera m’chombo, pakuti sadali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo.

Joh 21:9 Ndipo pamene adatulukira pamtunda, adapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate.

Joh 21:10 Yesu adanena nawo, Bweretsani nsomba zimene mwazigwira tsopano.

Joh 21:11 Simoni Petro adakwera m’chombo nakokera khoka kumtunda lodzala ndi nsomba zazikulu; zana limodzi, ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zidachuluka kotere; khoka silidang’ambika.

Joh 21:12 Yesu adanena nawo, Idzani mudye. Koma palibe m’modzi wa wophunzira adatha kumfunsa Iye, ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye.

Joh 21:13 Yesu adadza natenga mkate napatsa iwo, momwemonso nsomba.

Joh 21:14 Imeneyo ndi nthawi yachitatu yakudziwonetsera Yesu kwa wophunzira ake m’mene adauka kwa akufa.

Joh 21:15 Pamene adadya adanena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Adanena ndi Iye, Inde Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Adanena naye, Dyetsa ana a nkhosa zanga.

Joh 21:16 Adanena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Adanena ndi Iye, Inde,Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Adanena naye, dyetsa nkhosa zanga.

Joh 21:17 Adanena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro adamva chisoni kuti adati kwa Iye kachitatu, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu adanena naye, Dyetsa nkhosa zanga.

Joh 21:18 Indetu , indetu ndinena ndi iwe, pamene udali m’nyamata udadzimangira wekha m’chiuno lamba, ndipo udayenda kumene udafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina nadzakunyamula kumene sufuna.

Joh 21:19 Koma ichi adanena ndikuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m’mene adanena ichi, adati kwa iye, Nditsate Ine.

Joh 21:20 Petro m’mene adachewuka, adapenya wophunzira amene Yesu adamkonda alikutsata, amenenso adatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, Ndani iye wakupereka Inu?

Joh 21:21 Pamenepo Petro pakumuwona, adanena kwa Yesu, Ambuye, zidzakhala bwanji ndi munthu uyu?

Joh 21:22 Yesu adanena naye, ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe? Nditsate Ine.

Joh 21:23 Chifukwa chake mawu awa adatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa; koma Yesu sadanena kwa iye kuti sadzafa. Koma ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe?

Joh 21:24 Yemweyu ndiye wophunzira wakuchita umboni wa zinthu izi, ndipo adalemba zinthu izi, ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi wowona.

Joh 21:25 Koma palinso zina zambiri zimene Yesu adazichita, zoti zikadalembedwa zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nawo malo a mabuku amene akadalembedwa. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE