Titus


1

Tit 1:1 Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha wosankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha chowonadi chiri monga mwa chipembedzo. [Tit 1:2 M’chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, adalonjeza lisadakhale dziko lapansi; [Tit 1:3 Koma panyengo za Iye yekha adawonetsa mawu ake mu ulalikiro, umene adandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu; [Tit 1:4 Kwa Tito mwana wanga weni weni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse; chisomo, chifundo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu Mpulumutsi wathu. [Tit 1:5 Chifukwa cha ichi ndidakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukayike akulu m’mizinda yonse, monga ndidakulamulira: [Tit 1:6 Ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wamkazi m’modzi, wokhala nawo ana wokhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mawu. [Tit 1:7 Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliwuma, wosapsa mtima msanga, wosamwetsa vinyo, wosati wa chiwawa, wopanda ndewu, wosati wa chisiliro chonyansa. [Tit 1:8 Komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda anthu abwino, wosaledzera wolungama, woyera mtima, wodziletsa; [Tit 1:9 Wogwira mawu wokhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m’chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa wotsutsana naye. [Tit 1:10 Pakuti alipo ambiri wosamvera mawu, woyankhula zopanda pake, ndi wonyenga maka maka iwo a kumdulidwe: [Tit 1:11 Amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiliro chonyansa. [Tit 1:12 Wina wa mwa iwo, ndiye m’neneri wa iwo wokha, adati, Akrete ndiwo abodza masiku onse, zirombo zoyipa, aulesi ndi adyera. [Tit 1:13 Umboni uwu uli wowona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale wolama m’chikhulupiriro. [Tit 1:14 Osasamala nthano zachabe za chiyuda, ndi malamulo wa anthu wopatuka kusiyana nacho chowonadi. [Tit 1:15 Kwa oyera mtima zonse ndi zoyera: koma mwa iwo wodetsedwa ndi wosakhulupira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zawo ndi chikumbumtima chawo. [Tit 1:16 Abvomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana Iye, popeza ali wonyansitsa, ndi wosamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino wosatsimikizidwa. [ [

2

Tit 2:1 Koma iwe, yankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa: [Tit 2:2 Wokalamba akhale wodzisunga, wolemekezeka, wodziletsa, wolama m’chikhulupiriro, m’chikondi, m’chipiliro. [Tit 2:3 Momwemonso akazi wokalamba akhale nawo makhalidwe woyenera anthu woyera, wosasinjirira,wosamwetsa vinyo, akuphunzitsa zinthu zokoma. [Tit 2:4 Kuti akalangize akazi ang’ono kuti akhale wodziletsa akonde amuna awo, akonde ana awo,anzeru wosati achiwerewere. [Tit 2:5 Akhale wosunga nyumba abwino, akumvera amuna a iwo okha, kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano. [Tit 2:6 Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale wodziletsa. [Tit 2:7 Mzinthu zonse udziwonetsere wekha chitsanzo cha ntchito za bwino; m`chiphunzitso chako uwonetsere chosabvunda, ulemekezeko, ndi ulemu. [Tit 2:8 Mawu olama, wosatsutsika; kuti iye wakutsutsana nawe achite manyazi, posakhala nako kanthu koyipa kunenera inu. [Tit 2:9 Uwalimbikitse akapolo amvere ambuye wawo wa iwo wokha, nawakondweretse m`zinthu zonse; wosawiringula mawu awo; [Tit 2:10 Akhale wosaba, koma awonetsere kukhulupirika konse kwa bwino: kuti akakometsere chiphunzitso cha Mulungu Mpulumutsi wathu mzinthu zonse. [Tit 2:11 Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chibweretsa chipulumutso chawonekera kwa anthu onse, [Tit 2:12 Ndikutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo mdziko lino wodziletsa, ndi wolungama, ndi wopembedza; [Tit 2:13 Akulindirira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Khristu Yesu: [Tit 2:14 Amene anadzipereka yekha m`malo mwa ife, kuti akatiwombole ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake apaderadera achangu pa ntchito zabwino. [Tit 2:15 Izi yankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse iwe. [ [

3

Tit 3:1 Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro awamvere woweruza ndi kukhala okonzeka ku ntchito iliyonse yabwino, [Tit 3:2 Asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale odekha, nawonetsere chifatso chonse pa anthu onse. [Tit 3:3 Pakuti kale ifenso tidali opusa, osamvera, wonyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu mitundu, wokhala m`dumbo, ndi njiru, wodanidwa, wodana wina ndi mzake. [Tit 3:4 Koma zitapita izo kukoma mtima, ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chidawonekera kwa anthu. [Tit 3:5 Zosati zochokera m`ntchito za m`chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake adatipulumutsa ife, mwakutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe atsopano a Mzimu Woyera: [Tit 3:6 Amene adatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu: [Tit 3:7 Kuti poyesedwa wolungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe wolowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha. [Tit 3:8 Wokhulupirika mawuwa, ndipo za izi ndifuna ulimbitse mawu kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri antchito za bwino. Izi ndi zokoma ndi zopindulitsa anthu. [Tit 3:9 Koma pewa mafunso opusa ndi mawerengedwe amibado ndi ndewu, ndi makani apamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe. [Tit 3:10 Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamchenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize; [Tit 3:11 Podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha. [Tit 3:12 Pamene ndituma Artema kwa iwe, kapena Tukiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako kumeneko nyengo yozizira. [Tit 3:13 Bweretsani Zena woyimirirra milandu ndi Apolo mwachangu. Akonzereni za ulendo, kuti asasowe kanthu. [Tit 3:14 Ndipo anthu athu aphunzirenso kusunga ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale wosabala zipatso. [Tit 3:15 Akupatsani moni iwo wonse ali ndi ine. Apatseni moni wotikondawo m`chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE