Romans


1

Rom 1:1 Paulo mtumiki wa Yesu Khristu woyitanidwa kukhala mtumwi, wopatulidwa ku Uthenga Wabwino wa Mulungu.

Rom 1:2 (Umene Iye adalonjeza kale ndi mawu a aneneri ake m’malembo woyera)

Rom 1:3 Wakunena za Mwana wake Yesu Khristu Ambuye wathu, amene adabadwa ku mbewu ya Davide, monga mwa thupi;

Rom 1:4 Ndipo adatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndi Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, mwa kuwuka kwa akufa;

Rom 1:5 Mwa amene ife tidalandira naye chisomo ndi utumwi kukamvera chikhulupiriro pakati pa mitundu yonse chifukwa cha dzina lake ;

Rom 1:6 Mwa amenewo muli inunso, woyitanidwa a Yesu Khristu.

Rom 1:7 Kwa onse a ku Roma, wokondedwa a Mulungu, Woyitanidwa kuti akhale woyera mtima; chisomo chikhale ndi inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Rom 1:8 Poyamba ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka pa dziko lonse lapansi.

Rom 1:9 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga mu Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu, masiku onse m’mapemphero anga;

Rom 1:10 Kupempha kwanga ngati m’kutheka tsopano kapena mtsogolo mwa chifuniro cha Mulungu, ndikhale ndi ulendo wabwino, wakudza kwa inu.

Rom 1:11 Pakuti ndilakalaka kuwonana ndi inu, kuti ndikagawire kwa inu mphatso zina za uzimu, kuti inu mukhale okhazikika.

Rom 1:12 Ndiko kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa.

Rom 1:13 Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mukhale wosadziwa, kuti kawiri kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikawone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu yina.

Rom 1:14 Ine ndine wangongole kwa Ahelene ndi kwa akunja, kwa anzeru ndi wopanda nzeru.

Rom 1:15 Kotero, momwe ndingakhozere mwa ine, ndirikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma.

Rom 1:16 Pakuti sindichita manyazi ndi Uthenga wa Khristu; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wokhulupirira; kuyambira kwa Myuda, ndiponso Mhelene.

Rom 1:17 Pakuti m’menemo chawonetsedwa chilungamo cha Mulungu chobvumbulutsidwa kuchokera kuchikhulupiriro kupita kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.

Rom 1:18 Pakuti mkwiyo wa Muulngu, wochokera Kumwamba, wabvumbulutsidwa pa chisapembedzo chonse chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi chowonadi m’chosalungama chawo;

Rom 1:19 Chifukwa chodziwika cha Mulungu chawonekera m’kati mwawo; pakuti Mulungu adachiwonetsera kwa iwo.

Rom 1:20 Pakuti chilengedwere dziko lapansi zawoneka bwino zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi Umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhala opanda mawu akuwiringula;

Rom 1:21 Chifukwa kuti, ngakhale adadziwa Mulungu, sadamchitira ulemu woyenera Mulungu, ndipo sadamuyamika; koma adakhala wopanda pake m’maganizo awo, ndipo unada mtima wawo wopulukira.

Rom 1:22 Pobvomereza eni wokha kuti ali anzeru iwo adakhala wopusa.

Rom 1:23 Ndipo adasandutsa ulemerero wa Mulungu wosawonongeka, nawufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu wowonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zinthu zokwawa.

Rom 1:24 Chifukwa chake Mulungu adawapereka iwo m’zilakolako za mitima yawo, kuzonyansa, kuchititsana matupi awo wina ndi mzake zamanyazi.

Rom 1:25 Amene adasandutsa chowonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wodalitsika nthawi yosatha. Amen.

Rom 1:26 Chifukwa cha ichi Mulungu adawapereka iwo kuzilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi awo adasandutsa machitidwe awo achilengedwe akakhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe.

Rom 1:27 Ndipo chimodzimodzinso amuna adasiya machitidwe a chilengedwe cha akazi, natenthetsana ndi chilakolako chawo wina ndi mzake, amuna wokhawokha adachitirana chamanyazi, ndipo adalandira mwa iwo wokha mphotho yoyenera kulakwa kwawo.

Rom 1:28 Ndipo monga iwo adakana kukhala naye Mulungu m’chidziwitso chawo, adawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;

Rom 1:29 Wodzadzidwa ndi zosalungama zonse, chiwerewere kuyipa, kusilira, dumbo; wodzala ndi kaduka, kupha, ndewu, chinyengo, udani, miseche;

Rom 1:30 Akazitape, wosinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, wodzitama, amatukutuku, woyamba zoyipa, wosamvera akuwabala awo,

Rom 1:31 Wopanda nzeru, wosasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, wosayanjanitsika, wopanda chifundo;

Rom 1:32 Amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zinthu zotere ayenera imfa, azichita iwo wokha, ndiponso abvomerezana ndi iwo akuzichita.



2

Rom 2:1 Chifukwa chake ali wopanda mawu wowilingula munthu iwe, amene uli yense woweruza; pakuti m’mene uweruza wina:-momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zinthu zomwezo.

Rom 2:2 Koma tidziwa kuti chiweruzo cha Mulungu chili chowona kwa iwo amene akuchita motsutsana ndi zinthu zotere.

Rom 2:3 Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zinthu zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa chiweruzo cha Mulungu?

Rom 2:4 Kapena upeputsa kodi chuma cha ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukutsogolera kuti ulape?

Rom 2:5 Koma kolingana ndi kuwuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziwunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kubvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;

Rom 2:6 Amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake.

Rom 2:7 Kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisawonongeko, mwa kupilira pa ntchito zabwino; adzabwezera moyo wosatha:

Rom 2:8 Koma kwa iwo andewu, ndi wosamvera chowonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi ukali,

Rom 2:9 Chisautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoyipa, kwa Myuda, komanso Mhelene.

Rom 2:10 Koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira kwa Myuda, ndiponso Mhelene;

Rom 2:11 Pakuti Mulungu alibe tsankhu.

Rom 2:12 Pakuti onse amene adachimwa opanda lamulo adzawonongeka wopanda lamulo; ndi onse amene adachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo;

Rom 2:13 Pakuti womvera lamulo sakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzalungamitsidwa.

Rom 2:14 Pakuti pamene anthu amitundu akhala opanda lamulo amachita mwa iwo wokha zalamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira wokha ngati lamulo;

Rom 2:15 Popeza iwo awonetsa ntchito yalamulo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mzake anenezana kapena akanirana;

Rom 2:16 Tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Yesu Khristu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga wabwino.

Rom 2:17 Tawona iwe wakudzitcha wekha Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu,

Rom 2:18 Nudziwa chifuniro chake, nubvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m’chilamulo,

Rom 2:19 Nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima.

Rom 2:20 Mlangizi wa wopanda nzeru, mphunzitsi wa tiwana, wakukhala nacho chidziwitso ndi chowonadi cha m`chilamulo..

Rom 2:21 Iwe tsono wophunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wolalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha?

Rom 2:22 Iwe wonena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wodana nawo mafano, umafunkha za m’kachisi kodi?

Rom 2:23 Iwe wodzitamandira pa chilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m’chilamulo?

Rom 2:24 Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga kwalembedwa.

Rom 2:25 Inde pakuti mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa.

Rom 2:26 Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoyikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe?

Rom 2:27 Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi uweruza iwe, amene mwa malembo ndi mdulidwe womwe, ulakwira lamulo?

Rom 2:28 Pakuti sali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupi:

Rom 2:29 Koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mu mzimu, si m’malembo ayi; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu koma kwa Mulungu.



3

Rom 3:1 Ndipo potero Myuda aposa ninji? Kapena mdulidwe upindulanji?

Rom 3:2 Zambiri monse monse; choyamba, kuti mawu a Mulungu adaperekedwa kwa iwo.

Rom 3:3 Nanga bwanji ngati ena sadakhulupirira? Kodi kusakhulupirira kwawo kupangitsa chabe chikhulupiriro cha Mulungu chopanda mphamvu?

Rom 3:4 Msatero ayi, koma Mulungu akhale wowona, ndipo anthu onse akhale wonama: monga kwalembedwa; kuti Inu mukayesedwe wolungama m’maneno anu, ndi kuti mukalakike m’mene muweruzidwa.

Rom 3:5 Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu amene afikitsa mkwiyo? (ndilankhula monga munthu).

Rom 3:6 Msatero ayi; ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wadziko lapansi?

Rom 3:7 Pakuti ngati chowonadi cha Mulungu chichulukitsa ulemerero wake chifukwa cha bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa?

Rom 3:8 Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoyipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.

Rom 3:9 Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iyayi ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Ahelene omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo;

Rom 3:10 Monga kwalembedwa, palibe m’modzi wolungama, inde palibe m’modzi;

Rom 3:11 Palibe m’modzi wakudziwitsa, palibe m’modzi wakufunafuna Mulungu;

Rom 3:12 Onsewa apatuka njira, wonsewa pamodzi akhala wopanda phindu; palibe m’modzi wochita zabwino, inde, palibe m’modzi ndithu.

Rom 3:13 M’mero mwawo muli manda apululu; Ndi lilime lawo amanyenga; ululu wa njoka uli pansi pa milomo yawo;

Rom 3:14 M’kamwa mwawo mudzala ndi zotemberera ndi zowawa;

Rom 3:15 Miyendo yawo ichita liwiro kukhetsa mwazi;

Rom 3:16 Kusakaza ndi kusawuka kuli m’njira zawo;

Rom 3:17 Ndipo njira ya mtendere sadayidziwa;

Rom 3:18 Kumuopa Mulungu kulibe pamaso pawo.

Rom 3:19 Ndipo tidziwa kuti zinthu zili zonse chizinena chilamulo zichiyankhulira iwo ali pansi pa chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi likatsutsidwe pamaso pa Mulungu.

Rom 3:20 Chifukwa chake pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo.

Rom 3:21 Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chopanda lamulo chawonetsedwa, chochitiridwa umboni ndi lamulo ndi aneneri;

Rom 3:22 Ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;

Rom 3:23 Pakuti onse adachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

Rom 3:24 Alungamitsidwa kwa ulere ndi chisomo chake, mwa chiwombolo cha mwa Khristu Yesu;

Rom 3:25 Amene Mulungu adamuyika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m’mwazi wake, kuti awonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m’kulekerera kwake adalekerera machimo wochitidwa kale lomwe;

Rom 3:26 Kuti awonetse chilungamo chake m’nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.

Rom 3:27 Pamenepo kudzitamandira kuli kuti? Kwaletsedwa ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iyayi; koma ndi lamulo lachikhulupiriro.

Rom 3:28 Chifukwa chake timalizira ndikunene kuti munthu alungamitsidwa mwa chikhulupiriro, wopada ntchito za lamulo.

Rom 3:29 Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda wokhawokha kodi? Si wawo wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso:

Rom 3:30 Powona kuti ndiye Mulungu m’modzi, amene adzawayesa amdulidwe wolungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro.

Rom 3:31 Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ayi; koma tikhazikitsa lamulo.



4

Rom 4:1 Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, adalandira chiyani?

Rom 4:2 Pakuti ngati Abrahamu adalungamitsidwa mwa ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga pamaso pa Mulungu ayi.

Rom 4:3 Pakuti lembo likuti chiyani? Ndipo Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo chidaweregedwa kwa iye chilungamo.

Rom 4:4 Ndipo kwa iye amene agwira ntchito, mphotho siyiwerengedwa ya chisomo koma ya ngongole.

Rom 4:5 Koma kwa iye amene sagwira ntchito, koma akhulupirira Iye amene ayesa wosapembedza ngati wolungama, chikhulupiriro chake chiwerengedwa chilungamo.

Rom 4:6 Monganso Davide anena za mdalitso wake wa munthu, amene Mulungu amuwerengera chilungamo chopanda ntchito,

Rom 4:7 Ndi kuti, wodala iwo amene akhululukidwa zoyipa zawo, nakwiriridwa machimo awo.

Rom 4:8 Wodala munthu amene Ambuye samuwerengera tchimo

Rom 4:9 Mdalitso umenewu tsono uli kwa wodulidwa kodi kapena kwa wosadulidwa womwe? Pakuti timati, chikhulupiriro chidawerengedwa kwa Abrahamu chilungamo.

Rom 4:10 Tsono chidawerengedwa bwanji? M’mene iye adali wodulidwa kapena wosadulidwa ? sipamene adali wodulidwa ayi, koma wosadulidwa.

Rom 4:11 Ndipo iye adalandira chizindikiro cha mdulidwe ndicho chosindikiza chilungamo cha chikhulupiriro, chomwe iye adali nacho asanadulidwe; kuti kotero iye akhala tate wa onse wokhulupirira, angakhale iwo sanadulidwa, kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso;

Rom 4:12 Ndiponso tate wa mdulidwe wa iwo amene siyali a mdulidwe wokha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe achikhulupiriro chija cha tate wathu Abrahamu, chimene iye adali nacho asanadulidwe.

Rom 4:13 Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silidapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake mwa lamulo; koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.

Rom 4:14 Pakuti ngati iwo alamulo akhala wolowa nyumba, pamenepo chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndipo lonjezo layesedwa lopanda mphamvu;

Rom 4:15 Pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo pamenepo palibe kulakwa,

Rom 4:16 Chifukwa chake chilungamo chichokera m’chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbewu zonse; si kwa iwo a chilamulo wokhawokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye tate wa ife tonse.

Rom 4:17 Monga kwalembedwa, ndidakukhazika iwe tate wa mitundu yambiri ya anthu pamanso pa Mulungu amene iye adamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndikuyitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.

Rom 4:18 Amene adakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale tate wa mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi; mbewu yako idzakhala yotere.

Rom 4:19 Ndipo iye wosafoka m’chikhulupiriro sadalabadira thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, pokhala iye ngati zaka makumi khumi, ndi mimba ya Sara imene idali yowuma.

Rom 4:20 Ndipo poyang’anira lonjezo la Mulungu sadagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma adalimbitsa m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemerero;

Rom 4:21 Nakhazikikanso mumtima kuti, chimene iye adalonjeza, adali nayonso mphamvu yakuchichita.

Rom 4:22 Chifukwa chake ichi chidawerengedwa kwa iye chilungamo.

Rom 4:23 Tsopano ichi sichidalembedwa chifukwa cha iye yekha yekha, kuti chidawerengedwa kwa iye;

Rom 4:24 Koma chifukwa cha ifenso, kwa iwo amene chidzawerengedwa ngati tikhulupirira pa Iye amene adawukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu kuchokera kwa akufa;

Rom 4:25 Amene adaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, nawukitsidwanso chifukwa cha chilungamitso chathu.



5

Rom 5:1 Chifukwa chake pokhala wolungamitsidwa mwa chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;

Rom 5:2 Amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m’chisomo ichi m’mene tilikuyimamo; ndipo tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.

Rom 5:3 Ndipo sichotero chokha, komanso tikondwera m’zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiliro:

Rom 5:4 Ndi chipiliro, chizolowezi; ndi chizolowezi, chiyembekezo;

Rom 5:5 Ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chidatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Rom 5:6 Pakuti pamene tidali chikhalire wofoka, pa nyengo yake Khristu adawafera wosapembedza.

Rom 5:7 Pakuti ndi chibvuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.

Rom 5:8 Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire wochimwa, Khristu adatifera ife.

Rom 5:9 Ndipo tsono popeza tidayesedwa wolungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka ku mkwiyo mwa Iye.

Rom 5:10 Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tidayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.

Rom 5:11 Ndipo sichotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa iye talandira tsopano chiwombolo.

Rom 5:12 Chifukwa chake monga uchimo udalowa m’dziko lapansi mwa munthu m’modzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa idafikira anthu onse; chifukwa kuti onse adachimwa.

Rom 5:13 ( Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo udali m’dziko lapansi; koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo.

Rom 5:14 Komatu imfa idachita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sadachimwe monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la Iye wakudzayo.

Rom 5:15 Koma mphatso yaulere siyilingana ndi kulakwa pakuti ngati ambiriwo adafa chifukwa cha kulakwa kwa m’modziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere yochokera ndi munthu m’modziyo Yesu Khristu, idachulukira anthu ambiri.

Rom 5:16 Ndipo mphatso siyinadza monga mwa m’modzi wochimwa, pakuti mlandu ndithu udachokera kwa munthu m’modzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere idachokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa wolungama.

Rom 5:17 Pakuti ngati, ndikulakwa kwa m’modzi, imfa idachita ufumu mwa m’modziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso yachilungamo, adzachita ufumu m’moyo mwa m’modzi, ndiye Yesu Khristu.)

Rom 5:18 Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kudafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chidafikira anthu onse.

Rom 5:19 Pakuti ndi kusamvera kwa munthu m’modzi ambiri adayesedwa wochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa m’modzi ambiri adzayesedwa wolungama.

Rom 5:20 Momwemo lamulo lidalowa, kuti kulakwa kukachuluke. Koma pamene uchimo udachuluka, pomwepo chisomo chidachuluka koposa:

Rom 5:21 Kuti, monga uchimo udachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.



6

Rom 6:1 Tidzanena chiyani tsono? Tidzakhalabe mu uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke?

Rom 6:2 Msatero ayi. Ife amene tili akufa ku uchimo tidzakhala bwanji chikhalire m’menemo?

Rom 6:3 Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tidabatizidwa mwa Khristu Yesu; tidabatizidwa mu imfa yake?

Rom 6:4 Chifukwa chake tidayikidwa m’manda pa modzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu adaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m’moyo watsopano.

Rom 6:5 Pakuti ngati ife tidakhala pamodzi ndi Iye m’chifanizo cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizo cha kuwuka kwake.

Rom 6:6 Podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale udapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likawonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo.

Rom 6:7 Pakuti iye amene adafa adamasulidwa ku uchimo.

Rom 6:8 Koma ngati ife tidafa ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye;

Rom 6:9 Podziwa kuti Khristu adawukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siyichitanso ufumu pa Iye.

Rom 6:10 Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi, ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

Rom 6:11 Chotero inunso mudziwerengere inu nokha wofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Rom 6:12 Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m’thupi lanu la imfa kumvera zilakolako zake.

Rom 6:13 Ndipo musapereke ziwalo zanu ku uchimo, zikhale zida zachosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

Rom 6:14 Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma achisomo.

Rom 6:15 Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitiri a lamulo, koma a chisomo. Msatero ayi.

Rom 6:16 Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala atumiki ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?

Rom 6:17 Koma ayamikike Mulungu, kuti ngakhale mudakhala atumiki a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja achiphunzitso chimene chidakumasulani inu.

Rom 6:18 Ndipo pamene mudamasulidwa ku uchimo, mudakhala atumiki a chilungamo.

Rom 6:19 Ndiyankhula manenedwe a anthu chifukwa cha kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu mudapereka ziwalo zanu zikhale atumiki a chonyansa ndi akusayeruzika kuti zichite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale atumiki achilungamo kuti zichite chiyeretso.

Rom 6:20 Pakuti pamene inu mudali atumiki a uchimo, mudali wosatumikira chilungamo.

Rom 6:21 Ndipo mudali nazo zabala zanji nthawi ija, m’zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano pakuti chimaliziro cha zinthu zimenezo chili imfa?

Rom 6:22 Koma tsopano, pamene mudamasulidwa ku uchimo, ndi kukhala atumiki a Mulungu, muli nacho chobala chanu, chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.

Rom 6:23 Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.



7

Rom 7:1 Nanga kodi simudziwa, abale ( pakuti ndiyankhula ndi anthu wodziwa lamulo,) kuti lamulolo lichita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo?

Rom 7:2 Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.

Rom 7:3 Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa kulamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.

Rom 7:4 Chotero, abale anga inunso mudayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukwatiwe ndi wina, ndiye amene adawukitsidwa kwa akufa, kuti ife tim’balire Mulungu zipatso.

Rom 7:5 Pakuti pamene tidali m’thupi, zilakolako za machimo, zimene zidali mwa chilamulo, zidali kuchita m’ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso.

Rom 7:6 Koma tsopano tidamasulidwa kuchilamulo, popeza tidafa kwa ichi chimene tidagwidwa nacho kale; chotero kuti, titumikire mu mzimu watsopano, si m’chilembo chakale ayi.

Rom 7:7 Tidzanena chiyani tsono? Kodi chilamulo chiri uchimo? Msatero ayi.. Ayi, koma ine sindikadazindikira uchimo; koma mwa lamulo ndimo: pakuti sindikadazindikira chilakolako, chikadapanda chilamulo kunena kuti usasilire.

Rom 7:8 Koma uchimo, pamene udapeza chifukwa, udachita m’kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo uchimo uli wakufa.

Rom 7:9 Ndipo kale ine ndidali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo lidadza, uchimo udatsitsimuka, ndipo ine ndidafa.

Rom 7:10 Ndipo lamulo, limene lidali lopatsa moyo, ndidalipeza lopatsa imfa.

Rom 7:11 Pakuti uchimo, pamene udapeza chifukwa mwa lamulo, udandinyenga ine, ndikundipha.

Rom 7:12 Chotero chilamulo chiri choyera, ndi chilangizo chake n’choyera ndi cholungama, ndi chabwino.

Rom 7:13 Ndipo tsopano chabwino chija chidandikhalira imfa kodi? Msatero ayi. Koma uchimo, kuti uwoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa kwambiri mwa lamulo.

Rom 7:14 Pakuti tidziwa kuti chilamulo chiri chauzimu; koma ine ndiri wathupi, wogulitsidwa, ku uchimo.

Rom 7:15 Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi.

Rom 7:16 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndibvomerezana nacho chilamulo kuti chiri chabwino.

Rom 7:17 Ndipo tsopano si ine ndichichita, koma uchimo wokhalabe m’kati mwanga ndiwo.

Rom 7:18 Pakuti ndidziwa kuti m’kati mwanga, (ndiko m’thupi langa), simukhala chinthu chabwino: pakuti kufuna ndiri nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.

Rom 7:19 Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choyipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.

Rom 7:20 Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, sindinenso amene ndichichita, koma uchimo wokhalabe m’kati mwanga ndiwo.

Rom 7:21 Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti pamene ndifuna chabwino, choyipa chiriko mwa ine.

Rom 7:22 Pakuti ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu. Mwa munthu wa m’kati mwanga.

Rom 7:23 Koma ndiwona lamulo lina m’ziwalo zanga, lirikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundibweretsa ine mu ukapolo wa lamulo la chimo umene uli mziwalo zanga.

Rom 7:24 Ho! munthu wosauka ine! Adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?

Rom 7:25 Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtima nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo.



8

Rom 8:1 Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa amene iwo akuyenda osati mwa thupi koma mwa Mzimu.

Rom 8:2 Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Rom 8:3 Pakuti chimene chilamulo sichidathe kuchita popeza chidafoka mwa thupi, Mulungu adatumiza Mwana wake wa Iye yekha m’chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m’thupi:

Rom 8:4 Kuti chilungamo cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.

Rom 8:5 Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu zathupi; koma iwo ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu.

Rom 8:6 Pakuti chisamaliro cha thupi chiri imfa; koma chisamaliro cha mzimu chiri moyo ndi mtendere.

Rom 8:7 Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja kuchilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.

Rom 8:8 Chomwecho iwo amene ali m’thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.

Rom 8:9 Koma inu simuli m’thupi ayi, koma mumzimu ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Tsopano ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, si ali wake wa Khristu.

Rom 8:10 Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu ali wa moyo chifukwa cha chilungamo.

Rom 8:11 Koma ngati Mzimu wa Iye amene adawukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adawukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.

Rom 8:12 Chifukwa chake, abale, ife tiri angongole si ake a thupi ayi, kukhala ndi moyo monga mwa thupi.

Rom 8:13 Pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.

Rom 8:14 Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.

Rom 8:15 Pakuti inu simudalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma mudalandira mzimu wa umwana, umene tifuwula nawo, kuti, Abba, Atate.

Rom 8:16 Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu:

Rom 8:17 Ndipo ngati ana, pomweponso wolowa m’nyumba; inde wolowa m’nyumba ake a Mulungu, ndi wolowa amzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.

Rom 8:18 Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzabvumbulutsidwa kwa ife.

Rom 8:19 Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira kuwonekera kwa ana a Mulungu.

Rom 8:20 Pakuti cholengedwacho chigonjetsedwa ku utsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene adachigonjetsa, mchiyembekezo.

Rom 8:21 Pakuti cholengedwacho chidzamasulidwa ku ukapolo wachibvundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.

Rom 8:22 Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuwula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.

Rom 8:23 Ndipo sichotero, koma ife tomwe; tiri nazo zowundukula za Mzimu, inde ifenso tibuwula m’kati mwathu, ndi kulindilira umwana wathu, ndiwo chiwomboledwe cha thupi lathu.

Rom 8:24 Pakuti ife tidapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chiwoneka si chiri chiyembekezo ayi; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?

Rom 8:25 Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindilira ndi chipiriro.

Rom 8:26 Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti chimene tichipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuwula zosatheka kuneneka.

Rom 8:27 Ndipo Iye asanthula m’mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera woyera mtima monga mwa chifuniro cha Mulungu .

Rom 8:28 Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene ali woyitanidwa ku cholinga chake.

Rom 8:29 Chifukwa kuti iwo amene Iye adawadziwiratu, iwowa adawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri.

Rom 8:30 Ndipo amene Iye adawalamuliratuwo, Iye adawayitana ndipo iwo amene adawayitana adawalungamitsa,ndipo iwo amene adawalungamitsa adawapatsanso ulemerero.

Rom 8:31 Ndipo tidzanena chiyani kuzinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatitsutsa ndani?

Rom 8:32 Iye amene sadatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma adampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?

Rom 8:33 Ndani adzaneneza wosankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene adawalungamitsa.

Rom 8:34 Ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adawafera, inde makamaka, ndiye amene adawuka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja la manja la Mulungu, amenenso atipembedzera ife.

Rom 8:35 Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunzidwa, kapena njala, kapena usiwa, kapena zowopsa, kapena lupanga?

Rom 8:36 Monga kwalembedwa, chifukwa cha inu tiri kuphedwa dzuwa lonse; tidayesedwa monga nkhosa zokaphedwa.

Rom 8:37 Ayi, koma mzinthu zonsezi, ife ndife oposa agonjetsi, mwa Iye amene adatikonda.

Rom 8:38 Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale mphamvu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilimkudza,

Rom 8:39 Ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chili chonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu chimene chiri mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.



9

Rom 9:1 Ndinena zowona mwa Khristu, sindikunama ayi, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndi ine mwa Mzimu Woyera.

Rom 9:2 Kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphweteka mtima kosalekeza.

Rom 9:3 Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi:

Rom 9:4 Ndiwo a Israyeli, ali nawo umwana ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m’kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;

Rom 9:5 Iwo ali makolo, ndi kwa iwo ndiko adachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka ku nthawi zonse. Amen.

Rom 9:6 Koma sikuli ngati mawu a Mulungu adakhala chabe ayi. Pakuti onse wochokera kwa Israyeli siali onse a Israyeli:

Rom 9:7 Sikuti chifukwa ali mbewu ya Abrahamu, ali onse ana; koma adati, mwa Isake, mbewu yako idzayitanidwa.

Rom 9:8 Ndiko kuti, ana athupi sakhala iwo ana a Mulungu ayi; koma ana a lonjezo awerengedwa mbewu.

Rom 9:9 Pakuti mawu a lonjezo ndi amenewa, panyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.

Rom 9:10 Ndipo si chotero chokha, koma Rabekanso pamene adali ndi pakati pam’ modzi, ndiye kholo lathu Isake;

Rom 9:11 (Pakuti anawo asanabadwe, kapena asadachite kanthu kabwino kapena koyipa, kuti cholinga cha Mulungu monga mwa kusankha kukhale, sichifukwa cha ntchito ayi, koma chifukwa cha wakuyitanayo);

Rom 9:12 Pakuti kudanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala wotumikira wam’ng’ono.

Rom 9:13 Monga kwalembedwa, ndidakonda Yakobo, koma ndidamuda Esawu.

Rom 9:14 Ndipo tsono tidzanena chiyani? Kodi chiripo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ayi.

Rom 9:15 Pakuti adati ndi Mose, ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.

Rom 9:16 Chotero sichichokera kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.

Rom 9:17 Pakuti lembo linena kwa Farawo, chifukwa cha cholinga chomwechi, ndidakuutsa iwe, kuti ndikawonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.

Rom 9:18 Chotero iye achitira chifundo amene iye afuna, ndipo amene iye afuna amuwumitsa mtima.

Rom 9:19 Ndipo iwe pamenepo udzanena kwa ine chifukwa chiyani iye wapeza cholakwa? Pakuti ndani adakaniza chifuno chake?

Rom 9:20 Ayi, koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mawu? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene adachipanga, Undipangiranji ine chotero?

Rom 9:21 Kodi kapena wowumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuwumba ndi ntchintchi yomweyo chotengera chimodzi cha ulemu ndi china chamanyazi?

Rom 9:22 Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuwonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, adalekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko?

Rom 9:23 Ndikuti iye akadziwitse chuma cha ulemerero wake wawukulu pa zotengera za chifundo, zimene iye adazikonzeratu kuulemerero wake.

Rom 9:24 Ndiwo ife amenenso iye adatiyitana, si a mwa Ayuda wokhawokha, komanso a mwa anthu amitundu?

Rom 9:25 Monga iye adatinso mwa Hoseya, Ndidzawatcha anthu anga amene sadakhala anthu anga, ndi wokondedwa wake amene sadali wokondedwa.

Rom 9:26 Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kudanenedwa kwa iwo, simuli anthu anga ayi, pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.

Rom 9:27 Ndipo monga Yesaya afuwula za Israyeli, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israyeli ukhala monga m’chenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.

Rom 9:28 Pakuti iye adzatsiriza ntchito, ndi kuyichita mwa chidule m`chilungamo: chifukwa Ambuye adzatsiliza ntchito yake mwachidule pa dziko lapansi.

Rom 9:29 Ndipo monga Yesaya adati kale , Ngati Ambuye wa makamu adakapanda kutisiyira ife mbewu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.

Rom 9:30 Kodi tidzanena chiyani tsono? Kuti amitundu amene sadatsata chilungamo, adafikira kuchilungamo, ndicho chilungamo cha m`chikhulupiriro.

Rom 9:31 Koma Israyeli, potsata lamulo la chilungamo, sadafikira lamulo la chilungamo.

Rom 9:32 Chifukwa chiyani? Chifukwa kuti sadalitsata ndi chikhulupiro, koma monga ndi ntchito za lamulo. Adakhumudwa pamwala wokhumudwitsa.

Rom 9:33 Monganso kwalembedwa kuti; Onani ndikhazika m’Ziyoni mwala wokhumudwitsa nawo, ndi thanthwe lopunthwitsa; Ndipo wokhulupirira pa iye sadzachita manyazi.



10

Rom 10:1 Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero la kwa Mulungu kwa Israyeli ndilo kuti iwo apulumuke.

Rom 10:2 Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso.

Rom 10:3 Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo wokha, iwo sadagonja kuchilungamo cha Mulungu.

Rom 10:4 Pakuti Khristu ndi chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa amene aliyense akhulupirira.

Rom 10:5 Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m’lamulo, adzakhala nacho moyo.

Rom 10:6 Koma chilungamo cha chikhulupiriro chitero, Usamanena mumtima mwako. Adzakwera ndani kumwambako? (Ndiko kutsitsako Khristu:)

Rom 10:7 Kapena adzatsikira ndani kudzenjeko? (Ndiko kukweza Khristu kwa akufa.)

Rom 10:8 Koma akuti chiyani? Mawu ali pafupi ndi iwe, m’kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mawu achikhulupiriro, amene ife tiwalalikira;

Rom 10:9 Kuti ngati udzabvomereza m’kamwa mwako, Ambuye Yesu, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuwukitsa kwa akufa, udzapulumuka.

Rom 10:10 Pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m’kamwa abvomereza kutengapo chipulumutso.

Rom 10:11 Pakuti lembo likuti, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi.

Rom 10:12 Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene ayitana pa Iye;

Rom 10:13 Pakuti amene aliyense adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Rom 10:14 Ndipo iwo adzayitana bwanji pa Iye amene sadamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwnaji Iye amene sadamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?

Rom 10:15 Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Wokometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga wa mtendere wobweretsa chisangalalo muzinthu zabwino.

Rom 10:16 Koma sadamvera uthenga onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye , ndani adakhulupirira zonena zathu?

Rom 10:17 Chomwecho chikhulupiriro chidza, mwa kumvera ndi kumva mwa mawu a Mulungu.

Rom 10:18 Koma ine nditi, sadamva iwo kodi! Indetu, liwu lawo lidatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi mawu awo kumalekezero adziko lapansi.

Rom 10:19 Koma nditi, kodi Israyeli alibe kudziwa? Poyamba Mose anena, Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi iwo amene sakhala mtundu wa anthu, ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira.

Rom 10:20 Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati, Ndidapezedwa ndi iwo amene sadandifune; ndidawonekera kwa iwo amene sadandifunsa.

Rom 10:21 Koma kwa Israyeli anena, Tsiku lonse ndidatambalitsira manja anga kwa anthu wosamvera ndi wotsutsana.



11

Rom 11:1 Chifukwa chake ndinena, Mulungu adataya anthu ake kodi? Msatero ayi. Pakuti inenso ndiri mu Israyeli, wa mbewu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.

Rom 11:2 Mulungu sadataya anthu ake amene Iye adawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Pomwe Iye amachita mapembedzero kwa Mulungu chifukwa cha Israeyeli, ndi kuti,

Rom 11:3 Ambuye, adawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.

Rom 11:4 Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndidadzisiyira ndekha anthu amuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sadagwadira Baala.

Rom 11:5 Choteronso nthawi yatsopano chiripo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.

Rom 11:6 Ndipo ngati ndi chisomo mwa pamenepo sindi ntchito ayi; ndipo pakutero, chisomo sichikhalanso chisomo. Koma ngati chiri mwa ntchito pamenepo sichisomonso: ndipo pakutero ntchito sikhalanso ntchito.

Rom 11:7 Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israyeli afunafuna sadachipeza; koma osankhidwawo adachipeza, ndipo wotsalawo adachititsidwa khungu;

Rom 11:8 Monga kudalembedwa kuti, Mulungu adawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.

Rom 11:9 Ndipo Davide akuti, Gome lawo likhale kwa iwo ngati msampha, ndi ngati diwa, ndi monga chokhumudwitsa, ndi chowabwezera chilango iwo:

Rom 11:10 Maso awo adetsedwe, kuti asapenye, ndipo muweramitse msana wawo.

Rom 11:11 Chifukwa chake ndinena, Adakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ayi; koma ndi kugwa kwawo chipulumutso chidadza kwa amitundu, kudzachititsa iwo nsanje.

Rom 11:12 Ndipo ngati kugwa kwawo kwatengera dziko lapansi chuma, ndipo kuchepa kwawo kutengera anthu a mitundu chuma; koposa kotani nanga kudzaza kwawo?

Rom 11:13 Koma ndiyankhula ndi inu amitundu popeza ine ndiri mtumwi wa kwa amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;

Rom 11:14 Kuti ngati mkutheka ndikachititse mkwiyo iwo amene ndi a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo.

Rom 11:15 Pakuti ngati kuwataya kwawo kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwawo kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa?

Rom 11:16 Ndipo ngati zipatso zoyamba ziri zopatulika, choteronso zonse; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi.

Rom 11:17 Koma ngati nthambi zina zidathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wazitona wakuthengo, udamezetsanidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo.

Rom 11:18 Usadzitama iwe wekha motsutsana ndi nthambizo; Koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ayi, koma muzu ukunyamula iwe.

Rom 11:19 Ndipo kapena udzanena, nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikamezetsanidwemo.

Rom 11:20 Chabwino; chifukwa chakusakhulupirira iwo adakhala wothyoledwa, ndipo iwe uyima mwa chikhulupiriro. Usamadzikuza mumtima, koma wopatu:

Rom 11:21 Pakuti ngati Mulungu sadalekerera nthambi za mtundu wake, sadzakulekerera iwe.

Rom 11:22 Chifukwa chake wonani ubwino wake wa Mulungu ndi kuwuma mtima kwake kwa Mulungu; kwa iwo adagwa, kuwuma kwake; koma kwa iwe ubwino wake wa Mulungu, ngati ukhala chikhalire ubwinowo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.

Rom 11:23 Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire ndi chisakhulupiriro, adzawamezanitsanso pakuti Mulungu ndi wokwaniritsa kuwamezanitsanso.

Rom 11:24 Pakuti ngati iwe udasadzidwa ku mtengo wazitona wa mtundu wa kuthengo mwa chilengedwe, ndipo udamezetsanidwa kosiyana ndi chilengedwe ku mtengo wa azitona wabwino, mokaniza; koposa kotani nanga iwo, ndiwo wokhala chilengedwe nthambi zake, adzamezetsedwa ku mtengo wawo womwewo wa azitona?

Rom 11:25 Pakuti sindifuna, abale kuti mukhale wosadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nakha, kuti khungu lakusawona kudadza pang’ibi oa Usratekum kufikira a mitundu akwanire kulowamo.

Rom 11:26 Ndipo chotero Israyeli yense adzapulumuka; monganso kudalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo:

Rom 11:27 Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo pamene ndidzachotsa machimo awo.

Rom 11:28 Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ndi adani, chifukwa cha inu; koma ngati kunena za chisankhidwe, ali wokondedwa, chifukwa cha makolo.

Rom 11:29 Pakuti mphatso zake ndikuyitana kwake kwa Mulungu sizilapika.

Rom 11:30 Pakuti monga inunso kale simudakhulupirira Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusakhulupirira kwao.

Rom 11:31 Choteronso iwo sadakhulupirira tsopano, kuti iwonso mwa chifundo chawo kuti iwonso akalandire chifundo.

Rom 11:32 Pakuti Mulungu adatsekera pamodzi onse m’kusakhulupirira, kuti akachitire onse chifundo.

Rom 11:33 Ha! Kuya kwake kwa m`chuma pamodzi ndi nzeru ndi chidziwitso cha Mulungu.! Wosasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake mzosalondoleka!

Rom 11:34 Pakuti adadziwa ndani mtima wa Ambuye? Kapena adakhala phungu wake ndani?

Rom 11:35 Ndipo adayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzam’bwezeranso Iye?

Rom 11:36 Pakuti kuchokera kwa Iye ndi mwa Iye, ndi kwa Iye muli zinthu zonse: kwa Iyeyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse.



12

Rom 12:1 Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

Rom 12:2 Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe apansi pano; koma mukhale wosandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi cholandirika ndi changwiro.

Rom 12:3 Pakuti ndinena kupyolera mwa chisomo chopatsidwa kwa ine. Kwa munthu aliyense pakati pa inu, kuti asaganize mwa iye yekha koposa kumene ayenera kuganiza; koma aganize modziletsa yekha, kolingana ndi Mulungu wampatsila aliyense muyeso wa chikhulupiriro.

Rom 12:4 Pakuti monga m’thupi limodzi tiri nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo siziri nayo ntchito imodzimodzi;

Rom 12:5 Chomwecho ife, ndife ambiri tiri thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zimzake wina ndi wina.

Rom 12:6 Ndipo pokhala nazo ife mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chopatsidwa kwa ife, kapena mphatso yonenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro.

Rom 12:7 Kapena yotumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wophunzitsa, akaphunzitse;

Rom 12:8 Kapena iye wodandaulira, kukudandaulirako; wogawira achite ndi mtima wowona; iye woweruza, aweruze ndi changu; iye wochita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.

Rom 12:9 Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwirizana nacho chabwino.

Rom 12:10 M’chikondano cha anzanu wina ndi mzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Rom 12:11 Musakhale aulesi m’machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye;

Rom 12:12 Kondwerani m’chiyembekezo, pilirani m’masautso; limbikani chilimbikire m’kupemphera.

Rom 12:13 Patsani zosowa woyera mtima; cherezani, aulendo.

Rom 12:14 Dalitsani iwo akuzunza inu, dalitsani, musawatemberere.

Rom 12:15 Kondwani nawo iwo akukondwera; ndipo lirani nawo akulira.

Rom 12:16 Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mzake; musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nawo wodzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

Rom 12:17 Musabwezere munthu aliyense choyipa chosinthana ndi choyipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.

Rom 12:18 Ngati mkutheka monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.

Rom 12:19 Wokondedwa, musabwezere choyipa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.

Rom 12:20 Chifukwa chake ngati mdani wako akumva njala, um’dyetse, ngati akumva ludzu, umwetse; pakuti pakutero udzawunjika makala amoto pamutu pake.

Rom 12:21 Musagonje ku choyipa, koma ndi chabwino gonjetsani choyipa.



13

Rom 13:1 Anthu onse aliyense agonje ku mphamvu za udindo: pakuti palibe mphamvu za udindo wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo mphamvu za udindo zilipo ziyikidwa ndi Mulungu.

Rom 13:2 Kotero kuti aliyense wotsutsana nazo mphamvu za udindo, akaniza choyikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.

Rom 13:3 Pakuti woweruza sakhala wowopsa ku ntchito zabwino koma ku zoyipa. Ndipo ufuna kodi kusawopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m’menemo:

Rom 13:4 Pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, wochitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choyipa, wopatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoyipa.

Rom 13:5 Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale wogonja, sichifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.

Rom 13:6 Pakuti chifukwa cha ichi muperekenso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.

Rom 13:7 Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake akulipidwa; kuwopa kwa eni ake akuwawopa; ulemu kwa eni ake aulemu.

Rom 13:8 Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mzake wakwaniritsa lamulo.

Rom 13:9 Pakuti ili, usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, usasilire, ndipo lingakhale lamulo lina liri lonse, limangika pamodzi m’mawu amenewa, kuti, udzikonda mzako monga udzikondera iwe wekha.

Rom 13:10 Chikondano sichichitira mzake choyipa; chotero chikondanocho chiri chokwanitsa lamulo.

Rom 13:11 Ndipo kuti, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuwuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chiri pafupi koposa pamene tidayamba kukhulupirira.

Rom 13:12 Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; chifukwa chake tibvule ntchito za mdima, ndi tibvale chida cha kuwunika.

Rom 13:13 Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m’madyerero ndi kuledzera ayi, si m’chigololo ndi chonyansa ayi, si mundewu ndi nkhwidzi ayi.

Rom 13:14 Koma bvalani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.



14

Rom 14:1 Ndipo iye amene ali wofoka m’chikhulupiriro mumlandire, koma sikuchita naye makani wotsutsana ayi.

Rom 14:2 Munthu m’modzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofoka angodya zitsamba.

Rom 14:3 Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira iye.

Rom 14:4 Ndani iwe woweruza m’nyamata wa mwini wake? Iye ayimilira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzayimiliritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuyimiliritsa.

Rom 14:5 Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa limzake, wina aganizira kuti masiku onse wofanana. Munthu aliyense akhazikike konse mumtima mwake.

Rom 14:6 Iye wosamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye; ndipo iye wosasamalila tsiku salisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu.

Rom 14:7 Pakuti palibe m’modzi wa ife adzikhalira ndi moyo yekha, ndipo palibe m’modzi adzifera yekha.

Rom 14:8 Pakuti tingakhale tiri ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; chifukwa chake tingakhale ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye.

Rom 14:9 Pakuti chifukwa cha ichi Khristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti Iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo

Rom 14:10 Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzayimilira ku mpando wakuweruza wa Mulungu.

Rom 14:11 Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzabvomereza Mulungu.

Rom 14:12 Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.

Rom 14:13 Chifukwa chake tisaweruzanenso wina ndi mzake, koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asayike chokhumudwitsa pa njira ya mbale wake, kapena chompunthwitsa.

Rom 14:14 Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.

Rom 14:15 Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe yendayendanso ndi chikondano. Usamuwononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera.

Rom 14:16 Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire.

Rom 14:17 Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala m`chakudya ndi m`chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Rom 14:18 Pakuti iye amene atumikira Khristu mu zinthu izi akondweretsa Mulungu, nabvomerezeka ndi anthu.

Rom 14:19 Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mzake.

Rom 14:20 Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse ziri zoyera; koma kuli koyipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.

Rom 14:21 Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chiri chonse chokhumudwitsa ndi chopunthwitsa ndi kufowoketsa mbale wako.

Rom 14:22 Chikhulupiriro chimene uli nacho, ukhale nacho kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu. Wodala ndiye amene sadziweruza mwini yekha m’zinthu zomwe iye wazibvomereza.

Rom 14:23 Koma iye amene akayika kayika pakudya, atsutsika chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chiri chonse chosatuluka m’chikhulupiriro, ndicho uchimo.



15

Rom 15:1 Ndipo ife amene tiri wolimba, tiyenera kunyamula zofoka za wopanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.

Rom 15:2 Yense wa ife akondweretse mzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

Rom 15:3 Pakuti Khristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, minyozo ya iwo amene adakunyoza iwe idagwera pa Ine.

Rom 15:4 Pakuti zonse zidalembedwa kale zidalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiliro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.

Rom 15:5 Ndipo Mulungu wa chipiliro ndi wachitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mzake, monga mwa Khristu Yesu.

Rom 15:6 Kuti nonse pamodzi, m’kamwa m’modzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Rom 15:7 Chifukwa chake mulandirane wina ndi mzake, monganso Khristu anatilandira ife, ku ulemerero wa Mulungu.

Rom 15:8 Ndipo ndinena kuti Khristu adakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha chowonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo wopatsidwa kwa makolo,

Rom 15:9 Ndikuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo chake; monga kwalembedwa, chifukwa cha ichi ndidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzayimbira dzina lanu.

Rom 15:10 Ndiponso anena, kondwerani amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.

Rom 15:11 Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande Iye.

Rom 15:12 Ndiponso, Yesaya anati, Padzakhala muzu wa Jese, ndi Iye amene adzauka kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu a mitundu adzamukhulupirira.

Rom 15:13 Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mumphamvu ya Mzimu Woyera.

Rom 15:14 Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli wodzala ndi ubwino, wodzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mzake.

Rom 15:15 Koma mwina abale ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu.

Rom 15:16 Kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Khristu kwa amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kudzipereka kwao kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.

Rom 15:17 Chifukwa chake ndiri nacho chodzitamandira cha mwa Khristu Yesu mu zinthu zimene zili kwa Mulungu.

Rom 15:18 Pakuti sindingathe kulimba mtima kuyankhula zinthu zimene Khristu sadazichita mwa ine zakuwamvetsa anthu amitundu, ndi mawu ndi ntchito.

Rom 15:19 Kupyolera mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu wa Mulungu; kotero kuti kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iluriko, ndakwanitsa kulalikira Uthenga wa Khristu;

Rom 15:20 Inde chotero tidalimbika kulalikira Uthenga Wabwino, pamalopo Khristu sadatchulidwe kale, kuti ndisamange pa maziko a munthu wina.

Rom 15:21 Koma monga kwalembedwa kwa iwo amene sadayakhulidwe adzawona, ndipo kwa iwo amene sadamve adzazindikira.

Rom 15:22 Chifukwa chakenso ndidaletsedwa kawiri kawiri kudza kwa inu;

Rom 15:23 Koma tsopano pamene ndiribe malo m’mayiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero.

Rom 15:24 Pamene pali ponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndidzadza kwa inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kudzazidwa ndi gulu lanu.

Rom 15:25 Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, kukatumikira woyera mtima.

Rom 15:26 Pakuti kudakondweretsa aku Makedoniya ndi Akaya kusonkha chopereka cha wosauka a kwa woyera mtima aku Yerusalemu.

Rom 15:27 Pakuti chidakondweretsa iwo ndithu; ndipo iwo ali ndi ngongole nawo, Pakuti ngati amitundu wokhala wotengapo gawo pa zinthu zawo za uzimu, ntchito yawonso ndiyo kutumikira iwo ali mu zinthu zathupi.

Rom 15:28 Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzadutsa kwanu kupita ku Spaniya.

Rom 15:29 Ndipo ndidziwa kuti pamene ndidza kwanu, ndidzafika m’kudzaza kwake kwa m’dalitso wa uthnga wa Khristu.

Rom 15:30 Ndipo ndikudandaulirani, abale, chifukwa cha Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chifukwa cha chikondi cha Mzimu, kuti mumalimbika pamodzi ndi ine m’mapemphero anu a kwa Mulungu chifukwa cha ine;

Rom 15:31 Kuti ndikapulumutsidwe kwa wosamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi woyera mtima;

Rom 15:32 Pakuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuno cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.

Rom 15:33 Ndipo Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.



16

Rom 16:1 Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wa mkazi wa mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya;

Rom 16:2 Kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera woyera mtima, ndi kuti mumthandize m’zinthu ziri zonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha adali wothandiza ambiri, ndi ine ndemwe.

Rom 16:3 Apatseni moni Priska ndi Akula, antchito amzanga mwa Khristu Yesu.

Rom 16:4 Amene adapereka makosi awo chifukwa cha moyo wanga: amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu.

Rom 16:5 Ndipo patsani moni Mpingo wa Ambuye wa m’nyumba mwawo. Patsani moni Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso chowundukura cha Asiya cha kwa Khristu.

Rom 16:6 Patsani moni Mariya amene adadzilemetsa ndi ntchito zambiri zothandiza inu.

Rom 16:7 Patsani moni Androniko ndi Yuniya, anansi anga, ndi andende amzanga, amene ali womveka mwa atumwi, amenenso adali mwa Khristu ndisadakhale ine.

Rom 16:8 Patsani moni Ampliyato wokondedwa wanga mwa Ambuye.

Rom 16:9 Patsani moni Urbano wantchito mzathu mwa Khristu, ndi Staku wokondedwa wanga.

Rom 16:10 Patsani moni Apele, wobvomerezedwayo mwa Khristu. Patsani moni iwo a m`nyumba ya Aristobulo.

Rom 16:11 Patsani moni Herodiyona, mbale wanga. Patsani moni iwo a kwa Narikiso, amene ali mwa Ambuye.

Rom 16:12 Patsani moni Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye. Patsani moni Persida, wokondedwayo amene adagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye.

Rom 16:13 Patsani moni Rufo, wosankhidwayo mwa Ambuye ndi amayi ake ndi wanga.

Rom 16:14 Patsani moni Asunkrito, Felego, Herme, Partoba, Herma ndi abale amene ali nawo.

Rom 16:15 Patsani moni Filologo ndi Yuliya, Nereya ndi mlongo wake, ndi Olumpa, ndi woyera mtima onse ali pamodzi nawo.

Rom 16:16 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsompsono chopatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni inu.

Rom 16:17 Ndipo ndikudandaulirani, abale, zindikirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho mudachiphunzira inu; ndipo patukani pa iwo.

Rom 16:18 Pakuti wotere satumikira Ambuye wathu Yesu Khristu, koma mimba zawo; ndipo ndi mawu osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.

Rom 16:19 Pakuti kumvera kwanu kudabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pazabwino, koma opanda nzeru pa zoyipa.

Rom 16:20 Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwa. Chisomo cha Ambuye wathu Khristu chikhale ndi inu. Ameni

Rom 16:21 Timoteo wa ntchito mnzanga, ndi Lukiyo, ndi Yasoni, ndi Sosipatro abale anga akupatsani moni inu.

Rom 16:22 Ine Tertiyo, amene ndikulemba kalatayi ndi kupatsani moni mwa Ambuye.

Rom 16:23 Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupatsani moni inu. Erasto, msungachuma wa mzinda akupatsani moni, ndiponso Kwarto m`baleyo.

Rom 16:24 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Amen.

Rom 16:25 Tsopano kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwabvumbulutso la chinsinsi chimene mobisika kuyambira chilengedwere dziko lapansi.

Rom 16:26 Koma chawonetsedwa tsopano mwa malembo a aneneri, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti kudziwitsidwe kwa mitundu yonse kumvera kwa chikhulupiriro:

Rom 16:27 Kwa Mulungu wa nzeru yekhayo, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu ku nthawi zonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE