Revelation


1

Rev 1:1 “Chibvumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu adabvumbulutsira achiwonetsere atumiki ake, ndicho cha zinthu izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa m’ngelo wake adazindikiritsa izi kwa mtumiki wake Yohane:

Rev 1:2 Amene adachita umboni za mawu a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, ndi zinthu zonse zimene adaziwona.

Rev 1:3 Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mawu a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo: pakuti nthawi yayandikira.

Rev 1:4 Yohane kwa mipingo isanu ndi iwiri mu Asiya: chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Iye amene ali, ndi adali, ndi amene alimkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala ku mpando wachifumu wake.

Rev 1:5 Ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu adziko lapansi. Kwa Iye amene adatikonda ife, natimasula ku machimo athu ndi mwazi wake.

Rev 1:6 Ndipo adatiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemererro ndi ulamuriro kufikira nthawi za nthawi. Ameni.

Rev 1:7 Tawonani adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya Iye, iwonso amene adampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Ameni.

Rev 1:8 Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, atero Ambuye amene ali, amene adali, ndi amene alimkudza, wamphamvu yonse.

Rev 1:9 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m’chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu Khristu ndidakhala pa chisumbu chotchedwa Patimo, chifukwa cha mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu.

Rev 1:10 Ndidagwidwa ndi Mzimu pa tsiku la Ambuye, ndipo ndidamva kumbuyo kwanga mawu akulu, ngati a lipenga,

Rev 1:11 Ndikunena kuti, Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza: ndipo chimene upenya, lemba m’buku, nulitumize kwa mipingo isanu ndi iwiri, imene iri mu Asiya, Aefeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya.

Rev 1:12 Ndipo ndidacheuka kuwona wonena mawu amene adayankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndidawona zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi;

Rev 1:13 Ndipo pakati pa zoyikapo nyali zisanu ndi ziwirizo wina wonga Mwana wa munthu atabvala chobvala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolidi pachifuwa.

Rev 1:14 Ndipo tsitsi lapa mutu pake lidali loyera ngati ubweya woyera, kuyera ngati chipale chofewa; ndipo maso ake ngati lawi la moto;

Rev 1:15 Ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m’ng’anjo; ndi mawu ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.

Rev 1:16 Ndipo m’dzanja lake lamanja mudali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi mkamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konse konse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.

Rev 1:17 Ndipo pamene ndidamuwona Iye, ndidagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo adayika dzanja lake la manja pa ine, nati, Usawope, Ine ndine woyamba ndi wotsiriza.

Rev 1:18 Ndine wamoyoyo; ndipo ndidali wakufa, ndipo tawona ndiri wamoyo ku nthawi zonse. Ameni; ndipo ndiri nawo mafungulo a gahena ndi imfa.

Rev 1:19 Lemba zinthu zimene udaziwona, ndi zinthu zimene ziripo, ndi zinthu zimene zidzawoneka mtsogolomo;

Rev 1:20 Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri udaziwona pa dzanja langa la manja, ndi zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri za golidi. Nyenyezi zisanu ndi ziwirizo ndiwo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndiyo Mipingo isanu ndi iwiri.



2

Rev 2:1 Kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Aefeso lemba; zinthu izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m’dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoyikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi;

Rev 2:2 Ndidziwa ntchito zako ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sukhoza kulola woyipa, ndipo udayesa iwo amene adzitcha wokha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza iwo abodza.

Rev 2:3 Ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema.

Rev 2:4 Koma ndiri nako kanthu kotsutsana ndi iwe, chifukwa kuti udataya chikondi chako choyamba.

Rev 2:5 Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, msanga ndipo ndidzatulutsa choyikapo nyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.

Rev 2:6 Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolayi, zimene Inenso ndidana nazo.

Rev 2:7 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli pakati pa Paradiso wa Mulungu.

Rev 2:8 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Smurna lemba; zinthu izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene adali wakufa, koma ali ndi moyo;

Rev 2:9 Ndidziwa ntchito zako, ndi chisautso chako, ndi umphawi wako, (komatu uli wachuma), ndipo ndidziwa za mwano wa iwo akunena za iwo wokha kuti ali Ayuda, koma sali Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.

Rev 2:10 Usawope zimene uti udzamve kuwawa; tawona, mdierekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe Korona wa moyo.

Rev 2:11 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzachitidwa choyipa ndi imfa yachiwiri.

Rev 2:12 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba; zinthu izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konse konse;

Rev 2:13 Ndidziwa ntchito zako, ndi kumene ukhalako kuja kuli mpando wa chifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, wosakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m’masiku wa Antipasi mboni yanga, wophedwa, wokhulupirika wanga, amene adaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.

Rev 2:14 Komatu ndiri nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nawo komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene adaphunzitsa Balaki kuyika chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israyeli, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, ndikuti achite chiwerewere.

Rev 2:15 Kotero uli nawo akugwira chiphunzitso cha Anikolayi momwemonso. Chinthu chimene ndidana nacho.

Rev 2:16 Lapa; ndipo ngati sutero ndidzadza kwa iwe msanga, ndipo ndidzachita nawo nkhondo ndi lupanga la mkamwa mwanga.

Rev 2:17 Iye wakukhala nalo khutu amve chimeme Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa adye mana wobisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira.

Rev 2:18 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Tiyatira lemba; zinthu izi anena Mwana wa Mulungu, wakukhala nawo maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira;

Rev 2:19 Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi utumiki ndi chikhulupiriro, ndi chipiriro chako,ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo.

Rev 2:20 Koma ndiri nazo zinthu pang’ono zotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebeli, wodzitcha yekha m’neneri; ndipo aphunzitsa, nasokeretsa atumiki anga, kuti achite chiwerewere ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.

Rev 2:21 Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chiwerewere chake.

Rev 2:22 Tawona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m’chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zawo.

Rev 2:23 Ndipo ndidzapha ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.

Rev 2:24 Koma ndinena kwa iwe, kwa wotsala a ku Tiyatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sadazindikira zakuya za Satana, monga anena, sindidzakusanjikizani katundu wina.

Rev 2:25 Koma chimene uli nacho, gwiritsa kufikira ndidza.

Rev 2:26 Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzampatsa ulamuliro wa pa a mitundu.

Rev 2:27 Ndipo adzawalamulira iwo ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga Inenso ndalandira kwa Atate wanga.

Rev 2:28 Ndipo ndidzampatsa iye nyenyezi ya nthanda, yam’bandakucha.

Rev 2:29 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.



3

Rev 3:1 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa Sarde lemba; zinthu izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu; ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo ndiwe wakufa.

Rev 3:2 Khala wodikira, ndipo limbikitsa zinthu zotsalira, zimene zidafuna kufa; pakuti sindinapeza ntchito zako zangwiro pamaso pa Mulungu.

Rev 3:3 Chifukwa chake kumbukira momwe udalandirira ndikumvera; nusunge nulape: chifukwa chake ukapanda kudikira, ndidzafika kwa iwe ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.

Rev 3:4 Komatu uli nawo mayina wowerengeka mu Sardisi; amene sanadetsa zobvala zawo; ndipo adzayenda ndi Ine m’zoyera; chifukwa ali woyenera.

Rev 3:5 Iye amene alakika adzabvekedwa zobvala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m’buku lamoyo, koma ndidzabvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.

Rev 3:6 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa mipingo.

Rev 3:7 Ndipo kwa m’ngelo wa mpingo wa ku Filadelfeya lemba; zinthu izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula;

Rev 3:8 Ndidziwa ntchito zako; tawona ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo; kuti uli nayo mphamvu pang’ono, ndipo udasunga mawu anga, osakana dzina langa.

Rev 3:9 Tawona, ndikupatsa ena wotuluka m’sunagoge wa Satana, akudzinenera wokha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; tawona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.

Rev 3:10 Popeza udasunga mawu a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko lapansi.

Rev 3:11 Tawona, ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande Korona wako.

Rev 3:12 Iye wakulakika, ndidzamuyesa iye mzati wa mkachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m’Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndipo ndidzalemba pa iye dzina langa latsopano.

Rev 3:13 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa mipingo.

Rev 3:14 Ndipo kwa m’ngelo wa Mpingo wa ku Leodikaya lemba; zinthu izi anena Ameni, mboni yokhulupirika ndi yowona, woyamba wa chilengo cha Mulungu;

Rev 3:15 Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizila kapena wotentha; mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.

Rev 3:16 Kotero, popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulabvula mkamwa mwanga.

Rev 3:17 Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndiri nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu ndi wausiwa:

Rev 3:18 Ndikulangiza ugule kwa Ine golidi woyenga m’moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zobvala zoyera, kuti ukabvekedwe, ndi kuti manyazi a umaliseke wako usawonekere; ndi mankhwala wopaka m’maso mwako, kuti ukawone.

Rev 3:19 Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nulape.

Rev 3:20 Tawona, ndayima pakhomo, ndigogoda: ngati wina akumva mawu anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

Rev 3:21 Iye wakulakika, ndidzampatsa akhale pansi pamodzi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndidalakika, ndipo ndidakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.

Rev 3:22 Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.



4

Rev 4:1 Zitatha izi ndidapenya, ndipo tawonani, khomo lidatseguka m’Mwamba: ndipo mawu woyamba ndidawamva, ngati lipenga lakuyankhula ndi ine; amene adati, kwera kuno, ndipo ndidzakuwonetsa zinthu zimene ziyenera kuchitika mtsogolomo.

Rev 4:2 Ndipo nthawi yomweyo ndidali mu Mzimu: ndipo, tawonani padayikika mpando wachifumu m’Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina.

Rev 4:3 Ndipo mawonekedwe a Iye wokhalapo adafanana ndi mwala wa Jaspa, ndi Sardiyo: ndipo padali utawaleza wozinga mpando wachifumu, mawonekedwe ake ngati emaralido.

Rev 4:4 Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inayi: ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anayi atabvala zobvala zoyera ndipo pa mutu pawo padali a Korona agolidi.

Rev 4:5 Ndipo kuchokera kumpando wachifumuwo, mudatuluka mphezi ndi mawu ndi mabingu: Ndipo padali nyali zisanu ndi ziwiri zoyaka moto ku mpando wachifumu, ndiyo Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu.

Rev 4:6 Ndipo kumpando wachifumuwo, kudali nyanja yamandala yonga kusitalo; ndipo pakati pa mpando wachifumuwo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinayi zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.

Rev 4:7 Ndipo chamoyo choyamba chidafanana nawo mkango, ndi chamoyo chachiwiri chidafanana ndi mwana wang’ombe, chamoyo chachitatu chidali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinayi chidafanana ndi chiwombankhanga chakuwuluka.

Rev 4:8 Ndipo zamoyo zinayi, chonse pa chokha chidali nawo mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m’katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, Woyera, Woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvu yonse, amene adali, amene ali ndi amene alimkudza.

Rev 4:9 Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa Iye wakukhala pampando wa chifumu, kwa Iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi.

Rev 4:10 Akulu makumi awiri mphambu anayi amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, naponya pansi a Korona awo kumpando wachifumu, nanena,

Rev 4:11 Muyenera inu, Ambuye wathu kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu: chifukwa inu mudalenga zinthu zonse ndipo mwachifuniro chanu zidakhala ndipo zidalengedwa.



5

Rev 5:1 Ndipo ndidawona m’dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wa chifumu buku lolembedwa mkati ndi kunja kwake, losindikizidwa ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri.

Rev 5:2 Ndipo ndidawona m’ngelo wamphamvu wakulalikira ndi mawu akulu, ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?

Rev 5:3 Ndipo padalibe munthu m’modzi m’Mwamba, kapena padziko lapansi, kapena pansi pa dziko wakutsegula buku, kapena kulipenya;

Rev 5:4 Ndipo ndidalira kwambiri, chifukwa sadapezeke munthu woyenera kutsegula ndi kuwerenga buku kapena kulipenya.

Rev 5:5 Ndipo m’modzi wa akulu adanena ndi ine, Usalire: tawona, mkango wochokera mfuko la Yuda, muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi kumasula zosindikizira zake zisanu ndi ziwiri.

Rev 5:6 Ndipo ndidawona, ndipo tawonani pakati pa mpando wachifumu ndi wa zamoyo zinayi, ndi pakati pa akulu, mwana wankhosa ali chiliri ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m’dziko lonse lapansi.

Rev 5:7 Ndipo adadza, natenga buku ku dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu.

Rev 5:8 Ndipo pamene iye adatenga bukulo, zamoyo zinayi, ndi akulu makumi awiri mphambu anayi zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nawo, azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zonunkhira, ndizo mapemphero a woyera mtima.

Rev 5:9 Ndipo adayimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo ndi kumasula zosindikizira zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi a manenedwe onse, ndi mitundu ndi mafuko onse;

Rev 5:10 Ndipo mwatipanga ife mafumu ndi ansembe a kwa Mulungu wathu: ndipo tidzalamulira padziko lapansi.

Rev 5:11 Ndipo ndidawona, ndipo ndidamva mawu wa angelo ambiri pozinga mpando wachifumu ndi zamoyo ndi akulu: ndipo mawerengedwe awo adali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi;

Rev 5:12 Akunena ndi mawu akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kuti alandire mphamvu, ndi chuma, ndi nzeru, ndi chilimbiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi madalitso.

Rev 5:13 Ndipo cholengedwa chiri chonse chiri m’mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m’nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndidazimva ziri kunena, kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale madalitso, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.

Rev 5:14 Ndipo zamoyo zinayi zidati, Ameni. Ndipo akulu makumi awiri mphambu anayi adagwa pansi nalambira Iye amene akhala ndi moyo kunthawi za nthawi.



6

Rev 6:1 Ndipo ndidawona pamene Mwanawankhosa adatsegula chimodzi cha zosindikizira, ndipo ndidamva chimodzi mwa zamoyo zinayi, nichinena, ngati mawu abingu idza nuwone.

Rev 6:2 Ndipo ndidapenya, ndipo tawonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo adali nawo uta; ndipo adampatsa Korona; ndipo adapita kugonjetsa ndi kuti akagonjetse.

Rev 6:3 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachiwiri, ndidamva chamoyo chachiwiri nichinena, Idza, ndipo uwone.

Rev 6:4 Ndipo adatuluka kavalo wina, amene adali wofiyira: ndipo adampatsa iye womkwerayo mphamvu ya kuchotsa mtendere padziko lapansi, ndikuti aphane wina ndi mnzake: ndipo adampatsa iye lupanga lalikulu.

Rev 6:5 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira cha chitatu, ndidamva chamoyo chachitatu nichinena, Idza, nuwone. Ndipo ndidapenya, tawonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwerayo adali nawo muyeso m’dzanja lake.

Rev 6:6 Ndipo ndidamva mawu pakati pa zamoyo zinayi, nanena, Muyeso wa tirigu wogula lupiya; ndi miyeso itatu ya balele lupiya,tawona,iwe mafuta ndi vinyo usaziyipse.

Rev 6:7 Ndipo pamene adatsegura chosindikizira chachinayi, ndidamva mawu a chamoyo chachinayi nichinena, Idza nuwone.

Rev 6:8 Ndipo ndidapenya tawonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo Hade adatsatana naye; ndipo adawapatsa mphamvu padera lachinayi la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.

Rev 6:9 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachisanu, ndidawona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene adali nawo:

Rev 6:10 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, ndi kunena, kufikira liti, o! inu Ambuye, woyera ndi wowona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko lapansi?

Rev 6:11 Ndipo adapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso atumiki anzawo, ndi abale awo amene adzaphedwa monganso iwo eni kuti kukwaniritsidwe.

Rev 6:12 Ndipo ndidawona pamene adatsegula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo,tawonani padali chibvomezi chachikulu; ndi dzuwa linada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi udakhala ngati mwazi;

Rev 6:13 Ndipo nyenyezi za m’mwamba zidagwa padziko lapansi, monga mkuyu utaya nkhuyu zake zosapsa, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.

Rev 6:14 Ndipo Kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zidatunsidwa kuchoka m’malo mwawo.

Rev 6:15 Ndipo mafumu a dziko lapansi, ndi anthu akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi anthu amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi m’matanthwe a m’mapiri;

Rev 6:16 Ndipo adanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya Iye amene akhala pa mpando wa chifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa.

Rev 6:17 Chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wake wafika, ndipo akhoza kuyima ndani?



7

Rev 7:1 Ndipo zitatha zinthu izi ndidawona angelo anayi alimkuyimilira pa ngodya zinayi za dziko lapansi, akugwira mphepo zinayi za dziko lapansi,kuti mphepo zisawombe padziko lapansi kapena panyanja, kapena pa mtengo uli wonse.

Rev 7:2 Ndipo ndidawona m’ngelo wina, adakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chosindikizira cha Mulungu wa moyo: ndipo adafuwula ndi mawu akulu kwa angelo anayi, kwa iyeyu kudapatsidwa mphamvu yakuyipsa dziko ndi nyanja,

Rev 7:3 Nanena, Musayipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titasindikiza chizindikiro atumiki a Mulungu wathu, pa mphumi pawo.

Rev 7:4 Ndipo ndidamva chiwerengero cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi a onse amafuko a ana a Israyeli.

Rev 7:5 Mwa fuko la yuda adasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri: mwa fuko la Rubeni adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri: mwa fuko la Gadi adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri.

Rev 7:6 Mwa fuko la Aseri adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Nafitali adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Manase adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri.

Rev 7:7 Mwa fuko la Simeon adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Levi adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri.

Rev 7:8 Mwa fuko la Zebuloni adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Yosefe adasindikizidwa zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Benjamini adasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri.

Rev 7:9 Zitatha izi, ndidapenya, tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu adakhoza kuliwerenga, wochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuyimilira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atabvala zobvala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo;

Rev 7:10 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, nanena, chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.

Rev 7:11 Ndi kwa angelo onse akuyimilira pozinga mpando wa chifumu, ndi kwa akulu ndi zamoyo, zinayizo ndipo zidagwa nkhope zawo pansi ku mpando wachifumu nalambira Mulungu.

Rev 7:12 Ndi kunena, Ameni:Madalitso, ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi Ameni.

Rev 7:13 Ndipo m’modzi wa akulu adayankha, nanena ndi ine, Iwo wobvala zobvala zoyera ndiwo ayani? ndipo achokera kuti?

Rev 7:14 Ndipo ndidati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo adati kwa ine, Iwo ndiwo wochokera kutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo adatsuka zobvala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwana wankhosa.

Rev 7:15 Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku m’kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzakhala pakati pawo.

Rev 7:16 Sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena kutentha kulikonse.

Rev 7:17 Chifukwa Mwanawankhosa awkukhala pakati pa mpando wa chifumu adzawadyetsa, nadzawatsogolera ku akasupe amadzi amoyo: ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.



8

Rev 8:1 Ndipo pamene adatsegula chosindikizira chachisanu ndi chiwiri, mudakhala chete m’Mwamba monga kwa nthawi ya ola latheka.

Rev 8:2 Ndipo ndidawona angelo asanu ndi awiri amene adayimilira pamso pa Mulungu; ndipo adawapatsa malipenga asanu ndi awiri.

Rev 8:3 Ndipo adadza m’ngelo wina, nayima pa guwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolidi; ndipo adampatsa zofukiza zambiri, kuti aziyike pamodzi ndi mapemphero a woyera mtima onse pamwamba pa guwa la nsembe lagolidi, lokhala ku mpando wachifumu.

Rev 8:4 Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a woyera mtima udakwera kutuluka m’dzanja la m’ngelo, pamaso pa Mulungu.

Rev 8:5 Ndipo m’ngeloyo adatenga mbale ya zofukiza, nayidzaza ndi moto wopala pa guwa la nsembe nauponya padziko lapansi; ndipo padakhala mabingu, ndi mawu, ndi mphezi, ndi zibvomerezi.

Rev 8:6 Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nawo malipenga asanu ndi awiri adadzikonzekeretsa kuti awombe.

Rev 8:7 Ndipo m’ngelo woyamba adawomba, ndipo padagwa matalala ndi moto, zosanganizikirana ndi mwazi, ndipo adaziponya pa dziko lapansi: ndipo limodzi la magawo atatu la mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera.

Rev 8:8 Ndipo m’ngelo wachiwiri adawomba, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto lidaponyedwa m’nyanja: ndipo limodzi la magawo atatu la nyanja lidasanduka mwazi;

Rev 8:9 Ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zidali m’nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu la zombo lidawonongeka.

Rev 8:10 Ndipo m’ngelo wachitatu adawomba, ndipo idagwa kuchokera Kumwamba nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muwuni, ndipo idagwa pa limodzi ndi magawo atatu la mitsinje, la pa akasupe a madzi;

Rev 8:11 Ndipo dzina lake la nyenyeziyo alitcha chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu la madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti adasanduka wowawa.

Rev 8:12 Ndipo m’ngelo wachinayi adawomba, ndipo limodzi la magawo atatu la dzuwa lidamenyedwa, ndi limodzi la magawo atatu la mwezi ndi limodzi lamagawo atatu la nyenyezi; kuti limodzi la magawo awo atatu linadetsedwa, ndi ndipo limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usikunso chimodzimodzi.

Rev 8:13 Ndipo ndidawona, ndipo ndidamva m’ngelo akuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mawu akulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mawu wotsala a lipenga la angelo atatu asadawombe amene ayeneranso kuti awombe.



9

Rev 9:1 Ndipo m’ngelo wachisanu adawomba, ndipo ndidawona nyenyezi yochokera Kumwamba idagwa padziko; ndipo adampatsa iye chifunguliro cha dzenje la kupompho.

Rev 9:2 Ndipo adatsegula pa dzenje la pompho; ndipo udakwera utsi wotuluka m’dzenjemo, ngati utsi wa ng’anjo yayikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsiwo wa kudzenjewo.

Rev 9:3 Ndipo mu utsimo wa kudzenjewo mudatuluka dzombe padziko: ndipo adalipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko lapansi zirinayo mphamvu.

Rev 9:4 Ndipo adalilamulira ilo kuti lisayipse udzu wa padziko kapena chobiriwira chiri chonse, kapena mtengo uli wonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pawo ndiwo.

Rev 9:5 Ndipo kwa ilo adalipatsa mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe awo adali ngati mazunzidwe a chinkhanira, pamene chiluma munthu.

Rev 9:6 Ndipo m’masiku amenewo, anthu adzafunafuna imfa ndipo sadzayipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.

Rev 9:7 Ndipo mawonekedwe adzombelo adafanana ndi akavalo wokonzekera kukachita nkhondo; ndi pamitu pawo ngati a Korona wonga a golidi, ndi pankhope pawo ngati nkhope za anthu.

Rev 9:8 Ndipo adali nalo tsitsi longa tsitsi la akazi, ndipo mano awo adali ngati mano a mikango.

Rev 9:9 Ndipo adali nazo zikopa zapachifuwa ngati zikopa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko awo ngati mkokomo wa magareta, wa a kavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.

Rev 9:10 Ndipo lidali ndi michira yofanana ndi ya chinkhanira, ndipo mudali mbola m’michira yawo: ndipo mphamvu yawo yidali yakuyipsa anthu miyezi isanu.

Rev 9:11 Ndipo lidali nayo Mfumu yakulilamulira, ndiye m’ngelo wa pompho; dzina lake m’chihebri Abadoni, ndi m’chihelene ali nalo dzina Apoliyoni.

Rev 9:12 Tsoka loyamba lapita, ndipo tawonani, akudzanso matsoka awiri m’tsogolomo.

Rev 9:13 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chimodzi adawomba, ndipo ndidamva mawu wochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolidi liri pamaso pa Mulungu,

Rev 9:14 Nanena kwa m’ngelo wachisanu ndi chimmodzi wakukhala ndi lipenga, masula angelo anayi womangidwa pa mtsinje wa ukulu wa Firate.

Rev 9:15 Ndipo adamasulidwa angelo anayi, wokonzeka kufikira ola ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu la anthu.

Rev 9:16 Ndipo chiwerengero cha a nkhondo cha apakavalo ndicho zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi; ndipo ndidamva chiwerengero cha iwo,

Rev 9:17 Ndipo kotero ndidawona akavalo m’masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa zapachifuwa za moto, juwakinto ndi sulfure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo mkamwa mwawo mudatuluka moto ndi utsi ndi sulfure.

Rev 9:18 Ndi miliri imeneyi lidaphedwa limodzi la magawo atatu wa anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulfure, zotuluka m’kamwa mwawo.

Rev 9:19 Pakuti mphamvu yawo ili m’kamwa mwawo, ndi m’michira yawo; pakuti michira yawo ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo ndi iyo ndiyo yimene ayipsa nayo:

Rev 9:20 Ndipo anthu wotsala wosaphedwa nayo miliriyo sadalapa ntchito ya manja awo, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolidi, ndi siliva ndi amkuwa, ndi amwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya kapena kumva, kapena kuyenda:

Rev 9:21 Ndipo sadalapa umbanda wawo, kapena nyanga zawo, kapena chiwerewere chawo, kapena umbala wawo.



10

Rev 10:1 Ndipo ndidawona m’ngelo wina wamphamvu alikutsika Kumwamba, wobvala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto:

Rev 10:2 Ndipo adali nako m’dzanja lake kabuku kofunyulula: ndipo adaponda nalo phazi lake lamanja panyanja ndi lamanzere lake pa mtunda.

Rev 10:3 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, monga ngati mkango wubangula: ndipo pamene adafuwula mabingu asanu ndi awiri adayankhula mawu awo.

Rev 10:4 Ndipo pamene adayankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndidati ndilembe; ndipo ndidamva mawu wochokera Kumwamba nanena kwa ine, sindikiza nacho chizindikiro zinthu zimene adayankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe.

Rev 10:5 Ndipo m’ngelo amene ndidamuwona alikuyimilira pa nyanja ndi pa mtunda, adakweza dzanja lake lamanja kuloza Kumwamba,

Rev 10:6 Nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo ku nthawi za nthawi, amene adalenga m’Mwamba ndi zinthu ziri momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu ziri momwemo, ndi nyanja ndi zinthu ziri momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:

Rev 10:7 Komatu m’masiku amawu a m’ngelo wachisanu ndi chiwiri m’mene iye adzayamba kuwomba, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga adachinena kwa atumiki ake aneneri.

Rev 10:8 Ndipo mawu ndidawamva wochokera Kumwamba, adayankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku laling’ono lofunyululalo m’dzanja la m’ngelo wakuyimilira panyanja ndi padziko.

Rev 10:9 Ndipo ndidapita kwa m’ngelo, ndi kunena naye, ndipatse kabukuko. Ndipo adanena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m’mimba mwako, komatu m’kamwa mwako kadzazuna ngati uchi.

Rev 10:10 Ndipo ndidatenga kabuku m’dzanja la m’ngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kadali m’kamwa mwanga kozuna ngati uchi: ndipo pamene ndinakadya m’mimba mwanga mudawawa.

Rev 10:11 Ndipo adati kwa ine, uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.



11

Rev 11:1 Ndipo adandipatsa ine bango ngati ndodo: ndipo m’ngelo adayimirira, wakunena kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.

Rev 11:2 Ndipo bwalo lakunja kwa kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti lapatsidwa ilo kwa amitundu: ndipo mzinda wopatulika adzawupondereza miyezi makumi anayi mphambu iwiri.

Rev 11:3 Ndipo ndidzapatsa mphamvu mboni zanga ziwiri zonenera miyezi makumi anayi ndi iwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zitabvala chiguduli.

Rev 11:4 Izi ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoyikapo nyali ziwiri zakuyima pamaso pa Mulungu wa dziko lapansi.

Rev 11:5 Ndipo munthu wina akafuna kuyipsa izo, moto utuluka m’kamwa mwawo, nuwononga adani awo; ndipo wina akafuna kuyipsa izo, maphedwe ake ayenera kukhala wotero.

Rev 11:6 Izi ziri nawo ulamuliro wakutseka m’Mwamba, isagwe mvula masiku achinenero chawo: ndipo ulamuliro ziri nawo pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uli wonse nthawi ili yonse zifuna.

Rev 11:7 Ndipo pamene zidzatsiliza umboni wawo chirombo chokwera kutuluka m’pompho chidzachita nazo nkhondo, nichidzazilaka, nichidzazipha izo.

Rev 11:8 Ndipo mitembo yawo idzagona pa msewu wa mzinda waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, sodomu ndi Aigupto, umenenso Ambuye wathu adapachikidwa.

Rev 11:9 Ndipo mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe adzapenyera mitembo yawo masiku atatu ndi theka lake, ndipo sadzalola mitembo yawo iyikidwe m’manda.

Rev 11:10 Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwera pa iyo, nadzasekera, nadzatumizirana mphatso wina ndi mzake; chifukwa aneneri awa awiri adazunza iwo akukhala padziko lapansi.

Rev 11:11 Ndipo atapita masiku atatu ndi theka lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu udalowa mwa iwo, ndipo adayimirira chiliri; ndipo mantha akulu adawagwera iwo akuwapenya.

Rev 11:12 Ndipo adamva mawu akulu akuchokera Kumwamba akunena nawo, kwera kuno. Ndipo anakwera kumka Kumwamba; ndipo adani awo adawapenya.

Rev 11:13 Ndipo panthawi yomweyo padali chibvomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi la mzinda lidagwa; ndipo adaphedwa m’chibvomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri: ndipo wotsalawo adakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa Kumwamba.

Rev 11:14 Tsoka lachiwiri lachoka; ndipo tawonani, tsoka lachitatu lidza msanga.

Rev 11:15 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chiwiri adawomba, ndipo padakhala mawu akulu m’Mwamba, ndikunena, maufumu a dziko lapansi ayamba kukhala a Ambuye wathu, ndi a Khristu wake; ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.

Rev 11:16 Ndipo akulu makumi awiri mphambu anayi akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yawo, adagwa nkhope zawo pansi nalambira Mulungu.

Rev 11:17 Nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvu yonse, amene muli ndi mudali ndi mudzali popeza mwadzitengera mphamvu yanu yayikulu, ndipo mwachita ufumu.

Rev 11:18 Ndipo amitundu adakwiya, ndipo udadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakuti Inu mupereke mphotho kwa atumiki anu ndi aneneri, ndi woyera mtima, ndi iwo akuwopa dzina lanu, ang’ono ndi akulu; ndi kuwononga iwo amene adawononga dziko lapansi.

Rev 11:19 Ndipo adatsegulidwa kachisi wa Mulungu amene ali m’Mwamba; ndipo lidawoneka likasa la chipangano chake, m’kachisi mwake, ndipo padali mphezi, ndi mawu, ndi mabingu, ndi chibvomezi ndi matalala akulu.



12

Rev 12:1 Ndipo chodabwitsa chachikulu chidawoneka m’mwamba; mkazi wobvekedwa dzuwa ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake Korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri:

Rev 12:2 Ndipo adali ndi pakati; ndipo adafuwula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.

Rev 12:3 Ndipo chidawoneka chodabwitsa china m’mwamba, tawonani, chinjoka chofiyira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake akolona achifumu asanu ndi awiri.

Rev 12:4 Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu anyenyezi za kumwamba, nuziponya padziko lapansi. Ndipo chinjoka chidayimilira pamaso pa mkazi wakuti abale, kuti akabala, icho chikam’meze.

Rev 12:5 Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo adakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wachifumu wake.

Rev 12:6 Ndipo mkazi adathawira kuchipululu, kumene adali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

Rev 12:7 Ndipo mudali nkhondo m’mwamba: Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chidachita nkhondo,

Rev 12:8 Ndipo sichidalakika, ndipo sadapezekanso malo awo m’mwamba.

Rev 12:9 Ndipo chidaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana amene adanyenga dziko lonse lapansi: iye ada- ponyedwa pansi kudziko, ndi pamodzi ndi iye angelo ake.

Rev 12:10 Ndipo ndidamva mawu akulu m’Mwamba, nanena, Tsopano chafika chipulumutso ndi mphamvu, ndi ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake: pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.

Rev 12:11 Ndipo iwo adamlaka iye chifukwa cha mwazi wa Mwana wankhosa, ndi chifukwa cha mawu a umboni wawo; ndipo sadakonda moyo wawo ngakhale kufikira imfa.

Rev 12:12 Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu ndi inu akukhala momwemo, tsoka wokhala pa mtunda ndi a mnyanja! Chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi kochepa.

Rev 12:13 Ndipo pamene chinjoka chidawona kuti chidaponyedwa pansi padziko, chidazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna.

Rev 12:14 Ndipo adampatsa mkazi mapiko awiri achiwombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, kumbuto yake, kumene adyetsedwako kanthawi ndi nthawi, ndi theka lanthawi, wochotsedwa pa nkhope ya njoka.

Rev 12:15 Ndipo njokayo idalabvura mkamwa mwake madzi ngati chigumula, potsata mkazi, kuti akakokoloredwe mkazi nawo.

Rev 12:16 Ndipo dziko lidathandiza mkaziyo, pamene lidatsegula pakamwa pake, ndi kumeza madzi achigumula amene chinjoka chidalabvula m’kamwa mwake.

Rev 12:17 Ndipo chinjoka chidakwiya ndi mkazi, nichinachoka kumka kuchita nkhondo ndi otsala ambewu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu Khristu.



13

Rev 13:1 Ndipo ndidayimilira pa mchenga wa nyanja, ndipo ndidawona chirombo chakutuluka m’nyanja, chakukhala nayo mitu ndi iwiri, isanu ndi nyanga khumi ndi pamwamba pa nyanga zake akolona achifumu khumi, ndi pamitu yakeyo mayina a mwano.

Rev 13:2 Ndipo chirombo ndidachiwonacho chidafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi achimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chidampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.

Rev 13:3 Ndipo ndidawona umodzi wa mitu yake udakhala ngati udalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la ku imfa lidapola: ndipo dziko lonse lapansi lidazizwa potsata chirombocho.

Rev 13:4 Ndipo adalambira chinjoka, chimene chidachipatsa mphamvu chirombocho: ndipo adalambira chirombo ndi kunena, Afanana ndi chirombo ndani? Ndipo akhoza ndani kumenya nacho nkhondo?

Rev 13:5 Ndipo adachipatsa icho m’kamwa moyankhula zinthu zazikulu ndi zamwano; ndipo adachipatsa ulamuliro wakutero miyezi makumi anayi ndi iwiri

Rev 13:6 Ndipo chidatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala m’Mwamba.

Rev 13:7 Ndipo adachipatsa icho kuchita nkhondo ndi woyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo adachipatsa ulamuliro wa pafuko liri lonse, ndi malilime ndi manenedwe, ndi mitundu.

Rev 13:8 Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko lapansi, amene dzina lawo silidalembedwa m’buku la moyo la Mwana wankhosa wophedwa kuyambira kumaziko amakhazikitsidwe adziko lapansi.

Rev 13:9 Ngati munthu wina ali nalo khutu lakumva, amve.

Rev 13:10 Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka: munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiliro ndi chikhulupiriro cha woyera mtima.

Rev 13:11 Ndipo ndidawona chirombo china chirikutuluka pansi; ndipo chidali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wankhosa ndipo chidayankhula ngati chinjoka.

Rev 13:12 Ndipo chichita ulamuliro wonse wachirombo choyamba pamaso pake. Ndipo chichititsa dziko ndi iwo akukhala momwemo kuti alambire chirombo choyamba chimene bala lake lakuimfa lidapola.

Rev 13:13 Ndipo chichita zodabwitsa zazikulu, kutinso chitsitse moto uchokere m’mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.

Rev 13:14 Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko mwa machitidwe a zozizwitsa amene icho chidapatsidwa mphamvu yakuchita pamaso pa chirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chirombo, chimene chidali nalo bala la lupanga nichinakhalanso ndi moyo.

Rev 13:15 Ndipo chidali ndi mphamvu yakupatsa moyo fano la chirombo, kuti fano la chilombo liyankhule, nichipangitse kuti onse osalambira fano lachirombo aphedwe.

Rev 13:16 Ndipo chipangitsa kuti onse, ang’ono ndi akulu, achuma ndi wosauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire chilembo pa dzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.

Rev 13:17 Ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo, kapena dzina la chirombo, kapena chiwerengero cha dzina lake.

Rev 13:18 Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chirombocho: pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.



14

Rev 14:1 Ndipo ndidapenya, ndipo tawonani, Mwanawankhosayo alikuyimilira pa phiri la ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pawo.

Rev 14:2 Ndipo ndidamva mawu wochokera Kumwamba, ngati mau amkokomo wamadzi ambiri ndi ngati mawu a bingu lalikulu: ndipo mawu amene ndidawamva adakhala ngati a zeze akuyimba azeze awo:

Rev 14:3 Ndipo adayimba ngati nyimbo yatsopano ku mpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinayi, ndi akulu: ndipo palibe munthu adakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, wowomboledwa kuchokera kudziko lapansi.

Rev 14:4 Awa ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Awa ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kuli konse amukako. Iwowa adawomboledwa mwa anthu, amene ndiwo zipatso zowundukula za kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.

Rev 14:5 Ndipo m’kamwa mwawo simudapezeka chinyengo; popeza kuti ali wopanda chilema pamaso pampando wa Mulungu.

Rev 14:6 Ndipo ndidawona m’ngelo wina ali kuwuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko lapansi, kwa mtundu uli wonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.

Rev 14:7 Ndi kunena ndi mawu akulu, Wopani Mulungu, mpatseni ulemerero Iye; pakuti yafika nthawi yachiweruziro chake: ndipo mlambireni Iye amene adalenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe a madzi.

Rev 14:8 Ndipo adatsala m’ngelo wina, nanena, Wagwa, wagwa, Babulo mzinda waukulu wo umene udamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chiwerewere chake.

Rev 14:9 Ndipo adawatsata m’ngelo wina wachitatu, nanena ndi mawu akulu, Ngati wina alambira chirombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pa mphumi pake, kapena pa dzanja lake,

Rev 14:10 Iyenso adzamwako ku vinyo wa m’kwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m’chikho cha m’kwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi Sulfure, pamaso pa angelo woyera ndi pamaso pa Mwanawankhosa:

Rev 14:11 Ndipo utsi wa mazunzo awo ukwera ku nthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chirombocho ndi fano lake, ndi iye ali yense amene alandira chizindikiro cha dzina lake.

Rev 14:12 Pano pali chipiliro cha woyera mtima: cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.

Rev 14:13 Ndipo ndidamva mawu wochokera Kumwamba, ndikunena, kwa ine, Lemba, Wodala akufa amene akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; Inde, ananena, Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zawo; pakuti ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi.

Rev 14:14 Ndipo ndidapenya, tawonani, mtambo woyera, ndi pamtambopo padakhala wina monga Mwana wa munthu wakukhala naye Korona wa golidi pa mutu pake, ndi m’dzanja lake zenga lakuthwa.

Rev 14:15 Ndipo m’ngelo wina adatuluka m’kachisi, wofuwula ndi mawu akulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza zokolola za dziko zankhwima.

Rev 14:16 Ndipo Iye wokhala pamtambo adaponya zenga lake padziko, ndipo zokolola za dziko zidamwetedwa.

Rev 14:17 Ndipo m’ngelo wina adatuluka m’kachisi wokhala m’Mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso.

Rev 14:18 Ndipo m’ngelo wina adatuluka kuchokera paguwa la nsembe, ndiye wakukhala nayo mphamvu pamoto; nafuwula ndi mawu akulu kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m’dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu.

Rev 14:19 Ndipo m’ngelo adaponya zenga lake ku dziko nadula mphesa za m’munda wa ’dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.

Rev 14:20 Ndipo moponderanso mphesa adamupondera kunja kwa mzinda, ndipo mwazi udatuluka moponderamo mphesa, nufikira mpaka kuzomangira pakamwa za pa akavalo mpata wa mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.



15

Rev 15:1 Ndipo ndidawona chizindikiro china m’mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.

Rev 15:2 Ndipo ndidawona ngati nyanja yamandala yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene adachilaka chirombocho, ndi fano lake ndi chizindikiro chake ndi chiwerengero cha dzina lake, adayimilira pa nyanja ya mandala, akukhala nawo azeze a Mulungu.

Rev 15:3 Ndipo ayimba nyimbo ya Mose mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, ndikuti, ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu Wamphamvu zonse; njira zanu nzolungama ndi zowongoka. Mfumu Inu ya woyera mtima.

Rev 15:4 Ndani amene adzakhala wosawopa inu ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera: chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza ziweruziro zanu zawonetsedwa.

Rev 15:5 Ndipo zitatha izi ndidawona, ndipo tawonani, padatseguka pa kachisi wa chihema cha umboni m’Mwamba:

Rev 15:6 Ndipo adatuluka m’kachisi angelo asanu ndi awiri, akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atabvala chobvala choyera, ndi chonyezimira, namangira malamba agolidi pachifuwa pawo.

Rev 15:7 Ndipo chimodzi cha zamoyo zinayi chidapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolidi zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu, wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.

Rev 15:8 Ndipo kachisi adadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu adakhoza kulowa m’kachisi kufikira itakwaniritsidwa miliri isanu ndi awiri ya angelo asanu ndi iwiri.



16

Rev 16:1 Ndipo ndidamva mawu akulu wochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.

Rev 16:2 Ndipo adachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kudakhala chironda choyipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chirombo ndi pa iwo wolambira fano lake.

Rev 16:3 Ndipo m’ngelo wachiwiri adatsanulira mbale yake m’nyanja; ndipo kudakhala mwazi ngati wa munthu wakufa:ndipo zamoyo zonse za m’nyanja zidafa.

Rev 16:4 Ndipo m’ngelo wachitatu adatsanulira mbale yake ku mitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo adasanduka mwazi.

Rev 16:5 Ndipo ndidamva m’ngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, Ambuye amene muli, mudali, ndipo mudzakhala, chifukwa mudaweruza chotero.

Rev 16:6 Popeza adakhetsa mwazi wa woyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; pakuti ayenera iwo.

Rev 16:7 Ndipo ndidamva wina wa pa guwa la nsembe, alimkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvu yonse, chiweruziro chanu chiri chowona ndi cholungama.

Rev 16:8 Ndipo m’ngelo wachinayi, adatsanulira mbale yake padzuwa; ndipo mphamvu idapatsidwa kwa iye kuti atenthe anthu ndi moto.

Rev 16:9 Ndipo adatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo adachitirabe mwano dzina la Mulungu wokhala nayo mphamvu pa miliri iyi: ndipo sadalapa kuti akapatse Mulungu ulemerero.

Rev 16:10 Ndipo m’ngelo wa chisanu adatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chirombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa;ndipo adatafuna malilime awo chifukwa cha kuwawa.

Rev 16:11 Ndipo adachitira mwano Mulungu wa m’Mwamba chifukwa cha zowawa zawo ndi zironda zawo; ndipo sadalapa ntchito zawo.

Rev 16:12 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chimodzi adatsanulira mbale yake pa mtsinje waukulu wa Firate; ndipo madzi ake adaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu wochokera kummawa kotulukira dzuwa.

Rev 16:13 Ndipo ndidawona mizimu itatu yonyansa yokhala ngati achule ikutuluka m’kamwa mwa chinjoka ndi mkamwa mwa chirombo ndi mwa m’neneri wonyenga.

Rev 16:14 Pakuti ali mizimu ya ziwanda yakuchita zozizwitsa; imene ituluka kumka kwa mafumu akudziko ndi adziko lonse lapansi, kuwasonkhanitsira iwo ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvu yonse.

Rev 16:15 Tawonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zobvala zake, kuti angayende wamaliseke, nangapenye anthu manyazi ake.

Rev 16:16 Ndipo adawasonkhanitsira ku malo wotchedwa mchinenedwe cha m’chihebri Harmagedo.

Rev 16:17 Ndipo m’ngelo wachisanu ndi chiwiri adatsanyulira mbale yake mumlenga lenga; ndipo m’menemo mudatuluka mawu akulu wochokera kukachisi wakumwamba ,kuchokera kumpando wachifumu ndi kunena, Chachitika.

Rev 16:18 Ndipo padakhala mphezi, ndi mawu, ndi mabingu; ndi kung’anima, ndi chibvomezi chachikulu chotero chonga sichidawonekepo chiyambire anthu padziko, chibvomezi champhamvu chotero, ndipo ndichachikulu ndithu.

Rev 16:19 Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndipo mizinda ya amitundu idagwa; ndipo Babulo waukulu udakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake

Rev 16:20 Ndipo zilumba zonse zidathawa, ndipo mapiri sadapezeke.

Rev 16:21 Ndipo pamenepo adagwa pa anthu matalala akulu wochokera Kumwamba, ndipo mwala wa talala, liri lonse wolemera ngati talenti: ndipo anthu adachitira Mulungu mwano chifukwa cha muliri wa matalala, pakuti muliri wake udali waukulu ndithu.



17

Rev 17:1 Ndipo anadza m’modzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nayankhula ndi ine, nanena, idza kuno, ndidzakuwonetsa chiweruziro cha mkazi wa chigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri.

Rev 17:2 Amene mafumu adziko adachita chiwerewere naye, ndipo iwo akukhala padziko adaledzera ndi vinyo wa chiwerewere chake:

Rev 17:3 Ndipo adanditenga kunka nane kuchipululu, mu mzimu: ndipo ndidawona mkazi alinkukhala pa chirombo chamawangamawanga chofiritsa, chodzala ndi mayina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

Rev 17:4 Ndipo mkazi adabvala chobvala cha nsalu ya pepu ya mtundu wofiyiritsa, nakometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale, nakhala nacho m’dzanja lake chikho chagolidi chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chiwerewere chake:

Rev 17:5 Ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina CHINSINSI, BABULO WAUKULU, AMAYI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO LAPANSI.

Rev 17:6 Ndipo ndidawona mkazi woledzera ndi mwazi wa woyera mtima, ndi mwazi wa wophedwa a Yesu: ndipo ndidazizwa pakuwona iye ndikuzizwa kwakukulu.

Rev 17:7 Ndipo m’ngelo adati kwa ine, uzizwa chifukwa chiyani? Ine ndidzakuwuza iwe chinsinsi cha mkazi, ndi cha chirombo chakum’tenga iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

Rev 17:8 Ndipo chirombo chimene udachiwona chidaliko, koma kulibe; chidzatuluka m’pompho, ndi kumka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala pa dziko amene dzina lawo silidalembedwe m’buku la moyo chiyambire maziko a makhazikitsidwe adziko lapansi, pakuwona chirombo, kuti chidaliko, koma kulibe, ndipo chidzakhalako.

Rev 17:9 Pano pali mtima wakukhala nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalako.

Rev 17:10 Ndipo ali mafumu asanu ndi awiri: asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siyinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi kochepa.

Rev 17:11 Ndipo chirombo chimene chidaliko, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chiri mwa zisanu ndi ziwirizo, nichimuka kuchitayiko.

Rev 17:12 Ndipo nyanga khumi uziwona ndiwo mafumu khumi, amene sadalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu kwa ola limodzi pamodzi ndi chirombo.

Rev 17:13 Iwo ali nawo mtima umodzi, ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa chirombo.

Rev 17:14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka: chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu: ndi iwo akukhala naye, woyitanidwa, ndi wosankhidwa ndi wokhulupirika.

Rev 17:15 Ndipo adanena kwa ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.

Rev 17:16 Ndipo nyanga khumi udaziwona, pachirombocho, izi zidzadana ndi mkazi wa chigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wamaliseke, nizidzadya nyama yake, nizidzamuwotcha iye ndi moto.

Rev 17:17 Pakuti Mulungu adayika kumtima kwawo kukakwaniritsa za chifuniro chake ndikuchita za mtima umodzi ndi kupereka ufumu wawo kwa chirombo kufikira akwaniritsidwa mawu a Mulungu.

Rev 17:18 Ndipo mkaziyo udamuwona ndiye mzinda waukuluwo umene uchita ufumu pa mafumu a dziko lapansi.



18

Rev 18:1 Zitatha zinthu izi ndidawona m’ngelo wina wotsika pansi kuchokera Kumwamba wakukhala nawo ulamuliro waukulu; ndipo dziko lidaunikidwa ndi ulemerero wake.

Rev 18:2 Ndipo adafuwula ndi mawu wolimba, nanena, Wagwa, wagwa Babulo waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.

Rev 18:3 Chifukwa ndi kuledzera kwa vinyo wa mkwiyo wa chiwerewere chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu adziko adachita naye chiwerewere; ndipo wochita malonda adziko adalemera ndi mphamvu yakudyerera kwake.

Rev 18:4 Ndipo ndidamva mawu ena wochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;

Rev 18:5 Pakuti machimo ake adaunjikizana kufikira, m’Mwamba, ndipo Mulungu adakumbukira zosalungama zake.

Rev 18:6 Kumbwezera iye mphotho, monganso iyeyu adakubwezerani inu, ndipo mumuwirikizire ndi kumuwirikizira mobwereza, monga mwa ntchito zake; m’chikhomo adathiramo, mumuthirire chowirikiza.

Rev 18:7 Monga momwe adadzichitira iye ulemu, nadyerera, momwemo mumchitire chomuzunza ndi chomuliritsa maliro: pakuti adanena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosawona maliro konse ine.

Rev 18:8 Chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo adzapserera ndi moto: chifukwa Ambuye Mulungu wakumuweruza iye ndiye wolimba.

Rev 18:9 Ndipo mafumu a dziko wochita chiwerewere nadyerera naye, adzamlira iye nadzamlira maliro pamene adzawona utsi wakutentha kwake,

Rev 18:10 Poyima patali chifukwa chakuwopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babulo, mzinda wolimba! Pakuti mu ola limodzi chafika chiweruziro chako.

Rev 18:11 Ndipo wochita malonda am’dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ake:

Rev 18:12 Malonda a golidi, ndi siliva, ndi amwala wa mtengo wake, ndi a ngale ndi a nsalu ya bafuta, ndi ya pepu, ndi yonyezimira, ndi yofirira ya mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi zotengera ziri zonse za mtengo wake wapatali, ndi mkuwa ndi zachitsulo, ndi za nsangalabwi,

Rev 18:13 Ndi Kinamoni ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng’ombe, ndi nkhosa, ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a akapolo ndi miyoyo ya anthu.

Rev 18:14 Ndipo zipatso zimene moyo wako udazilakalaka zidakuchokera, ndipo zones zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzapezanso konse.

Rev 18:15 Wogulitsa zinthu izi, amene adalemera nazo, adzayima patali chifukwa cha mantha a chizunzo chake, nadzalira, ndi kuchita chifundo,

Rev 18:16 Nadzanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukulu wobvala bafuta ndi nsalu ya pepu ya mlangali wofiyiritsa wabwino, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale!

Rev 18:17 Pakuti mu ola limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere. Ndipo eni zombo, aliwonse, ndi wonse wopanga zombo, ndi onse akuchita malonda a panyanja, ndi amalinyero adayima patali,

Rev 18:18 Ndipo adalira ndi kufuwula powona utsi wa kutentha kwake, nanena, mzinda uti uwu ufanana ndi mzinda waukuluwo?

Rev 18:19 Ndipo adathira fumbi pamitu pawo, nafuwula ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka,mzinda waukuluwo, umene udalemera nawo onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa mwa kulemera kwake pa ola limodzi wasanduka bwinja.

Rev 18:20 Kondwera pa iye, m’mwamba iwe, ndi woyera mtima, ndi a tumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu wabwezerera inu pa iye.

Rev 18:21 Ndipo m’ngelo wolimba adanyamula mwala, ngati mphero yayikulu, nayiponya m’nyanja, nanena, chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.

Rev 18:22 Ndipo mawu wa anthu woyimba zeze, ndi a woyimba, ndi a woliza zitoliro, ndi a woomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo munthu waluso ndi luso lina lirilonse lokhalamo silidzapezekanso mwa iwe; ndi kulira kwa mwala wa mphero, sikudzamvekanso konse mwa iwe.

Rev 18:23 Ndipo kuwunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mawu amkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti wotsatsa malonda anu adali anthu womveka am’dziko; pakuti ndi nyanga za ufiti wako, mitundu yonse idasocheretsedwa.

Rev 18:24 Ndipo mwa iye mudapezeka mwazi wa aneneri ndi woyera mtima, ndi onse amene adaphedwa padziko lapansi.



19

Rev 19:1 Zitatha zinthu izi ndidamva ngati mawu akulu akhamu lalikulu m’Mwamba, liri kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi ulemu ndi mphamvu, zikhale kwa Ambuye Mulungu wathu:

Rev 19:2 Pakuti maweruzo ake ali wowona ndi wolungama: ndipo adaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene adayipsa dziko lapansi ndi chiwerewere chake, ndipo anambwezera chilango chifukwa cha mwazi wa atumiki ake pa dzanja la mkaziyo.

Rev 19:3 Ndipo adatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera ku nthawi za nthawi.

Rev 19:4 Ndipo adagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anayi ndi zamoyo zinayi, ndipo zidalambira Mulungu wakukhala pa mpando wa chifumu, nizinena, Ameni; Aleluya.

Rev 19:5 Ndipo mawu adachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, lemekezani Mulungu wathu atumiki ake, inu ndi inu nonse, akumuwopa Iye, ang’ono ndi akulu.

Rev 19:6 Ndipo ndidamva akukhala ngati mawu a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mawu a mabingu wolimba, nizinena, Aleluya: pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvu zonse.

Rev 19:7 Tiyeni tikondwere, tisekere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa: ndipo mkazi wake wadzikonzekeretsa.

Rev 19:8 Ndipo adampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu: pakuti bafuta ndiye zolungama za woyera mtima.

Rev 19:9 Ndipo adanena ndi ine, Lemba, wodala iwo amene ayitanidwa ku phwando lam’gonero la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo adanena ndi ine, awa ndiwo maneno owona a Mulungu.

Rev 19:10 Ndipo ndidagwa pamapazi ake kumlambira iye. Ndipo adanena ndi ine, tapenya, usatero; ine ndine mtumiki mzako, ndi mzawo wa abale ako akukhala nawo umboni wa Yesu: lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.

Rev 19:11 Ndipo ndidawona mutatseguka m’Mwamba; ndipo tawonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Wowona; ndipo mchilungamo Iye aweruza, nachita nkhondo.

Rev 19:12 Maso ake ali ngati lawi la moto, ndipo pamutu pake padali akolona a chifumu ambiri; ndipo adali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina aliyense koma Iye yekha.

Rev 19:13 Ndipo adabvekedwa ndichobvala choviyikidwa m’mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mawu a Mulungu.

Rev 19:14 Ndipo magulu a nkhondo wokhala m’Mwamba adamtsata Iye, wokwera pa akavalo woyera, wobvala bafuta woyera woti mbuu.

Rev 19:15 Ndipo m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu: ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo ya chitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo wa ukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvu yonse.

Rev 19:16 Ndipo ali nalo pa chobvala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.

Rev 19:17 Ndipo ndidawona m’ngelo alikuyima m’dzuwa; ndipo adafuwula ndi mawu akulu akunena ndi mbalame zonse zakuwuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani ku phwando la m’gonero la Mulungu wamkulu;

Rev 19:18 Kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitawo, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi nyama ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi ang’ono ndi akulu.

Rev 19:19 Ndipo ndidawona chirombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo awo, wosonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.

Rev 19:20 Ndipo chidagwidwa chirombocho, ndi pamodzi ndi m’neneri wonyenga amene adachita zozwizwitsa, pamaso pake, zimene adasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chirombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri adaponyedwa ali ndi moyo m’nyanja yamoto yakutentha ndi Sulfure.

Rev 19:21 Ndipo wotsalawa adaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lochokera kutuluka m’kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zidakhuta ndi nyama zawo.



20

Rev 20:1 Ndipo ndidawona m’ngelo adatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha pompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.

Rev 20:2 Ndipo adagwira chinjoka, njoka yokalamba yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi.

Rev 20:3 Namponya kupompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso a mitundu kufikira kukwaniritsidwa kwa zaka chikwi; patatha izi adzayenera kumasulidwa iye kanthawi.

Rev 20:4 Ndipo ndidawona mipando ya chifumu, ndi iwo akukhala pamenepo; ndipo adawapatsa chiweruziro; ndipo ndidawona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi iwo amene sadalambira chirombo, kapena fano lake, nisadalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lawo; ndipo adakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.

Rev 20:5 Koma wotsala wa akufa sadakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi.Uku ndiko kuwuka koyamba.

Rev 20:6 Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuwuka koyamba: pa iwowa imfa yachiwiri ilibe mphamvu; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.

Rev 20:7 Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, Satana adzamasulidwa m’ndende yake;

Rev 20:8 Ndipo adzatuluka kukanyenga amitundu ali mu ngodya zinayi za dziko lapansi, gogi ndi magogi, kudzawasonkhanitsa kuti achite nkhondo: chiwerengero chawo cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja.

Rev 20:9 Ndipo adakwera nafalikira m’dziko, nazinga msasa wa woyera mtima ndi mzinda wa wokondedwawo; ndipo udatsika moto wochokera kumwamba nuwanyeketsa.

Rev 20:10 Ndipo mdierekezi wakusocheretsa iwo adaponyedwa m’nyanja ya moto ndi Sulfure, kumeneko kulinso chirombocho ndi m’neneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.

Rev 20:11 Ndipo ndidawona mpando wa chifumu wa ukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m’Mwamba zidathawa pamaso pake, ndipo sadapezeka malo awo.

Rev 20:12 Ndipo ndidawona akufa, akulu ndi ang’ono alimkuyima pamaso pa Mulungu; ndipo mabuku adatsegulidwa; ndipo buku lina lidatsegulidwa, ndilo buku la moyo: ndipo akufa adaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabuku, monga mwa ntchito zawo.

Rev 20:13 Ndipo nyanja idapereka akufawo adali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zidapereka akufawo adali m’menemo: ndipo adaweruzidwa munthu ali yense monga mwa ntchito zake.

Rev 20:14 Ndipo imfa ndi Hade zidaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.

Rev 20:15 Ndipo ngati munthu aliyense sadapezedwa wolembedwa m’buku la moyo, adaponyedwa m’nyanja ya moto.



21

Rev 21:1 Ndipo ndidawona m’mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko lapansi loyamba zidachoka, ndipo kunalibenso nyanja.

Rev 21:2 Ndipo ine Yohane ndidawona mzinda woyerawo, Yerusaremu watsopano, wotsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu, wokonzedwa ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.

Rev 21:3 Ndipo ndidamva mawu akulu wochokera Kumwamba, ndi kunena, Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndipo Mulungu mwiniyekha adzakhala Mulungu wawo.

Rev 21:4 Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse kuyichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; kapena chisoni kapena maliro; ndipo sipadzakhalanso chowawitsa pamenepo; zoyambazo zapita.

Rev 21:5 Ndipo Iye wakukhala pa mpando wa chifumu adati, Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo adati kwa ine, Talemba; pakuti mawu awa ali wokhulupirika ndi wowona.

Rev 21:6 Ndipo adati kwa ine, zachitika. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe ku kasupe wa madzi a moyo kwa ulere.

Rev 21:7 Iye wakulakika adzalandira zinthu zonse; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndipo iye adzakhala mwana wanga.

Rev 21:8 Koma amantha, ndi wosakhulupirika, ndi wonyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi anyanga ndi wolambira mafano, ndi onse abodza, cholandira chawo chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndi Sulfure; ndiyo imfa yachiwiri.

Rev 21:9 Ndipo anadza m’modzi kwa ine wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo adayankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuwonetsa iwe mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.

Rev 21:10 Ndipo adanditenga mu mzimu kumka ku phiri lalikulu ndi lalitali, nandiwonetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu woyera, wotsika m’Mwamba kuchokera kwa Mulungu,

Rev 21:11 Wokhala nawo ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kudafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati Krustalo;

Rev 21:12 Ndipo udakhala nalo linga lalikulu ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pa zipata angelo khumi ndi awiri, ndi mayina wolembedwapo, ndiwo mayina a mafuko khumi ndi awiri wa ana a Israyeli.

Rev 21:13 Kum’mawa zipata zitatu; ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwera zipata zitatu ndi kumadzulo zipata zitatu.

Rev 21:14 Ndipo linga la mudziwo lidakhala nawo maziko khumi ndi awiri, ndi mmenemo mayina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.

Rev 21:15 Ndipo iye wakuyankhula ndi ine adali nawo muyeso, bango lagolidi, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake ndi linga lake.

Rev 21:16 Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa ngodya zonse; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake; ndipo adayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri, utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana.

Rev 21:17 Ndipo adayesa linga lake, mikono zana mphambu makumi anayi kudza zinayi, muyeso wa munthu, ndiye m’ngelo.

Rev 21:18 Ndipo milimo ya linga lake ndiye yaspi: ndipo mzindawo ngwagolidi woyengeka, wofanana ndi mandala woyera wowonekera bwino.

Rev 21:19 Ndipo maziko a linga la mzindawo adakometsedwa ndi miyala ya mtengo wapatali ya mitundu mitundu; maziko woyamba, ndi yaspi, achiwiri, ndi safiro; achitatu, ndi kalikedo; achinayi, ndi emaraldo;

Rev 21:20 Achisanu ndi sardoni; achisanu ndi chimodzi ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri ndi krusolito; achisanu ndi chitatu ndi berulo; achisanu ndi chinayi ndi topaziyo; akhumi ndi krusoprazo; khumi ndi chimodzi ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri ndi ametusto

Rev 21:21 Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chiri chonse pachokha cha ngale imodzi. Ndipo msewu wa mzinda ndi wagolidi woyengeka, ngati mandala wowonekera bwino.

Rev 21:22 Ndipo sindidawona kachisi mmenemo: pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvu yonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo kachisi wake.

Rev 21:23 Ndipo pamzindapo panalibe dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uwunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.

Rev 21:24 Ndipo mitundu ya iwo wopulumutsidwa adzayendayenda mwa kuwunika kwake: ndipo mafumu a dziko lapansi atenga ulemerero ndi ulemu wawo kulowa nawo momwemo.

Rev 21:25 Ndipo pazipata zake sipadzatsekedwa konse usana: pakuti sikudzakhala usiku komweko.

Rev 21:26 Ndipo adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nawo momwemo.

Rev 21:27 Ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kodetsedwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza: koma iwo wokhawo wolembedwa m’buku la moyo la Mwanawankhosa.



22

Rev 22:1 Ndipo adandiwonetsa mtsinje wangwiro wa madzi a moyo, wonyezimira ngati Krustalo, wotuluka ku mpando wa chifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.

Rev 22:2 Pakati pa msewu wake, ndi tsidya lirilonse la mtsinje, ndi tsidya lija padali pamenepo mtengo wa moyo, wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi: ndipo masamba amtengo ndiwo akuchiritsa nawo mafuko.

Rev 22:3 Ndipo sipadzakhalanso temberero liri lonse; koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo atumiki ake adzamtumikira Iye.

Rev 22:4 Ndipo adzawona nkhope yake; ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo.

Rev 22:5 Ndipo sikudzakhalanso usiku kumeneko; ndipo sikufunika kuwunika kwa nyali, ngakhale kuwunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawunikira umenewu: ndipo adzachita ufumu ku nthawi zanthawi.

Rev 22:6 Ndipo adati kwa ine, Mawu awa ali wokhulupirika ndi woona: ndipo Ambuye Mulungu wa aneneri woyera adatuma m’ngelo wake kuwonetsera atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika msanga.

Rev 22:7 Tawona, Ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mawu achinenero cha buku ili.

Rev 22:8 Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya zinthu izi. Ndipo pamene ndidamva ndi kupenya ndinagwa pansi kulambira pa mapazi am’ngelo wakundiwonetsa zinthu izi.

Rev 22:9 Ndipo adanena iye ndi ine, Tapenya, usachite chotero: ine ndine mtumiki mzako, ndi mzawo wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga zonenera za buku ili: lambira Mulungu.

Rev 22:10 Ndipo adanena ndi ine, kuti, Usasindikiza chizindikiro mawu awa achinenero cha buku ili: pakuti nthawi yayandikira.

Rev 22:11 Iye wakukhala wosalungama, akhale wosalungama: ndi iye wonyansa akhale wonyansa: ndi iye wakukhala wolungama akhale wolungama; ndi iye amene ali woyera akhale woyera.

Rev 22:12 Ndipo, Tawonani, ndidza msanga: ndipo mphotho yanga ndiri nayo yakupatsa munthu aliyense monga mwa ntchito yake.

Rev 22:13 Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza chiyambi ndi chitsiriziro.

Rev 22:14 Wodala iwo amene achita malamulo ake, kuti akakhale nawo ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe mu mzinda pa zipata.

Rev 22:15 Pakuti kunja kuli agalu, ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi wopembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.

Rev 22:16 Ine Yesu ndatuma m’ngelo wanga kukakuchitirani inu umboni wa zinthu izi m’Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda ya m’bandakucha.

Rev 22:17 Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idza. Ndipo iye wakumva ludzu adze; ndipo aliyense wofuna, muloleni atenge madzi a moyo kwaulere.

Rev 22:18 Pakuti ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mawu achinenero cha buku ili, ngati munthu adzawonjezera pa zinthu izi, Mulungu adzamuwonjezera iye miliri yolembedwa m’bukumu:

Rev 22:19 Ndipo ngati munthu ali yense adzachotsako pa mawu a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi mu mzinda woyerawo, ndi pa zinthu izi zilembedwa m’bukumu.

Rev 22:20 Iye amene akuchitira umboni zinthu izi, anena, Indetu; ndidza msanga Ameni; inde,idzani, Ambuye Yesu.

Rev 22:21 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE