Philippians


1

Php 1:1 Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa woyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi woyang’anira ndi atumiki:

Php 1:2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi zochokera kwa Ambuye Yesu Khristu.

Php 1:3 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu nonse.

Php 1:4 Nthawi zonse m’pembedzero langa la kwa inu nonse ndichita ndipemphera mokondwera.

Php 1:5 Chifukwa cha chiyanjano chanu mu Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

Php 1:6 Pokhala wotsimikizika, kuti Iye amene adayamba mwa inu ntchito yabwino, adzayitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu:

Php 1:7 Monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndiri nako mu mtima mwanga, kuti inu m’zomangira zanga, ndipo m’chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli woyanjana nane chisomo changa.

Php 1:8 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m’chikondi cha mwa Khristu Yesu.

Php 1:9 Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezeke, m’chidziwitso, ndi kuzindikira konse;

Php 1:10 Kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima wowona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu;

Php 1:11 Wodzala nacho chipatso chachilungamo, chimene chiri ,mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

Php 1:12 Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zinthu zija za ine zidachitika makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;

Php 1:13 Kotero kuti zomangira zanga zidawonekera mwa Khristu m`nyumba ya chifumu ndi malo ena onse;

Php 1:14 Ndi kuti ambiri mwa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m’zomangira zanga, alimbika mtima koposa kuyankhula mawu a Mulungu wopanda mantha.

Php 1:15 Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndewu; koma enanso chifukwa cha kukoma.

Php 1:16 Koma ena alalikira Khristu mochokera m’chotetana, kosati kowona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m’zomangira zanga.

Php 1:17 Ena atero ndi chikondi, podziwa kuti ndidayikidwa kuti ndikateteze Uthenga Wabwino;

Php 1:18 Nchiyani kodi? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m’chowonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m’menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

Php 1:19 Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu,

Php 1:20 Monga mwakulingiliritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m’thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.

Php 1:21 Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula.

Php 1:22 Koma ngati kukhala ndi moyo m’thupi, ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha;

Php 1:23 Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho chokhumba cha kuchoka kukakhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposa posatu:

Php 1:24 Koma kukhalabe m’thupi ndiko kufunika koposa, chifukwa cha inu.

Php 1:25 Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuwonjezera chimwemwe cha chikhulupiriro chanu;

Php 1:26 Kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke mwa Yesu Khristu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.

Php 1:27 Chokhachi, mayendedwe anu ayenera Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndiri mkudza ndi kuwona inu, ndingakhale nditi ndiri kwina, ndikamva zakwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino.

Php 1:28 Wosawopa adani m’kanthu konse, chimene chiri kwa iwowa chisonyezo cha chiwonongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

Php 1:29 Kuti kwapatsidwa kwa inu kwa ufulu chifukwa cha Khristu, siku khulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha lye;

Php 1:30 Ndikukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiwona mwa ine, nimukumva tsopano chiri mwa ine.



2

Php 2:1 Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati chikondi, ndi chisoni,

Php 2:2 Kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chofanana, amoyo umodzi, wolingalira mtima umodzi,

Php 2:3 Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndikudzichepetsa mtima yense ayese mzake womposa iye mwini.

Php 2:4 Munthu aliyense asapenyerere zinthu zake za iye yekha, koma aliyense apenyererenso za mzake.

Php 2:5 Mukhale nawo mtima mkati mwanu umene udalinso mwa Khristu Yesu:

Php 2:6 Ameneyo pokhala nawo mawonekedwe a Mulungu, sadachiyesa cholanda kukhala wofanana ndi Mulungu:

Php 2:7 Koma adadzikhuthula yekha, natenga mawonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu:

Php 2:8 Ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, adadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

Php 2:9 Mwa ichinso Mulungu adamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa mayina onse:

Php 2:10 Kuti m’dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko;

Php 2:11 Ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Php 2:12 Potero, wokondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano ine palibe, gwirani ntchito ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.

Php 2:13 Pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.

Php 2:14 Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani.

Php 2:15 Kuti mukakhale wopanda chilema ndi wowona, ana a Mulungu wopanda chilema pakati pa mbadwo wokhokhota ndi wopotoka, mwa iwo amene monga nyali m’dziko lapansi.

Php 2:16 Akuwonetsera mawu a moyo; kuti ine ndikakhale wachimwemwe nawo m’tsiku la Khristu, kuti sindidathamanga chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.

Php 2:17 Inde komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse.

Php 2:18 Momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

Php 2:19 Koma ndikhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.

Php 2:20 Pakuti ndiribe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima wowona.

Php 2:21 Pakuti onsewa atsata za iwo wokha, si zinthu za Yesu Khristu.

Php 2:22 Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, adatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.

Php 2:23 Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posachedwa m’mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani.

Php 2:24 Koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidza msanga.

Php 2:25 Koma ndidayesa nkufunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mzanga, ndi msilikali mzanga, ndiye mthenga wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa.

Php 2:26 Popeza adali wolakalaka inu nonse, nabvutika mtima chifukwa mudamva kuti adadwala.

Php 2:27 Pakutinso adadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu adamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chowonjezera pa chisomo.

Php 2:28 Chifukwa chake ndamtuma iye chifulumizire, kuti pakumuwona mukakondwerenso, ndi inenso, chindichepere chisoni.

Php 2:29 Chifukwa chake mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu woterewa:

Php 2:30 Pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu adafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa ine.



3

Php 3:1 Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundibvuta ine, koma kwa inu ndi chitetezo kukhazikitsa.

Php 3:2 Chenjerani ndi agalu, chenjerani ndi wochita zoyipa, chenjerani ndi a mdulidwe.

Php 3:3 Pakuti ife ndife mdulidwe, amene tipembedza Mulungu mu Mzimu ndi a chimwemwe mwa Yesu Khristu, ndipo tilibe kukhulupirira mthupi.

Php 3:4 Ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m’thupi; ngati munthu wina yense aganiza kukakhulupirira m’thupi, inenso kwambiri:

Php 3:5 Wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa m’bado wa Israyeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa ahebri, monga mwa lamulo; Mfarisi;

Php 3:6 Monga mwa changu, wozunza mpingo; monga mwa chilungamo cha m’lamulo wokhala wosalakwa ine.

Php 3:7 Komatu zinthu zonse zimene zidandipindulira, zomwezo ndidaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu.

Php 3:8 Inde nzosakayikitsa komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe achizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndidatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikapindule Khristu.

Php 3:9 Ndikupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m’lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro.

Php 3:10 Kuti ndimzindikire iye, ndi mphamvu yakuwuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake;

Php 3:11 Ngati nkotheka ndikafikire kuwuka kwa akufa.

Php 3:12 Sikunena kuti ndidalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene adandigwirira Khristu Yesu.

Php 3:13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poyiwaladi zinthu za m’mbuyo, ndikutambalitsira zinthu za m’tsogolo,

Php 3:14 Ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa mayitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

Php 3:15 Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli chinthu mulingirira nacho mumtima, ichinso Mulungu adzabvumbulutsira inu.

Php 3:16 Chokhachi,monga ndidachirandira kale tiyeni mu lamulo lomweli tiyende tiganizire chinthu chomwechi.

Php 3:17 Abale, khalani pamodzi akutsunza anga, ndipo yang’anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.

Php 3:18 (Pakuti ambiri amayenda, za amene ndidakuwuzani kawiri kawiri, ndipo tsopano ndikuwuzani ndi kulira, kuti ali adani a mtanda wa Khristu:

Php 3:19 Amene chitsiriziro chawo ndicho kuwonongeka, amene Mulungu wawo ndiyo mimba yawo, ulemerero wawo uli m’manyazi awo, amene alingirira za zinthu za padziko.

Php 3:20 Pakuti ubadwa wathu uli kumwamba; kuchokera komwekonso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu.

Php 3:21 Amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nawo zinthu zonse.



4

Php 4:1 Potero, abale anga wokondedwa, wolakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi Korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, wokondedwa anga.

Php 4:2 Ndidandaulira Euodiya, ndidandaulira Suntuke, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.

Php 4:3 Inde ndikupemphaninso, mzanga wa m’goli wowona, muthandize akazi awa amene adakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klementonso, ndi wotsala aja antchito amzanga, amene mayina awo ali m’buku la moyo.

Php 4:4 Kondwerani mwa Ambuye, nthawi zonse; ndibwerezanso kotero kondwerani.

Php 4:5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi:

Php 4:6 Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

Php 4:7 Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khiristu Yesu.

Php 4:8 Chotsatira abale, zinthu ziri zonse zowona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zomveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingilireni izi.

Php 4:9 Zinthu zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziwona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere akhale ndi inu.

Php 4:10 Koma ndidakondweradi mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano mudatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso mudalingirirako, koma mudasowa mpata.

Php 4:11 Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire ziri zonse ndiri nazo.

Php 4:12 Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

Php 4:13 Ndikhoza kuchita zinthu zonse mwa Khristu wondipatsa mphamvuyo.

Php 4:14 Koma mudachita bwino kuti mudayanjana nane m’chisautso changa.

Php 4:15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m’chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndidachoka kutuluka m’Makedoniya, siwudayanjana nane Mpingo umodzi wonse m’makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha.

Php 4:16 Pakuti m’Tesalonikanso mudanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.

Php 4:17 Sikuti chifukwa nditsata mphatso, komatu ndikhumba chipatso kuti mukachulukire ku mdalitso wanu.

Php 4:18 Koma ndiri nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, m’nunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.

Php 4:19 Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chiri chonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Php 4:20 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero ku nthawi za nthawi, Amen.

Php 4:21 Patsani moni kwa woyera mtima ali yense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine akupatsani moni inu.

Php 4:22 Woyera mtima onse akupatsani oni inu, koma maka maka iwo a banja la Kayisara.

Php 4:23 Chisomo cha Ambuye Yesu hristu chikhale ndi inu nonse.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE