Philemon


1

Phm 1:1 Paulo wandende wa Yesu Khristu, ndi Timoteyo mbale wathu, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mzathu,

Phm 1:2 Ndi kwa Apiya wokondedwa wathu, ndi Arkipo msilikali mzathu, ndi kwa Mpingo uli m’nyumba yako:

Phm 1:3 Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Phm 1:4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndikutchula iwe m’mapemphero anga,

Phm 1:5 Pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa woyera mtima onse.

Phm 1:6 Kuti chiyanjano cha chikhulupiriro chako chikhale champhamvu podziwa chabwino chiri chonse chiri mwa inu, cha kwa Khristu Yesu.

Phm 1:7 Pakuti ndidali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya woyera yatonthozeka mwa iwe mbale.

Phm 1:8 Momwemo ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukulu mwa Khristu kukulamulira chimene chiyenera,

Phm 1:9 Koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Yesu Khristu.

Phm 1:10 Ndikudandaulira chifukwa cha mwana wanga, amene ndambala m’ndende, Onesimo;

Phm 1:11 Amene kale sadakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;

Phm 1:12 Amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine;

Phm 1:13 Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m’malo mwako akadanditumikira ine m’ndende za Uthenga Wabwino.

Phm 1:14 Koma wopanda kudziwa mtima wako sindidafuna kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwa ufulu.

Phm 1:15 Pakuti kapena adasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi chifukwa cha ichi, ndi kuti udzamulandire nthawi zonse;

Phm 1:16 Osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga iwe, m’thupi ndiponso mwa Ambuye.

Phm 1:17 Ngati tsono undiyesa ine woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.

Phm 1:18 Koma ngati adakulakwira kanthu kapena kungongola kanthu, undiwerengere ine kameneko;

Phm 1:19 Ine Paulo, ndalemba ndi dzanja langa, ndidzalipira ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe wamangawa anga ngakhale iwe uli ndi mangawa ndi ine.

Phm 1:20 Inde, mbale ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Ambuye.

Phm 1:21 Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena.

Phm 1:22 Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndikhulupirira kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.

Phm 1:23 Epafra wandende mzanga mwa Khristu Yesu akupatsa iwe moni.

Phm 1:24 Ateronso, Marko, Aristarko, Dema, Luka, antchito amzanga.

Phm 1:25 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE