Matthew


1

Mat 1:1 Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.

Mat 1:2 Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake;

Mat 1:3 Ndipo Yuda anabala Faresi ndi Zara mwa Tamara; ndi Faresi anabala Ezironi; ndi Ezironi anabala Aramu;

Mat 1:4 Ndi Aramu anabala Aminadabu ndi Aminadabu anabala Naasoni; ndi Naasoni anabala Salimoni;

Mat 1:5 Ndi Salimoni anabala Boazi mwa Rahabe; ndi Boazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Jese;

Mat 1:6 Ndi Jese anabala Davide mfumuyo; ndipo Davide mfumuyo anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya;

Mat 1:7 Ndi Solomoni anabala Rehabiyamu; ndi Rehabiyamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa;

Mat 1:8 Ndi Asa anabala Yosafate; ndi Yosafate anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya;

Mat 1:9 Ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya;

Mat 1:10 Ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya;

Mat 1:11 Ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi ya kutengedwa kumka ku Babulo:

Mat 1:12 Ndipo pambuyo pake pa kutengedwa ku Babulo, Yekoniya anabala Salatiyeli; ndi Salatiyeli anabala Zerubabele;

Mat 1:13 Ndi Zerubabele anabala Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;

Mat 1:14 Ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliyudi;

Mat 1:15 Ndi Eliyudi adabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo;

Mat 1:16 Ndi Yakobo anabala Yosefe mwamuna wake wa Mariya, amene Yesu wotchedwa Khristu adabadwa mwa iye.

Mat 1:17 Motero mibado yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inayi; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kumka ku Babulo mibado khumi ndi inayi, ndi kuyambira pa kutengedwa kumka ku Babulo kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inayi.

Mat 1:18 Tsopano kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kudali kotere: Amayi wake Mariya adapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asadakomane iwowo, adapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.

Mat 1:19 Koma Yosefe, mwamuna wake, adali wolungama,ndiponso sadafuna kunyanzitsa iye, nalingirira mumtima kumleka iye m’seri.

Mat 1:20 Koma posinkhasinkha iye zinthu izi, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera kwa iye m’kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usawope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chiri cha Mzimu Woyera.

Mat 1:21 Ndipo adzabala mwana wa mwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iye adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.

Mat 1:22 Tsopano zonsezi zidakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa m’neneri, ndi kuti,

Mat 1:23 Onani namwali adzayima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutchadzina lake Emmanuel; ndilo losandulika, Mulungu ali nafe.

Mat 1:24 Ndipo Yosefe adawuka kutulo take, nachita monga adamuwuza m’ngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake;

Mat 1:25 Ndipo sadamdziwa iye kufikira adabala mwana wake woyamba wamwamuna; namutcha dzina lake Yesu.



2

Mat 2:1 Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m’masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum’mawa anafika ku Yerusalemu,

Mat 2:2 Nanena, Ali kuti amene adabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tidawona nyenyezi yake kum’mawa, ndipo tidabwera kudzamlambira Iye.

Mat 2:3 Pamene Herode mfumuyo adamva ichi adavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.

Mat 2:4 Ndipo pamene adasonkhanitsa ansembe akulu onse ndi alembi a anthu, adafunsira iwo, adzabadwira kuti Khristuyo?

Mat 2:5 Ndipo adamuwuza iye, M’Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kudalembedwa kotere ndi m’neneri kuti,

Mat 2:6 Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wam’ng’onong’ono mwa akulu a Yudeya; pakuti wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.

Mat 2:7 Pomwepo Herode adawayitana Anzeruwo m’seri, nafunsitsa iwo nthawi yake idawoneka nyenyeziyo.

Mat 2:8 Ndipo adawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mawu, kuti inenso ndidzadze kumlambira Iye.

Mat 2:9 Ndipo iwo, m’mene adamva mfumu, adamuka; ndipo onani, nyenyezi ija adayiwona kum’mawa, idawatsogolera iwokufikira idadza niyima pamwamba pomwe padali kamwanako.

Mat 2:10 Pamene adayiwona nyenyeziyo, adakondwera ndi kukondwa kwakukulu.

Mat 2:11 Ndipo pamene adafika ku nyumba adawona kamwanako ndi Mariya amake, ndipo adagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chawo, nampatsa Iye mphatso zawo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.

Mat 2:12 Ndipo iwo, pochenjezedwa ndi Mulungu m’kulota kuti asabwerere kwa Herode, adachoka kupita ku dziko lawo panjira yina.

Mat 2:13 Ndipo pamene iwo adachoka, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera kwa Yosefe m’kulota, nati Tawuka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Aigupto, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuwuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukawononga iko.

Mat 2:14 Ndipo iye adanyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Aigupto.

Mat 2:15 Ndipo adakhalabe kumeneko kufikira adamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa m’neneri kuti, ndidayitana Mwana wanga atuluke mu Aigupto.

Mat 2:16 Pamenepo Herode, powona kuti adampusitsa Anzeruwo, adapsa mtima ndithu natumiza ena kukawononga tiana ta m’Betelehemu ndi ta m’milaga yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating’ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye adafunsitsa kwa Anzeruwo.

Mat 2:17 Pomwepo chidachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya m’neneri, kuti,

Mat 2:18 Mawu adamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.

Mat 2:19 Koma pamene Herode adamwalira, onani, m’ngelo wa Ambuye adawonekera m’kulota kwa Yosefe mu Aigupto.

Mat 2:20 Nanena, Tawuka, nutenge kamwana ndi amake nupite kudziko la Israyeli; chifukwa adafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako.

Mat 2:21 Ndipo iye adawuka natenga kamwana ndi amake, nalowa m’dziko la Israyeli.

Mat 2:22 Koma pamene iye adamva kuti Arikelao adali mfumu ya Yudeya m’malo mwa atate wake Herode, adachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene adachenjezedwa ndi Mulungu m’kulota, adapita nalowa ku mdera lina la Galileya:

Mat 2:23 Ndipo adadza nakhazikika mumzinda wotchedwa Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.



3

Mat 3:1 Ndipo m’masiku aja adadza Yohane m’batizi, nalalikira m’chipululu cha Yudeya,

Mat 3:2 Nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

Mat 3:3 Pakuti uyu ndiye adanenayo Yesaya m’neneri, kuti, Mawu a wofuwula m’chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.

Mat 3:4 Ndipo Yohane yekhayo adali nacho chobvala chake cha ubweya wangamila, ndi lamba la chikopa m’chiwuno mwake; ndi chakudya chake chidali dzombe ndi uchi wa kuthengo.

Mat 3:5 Pamenepo padamtulukira iye aku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordano;

Mat 3:6 Ndipo adabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordano, ali kuwulula machimo awo.

Mat 3:7 Koma pamene iye adawona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki alimkudza ku ubatizo wake, adati kwa iwo, wobadwa a njoka inu, ndani adakulangizani kuthawa m’kwiyo ulimkudza?

Mat 3:8 Wonetsani inu zipatso zoyenera kutembenuka mtima:

Mat 3:9 Ndipo musamayese kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuwukitsira Abrahamu ana.

Mat 3:10 Ndipo tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chifukwa chake mtengo uli wonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.

Mat 3:11 Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wondiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto.

Mat 3:12 Chowuluzira chake chiri m’dzanja lake ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m’nkhokwe koma mankhusu adzatenthedwa ndi moto wosazimitsika.

Mat 3:13 Pamenepo Yesu adachokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye.

Mat 3:14 Koma Yohane adamkaniza, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?

Mat 3:15 Koma Yesu adayankha nati kwa iye, Balola tsopano; pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo adamlola Iye.

Mat 3:16 Ndipo Yesu, pamene adabatizidwa, pomwepo adatuluka m’madzi ndipo onani, miyamba idatsegukira Iye, ndipo adapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda, ndi kuwala kudatera pa Iye:

Mat 3:17 Ndipo onani, mawu akuchokera ku miyamba akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.”



4

Mat 4:1 Pamenepo Yesu adatsogozedwa ndi Mzimu kupita ku chipululu kukayesedwa ndi m’diyerekezi.

Mat 4:2 Ndipo pamene Iye adatha kusala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, pambuyo pake adamva njala.

Mat 4:3 Ndipo woyesayo adafika nati kwa Iye,Ngati muli Mwana wa Mulungu, lamulirani kuti miyala iyi ikhale mkate.

Mat 4:4 Koma Iye adayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse wotuluka m’kamwa mwa Mulungu.

Mat 4:5 Pamenepo m’diyerekezi adapita naye ku mzinda woyera; namuyika Iye pamwamba pa songa la denga la kachisi.

Mat 4:6 Ndipo adati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi; pakuti kwalembedwa kuti, Adzawuza angelo ake za inu, ndipo pamanja awo adzakunyamulani inu, mungagunde phazi lanu pa mwala.

Mat 4:7 Yesu adanena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

Mat 4:8 Pomwepo mdiyerekezi adapita naye ku phiri lalitali, namuwonetsa mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo;

Mat 4:9 Ndipo adati kwa Iye, Zinthu zonsezi ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndikundipembedza ine.

Mat 4:10 Pomwepo Yesu adanena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzampembedza ndipo Iye yekha yekha udzimtumikira.

Mat 4:11 Pomwepo m’diyerekezi adamsiya Iye, ndipo onani, angelo adadza, namtumikira Iye.

Mat 4:12 Tsopano pamene Yesu adamva kuti Yohane adaponyedwa mundende adapita ku kulowa mGalileya;

Mat 4:13 Ndipo adachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m’Kapenawo wa pambali pa nyanja m’malire a Zebuloni ndi Nafitali:

Mat 4:14 Kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi Yesaya m’neneri kuti,

Mat 4:15 Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordano, Galileya wa amitundu;

Mat 4:16 Anthu wokhala mumdima adawona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo wokhala m’malo a m’thunzi wa imfa, kuwala kudawatulukira iwo.

Mat 4:17 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kulalikira, ndikuti, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wakumwamba wayandikira.

Mat 4:18 Ndipo Yesu poyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, adawona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andreya m’bale wake, adalikuponya khoka m’nyanja popeza adali asodzi a nsomba.

Mat 4:19 Ndipo Iye adati kwa iwo, Nditsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.

Mat 4:20 Ndipo iwo adasiya pomwepo makoka awo namtsata Iye.

Mat 4:21 Ndipo popitilira Iye adawona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane m’bale wake, mu ngalawa, pamodzi ndi Zebedayo atate wawo, adalikusoka makoka awo; ndipo adawayitana iwo.

Mat 4:22 Ndipo adasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wawo; namtsata Iye.

Mat 4:23 Ndipo Yesu adayendayenda mu Galileya monse, adalikuphunzitsa mu masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumu, nachiritsa kudwala konse ndi nthenda zonse mwa anthu.

Mat 4:24 Ndipo mbiri yake inabuka ku Suriya konse; ndipo adatengera kwa Iye onse wodwala, wogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundu mitundu, ndi wogwidwa ndi mizimu yoyipa, ndi akhungu ndi amanjenje; ndipo Iye adawachiritsa.

Mat 4:25 Ndipo idamtsata mipingo mipingo ya anthu wochokera ku Galileya ndi ku Dekapole ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordano.



5

Mat 5:1 Ndipo powona makamu, adakwera m’phiri; ndipo m’mene Iye adakhala pansi adadza kwa Iye ophunzira ake;

Mat 5:2 Ndipo adatsegula pakamwa pake, nawaphunzitsa iwo; nati;

Mat 5:3 Odala ali wosauka mu mzimu; chifukwa uli wawo Ufumu wa kumwamba.

Mat 5:4 Odala ali achisoni: chifukwa adzatonthozedwa.

Mat 5:5 Odala ali wofatsa chifukwa adzalandira dziko lapansi.

Mat 5:6 Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhuta.

Mat 5:7 Odala ali akuchita chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.

Mat 5:8 Odala ali woyera mtima; chifukwa adzawona Mulungu.

Mat 5:9 Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Mat 5:10 Odala iwo akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo; chifukwa uli wawo Ufumu wa kumwamba.

Mat 5:11 Odala muli inu m’mene anthu adzanyanzitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoyipa ziri zonse chifukwa cha Ine.

Mat 5:12 Sekererani, sangalalani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu m’Mwamba; pakuti potero adazunza aneneri adakhalawo musadabadwe inu.

Mat 5:13 Inu ndinu m’chere wa dziko lapansi; koma m’cherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.

Mat 5:14 Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.

Mat 5:15 Palibe munthu ayatsa nyali nayibvundikira m’mbiya, koma amayiyika iyo pa choyikapo chake; ndipo imawunikira onse ali m’nyumbamo.

Mat 5:16 Chomwecho muwalitse inu kuwunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuwona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa kumwamba.

Mat 5:17 Musaganize kuti ndidadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri; sindinadza kupasula koma kukwaniritsa.

Mat 5:18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang’ono kamodzi kapena kasonga kake kamodzi sikadzachoka kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.

Mat 5:19 Chifukwa chake yense womasula limodzi la malamulo amenewa ang’onong’ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng’onong’ono mu Ufumu wa kumwamba; koma yense wochita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wa mkulu mu Ufumu wa kumwamba.

Mat 5:20 Pakuti ndinena ndi inu, Ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa kumwamba.

Mat 5:21 Mudamva kuti kudanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu:

Mat 5:22 Koma Ine ndinena kwa inu, Kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu; koma amene adzati, chitsilu iwe; adzakhala wopalamula gehena wamoto.

Mat 5:23 Chifukwa chake ngati wabweretsa mphatso yako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe;

Mat 5:24 Usiye pomwepo mphatso yako, patsogolo pa guwa, nupite, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndi pamenepo idza nupereke mphatso yako.

Mat 5:25 Fulumira kuyanjana ndi mdani wako, pamene uli naye panjira; kuti kapena mdani wako angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe m’nyumba yandende.

Mat 5:26 Indetu ndinena ndi iwe, Sudzatulukamo konse, koma utalipira kakobiri komaliza ndiko.

Mat 5:27 Mudamva kuti kudanenedwa, Usachite chigololo:

Mat 5:28 Koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense woyang’ana mkazi momkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.

Mat 5:29 Ndipo ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti n’kwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chiwonongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu gehena.

Mat 5:30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chiwonongeke, losamuka thupi lako lonse mu gehena.

Mat 5:31 Kudanenedwanso, yense wochotsa mkazi wake ampatse iye kalata wa chilekaniro:

Mat 5:32 Koma Ine ndinena kwa inu, Kuti yense wochotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chiwerewere, am’chititsa chigololo; ndipo amene adzakwatira wochotsedwayo achita chigololo.

Mat 5:33 Ndiponso, mudamva kuti kudanenedwa kwa iwo akale, Usadzilumbirire wekha, koma udzachita malumbiro ako kwa Ambuye.

Mat 5:34 Koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu:

Mat 5:35 Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa liri lopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yayikulu.

Mat 5:36 Kapena usalumbire ku mutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbuu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi.

Mat 5:37 Koma manenedwe anu akhale, inde, inde; Iyayi, iyayi; ndipo chowonjezedwa pa izo chichokera kwa woyipayo.

Mat 5:38 Mudamva kuti kudanenedwa, Diso kulipa diso, ndi Dzino kulipa dzino;

Mat 5:39 Koma ndinena kwa inu, Musakanize choyipa; koma amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, umtembenuzire iye linanso.

Mat 5:40 Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.

Mat 5:41 Ndipo amene akukakamiza kumperekeza ulendo wamtunda umodzi, upite naye mitunda iwiri.

Mat 5:42 Amene wakupempha umpatse, ndipo iye wofuna kukukongola usampotolokere.

Mat 5:43 Mudamva kuti kudanenedwa, Udzikondana ndi m’nansi wako, ndikudana ndi mdani wako.

Mat 5:44 Koma Ine ndinena kwa inu, kondanani nawo adani anu, ndi kudalitsa iwo akutemberera inu, chitirani zabwino iwo akuda inu, ndikupempherera iwo amene amakunyozetsani ndi kunzunza inu;

Mat 5:45 Kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa kumwamba; chifukwa Iye amakwezera, dzuwa lake pa woyipa ndi abwino nabvumbitsira mvula pa wolungama ndi pa wosalungama.

Mat 5:46 Chifukwa ngati muwakonda iwo akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?

Mat 5:47 Ndipo ngati muyankhula abale anu wokhawokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu amisonkho sachita chomwecho?

Mat 5:48 Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa kumwamba ali wangwiro.



6

Mat 6:1 Yang’anirani musachite zachifundo zanu pamaso pa anthu kuti muwonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa kumwamba.

Mat 6:2 Chifukwa chake pamene pali ponse upatsa mphatso za chifundo, usamawomba lipenga patsogolo pako, monga amachita wonyenga mmasunagoge,ndi m’makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo.

Mat 6:3 Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja:

Mat 6:4 Kotero kuti mphatso zako za chifundo zikhale za mseri; ndipo Atate wako mwiniyekha wokuwona mseri adzakupatsa iwe mowonekera.

Mat 6:5 Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga wonyengawo; chifukwa iwo akonda kuyimilira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti awonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo.

Mat 6:6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere kwa Atate wako ali mseri, ndipo Atate wako wakuwona mseri adzakupatsa iwe mowonekera.

Mat 6:7 Ndipo popemphera musabwereze bwereze chabe iyayi, monga amachita achikunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kuyankhula yankhula kwawo.

Mat 6:8 Chifukwa chake inu musafanane nawo; pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musadayambe kupempha Iye.

Mat 6:9 Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate Wathu Wakumwamba, dzina lanu Liyeretsedwe.

Mat 6:10 Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.

Mat 6:11 Mutipatse ife lero mkate wathu wa tsiku ndi tsiku.

Mat 6:12 Ndipo mutikhululukire ife mangawa athu, monga ifenso tiwakhululukira amangawa athu.

Mat 6:13 Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse ife kwa woyipayo.

Mat 6:14 Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa kumwamba.

Mat 6:15 Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.

Mat 6:16 Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope ya chisoni, ngati wonyengawo; pakuti ayipitsa nkhope zawo, kuti awonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya.Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zawo.

Mat 6:17 Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako;

Mat 6:18 Kuti usawonekere kwa anthu kuti ulimkusala kudya, koma kwa Atate wako ali mseri, ndipo Atate wako wokuwona mseri adzakubwezera iwe mowonekera.

Mat 6:19 Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zichiwononga; ndi pamene mbala zibowola ndi kuba:

Mat 6:20 Koma mudzikundikire nokha chuma m’Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala sizibowola ndi kuba;

Mat 6:21 Pakuti kumene kuli chuma chako, komweko udzakhala mtima wakonso.

Mat 6:22 Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa kwatunthu.

Mat 6:23 Koma ngati diso lako liri loyipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa kwatunthu. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu!

Mat 6:24 Palibe munthu angathe kutumikira ambuye awiri; pakuti pena adzamuda m’modziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa m’modzi, nadzanyoza

Mat 6:25 Chifukwa chake ndinena kwa inu, musadere nkhawa za moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu; chimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa chakudya ndi thupi liposa chobvala?

Mat 6:26 Tawonani mbalame za kumwamba sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa kumwamba azidyetsa. Nanga inu simuziposa kodi?

Mat 6:27 Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi?

Mat 6:28 Ndipo muderanji nkhawa ndi chobvala? Taganizirani za maluwa a kuthengo, makulidwe awo; sagwira ntchito, kapena sapota:

Mat 6:29 Ndipo ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sadabvala monga limodzi la amenewa.

Mat 6:30 Ngati Mulungu abveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga inu sadzakubvekani mopambana ndithu, inu wokhulupirira pang’ono?

Mat 6:31 Chifukwa chake musadele nkhawa, ndi kuti, tidzadya chiyani? Kapena tidzamwa chiyani? Kapena tidzabvala chiyani?

Mat 6:32 (Pakuti anthu amitundu:) azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.

Mat 6:33 Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.

Mat 6:34 Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo



7

Mat 7:1 Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.

Mat 7:2 Pakuti ndikuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nawo, mudzayesedwa nawo inunso.

Mat 7:3 Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la m’bale wako, koma mtengo uli m’diso la iwe mwini suwuganizira?

Mat 7:4 Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo wona, mtengowo uli m’diso lako.

Mat 7:5 Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m’diso lako mtengowo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa chitsotso m’diso la m’bale wako.

Mat 7:6 Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingapondereze ndi mapazi awo, ndi potembenuka zingang’ambe inu.

Mat 7:7 Pemphani ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;

Mat 7:8 Pakuti yense wopempha alandira; ndi wofunafunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.

Mat 7:9 Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate, adzampatsa mwala?

Mat 7:10 Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi?

Mat 7:11 Chomwecho ngati inu, muli woyipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wakumwamba sadzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? wokha. Zikwanire tsiku zobvuta zake

Mat 7:12 Chifukwa chake zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.

Mat 7:13 Lowani pachipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yopita nayo kuchiwonongeko ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho.

Mat 7:14 Pakuti chipata chimene chiri chopapatiza, nichepetsa njirayo yopita nayo kumoyo, ndipo wochipeza chimenecho ali wowerengeka.

Mat 7:15 Chenjerani ndi aneneri wonyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m’kati mwawo ali mimbulu yolusa.

Mat 7:16 Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?

Mat 7:17 Chomwecho mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphutsi upatsa chipatso choyipa.

Mat 7:18 Mtengo wabwino sungathe kupatsa chipatso choyipa, kapena mtengo wamphutsi kupatsa chipatso chokoma.

Mat 7:19 Mtengo uli wonse wosapatsa chipatso chokoma, awudula, nawutaya kumoto.

Mat 7:20 Chomwecho ndi zipatso zawo mudzawazindikira iwo.

Mat 7:21 Siyense wonena kwa Ine, Ambuye, Ambuyeadzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wochitayo chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba.

Mat 7:22 Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye,Ambuye,Kodi sitidanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoyipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri?

Mat 7:23 Ndipo pamenepo ndidzawawuza iwo, poyera, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu wochita kusaweruzika.

Mat 7:24 Chifukwa chimenechi yense amene akamva mawu anga amenewa, ndi kuwachita ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera amene adamanga nyumba yake pathanthwe.

Mat 7:25 Ndipo idagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zidawomba mphepo, zidagunda pa nyumbayo; koma siyidagwa; chifukwa idakhazikika pathanthwepo.

Mat 7:26 Ndipo yense akamva mawu anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe adamanga nyumba yake pamchenga;

Mat 7:27 Ndipo idagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zidawomba mphepo, zidagunda panyumbayo; ndipo idagwa; ndi kugwa kwake kudali kwakukulu.

Mat 7:28 Ndipo kudali kuti, pamene Yesu adatha mau amenewa, makamu wa anthu adazizwa ndi chiphunzitso chake:

Mat 7:29 Pakuti adawaphunzitsa monga mwini ulamuliro, wosanga alembi awo.



8

Mat 8:1 Ndipo pamene adatsika paphiripo, idamtsata mipingo yambiri ya anthu.

Mat 8:2 Ndipo onani, wakhate adadza namlambira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.

Mat 8:3 Ndipo Yesu adatambasula dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake lidachoka

Mat 8:4 Ndipo Yesu adanena naye, Iwe, usawuze munthu; koma pita, udziwonetsere wekha kwa wansembe, nupereke mphatso imene adayilamulira Mose, ikhale mboni kwa iwo.

Mat 8:5 Ndipo m’mene Iye adalowa mu Kapenawo anadza kwa Iye Kenturiyo, nampempha Iye,

Mat 8:6 Ndipo adati, Ambuye, wantchito wanga ali gone m’nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa kowopsa.

Mat 8:7 Ndipo Yesu adanena naye, Ndidzafika Ine, ndikumchiritsa iye.

Mat 8:8 Koma Kenturiyoyo adabvomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa denga langa ayi; koma mungonena mawu, ndipo adzachiritsidwa wantchito wanga.

Mat 8:9 Pakuti inenso ndiri munthu womvera ulamuliro, ndiri nawo asilikali akundimvera ine; ndipo ndikanena kwa uyu, pita, napita; ndi kwa wina, idza, nadza; ndi kwa wantchito wanga, chita ichi, nachita.

Mat 8:10 Pamene Iye adamva ichi, Yesu adazizwa, nati kwa iwo womutsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israyeli, sindidapeza chikhulupiriro chotere.

Mat 8:11 Ndipo ndinena ndi inu, Kuti ambiri a kum’mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, mu ufumu wa Kumwamba.

Mat 8:12 Koma anawo a ufumu adzatayidwa ku mdima wa kunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mat 8:13 Ndipo Yesu adati kwa Kenturiyoyo, Pita; kukhale kwa iwe monga udakhulupirira, ndipo kuchitike kwa iwe. Ndipo adachiritsidwa wantchitoyo nthawi yomweyo.

Mat 8:14 Ndipo pamene Yesu adafika kunyumba ya Petro, adawona mayi wamkazi wake wa Petro ali gone, alikudwala malungo.

Mat 8:15 Ndipo adamkhudza dzanja lake, ndipo malungo adamleka iye; ndipo adawuka, nawatumikira iwo.

Mat 8:16 Ndipo pakudza madzulo, anabwera nawo kwa Iye anthu ambiri wogwidwa ndi mizimu yoyipa; ndipo adatulutsa mizimuyo ndi mawu ake, nachiritsa wodwala onse;

Mat 8:17 Kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya m’neneri, kuti Iye yekha adatenga zofowoka zathu, nanyamula nthenda zathu.

Mat 8:18 Tsopano Yesu, powona makamu ambiri wa anthu womuzungulira Iye, adalamulira wophunzira amuke ku tsidya lina.

Mat 8:19 Ndipo adadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kuli konse mupitako.

Mat 8:20 Ndipo Yesu adanena kwa iye, Nkhandwe ziri ndi mayenje awo, ndi mbalame za mumlenga lenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe pogoneka mutu wake.

Mat 8:21 Ndipo wina wa wophunzira wake adati kwa Iye, Ambuye mundilole ine ndiyambe ndapita kuyika maliro wa atate wanga.

Mat 8:22 Koma Yesu adanena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa ayike akufa awo.

Mat 8:23 Ndipo pamene Iye adalowa mchombo wophunzira ake adamtsata Iye.

Mat 8:24 Ndipo wonani, padawuka namondwe wa mkulu panyanja, kotero kuti chombo chidafundidwa ndi mafunde; koma Iye adali m’tulo.

Mat 8:25 Ndipo wophunzira ake adadza, namudzutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tiri kuwonongeka.

Mat 8:26 Ndipo adanena Iye kwa iwo,Muli amantha bwanji, wokhulupirira pang’ono inu? Pomwepo Iye adadzuka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo padagwa bata lalikulu.

Mat 8:27 Ndipo adazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Mat 8:28 Ndipo pamene adafika Iye kutsidya lina, ku dziko la Agadara, adakomana naye awiri wogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, awukali ndithu, kotero kuti samkatha kupitapo munthu panjira imeneyo.

Mat 8:29 Ndipo onani, adafuwula nati, tiri nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siyidafike?

Mat 8:30 Ndipo padali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zirimkudya.

Mat 8:31 Ndipo mizimu yoyipayo idampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m’gulu la nkhumbazo.

Mat 8:32 Ndipo adati kwa iyo, Pitani. Ndipo pamene idatuluka, idapita, kukalowa mu nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse lidathamangira kunsi kuphompho m’nyanjamo, ndipo zidafa m’madzi.

Mat 8:33 Ndipo woziweta adathawa, napita kumzinda, nanena zonse, ndi zomwe zidamugwera waziwanda uja.

Mat 8:34 Ndipo onani, mzinda wonse udatuluka kukakumana naye Yesu, ndipo m’mene adamuwona Iye, adampempha Iye kuti achoke m’malire awo



9

Mat 9:1 Ndipo Iye adalowa mchombo, nawoloka, nafika ku mzinda wa kwawo.

Mat 9:2 Ndipo onani, adabwera naye kwa Iye munthu wodwala manjenje, wogona patchika; ndipo Yesu pakuwona chikhulupiriro chawo, adati kwa wodwala manjenjeyo, mwana; Kondwera machimo ako akhululukidwa.

Mat 9:3 Ndipo onani, ena mwa alembi adanena mwa iwo wokha, Munthu uyu achitira Mulungu mwano.

Mat 9:4 Ndipo Yesu pozindikira maganizo awo, adati, Chifukwa chiyani muli m’kuganizira zoyipa m’mitima yanu?

Mat 9:5 Pakuti chapafupi n’chiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka nuyende?

Mat 9:6 Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo adanena kwa wodwala manjenjeyo,) Tanyamuka, nutenge tchika lako, nupite ku nyumba kwako.

Mat 9:7 Ndipo adanyamuka nachoka napita kunyumba kwake.

Mat 9:8 Koma pamene makamu a anthu adachiwona, adazizwa, nalemekeza Mulungu, wopatsa anthu mphamvu yotere.

Mat 9:9 Ndipo Yesu podutsa kuchokera kumeneko, adawona munthu, dzina lake Mateyu, atakhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye adadzuka namtsata.

Mat 9:10 Ndipo padali pamene Yesu adali mkukhala pa chakudya m’nyumba, onani amisonkho ndi wochimwa ambiri adadza nakhala pansi pamodzi ndi Iye ndi wophunzira ake,

Mat 9:11 Ndipo pamene Afarisi adawona ichi, adanena kwa wophunzira ake, Chifukwa chiyani Mphunzitsi wanu alimkudya pamodzi ndi amisonkho ndi wochimwa?

Mat 9:12 Ndipo m’mene Yesu adamva ichi, adati, kwa iwo, Olimba safuna sing’anga ayi, koma wodwala.

Mat 9:13 Koma pitani muphunzire kuti n’chiyani ichi, ndifuna chifundo, si nsembe ayi; pakuti sindinadza kudzayitana wolungama, koma wochimwa kukulapa.

Mat 9:14 Pomwepo adadza kwa Iye wophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa chiyani ife ndi Afarisi tisala kudya kawiri kawiri, koma wophunzira anu sasala?

Mat 9:15 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Nanga ana a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nawo? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.

Mat 9:16 Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu ya tsopano pa chobvala chakale pakuti chigamba chake chizomoka ku chobvalacho, ndipo kuzomoka kwake kukhala kwakukulu.

Mat 9:17 Palibe munthu athira vinyo watsopano m’mabotolo akale; atatero mabotolo akhoza kusweka, ndipo vinyo akhoza kutayika, ndipo mabotolo angawonongeke; koma amathira vinyo watsopano m’mabotolo atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.

Mat 9:18 M’mene Iye adali kuyankhula nawo zinthu zimenezo, onani, adadza munthu wina wolamulira, nampembedza, Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mubwere muyike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.

Mat 9:19 Ndipo Yesu adanyamuka namtsata iye, nateronso wophunzira ake womwe.

Mat 9:20 Ndipo onani, mkazi adali ndi nthenda yokha mwazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, nadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chobvala chake;

Mat 9:21 Pakuti adalikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chobvala chake chokha ndidzachira.

Mat 9:22 Koma Yesu potembenuka ndi kuwona iye adati,Kondwera, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo adachira kuyambira nthawi yomweyo.

Mat 9:23 Ndipo pamene Yesu amalowa m’nyumba yake ya wolamulirayo, ndi powona woyimba zitoliro ndi khamu la anthu wobuma,

Mat 9:24 Iye adanena kwa iwo, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m’tulo. Ndipo adamseka Iye pwepwete.

Mat 9:25 Koma pamene anthuwo adatulutsidwa, Iye adalowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadawuka.

Mat 9:26 Ndipo mbiri yake imene inabuka m’dera lonse limenelo.

Mat 9:27 Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, adamtsata iye anthu awiri akhungu; wofuwula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, Mwana wa Davide.

Mat 9:28 Ndipo m’mene Iye adalowa m’nyumbamo, akhunguwo adadza kwa Iye; ndipo Yesu adati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Adanena kwa Iye, Inde Ambuye.

Mat 9:29 Pomwepo iye adakhudza maso awo, nati chichitidwe kwa inu monga chikhulupiliro chanu.

Mat 9:30 Ndipo maso awo adaphenyuka. Ndipo Yesu adawawuzitsa iwo, nanena, Yang’anani, asadziwe munthu aliyense.

Mat 9:31 Koma iwo atatulukamo, anabukitsa mbiri yake m’dziko lonselo.

Mat 9:32 Ndipo pamene iwo adalimkutuluka, onani, adabwera naye kwa Iye munthu wosayankhula, wogwidwa ndi chiwanda.

Mat 9:33 Ndipo m’mene chidatulitsidwa chiwandacho, wosayankhulayo adayankhula, ndipo makamu adazizwa, nanena, Kale lonse sichidawoneke chomwecho mwa Israyeli.

Mat 9:34 Koma Afarisi adati, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.

Mat 9:35 Ndipo Yesu adayenda yenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, naphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda ili yonse ndi zofowoka zonse.

Mat 9:36 Koma Iye, powona makamuwo, adagwidwa ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza adali wokambululudwa ndi womwazikana, akunga nkhosa zopanda m’busa.

Mat 9:37 Pomwepo Iye adanena kwa wophunzira ake, Zokolola zichulukadi, koma antchito ali wochepa.

Mat 9:38 Chifukwa chake pempherani mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.



10

Mat 10:1 Ndipo pamene Iye adadziyitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, adapatsa iwomphamvu pa mizimu yoyipa, yakuyitulutsa, ndikuchiza nthenda ili yonse ndi zodwala zonse.

Mat 10:2 Tsopano mayina wa atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa:- woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andreya m’bale wake; Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane m’bale wake;

Mat 10:3 Filipo, ndi Bartolomeyo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Lebayo amene dzina la atake ake ndi Tadeyo;

Mat 10:4 Simoni mkanani, ndi Yudasi Isikariyote amenenso adampereka Iye.

Mat 10:5 Awa, khumi ndi awiriwa, Yesu adawatumiza, ndikuwalamulira ndi kuti, Musapite ku njira ya kwa amitundu, ndi kumzinda uliwonse wa Asamariya musamalowamo:

Mat 10:6 Koma makamaka mupite ku nkhosa zosokera za banja la Israyeli;

Mat 10:7 Ndipo pamene muli kupita lalikani kuti, Ufumu wa kumwamba wayandikira.

Mat 10:8 Chiritsani wodwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda; mudalandira kwaulere, patsani kwaulere.

Mat 10:9 Musadzitengere ndalama zagolidi, kapena zasiliva, kapena zakobiri m’zikwama zanu,

Mat 10:10 Kapena thumba la kamba la panjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.

Mat 10:11 Ndipo mu mzinda uli wonse, kapena mudzi mukalowamo, mumfunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.

Mat 10:12 Ndipo polowa m’nyumba muwayankhule.

Mat 10:13 Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siyili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.

Mat 10:14 Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mutuluka m’nyumbayo, kapena mumzindamo, sasani fumbi m’mapazi anu.

Mat 10:15 Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wawo wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mzinda umenewo.

Mat 10:16 Tawonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani inu wochenjera monga njoka,ndi owona mtima monga nkhunda.

Mat 10:17 Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo;

Mat 10:18 Ndipo adzakutengerani kwa a kazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa amitundu.

Mat 10:19 Koma pamene pali ponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa kuti mudzayankhula bwanji kapena mudzanena chiyani; pakuti chimene mudzachiyankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo.

Mat 10:20 Pakuti woyankhula sindinu, koma Mzimu wa Atate wanu woyankhula mwa inu.

Mat 10:21 Ndipo mbale adzapereka mbale wake ku imfa, ndi atate mwana wake; ndipo ana adzawukira akuwabala, nadzawafetsa iwo.

Mat 10:22 Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wopilira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.

Mat 10:23 Koma pamene angakuzunzeni inu mumzinda uwu, thawirani inu mwina; indetu ndinena kwa inu, simudzayitha mizinda ya Israyeli, kufikira Mwana wa munthu atadza.

Mat 10:24 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena mtumiki saposa mbuye wake.

Mat 10:25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi mtumiki monga mbuye wake. Ngati adamutcha, mkulu wanyumba Belezebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?

Mat 10:26 Chifukwa chake musawopa iwo; pakuti palibe kanthu kanabvundikiridwa kamene sikadzawululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika

Mat 10:27 Chimene ndikuwuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m’khutu, muchilalikire pa madenga a nyumba.

Mat 10:28 Ndipo musamawopa iwo amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuwupha; koma makamaka muwope Iye, wokhoza kuwuwononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.

Mat 10:29 Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siyigwa pansi popanda Atate wanu;

Mat 10:30 Komatu inu, tsitsi lonse la m’mutu mwanu liwerengedwa.

Mat 10:31 Chifukwa chake musamawopa; inu mupambana mpheta zambiri.

Mat 10:32 Chifukwa chake yense amene adzabvomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzam’bvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

Mat 10:33 Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

Mat 10:34 Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.

Mat 10:35 Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake wamkazi..

Mat 10:36 Ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.

Mat 10:37 Iye wokonda atate kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.

Mat 10:38 Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine.

Mat 10:39 Iye amene apeza moyo wake, adzawutaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzawupeza.

Mat 10:40 Iye wolandira inu, andilandira Ine, ndi wondilandira Ine, amlandira Iye amene adanditumiza Ine.

Mat 10:41 Iye wolandira m’neneri, pa dzina la m’neneri, adzalandira mphotho ya m’neneri; ndipo iye wolandira munthu wolungama, mudzina la munthu wolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama.

Mat 10:42 Ndipo aliyense amene adzamwetsa m’modzi wa ang’ono awa chikho chokha cha madzi wozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.



11

Mat 11:1 Ndipo zitapita izi, pamene Yesu adatha kuwalamulira wophunzira ake khumi ndi awiri, Iye adachoka kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m’mizinda yawo.

Mat 11:2 Tsopano pamene Yohane pakumva m’nyumba yandende ntchito za Khristu, iye adatuma wophunzira ake awiri,

Mat 11:3 Ndipo anati kwa Iye, Inu ndinu wakudzayo kodi, kapena tiyembekezere wina?

Mat 11:4 Ndipo Yesu adayankha, nanena nao, Pitani mubwezere mawu kwa Yohane azimene mulikumva ndi kuziwona:

Mat 11:5 Akhungu akulandira kuwona kwawo, ndi wopunduka miyendo akuyenda, akhate akukonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa uthenga wabwino.

Mat 11:6 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

Mat 11:7 Ndipo m’mene iwo adalimkupita, Yesu adayamba kunena ndi makamu zokhudzana ndi Yohane. Mudatuluka kumka kuchipululu kukapenyanji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

Mat 11:8 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Munthu wobvala zofewa kodi? Onani, wobvala zofewa ali m’nyumba za mafumu.

Mat 11:9 Koma mudatuluka Kukawona chiyani m’neneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu,koma woposa m’neneri.

Mat 11:10 Uyu ndiye amene kudalembedwa za Iye, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m’tsogolo mwanu.

Mat 11:11 Indetu ndinena kwa inu, sadawuke wobadwa mwa mkazi munthu wa mkulu woposa Yohane M’batizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.

Mat 11:12 Ndipo kuyambira masiku a Yohane M’batizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wakumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.

Mat 11:13 Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chidanenera kufikira pa Yohane.

Mat 11:14 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.

Mat 11:15 Amene ali ndi makutu akumva, amve.

Mat 11:16 Koma ndidzafanizira ndi chiyani wobadwa awa a makono? Ali wofanana ndi ana wokhala m’mabwalo a malonda amene ali kuyitana anzawo,

Mat 11:17 Ndi kuti, Tidakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simudabvine; tidakubumirani maliro, ndipo inu simudalire.

Mat 11:18 Pakuti Yohane adadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, ali ndi chiwanda.

Mat 11:19 Mwana wa munthu adadza wakudya, ndi kumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyayidya ndi wakumwayimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi wochimwa! Ndipo nzeru yilungamitsidwa kwa ana ake.

Mat 11:20 Pomwepo Iye adayamba kutonza mizindayo, m’mene zidachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa iwo sadalape konse.

Mat 11:21 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsayida! Chifukwa ngati ntchito zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Turo ndi mu Sidoni, atalapa kale kale m’ziguduli ndi m’phulusa.

Mat 11:22 Koma ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wawo wa Turo ndi Sidoni udzachepa ndi wanu.

Mat 11:23 Ndipo iwe, Kapernawo, udzakwezedwa kodi kufikira kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira kugehena! Chifukwa ngati ntchito za mphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uwo ukadakhala kufikira lero.

Mat 11:24 Koma ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa koposa wako.

Mat 11:25 Nyengo imeneyo Yesu adayankha nati, Ndikuyamikani Inu Atate mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti mudabisira izi kwa anzeru ndi kwaw odziwitsa, ndipo mudaziwululira izi kwa makanda.

Mat 11:26 Indetu, Atate: chifukwa chotero chidakhala chokondweretsa pamaso panu.

Mat 11:27 Zinthu zonse zidaperedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana koma Atate yekha; ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha ndi iye amene Mwana afuna kumuwulullira.

Mat 11:28 Idzani kuno kwa Ine nonsenu wolema ndi wothodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.

Mat 11:29 Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

Mat 11:30 Pakuti goli langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka



12

Mat 12:1 Nyengo imeneyo Yesu adapita tsiku la sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipowophunzira ake adali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya.

Mat 12:2 Koma Afarisi pakuwona, adati kwa Iye, Tapenyani, wophunzira anu achita chosaloleka tsiku la sabata.

Mat 12:3 Koma Iye adati kwa iwo, Kodi simudawerenge chimene adachita Davide, pamene adali ndi njala, ndi iwo amene adali naye?

Mat 12:4 Kuti adalowa m’nyumba ya Mulungu, nadya mikate yowonetsa, imene idali yosaloleka kudya iye kapena amene adali naye, koma ansembe okhaokha.

Mat 12:5 Kapena simudawerenga kodi m’chilamulo, kuti tsiku la sabata ansembe m’kachisi amayipitsa tsiku la sabata, nakhala opanda tchimo?

Mat 12:6 Koma ndinena kwa inu, kuti woposa kachisiyo ali pompano.

Mat 12:7 Koma mukadadziwa n’chiyani ichi, ndifuna chifundo si nsembe ayi; simukadaweruza wolakwa iwo wosachimwa.

Mat 12:8 Pakuti Mwana wa munthu ali Mbuye mwini wa tsiku la Sabata.

Mat 12:9 Ndipo Iye adachokera pamenepo nalowa m’sunagoge mwawo;

Mat 12:10 Ndipo onani, mudali munthu wadzanja lopuwala. Ndipo adamfunsitsa Iye, ndi kuti, N’kuloleka kodi kuchiritsa tsiku la sabata? Kuti ampalamulitse mlandu.

Mat 12:11 Ndipo Iye adati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m’dzenje tsiku la sabata, kodi sadzayigwira ndikuyitulutsa.

Mat 12:12 Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa n’kotani? Chifukwa cha ichi n’kololeka kuchita zabwino tsiku la sabata.

Mat 12:13 Pomwepo adanena Iye kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako, ndipo iye adalitambasula, ndipo lidabwezedwa lamoyo longa limzake.

Mat 12:14 Pamenepo Afarisi adatuluka, nakhala upo womchitira Iye momwe angamuonongere.

Mat 12:15 Koma pamene Yesu adadziwa, adawachokera kumeneko; ndipo adamtsata Iye makamu akulu; ndipo Iye adawachiritsa iwo onse.

Mat 12:16 Ndipo adawalamulira ndi kuti asamuwulule Iye;

Mat 12:17 Kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi Yesaya m’neneri uja kuti;

Mat 12:18 Tawona mtumiki wanga, amene ndidamsankha, wokondedwa wanga amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzayika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa amitundu.

Mat 12:19 Sadzalimbana, sadzafuwula, ngakhale m’modzi sadzamva mawu ake m’makwalala;

Mat 12:20 Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzayizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.

Mat 12:21 Ndipo amitundu adzakhulupirira dzina lake.

Mat 12:22 Pomwepo adabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosayankhula; ndipo Iye adamchiritsa, kotero kuti wosanyankhulayo adayankhula, napenya.

Mat 12:23 Ndipo anthu onse adazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?

Mat 12:24 Koma Afarisi pakumva adati; Munthu uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebule,mkulu waziwanda.

Mat 12:25 Ndipo Yesu adadziwa maganizo awo, nati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mzinda uli wonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala;

Mat 12:26 Ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye wagawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake?

Mat 12:27 Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebule, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala woweruza anu.

Mat 12:28 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu wafika pa inu.

Mat 12:29 Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m’banja la munthu wolimba, ndi kuwononga akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzawononga za m’banja lake.

Mat 12:30 Iye wosakhala ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.

Mat 12:31 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse za mwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa.

Mat 12:32 Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoyipa, adzakhululukidwa; koma amene aliyense anganenere Mzimu Woyera zoyipa sadzakhululukidwa m`dziko lino kapena m`dziko liri mkudzalo.

Mat 12:33 Ukakoma mtengo chipatso chake chomwe chikoma; ukayipa mtengo, chipatso chake chomwe chiyipa; pakuti ndi chipatso chake, mtengo udziwika.

Mat 12:34 Wobadwa inu a njoka mungathe bwanji kuyankhula zabwino, inu wokhala woyipa? Pakuti m’kamwa mungoyankhula mwa kusefukira kwake kwa mtima.

Mat 12:35 Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma cha mtima wake wabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoyipa m’chuma chake choyipa.

Mat 12:36 Koma ndinena kwa inu, Kuti mawu onse wopanda pake, amene anthu adzayankhula, adzawawerenga mlandu wake tsiku lakuweruza.

Mat 12:37 Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mawu ako, ndipo ndi mawu ako omwe udzatsutsidwa.

Mat 12:38 Pomwepo mwa alembi ndi Afarisi ena adayankha nati, Mphunzitsi, tifuna kuwona chizindikiro chochokera kwa Inu.

Mat 12:39 Koma Iye adayankha nati kwa iwo, Wobadwa woyipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona m’neneri.

Mat 12:40 Pakuti monga Yona adali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu usana ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usana ndi usiku.

Mat 12:41 Anthu aku Nineve adzawuka pa mlandu pamodzi ndi wobadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo adalapa ndi kulalikira kwa Yona; ndipo onani, wamkulu woposa Yona ali pano.

Mat 12:42 Mfumukazi ya kumwera idzawuka pa mlandu pamodzi ndi wobadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye adachokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wamkulu woposa Solomo ali pano.

Mat 12:43 Pamene mzimu wonyansa, utuluka mwa munthu, umayenda nupitilira malo wopanda madzi kufunafuna mpumulo, koma osawupeza.

Mat 12:44 Pomwepo unena, ndidzabwerera kumka kunyumba kwanga, konkuja ndidatulukako; ndipo pakufikako uyipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.

Mat 12:45 Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu yina imzake isanu ndi iwiri yoyipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthuyo akhala woyipa woposa woyamba. Kotero kudzakhalanso kwa wobadwa woyipa amakono.

Mat 12:46 Pamene Iye adali chiyankhulire ndi anthu, onani, amake ndi abale ake adayima panja, nafuna kuyankhula naye.

Mat 12:47 Pamenepo m’modzi adati kwa Iye, Onani, amayi wanu ndi abale anu ayima pa bwalo, akufuna kuyankhula nanu.

Mat 12:48 Koma Iye adayankha, nati kwa iye wonenayo, Amayi wanga ndani? Ndi abale anga ndi ayani?

Mat 12:49 Ndipo adatambalitsa dzanja lake pa wophunzira ake, nati, Penyani amayi wanga ndi abale anga!

Mat 12:50 Pakuti ali yense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye m’bale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.



13

Mat 13:1 Tsiku lomwelo Yesu adatuluka m’nyumbamo, nakhala pansi m’mbali mwa nyanja.

Mat 13:2 Ndipo makamu ambiri wa anthu adasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye adalowa m`chombo, nakhala pansi, ndipo khamu lonse lidayima pamtunda.

Mat 13:3 Ndipo Iye adayankhula zinthu zambiri kwa iwo m’mafanizo, nanena, Onani, wofesa adatuluka kukafesa.

Mat 13:4 Ndipo m’kufesa kwake mbewu zina zidagwa m’mbali mwa njira ndipo zinadza mbalame, nizitolatola izo.

Mat 13:5 Zina zinagwa pa miyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zidamera koma zidalibe dothi la kuya:

Mat 13:6 Ndipo m’mene dzuwa lidakwera zidafota ndipo zidapserera; popeza zidalibe mizu yozama.

Mat 13:7 Ndipo zina zidagwera paminga, ndipo mingayo idayanga, nizitsamwitsa izo;

Mat 13:8 Koma zina zidagwera pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.

Mat 13:9 Iye amene ali ndi makutu akumva, amve.

Mat 13:10 Ndipo wophunzirawo adadza, nati kwa Iye, chifukwa chiyani muyankhula ndi iwo m’mafanizo?

Mat 13:11 Iye adayankha nati kwa iwo, chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa kumwamba, koma sikudapatsidwa kwa iwo.

Mat 13:12 Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndipo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.

Mat 13:13 Chifukwa chake ndiyankhula kwa iwo m’mafanizo; Chifukwa kuti akuwona koma wosaonetsetsa, ndi akumva koma wosamvetsetsa, kapena samadziwitsitsa.

Mat 13:14 Ndipo mwa iwo mwadzaza uneneri wa Yesaya, amene adati, pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzawona konse;

Mat 13:15 Chifukwa udalemera mtima wa anthu awa, ndipo m’makutu mwawo adamva mogontha, ndipo maso awo adatsinzina; kuti asawone konse ndi maso awo, asamve ndi makutu awo, asazindikire ndi mtima wawo, asatembenuke ndipo ndisawachiritse iwo.

Mat 13:16 Koma maso anu ali wodala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva.

Mat 13:17 Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu wolungama adalakalaka kupenya zimene muziwona, koma sadaziwona; ndi kumva zimene muzimva, koma sadazimva.

Mat 13:18 Ndipo tsono mverani inu fanizo la wofesa.

Mat 13:19 Munthu aliyense wakumva mawu a Ufumu, osawadziwitsayi, woyipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m’mbali mwa njira.

Mat 13:20 Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mawu, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;

Mat 13:21 Ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaying’ono; ndipo pakudza msautso kapena mazunzo chifukwa cha mawu, iye akhumudwa pomwepo.

Mat 13:22 Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mawu; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mawu,ndipo akhala wopanda chipatso.

Mat 13:23 Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mawu nawadziwitsa; amene abaladi chipatso, nafikitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.

Mat 13:24 Fanizo lina Iye adawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu amene adafesa mbewu zabwino m’munda mwake;

Mat 13:25 Koma pamene anthu adalimkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati patirigu, nachokapo.

Mat 13:26 Koma pamene m’mela udakula nubala chipatso, pomwepo adawonekeranso namsongole.

Mat 13:27 Ndipo atumiki ake a mwini nyumbayo adadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simudafesa mbewu zabwino m’munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo?

Mat 13:28 Ndipo iye adanena kwaiwo, munthu m’dani wanga wachichita ichi. Ndipo atumiki adati kwa iye, kodi mufuna tsopano kuti tipite, tikansonkhanitse uyo pamodzi?

Mat 13:29 Koma iye adati, ayi, kuti kapena m’mene musonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.

Mat 13:30 Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m’nyengo yakututa ndidzawuza wotutawo, muyambe kusonkhanitsa namsongole, mum’mange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m’nkhokwe yanga.

Mat 13:31 Fanizo lina Iye adawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi kambewu kampiru, kamene adakatenga munthu, nakafesa pa munda pake;

Mat 13:32 Kamene kakhaladi kakang’ono koposa mbewu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mumlengalenga zimadza, nizibindikira munthambi zake.

Mat 13:33 Fanizo lina adanena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chotupitsa mkate, chimene mkazi adachitenga, nachibisa m’miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse udatupa.

Mat 13:34 Zinthu zonsezi Yesu adaziyankhula m’mafanizo kwa makamu; ndipo kopanda fanizo sadayankhula kanthu kwa iwo.

Mat 13:35 Kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi m’neneri, kuti Ndidzatsegula pakamwa panga m`mafanizo kuwulula zinthu zobisika zimene chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.

Mat 13:36 Pomwepo Yesu adabalalitsa makamuwo, Iye nalowa m’nyumba; ndimo wophunzira ake adadza kwa Iye, nanena, mutitanthawuzire fanizo lija la namsongole wa m’munda.

Mat 13:37 Iye adawayankha nati kwa iwo, Wofesa mbewu yabwino ndiye Mwana wa munthu;

Mat 13:38 Munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbewu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woyipayo;

Mat 13:39 Mdani amene adafesa uyu, ndiye m’dierekezi; ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi wotutawo ndiwo angelo.

Mat 13:40 Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, motero mudzakhala m’chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mat 13:41 Mwana wa munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi iwo wochita kusayeruzika,

Mat 13:42 Ndipo adzawataya iwo m’ng’anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mat 13:43 Pomwepo wolungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu akumva amve.

Mat 13:44 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m’munda; chimene munthu adachipeza, nachibisa; ndipo m’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse adali nazo, nagula munda umenewu.

Mat 13:45 Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wofuna ngale zabwino;

Mat 13:46 Amene adayipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, adapita, nagulitsa zonse adali nazo nayigula imeneyo.

Mat 13:47 Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m’nyanja, limene lidasonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse.

Mat 13:48 Limene podzaza adalibvuwulira pa mtunda; ndipo m’mene adakhala pansi, adasonkhanitsa zabwino mu zotengera, koma zoyipa adazitaya kuthengo.

Mat 13:49 Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; angelo adzatuluka, nadzawasankhula woyipa pakati pa abwino.

Mat 13:50 Nadzawataya iwo m’ng’anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukuta mano.

Mat 13:51 Yesu adati kwa iwo, mwamvetsetsa zonsezi kodi? Iwo adati kwa Iye, Inde Ambuye.

Mat 13:52 Pamenepo Iye adati kwa iwo, chifukwa chake mlembi ali yense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m’chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.

Mat 13:53 Ndipo panali, pamene Yesu adatha mafanizo awa, adachoka kumeneko.

Mat 13:54 Ndipo pamene adafika kudziko la kwawo, adaphunzitsa iwo m’masunagoge mwawo, kotero kuti adazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi ntchito zamphamvu izi?

Mat 13:55 Kodi uyu si mwana wa m’misiri wamatabwa? Kodi dzina lake la amake si Mariya? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda

Mat 13:56 Ndipo alongo ake Sali ndi ife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti?

Mat 13:57 Ndipo iwo adakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu adati kwa iwo, M’neneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko la kwawo ndiko, ndi kubanja kwake.

Mat 13:58 Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, sadachita kumeneko ntchito zamphamvu zambiri.



14

Mat 14:1 Nthawi imeneyo Herode mfumu adamva mbiri ya Yesu.

Mat 14:2 Ndipo adati kwa atumiki ake, Uyu Yohane M`batizi; adawuka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi ntchito zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye.

Mat 14:3 Pakuti Herode adamgwira Yohane, nam’manga, namuyika m’nyumba yandende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa m’bale wake Filipo.

Mat 14:4 Pakuti Yohane adanena kwa iye, sikuloledwa kwa iwe kukhala naye.

Mat 14:5 Ndipo pofuna kumupha iye, adawopa khamu la anthu, popeza adamuyesa iye m’neneri.

Mat 14:6 Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiya adabvina pakati pawo, namkondweretsa Herode.

Mat 14:7 Pomwepo iye adamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chiri chonse akapempha.

Mat 14:8 Ndipo iye atampangira amake, adati, Ndipatseni ine kuno m’mbale mutu wa Yohane M’batizi.

Mat 14:9 Ndipo Mfumuyo idamva chisoni koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo adali naye pachakudya, adalamulira kuti upatsidwe kwa iye;

Mat 14:10 Ndipo adawatumiza kukadula mutu wa Yohane m’nyumba yandende.

Mat 14:11 Ndipo adawutenga mutu wake m’mbalemo, napatsa buthulo; ndipo iye adamuka nawo kwa amake.

Mat 14:12 Ndipo wophunzira ake adadza, natenga thupi, naliyika m`manda; ndipo adadza nawuza Yesu.

Mat 14:13 Ndipo Yesu pakumva, adachokera kumeneko m’chombo, kupita ku malo a chipululu pa yekha; ndipo anthu, pamene adamva, adamtsata Iye poyenda pamtunda kuchokera m’mizinda.

Mat 14:14 Ndipo Yesu adatuluka, nawona khamu lalikulu, ndipo adagwidwa ndi chifundo ndipo anachiritsa wodwala awo.

Mat 14:15 Ndipo pamene panali madzulo, wophunzira ake adafika kwa Iye, nanena, Malo ano ngachipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kawuzeni khamulo lidzipita ku midzi likadzigulire lokha kamba.

Mat 14:16 Koma Yesu adati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa chopitira, apatseni ndinu adye.

Mat 14:17 Ndipo iwo adanena kwa Iye, Ife tiribe kanthu pano koma mikate isanu ndi nsomba ziwiri.

Mat 14:18 Ndipo Iye adati, Mudze nazo kuno kwa Ine.

Mat 14:19 Ndipo Iye adalamulira khamulo kuti likhale pansi pa udzu; ndipo Iye adatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m’mene adayang’ana Kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa wophunzira ake ndi wophunzira kwa khamulo.

Mat 14:20 Ndipo adadya onse, nakhuta; ndipo adatola makombo wotsala, mitanga khumi ndi iwiri yodzala.

Mat 14:21 Ndipo adadyawo adali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.

Mat 14:22 Ndipo pomwepo Iye adafulumiza wophunzira alowe m’chombo, ndi kumtsogolera Iye ku tsidya lina, kufikira Iye atawuza makamu apite.

Mat 14:23 Ndipo pamene Iye adawawuza makamuwo kuti achoke, adakwera m’phiri pa yekha kukapemphera: ndipo pamene padali madzulo, Iye adakhala kumeneko yekha.

Mat 14:24 Koma chombo tsopano chidafika pakati pa nyanja, chozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo idadza mokomana nacho.

Mat 14:25 Ndipo pa ulonda wa chinayi wa usiku, Yesu adadza kwa iwo, akuyenda pamwamba pa nyanja.

Mat 14:26 Ndipo m’mene wophunzirawo adamuwona Iye, alikuyenda panyanja, adanthunthumira, nati, Ndi mzukwa! Ndipo adafuwula ndi mantha.

Mat 14:27 Koma pomwepo Yesu adayankhula nawo, nati, Kondwerani; Ndine; musaope.

Mat 14:28 Ndipo Petro adamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiwuze ndidze kwa inu pamadzi.

Mat 14:29 Ndipo Iye adati, Idza. Ndipo pamene Petro adatsika m’chombo, nayenda pamwamba pamadzi, kupita kwa Yesu.

Mat 14:30 Koma m’mene iye adawona mphepo yamkuntho, adawopa; ndipo adayamba kumira, nafuwula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!

Mat 14:31 Ndipo pomwepo Yesu adatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, iwe wokhulupirira pang’ono, wakayikiranji mtima?

Mat 14:32 Ndipo pamene iwo adalowa m’chombomo, mphepo idaleka.

Mat 14:33 Pamenepo iwo amene adali m’chombomo adampembedza Iye, nanena, Zowonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.

Mat 14:34 Ndipo pamene iwo adawoloka, adafika kumtunda, ku Genesarete.

Mat 14:35 Ndipo m’mene amuna a pamenepo adamzindikira Iye, adatumiza ku dziko lonse lozungulira, nadza nawo kwa Iye onse wokhala ndi nthenda.

Mat 14:36 Ndipo adampempha Iye, kuti angokhudza kokha mphonje yachobvala chake; ndipo onse amene adamkhudza adachiritsidwa.



15

Mat 15:1 Pomwepo adadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, wochokera ku Yerusalemu, nati,

Mat 15:2 Kodi chifukwa chiyani wophunzira anu akulumpha miyambo ya akulu? Pakuti sasamba manja awo pakudya mkate?

Mat 15:3 Koma Iye adayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?

Mat 15:4 Pakuti Mulungu adalamulira kuti, lemekeza atate wako ndi amako; ndipo wotemberera atate wake ndi amake, afe ndithu.

Mat 15:5 Koma inu munena, aliyense wonena kwa atate wake kapena amake, Mphatso iyi ndi ya Mulungu ndipo simungathe kulandira thandizo kuchokera kwa ine;

Mat 15:6 Ndipo nakhala wosalemekeza atate wake kapena amake adzakhala wopanda m`mlandu. Inu mupeputsa malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.

Mat 15:7 Wonyenga inu! Yesaya adanenera bwino za inu, ndi kuti,

Mat 15:8 Anthu awa ayandikira chifupi ndi Ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo ulikutali ndi Ine.

Mat 15:9 Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa ziphunzitso, malangizo wa anthu.

Mat 15:10 Ndipo Iye adayitana khamulo, nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;

Mat 15:11 Sichimene chilowa m’kamwa mwake chiyipitsa munthu; koma chimene chituluka m’kamwa mwake, ndicho chiyipitsa munthu.

Mat 15:12 Pomwepo adadza wophunzira ake, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi adakhumudwa pakumva chonenacho?

Mat 15:13 Koma Iye adayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa kumwamba sadawubzala, udzazulidwa.

Mat 15:14 Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwera m’mbuna.

Mat 15:15 Pamenepo Petro adayankha nati kwa Iye, mutifotokozere ife fanizoli.

Mat 15:16 Ndipo Yesu adati, Kodi inunso muli wosazindikira?

Mat 15:17 Kodi simudziwa kuti zonse zolowa m’kamwa zipita m’mimba, ndipo zitayidwa kuthengo?

Mat 15:18 Koma zotuluka m’kamwa zichokera mumtima; ndizo ziyipitsa munthu.

Mat 15:19 Pakuti mumtima muchokera maganizo woyipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama ndi zamwano.

Mat 15:20 Izi ndizo ziyipitsa munthu,koma kudya osasamba manja sikuyipitsa munthu ayi.

Mat 15:21 Pamenepo Yesu adatulukapo napatukira ku mbali za Turo ndi Sidoni.

Mat 15:22 Ndipo, Onani, mkazi wa ku Kenani adatuluka m’malire, nafuwulira kwa Iye, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye Mwana wa Davide; mwana wanga wa mkazi wabvutitsidwa kowopsa ndi chiwanda.

Mat 15:23 Koma Iye sadamyankha ngakhale mawu amodzi. Ndipo wophunzira ake adadza, nampempha Iye, nati, Mumuwuze apite; pakuti afuwula pambuyo pathu.

Mat 15:24 Koma Iye adayankha nati, Sindidatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israyeli.

Mat 15:25 Pamenepo iye adadza, nampembedza Iye nanena, Ambuye, ndithangateni ine.

Mat 15:26 Koma Iye adayankha nati, Sichabwino kutenga chakudya cha ana, ndi kuponyera agalu.

Mat 15:27 Ndipo iye adati, Zowona, Ambuye, pakutinso agalu amadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye wawo.

Mat 15:28 Pomwepo Yesu adayankha nati kwa iye, mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake adachira nthawi yomweyo.

Mat 15:29 Ndipo Yesu adachoka kumeneko, nadza ku nyanja ya Galileya, nakwera m’phiri, nakhala pansi pamenepo.

Mat 15:30 Ndipo makamu ambiri adadza kwa Iye, ali nawo wopunduka miyendo, akhungu, osayankhula, wopunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake; ndipo Iye adawachiritsa;

Mat 15:31 Kotero kuti khamulo lidazizwa pamene adawona osayankhula nayankhula, wopunduka ziwalo nachira, ndi wopunduka miyendo nayenda, ndi a khungu napenya ndipo iwo adalemekeza Mulungu wa Israyeli;

Mat 15:32 Pamenepo Yesu adayitana wophunzira ake kwa Iye, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamuli la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya ndipo sindifuna kuwawuza iwo apite osadya, kuti angakomoke panjira.

Mat 15:33 Ndipo wophunizira ake adanena kwa Iye, tiyiwona kuti mikate yotere m’chipululu yokhutitsa unyinji wotere wa anthu?

Mat 15:34 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo adati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang’ono.

Mat 15:35 Ndipo Iye adalamulira khamulo kuti likhale pansi;

Mat 15:36 Ndipo adatenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika, nanyema, napatsa kwa wophunizira ake, ndi wophunzira ake kwa makamuwo,

Mat 15:37 Ndipo onsewo adadya, nakhuta; ndipo adatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzadza.

Mat 15:38 Ndipo amene adadyawo adali amuna zikwi zinayi kuwaleka akazi ndi ana.

Mat 15:39 Ndipo adawawuza makamuwo kuti apite,ndipo adalowa m’chombo, nafika m’malire a Magadala.



16

Mat 16:1 Afarisi ndi Asaduki adabweranso, namuyesa, namfunsa Iye kuti awawonetse chizindikiro cha Kumwamba.

Mat 16:2 Iye adayankha, nati kwa iwo, Pamene pakhala madzulo munena, kudzakhala ngwe; popeza thambo liri lacheza.

Mat 16:3 Ndipo m’mawa, Lero n’kwamphepo: popeza thambo liri la cheza chodera.Wonyenga inu mudziwa kuzindikira za nkhope yake ya thambo; koma simuzindikira zizindikiro za nyengo yino.

Mat 16:4 Wobadwa woyipa ndi a chigololo wofunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona m`neneri. Ndipo Iye adawasiya, nachokapo.

Mat 16:5 Ndipo pamene wophunzira adafika tsidya linalo, adayiwala kutenga mikate.

Mat 16:6 Pamenepo Yesu adati kwa iwo, chenjerani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.

Mat 16:7 Ndipo iwo adafunsana wina ndi mnzake, nati, Kodi ndi chifukwa kuti sitidatenge mikate?

Mat 16:8 Koma Yesu, m’mene adadziwa, adati, Ha, inu wokhulupirira pan’gono, mufunsana chifukwa chiyani wina ndi mzake, chifukwa kuti simudatenge mikate?

Mat 16:9 Kodi simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya zikwi zisanu, ndi mitanga ingati mudayitola?

Mat 16:10 Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya zikwi zinayi, ndi madengu angati mudatola?

Mat 16:11 Bwanji nanga simukudziwa kuti sindidanena kwa inu za mikate? Koma pewani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki.

Mat 16:12 Pomwepo adadziwitsa kuti sadawawuza kupewa chotupitsa cha mkate, koma chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.

Mat 16:13 Pamene Yesu, adadza kudziko la ku Kayisareya wa Filipi, adafunsa wophunzira ake, kuti, anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani?

Mat 16:14 Ndipo iwo adati, Ena ati, ndinu Yohane M’batizi; koma ena Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena m’modzi wa aneneri.

Mat 16:15 Iye adanena kwa iwo, koma inu mukuti ndine yani?

Mat 16:16 Ndipo Simoni Petro adayankha nati, Inu ndinu Khristu Mwana wa Mulungu wamoyo.

Mat 16:17 Ndipo Yesu adayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Ba-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizidakuwululira ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.

Mat 16:18 Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanhtwe ili ndidzamanga mpingo wanga; ndipo zipata za gahena sizidzawungonjetsa uwo.

Mat 16:19 Ndipo ndidzakupatsa iwe mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene chili chonse uchimanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba; ndipo chimene chilichonse uchimasula pa dziko lapansi chidzakhala chomasulidwa Kumwamba.

Mat 16:20 Pamenepo adalamulira wophunzira ake kuti asawuze munthu kuti Iye ndiye Yesu Khristu.

Mat 16:21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu adayamba kuwalangiza wophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu ndi, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa; ndi tsiku lachitatu kuwuka kwa akufa.

Mat 16:22 Ndipo Petro adamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Chikhale kutali ndi Inu, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ayi.

Mat 16:23 Koma Iye adapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chokhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu koma za anthu.

Mat 16:24 Pomwepo Yesu adati kwa wophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.

Mat 16:25 Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya; ndipo iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza.

Mat 16:26 Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake/ kapena munthu adzaperekanji chosinthana ndi moyo wake?

Mat 16:27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera mphoto kwa munthu aliyense monga mwa ntchito zake.

Mat 16:28 Indetu ndinena kwa inu, Kuti alipo ena a iwo ayima pano amene sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzawona Mwana wa munthu akudza mu Ufumu wake.



17

Mat 17:1 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane m’bale wake, napita nawo pa wokha pa phiri lalitali.

Mat 17:2 Ndipo Iye adasandulika pamaso pawo; ndipo nkhope yake idawala monga dzuwa, ndi chobvala chake chidakhala choyera mbu monga kuwala.

Mat 17:3 Ndipo onani, Mose ndi Eliya adawonekera kwa iwo, alimkuyankhula ndi Iye.

Mat 17:4 Pamenepo Petro adayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola kuti timange pano mahema atatu; imodzi ya Inu, ndi yina ya Mose, ndi yina ya Eliya.

Mat 17:5 Akali chiyankhulire, onani, mtambo wowala udawaphimba iwo; ndipo onani, mawu ali kutuluka mumtambo akunena, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa mwa Iyeyu ndisangalitsidwa, mverani Iye.

Mat 17:6 Ndipo pamene wophunzira adamva, adagwa nkhope zawo pansi, nawopa kwakukulu.

Mat 17:7 Ndipo Yesu adadza, nawakhudza iwo nati, Ukani, musamawopa.

Mat 17:8 Ndipo pamene adakweza maso awo, sadawona munthu, koma Yesu yekha.

Mat 17:9 Ndipo pamene adali kutsika pa phiri, Yesu adawalamulira iwo kuti, Musakawuze munthu masomphenyawo, kufikira Mwana wa Munthu atadzawuka kwa akufa.

Mat 17:10 Ndipo wophunzira ake adamfunsa Iye, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza?

Mat 17:11 Ndipo Yesu adayankha, nati kwa iwo, Eliya zowonadi ayenera ayambe kudza, nadzabwezeretsa zinthu zonse.

Mat 17:12 Koma ndinena kwa inu, Kuti Eliya adadza kale, ndipo iwo sadamdziwa iye, koma adamchitira zonse zimene zidalembedwa.

Mat 17:13 Pomwepo wophunzira adazindikira kuti adayankhula nawo za Yohane M’batizi.

Mat 17:14 Ndipo pamene iwo adadza ku khamulo, kudafika kwa Iye munthu, nam’gwadira Iye, nati,

Mat 17:15 Ambuye, chitirani wana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, akuzunzika koyipa; pakuti amagwa kawiri kawiri pamoto, ndi kawiri kawiri m’madzi.

Mat 17:16 Ndipo ndidadza naye kwa wophunzira anu, koma iwo sadathe kumchiritsa.

Mat 17:17 Ndipo Yesu adayankha nati, Ha, wobadwa wosakhulupilira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? M`bweretseni kwa Ine.

Mat 17:18 Ndipo Yesu adamdzudzula woyipayo: ndipo adatuluka mwa iye; ndipo mwanayo adachiritsidwa kuyambira nthawi yomweyo.

Mat 17:19 Pamenepo wophunzira adadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, chifukwa chiyani ife sitidakhoza kumtulutsa iye?

Mat 17:20 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, chifukwa chakusakhulupirira kwanu: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri ili, senderapo upite kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakhala kosatheka ndi inu.

Mat 17:21 Mtundu uwu sutuluka wamba koma pokhapokha umatuluka ndi pemphero ndi kusala kudya.

Mat 17:22 Ndipo m’mene adali kukhalabe m’Galileya, Yesu adanena nawo, Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja a anthu;

Mat 17:23 Ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzawukitsidwanso tsiku lachitatu. Ndipo iwo adali ndi chisoni chachikulu.

Mat 17:24 Ndipo pamene adafika ku Kapenawo amene aja wolandira ndalama za msonkho adadza kwa Petro ndipo adati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka msonkho?

Mat 17:25 Iye adabvomeza Inde, apereka. Ndipo pamene iye amalowa m’nyumba, Yesu adatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana awo kodi, kapena kwa alendo.

Mat 17:26 Petro adati kwa iye, kwa alendo. Yesu adanena kwa iye, Ndiye kuti anawo ali a ufulu.

Mat 17:27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuyitole nsomba yoyamba kuyiwedza; ndipo ukayikanula pakamwa pake udzapezamo ndalama; tatenga imeneyi; nuwapatse iyo pa iwe ndi ine.



18

Mat 18:1 Nthawi yomweyo wophunzira adadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wamkulukulu mu Ufumu wa Kumwamba?

Mat 18:2 Ndipo Yesu adayitana kamwana kakang`ono nakayimika pakati pawo.

Mat 18:3 Ndipo adati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka mtima, nimukhala ngati tianato, simudzalowa konse mu ufumu wa Kumwamba.

Mat 18:4 Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wamkulukulu mu Ufumu wa Kumwamba.

Mat 18:5 Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka chifukwa cha dzina langa, alandira Ine;

Mat 18:6 Koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi katiana iti, takukhulupilira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yayikulu yamwala ikolowekedwe m’khosi mwake, namizidwe pakuya panyanja.

Mat 18:7 Tsoka liri ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka liri ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye!

Mat 18:8 Chomwecho ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; n’kwabwino kuti ulowe moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m’moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri.

Mat 18:9 Ndipo ngati diso likukhumudwitsa, ulikolowore, nulitaye; n’kwabwino kuti ulowe m’moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa m’gehena wa moto, uli ndi maso awiri.

Mat 18:10 Yang`anirani kuti musanyoza m’modzi wa ang’ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo awo apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

Mat 18:11 Pakuti Mwana wa Munthu adadza kudzapulumutsa chotayikacho.

Mat 18:12 Mukuganiza motani? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi,ndipo isokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, napita kumapiri, kukafunafuna yosokerayo?

Mat 18:13 Ndipo ngati ayipeza, indetu ndinena kwa inu, akondwera koposa chifukwa cha nkhosayo ndi makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi zosasokera.

Mat 18:14 Chomwecho sichiri chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti m’modzi wa ang’ono awa atayike.

Mat 18:15 Chomwecho ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numuwuze panokha iwe ndi iye, ngati akumvera iwe, wam’bweza mbale wako.

Mat 18:16 Koma ngati sakumvera iwe, wonjeza kutenga ndi iwe wina m’modzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.

Mat 18:17 Ndipo ngati iye samvera iwo, uwuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga munthu wakunja ndi wamsonkho.

Mat 18:18 Indetu ndinena kwa inu, Ziri zonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba; ndipo ziri zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.

Mat 18:19 Ndiponso ndinena kwa inu, Kuti ngati awiri a inu abvomerezana pansi pano chinthu chiri chonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira.

Mat 18:20 Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndiri komweko pakati pawo.

Mat 18:21 Pamenepo Petro anadza kwa Iye nati, Ambuye, m`bale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi?

Mat 18:22 Yesu adanena kwa iye, sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.

Mat 18:23 Chifukwa chake Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi, mfumu ina amene adafuna kuwerengera nawo atumiki ake.

Mat 18:24 Ndipo pamene adayamba kuwerengera, adadza kwa iye ndi wina wa mangawa a ndalama za matalente zikwi khumi.

Mat 18:25 Koma popeza iye adasowa kanthu kom’bwezera, mbuye wake adalamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse adali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.

Mat 18:26 Mtumikiyo choncho adagwa pansi, nampembedza, nati,Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzakubwezerani inu.

Mat 18:27 Pamenepo mbuye wa mtumikiyo adagwidwa ndi chisoni mumtima, nam’masula iye, namkhululukira ngongoleyo.

Mat 18:28 Koma mtumiki uyu, potuluka adapeza wina wa atumiki amzake yemwe adamkongola iye malupiya zana, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Ndibwezere zija udandikongola.

Mat 18:29 Ndipo mtumiki mzakeyu adagwa pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekezera ine, ndipo ndidzakubwezera iwe yonse.

Mat 18:30 Ndipo iye sadafuna; koma adapita, namponya iye m’nyumba yandende, kufikira atam’bwezera ngongole.

Mat 18:31 Choncho pamene mtumiki amzake adawona zochitidwazo, adagwidwa ndi chisoni chachikulu, nadza, nafotokozera mbuye wawo zonse zimene zidachitidwa.

Mat 18:32 pomwepo mbuye wake adamuyitana iye, nanena naye, kapolo iwe woyipa ndidakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja udandipempha ine;

Mat 18:33 Kodi iwenso sukadamchitira mtumiki mzako chisoni, monga inenso ndidakuchitira iwe chisoni?

Mat 18:34 Ndipo mbuye wake adakwiya, nampereka kwa azunzi kufikira akabwezere iye mangawa onse.

Mat 18:35 Chomwecho Atate wanga wa Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense m’bale wake ndi mitima yanu.



19

Mat 19:1 Ndipo panali pamene Yesu adatha mawu amenewa, adachokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordano.

Mat 19:2 Ndipo makamu akulu adamtsata Iye; ndipo Iye adawachiritsa kumeneko.

Mat 19:3 Ndipo Afarisi adadzanso kwa Iye, namuyesa Iye, nanena kwa Iye, Kodi n’kololedwa kuti munthu achotse mkazi wake pachifukwa chiri chonse?

Mat 19:4 Ndipo Iye adayankha, nati kwa iwo, Kodi simudawerenga kuti Iye amene adapanga iwo pachiyambi, adawapanga iwo mwamuna ndi mkazi.

Mat 19:5 Ndipo adati, pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?

Mat 19:6 Kotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu adachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.

Mat 19:7 Iwo adanena kwa Iye, Nanga n’chifukwa chiyani Mose adalamulira kupatsa kalata wa chilekaniro, ndi kumchotsa?

Mat 19:8 Iye adanena kwa iwo, chifukwa cha kuwuma mtima kwanu, Mose adakulolezani kumchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikudakhala chomwecho.

Mat 19:9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene ali yense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chiwerewere, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndi iye amene akwatira wochotsedwayo achita chigololo.

Mat 19:10 Wophunzira ake adanena kwa Iye, ndipo ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.

Mat 19:11 Koma Iye adati kwa iwo, Anthu onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa.

Mat 19:12 Pakuti pali osabala, amene anabadwa wotero m’mimba ya amawo: ndipo pali osabala ena adawafula anthu; ndipo pali osabala ena amene adadzifula wokha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.

Mat 19:13 Pamenepo anadza nato tiana tating`ono kwa Iye, kuti Iye ayike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma wophunzirawo adawadzudzula.

Mat 19:14 koma Yesu adati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine; chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.

Mat 19:15 Ndipo Iye adayika manja ake pa ito, nachokapo.

Mat 19:16 Ndipo onani, m’modzi anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, wabwino, chabwino n’chiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?

Mat 19:17 Ndipo Iye adati kwa iye, unditcha bwanji kuti ndine wabwino? Kulibe wabwino, koma m’modzi, ndiye Mulungu: koma ngati ufuna kulowa m’moyo, sunga malamulo.

Mat 19:18 Iye adanena kwa iye Wotani? Yesu adati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama.

Mat 19:19 Lemekeza atate wako ndi amako, ndipo, Udzikonda mzako monga udzikonda iwe mwini.

Mat 19:20 M’nyamata wachichepereyo adanena kwa Iye, Zonsezi ndidazisunga kuyambira ndiri mwana, ndisowanso chiyani?

Mat 19:21 Yesu adanena kwa iye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.

Mat 19:22 Koma pamene m’nyamatayo adamva chonenacho, adapita ali wachisoni; pakuti adali nacho chuma chambiri.

Mat 19:23 Pamenepo Yesu adati kwa wophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti wa chuma adzalowa mobvutika mu Ufumu wa Kumwamba.

Mat 19:24 Ndiponso ndinena kwa inu, N’kwapafupi kuti ngamila ipyole pa diso la singano, koposa munthu wa chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.

Mat 19:25 Pamene wophunzira ake adamva ichi, adazizwa kwambiri, nanena, Ngati n’kutero angapulumuke ndani?

Mat 19:26 Koma Yesu adawayang’ana iwo, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.

Mat 19:27 Pomwepo adayankha Petro, nati kwa Iye, Onani, ife tidasiya zonse ndi kutsata inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?

Mat 19:28 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Kuti inu amene mudanditsata Ine, n’kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.

Mat 19:29 Ndipo ali yense amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena mkazi, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa mazanamazana, nadzalowa moyo wosatha.

Mat 19:30 Koma ambiri woyamba adzakhala akumapeto, ndi akumapeto adzakhala woyamba.



20

Mat 20:1 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene adatuluka mamawa kukalembera antchito m’munda wake wampesa.

Mat 20:2 Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa khobiri limodzi patsiku, ndipo iye adawatumiza iwo kumunda wake.

Mat 20:3 Ndipo iye adatuluka kubwalo pa ola la chitatu, nawona ena atangoyima pa malo wochitira malonda.

Mat 20:4 Ndipo adati kwa iwo, Pitani inunso kumunda wa mpesa, ndipo ndidzakupatsani chimene chiri choyenera. Ndipo iwo adapita.

Mat 20:5 Ndiponso adatuluka pa ola la chisanu ndi limodzi ndinso la chisanu ndi chinayi nachita chimodzi modzi.

Mat 20:6 Ndipo pa ora la khumi ndi limodzi adatuluka, napeza ena atangoyima chabe, ndipo adati kwa iwo, Chifukwa chiyani mwangoyima pano chabe tsiku lonse?

Mat 20:7 Iwo adanena kwa iye, chifukwa palibe munthu adatilemba. Iye adati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa; ndipo ndidzakupatsani chimene chiri choyenera.

Mat 20:8 Ndipo pakufika madzulo, mwini munda adati kwa kapitawo wake, Kayitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwawo, uyambe kwa womarizira kufikira kwa woyamba.

Mat 20:9 Ndipo pamene adafika kwa iwo wolembedwawo pa ora la khumi ndi limodzi munthu aliyense adalandira khobiri.

Mat 20:10 Koma pamene woyamba adadza, adalingalira kuti adzalandira zambiri, ndipo iwonso adalandira onse khobiri.

Mat 20:11 Ndipo m’mene iwo adalandira, anadandawula motsutsana ndi mwini nyumba wa bwinoyo.

Mat 20:12 Nati, Omalizira awa adagwira ntchito kwa ola limodzi, ndipo mudawalinganiza ndi ife amene tidapilira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake kwa tsiku.

Mat 20:13 Koma iye adayankha m’modzi wa iwo, ndipo adati; Mzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sudapangana ndi ine pa khobiri limodzi?

Mat 20:14 Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe.

Mat 20:15 Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako layipa kodi chifukwa ine ndiri wabwino?

Mat 20:16 Chomwecho omalizira adzakhala woyamba, ndipo woyamba womalizira pakuti woyitanidwa ndi ambiri koma wosankhidwa ndi wowerengeka.

Mat 20:17 Ndipo pamene Yesu adalikukwera ku Yerusalemu, adatenga wophunzira khumi ndi awiri aja napita nawo pa wokha, ndipo panjira adati kwa iwo,

Mat 20:18 Onani tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi, ndipo iwo adzamutsutsa kuti ayenera imfa.

Mat 20:19 Ndipo adzampereka kwa anthu amitundu kuti am’nyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika Iye; ndipo Iye adzawukitsidwa tsiku lachitatu.

Mat 20:20 Pomwepo adadza kwa Iye amake a ana a Zebedayo ndi ana ake omwe, nampembedza ndi kumpempha kanthu kena.

Mat 20:21 Ndipo Iye adati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye adanena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu la manja, ndi wina kulamanzere, mu Ufumu wanu.

Mat 20:22 Koma Yesu adayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Ndikubatizidwa ubatizo umene ndibatizidwa nawo? Iwo adanena kwa Iye, Ife tikhoza.

Mat 20:23 Iye adanena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi,ndikubatizidwa ubatizo ndi batizidwa nawo, koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kudzapatsidwa kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga

Mat 20:24 Ndipo m’mene khumiwo adamva, adapsa mtima ndi abale awiriwo.

Mat 20:25 Koma Yesu adawayitana, nati kwa iwo, Mudziwa kuti mafumu amitundu amachita ufumu pa iwo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo.

Mat 20:26 Koma sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma aliyense amene akufuna kukhala wamkulu, mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;

Mat 20:27 Ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;

Mat 20:28 Monga Mwana wa Munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo kwa anthu ambiri.

Mat 20:29 Ndipo pamene iwo analikutuluka mu Yeriko, khamu lalikulu lidamtsata Iye.

Mat 20:30 Ndipo onani, amuna akhungu awiri adakhala m’mphepete mwa njira; m’mene iwo adamva kuti Yesu adalikupitilirapo, adafuwula nati, Mutichitire ife chifundo Ambuye, Inu Mwana wa Davide.

Mat 20:31 Ndipo khamulo lidawadzudzula iwo, kuti atonthole; koma adakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide.

Mat 20:32 Ndipo Yesu adayima, nawayitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitire chiyani?

Mat 20:33 Iwo adanena kwa Iye Ambuye, kuti maso athu aphenyuke.

Mat 20:34 Ndipo Yesu adagwidwa chifundo ndi iwo, ndipo adakhudza maso awo; ndipo pomwepo adapenyanso, namtsata Iye.



21

Mat 21:1 Ndipo pamene iwo adayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, ku phiri la Azitona, pamenepo Yesu adatumiza wophunzira awiri;

Mat 21:2 Nanena kwa iwo, Mukani ku mudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nawo kwa Ine.

Mat 21:3 Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye afuna iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.

Mat 21:4 Ndipo ichi chidatero, kuti chikakwaniritsidwe chonenedwa ndi m’neneri kuti,

Mat 21:5 Tawuzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Tawona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.

Mat 21:6 Ndipo wophunzirawo adapita, nachita monga Yesu adawalamulira iwo;

Mat 21:7 Ndipo anabwera ndi bulu ndi mwana wake, nayika pa iwo zobvala zawo, nakhazika Iye pamenepo.

Mat 21:8 Ndipo chikhamu chachikulucho chidayala zobvala zawo panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo naziyala m’njiramo.

Mat 21:9 Ndipo makamuwo akumtsogolera ndi akumtsatira, adafuwula, kuti, Hossana kwa Mwana wa Davide! Wodalitsika ndiye wakudza m’dzina la Ambuye! Hossana Wam`mwamba mwamba!

Mat 21:10 Ndipo m’mene adalowa mu Yerusalemu muzinda wonse udasokonezeka, nanena, Ndani uyu?

Mat 21:11 Ndipo makamu adati, Uyu ndi m’neneri Yesu wa ku Nazarete wa Galileya.

Mat 21:12 Ndipo Yesu adalowa ku kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse wogulitsa ndi kugula malonda, nagudubuza magome a wosintha ndalama, ndi mipando ya wogulitsa nkhunda.

Mat 21:13 Ndipo adati kwa iwo, Kwalembedwa, Nyumba yanga idzatchedw nyumba yopemphereramo; koma inu mwayipanga kukhala phanga la mbava.

Mat 21:14 Ndipo adadza kwa Iye kukachisiko akhungu ndi wopunduka miyendo, ndipo adachiritsidwa iwo.

Mat 21:15 Ndipo pamene ansembe akulu ndi alembi, m’mene adawona zozizwitsa zomwe Iye adazichita, ndi ana alimkufuwula ku kachisiko kuti, Hossana kwa Mwana wa Davide; adapsa mtima kwambiri.

Mat 21:16 Ndipo adati kwa Iye, Mulikumva kodi chimene ali kunena awa? Ndipo Yesu adanena kwa iwo, Inde, simudawerenga kodi, Mkamwa mwa makanda ndi woyamwa mudafotokozera zolemekeza?

Mat 21:17 Ndipo Iye adawasiya natuluka mu mzinda napita ku Betaniya, nagona kumeneko.

Mat 21:18 Ndipo mamawa m’mene Iye adali kupitanso kumzinda, adamva njala.

Mat 21:19 Ndipo pamene adawona mkuyu umodzi panjira, adafika pamenepo, napeza popanda kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso ku nthawi zonse.

Mat 21:20 Ndipo pamene wophunzira adawona ichi adazizwa, nati, Mkuyu udafota bwanji msanga?

Mat 21:21 Yesu adayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiliro, osakayika kayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja, chidzachitidwa.

Mat 21:22 Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m’kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.

Mat 21:23 Ndipo pamene Iye adalowa m’kachisi, ansembe akulu ndi akulu a anthu adadza kwa Iye ali kuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani adakupatsani ulamuliro wotere?

Mat 21:24 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani chinthu chimodzi, amene ngati mundiwuza Inenso ndikuwuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi:

Mat 21:25 Ubatizo wa Yohane, udachokera kuti, kumwamba kapena kwa anthu? Koma iwo adafunsana wina ndimzake, kuti, Tikati uchokera Kumwamba, Iye adzati kwa ife, mudalekeranji kukhulupirira iye?

Mat 21:26 Koma tikati, kwa anthu, tiwopa anthu ; pakuti onse amuyesa Yohane m’neneri.

Mat 21:27 Ndipo adamuyankha Yesu, nati, sitinganene ife. Iyenso adanena nawo, Inenso sindikuwuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.

Mat 21:28 Koma mukuganiza bwanji inu? Munthu wina adali nawo ana amuna awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito ku munda wanga wampesa.

Mat 21:29 Iye adayankha nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake adalapa napita.

Mat 21:30 Ndipo adadza kwa wachiwiriyo, natero momwemo.ndipo Iye adabvomera, nati, ndipita mbuye; koma sadapite.

Mat 21:31 Ndani wa awiriwo adachita chifuniro cha atate wawo? Iwo adanena kwa Iye, Woyambayo. Yesu adanena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi a chiwerewere adzatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Mulungu.

Mat 21:32 Popeza Yohane adadza kwainu m’njira ya chilungamo, ndipo simudakhulupirira iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere adakhulupirira iye; ndipo inu, m’mene mudachiwona, simudalapa pambuyo pake, kuti mukhulupirire iye.

Mat 21:33 Mverani fanizo lina; Padali munthu, mwini banja, amene adalima munda wamphesa, nawuzunguliza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, nawubwereketsa kwa wolima munda, napita ku dziko lakutali.

Mat 21:34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso idayandikira, adatumiza atumiki ake kwa wolima munda aja, kukalandira zipatso zake.

Mat 21:35 Ndipo wolimawo adatenga atumikiwo, nampanda m’modzi, wina namupha, wina namponya miyala.

Mat 21:36 Adatumizanso atumiki ena, wochuluka kuposa woyambawo; ndipo adawachitira iwo momwemo.

Mat 21:37 Koma potsiriza pake adatumiza kwa iwo mwana wake wa mwamuna, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu.

Mat 21:38 Koma pamene wolimawo adawona mwana wa mwamunayo, adanena wina ndi mzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.

Mat 21:39 Ndipo adamgwira iye, namponya kunja kwa munda, namupha.

Mat 21:40 Tsono atabwera mwini munda, adzachitira wolimawo chiyani?

Mat 21:41 Iwo adanena kwa Iye, Adzawononga moyipa anthu woyipawo, nadzapereka mundawo kwa wolima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.

Mat 21:42 Yesu adati kwa iwo, Kodi simudawerenga konse m’malembo, Mwala umene adawukana womanga nyumba womwewo udakhala mutu wa pangodya; Awa ndiwo machitidwe a Ambuye ndipo ali wozizwitsa m’maso mwathu?

Mat 21:43 Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.

Mat 21:44 Ndipo aliyense wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma kwa iye amene udzamgwera, udzampera iye monga ufa.

Mat 21:45 Ndipo pamene akulu ansembe ndi Afarisi, pakumva mafanizo ake, adazindikira kuti adali kunena za iwo.

Mat 21:46 Ndipo pamene adafuna kumgwira Iye, adawopa khamu, chifukwa adamuyesa Iye m’neneri.



22

Mat 22:1 Ndipo Yesu adayankha, nayankhulanso kwa iwo m’mafanizo, nati, Mat 22:2 Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi mfumu ndi mfumu ina imene mwana wake wamwamuna phwando la ukwati. Mat 22:3 Natumiza atumiki ake kukayitana iwo woyitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sadafuna kudza. Mat 22:4 Pomwepo adatumizanso atumiki ena, nanena, Uzani woyitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng’ombe zanga, ndi zonenepa ndidazipha ndipo zinthu zonse zapsa:bwerani ku ukwati. Mat 22:5 Koma iwo adanyalanyaza, nachoka, wina ku munda wake, wina ku malonda ake: Mat 22:6 Ndipo wotsala adagwira atumiki ake, nawachitira chipongwe, nawapha. Mat 22:7 Koma pamene mfumu idamva idakwiya; idatuma asilikali ake napululutsa ambanda aja; nitentha mzinda wawo. Mat 22:8 Pomwepo idanena kwa atumiki ake, Za ukwati tsopano zapsa, koma iwo woyitanidwawo sadali woyenera. Mat 22:9 Chifukwa chake, Pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeza, muyitaneni ku ukwatiwu. Mat 22:10 Ndipo atumikiwo adapita kunjira, nasonkhanitsa onse amene adawapeza, ngakhale woyipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo udadzala ndi alendo wokhala pachakudya Mat 22:11 Ndipo pamene mfumuyo idabwera kudzawona woyitanidwawo, adapenya momwemo munthu wosabvala chobvala cha ukwati; Mat 22:12 Ndipo adanena kwa iye, Mzanga udalowa bwanji muno wosakhala nacho chobvala cha ukwati? Ndipo iye adalibe mawu. Mat 22:13 Pomwepo mfumu idati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumtenge ndi kumponya ku mdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Mat 22:14 Pakuti woyitanidwa ndiwo ambiri, koma wosankhidwa ndiwo wowerengeka. Mat 22:15 Pomwepo Afarisi adapita, nakhala upo wakumkolera Iye m’kuyankhula kwake. Mat 22:16 Ndipo adatumiza kwa Iye wophunzira awo, pamodzi ndi Aherode nanena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli wowona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu mowona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang’anira pa nkhope ya anthu. Mat 22:17 Chifukwa chake mutiwuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kayisara, kapena iyayi? Mat 22:18 Koma Yesu adadziwa kuyipa kwawo, nati, Mundiyeseranji Ine, wonyenga inu? Mat 22:19 Tandiwonetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo adadza nalo kwa Iye khobiri. Mat 22:20 Ndipo Iye adati kwa iwo, N’chayani chithunzithunzi ichi, ndikulemba kwake? Mat 22:21 Nanena iwo kwa Iye, Cha Kaisara. Pomwepo Iye adati kwa iwo, chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu. Mat 22:22 Ndipo pamene iwo adamva mawu awa, adazizwa, namsiya Iye, nachokapo. Mat 22:23 Tsiku lomwelo adadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa; namfunsa Iye, Mat 22:24 Nanena, Mphunzitsi, Mose adati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, m`bale wake adzakwatira mkazi wake, nadzamuwukitsira m’bale wake mbewu. Mat 22:25 Tsono padali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba adakwatira, namwalira wopanda mbewu, nasiyira m’bale wake mkazi wake; Mat 22:26 Chimodzimodzi wachiwiri, ndi wachitatu kufikira wachisanu ndi chiwiri. Mat 22:27 Ndipo pomalizira adamwaliranso mkaziyo. Mat 22:28 Chifukwa chake m’kuwuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wayani wa asanu ndi awiriwo? Pakuti onse adakhala naye. Mat 22:29 Koma Yesu adayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu. Mat 22:30 Pakuti mkuwuka kwa akufa sakwatira kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Mulungu akumwamba. Mat 22:31 Koma za kuwuka kwa akufa, simudawerenga kodi chomwe chidanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti, Mat 22:32 Ine Ndiri Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Mulungu Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo. Mat 22:33 Ndipo pamene khamu lidamva, lidazizwa ndi chiphunzitso chake. Mat 22:34 Koma pamene Afarisi adamva kuti Iye adatontholetsa Asaduki, adasokhana pamodzi. Mat 22:35 Ndipo m’modzi wa iwo, mphunzitsi wa chilamulo, adamfunsa Iye funso ndi kumuyesa Iye, nati, Mat 22:36 Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndi liti la m’chilamulo Mat 22:37 Ndipo Yesu adati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. Mat 22:38 Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Mat 22:39 Ndipo lachiwiri lofanana nalo ndi ili, Uzikonda mzako monga uzikonda iwe mwini. Mat 22:40 Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri. Mat 22:41 Ndipo pamene Afarisi adasonkhana pamodzi, Yesu adawafunsa iwo, Mat 22:42 Nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo adanena kwa Iye Mwana wa Davide. Mat 22:43 Iye adati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena, Mat 22:44 Ambuye adanena kwa Ambuye wanga, Khala pa dzanja la manja langa, kufikira Ine ndidzayika adani ako pansi pamapazi ako. Mat 22:45 Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji? Mat 22:46 Ndipo padalibe m`modzi adatha kumuyankha mawu. Ndipo sadalimbika mtima munthu aliyense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo.



23

Mat 23:1 Pamenepo Yesu adayankhula kwa makamu ndi wophunzira ake.

Mat 23:2 Nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose:

Mat 23:3 Chifukwa chake zinthu ziri zonse zimene iwo akawuza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zawo;pakuti iwo amayankhula, koma samachita.

Mat 23:4 Pakuti amanga akatundu wolemera ndi wosawutsa ponyamula, nawasenzetsa pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.

Mat 23:5 Koma amachita ntchito zawo zonse kuti awonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chithando chake cha njilisi zawo, nakulitsa mphonje.

Mat 23:6 Nakonda malo a ulemu pamaphwando, ndi mipando ya ulemu m’masunagoge,

Mat 23:7 Ndi kuyankhulidwa m’misika, ndi kutchulidwa ndi anthu, Rabi, Rabi.

Mat 23:8 Koma inu musamatchedwa Rabi, pakuti Mphunzitsi wanu ali modzi ndiye Khristu, ndipo inu muli abale.

Mat 23:9 Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo m’modzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.

Mat 23:10 Ndipo musatchulidwa Ambuye, pakuti alipo m’modzi Ambuye wanu, ndiye Khristu.

Mat 23:11 Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.

Mat 23:12 Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

Mat 23:13 Koma tsoka inu, Alembi, ndi Afarisi wonyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pawo; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa kuti asalowemo.

Mat 23:14 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mukwawira m’nyumba za amayi amasiye, ndipo mupemphera pemphero lalitali; chifukwa chake mudzalandira chilango chachikulu.

Mat 23:15 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mupitapita ku nyanja ndi kumtunda kuyesa munthu m’modzi m’tembenuki; ndipo m’mene akhala wotere,mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri.

Mat 23:16 Tsoka pa inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golidi wa kachisi, wamangawa.

Mat 23:17 Inu wopusa, ndi akhungu; pakuti choposa n’chiti, golidi kodi, kapena kachisi amene ayeretsa golidiyo?

Mat 23:18 Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mphatso za pamwamba pake wachimwa.

Mat 23:19 Inu wopusa ndi akhungu, pakuti choposa n’chiti, mphatso kodi, kapena guwa lansembe limene liyeretsa mphatsoyo?

Mat 23:20 Chifukwa chake wolumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake.

Mat 23:21 Ndipo wolumbira kutchula kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wokhala momwemo.

Mat 23:22 Ndipo wolumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wokhala pomwepo.

Mat 23:23 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi tsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro: koma zijazo mudayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.

Mat 23:24 Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma ngamila mumeza.

Mat 23:25 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.

Mat 23:26 Mfarisi iwe wa khungu, yambakutsuka m’kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.

Mat 23:27 Tsoka pa inu, Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mufanana ndi manda wopaka njereza, amene awonekera wokoma kunja kwake, koma adzala m’katimo ndi mafupa wa anthu akufa ndi zonyansa zonse.

Mat 23:28 Chomwecho inunso muwonekera wolungama pa maso pa anthu, koma m’kati muli wodzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.

Mat 23:29 Tsoka pa inu Alembi ndi Afarisi, wonyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda wa aneneri, ndipo mukonza manda a anthu wolungama,

Mat 23:30 Ndikuti, ife tikadakhala m’masiku a makolo wathu, sitikadakhala woyanjana nawo pa mwazi wa aneneri.

Mat 23:31 Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene adapha aneneri.

Mat 23:32 Dzazani inu muyeso wa makolo anu.

Mat 23:33 Njoka inu, wobadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa gehena?

Mat 23:34 Chifukwa cha ichi, Onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, ndikuwapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m’masunagoge mwanu, ndi kuwazunza kuchokera ku mzinda umodzi kufikira ku mzinda wina.

Mat 23:35 Kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wolungama wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira mwazi wa Zakariya mwana wa Barakiya, amene mudamupha pakati pa kachisi ndi guwa la nsembe.

Mat 23:36 Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono.

Mat 23:37 Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo wotumidwa kwa iwe! Ine ndidafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simudafuna ayi!

Mat 23:38 Onani nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.

Mat 23:39 Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandiwonanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wodala Iye amene akudza m’dzina la Ambuye



24

Mat 24:1 Ndipo Yesu adatuluka nachoka ku kachisi; ndipo wophunzira ake adadza kwa Iye kudzamuwonetsa mamangidwe a kachisiyo.

Mat 24:2 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Simuwona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa umzake, umene sudzagwetsedwa pansi.

Mat 24:3 Ndipo pamene Iye adalikukhala pansi pa phiri la Azitona, wophunzira adadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiwuze ife zija zidzawoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?

Mat 24:4 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Chenjerani, kuti asasokeretse inu munthu.

Mat 24:5 Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.

Mat 24:6 Ndipo inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi ziwoneke; koma chitsiriziro sichinafike.

Mat 24:7 Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu udzawukirana ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi miriri ndi zibvomerezi m’malo akuti akuti.

Mat 24:8 Zonsezi ndicho chiyambi cha zowawa.

Mat 24:9 Pamenepo adzakuperekani kuzosautsa nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.

Mat 24:10 Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mzake, nadzadana wina ndi mzake.

Mat 24:11 Ndipo aneneri wonama ambiri adzawuka, nadzasokeretsa anthu ambiri.

Mat 24:12 Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala.

Mat 24:13 Koma iye wakupirirabe kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.

Mat 24:14 Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.

Mat 24:15 Pamene mudzawona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danieli m’neneri, chitayima m’malo woyera (iye amene awerenga azindikire.)

Mat 24:16 Pomwepo iwo ali mu Yudeya athawire kumapiri:

Mat 24:17 Iye ali pamwamba pa denga asatsike kukanyamula za m’nyumba mwake;

Mat 24:18 Ndi iye ali m’munda asabwere kutenga chofunda chake.

Mat 24:19 Koma tsoka ali nalo iwo wokhala ndi mwana, ndi woyamwitsa ana m’masiku amenewo!

Mat 24:20 Koma pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzakhale pa nyengo yozizira, kapena pa tsiku la Sabata.

Mat 24:21 Pakuti pomwepo padzakhala masautso akulu, monga sipadakhale wotero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.

Mat 24:22 Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense; koma chifukwa cha wosankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.

Mat 24:23 Pomwepo ngati munthu anena kwa inu, Onani, Khristu ali kuno, kapena uko musakhulupirire;

Mat 24:24 Chifukwa Akhristu wonama adzawuka, ndi aneneri wonama nadzawonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa; kotero kuti akanyenge, ngati n’kotheka, wosankhidwa womwe.

Mat 24:25 Onani ndakuwuziranitu pasadafike.

Mat 24:26 Chifukwa chake akanena kwa inu, Onani, iye ali m’chipululu; musamukeko. Onani, ali m’zipinda; musakhulupirire.

Mat 24:27 Pakuti monga mphezi idzera kum’mawa, niwonekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.

Mat 24:28 Pakuti kumene kuli konse uli mtembo, miphamba imasonkhana komko.

Mat 24:29 Koma pomwepo, atapita masautso a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzawonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:

Mat 24:30 Ndipo pomwepo padzawoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzalira, nidzapenya Mwana wa munthu alimkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero wa ukulu.

Mat 24:31 Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake ku mphepo zinayi, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.

Mat 24:32 Tsopano phunzirani fanizo la mtengo wa mkuyu; Pamene nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja likuyandikira;

Mat 24:33 Chomwechonso inu, pamene mudzawona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo.

Mat 24:34 Indetu ndinena kwa inu, m`bado uwu sudzachoka, kufikira zinthu zonsezi zidzakwaniritsidwa.

Mat 24:35 Thambo ndi dziko la pansi zidzachoka, koma mawu anga sadzachoka ayi.

Mat 24:36 Koma za tsiku ilo ndi nthawi yake sadziwa munthu ali yense, angakhale angelo a Kumwamba, koma Atate yekha.

Mat 24:37 Ndipo monga kudali masiku a Nowa, koteronso kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.

Mat 24:38 Pakuti monga m’masiku aja, chisadafike chigumula, anthu adali mkudya ndi kumwa, adalikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa adalowa m’chingalawa,

Mat 24:39 Ndipo iwo sadadziwe kanthu, kufikira pamene chigumula chidadza, chidapululutsa iwo onse, koteronso kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.

Mat 24:40 Pomwepo adzakhala awiri m’munda; m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa:

Mat 24:41 Akazi awiri adzakhala akupera pamphero; m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa

Mat 24:42 Chenjerani, pakuti simudziwa nthawi yake yakufika Ambuye wanu.

Mat 24:43 Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibowoledwe.

Mat 24:44 Chifukwa chake khalani inunso wokonzekeratu; chifukwa munthawi imene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.

Mat 24:45 Ndani kodi ali mtumiki wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adamkhazika woyang’anira banja lake, pakuwapatsa zakudya pa nthawi yake?

Mat 24:46 Wodala mtumiki amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye ali kuchita chotero.

Mat 24:47 Indetu, ndinena kwa inu, Adzamkhazika iye womulamulira zinthu zake zonse.

Mat 24:48 Koma mtumiki woyipa akanena mu mtima mwake, Mbuye wanga wachedwa:

Mat 24:49 Nadzayamba kupanda mtumiki amzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi woledzera;

Mat 24:50 Mbuye wa mtumikiyo adzafika tsiku losamuyembekezera Iye, ndi nthawi yosadziwa iye.

Mat 24:51 Nadzamdula, nadzayika pokhala pake ndi anthu wonyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.



25

Mat 25:1 Pomwepo Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi anamwali khumi, amene adatenga nyali zawo, natuluka kukakomana ndi mkwati.

Mat 25:2 Ndipo asanu a iwo adali wopusa, ndi asanu adali wochenjera.

Mat 25:3 pakuti wopusawo, m’mene adatenga nyali zawo sadadzitengeranso mafuta.

Mat 25:4 Koma anzeruwo adatenga mafuta msupa zawo, pamodzi ndi nyali zawo.

Mat 25:5 Ndipo pamene mkwati adachedwa, onsewo adawodzera, nagona tulo.

Mat 25:6 Koma pakati pa usiku padali kufuwula, Onani mkwati ali mkudza! Tulukani kukakomana naye.

Mat 25:7 Pomwepo adauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zawo.

Mat 25:8 Ndipo wopusa adati kwa wochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu ziri kuzima.

Mat 25:9 Koma wochenjera adayankha nati, Iyayi kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa wogulitsa malonda, mukadzigulire nokha.

Mat 25:10 Ndipo pamene iwo adalikumuka kukagula, mkwati adafika; ndipo wokonzekawo adalowa naye pamodzi mu ukwati; ndipo adatseka pakhomo.

Mat 25:11 Koma pambuyo pake adadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife.

Mat 25:12 Koma Iye adayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani inu.

Mat 25:13 Chifukwa chake, dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake yakudza Mwana wamunthu.

Mat 25:14 Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu wakumka ulendo, kudziko lakutali amene adayitana atumiki ake, napereka kwa iwo chuma chake.

Mat 25:15 Ndipo m’modzi adampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo; namuka iye.

Mat 25:16 Pomwepo uyo amene adalandira ndalama zisanu, adapita nagula nazo malonda, napindulapo ndalama zina zisanu.

Mat 25:17 Chimodzimodzi uyo waziwirizo, adapindulapo zina ziwiri.

Mat 25:18 Koma uyo amene adalandira imodziyo adamuka, nakumba pansi, nayibisa ndalama ya mbuye wake.

Mat 25:19 Ndipo itapita nthawi yayikulu, anabwera mbuye wa atumiki awo, nawerengera nawo pamodzi.

Mat 25:20 Ndipo uyo adalandira ndalama za matalente zisanu adadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena,Mbuye mudandipatsa ndalama za matalente zisanu, onani ndapindulapo ndalama zisanu zina.

Mat 25:21 Ndipo mbuye wake adati kwa iye, chabwino, mtumiki iwe wabwino ndi wokhulupirika popeza iwe udakhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe wolamulira pa zinthu zazikulu; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wanga.

Mat 25:22 Ndipo wa ndalama ziwiriyo anadzanso, nati, mbuye, mudandipatsa ine ndalama ziwiri; onani, ndapindulapo ndalama zina ziwiri.

Mat 25:23 Ndipo mbuye wake adati kwa iye, chabwino, mtumiki iwe wabwino ndi wokhulupirika; udali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe wolamulira pa zinthu zazikulu; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wanga.

Mat 25:24 Ndipo uyonso amene adalandira ndalama imodzi, adadza, nati, mbuye, ndidakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simudafesa, ndi kusonkhanitsa kumene simudafese:

Mat 25:25 Ndidawopa ine, ndidapita, ndidabisa pansi ndalama yanu: Onani, siyi yanu.

Mat 25:26 Koma mbuye wake adayankha, nati kwa iye, mtumiki iwe woyipa ndi waulesi, udadziwa kuti ndimatuta kumene sindidafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindidawaza:

Mat 25:27 Chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa wokongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake.

Mat 25:28 Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muyipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.

Mat 25:29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene ali nacho.

Mat 25:30 Ndikuponya mtumiki wopanda pake ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mat 25:31 Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake , ndi angelo woyera onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake:

Mat 25:32 Ndipo adzasonkhanitsidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi:

Mat 25:33 Nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake la manja, koma mbuzi kulamanzere.

Mat 25:34 Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu wodalitsika wa Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:

Mat 25:35 Pakuti ndidali ndi njala, ndipo mudandipatsa Ine kudya; ndidali ndi ludzu, ndipo mudandimwetsa Ine; ndidali mlendo, ndipo mudandichereza Ine.

Mat 25:36 Wamaliseche Ine, ndipo mudandibveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndidali m’nyumba yandende ndipo munadza kwa Ine.

Mat 25:37 Pomwepo wolungama adzayankha Iye kuti, Ambuye tidakuwonani Inu liti wanjala, ndikukudyetsani? Kapena wa ludzu ndikukumwetsani?

Mat 25:38 Ndipo tidawona Inu liti mlendo, ndikukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukubvekani?

Mat 25:39 Ndipo tidakuwonani Inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tidadza kwa Inu?

Mat 25:40 Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, chifukwa mudachitira ichi m’modzi wa abale anga, ngakhale ang’ono ngono awa, mudandichitira ichi Ine.

Mat 25:41 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo akudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine wotembereredwa inu, ku moto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake.

Mat 25:42 Pakuti ndidali wa njala, ndipo simudandipatsa Ine kudya: ndidali ndi ludzu ndipo simudandimwetsa Ine:

Mat 25:43 Ndidali mlendo, ndipo simudandilandira Ine; wamaliseche ndipo simudandibveka Ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simudadza kundiwona Ine.

Mat 25:44 Pomwepo iwonso adzayankha Iye kuti, Ambuye tidakuwonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena wodwala kapena m’nyumba ya ndende, ndipo ife sitidakutumikirani Inu?

Mat 25:45 Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa mudalibe kuchitira ichi m’modzi wa ang’onong’ono awa, mudalibe kundichitira ichi Ine.

Mat 25:46 Ndipo amenewa adzachoka kumka ku chilango chosatha; koma wolungama ku moyo wosatha.



26

Mat 26:1 Ndipo padali pamene Yesu adatha mawu onse amenewa, adati kwa wophunzira ake,

Mat 26:2 Mudziwa kuti akapita masiku awiri, ndi phwando la paskha, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kukapachikidwa.

Mat 26:3 Pomwepo adasonkhana ansembe akulu ndi alembi ndi akulu a anthu, ku bwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa.

Mat 26:4 Nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi mochenjera, namuphe Iye.

Mat 26:5 Koma adanena iwo, Osati pa tsiku la phwando, kuti pasakhale chipolowe pakati pa anthu.

Mat 26:6 Ndipo pamene Yesu adali mu Betaniya, m’nyumba ya Simoni wakhate,

Mat 26:7 Anadza kwa Iye mkazi, adali nayo msupa ya alabastero ndi mafuta wonunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m’mene Iye adalikukhala pachakudya.

Mat 26:8 Koma m’mene wophunzira ake adawona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuwononga kumeneku?

Mat 26:9 Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kupatsa anthu aumphawi.

Mat 26:10 Koma Yesu podziwa, adati kwa iwo, Mumbvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino.

Mat 26:11 Pakuti nthawi zonse muli nawo aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

Mat 26:12 Pakuti mkaziyo, m’mene adathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuyikidwa kwanga m`manda.

Mat 26:13 Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m’dziko lonse lapansi ichi chimene mkaziyo adachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.

Mat 26:14 Pomwepo m’modzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudase Isikariyote, adamuka kwa ansembe akulu,

Mat 26:15 Nati kwa iwo, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo adamuwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.

Mat 26:16 Ndipo kuyambira pamenepo iye adafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.

Mat 26:17 Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, wophunzira anadza kwa Yesu nati kwa Iye, Mufuna tikakonzere kuti Paskha, kuti mukadye?

Mat 26:18 Ndipo Iye adati, Mukani kumzinda kwa munthu wakuti, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena, nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi wophunzira anga.

Mat 26:19 Ndipo wophunzira adachita monga Yesu adawauza, nakonza Paskha.

Mat 26:20 Ndipo pakufika madzulo, Iye adalikukhala pachakudya pamodzi ndi wophunzira khumi ndi awiri.

Mat 26:21 Ndipo m’mene adalimkudya Iye adati, Indetu ndinena kwa inu, m’modzi wa inu adzandipereka Ine.

Mat 26:22 Ndipo iwo adagwidwa ndi chisoni chachikulu, nayamba kunena kwa Iye m’modzi m’modzi, Kodi ndine Ambuye?

Mat 26:23 Ndipo Iye adayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lake m’mbale, yemweyu adzandipereka Ine.

Mat 26:24 Mwana wa munthu achokatu, monga kudalembedwa za Iye: koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.

Mat 26:25 Ndipo Yudase, wompereka Iye adayankha nati, Ambuye, kodi ndine? Iye adanena kwa iye, Iwe watero.

Mat 26:26 Ndipo pamene iwo adalimkudya, Yesu adatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m’mene adapatsa kwa wophunzira, adati, Tengani, idyani; Ili ndi thupi langa.

Mat 26:27 Ndipo pamene adatenga chikho, adayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse.

Mat 26:28 Pakuti uwu ndiwo mwazi wanga wa chipangano chatsopano, wokhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuchotsa machimo.

Mat 26:29 Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi cha mpesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu mu Ufumu wa Atate wanga.

Mat 26:30 Ndipo pamene adayimba nyimbo, adatuluka kumka ku phiri la Azitona.

Mat 26:31 Pomwepo Yesu adanena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno: pakuti kwalembedwa, ndidzakantha m`busa, ndipo zidzabalalika nkhosa zagulu.

Mat 26:32 Ndipo nditawukitsidwanso ndidzatsogolera inu ku Galileya.

Mat 26:33 Koma Petro adanena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.

Mat 26:34 Yesu adati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asadalire, udzandikana Ine katatu.

Mat 26:35 Petro adanena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafe pamodzi ndi inu, sindidzakukanani Inu ayi. Adateronso wophunzira onse.

Mat 26:36 Pomwepo Yesu anadza ndi iwo ku malo wotchedwa Getsemane, nanena kwa wophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.

Mat 26:37 Ndipo adatenga Petro ndi ana awiri a Zebedeyo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi kulemedwa kwambiri ndi chisoni .

Mat 26:38 Pamenepo adanena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho ku imfa: khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine.

Mat 26:39 Ndipo adamuka patsogolo pang’ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate anga, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine: koma si monga ndifuna Ine, koma monga mufuna inu.

Mat 26:40 Ndipo adadza kwa wophunzira, nawapeza iwo ali m’tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Kodi Simukhoza kuchezera ndi Ine ora limodzi?

Mat 26:41 Khalani maso ndi kupemphera, kuti mungalowe m’kuyesedwa: mzimu ndithu ali wakufuna, koma thupi liri lolefuka.

Mat 26:42 Adamukanso kachiwiri, napemphera, nanena, Atate wanga, ngati chikho ichi sichingandipitirire ine chabwino, ndimwera ichi, kufuna kwanu kuchitidwe.

Mat 26:43 Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali mtulo, pakuti maso awo adalemera ndi tulo.

Mat 26:44 Ndipo iye adawasiya nachokanso, napemphera kachitatu, nateronso mawu womwewo.

Mat 26:45 Pomwepo anadza kwa wophunzira ake, nanena kwa iwo, Gonani tsopano, mupumule; onani, nthawi yayandikira, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa m’manja a wochimwa.

Mat 26:46 Ukani, timuke; tawonani, iye wakundipereka wayandikira.

Mat 26:47 Ndipo Iye ali chiyankhulire, onani, Yudase m’modzi wa khumi ndi awiriwo, anadza ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu, ndi malupanga ndi zibonga, kuchokera kwa ansembe akulu ndi akulu a anthu.

Mat 26:48 Koma wompereka Iye adawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsopsona ndiyeyo, mumgwire Iye.

Mat 26:49 Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuwoneni, Rabi; ndipo adampsopsona Iye.

Mat 26:50 Ndipo Yesu adati kwa iye, Mzanga wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namtenga Iye.

Mat 26:51 Ndipo onani, m’modzi wa iwo adali pamodzi ndi Yesu, adatansa dzanja lake, nasolola lupanga lake, nakantha mtumiki wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.

Mat 26:52 Pomwepo Yesu adanena kwa iye, Tabwezera lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.

Mat 26:53 Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera tsopano kwa Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino magulu a angelo woposa khumi ndi awiri?

Mat 26:54 Koma pakutero malembo adzakwaniritsidwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?

Mat 26:55 Nthawi yomweyo Yesu adati kwa makamuwo, Kodi mudatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi zibonga, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m’kachisi kuphunzitsa, ndipo simudandigwira.

Mat 26:56 Koma izi zonse zidachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniritsidwe. Pomwepo wophunzira onse adamsiya Iye, nathawa.

Mat 26:57 Ndipo iwo akugwira Yesu adamka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe.

Mat 26:58 Koma Petro adamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi atumiki kuti awone chimaliziro.

Mat 26:59 Ndipo ansembe akulu ndi akulu a milandu onse adafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;

Mat 26:60 Koma sadaupeza zingakhale mboni zonama zambiri zidadza, koma sadawupeze umboni koma pamapeto pake zidadza mboni ziwiri zonama.

Mat 26:61 Ndipo adati, Munthu uyu adanena kuti, Ndikhoza kupasula kachisi wa Mulungu, ndi kum’manganso masiku atatu.

Mat 26:62 Ndipo mkulu wa ansembe adayimilira, nati kwa Iye, Sukuyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe?

Mat 26:63 Koma Yesu adangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe adanena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wa moyo, kuti utiwuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu wa moyo

Mat 26:64 Yesu adati kwa iye, Mwatero ndinu: koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzawona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja la manja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya Kumwamba

Mat 26:65 Pomwepo mkulu wa ansembe adang’amba zobvala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo.

Mat 26:66 Muganiza bwanji? Iwo adayankha nati, Ali wochimwa woyenera kumupha.

Mat 26:67 Pomwepo iwo adamlabvulira malobvu pankhope pake, nam’bwanyula Iye; ndipo ena adampanda ndi manja awo,

Mat 26:68 Nati, Utilote ife, Khristu iwe, wakumenya iwe ndani?

Mat 26:69 Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo buthu linadza kwa iye, linena, Iwenso udali ndi Yesu wa ku Galileya.

Mat 26:70 Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, kuti, Chimene unena sindichidziwa.

Mat 26:71 Ndipo pamene iye adatuluka kumka kuchipata, mkazi wina adamuwona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyunso adali ndi Yesu wa ku Nazarete.

Mat 26:72 Ndipo adakananso ndi chilumbiro, kuti Sindidziwa munthuyo.

Mat 26:73 Ndipo popita nthawi yaying’ono iwo akuyimapo anadza, nati kwa Petro, Zowonadi, iwenso uli m`modzi wa iwo; pakuti mayankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.

Mat 26:74 Pamenepo iye adayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindimdziwa munthuyo. Ndipo nthawi yomweyo tambala adalira.

Mat 26:75 Ndipo Petro adakumbukira mawu a Yesu amene adati kwa iye, Asadalire tambala udzandikana Ine katatu. Ndipo adatuluka kunja, nalira ndi kuwawa mtima.



27

Mat 27:1 Ndipo pakudza m`mawa, ansembe akulu ndi akulu a anthu onse adakhala upo wakumchitira Yesu kuti amuphe:

Mat 27:2 Ndipo adam’manga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.

Mat 27:3 Pamenepo Yudase yemwe adampereka Iye, powona kuti Iye adatsutsidwa, adalapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe akulu ndi akulu a anthu.

Mat 27:4 Nanena, Ndidachita koyipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo adati, Tiri nacho chiyani ife? Udziwonere wekha izo.

Mat 27:5 Ndipo iye adataya pansi ndalamazo m`kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi.

Mat 27:6 Ndipo ansembe akulu adatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziyika izi m’chosungiramo ndalama, chifukwa ndizo za mtengo wa mwazi.

Mat 27:7 Koma adapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda wa alendo.

Mat 27:8 Chifukwa chake munda umenewu adautcha Munda-wa-Mwazi kufikira lero lino.

Mat 27:9 Pamenepo chidakwaniritsidwa chonenedwa ndi Yeremiya m’neneri, ndi kuti, Ndipo iwo adatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa uja wowerengeredwa mtengo wake, amene iwo ana a Israyeli adawerenga mtengo wake;

Mat 27:10 Ndipo adazipereka kugula munda wa woumba mbiya, monga Ambuye adandilamulira ine.

Mat 27:11 Ndipo Yesu adayimilira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo adamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu adati kwa iye, Mwatero ndinu.

Mat 27:12 Ndipo pakum’nenera Iye ansembe akulu ndi akulu a anthu, Iye sadayankha kanthu.

Mat 27:13 Pomwepo Pilato adanena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe?

Mat 27:14 Ndipo sadayankha Iye, ngakhale mawu amodzi, kotero kuti kazembe adazizwa ndithu.

Mat 27:15 Ndipo pa Paskha kazembe adazolowera kumasulira munthu m’modzi wandende, amene iwo adafuna.

Mat 27:16 Ndipo panthawi yomweyo adali ndi wandende wodziwika, dzina lake Baraba.

Mat 27:17 Chifukwa chake pamene adasonkhana pamodzi, Pilato adanena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu?

Mat 27:18 Pakuti adadziwa kuti adampereka Iye mwanjiru.

Mat 27:19 Ndipo pamene Pilato adalikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake adatumiza mawu kwa iye, nanena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m’kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.

Mat 27:20 Koma ansembe akulu adakopa khamu kuti lipemphe Baraba, ndikuwononga Yesu.

Mat 27:21 Koma kazembe adayankha nati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo adati, Baraba.

Mat 27:22 Pilato adanena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Ndipo onse adati, Apachikidwe.

Mat 27:23 Ndipo kazembe adati, Chifukwa chiyani? Adachita choyipa chotani? Koma iwo adafuwulitsa kopambana nati, Apachikidwe.

Mat 27:24 Koma Pilato powona kuti sadafitse, koma kuti lidapambana phokoso, adatenga madzi, nasamba m`manja pamaso pa khamulo nati, Ine ndiribe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudziwonere nokha.

Mat 27:25 Ndipo anthu onse adayankha nati, Mwazi wake ukhale pa ife ndi pa ana athu.

Mat 27:26 Pomwepo iye adamasulira iwo Baraba, koma adakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike.

Mat 27:27 Pomwepo asilikali a kazembe adamuka naye Yesu ku bwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye gulu la asirikali lonse.

Mat 27:28 Ndipo adambvula malaya ake, nambveka malaya wofiyira achifumu.

Mat 27:29 Ndipo adaluka Korona waminga, nambveka pamutu pake, namgwiritsa bango m’dzanja lamanja lake; ndipo adagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda!

Mat 27:30 Ndipo adamulabvulira malobvu Iye, natenga bango, nampanda Iye pamutu.

Mat 27:31 Ndipo pamene adatha kumchitira Iye chipongwe, adambvula malaya aja, nambveka Iye malaya ake, namtsogoza Iye kukampachika.

Mat 27:32 Ndipo pakutuluka pawo adapeza munthu wa ku Kurene, dzina lake Simoni, namkangamiza iye kuti anyamule mtanda wake.

Mat 27:33 Ndipo pamene adadza kumalo dzina lake Gologota, ndiko kunena kuti, Malo a Chigaza,

Mat 27:34 Adampatsa Iye vinyo wosanganiza ndi ndulu; ndipo Iye m’mene adalawa, sadafuna kumwa.

Mat 27:35 Ndipo pamene adampachika Iye, adagawana zobvala zake pakuchita mayere: kuti zikwaniritsidwe zonenedwa ndi aneneri, kuti, Iwo adagawana zobvala zanga mwa iwo wokha nachita mayere kuti aliyense adzatenga chiyani.

Mat 27:36 Ndipo adakhala iwo pansi namdikira Iye pamenepo.

Mat 27:37 Ndipo adayika pamwamba pa mutu pake mawu wolembedwa; UYU NDI YESU

Mat 27:38 Pamenepo adapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri, m’modzi ku dzanja lamanja, ndi wina kulamanzere.

Mat 27:39 Ndipo anthu wodutsapo adamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yawo,

Mat 27:40 Nati, Nanga Iwe, wopasula, kachisi ndi kum’manganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.

Mat 27:41 Chomwechonso ansembe akulu pamodzi ndi alembi ndi akulu adamchitira chipongwe, nati

Mat 27:42 Adapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ngati ndiye Mfumu ya Israyeli; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.

Mat 27:43 Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti adati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.

Mat 27:44 Ndiponso achifwambawo wopachikidwa pamodzi ndi Iye, adamlalatira Iye mawu amodzimodzi.

Mat 27:45 Ndipo ola lachisanu ndi chimodzi padali mdima padziko lonse, kufikira ola lachisanu ndi chinayi.

Mat 27:46 Ndipo poyandikira ola lachisanu ndi chinayi, Yesu adafuwula ndi mawu akulu nanena, Eli Eli, Lamasabakitani? Ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?

Mat 27:47 Ndipo ena a iwo akuyimilira komweko, pamene adamva, adanena, munthu uyu ayitana Eliya.

Mat 27:48 Ndipo pomwepo m’modzi wa iwo adathamanga, natenga chinkhupule nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiyika pa bango, nampatsa Iye kuti amwe.

Mat 27:49 Koma ena adati, Taleka, tiwone ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa.

Mat 27:50 Ndipo Yesu pamene adafuwula ndi mawu akulu, adapereka Mzimu wake.

Mat 27:51 Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha m’kachisi chidang’ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko lidagwedezeka, ndi miyala idang’ambika;

Mat 27:52 Ndipo manda adatseguka ndi matupi ambiri a anthu woyera mtima, akugona kale adawuka,

Mat 27:53 Ndipo adatuluka m’manda mwawo pambuyo pa kuuka kwake, nalowa mu mzinda woyera, nawonekera kwa ambiri.

Mat 27:54 Ndipo pamene Kenturiyo ndi iwo adali naye akuyang`ana Yesu, powona chibvomerezi, ndi zinthu zimene zidachitidwa, adawopa kwambiri, nanena, Indedi, Uyo ndiye Mwana wa Mulungu.

Mat 27:55 Ndipo adali pomwepo akazi ambiri, akuyang’anira patali, omwe adatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira Iye;

Mat 27:56 Mwa iwo amene mudali Mariya wa Magadala, ndi Mariya amake wa Yakobo, ndi wa Yose, ndi amake a ana a Zebedayo.

Mat 27:57 Ndipo pamene padali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe, amene adalinso wophunzira wa Yesu;

Mat 27:58 Iyeyo adapita kwa Pilato, napempha thupi la Yesu. Pomwepo Pilato adalamulira kuti thupiulo liperekedwe.

Mat 27:59 Ndipo Yosefe atatenga thupilo, adalikulunga m’nsalu yabafuta yoyeretsetsa,

Mat 27:60 Naliyika m’manda ake atsopano, wosemedwa m’mwala, nakunkhumizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.

Mat 27:61 Ndipo Mariya wa Magadala adali pamenepo, ndi Mariya winayo, adakhala pansi popenyana ndi mandawo.

Mat 27:62 Ndipo m’mawa mwake, ndilo dzuwa lotsatana ndi tsiku lokonzekera, ansembe akulu ndi Afarisi adasonkhana kwa Pilato

Mat 27:63 Nanena, Mfumu takumbukira ife kuti wonyenga uja adati, pamene adali ndi moyo, ndidzawuka pakutha masiku atatu.

Mat 27:64 Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena wophunzira ake angadze usiku, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu kuti Iye adawuka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho.

Mat 27:65 Pilato adati kwa iwo, Tengani alonda; mukani kalondereni monga mudziwa.

Mat 27:66 Ndipo iwo adamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo. Naikapo woyang`anira.



28

Mat 28:1 Ndipo kumathero kwa tsiku la Sabata, mbanda kucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Mariya Magadalene, ndi Mariya winayo, kudzawona manda.

Mat 28:2 Ndipo onani, padali chibvomezi chachikulu; pakuti m’ngelo wa Ambuye adatsika kuchokera Kumwamba nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.

Mat 28:3 Kuwonekera kwake kudali ngati mphezi, ndi chobvala chake choyeretsetsa ngati matalala:

Mat 28:4 Ndipo ndikuwopsa kwake alondawo adanthunthumira, nakhala ngati anthu akufa.

Mat 28:5 Koma m’ngelo adayankha, nati kwa akaziwo, Musawope inu: pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene adapachikidwa.

Mat 28:6 Iye mulibe muno iyayi: pakuti adauka, monga adanena. Idzani munomudzawone malo m’mene adagonamo Ambuye.

Mat 28:7 Ndipo pitani msanga, muwuze wophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuwona Iye komweko; onani, ndakuwuzani inu.

Mat 28:8 Ndipo iwo adachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukawuza wophunzira ake.

Mat 28:9 Ndipo pamene amamka kukawuza wophunzira ake, onani, Yesu adakomana nawo, nanena, Tikuwoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, nampembedza Iye.

Mat 28:10 Pomwepo Yesu adanena kwa iwo, Musawope; pitani, kawuzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiwona Ine kumeneko.

Mat 28:11 Ndipo pamene iwo adalikupita, onani, ena a alonda adafika ku mzinda nawuza ansembe akulu zonse zimene zidachitidwa.

Mat 28:12 Ndipo pamene adasonkhana pamodzi ndi akulu, adakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri.

Mat 28:13 Nanena, Kadzinenani kuti wophunzira ake anadza usiku namuba Iye m’mene ife tidali mtulo.

Mat 28:14 Ndipo ngati ichi chidzamveka ku makutu a kazembe, ife tidzamunyengerera iye ndi kukutetezani inu.

Mat 28:15 Ndipo iwo adalandira ndalamazo, nachita monga adawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.

Mat 28:16 Pamenepo wophunzira khumi ndi m’modziyo adamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu adapangana nawo.

Mat 28:17 Ndipo pamene adamuwona Iye, adamlambira; koma ena adakayika.

Mat 28:18 Ndipo Yesu anadza nayankhula nawo, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi dziko lapansi.

Mat 28:19 Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera:

Mat 28:20 Ndikuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndidakulamulirani inu: ndipo onani Ine ndiri pamodzi ndi inu nthawi zonse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE