Mark


1

Mar 1:1 Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.

Mar 1:2 Monga mwalembedwa mwa aneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.

Mar 1:3 Mawu a wofuwula, m’chipululu, Konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.

Mar 1:4 Yohane anadza nabatiza m’chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima woloza kuchikhululukiro cha machimo.

Mar 1:5 Ndipo adatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje wa Yordano, powulula machimo awo.

Mar 1:6 Ndipo Yohane amkabvala ubweya wangamila, ndi lamba lachikopa m’chuwuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wa kuthengo.

Mar 1:7 Ndipo adalalikira kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zake ine.

Mar 1:8 Ine zowonadi ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.

Mar 1:9 Ndipo kudali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m’Yordano.

Mar 1:10 Ndipo pomwepo, potuluka m’madzi, adawona Iye thambo litatseguka ndipo Mzimu adatsikira pa Iye monga nkhunda:

Mar 1:11 Ndipo mawu adatuluka kumwamba, wonena, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa , mwa Iyeyu ndikondwera bwino.

Mar 1:12 Ndipo pomwepo Mzimu udampititsa Iye kuchipululu.

Mar 1:13 Ndipo adakhala m’chipululu masiku makumi anayi nayesedwa ndi Satana; nakhala ndi zirombo, ndipo angelo adamtumikira Iye.

Mar 1:14 Tsopano atatha kuperekedwa Yohane mundende, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,

Mar 1:15 Nanena, nthawi yakwanira ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; lapani, khulupirirani Uthenga Wabwino.

Mar 1:16 Ndipo pakuyenda m’mbali mwa nyanja ya galileya, adawona Simoni ndi Andreya, mbale wake, alimkuponya khoka m’nyanja; pakuti adali asodzi.

Mar 1:17 Ndipo Yesu adanena nawo, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu

Mar 1:18 Ndipo pomwepo adasiya makoka awo, namtsata Iye.

Mar 1:19 Ndipo atapita patsogolo pang’ono, adawona Yakobo, mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wake, iwonso adali m’chombo ali kusoka makoka awo:

Mar 1:20 Ndipo pomwepo adawayitana iwo; ndipo adasiya atate wawo Zebedayo m’chombomo pamodzi ndi antchito wolembedwa, namtsata Iye.

Mar 1:21 Ndipo iwo adalowa m’Kapernawo; ndipo pomwepo pa tsiku la sabata Iye adalowa m’sunagoge naphunzitsa.

Mar 1:22 Ndipo adazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti adaphunzitsa monga mwini mphamvu, simonga alembi.

Mar 1:23 Ndipo pomwepo padali munthu m’sunagoge mwawo adali ndi mzimu wonyansa; ndipo adafuwula iye,

Mar 1:24 Kuti, Tisiyeni, tiri ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzatiwononga ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.

Mar 1:25 Ndipo Yesu adawudzudzula, kuti, Khala chete, nutuluke mwa iye.

Mar 1:26 Ndipo pamene mzimu wonyansa, pom’ng’amba iye ndi kufuwula ndi mawu akulu, udatuluka mwa iye.

Mar 1:27 Ndipo adazizwa onse, kotero kuti adafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu Iye alamula ngakhale mizimu yonyansa, ndipo idamvera Iye.

Mar 1:28 Ndipo kutchuka kwake kudabuka pompaja ku dziko lonse la Galileya lozungulurapo.

Mar 1:29 Ndipo pomwepo, potuluka m’sunagoge, iwo adalowa m’nyumba ya Simoni ndi Andreya pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.

Mar 1:30 Ndipo mayi wake amkazi wa Simoni adali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo adamuwuza za iye!

Mar 1:31 Ndipo anadza namgwira Iye pa dzanja, namuwutsa; ndipo nthawi yomweyo malungo adamleka, ndipo adawatumikira iwo.

Mar 1:32 Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nawo kwa Iye onse wodwala, ndi wogwidwa ndi ziwanda.

Mar 1:33 Ndipo mzinda wonse udasonkhana pakhomo

Mar 1:34 Ndipo adachiritsa anthu ambiri wodwala nthenda za mitundu mitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sadalole ziwandazo kuyankhula, chifukwa zidamdziwa Iye.

Mar 1:35 Ndipo m’mawa mwake adawuka usikusiku, natuluka napita pa yekha, napemphera kumeneko.

Mar 1:36 Ndipo Simoni ndi amzake adali naye, adamtsata Iye.

Mar 1:37 Ndipo pamene adampeza Iye, adanena naye, Akufunani Inu anthu onse.

Mar 1:38 Ndipo adanena kwa iwo, Tiyeni kwina, ku mizinda ili pafupi apa, kuti ndikalalikire komweko; pakuti ndadzera ntchito imeneyi.

Mar 1:39 Ndipo adalowa m’masunagoge mwawo m’Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.

Mar 1:40 Ndipo adadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira Iye, ndi kunena ndi Iye. Ngati mufuna mukhoza kundikonza.

Mar 1:41 Ndipo Yesu adagwidwa chifundo, natambasula dzanja lake namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.

Mar 1:42 Ndipo atangoyankhula nthawi yomweyo, khate lidamchoka, ndipo adakonzedwa.

Mar 1:43 Ndipo adamulamulira iye, namtulutsa pomwepo;

Mar 1:44 Ndipo adanena kwa iye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense; koma pita, ukadziwonetse wekha kwa wansembe, nuperekepo makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo

Mar 1:45 Ndipo iye adatuluka nayamba kulengeza ndithu, ndi kubukitsa nkhaniyo, kotero kuti Yesu sadakhoze kulowanso poyera mu mzinda, koma adakhala padera m’zipululu; ndipo anadza kwa Iye anthu wochokera ku madera onse.



2

Mar 2:1 Ndipo Iye adalowanso m’Kapernawo atapita masiku ena, ndipo kudamveka kuti adali m’nyumba.

Mar 2:2 Ndipo ambiri adasonkhana pamodzi, kotero kuti adasowa malo wowalandirirapo, ngakhale pakhomo pomwe. Ndipo adawalalikira iwo mawu.

Mar 2:3 Ndipo anadza kwa Iye wotenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anayi.

Mar 2:4 Ndipo pamene sadakhoze kufika kudali Iye, chifukwa cha khamu la anthu, adasasula denga pokhala Iye; ndipo pamene adatha kulibowola adatsitsa kama amene wodwala manjenjeyo adagona.

Mar 2:5 Pamene Yesu adawona chikhulupiriro chawo, adanena kwa wodwala manjenjeyo, Mwana, machimo ako akhululukidwa.

Mar 2:6 Koma adakhalapo ena alembi pamenepo amene adaganizira mumtima mwawo,

Mar 2:7 Kodi n’chifukwa chiyani munthu ameneyu akuchitira Mulungu mwano wotere? Akhoza ndani kukhululukira machimo, koma m’modzi, ndiye Mulungu?

Mar 2:8 Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mu mzimu wake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, adanena nawo, Muganiza bwanji zinthu izi m’mitima yanu?

Mar 2:9 Chapafupi n’chiti, kapena kumuwuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?

Mar 2:10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nazo mphamvu zakukhululukira machimo pa dziko lapansi (adanena ndi wodwala manjenjeyo,)

Mar 2:11 Ndikuwuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.

Mar 2:12 Ndipo pomwepo adanyamuka iye, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, zotere sitidaziwonepo ndi kale lonse.

Mar 2:13 Ndipo adatulukanso kumka m’mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo adawaphunzitsa.

Mar 2:14 Ndipo popita adawona Levi mwana wa Alifeyo atakhala polandirira msonkho, ndipo adanena naye, Tsata Ine, ndipo adanyamuka namtsata Iye.

Mar 2:15 Ndipo kudali kuti Yesu atakhala pachakudya m’nyumba mwake, ndipo amisonkho, ndi wochimwa ambiri adakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi wophunzira ake, pakuti adali ambiri, ndipo adamtsata Iye.

Mar 2:16 Ndipo pamene Alembi ndi Afarisi adawona Iye kuti alimkudya nawo wochimwa ndi amisonkho, adanena ndi wophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nawo amisonkho ndi wochimwa?

Mar 2:17 Ndipo pamene Yesu adamva ichi, adanena nawo, Wolimba safuna sing’anga, koma wodwala ndiwo; sindidadza kudzayitana wolungama, koma wochimwa kuti alape.

Mar 2:18 Ndipo wophunzira a Yohane ndi Afarisi adalimkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya wophunzira a Yohane, ndi wophunzira Afarisi, koma wophunzira anu sasala kudya?

Mar 2:19 Ndipo Yesu adanena nawo, Kodi akhoza kusala kudya ana a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nawo? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala.

Mar 2:20 Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya m`masiku amenewo.

Mar 2:21 Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yatsopano pa chobvala chakale; mwina chigamba chatsopanocho chikhoza kuzomoka kuyakaleyo, ndipo chibowo chake chikhala chachikulu.

Mar 2:22 Ndipo palibe munthu amathira vinyo watsopano m’mabotolo akale; pena vinyo adzaswa mabotolo, ndipo akhoza kuwonongeka vinyo, ndi mabotolo omwe; koma vinyo watsopano, amathiridwa m’mabotolo atsopano.

Mar 2:23 Ndipo kunali kuti adapita Iye pakati pa minda ya tirigu tsiku la sabata; ndipo wophunzira ake poyenda adayamba kubudula ngala za tirigu.

Mar 2:24 Ndipo Afarisi adanena kwa Iye, Tawonani, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la sabata?

Mar 2:25 Ndipo adanena nawo, simudawerenga konse chimene adachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene adali pamodzi naye?

Mar 2:26 Kuti adalowa m’nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yowonetsera yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo adawapatsanso iwo amene adali naye?

Mar 2:27 Ndipo adanena kwa iwo, sabata lidayikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha sabata:

Mar 2:28 Motero Mwana wa munthu ali Mbuye wa Sabata.



3

Mar 3:1 Ndipo adalowanso m’sunagoge; ndipo mudali munthu m’menemo adali ndi dzanja lake lopuwala.

Mar 3:2 Ndipo adamuyang’anira Iye ngati adzamchiritsa iye tsiku la sabata; kuti amtsutse Iye.

Mar 3:3 Ndipo Iye adanena ndi munthu adali ndi dzanja lopuwala, Tayimilira.

Mar 3:4 Ndipo adanena kwa iwo, N’kololedwa tsiku la sabata kuchita zabwino, kapena zoyipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma adakhala chete.

Mar 3:5 Ndipo m’mene adawawunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuwuma kwa mitima yawo, adanena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo adalitambasula; ndipo lidachira dzanja monga limzake.

Mar 3:6 Ndipo Afarisi adatuluka, ndipo pomwepo adamkhalira upo ndi Aherode monga momwe angamuwonongere Iye.

Mar 3:7 Ndipo Yesu adachokako pamodzi ndi wophunzira ake namka kunyanja; ndipo lidamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi la aku Yudeya,

Mar 3:8 Ndi wochokera ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordano, ndi a kufupi ku Turo ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo adazichita, linadza kwa Iye.

Mar 3:9 Ndipo adayankhula kwa wophunzira ake, kuti chombo chaching`ono chidikire Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye.

Mar 3:10 Pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse wokhala nayo miliri adamkanikiza Iye, kuti akamkhudze,

Mar 3:11 Ndipo mizimu yonyansa, m’mene idamuwona Iye, idagwa pansi pamaso pake, nifuwula, niyiti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.

Mar 3:12 Ndipo pomwepo Iye adayilamulira kuti isamuwulule Iye.

Mar 3:13 Ndipo Iye adakwera m’phiri, nadziyitanira iwo amene adawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye.

Mar 3:14 Ndipo adasanjika manja pa khumi ndi awiri kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kukalalikira.

Mar 3:15 Ndi kuti akhale nazo mphamvu zochiritsa ndi zotulutsa ziwanda.

Mar 3:16 Ndipo Simoni adamutcha Petro.

Mar 3:17 Ndi Yakobo mwana wa Zebedeyo, ndi Yohane m’bale wake wa Yakobo, iwo adawatcha Boanerge, ndiko kuti Ana a bingu;

Mar 3:18 Ndi Andreya, ndi Filipo ndi Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi ndi Yakobo mwana waAlifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,

Mar 3:19 Ndi Yudase Isikariyote, ndiye amene adampereka Iye. Ndipo adalowa m’nyumba.

Mar 3:20 Ndipo khamulo lidasonkhananso, kotero kuti sadadye iwo konse mkate.

Mar 3:21 Ndipo pamene abwenzi ake adamva adadza kudzamgwira Iye; pakuti adati adayaluka.

Mar 3:22 Ndipo alembi amene adatsika kuchokera ku Yerusalemu adati, Ali ndi Belizebule, ndipo ndi mkulu wawo wa ziwanda atulutsa ziwanda.

Mar 3:23 Ndipo adawayitana iwo, nanena nawo m’mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana?

Mar 3:24 Ndipo ufumu ukagawanika pa wokha, sukhoza kukhazikika.

Mar 3:25 Ndipo ngati nyumba igawanika pa iyo yokha, siyikhoza kukhazikika nyumbayo payokha.

Mar 3:26 Ndipo ngati Satana adziwukira mwini yekha, nagawanika sakhoza kuyima payekha, koma atsirizika.

Mar 3:27 Palibe munthu akhoza kulowa m’nyumba ya munthu wa mphamvu, ndi kuwononga katundu wake, koma ayambe wamanga munthu wa mphamvuyo; ndipo pamenepo adzawononga za m’nyumba mwake.

Mar 3:28 Indetu, ndinena ndi inu, Machimo onse ana anthu, ndi zamwano zili zonse adzachita adzakhululukidwa,

Mar 3:29 Koma ali yense amene adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma ali m’chiweruziro chowopsa chosantha;

Mar 3:30 Chifukwa adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.

Mar 3:31 Ndipo anadza amake ndi abale ake, nayima kunja, namtumizira uthenga kumuyitana.

Mar 3:32 Ndipo khamu lambiri lidakhala pansi momzungulira; nanena kwa Iye, Onani, amayi anu ndi abale anu ali kunja akukufunani Inu.

Mar 3:33 Ndipo adawayankha iwo nanena, Amayi wanga ndi abale anga ndani?

Mar 3:34 Ndipo adawunguza wunguza iwo amene adakhala momzungulira Iye, nanena, Tawonani, amayi wanga ndi abale anga.

Mar 3:35 Pakuti ali yense adzachita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga ndi mlongo, ndi amayi.



4

Mar 4:1 Ndipo adayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo adasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti adalowa Iye m`chombo, nakhala m’nyanja; ndipo khamu lonse lidakhala pamtunda m’bali mwa nyanja.

Mar 4:2 Ndipo adawaphunzitsa zinthu zambiri m’mafanizo, nanena nawo m’chiphunzitso chake,

Mar 4:3 Mverani; Tawonani, wofesa adatuluka kukafesa:

Mar 4:4 Ndipo kudali, zitapita izi pamene amkafesa, zina zidagwa m’mbali mwa njira ndi mbalame zamumlengalenga zinadza ndi kuzidya.

Mar 4:5 Ndipo zina zinagwa pa nthaka ya mwala pamene panalibe dothi lambiri, ndipo pomwepo zidamera, koma zinalibe dothi lakuya:

Mar 4:6 Ndipo pamene dzuwa lidakwera zidapserera; ndipo popeza zidalibe mizu zidafota

Mar 4:7 Ndipo zina zinagwa pakati pa minga, ndipo minga idakula, nizitsamwitsa, ndipo sizinabala zipatso.

Mar 4:8 Ndipo zina zinagwa m’nthaka yabwino, ndipo zidapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.

Mar 4:9 Ndipo adanena kwa iwo, Amene ali nawo makutu akumva amve.

Mar 4:10 Ndipo pamene adakhala pa yekha, iwo amene adali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo adamfunsa Iye za mafanizo.

Mar 4:11 Ndipo Iye adanena nawo, Kwa inu kwapatsidwa kudziwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonsezi zichitidwa m’mafanizo.

Mar 4:12 Kuti kupenya apenye koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwe; kuti pena angatembenuke mtima ndi kukhululukidwa machimo awo.

Mar 4:13 Ndipo adanena nawo, Simudziwa kodi fanizo ili? ndipo mudzazindikira bwanji mafanizo onse?

Mar 4:14 Wofesa afesa mawu.

Mar 4:15 Ndipo iwo ndiwo am’mbali mwa njira mofesedwamo mawu; ndipo pamene adamva, pomwepo anadza Satana nachotsa mawu wofesedwa m`mitima mwawo.

Mar 4:16 Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pamwala, atamva mawu, awalandira pomwepo ndi kusekerera;

Mar 4:17 Ndipo alibe mizu mwa iwo wokha, koma apilira kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mawu, pomwepo akhumudwa.

Mar 4:18 Ndipo awa ndiwo wofesedwa paminga; iwo ndiwo amene adamva mawu,

Mar 4:19 Ndipo chisamaliro cha dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mawu, ndipo akhala wopanda chipatso.

Mar 4:20 Ndipo awa ndiwo wofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mawu, nawalandira, nabala zipatso zopindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.

Mar 4:21 Ndipo adanena ndi iwo, kodi atenga nyali kuti akayibvundikire mbiya, kapena akayiyika pansi pa kama, osati kuti akayiyike pa choyikapo chake?

Mar 4:22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, kamene sikadzawonetsedwa; kapena kulibe kanthu kakukhala m’seli, kamene sikadzawululidwa.

Mar 4:23 Ngati munthu aliyense ali nawo makutu akumva, amve.

Mar 4:24 Ndipo adanena nawo, Samalirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesa nawo udzayesedwa kwa inu; ndipo inu amene mukumva kudzawonjezeredwa kwa inu.

Mar 4:25 Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kali konse ali nako.

Mar 4:26 Ndipo adanena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbewu panthaka;

Mar 4:27 Ndipo akagona ndi kuwuka, usiku ndi usana, ndipo mbewu zikamera ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.

Mar 4:28 Pakuti nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba m’mera, zitsata ngala, pamenepo maso wokhwima m’ngalamo.

Mar 4:29 Zikakhwima zipatso, pamenepo atumiza chikwanje, pakuti nthawi yokolola yafika.

Mar 4:30 Ndipo adanena, Tidzafanizira ndi chiyani Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzawulinganiza ndi fanizo lotani?

Mar 4:31 Uli ngati mbewu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ili yaying’ono mwa mbewu zonse za padziko lapansi.

Mar 4:32 Koma pamene ifesedwa, imela nikula koposa zitsamba zonse, nichita nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za mu mlengalenga zikhoza kubindikira munthunzi mwake.

Mar 4:33 Ndipo ndi mafanizo otere ambiri adayankhula nawo mawu, monga adakhoza kumva;

Mar 4:34 Ndipo sadayankhule nawo wopanda fanizo: koma mseli adatanthawuzira zonse kwa wophunzira ake.

Mar 4:35 Ndipo tsiku lomwelo, pofika madzulo, adanena kwa iwo, Tiwolokere tsidya lina.

Mar 4:36 Ndipo pamene adalitumiza khamulo adamtenga Iye, monga momwe adali, chombo. Ndipo padali zombo zazing`ono zina pamodzi ndi Iye.

Mar 4:37 Ndipo padawuka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde adagabvira m`chombo, motero kuti chombo chidayamba kudzaza.

Mar 4:38 Ndipo Iye mwini adali ku chiwongolero, chachombo nagona tulo, pamtsamiro; ndipo adamudzutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti tiri kuwonongeka ife?

Mar 4:39 Ndipo adadzuka, nadzudzula mphepo,nati kwa nyanja kuti, Tonthola nukhale bata, ndipo kudagwa bata lalikulu ndipo mphepo idaleka ndikugwa bata lalikulu.

Mar 4:40 Ndipo adanena nawo, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi?

Mar 4:41 Ndipo iwo adachita mantha akulu, nanena wina ndi mzake, Munthu uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?



5

Mar 5:1 Ndipo adafika tsidya lina la nyanja, ku dziko la Agerasa.

Mar 5:2 Ndipo pamene adatuluka m`chombomo, pomwepo adakomana naye munthu wotuluka ku manda wogwidwa ndi mzimu wonyansa.

Mar 5:3 Amene adayesa nyumba yake kumanda; ndipo panalibe munthu adakhoza kum’manganso, inde ngakhale ndi unyolo.

Mar 5:4 Pakuti ankamangidwa kawiri kawiri ndi matangadza ndi unyolo, ndipo adamwetula unyolo, naduladula matangadza; ndipo panalibe munthu adali ndi mphamvu yakumgwira.

Mar 5:5 Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, adakhala m’mapiri ndi m’manda, nafuwula, nadzitematema ndi miyala.

Mar 5:6 Ndipo pamene adamuwona Yesu kutali, adathamanga nampembedza Iye,

Mar 5:7 Ndipo adafuwula ndi mawu akulu, nanena, Ndiri ndi chiyani ndi inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikulumbirirani pa Mulungu musandizunze.

Mar 5:8 Pakuti adanena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.

Mar 5:9 Ndipo adamfunsa iye, Dzina lako ndani? Ndipo adayankha kuti, Dzina langa ndine Legiyo; chifukwa tiri ambiri.

Mar 5:10 Ndipo adampempha Iye kwambiri kuti asayitulutsire kunja kwake kwa dziko.

Mar 5:11 Ndipo pamenepo padali gulu lalikulu la nkhumba zidali kudya kuphiri.

Mar 5:12 Ndipo mizimu yonse yoyipa idampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo.

Mar 5:13 Ndipo Yesu adayilola kuti ichoke. Ndipo mizimu yonyansa idatuluka, nilowa munkhumba; ndipo gulu lidatsika ndi liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zidatsamwa m’nyanja.

Mar 5:14 Ndipo woziweta adathawa, nakanena ku m`mzinda, ndi kudziko. Ndipo adatuluka kudzawona chochitikacho.

Mar 5:15 Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo atakhala pansi, wobvala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene adali ndi Legiyo; ndipo adawopa iwo.

Mar 5:16 Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo adachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo.

Mar 5:17 Ndipo adayamba kumpempha Iye kuti achoke m’malire awo.

Mar 5:18 Ndipo m’mene Iye adali kulowa m`chombo, adampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye.

Mar 5:19 Ndipo Yesu sadamulole, koma adanena naye, Pita kwanu kwa abwenzi ako, nuwawuze zinthu zazikulu adakuchitira Ambuye, ndi kuti adakuchitira chifundo.

Mar 5:20 Ndipo adachoka nayamba kulalikira ku Dekapolisi zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse adazizwa. Yesu achiritsa mkazi kunthenda yokha mwazi, naukitsa mwana

Mar 5:21 Ndipo pamene Yesu adawolokanso m`chombo kupita tsidya lina, khamu lalikulu lidasokhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.

Mar 5:22 Ndipo wonani, adadzako m’modzi wa akulu a sunagoge dzina lake Yairo; ndipo pakuwona, iye adagwada pamapazi ake.

Mar 5:23 Ndipo nampepha Iye kwambiri nanena naye, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalimkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muyike manja anu pa iko, kuti kachiritsidwe, ndi kukhala ndi moyo.

Mar 5:24 Ndipo Yesu adamka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu lidamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye.

Mar 5:25 Ndipo mkazi wina amene adali ndi nthenda ya mwazi kwa zaka khumi ndi ziwiri,

Mar 5:26 Ndipo adamva zowawa zambiri mwa a sing’anga ambiri, nalipira zonse adali nazo osachira m’pang’ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula,

Mar 5:27 Ndipo m’mene iye adamva mbiri yake ya Yesu, anadza m’khamu kumbuyo kwake, nakhudza chobvala chake.

Mar 5:28 Pakuti adanena iye, Ngati ndikhudza ngakhale zobvala zake ndidzachiritsidwa.

Mar 5:29 Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake ya mwazi idaphwa; ndipo adazindikira m’thupi kuti adachiritsidwa ku m`liri wake.

Mar 5:30 Ndipo pomwepo Yesu, pamene adazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, adapotolokera kwa womkanikizawo, nanena, Ndani adakhudza zobvala zanga?

Mar 5:31 Ndipo wophunzira ake adanena kwa Iye, Mukuwona kuti khamu liri kukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani?

Mar 5:32 Ndipo Iye adawunguzawunguza kuti awone iye amene adachita ichi.

Mar 5:33 Koma mkaziyo powopa ndi kunthunthumira, podziwa chimene adamchitira mwa iye, adadza, nagwa pa Iye, namuwuza Iye chowona chonse.

Mar 5:34 Ndipo Iye adati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; pita mu mtendere, nukhale wochira kumliri wako.

Mar 5:35 M’mene Iye adali chiyankhulire, adafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; ubvutiranjinso Mphunzitsi?

Mar 5:36 Mwamsanga atamva Yesu mawu adayankhulidwawo adanena kwa mkulu wa sunagoge, Usawope, khulupilira kokha.

Mar 5:37 Ndipo sadalole munthu aliyense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane m’bale wake wa Yakobo.

Mar 5:38 Ndipo adafika ku nyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo adawona chipiringu, ndi wochita maliro ndi wokuwa ambiri.

Mar 5:39 Ndipo m’mene adalowa, adanena nawo, Mubuma ndi kulira chifukwa chiyani? Buthuli silidafe koma liri m’tulo.

Mar 5:40 Ndipo adamseka Iye pwepwete, koma pamene Iye adawatulutsa onse, adatenga atate ndi amake abuthulo ndi ajawo adali naye, nalowa m’mene mudali buthulo

Mar 5:41 Ndipo adagwira dzanja lake la buthulo, nanena kwa iye, Talita koumi; ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe. Uka.

Mar 5:42 Ndipo pomwepo buthulo lidawuka niliyenda; pakuti lidali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.

Mar 5:43 Ndipo adawalamulira kwambiri kuti asadziwe, ichi munthu m’modzi, nawawuza kuti ampatse iye kudya.



6

Mar 6:1 Ndipo Iye adatuluka kumeneko; nafika ku dziko la kwawo; ndipo wophunzira ake adamtsata.

Mar 6:2 Ndipo pofika tsiku la sabata, adayamba kuphunzitsa m’sunagoge; ndipo ambiri adamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani? Ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake?

Mar 6:3 Kodi uyu sim’misiri wa matabwa, mwana wa Mariya, m’bale wawo wa Yakobo, ndi Yosefe, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ake Sali nafe pano kodi? Ndipo adakhumudwa ndi Iye.

Mar 6:4 Ndipo Yesu adanena kwa iwo, M’neneri sakhala wopanda ulemu, koma m’dziko la kwawo ndimo ndi pakati pa abale ake, ndi m’nyumba yake.

Mar 6:5 Ndipo kumeneko sadakhoza Iye kuchita ntchito zamphamvu konse, koma kuti adayika manja ake pa anthu wodwala wowerengeka, nawachiritsa.

Mar 6:6 Ndipo adazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Ndipo adayendayenda m’midzi yozungulirapo, naphunzitsa

Mar 6:7 Ndipo adadziyitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiri awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;

Mar 6:8 Ndipo adawalamulira kuti asatenge kanthu ka pa ulendo wawo, koma ndodo yokha; asatenge lamba, mkate, kapena ndalama m’matumba awo;

Mar 6:9 Koma abvale nsapato; ndipo osati abvale malaya awiri.

Mar 6:10 Ndipo adanena nawo, Kumalo kuli konse mukalowa m’nyumba, khalani komweko kufikira mutachokako.

Mar 6:11 Ndipo aliyense amene sakulandirani, kapena kumvera inu, pochoka kumeneko sansani fumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo. Indetu ndinena ndi inu kuti patsiku la chiweruziro mlandu wa mzindawo udzakhala waukulu koposa wa Sodomu ndi Gomora.

Mar 6:12 Ndipo adatuluka nalalikira kuti anthu alape.

Mar 6:13 Ndipo adatulutsa mizimu yoyipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri, wodwala, nawachiritsa.

Mar 6:14 Ndipo mfumu Herode adamva za Iye; (pakuti dzina lake lidatchuka ponse ponse) ndipo adanena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake ntchito za mphamvuzi zichitachita mwa Iye.

Mar 6:15 Koma ena adanena kuti, Ndiye Eliya, Adati enanso, ndiye m’neneri, kapena m`modzi wa aneneriwo.

Mar 6:16 Koma pamene Herode adamva, adanena, Ndi Yohane amene ndinamdula mutu, wawuka kwa akufa.

Mar 6:17 Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nam’manga m’nyumba ya ndende, chifukwa cha Herodiya, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.

Mar 6:18 Pakuti Yohane adanena kwa Herode, sikuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu.

Mar 6:19 Chifukwa cha ichi adakangana momtsutsa Herodiya nafuna kumumpha iye koma adalemphera.

Mar 6:20 Pakuti Herode adawopa Yohane podziwa kuti adali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo adamsunga iye. Ndipo pamene adamva iye, adachita zambiri, nakondwera pakumva iye.

Mar 6:21 Ndipo pamene lidafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye adawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu wotchuka a ku Galileya;

Mar 6:22 Ndipo pamene mwana wa mkazi wa Herodiya adalowa yekha nabvina, adakondweretsa Herode ndi iwo wokhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo idati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chiri chonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe.

Mar 6:23 Ndipo adamlumbirira iye, kuti, chiri chonse ukandipempha ndidzakupatsa, ngakhale kukugawira ufumu wanga.

Mar 6:24 Ndipo adatuluka, nati, kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye adati, Mutu wake wa Yohane M’batizi.

Mar 6:25 Ndipo pomwepo adalowa mwachangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane M’batizi m`mbale.

Mar 6:26 Ndipo mfumu idamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo wokhala pa chakudya, sadafune kumkaniza.

Mar 6:27 Ndipo pomwepo mfumu idatuma wokamumpha, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye adapita namdula mutu m’nyumba ya ndende.

Mar 6:28 Ndipo adamtengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthulo lidaupereka kwa amake.

Mar 6:29 Ndipo m’mene wophunzira ake adamva, anadza nanyamula mtembo wake nawuyika m’manda.

Mar 6:30 Ndipo atumwi adasonkhana mwa iwo wokha kwa Yesu; namuwuza zinthu ziri zonse adazichita, ndi kuziphunzitsa.

Mar 6:31 Ndipo Iye adanena nawo, Idzani inu nokha padera ku malo a chipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka adali piringu piringu ndipo adalibe nthawi yokwanira kuti adye

Mar 6:32 Ndipo adachoka pa chombo kupita ku malo achipululu padera.

Mar 6:33 Ndipo anthu adawawona ali kupita, ndipo ambiri adawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, nadza pamodzi kwa Iye wochokera m’mizinda yonse nawapitirira.

Mar 6:34 Ndipo Yesu pamene adatuluka, nawona khamu lalikulu la anthu, anagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa adali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo adayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

Mar 6:35 Ndipo pamene tsiku lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye wophunzira ake, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yatha ndithu.

Mar 6:36 Muwatumize iwo kuti apite, alowe ku milaga ndi ku midzi yozungulira, kuti akadzigulire wokha kanthu kakudya. Pakuti alibe kanthu kakudya.

Mar 6:37 Koma Iye adayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo adanena naye, kodi tipite ife ndi kugula mikate ya makobiri mazana awiri ndi kuwapatsa kudya?

Mar 6:38 Ndipo Iye adanena kwa iwo, kuti, Muli nayo mikate ingati? Pitani mukawone. Ndipo m’mene adadziwa adanena, Isanu ndi nsomba ziwiri.

Mar 6:39 Ndipo adawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulu magulu pawudzu.

Mar 6:40 Ndipo adakhala pansi mabungwe mabungwe a makumi khumi ndi a makumi asanu.

Mar 6:41 Ndipo pamene Iye adatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo adayang’ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa iyo kwa wophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri adagawira onsewo.

Mar 6:42 Ndipo anadya iwo onse, nakhuta.

Mar 6:43 Ndipo adatola makombo, mitanga khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba.

Mar 6:44 Ndipo amene adadya mikateyo adali amuna zikwi zisanu.

Mar 6:45 Ndipo pomwepo Iye adalamulira wophunzira ake alowe m`chombo, ndi kutsogolera kupita kutsidya lija ku Betsayida, m’mene Iye yekha adali kuwuza khamulo kuti lichoke.

Mar 6:46 Ndipo atatsanzikana nalo, adachoka Iye, nalowa m’phiri kukapemphera.

Mar 6:47 Ndipo pofika madzulo chombo chidali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha adali pamtunda.

Mar 6:48 Ndipo pakuwawona ali kubvutika ndi kupalasa, pakuti mphepo idadza mokomana nawo, ndipo pa ulonda wachinayi wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire.

Mar 6:49 Koma iwo, pamene adamuwona Iye alikuyenda panyanja, adayesa kuti ndi mzukwa, nafuwula:

Mar 6:50 Pakuti iwo onse adamuwona Iye, nabvutika. Koma pomwepo adawayankhula nanena kwa iwo, Kondwerani; Ndinetu, musawope.

Mar 6:51 Ndipo Iye adakwera, nalowa kwa iwo chombo, ndipo mphepo idaleka; ndipo anadabwa kwakukulu koposa muyeso mwa iwo wokha.

Mar 6:52 Pakuti sadazindikire za chozizwitsa cha mikateyo, pakuti mitima yawo idawumitsidwa.

Mar 6:53 Ndipo atawoloka iwo, adafika pamtunda ku Genesarete, nakocheza padowoko.

Mar 6:54 Ndipo pamene adatuluka m’chombo adamzindikira Iye pomwepo.

Mar 6:55 Ndipo adathamanga dziko lonselo mozungulira nayamba kunyamula anthu wodwala pamphasa zawo, kufika nawo kumene adamva kuti analiko Iye.

Mar 6:56 Ndipo kumene kulikonse adalowa Iye m’midzi, kapena m’mizinda, kapena m’milaga, anthu adagoneka wodwala m`misewu, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chobvala chake; ndipo onse amene adamkhudza adachiritsidwa.



7

Mar 7:1 Ndipo adasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi ena alembi, wochokera ku Yerusalemu.

Mar 7:2 Ndipo pamene adawona ena a wophunzira ake akudya mkate ndi m’manja mwakuda, ndi mosasamba, adampezerapo chifukwa.

Mar 7:3 Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse samadya osasamba m’manja mwawo, kuti asunge mwambo wa akulu.

Mar 7:4 Ndipo pochokera ku m’sika, sakudya asanasambe m’thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri adazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa ndi magome.

Mar 7:5 Ndipo Afarisi ndi alembi adamfunsa Iye, Bwanji wophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wawo ndi m’manja mwakuda?

Mar 7:6 Iye adawayankha nati kwa iwo, Yesaya adanenera bwino za inu wonyenga, monga kwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ikhala kutali ndi Ine.

Mar 7:7 Koma andilambira Ine kwa chabe, ndi kuphunzitsa ziphunzitso za malamulo a anthu.

Mar 7:8 Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu, monga kutsuka miphika ndi zikho; ndi zinthu zina zambiri zimene muchita.

Mar 7:9 Ndipo adanena nawo, Mochenjera mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu.

Mar 7:10 Pakuti Mose adati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo iye wonenera zoyipa atate wake kapena amayi wake, afe imfa:

Mar 7:11 Koma inu munena, Ngati munthu akati kwa atate wake, kapena amayi wake, Korbani, ndiko kuti mphatso imene ukadathandizidwa nayo ndi ine; adzakhala womasulidwa.

Mar 7:12 Ndipo simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amayi wake;

Mar 7:13 Muyesa achabe mawu a Mulungu monga mwa mwambo wanu, umene mudaupereka; ndi zinthu zotere zambiri muzichita.

Mar 7:14 Ndipo pamene adadziyitaniranso khamu la anthu kwa Iye, adanena nawo, Mverani Ine nonsenu ndipo mudziwitse:

Mar 7:15 Kulibe kanthu kunja kwa munthu kolowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zotuluka mwa iye, ndizo zomdetsa munthu.

Mar 7:16 Ngati munthu ali nawo makutu akumva, muloleni amve.

Mar 7:17 Ndipo m’mene Iye adalowa m’nyumba kusiyana ndi khamulo, wophunzira ake adamfunsa Iye za fanizolo.

Mar 7:18 Ndipo adanena nawo, Inunso mukhala wopanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kali konse kochokera kunja kolowa mwa munthu sikangathe kumdetsa iye;

Mar 7:19 Chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m’mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo ndipo potero adayeretsa zakudya zonse.

Mar 7:20 Ndipo adati, chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu.

Mar 7:21 Pakuti m’kati mwake mwa mitima ya anthu mutuluka maganizo woyipa, za chigololo, chiwerewere, kupha,

Mar 7:22 Kuba, kusilira kuchita zoyipa, chinyengo, chinyanso, diso loyipa, mwano, kudzikuza, kupusa:

Mar 7:23 Zoyipa izi zonse zichokera mkati nizidetsa munthu.

Mar 7:24 Ndipo Iye adawuka nachoka kumeneko, nanka ku malire a ku Turo ndi Sidoni. Ndipo adalowa m’nyumba, nafuna kuti asadziwe munthu aliyense; ndipo sadakhoza kubisika.

Mar 7:25 Pakuti mkazi wina amene adali ndi kabuthu kake kamene kadali ndi mzimu wonyansa. Pamene adamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake.

Mar 7:26 Koma mkaziyo adali Mhelene, mtundu wake Msuro-Fonika. Ndipo adampempha Iye kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake.

Mar 7:27 Koma Yesu adanena naye, Baleka, ayambe akhuta ana; pakuti sibwino kutenga mkate wa ana, ndi kuwutayira tiagalu.

Mar 7:28 Ndipo iye adayankha nati kwa Iye, Inde Ambuye: tingakhale tiagalu tapansi pa gome timadyako nyenyeswa za ana.

Mar 7:29 Ndipo adati kwa iye, Chifukwa cha mawu amenewa, Pita; chiwanda chatuluka mwa mwana wako wamkazi.

Mar 7:30 Ndipo pamene adafika kunyumba kwake, adapeza mwana wakeyo atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.

Mar 7:31 Ndipo adatulukanso m’malire a ku Turo, ndi Sidoni, adafika ku nyanja ya Galileya, kupyola pakati pa mayiko a Dekapoli.

Mar 7:32 Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wa chibwibwi; ndipo adampempha Iye kuti ayike manja ake pa iye.

Mar 7:33 Ndipo adampatula pa khamu la anthu pa yekha, namulonga zala zake m’makutu mwake, nalabvula malobvu, nakhudza lilime lake;

Mar 7:34 Ndipo pakuyang`ana kumwamba, adawusa moyo, nanena kwa iye Efata ndiko kuti, Tatseguka.

Mar 7:35 Ndipo pomwepo makutu ake adatseguka, ndipo chomangira lilime lake chidamasulidwa ndipo adayankhula chilunjikire.

Mar 7:36 Ndipo adalengeza kopambana kuti asawuze munthu aliyense; koma monga momwe Iye adawalamulitsa momwenso makamaka adalengeza kopambana.

Mar 7:37 Ndipo anadabwa kwakukulu, koposa muyeso nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale wogontha awamvetsa, ndi wosayankhula awayankhulitsa.



8

Mar 8:1 Masiku amenewo pakukhalanso khamu lalikulu la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, Yesu adadziyitanira wophunzira ake kwa Iye yekha, nanena nawo.

Mar 8:2 Ndikumva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi Ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya.

Mar 8:3 Ndipo ngati ndiwawuza iwo kuti azipita kwawo osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali.

Mar 8:4 Ndipo wophunzira ake adamuyankha Iye, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yokhutitsa anthu awa m’chipululu muno?

Mar 8:5 Ndipo adawafunsa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo adati, Isanu ndi iwiri.

Mar 8:6 Ndipo adalamulira anthu kuti akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa wophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo adapereka kwa anthuwo.

Mar 8:7 Ndipo adali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anadalitsa, nalamulira kuti iwo atipereke itonso.

Mar 8:8 Ndipo adadya, nakhuta; ndipo adatola makombo madengu asanu ndi awiri.

Mar 8:9 Ndipo iwo amene adadya adali ngati zikwi zinayi; ndipo Iye adawatumiza apite.

Mar 8:10 Ndipo pomwepo adalowa m’chombo ndi wophunzira ake, ndipo adafika ku mbali ya ku Dalimanuta.

Mar 8:11 Ndipo Afarisi adatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera kumwamba, kumuyesa Iye.

Mar 8:12 Ndipo adawusa moyo mu mzimu wake, nanena, Anthu a m’badwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati Chizindikiro sichidzapatsidwa kwa m’badwo uno!

Mar 8:13 Ndipo adawasiya iwo, nalowanso m’chombo, nachoka kupita kutsidya lina.

Mar 8:14 Ndipo wophunzira adayiwala kutenga mikate, ndipo adalibe mkate m’chombo koma umodzi wokha.

Mar 8:15 Ndipo Iye adawalamulira iwo, nanena, chenjerani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.

Mar 8:16 Ndipo adatsutsana wina ndi mzake, nanena kuti, chifukwa chakuti tiribe mikate.

Mar 8:17 Ndipo pamene Yesu adazindikira, adanena nawo, Bwanji mukutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, ndikudziwitsa? Kodi mitima yanu ndi yowuma?

Mar 8:18 Pokhala nawo maso simupenya kodi? Ndipokhala nawo makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi?

Mar 8:19 Pamene tidanyema mikate isanu ndi kugawira kwa anthu zikwi zisanu, Kodi mudatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Iwo adanena kwa Iye, khumi ndi iwiri.

Mar 8:20 Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinayi, mudatola mitanga ingati yodzala ndi makombo? Ndipo adanena, Isanu ndi iwiri.

Mar 8:21 Ndipo Iye adanena nawo, Nanga n’chifukwa chiyani simukuzindikira?

Mar 8:22 Ndipo anadza ku Betsaida; ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze iye.

Mar 8:23 Ndipo adamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mzinda; ndipo atamthira malobvu m’maso mwake, nayika manja pa iye, adamfunsa iye, Uwona kanthu kodi?

Mar 8:24 Ndipo adakweza maso, nanena ndikuwona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.

Mar 8:25 Patatha izi adayikanso manja m’maso mwake, ndipo adampenyetsa kumwamba, nachiritsidwa, nawona munthu aliyense bwino bwino.

Mar 8:26 Ndipo adamtumiza apite kwawo, nanena, Usalowe konse m’muzinda kapena kuwuza wina ali yense mumzinda

Mar 8:27 Ndipo adatuluka Yesu ndi wophunzira ake, nalowa ku mizinda ya ku Kayisareya wa Filipi; ndipo panjira adawafunsa wophunzira ake, nanena nawo, Kodi anthu amanena kuti Ine ndine yani?

Mar 8:28 Ndipo adayankha nati, Yohane M`batizi; ndi ena Eliya; koma ena, M’modzi wa aneneri.

Mar 8:29 Ndipo Iye adati kwa iwo, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro adayankha nanena naye, Ndinu Khristu.

Mar 8:30 Ndipo adawalamulira iwo kuti asawuze munthu ndi m’modzi za Iye.

Mar 8:31 Ndipo adayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe akulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo pakutha masiku atatu akawuke.

Mar 8:32 Ndipo mawuwo adanena poyera. Ndipo Petro adamtenga Iye, nayamba kumdzudzula Iye.

Mar 8:33 Koma pamene adapotoloka, napenya wophunzira ake, adamdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu koma za anthu.

Mar 8:34 Ndipo pamene adadziyitanira anthu pamodzi ndi wophunzira ake, adati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine.

Mar 8:35 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya; ndipo yense wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino adzaupulumutsa.

Mar 8:36 Pakuti munthu apindulanji akadzilemeleretsa dziko lonse lapansi, natayapo moyo wake?

Mar 8:37 Kapena munthu adzapereka chiyani chosinthana ndi moyo wake?

Mar 8:38 Pakuti aliyense wochita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mawu anga mu m’badwo uno wachigololo ndi wochimwa. Mwana wa munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nawo angelo ake woyera, mu ulemerero wa Atate wake.



9

Mar 9:1 Ndipo adanena nawo, Indetu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena ayimilira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira atawona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.

Mar 9:2 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, ndi Yakobo ndi Yohane, nakwera nawo pa phiri lalitali padera pa wokha; ndipo adasinthika pamaso pawo:

Mar 9:3 Ndipo zobvala zake zidakhala zonyezimira, zoyera mbu kuposa; monga ngati muwomba wotsuka nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsayi.

Mar 9:4 Ndipo adawonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikuyankhulana ndi Yesu.

Mar 9:5 Ndipo Petro adayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, Kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange mahema atatu; imodzi yanu, ndi wina wa Mose ndi wina wa Eliya.

Mar 9:6 Pakuti sadadziwa chimene adzanena; chifukwa adachita mantha ndithu.

Mar 9:7 Ndipo padadza mtambo wophimba iwo, ndipo mawu adatuluka mu mtambowo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.

Mar 9:8 Ndipo dzidzidzi powunguzawunguza, sadapenya munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.

Mar 9:9 Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye adawalamulira kuti asawuze munthu aliyense zinthu zimene adaziwona kufikira pamene Mwana wa munthu akadzawuka kwa akufa ndipo.

Mar 9:10 Ndipo adasunga mawuwo mwa iwo wokha, nafunsana mwa iwo wokha, kuti kuwuka kwa akufa kutanthawuzanji?

Mar 9:11 Ndipo adamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena bwanji kuti adzayamba kufika Eliya?

Mar 9:12 Ndipo Iye adayankha nanena nawo, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzabwezeretsa zinthu zonse; nanga zalembedwa bwanji za Mwana wa munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe?

Mar 9:13 Koma ndinena ndi inu Kuti Eliya adabwera kale, ndipo adamchitiranso ziri zonse iwo adazifuna, monga kwalembedwa za iye.

Mar 9:14 Ndipo pamene anadza kwa wophunzira ake, adawona khamu lalikulu la anthu wozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nawo.

Mar 9:15 Ndipo pomwepo anthu onse, pakumuwona Iye, adazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namulonjera.

Mar 9:16 Ndipo adafunsa alembi, Mufunsana nawo chiyani?

Mar 9:17 Ndipo wina wa m’khamulo adamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nawo mzimu wosayankhula;

Mar 9:18 Ndipo ponse pamene umtenga iye, ung`amba iye; ndipo achita thobvu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndidayankhula nawo wophunzira anu kuti awutulutse; koma sadakhoza.

Mar 9:19 Ndipo Iye adawayankha iwo nanena, M`bado wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu nthawi yaitali yanji? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.

Mar 9:20 Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuwona iye, pomwepo mzimuwo udam’ng’amba kowopsa; ndipo adagwa pansi nabvimbvinika ndi kuchita thobvu.

Mar 9:21 Ndipo Iye adafunsa atate wake, kuti chimenechi chidayamba liti kumgwira? Ndipo adati, akali mwana.

Mar 9:22 Ndipo kawiri kawiri umamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuwononga iye; koma ngati mukhoza kuchita kanthu tithandizeni, ndi kutichitira chifundo.

Mar 9:23 Ndipo Yesu adanena naye, Ngati mukhulupilirira, zinthu zonse zitheka kwa iye wokhulupirira.

Mar 9:24 Pomwepo atate wa mwana adafuwula, nanena ndi misozi, Ambuye, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.

Mar 9:25 Ndipo pamene Yesu adawona kuti khamu la anthu liri kuthamangira pamodzi, adadzudzula mzimu woyipawo, nanena ndi uwo, mzimu wosayankhula ndi wongontha iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

Mar 9:26 Ndipo mzimu udafuwula, num’ngambitsa, udatuluka, ndipo mwana adakhala ngati wakufa, kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.

Mar 9:27 Koma Yesu adagwira dzanja lake, nam’nyamutsa; ndipo adayimilira.

Mar 9:28 Ndipo pamene Iye adalowa m’nyumba, wophunzira ake adafunsa mtseri kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuwutulutsa?

Mar 9:29 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi pemphero ndi kusala kudya.

Mar 9:30 Ndipo adachoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sadafune kuti munthu aliyense adziwe.

Mar 9:31 Pakuti adaphunzitsa wophunzira ake, nanena nawo kuti, Mwana wa munthu aperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzawukanso tsiku lachitatu.

Mar 9:32 Koma iwo sadazindikira mawuwo, nawopa kumfunsa Iye.

Mar 9:33 Ndipo Iye anadza ku Kapernao; ndipo pamene adakhala m’nyumba, Iye adawafunsa, Mudali kutsutsana chiyani panjira?

Mar 9:34 Koma iwo adakhala chete; pakuti adatsutsana wina ndi mzake panjira kuti, wamkulu ndani?

Mar 9:35 Ndipo m’mene adakhala pansi adayitana khumi ndi awiriwo; nanena nawo, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wa kuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.

Mar 9:36 Ndipo adatenga kamwana, nakayika pakati pawo, ndipo pamene adakayangata m`manja, ananena nawo,

Mar 9:37 Munthu aliyense amene adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, adzalandira Ine; ndipo yense amene adzalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene adandituma Ine.

Mar 9:38 Ndipo Yohane adamuyankha Iye, nati: Mpulumutsi, tidawona munthu alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tidamletsa, chifukwa sadali kutsata ife.

Mar 9:39 Koma Yesu adati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita chozizwa m’dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoyipa.

Mar 9:40 Pakuti iye wosatsutsana ndi ife ali kumbali yathu.

Mar 9:41 Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m’dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.

Mar 9:42 Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi katiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wa mphero ukolowekedwe m’khosi mwake, naponyedwe m’nyanja.

Mar 9:43 Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: n’kwabwino kwa iwe kulowa m’moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m’gehena, wa moto umene sudzakhoza kuzimitsidwa

Mar 9:44 Kumene mphutsi yawo siyifa, ndipo moto suzimitsidwa.

Mar 9:45 Ndipo ngati phazi likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m`moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino kuposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa m’gehena wa moto umene sudzakhoza kuzimitsidwa.

Mar 9:46 Kumene mphutsi yawo simafa ndiponso moto suzimitsidwa.

Mar 9:47 Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe mu Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m’gehena wa moto.

Mar 9:48 Kumeneko mphutsi yawo siyikufa, ndipo moto suzimitsidwa.

Mar 9:49 Pakuti onse adzathiridwa ndi mchere wa moto, ndi nsembe ili yonse idzathiridwa ndi m’chere.

Mar 9:50 Mchere ndi wabwino; koma ngati mchere usukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nawo mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mzake.



10

Mar 10:1 Ndipo adanyamuka Iye kumeneko, nadza ku malire a ku Yudeya ndi kutsidya lija la Yordano; ndipo adasonkhananso kwa Iye anthu ; ndipo monga adazolowera, adawaphunzitsanso.

Mar 10:2 Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, adamfunsa Iye: kodi nkololedwa kuti munthu achotse mkazi wake? kumuyesa Iye.

Mar 10:3 Ndipo Iye adayankha nati kwa iwo, Kodi Mose adakulamulirani inu chiyani?

Mar 10:4 Ndipo adati Mose adalola kulembera kalata wachilekaniro, ndi kumchotsa iye.

Mar 10:5 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Chifukwa cha kuuma kwa mitima yanu adakulemberani lamulo ili.

Mar 10:6 Koma kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe Mulungu adawapanga iwo mwamuna ndi mkazi.

Mar 10:7 Pachifukwa ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi ake, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wake;

Mar 10:8 Ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi.

Mar 10:9 Chifukwa chake chimene Mulungu adachimanga pamodzi, asachilekenitse munthu.

Mar 10:10 Ndipo m’nyumba wophunzira adamfunsanso za chinthu ichi.

Mar 10:11 Ndipo Iye adanena nawo, munthu ali yense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo.

Mar 10:12 Ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu.

Mar 10:13 Ndipo adadza nato kwa Iye tiana, kuti atikhudze: ndipo wophunzira ake adawadzudzula iwo amene adadza nato.

Mar 10:14 Koma pamene Yesu adawona adakwiya kwambiri, ndipo adati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.

Mar 10:15 Indetu ndinena ndi inu, munthu ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.

Mar 10:16 Ndipo Iye adatiyangata ndi manja ake, natidalitsa, ndi kuyika manja ake pa ito.

Mar 10:17 Ndipo pamene Iye adatuluka kutsata njira, adamthamangira m`modzi wolamulira, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?

Mar 10:18 Ndipo Yesu adati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma m’modzi ndiye Mulungu.

Mar 10:19 Udziwa malamulo usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, usanyenge, lemekeza atate wako ndi amako.

Mar 10:20 Ndipo iye adayankha nati kwa Iye, Mphunzitsi, zonsezi ndidazisunga kuyambira ndiri mwana.

Mar 10:21 Ndipo Yesu adamyang’ana, namkonda, nati kwa iye. Chinthu chimodzi chikusowa: pita gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m’mwamba; ndipo ukadze kuno,senza mtanda unditsate Ine.

Mar 10:22 Ndipo adakhumudwa ndi mawu awa, ndipo adachoka iye ali ndi chisoni; pakuti adali ndi chuma chambiri.

Mar 10:23 Ndipo Yesu adawunguzawunguza, nanena ndi wophunzira ake, Wokhala ndi chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu mobvutika kwambiri!

Mar 10:24 Ndipo wophunzirawo adazizwa ndithu ndi mawu ake. Koma Yesu adayankhanso nanena nawo, Ananu, nkobvuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu!

Mar 10:25 Ndi kwapafupi kuti ngamila ipyole pa diso la singano koposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu.

Mar 10:26 Ndipo anadabwa koposa muyeso, nanena kwa iwo wokha, ndipo angathe kupulumuka ndani?

Mar 10:27 Yesu adawayang’ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu: koma kutheka ndi Mulungu pakuti ndi Mulungu zinthu zonse zitheka.

Mar 10:28 Petro adayamba kunena naye, Onani, ife tidasiya zonse, ndipo tidakutsatani Inu.

Mar 10:29 Yesu adayankha nati, Indetu ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga wabwino.

Mar 10:30 Koma adzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale ndi alongo ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi ili mkudza, moyo wosatha.

Mar 10:31 Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala woyamba.

Mar 10:32 Ndipo iwo adali m’njira ali kupita kumka ku Yerusalemu; ndipo Yesu adalikuwatsogolera; ndipo iwo adazizwa; ndipo pamene adalikumtsata adachita mantha. Ndipo Iye adatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwawuza zinthu zimene zidzamchitikira Iye.

Mar 10:33 Nati, Tawonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi; ndipo iwo adzamuweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu.

Mar 10:34 Ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malobvu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo patsiku la chitatu adzawukanso.

Mar 10:35 Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chiri chonse tidzakhumba kwa Inu.

Mar 10:36 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakuchitireni inu chiyani?

Mar 10:37 Ndipo iwo adati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale m’modzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, muulemerero wanu.

Mar 10:38 Koma Yesu adati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndidzabatizidwa nawo Ine?

Mar 10:39 Ndipo adati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu adati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamweradi; ndipo ubatizo ndibatizidwa nawo Ine, mudzabatizidwadi nawo.

Mar 10:40 Koma kukhala ku dzanja langa lamanja, kapena kulamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kudzapatsidwa kwa iwo amene kudakonzedweratu.

Mar 10:41 Ndipo pamene khumiwo adamva, adayamba kusasangalalitsidwa ndi Yakobo ndi Yohane.

Mar 10:42 Ndipo Yesu adawayitana, nanena nawo, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye wa amitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu awo amachita ulamuliro pa iwo.

Mar 10:43 Koma mwa inu sikutero ayi; koma amene aliyense afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu;

Mar 10:44 Ndipo amene ali yense afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala mtumiki wa onse.

Mar 10:45 Pakuti ndithu, Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa ambiri.

Mar 10:46 Ndipo iwo adafika ku Yeriko; ndipo m’mene Iye adalikutuluka mu Yeriko, ndi wophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Tineyu, Bartimeyu wakhungu adakhala pansi m’mbali mwa njira kumapempha.

Mar 10:47 Ndipo pamene adamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, adayamba kufuwula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo.

Mar 10:48 Ndipo ambiri adamudzudzula kuti atonthole; koma makamaka adafuwulitsa kuti, Inu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.

Mar 10:49 Ndipo Yesu adayima nati, Mwitaneni. Ndipo adayitana munthu wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka akuyitana.

Mar 10:50 Ndipo iye adataya chofunda chake, nadzuka, nadza kwa Yesu.

Mar 10:51 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo munthu wakhunguyo adati kwa Iye, Ambuye, ndilandire kuwona kwanga.

Mar 10:52 Ndipo Yesu adati kwa iye, Pita; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo adapenyanso; namtsata Yesu panjira.



11

Mar 11:1 Ndipo pamene iwo adayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, adatuma awiri mwa wophunzira ake.

Mar 11:2 Ndipo adati kwa iwo, Pitani lowani m’mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu adakhalapo kale lonse; m’masuleni iye, ndipo mubwere naye.

Mar 11:3 Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Mukati, Ambuye akumfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.

Mar 11:4 Ndipo adachoka napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo pamphambano pamene njira ziwiri zakumana, nam`masula iye.

Mar 11:5 Ndipo ena woyima kumeneko adanena nawo, Muchita chiyani ndi kumasula mwana wa bulu?

Mar 11:6 Ndipo adati kwa iwo monga momwe adawalamulira Yesu: ndipo adawalola iwo apite naye.

Mar 11:7 Ndipo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, nayika zobvala zawo pa iye, ndipo Iye adakhala pamenepo.

Mar 11:8 Ndipo ambiri adayala zobvala zawo panjira; ndipo ena anadadula nthambi zamitengo naziyala njira.

Mar 11:9 Ndipo iwo amene adatsogola ndi iwo ankamtsata, adafuwula nanena, Hosana wodalitsika Iye amene akudza m`dzina la Ambuye.

Mar 11:10 Wodalitsika ukhale ufumu wa atate wathu Davide umene ukudza dzina la Ambuye: Hosana m` Mwambamwamba.

Mar 11:11 Ndipo Yesu adalowa mu Yerusalemu, ndipo nalowa m’kachisi; ndipo m’mene adawunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo adatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

Mar 11:12 Ndipo m’mawa mwake, atatuluka ku Betaniya, Iye adamva njala.

Mar 11:13 Ndipo adawona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye mokondwera, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m’mene adafikako adapeza palibe kanthu koma masamba wokha; pakuti sidali nyengo yake ya nkhuyu.

Mar 11:14 Ndipo Yesu adayankha nanena ndi uwo, munthu sadzadyanso zipatso zako kuyambira tsopano mpaka nthawi zonse. Ndipo wophunzira ake adamva.

Mar 11:15 Ndipo adafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Yesu adalowa m’kachisi, nayamba kutulutsa wogulitsa ndi wogula malonda m’kachisimo, nagubuduza magome a wosinthana ndalama, ndi mipando ya wogulitsa nkhunda.

Mar 11:16 Ndipo sadalole kuti munthu aliyense anyamule chotengera kupyola pakati pa kachisi.

Mar 11:17 Ndipo adaphunzitsa, nanena nawo, Sikudalembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwayiyesa phanga la mbava.

Mar 11:18 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adamva, nafunafuna njira yomuwonongera Iye; pakuti adamuwopa, chifukwa khamu lonse la anthu lidazizwa ndi chiphunzitso chake.

Mar 11:19 Ndipo pakufika madzulo adatuluka Iye mumzinda.

Mar 11:20 Ndipo m’mene adapitapo m’mawa mwake, adawona kuti mkuyu uja udawuma kuyambira kumizu.

Mar 11:21 Ndipo Petro adakumbukira, nanena naye, Amphunzitsi, onani, wafota mkuyu uja mudautemberera.

Mar 11:22 Ndipo Yesu adayankha nanena nawo, Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.

Mar 11:23 Indetu ndinena ndi inu, Kuti munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupilira kuti chimene achinena chidzachitidwa, adzakhala nazo zonse zimene azinena.

Mar 11:24 Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu ziri zonse mukazikhumba pamene mupemphera, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.

Mar 11:25 Ndipo pamene muyimilira ndi kupemphera, khululukirani ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.

Mar 11:26 Koma ngati simukhululukira Atate wanu ali m’mwamba sadzakukhululukiranso inu zochimwa zanu.

Mar 11:27 Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m’mene Iye adali kuyenda m’kachisi, adafika kwa Iye ansembe akulu, ndi alembi ndi akulu;

Mar 11:28 Ndipo adati kwa iye, Izi muzichita ndi ulamuliro wotani? Kapena adakupatsani ndani ulamuliro uwu wochita izi?

Mar 11:29 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Ndikufunsaninso inu funso limodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuwuzani ulamuliro umene ndichita nawo zinthu zimenezi.

Mar 11:30 Kodi ubatizo wa Yohane uchokera kumwamba kapena kwa anthu? Mundiyankhe Ine.

Mar 11:31 Ndipo adatsutsana mwa iwo wokha, nanena, Tikati, udachokera kumwamba; adzanena Iye, ndipo simudakhulupirira iye bwanji?

Mar 11:32 Koma tikati kwa anthu; iwo adawopa anthuwo; pakuti anthu onse adamuyesa Yohane m’neneri ndithu.

Mar 11:33 Ndipo iwo adayankha nati kwa Yesu, Sitingakuwuzeni. Ndipo Yesu adanena nawo, Inenso sindikuwuzani ulamuliro umene ndichita nawo zinthu zimenezi



12

Mar 12:1 Ndipo Iye adayamba kuyankhula nawo m’mafanizo. Munthu wina adalima munda wa mphesa, nawuzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa wolima munda, napita kudziko lakutali.

Mar 12:2 Ndipo m’nyengo yake adatuma mtumiki kwa wolimawo, kuti akalandireko kwa wolimawo zipatso za m’munda wamphesa.

Mar 12:3 Ndipo iwo adamgwira iye, nam’menya, namchotsa wopanda kanthu.

Mar 12:4 Ndipo adatumanso mtumiki wina kwa iwo; ndipo ameneyu adamponya miyala, namubvulaza m’mutu, namchotsa mwamanyazi wopanda kanthu.

Mar 12:5 Ndipo adatuma wina; iyeyu adamupha; ndi ena ambiri; ena adawamenya, ndi ena adawapha.

Mar 12:6 Adatsalira m’modzi, ndiye mwana wake wokondedwa; potsiriza adamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamchitira ulemu mwana wanga.

Mar 12:7 Koma wolima ajawo, adanena mwa iwo wokha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu.

Mar 12:8 Ndipo adamtenga namupha iye, namtaya kunja kwa munda.

Mar 12:9 Kodi pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzawononga wolimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.

Mar 12:10 Kodi simudawerenga ngakhale lembo ili; Mwala umene adawukana womanga nyumba, womwewu udayesedwa mutu wa pangodya.

Mar 12:11 Awa ndi machitidwe Ambuye, ndipo ali wozizwitsa m’maso mwathu?

Mar 12:12 Ndipo adayesa kuti amgwire Iye; koma adawopa anthu, pakuti adazindikira kuti Iye adakamba fanizo ili potsutsa iwo; ndipo adamsiya Iye, nachoka.

Mar 12:13 Ndipo adatuma kwa Iye ena wa Afarisi ndi a Herode, kuti akamkole Iye m’kuyankhula kwake.

Mar 12:14 Ndipo pamene adafika, adanena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli wowona, ndipo simusamala munthu pakuti simuyang’ana nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu mowona: nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena ayi?

Mar 12:15 Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye podziwa chinyengo chawo, adati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni khobiri latheka, kuti ndiliwone.

Mar 12:16 Ndipo adalitenga. Ndipo adati kwa iwo, Chithunzi ichi, ndi chilembo chake ziri za yani? Ndipo adati kwa Iye, za Kaisara.

Mar 12:17 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo adazizwa naye.

Mar 12:18 Ndipo anadza kwa Iye Asaduki amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa; ndipo adamfunsa Iye, nanena

Mar 12:19 Mphunzitsi, Mose adatilembera ife kuti, Akafa m`bale wake wa munthu, nasiya mkazi, wosasiyapo mwana, m`bale wake atenge mkazi wake namuukitsire mbale wakeyo mbewu.

Mar 12:20 Adalipo abale asanu ndi awiri; woyamba adakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbewu;

Mar 12:21 Ndipo wachiwiri adamkwatira iye nafa, wosasiya mbewu; ndipo wachitatunso adatero momwemo;

Mar 12:22 Ndipo asanu ndi awiriwo adakhala naye ndipo sadasiya mbewu. Potsiriza pake pa onse mkaziyo adafanso.

Mar 12:23 Chotero pakuwuka kwa akufa adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wawo.

Mar 12:24 Ndipo Yesu poyankha adati, simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu?

Mar 12:25 Pakuti pamene adzawuka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa, koma akhala ngati angelo akumwamba.

Mar 12:26 Koma za akufa, kuti adzaukitsidwa simudawerenga m’buku la Mose kodi, momwe adalikuthengo, kuti Mulungu adati kwa iye, nanena, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Mulungu wa Yakobo?

Mar 12:27 Iye sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu.

Mar 12:28 Ndipo anadza m’modzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo podziwa kuti adawayankha bwino, adamfunsa Iye, Lamulo loyamba la onse ndi liti?

Mar 12:29 Ndipo Yesu adamuyankha iye, Kuti lamulo loyamba la onse ndi ili, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu ndiye m’modzi.

Mar 12:30 Ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse: Ili ndi lamulo loyamba.

Mar 12:31 Ndipo lachiwiri ndi ili, uzikonda mzako monga uzikonda iwe mwini. Palibe lamulo lina loposa awa.

Mar 12:32 Ndipo mlembiyo adati kwa Iye, Chabwino, mphunzitsi, mwanena zowona kuti ndi Mulungu m’modzi; ndipo palibe wina, koma Iye.

Mar 12:33 Ndipo kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mzako monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.

Mar 12:34 Ndipo Yesu pakuwona adayankha ndi nzeru adati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu adalimbanso mtima kumfunsa Iye ndithu.

Mar 12:35 Ndipo Yesu adayankha nati, pamene adali kuphunzitsa m’kachisi, Bwanji alembi akunena kuti Khristu ndiye mwana wa Davide?

Mar 12:36 Pakuti Davide mwini yekha adati mwa Mzimu Woyera, Ambuye adati kwa Ambuye wanga, khala ku dzanja langa lamanja, kufikira nditawayika adani ako popondapo mapazi ako.

Mar 12:37 Chomwecho Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo adakondwa kumva Iye.

Mar 12:38 Ndipo Iye adati kwa iwo m’chiphunzitso chake, Chenjerani ndi alembi, akonda kubvala miyinjiro nakonda kulandira ulemu m’misika.

Mar 12:39 Nakhala nayo mipando yaulemu m’sunagoge, ndi malo a ulemu pamaphwando;

Mar 12:40 Amenewo alusira nyumba za akazi a masiye, napemphera monyenga mawu ambiri, amenewa adzalandira kulanga koposa.

Mar 12:41 Ndipo Yesu adakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya momwe anthu adali kuponyera ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri adaponyamo zambiri.

Mar 12:42 Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye adaponyamo tindalama tiwiri tating’ono topanga khobiri limodzi.

Mar 12:43 Ndipo adayitana wophunzira ake, nati kwaiwo, ndithu ndinena ndi inu, mkazi wamasiye amene waumphawi adaponya zambiri koposa onse woponya mosungiramo:

Mar 12:44 Pakuti onse adaponyamo mwa zochuluka zawo; koma iye adaponya mwa kusowa kwake zonse adali nazo, inde ndi za moyo wake wonse.



13

Mar 13:1 Ndipo pamene Iye adalikutuluka m’kachisi m’modzi wa wophunzira ake adanena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.

Mar 13:2 Ndipo Yesu poyankha adati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa umzake, umene sudzagwetsedwa pansi.

Mar 13:3 Ndipo pamene Iye adakhala pa phiri la Azitona, popenyana ndi kachisi adamfunsa Iye mseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane ndi Andreya kuti,

Mar 13:4 Tiwuzeni zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake pamene zinthu izi zonse zidzakwaniritsidwa?

Mar 13:5 Ndipo Yesu powayankha iwo adanena nawo, Chenjerani kuti munthu asakusocheretseni:

Mar 13:6 Pakuti ambiri adzafika m’dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu; nadzasocheretsa ambiri.

Mar 13:7 Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichidafike chimaliziro.

Mar 13:8 Pakuti mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu wina umzake; padzakhala zibvomerezi m’malo osiyanasiyana; padzakhala njala ndi mabvuto; Izi ndi zoyambira za zowawa.

Mar 13:9 Koma inu mudziyang’anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m’masunagoge mwao; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzayimilira chifukwa cha Ine, kukhala umboni kwa iwo.

Mar 13:10 Ndipo Uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.

Mar 13:11 Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa chimene mudzayankhula; kapena kulingalira koma chimene chidzapatsidwa kwa inu ora lomwelo, muchiyankhule; pakuti woyankhula si inu, koma Mzimu Woyera.

Mar 13:12 Ndipo m’bale adzapereka m`bale wake kuti aphedwe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzawukirana ndi akuwabala nadzawaphetsa.

Mar 13:13 Ndipo mudzadedwa ndi anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wopilira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.

Mar 13:14 Ndipo pamene mudzawona chonyansa cha kupululutsa chimene chidayankhulidwa ndi Danieli m`neneri (iye amene awerenga azindikire ) chitayima pomwe sichiyenera kuyima pamenepo iwo ali mu Yudeya athawire ku mapiri:

Mar 13:15 Ndipo iye amene ali pamwamba pa denga asatsike, kapena asalowe kukatulutsa kanthu m’nyumba mwake;

Mar 13:16 Ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake.

Mar 13:17 Koma tsoka kwa iwo wokhala ndi mwana ndi iwo akuyamwitsa m`masiku amenewo!

Mar 13:18 Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzakhale m’nyengo yozizira.

Mar 13:19 Pakuti masiku amenewo padzakhala chisautso, chonga sichidakhalepo chimzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu adachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso nthawi zonse.

Mar 13:20 Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu m’modzi yense; koma chifukwa cha wosankhidwa amene adawasankha, adafupikitsa masikuwo.

Mar 13:21 Ndipo pamenepo ngati munthu wina anena kwa inu, Onani Khristu ali pano; kapena Onani, ali uko; musakhulupirire;

Mar 13:22 Pakuti adzawuka Akhristu wonyenga ndi aneneri wonyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati n’kutheka, wosankhidwa omwe.

Mar 13:23 Koma inu chenjerani; Onani, ndakuwuziranitu zinthu zonse, zisadafike.

Mar 13:24 Koma m’masiku amenewo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa ndi mwezi sudzapatsa kuwunika kwake.

Mar 13:25 Ndipo nyenyezi zidzagwa kuchokera m’mwamba ndi mphamvu ziri m’mwamba zidzagwedezeka.

Mar 13:26 Ndipo pamenepo adzawona Mwana wa Munthu ali mkudza m’mitambo ndi mphamvu yayikulu, ndi ulemerero.

Mar 13:27 Ndipo pamenepo adzatuma angelo ake, nadzasonkhanitsa wosankhidwa ake wochokera ku mphepo zinayi, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.

Mar 13:28 Tsopano phunzirani fanizo la mtengo wa mkuyu; pamene pafika kuti nthambi yake yanthete, ndipo akaphuka masamba ake, muzindikira kuti layandikira dzinja.

Mar 13:29 Chomwecho inunso, pamene mudzawona zinthu izi zili kuchitika, zindikirani kuti ali pafupi, inde pakhomo.

Mar 13:30 Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika.

Mar 13:31 Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mawu anga sadzapita.

Mar 13:32 Koma za tsikulo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo m’mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye adziwa.

Mar 13:33 Chenjerani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake.

Mar 13:34 Pakuti Mwana wa Munthu ali monga ngati munthu wa pa ulendo, amene adachoka kunyumba kwake, nawapatsa atumiki ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamulira wapakhomo adikire.

Mar 13:35 Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa inu nthawi yake yobwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;

Mar 13:36 Kuti angabwere modzidzimutsa nadzakupezani muli mtulo.

Mar 13:37 Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.



14

Mar 14:1 Ndipo popita masiku awiri kudali phwando la Paskha ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo ansembe akulu ndi alembi adafunafuna momwe angamgwirirre momchenjerera, ndi kumupha;

Mar 14:2 Koma adati, paphwando ayi, kuti pangakhale phokoso chipolowe cha anthu.

Mar 14:3 Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate, m’mene adasayama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabasitala ya mafuta wonunkhira bwino a nardo weni weni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.

Mar 14:4 Koma adakhalako ena adabvutika mtima mwa iwo wokha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji?

Mar 14:5 Pakuti mafuta amene akadagulitsa makobiri oposa mazana atatu ndi mphambu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo adanyinyirika motsutsana ndi iye.

Mar 14:6 Ndipo Yesu adati, Mulekeni, mumbvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino.

Mar 14:7 Pakuti muli nawo aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo pali ponse pamene mufuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.

Mar 14:8 Iye wachita chimene wakhoza; adandidzozeratu thupi langa ku kuyikidwa m’manda.

Mar 14:9 Indetu ndinena ndi inu; paliponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino ku dziko lonse lapansi, ichinso chimene adachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.

Mar 14:10 Ndipo Yudasi Isikariyote, ndiye m’modzi wa khumi ndi awiriwo, adachoka napita kwa ansembe akulu,kuti akampereke Iye kwa iwo.

Mar 14:11 Ndipo pamene iwo adamva, adasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye adafunafuna momwe angamperekere Iye bwino.

Mar 14:12 Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paskha, wophunzira ake adanena naye, Mufuna tipite kuti, tikakonze mukadyereko Paskha?

Mar 14:13 Ndipo adatuma awiri awophunzira ake, nanena nawo, Lowani mu mzinda, ndipo mudzakomana ndi munthu wosenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye;

Mar 14:14 Ndipo kumene adzalowako iye, munene naye mwini nyumba wabwino, Mphunzitsi anena, chiri kuti chipinda cha alendo m’menemo ndidzadyera Paskha ndi wophunzira anga?

Mar 14:15 Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda, chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m’menemo mutikonzere ife.

Mar 14:16 Ndipo wophunzira adatuluka, nafika mu mzinda, napeza monga adati kwa iwo; ndipo adakonza Paskha.

Mar 14:17 Ndipo madzulo adafika, Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

Mar 14:18 Ndipo pamene iwo adakhala pansi ndi kudya, Yesu adati, Indetu ndinena ndi inu, m’modzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.

Mar 14:19 Ndipo iwo adayamba kukhala ndi chisoni, ndi kunena naye m’modzi m’modzi, kuti Ndine kodi? Ndipo wina adati kodi ndine?

Mar 14:20 Ndipo adati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo,ndiye wosunsa pamodzi ndi ine m’bale.

Mar 14:21 Pakuti Mwana wa munthu amukadi; monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa munthu! Kukadakhala kwabwino kwa munthu ameneyo akadakhala kuti sadabadwe.

Mar 14:22 Ndipo pamene analikudya, Yesu adatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, adanyema, napereka kwa iwo, nati: Tengani, idyani, ili ndi thupi langa.

Mar 14:23 Ndipo adatenga chikho, ndipo pamene adayamika, adapereka kwa iwo, ndipo iwo onse adamweramo.

Mar 14:24 Ndipo Iye adati kwa iwo, Uwu ndi mwazi wanga wa pangano latsopano, wokhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri.

Mar 14:25 Indetu ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.

Mar 14:26 Ndipo atayimba nyimbo, adatuluka, napita ku phiri la Azitona.

Mar 14:27 Ndipo Yesu adati kwa iwo, mudzakhumudwa nonsenu usiku uno chifukwa cha Ine; pakuti kwalembedwa; Ndidzakantha m`busa, ndi nkhosa zidzabalalika.

Mar 14:28 Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.

Mar 14:29 Koma Petro adati kwa Iye, Angakhale adzakhumudwa onse komatu ine ayi.

Mar 14:30 Ndipo Yesu adati kwa iye, Indetu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asadalire kawiri udzandikana Ine katatu.

Mar 14:31 Koma iye adayankhula molimbitsa mawu kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo adatero.

Mar 14:32 Ndipo iwo anadza ku malo dzina lake Getsemane; ndipo adanena kwa wophunzira ake, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera.

Mar 14:33 Ndipo adatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kulemedwa mtima ndithu.

Mar 14:34 Ndipo adati kwa iwo, Moyo wanga uli wa chisoni chambiri kufikira imfa. Bakhalani pano, nimudikire.

Mar 14:35 Ndipo Iye anapita m’tsogolo pang’ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati n’kutheka nthawi imeneyi indipitirire Ine.

Mar 14:36 Ndipo Iye adati, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu, mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.

Mar 14:37 Ndipo anadza nawapeza iwo ali m’tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Ulibe mphamvu yakudikira ola limodzi kodi?

Mar 14:38 Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m’kuyesedwa; mzimutu ali wofuna, koma thupi liri lolefuka.

Mar 14:39 Ndipo adachokanso, napemphera, nanena mawu womwewo.

Mar 14:40 Ndipo anadzanso nawapeza ali m’tulo, pakuti maso awo adalemeradi; ndipo sadadziwe chomuyankha Iye.

Mar 14:41 Ndipo anadza kachitatu, nanena nawo, Gonani tsopano; nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa munthu aperekedwa m’manja wa anthu wochimwa.

Mar 14:42 Ukani, tidzipita; onani wondiperekayo ali pafupi.

Mar 14:43 Ndipo pomwepo Iye ali chiyankhulire, anadza Yudase, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nawo malupanga ndi zibonga, wochokera kwa ansembe akulu ndi alembi ndi akulu.

Mar 14:44 Ndipo wompereka Iye adawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsopsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire.

Mar 14:45 Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena Mphunzitsi, mphunzitsi: nampsopsonetsa Iye.

Mar 14:46 Ndipo adamthira manja, namgwira namtenga Iye.

Mar 14:47 Ndipo m’modzi wina wa iwo woyimilira pamenepo, adasolola lupanga lake, nakantha mtumiki wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake.

Mar 14:48 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka ndi malupanga ndi zibonga kundigwira Ine monga bava?

Mar 14:49 Masiku onse ndidali nanu m’kachisi ndiri kuphunzitsa, ndipo simudandigwire Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwaniritsidwe.

Mar 14:50 Ndipo iwo onse adamsiya Iye, nathawa.

Mar 14:51 Ndipo m’nyamata wina adamtsata Iye, atafundira pathupi bafuta yekha kubisa umaliseche wake; ndipo anyamatawo adamuyimitsa Iye;

Mar 14:52 Ndipo iye adasiya bafutayo, nathawa wamaliseche.

Mar 14:53 Ndipo adamka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo adasonkhana kwa iye ansembe akulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi.

Mar 14:54 Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m’bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo adali kukhala pansi pamodzi ndi atumiki, ndi kuwotha moto.

Mar 14:55 Ndipo ansembe akulu ndi akulu a milandu onse adafunafuna umboni womutsutsa nawo Yesu kuti amuphe Iye; koma sadaupeze.

Mar 14:56 Pakuti ambiri adamchitira umboni wonama, ndipo umboni wawo sudalingane.

Mar 14:57 Ndipo adanyamukapo ena, namchitira umboni wonama, nanena kuti,

Mar 14:58 Ife tidamumva Iye alikunena kuti Ine ndidzawononga kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosamangidwa ndi manja.

Mar 14:59 Ndipo ngakhale momwemo umboni wawo sudafanane.

Mar 14:60 Ndipo mkulu wa ansembe adanyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira umboni mokutsutsa Iwe.

Mar 14:61 Koma adakhala chete, osayankha kanthu. Mkulu wa ansembe adamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Khristu, Mwana wake wa Wodalitsika?

Mar 14:62 Ndipo Yesu adati, Ndine amene; ndipo mudzawona Mwana wa munthu alikukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo yakumwamba.

Mar 14:63 Ndipo mkulu wa ansembe adang’amba malaya ake, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?

Mar 14:64 Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse adamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.

Mar 14:65 Ndipo ena adayamba kumthira malobvu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kum’bwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo atumikiwo adampanda Iye khofi ndi manja awo.

Mar 14:66 Ndipo pamene Petro adali pansi m’bwalo, anadzapo m’modzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;

Mar 14:67 Ndipo pamene adamuwona Petro alikuwotha moto, namuyang’ana iye, adanena, Iwenso udali naye Yesu ku Mnazarete.

Mar 14:68 Koma adakana, nanena, Sindimdziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo adatuluka kupita kuchipata; ndipo tambala adalira.

Mar 14:69 Ndipo mdzakaziyo adamuwonanso iye, nayambanso kunena ndi iwo akuyimilirapo, Uyu ndi m`modzi wa iwo.

Mar 14:70 Ndipo adakananso. Ndipo patapita mphindi, akuyimilirapo adanenanso ndi Petro, zowonadi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya. Pakuti ndi mayankhulidwe ako agwirizana ndi iwo.

Mar 14:71 Koma iye adayamba kutemberera, ndi kulumbira, ndikunena, Sindidziwa za munthuyu amene inu muyankhula za Iye.

Mar 14:72 Ndipo tambala adalira kachiwiri, Ndipo Petro adakumbukira umo Yesu adati kwa iye, kuti, Tambala asadalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo poganizira ichi adalira misozi.



15

Mar 15:1 Ndipo pomwepo m`mawa adakhala upo ansembe akulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.

Mar 15:2 Ndipo Pilato adamfunsa Iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo poyankha adati kwa iye, Mwatero ndinu.

Mar 15:3 Ndipo ansembe akulu adamnenera Iye zinthu zambiri koma sadayakhe kanthu.

Mar 15:4 Ndipo Pilato adamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Tawona, akuchitira umboni Iwe mokutsutsa zinthu zambiri zotere.

Mar 15:5 Koma Yesu sadayankhenso kanthu; kotero Pilato adazizwa.

Mar 15:6 Tsopano amkawamasulira paphwando wa mndende m’modzi, amene iwo adamfuna.

Mar 15:7 Ndipo adalipo wina dzina lake Baraba, womangidwa pamodzi ndi ena wopanduka, amene adapha munthu mumpanduko.

Mar 15:8 Ndipo khamu lidafuwuula niliyamba kupempha Iye kuti achite monga adali kuwachitira iwo.

Mar 15:9 Koma Pilato adawayankha iwo, nanena Kodi mufuna ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?

Mar 15:10 Pakuti adazindikira kuti ansembe akulu adampereka Iye mwa njiru.

Mar 15:11 Koma ansembe akulu adasonkhezera anthu, kuti makamaka awamasulire Baraba.

Mar 15:12 Ndipo Pilato adayankha natinso kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula Mfumu ya Ayuda?

Mar 15:13 Ndipo adafuwulanso, Mpachikeni Iye.

Mar 15:14 Pamenepo Pilato adanena nawo, Chifukwa chiyani, Iye adachita choyipa chotani? Koma iwo adafuwulitsatu, Mpachikeni Iyeyo.

Mar 15:15 Ndipo Pilato pofuna kuwakhazikitsa mtima anthuwo, adawamasulira Baraba, nampereka Yesu, atamkwapula kuti akapachikidwe.

Mar 15:16 Ndipo asilikali adachoka naye nalowa m’bwalo, ndilo Pretoriyo; nasonkhanitsa gulu lawo lonse.

Mar 15:17 Ndipo adambveka Iye chibakuwa, naluka korona wa minga, nambveka pa mutu pake.

Mar 15:18 Ndipo adayamba kumulonjera Iye, nati, Tikuwoneni, Mfumu ya Ayuda!

Mar 15:19 Ndipo adampanda Iye pamutu pake ndi bango, namthira malobvu, nampindira mawondo, namlambira.

Mar 15:20 Ndipo atatha kum’nyoza adambvula chibakuwacho nam’bveka Iye zobvala zake. Ndipo adatuluka naye kuti akampachike Iye.

Mar 15:21 Ndipo adamkangamiza wina, Simoni wa ku Kerene, amene amapitirirapo kuchokera kumudzi, atate wawo wa Alesandere ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake.

Mar 15:22 Ndipo adamtenga kupita naye ku malo Gologota, ndiwo wosandulika, Malo achigaza.

Mar 15:23 Ndipo adampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sadamlandire

Mar 15:24 Ndipo pamene adampachika Iye, adagawana zobvala zake, ndi kuchita mayere pa izo, kuti adziwe yense adzatenga chiyani.

Mar 15:25 Ndipo lidali ora lachitatu ndipo iwo adampachika Iye.

Mar 15:26 Ndipo lembo la mlandu wake lidalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.

Mar 15:27 Ndipo adampachika pamodzi ndi achifwamba awiri; m’modzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamazere.

Mar 15:28 Ndipo malemba adakwaniritsidwa, amene adati, Ndipo adawerengedwa pamodzi ndi omphwanya malamulo.

Mar 15:29 Ndipo iwo wodutsapo adamchitira Iye mwano, napukusa mitu yawo nanena, Ha! Iwe wopasula kachisi ndi kum’manga masiku atatu,

Mar 15:30 Udzipulumutse wekha, nutsike pamtandapo.

Mar 15:31 Moteronso ansembe akulu adamtoza mwa iwo wokha pamodzi ndi alembi’nanena, Adapulumutsa ena; Iye yekha sakhoza kudzipulumutsa.

Mar 15:32 Atsike tsopano pamtanda, Khristu Mfumu ya Israyeli, kuti tiwone ndipo tikhulupirire. Ndipo iwo wopachikidwa naye adamlalatira.

Mar 15:33 Ndipo pofika ola la chisanu ndi limodzi, padali mdima padziko lonse, kufikira ola la chisanu ndi chinayi.

Mar 15:34 Ndipo pa ola la chisanu ndi chinayi Yesu adafuwula ndi mawu wokweza, Eloi, Eloi, lamasabakitani? Ndiko kutathauza, Mulungu wanga Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?

Mar 15:35 Ndipo ena woyimilirapo, pakumva adanena, Taonani akuyitana Eliya.

Mar 15:36 Ndipo adathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiyika pa bango, nampatsa kuti amwe, nanena, Mulekeni; tiwone ngati Eliya adza kudzamtsitsa.

Mar 15:37 Ndipo Yesu adafuula mokwezetsa mawu, napereka Mzimu wake.

Mar 15:38 Ndipo chinsalu chotchinga cha m’kachisi chidang’ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi.

Mar 15:39 Ndipo pamene Kenturiyo, woyimilirapo popenyana ndi Iye, adawona kuti adapereka Mzimu kotero, adati, Zowonadi, munthu uyu adali Mwana wa Mulungu.

Mar 15:40 Ndipo adaliponso pamenepo akazi akuyang’anira patali; mwa iwo padali Mariya wa Magadala ndi Mariya amake wa Yakobo wam’ng’ono ndi wa Yose, ndi Salome.

Mar 15:41 (Amene adamtsata Iye, pamene adali mu Galileya, namtumikira Iye;) ndi akazi ena ambiri, amene adakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.

Mar 15:42 Ndipo tsono atafika madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa sabata.

Mar 15:43 Adadzapo Yosefe wa ku Arimateya, mkulu wa milandu wotchuka, amene yekha adali kuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu.

Mar 15:44 Ndipo Pilato adazizwa ngati adamwaliradi; nayitana Kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.

Mar 15:45 Ndipo pamene adachidziwa ndi Kenturiyo, adampatsa Yosefe mtembowo.

Mar 15:46 Ndipo adagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m’bafutamo, namuyika m’manda wosemedwa m’thanthwe; nakunkhunizira mwala pa khomo la manda.

Mar 15:47 Ndipo Mariya wa Magadala ndi Mariya amake a Yosefe adapenya pomwe adayikidwapo





16

Mar 16:1 Ndipo litapita sabata, Mariya wa Magadala, ndi Mariya amake wa Yakobo, ndi Salome, adagula zonunkhira, kuti akadze kumdzodza Iye.

Mar 16:2 Ndipo anadza kumanda m`mawa tsiku loyamba la Sabata, litatuluka dzuwa.

Mar 16:3 Ndipo adalikunena mwa wokha, Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pakhomo la manda?

Mar 16:4 Ndipo pamene adakweza maso adawona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti udali waukulu ndithu.

Mar 16:5 Ndipo pamene adalowa m’manda, adawona m’nyamata atakhala kumbali ya ku dzanja lamanja, wobvala mwinjiro woyera; ndipo iwo Adachita mantha.

Mar 16:6 Ndipo iye adanena nawo, musaope: Muli kufuna Yesu Mnazarete amene adapachikidwa; adawuka; Sali pano; tawonani, mbuto m’mene adayikamo Iye.

Mar 16:7 Koma mukani uzani wophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolereni inu ku Galileya; kumeneko mudzamuwona Iye, monga adanena ndi inu.

Mar 16:8 Ndipo adatuluka mwamsanga, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndipo anadabwa; ndipo sadawuze kanthu munthu aliyense; pakuti adachita mantha.

Mar 16:9 Ndipo pamene Yesu adawuka mamawa tsiku loyamba la sabata, adayamba kuwonekera kwa Mariya wa Magadala, amene adamtulutsa ziwanda zisanu ndi ziwiri.

Mar 16:10 Ndipo Iye adapita kukawauza iwo amene amakhala naye, ali ndi chisoni ndipo kungolira.

Mar 16:11 Ndipo iwowo, pamene adamva kuti ali ndi moyo, ndi kuti adawonekera kwa iye, sadakhulupirire.

Mar 16:12 Ndipo zitatha izi; adawonekeranso iye m’mawonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali kupita kumudzi.

Mar 16:13 Ndipo iwowa adachoka nawauza wotsala; koma palibe amene adakhulupirira iwo.

Mar 16:14 Ndipo chitatha icho adawonekera kwa khumi ndi m;modzi, alikuseyama pachakudya; ndipo adawadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndi kuwumitsa mtima, popeza sadakhulupilira iwo amene adamuwona, atawuka Iye.

Mar 16:15 Ndipo adanena nawo, Mukani ku dziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa wolengedwa onse.

Mar 16:16 Amene akhulupilira nabatizidwa, adzapulumuka; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.

Mar 16:17 Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupilira; m’dzina langa adzatulutsa ziwanda, adzayankhula ndi malilime atsopano;

Mar 16:18 Adzatola njoka ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzayika manja awo pa wodwala, ndipo adzachira.

Mar 16:19 Pamenepo Ambuye, atatha kuyankhula nawo, adalandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja la manja la Mulungu.

Mar 16:20 Ndipo iwowa adatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye adagwira ntchito nawo pamodzi, natsimikiza mawu ndi zizindikiro zakutsatapo. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE