Luke


1

Luk 1:1 Popeza ambiri adayesa kulongosola nkhani ya zinthu zokhulupiridwa zimene zidachitika pakati pa ife,

Luk 1:2 Monga adazipereka kwa ife iwo amene kuyambira pachiyambi adakhala mboni yowona ndi maso ndi atumiki a mawu;

Luk 1:3 Kuyambira pachiyambi, ndidayesa nkokoma kwa inenso, amene ndidalondalonda mosamalitsa, zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe.

Luk 1:4 Kuti iwe udziwitse zowona zake za zinthu zimene iwe udaphunzitsidwa. Aneneratu za kubadwa kwa Yohane Mbatizi

Luk 1:5 Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kudali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana akazi a fuko la Aroni, dzina lake adali Elizabeti.

Luk 1:6 Ndipo onse awiri adali wolungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse a zoyikika za Ambuye wopanda banga.

Luk 1:7 Ndipo adalibe mwana, popeza Elizabeti adali wouma, ndipo onse awiri adali wokalamba.

Luk 1:8 Ndipo padali pakuchita iye ntchito yopereka nsembe m’dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu.

Luk 1:9 Monga mwa machitidwe a kupereka nsembe adamgwera mayere akufukiza zonunkhira polowa iye m’kachisi wa Ambuye.

Luk 1:10 Ndipo khamu lonse la anthu lidali kupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.

Luk 1:11 Ndipo adamuwonekera iye m’ngelo wa Ambuye, nayimilira kudzanja la manja la guwa la nsembe la zonunkhira.

Luk 1:12 Ndipo Zakariya anadabwa pamene adamuwona,ndipo mantha adamgwira.

Luk 1:13 Koma m’ngelo adati kwa iye, Usawope Zakariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.

Luk 1:14 Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake.

Luk 1:15 Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena chakumwa cha ukali; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asadabadwe.

Luk 1:16 Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israyeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo.

Luk 1:17 Ndipo adzamtsogolera iye, ndi Mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana awo, ndi wosamvera kuti atsate nzeru ya wolungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu wokonzeka.

Luk 1:18 Ndipo Zakariya adati kwa m’ngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka.

Luk 1:19 Ndipo m’ngelo poyankha adati kwa iye, Ine ndine Gabrieli; amene amayimilira pa maso pa Mulungu; ndipo ndidatumidwa kwa iwe kudzayankhula nawe, ndikuwuza iwe uthenga uwu wabwino.

Luk 1:20 Ndipo tawona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kuyankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi; popeza kuti sudakhulupirire mawu anga, amene adzakwaniritsidwa pa nyengo yake.

Luk 1:21 Ndipo anthu analikulindira Zakariya, nazizwa ndi kuchedwa kwake m’kachisimo.

Luk 1:22 Ndipo pamene iye adatulukamo, sadathe kuyankhula nawo; ndipo adazindikira kuti iye adawona masomphenya m’kachisimo. Ndipo iye adalimkukodola iwo, nakhalabe wosayankhula.

Luk 1:23 Ndipo kudali, pamene masiku a utumiki wake adamalizidwa, adapita kunyumba kwake.

Luk 1:24 Ndipo atatha masiku awa, Elizabeti mkazi wake adayima; nadzibisa miyezi isanu, nati,

Luk 1:25 Ambuye wandichitira chotero m’masiku omwe Iye adandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.

Luk 1:26 Ndipo mwezi wa chisanu ndi umodzim’ngelo Gabrieli adatumidwa ndi Mulungu kupita ku mzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete.

Luk 1:27 Kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Mariya.

Luk 1:28 Ndipo m’ngelo polowa adati kwa iye, Tikuwoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe. Wodala iwe mwa amayi.

Luk 1:29 Ndipo pamene adamuwona iye, adanthunthumira ndi mawu awa, nasinkhasinkha kuyankhula uku nkutani.

Luk 1:30 Ndipo m’ngelo adati kwa iye, Usawope Mariya, pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu.

Luk 1:31 Ndipo tawona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wa mwamuna, nudzamutcha dzina lake YESU

Luk 1:32 Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulu-kulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake.

Luk 1:33 Ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.

Luk 1:34 Pamenepo Mariya adati kwa m’ngelo, ichi chidzachitika bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna.

Luk 1:35 Ndipo m’ngelo adayankhula, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulu-kulu idzakuphimba iwe; chifukwa chakenso choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.

Luk 1:36 Ndipo tawona, Elizabeti msuwani wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi umodzi wa iye amene adanenedwa wouma.

Luk 1:37 Chifukwa ndi Mulungu palibe zinthu zidzakhala zosatheka.

Luk 1:38 Ndipo Mariya adati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mawu anu. Ndipo m’ngelo adachoka kwa iye.

Luk 1:39 Ndipo Mariya adanyamuka masiku amenewo, napita ndi changu ku dziko la mapiri ku mzinda wa Yuda.

Luk 1:40 Ndipo adalowa m’nyumba ya Zakariya, nayankhula kwa Elizabeti.

Luk 1:41 Ndipo padali pamene Elizabeti adamva kuyankhula kwake kwa Mariya, mwana wosabadwayo, adatsalima m’mimba mwake; ndipo Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera.

Luk 1:42 Ndipo adayankhula mawu mokweza ndi mfuwu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako.

Luk 1:43 Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga?

Luk 1:44 Pakuti wona, pamene mawu akuyankhula kwako adalowa m’makutu anga, mwana adatsalima ndi msangalalo m’mimba mwanga.

Luk 1:45 Ndipo wodala ali iye amene adakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye adayankhula naye.

Luk 1:46 Ndipo Mariya adati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye.

Luk 1:47 Ndipo Mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

Luk 1:48 Chifukwa Iye adayang’anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti tawonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala.

Luk 1:49 Chifukwa Iye Wamphamvuyo adandichitira ine zazikulu; ndipo dzina lake liri loyera.

Luk 1:50 Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwo mibadwo pa iwo amene amuwopa Iye.

Luk 1:51 Iye adachita za mphamvu ndi mkono wake; Iye anabalalitsa wodzitama ndi malingaliro a mtima wawo.

Luk 1:52 Iye adatsitsa mafumu pa mipando yawo ya chifumu,ndipo adakweza aumphawi.

Luk 1:53 Adawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma adawachotsa wopanda kanthu.

Luk 1:54 Adathangatira Israyeli mtumiki wake, kuti akakumbukire chifundo chake;

Luk 1:55 Monga adayankhula kwa atate athu, kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake ku nthawi yonse.

Luk 1:56 Ndipo Mariya adakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabwereranso kunyumba kwake.

Luk 1:57 Tsopano idakwanira nthawi ya Elizabeti ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna.

Luk 1:58 Ndipo anansi ake ndi abale ake adamva kuti Ambuye adakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.

Luk 1:59 Ndipo padali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo adadza kudzadula kamwanako; ndipo amkati amutche dzina la atate wake Zakariya.

Luk 1:60 Ndipo amake adayankha, kuti, Ayi; koma adzatchedwa Yohane.

Luk 1:61 Ndipo iwo adati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili.

Luk 1:62 Ndipo adakodola atate wake, kuti afuna amutche dzina liti?

Luk 1:63 Ndipo iye adafunsa cholemberapo, nalemba kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo adazizwa onse.

Luk 1:64 Ndipo pomwepo padatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake lidamasuka, ndipo iye adayankhula, nalemekeza Mulungu.

Luk 1:65 Ndipo padagwa mantha pa iwo onse wokhala moyandikana nawo; ndipo adayankhulayankhula nkhani izi zonse m’dziko lonse la mapiri a Yudeya.

Luk 1:66 Ndipo onse amene adazimva adazisunga m’mitima mwawo, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye lidakhala pamodzi ndi iye.

Luk 1:67 Ndipo atate wake Zakariya adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,

Luk 1:68 Wodalitsika Ambuye, Mulungu wa Israyeli; chifukwa Iye adayang’ana, nachitira anthu ake chiwombolo.

Luk 1:69 Ndipo Iye adatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake.

Luk 1:70 Monga Iye adayankhula ndi m’kamwa mwa aneneri ake woyera mtima, akale lomwe;

Luk 1:71 Kuti tipulumuke kwa adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife;

Luk 1:72 Ndikuchitira atate wathu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika;

Luk 1:73 Chilumbiro chimene Iye adachilumbira kwa Abrahamu atate wathu.

Luk 1:74 Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa ku dzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, wopand

Luk 1:75 Mchiyero ndi m’chilungamo pamaso pake, masiku onse a moyo wathu.

Luk 1:76 Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa m’neneri wa Wamkulukulu. Pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake;

Luk 1:77 Kuwapatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso, ndi makhululukidwe amachimo awo.

Luk 1:78 Chifukwa cha mtima wa chifundo wa Mulungu wathu. M’menemo m’banda kucha wa Kumwamba udzatichezera ife;

Luk 1:79 Kuwalitsira iwo wokhala mu mdima ndi mu mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere.

Luk 1:80 Ndipo mwanayo adakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye adali m’zipululu, kufikira masiku akudziwonetsa yekha kwa Israyeli.



2

Luk 2:1 Ndipo kudali masiku aja, kuti lamulo lidatuluka kwa Kayisala Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe.

Luk 2:2 Ndiko kulembera koyamba pokhala Kureniyo kazembe wa Suriya.

Luk 2:3 Ndipo onse adapita kukalembedwa, munthu aliyense ku mzinda wake.

Luk 2:4 Ndipo Yosefe yemwe adakwera kuchokera ku Galileya, ku mzinda wa Nazarete, kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, (chifukwa iye adali wa banja ndi fuko lake la Davide:)

Luk 2:5 Kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Mariya, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu adali ndi pakati.

Luk 2:6 Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala adakwanira kuti abeleke.

Luk 2:7 Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namukulunga Iye mu nsalu, namgoneka modyera ng’ombe, chifukwa kuti adasowa malo m’nyumba ya alendo.

Luk 2:8 Ndipo padali abusa m’dziko lomwelo, wokhala kubusa ndi kuyang’anira zoweta zawo usiku.

Luk 2:9 Ndipo m’ngelo wa Ambuye adayimilira paiwo, ndi kuwala kwa Ambuye kudawaunikira mozungulira: ndipo adawopa ndi mantha akulu.

Luk 2:10 Ndipo m’ngelo adati kwa iwo, Musawope; pakuti onani, ndikuwuzani inu uthenga wabwino wa chikondwerero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse.

Luk 2:11 Pakuti wakubadwirani inu lero, m’mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.

Luk 2:12 Ndipo ichi ndichizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera.

Luk 2:13 Ndipo dzidzidzi padali pamodzi ndi m’ngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu nanena,

Luk 2:14 Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.

Luk 2:15 Ndipo padali, pamene angelo adachoka kwa iwo kupita Kumwamba, abusa adati wina ndi mzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikawone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye adatidziwitsira ife.

Luk 2:16 Ndipo iwo anadza mwachangu, napeza Mariya, ndi Yosefe ndi mwana wakhanda atagona modyera.

Luk 2:17 Ndipo pamene iwo adawona, adadziwitsa anthu za mawu adayankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.

Luk 2:18 Ndipo anthu onse amene adamva adazizwa ndi zinthu zimene abusa adayankhula nawo.

Luk 2:19 Koma Mariya adasunga mawu awa onse, nawalingalira mumtima mwake.

Luk 2:20 Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse adazimva, naziwona, monga kudayankhulidwa kwa iwo.

Luk 2:21 Ndipo pamene adakwanira masiku asanu ndi atatu a kumdula Iye, adamutcha dzina lake YESU, limene adatchula m’ngeloyo asanalandiridwe Iye m’mimba.

Luk 2:22 Ndipo pamene adakwanira masiku a kukonza kwawo, monga mwa chilamulo cha Mose iwo adakwera naye kupita ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye;

Luk 2:23 (Monga mwalembedwa m’chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna ali yense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye;)

Luk 2:24 Ndikukapereka nsembe monga mwanenedwa m’chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri kapena mawunda awiri.

Luk 2:25 Ndipo onani, mu Yerusalemu mudali munthu, dzina lake Simioni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopembedza, adalikulindira matonthozedwe a Israyeli; ndipo Mzimu Woyera adali pa iye.

Luk 2:26 Ndipo adamuwululira Mzimu Woyera kuti sadzawona imfa, kufikira adzawona Khristu wake wa Ambuye.

Luk 2:27 Ndipo iye adalowa ku kachisi ndi Mzimu; ndipo pamene atate ndi amake adalowa ndi kamwanako Yesu kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo;

Luk 2:28 Ndipo pomwepo iye adamlandira Iye m’manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati,

Luk 2:29 Tsopano Ambuye monga mwa mawu anu aja; lolani ine mtumiki wanu, ndichoke mumtendere.

Luk 2:30 Chifukwa maso anga adawona chipulumutso chanu.

Luk 2:31 Chimene mudakonzera pamaso pa anthu onse;

Luk 2:32 Kuwunika kukawalire anthu amitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.

Luk 2:33 Ndipo Yosefe ndi amake adali kuzizwa ndi zinthu zoyankhulidwa za Iye.

Luk 2:34 Ndipo Simioni adawadalitsa, nati kwa Mariya amake, tawona, Uyu wayikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israyeli; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;

Luk 2:35 ( Eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako;) manganizo a mitima yambiri ikawululidwe

Luk 2:36 Ndipo padali Anna, m’neneri wamkazi, mwana wa Fanuweli, wa fuko la Aseri; amene adali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, zaka zisanu ndi ziwiri.

Luk 2:37 Ndipo adali wamasiye kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi, amene sadachoke ku kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.

Luk 2:38 Ndipo iye adafikako pa nthawi yomweyo, nabvomerezanso kutama Ambuye, nayankhula za Iye kwa anthu onse woyembekeza chiwombolo cha Yerusalemu.

Luk 2:39 Ndipo pamene iwo adatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, ku mzinda kwawo, ku Nazarete.

Luk 2:40 Ndipo mwanayo adakula nalimbika, nadzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chidali pa Iye.

Luk 2:41 Tsopano makolo ake amkapita chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku phwando la Paskha.

Luk 2:42 Ndipo pamene Iye adali ndi zaka khumi ndi ziwiri, adakwera iwo ku Yerusalemu monga machitidwe a phwando.

Luk 2:43 Ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwerera iwo, mwanayo Yesu adatsalira m’mbuyo ku Yerusalemu; ndipo atate ndi amake sadadziwa.

Luk 2:44 Koma iwo adaganiza kuti Iye adali m’chipilingu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo adayamba kumfunafuna Iye mwa abale awo ndi mwa anansi awo.

Luk 2:45 Ndipo pamene sadampeza, adabwerera ku Yerusalemu, kukamfunafuna Iye.

Luk 2:46 Ndipo pakupita masiku atatu, adampeza Iye ali m’kachisi, alikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsa mafunso.

Luk 2:47 Ndipo onse amene adamva Iye adadabwa ndi kudziwa kwake, ndi mayankho ake.

Luk 2:48 Ndipo m’mene adamuwona Iye, anadabwa; ndipo amake adati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; tawona, atate wako ndi ine tidali kufunafuna iwe ndi kuda nkhawa.

Luk 2:49 Ndipo Iye adati kwa iwo, Kuli bwanji kuti mudali kundifunafuna Ine? Simudziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?

Luk 2:50 Ndipo sadadziwitsa mawu amene Iye adayankhula nawo.

Luk 2:51 Ndipo adatsika nawo pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo; ndipo amake adasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.

Luk 2:52 Ndipo Yesu adakulabe mu nzeru ndi mu msinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.



3

Luk 3:1 Tsopano m’chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko l Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lusaniyo chiwanga cha Abilene;

Luk 3:2 Anasi ndi Kayafa pakukhala ansembe akulu panadza mawu a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m’chipululu.

Luk 3:3 Ndipo iye anadza ku dziko lonse la mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wakulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo;

Luk 3:4 Monga mwalembedwa m’buku la mawu a Yesaya m’neneri, kuti, Mawu a wofuwula m’chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.

Luk 3:5 Chigwa chiri chonse chidzadzazidwa,ndipo phiri liri lonse ndi mtunda uliwonse zidzachepetsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama. Ndipo njira za zigolowondo zidzakhala zosalala.

Luk 3:6 Ndipo anthu onse adzawona chipulumutso cha Mulungu.

Luk 3:7 Pamenepo iye adati kwa makamu amene anadza kudzabatizidwa ndi iye, Wobadwa anjoka inu, ndani adakulangizani kuthawa mkwiyo ulimkudza?

Luk 3:8 Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye ndiye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuwukitsira Abrahamu ana.

Luk 3:9 Ndipo tsopano lino nkhwangwa yayikidwa pamizu ya mitengo; chotero mtengo uli wonse wosabala chipatso cha bwino udulidwa, nuponyedwa pa moto.

Luk 3:10 Ndipo anthu adamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tidzichita chiyani?

Luk 3:11 Iye adayankha nati kwa iwo, Iye amene ali nawo malaya awiri agawireko iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.

Luk 3:12 Pamenepo amisonkho anadza kwa iye kudzabatizidwanso, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani?

Luk 3:13 Ndipo iye adati kwa iwo, Musamawonjezerapo kanthu konse kakuposa chimene adakulamulirani.

Luk 3:14 Ndipo asilikali omwe adamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye adati kwa iwo, Musawopseze, musamanamize munthu ali yense; khalani wokhutitsidwa ndi kulipidwa kwanu.

Luk 3:15 Ndipo pamene anthu adali kuyembekezera, ndipo onse adaganizaganiza m’mitimu yawo za Yohane, ngati kapena iye adali Khristu kapena ayi:

Luk 3:16 Yohane adayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alimkudza amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

Luk 3:17 Amene chowuluzira chake chiri m’dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndikusonkhanitsa tirigu m’nkhokwe yake; koma mankhusu adzatenthedwa m’moto wosazima.

Luk 3:18 Choteretu iye adawuza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri.

Luk 3:19 Koma Herode chiwangacho, m’mene Yohane adamdzudzula chifukwa cha Herodiya mkazi wa m’bale wake Filipo, ndi cha zinthu zonse zoyipa Herode adazichita.

Luk 3:20 Adawonjeza pa zonsezi ichinso, kuti adatsekera Yohane m’nyumba yandende.

Luk 3:21 Tsopano pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa nalikupemphera, pathambo padatseguka,

Luk 3:22 Ndipo Mzimu Woyera adatsika ndi mawonekedwe athupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo mudatuluka mawu m’thambo, kuti Iwe ndiwe Mwana wanga Wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Luk 3:23 Ndipo Yesuyo, adali wa zaka makumi atatu, (monga momwe adali) mwana wa Yosefe amene adali, mwana wa Heli.

Luk 3:24 Mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Melki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe.

Luk 3:25 Amene adali mwana wa Matatio, mwana wa Amosi, mwana wa Naumi, mwana wa Esli, mwana wa Nagai,

Luk 3:26 Amene adali mwana wa Maati, mwana wa Matatio, mwana Semeini, mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda,

Luk 3:27 Amene adali mwana wa Joanani, amene adali mwana wa Resa, mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli, mwana wa Neri,

Luk 3:28 Amene adali mwana wa Melki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,

Luk 3:29 Amene adali mwana wa Jose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,

Luk 3:30 Amene adali mwana wa Sumioni, mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu,

Luk 3:31 Amene adali mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natanu, mwana wa Davide,

Luk 3:32 Amene adali mwana wa Jese, mwana wa Obede, mwana wa Boazi, mwana wa Salmoni, mwana wa Naasoni,

Luk 3:33 Amene adali mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni, mwana wa Ezironu, mwana wa Farese, mwana wa Yuda,

Luk 3:34 Amene adali mwana wa Yakobo, mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana waNakoro,

Luk 3:35 Amene adali mwana wa Seruki, mwana wa Reu, mwana wa Pelege, mwana wa Ebere, mwana wa Sala,

Luk 3:36 Amene adali mwana wa Kainane, mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameke,

Luk 3:37 Amene adali mwana wa Metusela, mwana wa Enoke, mwana wa Yaredi, mwana wa Malaleeli, mwana wa Kayinane,

Luk 3:38 Amene adali mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.



4

Luk 4:1 Ndipo Yesu wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kupita kuchipululu,

Luk 4:2 Ndipo pakukhala masiku makuni anayi nayesedwa ndi mdierekezi, sanadye kanthu kena kali konse m’masiku amenewo; ndipo pamen adatha adamva njala.

Luk 4:3 Ndipo mdierekezi adati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, lamulirani mwala uwu kuti ukhale mkate.

Luk 4:4 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Kwalembedwa kuti, munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu ali wonse a Mulungu.

Luk 4:5 Ndipo mdierekezi adamtenga Iye, nakwera naye pa phiri, namuwonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m’kamphindi kakang’ono.

Luk 4:6 Ndipo mdierekezi adati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wawo; chifukwa udaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupereka kwa iye amene ndifuna.

Luk 4:7 Chifukwa chake ngati Inu mudzandipembedza pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.

Luk 4:8 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti Ambuye Mulungu wako udzipembedza ndipo Iye yekha yekha uzimtumikira. Choka kumbuyo kwanga Satana;

Luk 4:9 Ndipo adamtsogolera Iye ku Yerusalemu, namuyika Iye pamwamba pa msonga ya kachisi, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi;

Luk 4:10 Pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamulira angelo ake za inu kuti akusungeni.

Luk 4:11 Ndipo pa manja awo adzakunyamulani Inu, kuti mungagunde konse phazi lanu pamwala.

Luk 4:12 Ndipo Yesu adayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

Luk 4:13 Ndipo mdierekezi, m’mene adamaliza mayesero onse, adalekana naye kufikira nthawi yina.

Luk 4:14 Ndipo Yesu adabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

Luk 4:15 Ndipo Iye adaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalemekezedwa ndi anthu onse.

Luk 4:16 Ndipo anadza ku Nazarete, kumene adaleredwa; ndipo tsiku la sabata adalowa m’sunagoge, monga adazolowera, adayimiliramo kuwerenga.

Luk 4:17 Ndipo adapereka kwa Iye buku la Yesaya m’neneri. Ndipo m’mene Iye adafunyulula bukulo, adapeza pomwe padalembedwa,

Luk 4:18 Mzimu wa Ambuye ali pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiwuze anthu osauka Uthenga Wabwino: kukachiritsa a mtima wosweka, adandituma Ine kulalikira a m`singa mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyenso, kupatsa ufulu wobvulazidwa.

Luk 4:19 Kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye.

Luk 4:20 Ndipo m’mene adapinda bukulo, adalipereka kwa m’nyamata, adakhala pansi; ndipo maso awo wa anthu onse m’sunagogemo adam’yang’anitsa Iye.

Luk 4:21 Ndipo adayamba kunena kwa iwo, kuti Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu.

Luk 4:22 Ndipo onse adamchitira Iye umboni nazizwa ndi mawu a chisomo akutuluka m’kamwa mwake; nanena, kodi uyu simwana wa Yosefe?

Luk 4:23 Ndipo Iye adati, kwa iwo Kwenikweni mudzati kwa Ine mwambi uwu, Sing’anga iwe, tadzichiritsa wekha; zonse zija tazimva zidachitidwa ku Kapenawo, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.

Luk 4:24 Ndipo Iye adati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, palibe m’neneri alandirika ku dziko la kwawo.

Luk 4:25 Koma zowonadi ndinena kwa inu, kuti, Mudali akazi a masiye ambiri mu Israyeli masiku ake a Eliya, pamene kudatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene padakhala njala yaikulu pa dziko lonselo;

Luk 4:26 Ndipo Eliya sadatumidwa kwa m’modzi wa iwo, koma ku Sarepta mzinda wa ku Sidoniya, kwa mkazi wa masiye.

Luk 4:27 Ndipo mudali akhate ambiri mu Israyeli masiku a Elisa m’neneri; ndipo palibe m’modzi wa iwo adakonzedwa, koma Namani, yekha wa ku Suriya.

Luk 4:28 Ndipo onse a m’sunagoge adadzala ndi m’kwiyo pakumva izi;

Luk 4:29 Ndipo adanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mzindawo, napita naye pamwamba pa phiri pamene padamangidwa mzinda wawo, kuti akamponye pansi.

Luk 4:30 Koma Iye adapyola pakati pawo, nachokapo.

Luk 4:31 Ndipo Iye adatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya, ndipo adali kuwaphunzitsa iwo m`masiku a Sabata

Luk 4:32 Ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake. Chifukwa mawu ake adali ndi mphamvu.

Luk 4:33 Ndipo m’sunagoge mudali munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuwula ndi mawu wolimba,

Luk 4:34 Nanena, Tilekeni; kodi tiri ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi mudadza kudzatiwononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu.

Luk 4:35 Ndipo Yesu adamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m’mene chidamgwetsa iye pakati, chidatuluka mwa iye chonsampweteka konse.

Luk 4:36 Ndipo anthu onse anadabwa, nayankhulana wina ndi mzake, nanena,Mawu amenewa ali wotani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.

Luk 4:37 Ndipo mbiri yake ya Iye idafalikira ku malo onse a dziko loyandikira.

Luk 4:38 Ndipo Iye adanyamuka kuchokera m’sunagoge, nalowa m’nyumba ya Simoni. Ndipo momwemo mudali amai ake a mkazi wake wa Simoni, adagwidwa ndi nthenda yolimba ya malungo; ndipo adampempha Iye za iye.

Luk 4:39 Ndipo Iye adayimilira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo idamleka iye; ndipo adauka msangatu, nawatumikira.

Luk 4:40 Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene adali nawo wodwala ndi nthenda za mitundu mitundu, anadza nawo kwa Iye, ndipo Iye adayika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa.

Luk 4:41 Ndipo ziwanda zomwe zidatuluka mwa ambiri, ndi kufuwula, kuti, Inu ndinu Khristu Mwana wa Mulungu! Ndipo Iye adazidzudzula wosazilola kuyankhula, chifukwa zidamdziwa kuti Iye ndiye Khristu.

Luk 4:42 Ndipo kutacha adatuluka Iye napita ku malo achipululu; ndipo anthu adalikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere.

Luk 4:43 Ndipo adati kwa iwo, kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku mizinda yinanso: chifukwa ndidatumidwa kudzatero.

Luk 4:44 Ndipo Iye adalalikira m’masunagoge aku Galileya.



5

Luk 5:1 Ndipo padali pakumkanikiza anthu, kudzamva mawu a Mulungu, Iye adali kuyimilira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete;

Luk 5:2 Ndipo adawona zombo ziwiri zitakhala m’mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m’menemo, nalikutsuka makoka awo.

Luk 5:3 Ndipo adakhala pansi naphunzitsa anthu kuchokera m`chombo. Ndipo Iye adalowa m`chombo chimodzi, ndicho chake cha Simoni, nampempha iye akankhe pang’ono kuchoka kumtunda.

Luk 5:4 Tsopano pamene Iye adaleka kuyankhula, adati kwa Simoni, kankhira kwakuya, nimuponye makoka anu kusodza.

Luk 5:5 Ndipo Simoni adayankha, nati kwa Iye, Ambuye, tidagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mawu anu ndidzaponya makoka.

Luk 5:6 Ndipo pamene adachita ichi, adazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka awo adalikung’ambika.

Luk 5:7 Ndipo adakodola amzawo amene adali m`chombo china kuti, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza zombo zonse ziwiri, motero kuti zidayamba kumila.

Luk 5:8 Ndipo pamene Simoni Petro adawona, adagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye chifukwa ndine munthu wochimwa.

Luk 5:9 Pakuti iye adazizwa ndi onse amene adali naye, pa zakasodzedwe kansomba zimene adazikola.

Luk 5:10 Ndipo chimodzi modzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene adali amzake a Simoni. Ndipo Yesu adati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

Luk 5:11 Ndipo m’mene iwo adakocheza zombo zawo pamtunda, adasiya zonse, namtsata Iye.

Luk 5:12 Ndipo padali pamene Iye adali m’mzinda wina, tawona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene adawona Yesu, adagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.

Luk 5:13 Ndipo Iye adatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate lidachoka kwa iye.

Luk 5:14 Ndipo iye adawalamulira, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke nudziwonetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.

Luk 5:15 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo makamu adasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zawo.

Luk 5:16 Ndipo Iye adachoka mwini yekha napita kuchipululu kukapemphera.

Luk 5:17 Ndipo padali tsiku lina, pamene Iye adali kuphunzitsa, ndipo padali Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene adachokera ku mizinda yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu; ndipo mphamvu ya Ambuye idali ndi Iye yakuwachiritsa iwo.

Luk 5:18 Ndipo onani, anthu adanyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna njira yobwera naye, ndi kumuyika pamaso pa Iye.

Luk 5:19 Ndipo pamene adalemphera kupeza polowa naye, chifukwa cha khamu, adakwera pamwamba pa denga, namtsitsira iye pobowola pa denga ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.

Luk 5:20 Ndipo Iye, pakuwona chikhulupiliro chawo, adati, kwa iye, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa .

Luk 5:21 Ndipo alembi ndi Afarisi adayamba kulingalira kuti, Ndani Uyu ayankhula zomchitira Mulungu mwano?ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha.

Luk 5:22 Koma pamene Yesu adadziwa malingaliro awo, nayankha, nati kwa iwo, mukulingalira chiyani m’mitima yanu?

Luk 5:23 Chapafupi n’chiti kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena Tawuka, nuyende?

Luk 5:24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira machimo (adati Iye kwa wodwala manjenjeyo). Ndinena kwa iwe, Tawuka, nusenze kama wako numuke kunyumba kwako.

Luk 5:25 Ndipo pomwepo adayimilira pamaso pawo, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kupita kunyumba kwake, ali kulemekeza Mulungu.

Luk 5:26 Ndipo onse adazizwa, ndipo adalemekeza Mulungu, nadzadzidwa ndi mantha, nanena kuti Lero tawona zodabwitsa.

Luk 5:27 Ndipo zitatha zinthu izi Iye adatuluka, nawona munthu wamsonkho dzina lake Levi, atakhala polandirira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine.

Luk 5:28 Ndipo iye adasiya zonse, nanyamuka, namtsata Iye.

Luk 5:29 Ndipo Levi adamkonzera Iye mphwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo padali khamu lalikulu la a misonkho, ndi enanso amene adalikuseyama pa chakudya pamodzi nawo.

Luk 5:30 Ndipo Afarisi ndi alembi awo adang’ung’uza kwa wophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi wochimwa?

Luk 5:31 Ndipo Yesu adayankha, nati kwa iwo, Amene ali wolimba safuna sing’anga; koma wodwala ndiwo,

Luk 5:32 Sindinadza Ine kuyitana wolungama, koma wochimwa kuti alape.

Luk 5:33 Ndipo iwo adati kwa Iye, Wophunzira a Yohane a masala kudya kawiri kawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso a Afarisi; koma anu amangodya ndi kumwa.

Luk 5:34 Koma Iye adati kwa iwo, Kodi mungathe kuwapanga ana a ukwati kuti asale, pamene mkwati ali nawo pamodzi?

Luk 5:35 Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku amenewo.

Luk 5:36 Ndipo Iye adayankhulanso fanizo kwa iwo, kuti palibe munthu ayika chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong’ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo.

Luk 5:37 Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m’mabotolo akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa mabotolowo, ndipo ameneyo adzatayika, ndipo mabotolo adzawonongeka.

Luk 5:38 Koma vinyo watsopano ayenera atsanulidwe m’mabotolo atsopano. Ndipo onse asungika.

Luk 5:39 Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena wakale ali wokoma.



6

Luk 6:1 Ndipo kudali kuti tsiku la Sabata yachiwiri itatha yoyamba, Iye adalimkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo wophunzira ake adalimkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m’manja mwawo, nadya.

Luk 6:2 Ndipo Afarisi ena adati kwa iwo, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika m`masiku a Sabata?

Luk 6:3 Ndipo Yesu adayankha iwo nati, Kodi simudawerengenso ngakhale chimene adachita Davide, pamene paja adamva njala, iye ndi iwo adali naye pamodzi;

Luk 6:4 Kuti adalowa m’nyumba ya Mulungu, natenga mikate yowonetsera, nadya, napatsanso iwo adali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe wokha?

Luk 6:5 Ndipo Iye adati kwa iwo, kuti, Mwana wa munthu ali Mbuye wa tsiku la sabata.

Luk 6:6 Ndipo kudali tsiku lina la sabata, Iye adalowa m’sunagoge, naphunzitsa. Ndipo mudali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja lidali lopuwala.

Luk 6:7 Ndipo alembi ndi Afarisi adalikumzonda momuyang`anitsitsa Iye, ngati adzachiritsa pa tsiku la sabata; kuti akampeze choneneza motsutsa Iye.

Luk 6:8 Koma Iye adadziwa maganizo awo; nati kwa munthuyo wa dzanja lopuwala, Nyamuka, nuyimilire pakatipo. Ndipo iye adanyamuka, nayimilira.

Luk 6:9 Ndipo pamenepo Yesu adati kwa iwo, Ndikufunsani inu chinthu chimodzi, Kodi kuloleka tsiku la sabata kuchita zabwino, kapena kuchita zoyipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuwuwononga?

Luk 6:10 Ndipo pamene adaunguzaunguza paiwo onse, adati kwa munthuyo Tambasula dzanja lako. Ndipo iye adatero, ndipo dzanja lake lidabwerera monga limzake.

Luk 6:11 Ndipo iwo adagwidwa ndi misala; nayankhulana wina ndi mzake kuti adzamchitira Yesu chiyani.

Luk 6:12 Ndipo kudali masiku amenewo, Iye adatuluka napita kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m’kupemphera kwa Mulungu.

Luk 6:13 Ndipo kutacha adayitana wophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene adawatchanso dzina lawo atumwi;

Luk 6:14 Simoni (amene adamutchanso Petro) ndi Andreya mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo.

Luk 6:15 Mateyu, ndi Tomasi ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa Zelote.

Luk 6:16 Ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Isikariyote, amene adali wompereka Iye.

Luk 6:17 Ndipo Iye adatsika nawo, nayima pachidikha, ndi gulu la wophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a kumbali ya nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene adadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zawo.

Luk 6:18 Ndipo iwo amene adabvutika ndi mizimu yonyansa adachiritsidwa.

Luk 6:19 Ndipo khamu lonse lidafuna kumkhudza Iye; chifukwa mudatuluka mphamvu mwa Iye, nachiritsidwa onse.

Luk 6:20 Ndipo Iye adakweza maso ake kwa wophunzira ake nanena, Wodala wosauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

Luk 6:21 Wodala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Wodala inu akulira tsopano; chifukwa mudzasekera.

Luk 6:22 Wodala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loyipa, chifukwa cha Mwana wa munthu.

Luk 6:23 Kondwerani tsiku lomwelo, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo awo adawachitira aneneri zonga zomwezo.

Luk 6:24 Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandiriratu chisangalatso chanu.

Luk 6:25 Tsoka kwa inu wokhuta! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka kwa inu wosekerera tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.

Luk 6:26 Tsoka kwa inu, pamene anthu adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo awo adawatero momwemo aneneri wonama.

Luk 6:27 Koma ndinena kwa inu akumva, kondanani nawo adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu.

Luk 6:28 Dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.

Luk 6:29 Ndipo kwa Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso limzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya akonso.

Luk 6:30 Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.

Luk 6:31 Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitireni inu, muwachitire iwo motero inu momwemo.

Luk 6:32 Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti wochimwa womwe akonda iwo akukondana nawo.

Luk 6:33 Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu wochimwa amachitanso chomwecho.

Luk 6:34 Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti onse anthu wochimwa amakongoletsa kwa wochimwa amzawo, kuti alandirenso momwemo.

Luk 6:35 Koma kondanani nawo adani anu, ndikuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekezera kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yayikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma osayamika ndi woyipa.

Luk 6:36 Khalani inu a chifundo monga Atate wanu ali wachifundo.

Luk 6:37 Ndipo musaweruze ndipo simudzaweruzidwa, musawatsutse ndipo simudzatsutsidwa, khululukirani ndipo mudzakhululukidwa.

Luk 6:38 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani pa chifuwa chanu, pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.

Luk 6:39 Ndipo Iye adawayankhulira fanizo, kodi wa khungu angatsogolere wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m’dzenje?

Luk 6:40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, amene adzakhala wangwiro, adzafanana ndi mphunzitsi wake.

Luk 6:41 Ndipo uyang’anitsitsiranji kachitsotso kali m’diso la m’bale wako, koma mtengo wa m’diso la iwe mwini suwuzindikira?

Luk 6:42 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, leka ndichotse kachitsotso kali m’diso lako, wosayang’anitsitsa bwino iwe mwini mtengo uli m’diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtengowo uli m’diso lako, ndipo pomwepo udzayang’anitsitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m’diso la m’bale wako.

Luk 6:43 Pakuti palibe mtengo wabwino upatsa zipatso zobvunda; kapenanso mtengo woyipa upatsa zipatso zabwino.

Luk 6:44 Pakuti mtengo uli wonse uzindikirika ndi chipatso chake pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa.

Luk 6:45 Munthu wabwino atulutsa zabwino m’chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woyipa atulutsa zoyipa m’choyipa chake; pakuti m’kamwa mwake mwa munthu mungoyankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.

Luk 6:46 Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene Ine ndizinena?

Luk 6:47 Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mawu anga, ndi kuwachita ndidzakusonyezani amene afanana naye.

Luk 6:48 Iye afanana ndi munthu womanga nyumba, amene adakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje udagunda pa nyumayo, ndipo sudakhoza kuyigwedeza; chifukwa idamangidwa pa thanthwe.

Luk 6:49 Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo udagunda mtsinje, ndipo idagwa pomwepo; ndipo kugwa kwake kwa nyumbayo kudali kwakukulu.



7

Luk 7:1 Tsopano pamene adatsiriza mawu ake onse m’makutu wa anthu, Iye adalowa m’Kapernao.

Luk 7:2 Ndipo mtumiki wa Kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kufa.

Luk 7:3 Ndipo pamene iye adamva za Yesu, adatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa mtumiki wake.

Luk 7:4 Ndipo pamene iwo adafika kwa Yesu, adampempha Iye nthawi yomweyo, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi;

Luk 7:5 Pakuti akonda mtundu wathu, ndipo adatimangira ife sunagoge.

Luk 7:6 Pamenepo Yesu adapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi panyumba yake, Kenturiyo adatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzibvute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa denga langa.

Luk 7:7 Chifukwa chake ine sindidadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu; koma nenani mawu, ndipo mtumiki wanga adzachiritsidwa.

Luk 7:8 Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera ulamiliro, ndiri nawo asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, pita, napita; ndi kwa wina, idza, nadza; ndipo kwa mtumiki wanga tachita ichi, nachita.

Luk 7:9 Pamene Yesu adamva zinthu zimenezi adazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo womutsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindidapeza ngakhale mwa Israyeli, chikhulupiliro chachikulu chotere.

Luk 7:10 Ndipo pakubwera kunyumba wotumidwawo, adapeza mtumikiyo atachira ndithu.

Luk 7:11 Ndipo kudali, litapita tsiku ili, Iye adapita kumzinda, dzina lake Nayini; ndipo ambiri a wophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu udapita naye.

Luk 7:12 Ndipo pamene adayandikira ku chipata cha mzindawo, onani pamenepo padali munthu wakufa wonyamulidwa, mwana wamwamuna m’modzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amu mzindawo adali pamodzi naye.

Luk 7:13 Ndipo pamene Ambuye adamuwona, adagwidwa ndi chifundo cha iye, nanena naye, Usalire.

Luk 7:14 Ndipo adayandikira, nakhudza chithatha; ndi womunyamulawo adayima. Ndipo Iye adati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tawuka.

Luk 7:15 Ndipo wakufayo adakhala tsonga, nayamba kuyankhula. Ndipo adampereka kwa amake.

Luk 7:16 Ndipo mantha adagwira onsewo: ndipo adalemekeza Mulungu nanena kuti, Mneneri wamkulu wawuka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.

Luk 7:17 Ndipo mbiri yake imeneyi inabuka ku Yudeya konse, ndi ku dziko lonse loyandikira.

Luk 7:18 Ndipo wophunzira a Yohane adamuwuza iye zonsezi.

Luk 7:19 Ndipo Yohane adayitana awiri a wophunzira ake, nawatuma kwa Yesu, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

Luk 7:20 Ndipo pamene anthuwo adafika kwa Iye, adati, Yohane M’batizi watituma ife kwa inu, kuti, kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

Luk 7:21 Ndipo nthawi yomweyo Iye adachiritsa ambiri nthenda zawo, ndi zobvuta, ndi mizimu yoyipa; napenyetsanso akhungu ambiri.

Luk 7:22 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, Pitani, mumuwuze Yohane zimene mwaziwona, ndi kuzimva kuti; anthu akhungu alandira kuwona kwawo, wopunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, wogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

Luk 7:23 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

Luk 7:24 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye adayamba kunena kwa anthu zokhudzana ndi Yohane, nati, Mudatuluka kupita kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

Luk 7:25 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Munthu wobvala zobvala zofewa kodi? Onani, iwo wobvala zolemera, ndi wokhala modyerera, ali m’nyumba za mafumu.

Luk 7:26 Koma mudatuluka kukawona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo woposa mneneri.

Luk 7:27 Uyu ndi uja amene adalembedwera za iye, ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere, amene adzakonzera njira yako pamaso pako.

Luk 7:28 Pakuti ndinena kwa inu, kuti Mwa wobadwa ndi akazi palibe m’modzi m`neneri wamkulu woposa Yohane M`batizi; koma iye amene ali wam’ng’ono mu Ufumu wa Mulungu ali wamkulu womposa iye.

Luk 7:29 Ndipo anthu onse amene adamva Iye ndi amisonkho omwe, adabvomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza adabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

Luk 7:30 Koma Afarisi ndi achilamulo adakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo wokha, popeza sadabatizidwa ndi iye.

Luk 7:31 Ndipo Ambuye adati, Ndidzafanizira ndi chiyani anthu am’badwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani?

Luk 7:32 Angofanana ndi ana wokhala pa msika, ndi kuyitanizana wina ndi mzake, ndi kunena, ife tidakulizirani chitoliro, ndipo inu simudabvine ayi; tinabuma maliro, ndipo simudalire ayi.

Luk 7:33 Pakuti Yohane M’batizi adafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo mudanena, Ali ndi chiwanda.

Luk 7:34 Mwana wa munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi kumwayimwa vinyo, bwenzi la amisokho ndi anthu wochimwa!

Luk 7:35 Koma nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse.

Luk 7:36 Ndipo m’modzi wa Afarisi adakhumba Iye kuti akadye naye. Ndipo adalowa m’nyumba ya Mfarisi, naseyama pachakudya.

Luk 7:37 Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene adali m’mzindamo; ndipo pakudziwa kuti Yesu adali kuseyama pachakudya m’nyumba ya Mfarisi, adatenga msupa ya alabastara ya mafuta wonunkhira bwino.

Luk 7:38 Ndipo adayimilira kumbuyo kwake, pa mapazi ake, nalira, nayamba nasambitsa mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsopsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta wonunkhira bwino.

Luk 7:39 Koma Mfarisi, amene adamuyitana Iye, pakuwona, adanena mwa iye yekha, nati, Munthu uyu, ngati akadakhala m’neneri, akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.

Luk 7:40 Ndipo Yesu adayankha kwa iye, Simoni, ndiri ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye adati, Ambuye, nenani.

Luk 7:41 Munthu wokongoletsa ndalama adali nawo angongole awiri; m’modziyo adali ndi ngongole yake ya makobiri mazana asanu koma mzake makumi asanu.

Luk 7:42 Ndipo popeza adalibe chobwezera, iye adawakhululukira onse awiri. Tandiwuzani, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?

Luk 7:43 Simoni adayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene adamkhululukira zoposa ndipo adanena kwa iye, Wayankha bwino.

Luk 7:44 Ndipo Iye adachewukira kwa mkaziyo, nati kwa Simoni, upenya mkazi ameneyu kodi? Ndidalowa m’nyumba yako, sudandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu wasambitsa mapazi anga ndi misozi nawapukuta ndi tsitsi lapamutu pake.

Luk 7:45 Sudandipatsa mpsopsono wa chibwenzi; koma uyu sadaleka kupsopsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine.

Luk 7:46 Sudandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma mkazi uyu adadzoza mapazi anga ndi mafuta wonunkhira bwino.

Luk 7:47 Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa adakonda kwambiri; koma munthu amene adamkhululukidwa pang’ono, iye akonda pang’ono.

Luk 7:48 Ndipo adati kwa mkaziyo, machimo ako akhululukidwa.

Luk 7:49 Ndipo iwo akuseyama naye pachakudya adayamba kunena mwa wokha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo?

Luk 7:50 Ndipo Iye adati kwa mkaziyo, chikhulupiliro chako chakupulumutsa iwe; pita ndi mtendere.



8

Luk 8:1 Ndipo kudali; katapita kamphindi adayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo.

Luk 8:2 Ndipo akazi ena amene adachiritsidwa mizimu yoyipa ndi nthenda zawo,ndiwo Mariya wonenedwa Magadalene, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zidatuluka mwa iye.

Luk 8:3 Ndipo Jowana mkazi wake wa Kuza kapitawo wa Herode, ndi Susana, ndi ena ambiri, amene adawatumikira ndi chuma chawo.

Luk 8:4 Ndipo pamene anthu ambiri adasonkhana ndipo adadza kwa Iye ochokera kumidzi yonse ndipo adayankhula nawo mwa fanizo.

Luk 8:5 Wofesa adatuluka kukafesa mbewu zake; ndipo mkufesa kwake zina zidagwa m’mbali mwa njira; ndipo zidapondedwa ndi mbalame za mu mlengalenga zidatha kuzidya.

Luk 8:6 Ndipo zina zidagwa pathandwe; ndipo pakumera zidafota msanga, chifukwa zidalibe m’nyontho.

Luk 8:7 Ndipo zina zidagwa pakati pa minga; ndi mingayo idaphuka pamodzi nazo, nizitsamwitsa.

Luk 8:8 Ndipo zina zidagwa pa nthaka yabwino, ndipo zidamera, ndi kupatsa zipatso za makumi khumi. Pakunena Iye izi adafuwula, iye amene ali ndi makutu akumva amve.

Luk 8:9 Ndipo wophunzira ake adamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili liri lotani?

Luk 8:10 Ndipo Iye adati, kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena wotsala ndinena nawo mwa mafanizo; kuti pa kuwona sangawone, kuti pakumva sangadziwitse.

Luk 8:11 Tsopano fanizolo ndi ili: Mbewuzo ndizo mawu a Mulungu.

Luk 8:12 Ndipo za m’mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mawu m’mitima yawo, kuti angakhulupirire ndi kupulumutsidwa.

Luk 8:13 Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mawu ndi kukondwera; koma alibe mizu, akhulupilira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesero amagwa.

Luk 8:14 Ndipo zija zidagwa ku mingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m’kupita kwawo atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo uno, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

Luk 8:15 Koma zija za m’nthaka yabwino, ndiwo amene adamva mawu nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupilira.

Luk 8:16 Palibe munthu, ayatsa nyali nayibvundikira ndi chotengera, kapena kuyiyika pansi pa kama; koma ayiyika pa choyikapo, kuti iwo akulowamo awone kuwala.

Luk 8:17 Pakuti palibe chinthu chobisika, chimene sichidzakhala chowonekera; kapena chinsinsi chimene sichidzadziwika ndi kubvumbuluka.

Luk 8:18 Chifukwa chake samalirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija awoneka ngati ali nacho.

Luk 8:19 Ndipo adadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sadakhoza kufika kwa Iye, chifukwa cha khamu la anthu.

Luk 8:20 Ndipo adamuwuza Iye kuti Amayi anu ndi abale anu ayima kunja akufuna kuwonana ndi Inu.

Luk 8:21 Koma Iye adayankha, nati kwa iwo, Amayi anga ndi abale anga ndi awa amene akumva mawu a Mulungu, nawachita.

Luk 8:22 Ndipo pamene zidatha izi tsiku linalo, Iye adalowa m’chombo, ndi wophunzira ake; nati kwa iwo, Tiwolokere tsidya lija la nyanja. Ndipo adapita.

Luk 8:23 Ndipo m’mene iwo adali kupita pamadzi, Iye adagona tulo. Ndipo panyanja padatsira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, adawopsezedwa.

Luk 8:24 Ndipo adadza kwa Iye, namudzutsa, nanena, Ambuye, Ambuye tikuwonongeka. Ndipo adadzuka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zidaleka, ndipo padagwa bata.

Luk 8:25 Ndipo Iye adati kwa iwo, chikhulupiriro chanu chiri kuti? Ndipo m’kuchita mantha adazizwa iwo, nanena wina ndi mzake, Munthu uyu ndi wotani, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?

Luk 8:26 Ndipo iwo adakocheza ku doko la dziko la Agerasa, ndilo lopenyana ndi Galileya.

Luk 8:27 Ndipo Iye adatuluka pamtunda, adakomana naye mwamuna wa mzinda, amene adali nazo ziwanda kwa nthawi yayitali; ndipo iye samabvala, ndipo samakhala m’nyumba, koma m’manda.

Luk 8:28 Pamene adamuwona Yesu, iye adafuwula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mawu akulu, Ndiri nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze ayi.

Luk 8:29 Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri amasungidwa womangidwa ndi unyolo ndi matangadza; ndipo adamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kuzipululu.

Luk 8:30 Ndipo Yesu adamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo adati, Legiyo, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.

Luk 8:31 Ndipo zidampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa kupompho.

Luk 8:32 Ndipo pamenepo padali gulu la nkhumba zambiri zimadya m’phiri. Ndipo zidapempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo adazilola.

Luk 8:33 Ndipo ziwandazo zidatuluka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo lidatsika mwaliwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanjamo,ndipo zidamira .

Luk 8:34 Ndipo wowetawo m’mene adawona chimene chidachitika, adathawa, nawuza akumzinda ndi akumidzi.

Luk 8:35 Ndipo iwo adatuluka kukawona chimene chidachitika; ndipo adadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zidatuluka mwa iye, atakhala pansi ku mapazi a Yesu wobvala ndi wanzeru zake; ndipo iwo adawopa.

Luk 8:36 Ndipo iwo amene adawona adawawuza za machiritsidwe ake a wogwidwa chiwandayo.

Luk 8:37 Ndipo khamu lonse la dziko la Agerasa loyandikira adamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa adagwidwa ndi mantha akulu ndipo adapita nalowa m`chombo nabwerera.

Luk 8:38 Tsopano munthu amene ziwanda zidatuluka mwa iye adampempha Iye akhale ndi Iye; koma Yesu adamuwuza kuti apite, nanena,

Luk 8:39 Pita kunyumba kwako, nukafotokozere zazikuluzo adakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye adachoka, nalalikira ku mzinda wonse zazikuluzo Yesu adamchitira iye.

Luk 8:40 Ndipo patapita izi pamene Yesu adabwerera, anthu adamulandira Iye mokondwera chifukwa onse adali kumuyembekezera Iye.

Luk 8:41 Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wa sunagoge; ndipo adagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze ku nyumba kwake;

Luk 8:42 Chifukwa adali naye mwana wamkazi m’modzi yekha, wa zaka zake ngati khumi ndi ziwiri, ndipo adalimkumwalira iye. Koma pakupita Iye anthu adakanikizana naye.

Luk 8:43 Ndipo mkazi, adali ndi nthenda zaka khumi ndi ziwiri yotaya mwazi, amene adalipira kwa asing’anga za moyo wake zonse, ndipo sadathe kuchiritsidwa ndi m’modzi yense,

Luk 8:44 Anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chobvala chake; ndipo pomwepo nthenda yake idaleka.

Luk 8:45 Ndipo Yesu adati, wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse adakana, Petro ndi iwo wokhala naye adati, Ambuye, khamu likukankhana pa Inu ndi kukanikizana, ndipo munena kuti, Ndani wandikhudza Ine?

Luk 8:46 Ndipo Yesu adati, Wina wandikhudza Ine; pakuti ndazindikira Ine kuti mphamvu yatuluka mwa Ine.

Luk 8:47 Ndipo pamene mkaziyo adawona kuti sadabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti adachiritsidwa pomwepo.

Luk 8:48 Ndipo Iye adati kwa iyeyu, Mwana wamkaziwe kondwera, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; pita ndi mtendere.

Luk 8:49 M’mene Iye adali chiyankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wamkazi wafa; usambvute Mphunzitsi.

Luk 8:50 Koma pamene Yesu adamva, adamuyankha iye, kuti, Usawope; khulupirira kokha, ndipo iye adzachiritsidwa.

Luk 8:51 Ndipo pamene iye adafika kunyumbako, sadaloleza munthu wina aliyense kulowa naye pamodzi, koma Petro ndi Yohane ndi Yakobo, ndi atate ndi amake amwanayo.

Luk 8:52 Ndipo onse adali kumlira iye ndi kudziguguda pa chifuwa. Koma Iye adati; Musalire; pakuti iye sadafe, koma wagona tulo.

Luk 8:53 Ndipo adamseka Iye pwepwete podziwa kuti adafa.

Luk 8:54 Ndipo Iye adawatulutsa onse kubwalo namgwira dzanja lake, nayitana, nati, Buthu, tawuka.

Luk 8:55 Ndipo mzimu wake udabwera, ndipo adauka pomwepo; ndipo Iye adawalamulira kuti ampatse kanthu kakudya.

Luk 8:56 Ndipo makolo ake anadabwa; ndipo adalamulira iwo asauze munthu ali yense chimene chidachitika.



9

Luk 9:1 Ndipo Iye adayitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.

Luk 9:2 Ndipo adawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu wodwala.

Luk 9:3 Ndipo Iye adati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka pa ulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nawo malaya awiri.

Luk 9:4 Ndipo m’nyumba ili yonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko.

Luk 9:5 Ndipo onse amene sakakulandirani inu, m’mene mutuluka m’mzinda womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya pa iwo.

Luk 9:6 Ndipo iwo adatuluka, napita m’mizinda, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuchiritsa ponse.

Luk 9:7 Ndipo Herode chiwangacho adamva mbiri yake ya zonse zidachitika; ndi Iye: ndipo zidamthetsa nzeru, chifukwa adanena anthu ena, kuti Yohane adauka kwa akufa;

Luk 9:8 Koma ena, kuti Eliya adawoneka; ndipo ena, kuti m’neneri wina wa akale aja adauka.

Luk 9:9 Ndipo Herode adati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo adakhumba kumuona Iye.

Luk 9:10 Ndipo atumwi atabwera, adamfotokozera Iye zonse adazichita. Ndipo Iye adawatenga, napatuka nawo pa wokha kumka ku mzinda dzina lake Betsaida.

Luk 9:11 Ndipo anthu, pamene adadziwa, adamtsata Iye; ndipo Iye adawalandira, nayankhula nawo za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene adasowa kuchiritsidwa.

Luk 9:12 Koma pamene tsiku limapita kumapeto pamenepo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu amuke, kuti apite ku mizinda yoyandikira ndi kumidzi, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tiri ku malo a chipululu kuno.

Luk 9:13 Koma Iye adati kwa iwo, muwapatse chakudya ndinu. Koma adati, ife tiribe yochuluka koma isanu yokha ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya.

Luk 9:14 Pakuti adali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye adati kwa wophunzira ake, khalitsani iwo pansi m`magulu, a makumi asanu asanu.

Luk 9:15 Ndipo adatero, nawakhalitsa pansi onsewo.

Luk 9:16 Ndipo iye m’mene adatenga, mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri adayang’ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa wophunzira apereke kwa makamuwo.

Luk 9:17 Ndipo anadya nakhuta onsewo; natola makombo, mitanga khumi ndi iwiri.

Luk 9:18 Ndipo kudali, pamene Iye adali kupemphera payekha wophunzira adali naye; ndipo adawafunsa iwo, kuti, anthu anena kuti Ine ndine yani?

Luk 9:19 Iwo adayankha nati, Yohane M’batizi; koma ena ati Eliya; ndi ena ati, kuti adauka m’modzi wa aneneri akale.

Luk 9:20 Iye adati kwa iwo, koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo adayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu.

Luk 9:21 Ndipo Iye adawauzitsa iwo, nawalamulira kuti asanene ichi kwa munthu ali yense.

Luk 9:22 Nanena, kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi ndi kuphedwa, ndi kuwuka tsiku la chitatu.

Luk 9:23 Ndipo Iye adanena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.

Luk 9:24 Pakuti amene adzapulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupulumutsa.

Luk 9:25 Pakuti munthu adzapindulanji akadzilemeretsa dziko lonse lapansi nadzatayapo, kapena kulipa moyo wake?

Luk 9:26 Pakuti amene ali yense adzachita manyazi chifukwa cha Ine, ndi mawu anga, Mwana wa munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika mu ulemerero wake ndi wa Atate ake ndi wa angelo woyera.

Luk 9:27 Koma Ine ndinena ndi inu zowonadi, pali ena a iwo ayima pano, amene sadzalawa imfa, kufikira kuti adzawona Ufumu wa Mulungu.

Luk 9:28 Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mawu amenewa, Iye adatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo adapita nawo, nakwera m’phiri kukapemphera.

Luk 9:29 Ndipo m’kupemphera kwake, mawonekedwe a nkhope yake adasandulika, ndi chobvala chake chidayera ndi kunyezimira.

Luk 9:30 Ndipo onani, adalikuyankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya.

Luk 9:31 Amene adawonekera mu ulemerero, nanena za imfa yake imene Iye ati idzachitikira ku Yerusalemu.

Luk 9:32 Koma Petro ndi iwo adali naye adalemedwa ndi tulo; pamene adadzuka, adawona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo amene adayima ndi Iye.

Luk 9:33 Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro adati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tikhale pano; ndipo timange mahema atatu, imodzi ya Inu, ndi yina ya Mose, ndi yina ya Eliya; wosadziwa chimene iye adali kunena.

Luk 9:34 Ndipo ali chiyankhulire izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo adawopa pakulowa iwo mumtambowo.

Luk 9:35 Ndipo mudatuluka mawu mu mtambo nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wokondedwa; mverani Iye.

Luk 9:36 Ndipo pakutha mawuwo, Yesu adapezeka ali yekha. Ndipo iwo adakhala chete, ndipo sadauza munthu ali yense masiku aja kanthu konse ka izo adaziwona.

Luk 9:37 Ndipo panali, m’mawa mwake atatsika m’phiri anthu ambiri adakomana naye.

Luk 9:38 Ndipo onani, munthu wa m’khamulo adafuwula, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang’anireni mwana wanga; chifukwa ndiye m’modzi yekha wa ine:

Luk 9:39 Ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuwula modzidzimuka; ndipo umam’ng’amba iye ndi kumchititsa thobvu pakamwa nubvulaza, nuchoka kwa iye.

Luk 9:40 Ndipo ndidawapempha wophunzira anu kuti awutulutse; koma sadathe.

Luk 9:41 Ndipo Yesu adayankha, nati, Ha! Wobadwa inu wosakhulupilira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndikulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako.

Luk 9:42 Ndipo pamene iye adali mkudza, chiwandacho chidamgwetsa pansi, ndi kum’ng’ambitsa. Koma Yesu adadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mwanayo, nam’bwezera iye kwa atate wake.

Luk 9:43 Ndipo onse anadabwa ndi mphamvu ya ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse adalikuzizwa ndi zonse zimene Yesu adazichita, Iye adati kwa wophunzira ake,

Luk 9:44 Alowe mawu amenewa m’makutu anu; pakuti mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja a anthu.

Luk 9:45 Koma iwo sadadziwitse mawu awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo adawopa kumfunsa za mawu awa.

Luk 9:46 Ndipo adayamba kutsutsana mwa iwo wokha kuti wa mkulu mwa iwo ndani.

Luk 9:47 Koma Yesu pakuwona kutsutsana kwa mitima yawo, adatenga kamwana, nakayimika pambali pake, nati kwa iwo.

Luk 9:48 Ndipo Iye adati kwa iwo, Amene ali yense adzalandira kamwana aka m’dzina langa alandira Ine; ndipo amene aliyense andilandira Ine alandira Iye amene adandituma Ine; pakuti iye wakukhala wam’ng’onong’ono wa inu nonse yemweyu ndiye adzakhala wamkulu.

Luk 9:49 Ndipo Yohane adayankha nati, Ambuye, tidawona wina ali kutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tidamletsa , chifukwa sadatsatana nafe.

Luk 9:50 Koma Yesu adati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nafe athandizana nafe.

Luk 9:51 Ndipo padali pamene adayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye Kumwamba, Iye adatsimikiza kuloza nkhope yake kumka ku Yerusalemu.

Luk 9:52 Ndipo adatumiza a mithenga patsogolo pake; ndipo adamka, nalowa m’mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo.

Luk 9:53 Ndipo iwo sadamlandire Iye, chifukwa nkhope yake idali yoloza kumka ku Yerusalemu.

Luk 9:54 Ndipo pamene wophunzira ake Yakobo ndi Yohane adawona izi , adati, Ambuye, kodi mufuna kuti ife tiwuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo monga Eliya adachitira?

Luk 9:55 Koma Iye adapotoloka nawadzudzula iwo, nati, Inu simukudziwa za mtundu wa mzimu muli nawo.

Luk 9:56 Pakuti Mwana wa munthu sanadza kudzawononga miyoyo ya anthu, koma kuwapulumutsa iwo. Ndipo adapita kumudzi kwina.

Luk 9:57 Ndipo m’mene iwo adalikuyenda m’njira, munthu wina adati kwa Iye, Ambuye, Ine ndidzakutsatani kumene kuli konse mukapitako.

Luk 9:58 Ndipo Yesu adati kwa iye, Nkhandwe ziri nazo mayenje, ndi mbalame za mulengalenga zisa, koma Mwana wa munthu alibe potsamila mutu wake.

Luk 9:59 Ndipo adati kwa wina, Unditsate Ine. Koma iye adati, Ambuye, Mundilole ine; choyamba ndi yambe ndapita kukayika maliro a atate wanga.

Luk 9:60 Koma Yesu adati kwa iye, Leka akufa ayike akufa awo wokha; koma muka iwe nukalalikire Ufumu wa Mulungu.

Luk 9:61 Ndipo winanso adati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muyambe mwandilola kulawirana nawo a kunyumba kwanga.

Luk 9:62 Koma Yesu adati kwa iye, palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang’ana za kumbuyo, ali woyenera Ufumu wa Mulungu.



10

Luk 10:1 Zitatha izi Ambuye adasankha ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiri awiri pamaso pake ku mzinda uli wonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini yekha.

Luk 10:2 Chifukwa chake adanena kwa iwo, Zokolola zichulukadi, koma antchito ali wochepa; potero pemphererani kwa Mbuye wa zokolola, kuti atumize antchito kukakolola.

Luk 10:3 Mukani; tawonani Ine ndituma inu ngati ana a nkhosa pakati pa mimbulu.

Luk 10:4 Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; ndipo musayankhule munthu panjira.

Luk 10:5 Ndipo m’nyumba ili yonse mukalowamo muyambe mwanena kuti, Mtendere ukhale pa nyumba iyi.

Luk 10:6 Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m’menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.

Luk 10:7 Ndipo m’nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa zamomwemo monga akupatsani; pakuti wantchito ayenera kulandira mphotho yake; musachoka kupita m’nyumba ina ndi ina.

Luk 10:8 Ndipo mumzinda uli wonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani;

Luk 10:9 Ndipo chiritsani wodwala ali momwemo nimunene nawo, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.

Luk 10:10 Koma kumzinda uli wonse mukalowako, ndipo salandira inu pitani kunjira za kumakhwalala ake a kumeneko ndi kunena.

Luk 10:11 Lingakhale fumbi lochokera kumzinda kwanu, lomamatika ku mapazi athu, tilisansiramotsutsana ndi inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.

Luk 10:12 Koma ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodoma kudzapilirika kuposa mzinda umenewo.

Luk 10:13 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikachitika m’Turo ndi Sidoni ntchito zamphamvuzi zimene zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi wobvala chiguduli ndi phulusa.

Luk 10:14 Koma ku Turo ndi ku Sidoni kudzapiririka, pachiweruziro, koposa inu.

Luk 10:15 Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku gehena.

Luk 10:16 Iye womvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wonyoza inu, andinyoza Ine; ndipo iye wonyoza Ine am`nyoza Iye amene adandituma Ine.

Luk 10:17 Ndipo makumi asanu ndi awiriwo anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zidatigonjera ife m’dzina lanu.

Luk 10:18 Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndidawona Satana alimkugwa ngati mphenzi wochokera kumwamba.

Luk 10:19 Tawonani, ndakupatsani inu mphamvu yoponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu ili yonse ya m’daniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakupwetekani konse.

Luk 10:20 Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti mayina anu alembedwa m’Mwamba.

Luk 10:21 Nthawi yomweyo Yesu adakondwera mu mzimu, nati, Ndiyamika Inu, Atate, Ambuye wa Kumwamba ndi wa dziko la pansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi wozindikira, ndipo mudaziwululira ana amakanda; indedi; Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.

Luk 10:22 Zinthu zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma atate, ndi iye amene Mwana afuna kumuwululira Iye.

Luk 10:23 Ndipo Iye m’mene adapotolokera kwa wophunzira ake, ali pa wokha, adati, Wodala masowo akuwona zimene muwona.

Luk 10:24 Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri adafuna kuwona zimene inu muziwona, koma sadaziwona; ndi kumva zimene mukumva, koma sadazimva.

Luk 10:25 Ndipo tawonani, wachilamulo wina adayimilira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?

Luk 10:26 Ndipo adati kwa iye, M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji?

Luk 10:27 Ndipo Iye adayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi m’nansi wako monga iwe mwini.

Luk 10:28 Ndipo Iye adati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.

Luk 10:29 Koma iye, pofuna kudziyesa wolungama yekha, adati kwa Yesu, Ndipo m’nansi wanga ndani?

Luk 10:30 Ndipo Yesu adayankha, nati, Munthu wina adatsika kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko; ndipo anagwa m’manja wa achifwamba amene adambvula zobvala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa.

Luk 10:31 Ndipo kudangotero kuti wansembe wina adatsika njirayo, ndipo pakumuwona iye anadutsa mbali yina.

Luk 10:32 Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuwona Iye, anadutsa mbali yina.

Luk 10:33 Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake adafika padali iye; ndipo pakumuwona, adagwidwa chifundo ndi iye,

Luk 10:34 Ndipo anadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo adamuyika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye ku nyumba ya alendo, namsamalira iye.

Luk 10:35 Ndipo pamene m’mawa mwake amapita adatulutsa makobiri nampatsa mwini nyumba ya alendo, nati, kwa iye msamalireni iye, ndipo chiri chonse muononga koposa, ine, pobweranso ndidzakubwezera iwe.

Luk 10:36 Uti wa awa atatu, uyesa iwe, adakhala m’nansi wa iye uja adagwa m’manja mwa achifwamba?

Luk 10:37 Ndipo Iye adati, Iye amene adachita chifundo. Ndipo Yesu adati kwa iye, Pita, nuchite iwe momwemo.

Luk 10:38 Tsopano pakupita pa ulendo pawo Iye adalowa m’mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita adamlandira Iye kunyumba kwake.

Luk 10:39 Ndipo iye adali ndi mbale wake wotchedwa Mariya, ndiye wakukhala pa mapazi a Yesu, namva mawu ake.

Luk 10:40 Koma Marita adatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo adadza kwa Iye, nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga wandisiya nditumikire ndekha? Mumuwuze iye tsono kuti andithandize.

Luk 10:41 Koma Yesu adayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nubvutika ndi zinthu zambiri:

Luk 10:42 Koma chifunika chinthu chimodzi, pakuti Mariya wasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.



11

Luk 11:1 Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m’mene adaleka, wina wa wophunzira ake adati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane adaphunzitsa wophunzira ake.

Luk 11:2 Ndipo Iye adati kwa iwo, pamene mupemphera nenani, Atate wathu, amene muli m’Mwamba, dzina lanu liyeretsedwe; Ufumu wanu udze; kufuna kwanu kuchitidwe monga Kumwamba chomwecho pansi pano.

Luk 11:3 Tipatseni ife tsiku ndi tsiku mkate wa pa tsiku.

Luk 11:4 Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa; koma mutipulumutse ife kuchoka kwa woyipayo.

Luk 11:5 Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;

Luk 11:6 Popeza wandidzera bwenzi langa lochokera pa ulendo, ndipo ndiribe chompatsa.

Luk 11:7 Ndipo iyeyu wa m’katimo poyankha adati, Usandibvuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pakama; sindikhoza kuwuka ndi kukupatsa.

Luk 11:8 Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma lake adzauka nadzampatsa iye ziri zonse azifuna.

Luk 11:9 Ndipo Ine ndinena ndi inu, pemphani, ndipo adzakupatsani, funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.

Luk 11:10 Pakuti yense wopempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

Luk 11:11 Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, kodi adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzam’ninkha njoka m’malo mwa nsomba kodi?

Luk 11:12 Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira?

Luk 11:13 Potero inu, ngati inu, wokhala woyipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?

Luk 11:14 Ndipo adali kutulutsa chiwanda chosayankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosayankhulayo adayankhula; ndipo anthu adazizwa.

Luk 11:15 Koma ena mwa iwo adati, Ndi Belezebule mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.

Luk 11:16 Koma ena adamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba.

Luk 11:17 Koma Iye, podziwa zolingilira zawo, adati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m’kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m’kati mwake igwa.

Luk 11:18 Ndiponso ngati satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzayima bwanji Ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi belezebule.

Luk 11:19 Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi belezebule, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala woweruza anu.

Luk 11:20 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu popanda kukayika, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.

Luk 11:21 Pamene pali ponse munthu wa mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake ziri mumtendere;

Luk 11:22 Koma pamene pali ponse akamdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka amchotsera zida zake zonse, zimene adazikhulupirira, nagawa zofunkha zake.

Luk 11:23 Iye wosabvomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.

Luk 11:24 Pamene mzimu wonyansa utuluka mwa munthu, upyola malo wopanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera ku nyumba kwanga kumene ndidatulukako,

Luk 11:25 Ndipo pofika, uyipeza yosesa ndi yokonzeka.

Luk 11:26 Pomwepo upita nutenga mizimu yina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe wotsiriza a munthu uyu ayipa koposa woyambawo.

Luk 11:27 Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina wa khamu la anthu adakweza mawu, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene mudayamwa.

Luk 11:28 Koma Iye adati, Inde, koma wodala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.

Luk 11:29 Ndipo pamene adasonkhana anthu, adayamba kunena, mbado uno ndi mbado woyipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona m`neneri.

Luk 11:30 Pakuti monga ngati Yona adali chizindikiro kwa Anineve, chotero adzakhalanso Mwana wa munthu kwa mbado uno.

Luk 11:31 Mfumu yaikazi ya kumwera idzayimilira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbado uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera ku malekezero adziko kudzamva nzeru za Solomo; ndipo onani wamkulu, woposa Solomo ali pano.

Luk 11:32 Amuna aku Nineve adzayimilira pakuweruza kotsiriza pamodzi ndi anthu a mbado uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo adalapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo onani wamkulu, woposa Yona ali pano.

Luk 11:33 Palibe munthu, atayatsa nyali, ayiyika malo obisika, kapena pansi pa muyeso, koma pa choyikapo chake, kuti iwo akulowamo awone kuwala.

Luk 11:34 Nyali yathupi ndiyo diso; pamene pali ponse diso lako liri langwiro thupi lako lonse liwunikidwanso monsemo; koma likakhala loyipa, thupi lako lomwe liri la mdima wokha wokha.

Luk 11:35 Potero yang’anira kuti kuwunika kuli mwa iwe kungakhale mdima.

Luk 11:36 Pamenepo ngati thupi lako lonse liwunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lowunikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuwunikira iwe.

Luk 11:37 Ndipo pakuyankhula Iye, adamuyitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo Iye adakhala pansi nadya.

Luk 11:38 Ndipo pamene Mfarisiyo adawona adazizwa, pakuwona kuti adayamba kudya asadasambe.

Luk 11:39 Koma Ambuye adati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’kati mwanu mudzala zolanda ndi zoyipa.

Luk 11:40 Wopusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapanganso m’kati mwake?

Luk 11:41 Koma patsani mphatso ya chifundo za m’katimo; ndipo onani, zonse ziri zoyera kwa inu.

Luk 11:42 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruziro ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.

Luk 11:43 Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando ya ulemu m’masunagoge, ndi kuyankhulidwa m’misika.

Luk 11:44 Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda wosawoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pawo sadziwa.

Luk 11:45 Ndipo m’modzi wa a chilamulo adayankha, nanena kwa Iye, mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.

Luk 11:46 Ndipo Iye adati, Tsoka inunso, a chilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu wosautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.

Luk 11:47 Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda wa aneneri, ndi makolo anu adawapha.

Luk 11:48 Chomwecho muli mboni, ndipo mubvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu adawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.

Luk 11:49 Mwa ichinso nzeru ya Mulungu idati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;

Luk 11:50 Kuti mwazi wa aneneri onse, udakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;

Luk 11:51 Kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zakariya, amene adamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

Luk 11:52 Tsoka inu, a chilamulo! Chifukwa mumachotsa chifungulo cha nzeru; inu simudalowamo nokha, ndipo mudawaletsa iwo adalinkulowa.

Luk 11:53 Ndipo pamene Iye adanena zinthu izi kwa iwo, alembi ndi Afarisi adayamba kutsutsana naye kolimba, ndi kumputa Iye kuti ayankhule zinthu zambiri;

Luk 11:54 Nadikirira Iye ndikufuna kuti akakole kanthu kotuluka m’kamwa mwake, ndi kuti akamtsutse



12

Luk 12:1 Pomwepo pamene anthu a zikwi zikwi a khamu adasonkhana, pamodzi, kotero kuti adapondana, Iye adayamba kunena kwa wophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chiri chinyengo.

Luk 12:2 Pakuti kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

Luk 12:3 Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mu mdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwayankhula m’khutu, m’zipinda za mkati chidzalalikidwa pa madenga a nyumba.

Luk 12:4 Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musawope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita.

Luk 12:5 Koma ndidzakulangizani amene muzimuwopa; tawopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kugehena, inde, ndinena ndi inu wopani ameneyo.

Luk 12:6 Kodi mpheta zisanu sizigulitsidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iyiwalika pamaso pa Mulungu.

Luk 12:7 Komatu ngakhale tsitsi lonse la pamutu panu liwerengedwa. Musawopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.

Luk 12:8 Ndiponso ndinena kwa inu, Amene ali yense adzabvomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa munthu adzambvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu:

Luk 12:9 Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.

Luk 12:10 Ndipo ali yense amene adzanenera Mwana wa munthu zoyipa adzakhululukidwa; koma amene adzanenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

Luk 12:11 Ndipo pamene pali ponse adzapita nanu ku mlandu wa m’sunagoge ndi kwa akulu, ndi a mphamvu, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo mawu wotani, kapena mukanena chiyani;

Luk 12:12 Pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.

Luk 12:13 Ndipo munthu wa m’khamulo adati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma cha masiye.

Luk 12:14 Ndipo adati kwa iye, Munthu iwe, ndani adandiyika Ine ndikhale woweruza, kapena wogawira inu?

Luk 12:15 Ndipo Iye adati kwa iwo, Yang’anirani, mudzisungire kupewa msiliro uli wonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

Luk 12:16 Ndipo Iye adanena nawo fanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma udapatsa zambiri:

Luk 12:17 Ndipo adaganizaganiza mwa yekha, nanena, Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga?

Luk 12:18 Ndipo iye adati, Ndidzatere; ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiranso dzinthu zanga zonse, ndi katundu wanga.

Luk 12:19 Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli ndi katundu wambiri wosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere,

Luk 12:20 Koma Mulungu adati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene udazisunga zidzakhala za yani?

Luk 12:21 Atero iye wodziwunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.

Luk 12:22 Ndipo Iye adati kwa wophunzira ake, chifukwa chake ndinena ndi inu, musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzabvala.

Luk 12:23 Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chobvala.

Luk 12:24 Lingilirani makungubwe, kuti samafesayi, kapena kutemayi, alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu amawadyetsa: nanga inu simuziposa mbalame kwambiri?

Luk 12:25 Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuwonjeza mkono pa msinkhu wake?

Luk 12:26 Kotero ngati simungathe ngakhale chaching’onong’ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?

Luk 12:27 Lingalirani maluwa, makulidwe awo; sagwilitsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemerero wake wonse sadabvala ngati limodzi la awa.

Luk 12:28 Koma ngati Mulungu abveka kotere udzu wa kuthengo wokhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu wokhulupirira pang’ono.

Luk 12:29 Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.

Luk 12:30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi inu.

Luk 12:31 Makamaka tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuwonjezerani.

Luk 12:32 Musawopa, kagulu kankhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

Luk 12:33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba andalama amene sakutha, chuma chosatha m’Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete sizichiwononga.

Luk 12:34 Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

Luk 12:35 Khalani wodzimangira m’chiwuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

Luk 12:36 Ndipo inu nokha khalani wofanana ndi anthu woyembekezera mbuye wawo, pamene ati abwera kuchokera ku ukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

Luk 12:37 Wodala atumikiwo amene mbuye wawo, pakudza iye, adzawapeza wodikira; indetu ndinena ndi inu, kuti iye adzadzimangira m’chiwuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

Luk 12:38 Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, wodala atumiki amenewa.

Luk 12:39 Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba wabwino akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibowoledwe.

Luk 12:40 Khalani wokonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingilira, Mwana wa munthu adzadza.

Luk 12:41 Ndipo Petro adati kwa Iye, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?

Luk 12:42 Ndipo Ambuye adati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wa nzeru, amene mbuye wake adzamuyika kapitawo wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lawo pa nthawi yake?

Luk 12:43 Wodala mtumikiyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero.

Luk 12:44 Ndinena ndi inu zowona, kuti adzamuyika iye kapitawo wa pa zonse ali nazo.

Luk 12:45 Koma mtumiki uyo akanena mu mtima mwake, mbuye wanga achedwa azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;

Luk 12:46 Mbuye wa mtumiki uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera ndi nthawi yakuti sayidziwa, nadzamdula iye pakati, nadzamuyika dera lake pamodzi ndi anthu wosakhulupirira.

Luk 12:47 Ndipo mtumiki uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sadakonza, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.

Luk 12:48 Koma iye amene sadachidziwa, ndipo adazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang’ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene adamuyikizira zambiri, adzamuwuza abwezere zoposa.

Luk 12:49 Ine ndinadzera kuponya moto pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji ngati udatha kuyatsidwa?

Luk 12:50 Koma ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nawo; ndipo ndikakamizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

Luk 12:51 Kodi muyesa kuti ndidadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapansi? Ndinena kwa inu, Ayitu, komatu kungawanikana;

Luk 12:52 Pakuti kuyambira tsopano adzakhala m’nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

Luk 12:53 Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake, amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wa mkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.

Luk 12:54 Ndipo Iye adatinso kwa anthu, pamene pali ponse muwona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti ikudza mimvumbi; ndipo itero.

Luk 12:55 Ndipo pamene muwona mphepo ya kumwera iwomba; munena, kuti kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.

Luk 12:56 Wonyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo yino?

Luk 12:57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

Luk 12:58 Pakuti pamene uli kupita naye m`dani wako kwa woweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa woweruza, ndipo woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m’nyumba yandende.

Luk 12:59 Ine ndinena kwa iwe, sudzatulukamo konse kufikira utalipira kakobiri komaliza.



13

Luk 13:1 Ndipo adakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene adamuwuza Iye za Agalileya, amene Pilato adasanganiza mwazi wawo ndi nsembe zawo. Luk 13:2 Ndipo Yesu adayankha nati kwa iwo, kodi muyesa kuti Agalileya aja adali anthu wochimwa koposa, Agalileya onse, chifukwa adamva zowawa izi? Luk 13:3 Ndinena kwa inu, Iyayitu, koma ngati inu simulapa, mudzawonongeka nonse momwemo. Luk 13:4 Kapena aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yayitali ya m’Siloamu idawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo adali wochimwa koposa anthu onse wokhala m’Yerusalemu? Luk 13:5 Ndinena kwa inu, Iyayitu; koma ngati simulapa mudzawonongeka nonse chimodzimodzi. Luk 13:6 Iye adanenanso fanizo ili: Munthu wina adali ndi mtengo wa mkuyu wowoka m’munda wake wamphesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma adapeza palibe. Luk 13:7 Ndipo adati kwa wosungira munda wa mphesa, Tawona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mtengo wa mkuyu uwu; ndipo ndimapeza palibe: tawulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake? Luk 13:8 Ndipo iye adayankha nati kwa Iye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe. Luk 13:9 Ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino koma ngati ayi, mudzaulikhatu. Luk 13:10 Ndipo adalikuphunzitsa m’sunagoge mwina, tsiku la Sabata. Luk 13:11 Ndipo tawonani, padali mkazi amene adali nawo mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopweteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka. Luk 13:12 Ndipo Yesu m’mene adamuwona, adamuyitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kuzopweteka zako. Luk 13:13 Ndipo adayika manja ake pa iye; ndipo pomwepo adawongoledwa, nalemekeza Mulungu. Luk 13:14 Ndipo mkulu wa sunagoge adabvutika mtima, chifukwa Yesu adachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa anthuwo, Alipo masiku asanu ndi limodzi m’menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ayi. Luk 13:15 Koma Ambuye adamyankha iye, nati Wonyenga iwe, kodi munthu aliyense wa inu samayimasula ng’ombe yake, kapena bulu wake kuchodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukayimwetsa madzi? Luk 13:16 Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana adam’manga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata? Luk 13:17 Ndipo pamene Iye adatero, onse aja wotsutsana naye adanyanzitsidwa; ndipo anthu onse adakondwera ndi zinthu zonse za ulemerero zidachitidwa ndi Iye. Luk 13:18 Pamenepo Iye adanena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani? Luk 13:19 Ufanana ndi kambewu kampiru, kamene munthu adatenga, nakaponya m’munda wake wake, ndipo kadamera, ndikukhala mtengo wa ukulu; ndipo mbalame za mumlengalenga zinabindikira mu nthambi zake. Luk 13:20 Ndiponso Iye adati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Luk 13:21 Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi adatenga, nachibisa mu miyeso itatu yaufa, kufikira udatupa wonsewo. Luk 13:22 Ndipo Iye adapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kumkabe ku Yerusalemu. Luk 13:23 Ndipo munthu adati kwa Iye, Ambuye wopulumutsidwa ndiwo wowerengeka kodi? Koma Iye adati kwa iwo, Luk 13:24 Yesetsani kulowa chipata chopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuwuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza. Luk 13:25 Pamene atawuka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuyima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati kwa inu; sindidziwa inu kumene muchokerako: Luk 13:26 Pomwepo mudzayamba kunena, ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo mudaphunzitsa m’makwalala a kwathu. Luk 13:27 Ndipo Iye adzati, Sindikudziwani kumene inu muchokera. Chokani kwa Ine inu akuchita kusaweruzika. Luk 13:28 Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzawona Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo ndi aneneri onse mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mukutulutsidwa kunja. Luk 13:29 Ndipo anthu adzachokera kum’mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu. Luk 13:30 Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala woyamba, ndipo alipo woyamba adzakhala akuthungo. Luk 13:31 Tsiku lomwelo adadzapo Afarisi ena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwa Herode afuna kupha inu. Luk 13:32 Ndipo Iye adati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Tawonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa,ndipo mkucha ndidzakhalitsidwa wangwiro. Luk 13:33 Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi m’kucha, chifukwa sikuloleka kuti m’neneri awonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu. Luk 13:34 Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi woponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawiri kawiri ndidafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m’mapiko ake, ndipo simudafuna ayi! Luk 13:35 Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, simudzandiwona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m’dzina la Ambuye.



14

Luk 14:1 Ndipo padali pamene Iye adalowa m’nyumba ya m’modzi wa akulu afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo adalikumzonda Iye.

Luk 14:2 Ndipo onani, padali pamaso pake munthu wambulu.

Luk 14:3 Ndipo Yesu adayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena ayi?

Luk 14:4 Koma iwo adakhala chete. Ndipo adamtenga namchiritsa, namuwuza apite.

Luk 14:5 Ndipo adati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng’ombe yake itagwa m’chitsime, ndipo sadzayitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?

Luk 14:6 Ndipo iwo sadatha kumuyankha pa zinthu izi.

Luk 14:7 Ndipo Iye adanena fanizo kwa woyitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo.

Luk 14:8 Pamene pali ponse wayitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati, usakhale pa mpando wa ulemu; kuti kapena wina wa ulemu woposa iwe adzayitanidwa ndi iye,

Luk 14:9 Ndipo pakufika iye amene adayitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba kuchita manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.

Luk 14:10 Koma pamene pali ponse wayitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye adakuyitana iwe akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse, akuseyama pachakudya pamodzi ndi iwe.

Luk 14:11 Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wodzichepetsa adzakulitsidwa.

Luk 14:12 Pamenepo Iye adanenanso kwa iye amene adamuyitana, pamene ukonza chakudya cha pa usana kapena cha madzulo, usayitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuyitana iwe, ndipo udzakhala nako kubwezeredwa.

Luk 14:13 Koma pamene ukonza phwando uyitane a umphawi, wopunduka, wotsimphina, akhungu;

Luk 14:14 Ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuwuka kwa wolungama.

Luk 14:15 Ndipo pamene wina wa iwo akukhala pachakudya pamodzi ndi Iye atamva izi, adati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.

Luk 14:16 Koma adati kwa iye, Munthu wina adakonza phwando lalikulu; nayitana anthu ambiri;

Luk 14:17 Ndipo adatumiza mtumiki wake pa nthawi ya mphwando kukanena kwa woyitanidwawo, idzani chifukwa zonse zakonzeka tsopano.

Luk 14:18 Ndipo onse ndi mtima umodzi adayamba kuwilingula. Woyamba adati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituluke ndikawuwone; ndikupempha undilole ine ndisafike.

Luk 14:19 Ndipo wina adati, Ine ndagula ng’ombe za magoli asanu, ndipo ndimka kukaziyesa; ndikupempha undilole ndisafike.

Luk 14:20 Ndipo wina adati, ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza.

Luk 14:21 Ndipo mtumikiyo pakubwera adawuza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba adakwiya, nati kwa mtumiki wakeyo, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mudzi, nubwere nawo muno aumphawi ndi wopunduka ndi akhungu ndi wotsimphina.

Luk 14:22 Ndipo mtumikiyo adati, ‘Ambuye, chimene mudachilamulira chachitika, ndipo malo akadalipobe’.

Luk 14:23 Ndipo mbuye adanena kwa mtumikiyo, Tuluka, nupite ku misewu ndi njira za kuminda, nuwawumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale.

Luk 14:24 Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe m’modzi wa amuna woyitanidwa aja adzalowa phwando langa.

Luk 14:25 Ndipo khamu lalikulu lidapita naye; ndipo Iye adapotoloka nati kwa iwo,

Luk 14:26 Ngati munthu adza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale ake, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.

Luk 14:27 Ndipo amene ali yense sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga.

Luk 14:28 Pakuti ndani wa inu amene akufuna kumanga nsanja yayitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, awone ngati ali nazo zakuyimaliza?

Luk 14:29 Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya maziko ake, wosakhoza kuyimaliza, anthu onse woyang’ana adzayamba kumseka iye.

Luk 14:30 Ndikunena kuti, Munthu uyu adayamba kumanga, koma sadathe kumaliza.

Luk 14:31 Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu imzake, siyiyamba yakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikari ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikari zikwi makumi awiri?

Luk 14:32 Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.

Luk 14:33 Chomwecho ndinena kwa inu, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga.

Luk 14:34 Mchere ndi wa bwino; koma ngati mchere usukuluka adzaukoleretsa ndi chiyani?

Luk 14:35 Suyenera kuwuthira pamunda kapena padzala, anthu autaya kunja. Amene ali nawo makutu akumva amve.



15

Luk 15:1 Pamenepo adayandikira kwa Iye a misonkho onse ndi anthu wochimwa kudzamva Iye.

Luk 15:2 Ndipo Afarisi ndi alembi adanyinyirika nati, Munthu uyu alandira anthu wochimwa, nadya nawo.

Luk 15:3 Ndipo Iye adayankhula fanizo ili kwa iwo, nanena,

Luk 15:4 Munthu ndani wa inu, ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, nalondola yotaikayo, kufikira atayipeza?

Luk 15:5 Ndipo pamene ayipeza, ayisenza pa mapewa ake mokondwera.

Luk 15:6 Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nawo, kondwerani ndi ine, chifukwa ndayipeza nkhosa yanga yotayikayo.

Luk 15:7 Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa m’modzi wolapa, koposa anthu wolungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene alibe kusowa kulapa.

Luk 15:8 Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama za siliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m’nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira atayipeza?

Luk 15:9 Ndipo m’mene ayipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndidayipeza ndalama ndidatayayo.

Luk 15:10 Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa m’modzi amene walapa.

Luk 15:11 Ndipo Iye adati, Munthu wina adali ndi ana amuna awiri: (Kuyenda ulendo)

Luk 15:12 Ndipo wam’ng’onoyo adati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye adamugawira za moyo wake.

Luk 15:13 Ndipo pakupita masiku wowerengeka mwana wam’ng’ono adasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake ku dziko lakutali; ndipo komweko adamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko. ( Umphawi wa kudziko lakutali )

Luk 15:14 Ndipo pamene adatha zake zonse, padakhala njala yayikulu m’dziko muja, ndipo iye adayambakusowa.

Luk 15:15 Ndipo adapita nadziphatikiza kwa mfulu imodzi yadziko lija; ndipo uyu adamtumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba.

Luk 15:16 Ndipo adalakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu adam’ninkha kanthu. (Kulapa)

Luk 15:17 Koma pamene adakumbukira mumtima, adati, Antchito wolipidwa ambiri wa atate wanga, ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndiwonongeke kuno ndi njala?

Luk 15:18 Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndidachimwira kumwamba ndi pamaso panu.

Luk 15:19 Ndipo sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati m’modzi wa antchito anu.

Luk 15:20 Ndipo iye adanyamuka, nadza kwa atate wake, koma pakudza iye kutali, atate wake adamuwona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsopsonetsa.

Luk 15:21 Ndipo mwanayo adati kwa iye, Atate ndidachimwira kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.

Luk 15:22 Koma atateyo adati kwa atumiki ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumbveke; ndipo mpatseni mphete ku dzanja lake ndi nsapato ku mapazi ake; ( Chisangalalo )

Luk 15:23 Ndipo idzani naye mwana wa ng’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere.

Luk 15:24 Chifukwa mwana wanga uyu adali wokufa, ndipo tsopano wakhala ndi moyo. Ndipo adayamba kusekera. ( Mfarisi )

Luk 15:25 Koma mwana wake wamkulu adali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, adamva kuyimba ndi kubvina.

Luk 15:26 Ndipo iye adayitana m’modzi wa mtumiki, namfunsa, zinthu izi nzotani?

Luk 15:27 Ndipo iye adati kwa iye, M’ng’ono wako wafika; ndipo atate wako adapha mwana wa ng’ombe wonenepa, chifukwa adamlandira iye wamoyo.

Luk 15:28 Koma iye adakwiya ndipo sadafuna kulowanso. Ndipo atate wake adatuluka namdandaulira.

Luk 15:29 Koma iye adayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndidakhala mtumiki wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindidalakwira lamulo lanu nthawi ili yonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga.

Luk 15:30 Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha za moyo zanu ndi akazi achiwerewere, mudamphera iye mwana wa ng’ombe wonenepa.

Luk 15:31 Koma iye adanena naye, Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthawi zonse, ndipo zanga zonse ziri zako.

Luk 15:32 Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwera: chifukwa m’ng’ono wako uyu adali wakufa ndipo ali ndi moyo; adatayika, ndipo wapezeka.



16

Luk 16:1 Ndipo Iye adanenanso kwa wophunzira ake, padali munthu mwini chuma, adali ndi kapitawo wake; ndipo ameneyu adanenezedwa kwa iye kuti adali kumwaza chuma chake.

Luk 16:2 Ndipo adamuyitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitawo wako, pakuti sungathe kukhalabe kapitawo.

Luk 16:3 Ndipo kapitawo uyu adati mumtima mwake, ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga wandichotsera ukapitawo? Kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi.

Luk 16:4 Ndidziwa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene anditulutsa mu ukapitawo, anthu akandilandire kunyumba kwawo.

Luk 16:5 Ndipo adadziyitanira m’modzi ndi m’modzi amangawa onse a mbuye nati kwa woyamba, udakongola chiyani kwa mbuye wanga?

Luk 16:6 Ndipo adati, mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye adanena naye, tenga, nukhale pansi msanga, nulembere, makumi asanu.

Luk 16:7 Pomwepo adati kwa wina, ndipo iwe uli nawo mangawa wotani? Ndipo uyu adati; Mitanga ya tirigu zana. Iye adanena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu.

Luk 16:8 Ndipo mbuye wake adatama kapitawo wonyengayo, kuti adachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m’mbadwo wawo koposa ana a kuwunika.

Luk 16:9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani; iwo akalandire inu m’mahema wosatha.

Luk 16:10 Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m’chaching’ono alinso wosalungama m’chachikulu.

Luk 16:11 Chifukwa chake ngati simukhala wokhulupirika m’chuma chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma chowona?

Luk 16:12 Ndipo ngati simudakhala wokhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?

Luk 16:13 Palibe m’mtumiki wa m’nyumba akhoza kukhala mtumiki wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina; nadzakonda winayo kapena adzakangamira winayo; nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala mtumiki wa Mulungu ndi wa chuma.

Luk 16:14 Koma Afarisi, ndiwo wokonda ndalama, adamva izi zonse; ndipo adamseka Iye.

Luk 16:15 Ndipo Iye adati kwa iwo, Inu ndinu wodziyesera nokha wolungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa chake ichi chimene chilemekezedwa koposa pakati pa anthu ndi chonyansa pamaso pa Mulungu.

Luk 16:16 Chilamulo ndi aneneri adalipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu ali yense akangamira kulowamo.

Luk 16:17 Kuti Kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang’ono kachilamulo kagwe nkwapatali.

Luk 16:18 Aliyense wosudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.

Luk 16:19 Ndipo padali munthu mwini chuma amabvala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse:

Luk 16:20 Ndipo padali wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adayikidwa pachipata pake wodzala ndi zilonda,

Luk 16:21 Ndipo adafuna kukhuta ndi zakugwa pagome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zironda zake;

Luk 16:22 Ndipo kudali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti adatengedwa iye ndi angelo kupita ku chifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, nayikidwa m’manda.

Luk 16:23 Ndipo m’gehena adakweza maso ake, pokhala nawo mazunzo, nawona Abrahamu patali, ndi Lazaro m’chifukwa mwake.

Luk 16:24 Ndipo adakweza mawu nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti abviyike msonga ya chala chake m’madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m’lawi ili lamoto.

Luk 16:25 Koma Abrahamu adati, Mwana, kumbukira kuti udalandira zokoma zako pakukhala m’moyo iwe, momwemonso Lazaro zoyipa; ndipo tsopano iye atonthozedwa pano, koma iwe uzunzidwadi.

Luk 16:26 Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo wofuna kuwoloka kuchokera kuno kupita kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife sangathenso.

Luk 16:27 Koma iye adati, pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga;

Luk 16:28 Pakuti ndiri nawo abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze ku malo ano a mazunzo.

Luk 16:29 Abrahamu adati; Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.

Luk 16:30 Koma iye adati, Iyayi, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa akufa adzalapa.

Luk 16:31 Koma adati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akawuka kwa akufa.



17

Luk 17:1 Ndipo adati Iye kwa wophunzira ake, sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo.

Luk 17:2 Ndi kwabwino kwa iye kukolowekedwa mwala wa mphero m’khosi mwake ndi kuponyedwa iye m’nyanja nkwapafupi koposa, kukhumudwitsa m’modzi wa ang’ono awa.

Luk 17:3 Kadzichenjerani akachimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire.

Luk 17:4 Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; Udzimkhululukira.

Luk 17:5 Ndipo atumwi adati kwa Ambuye, wonjezerani chikhulupiriro chathu.

Luk 17:6 Koma Ambuye adati ngati, Mukadakhala nacho chikhulupiriro ngati kambewu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wa mkuyu, Uzulidwe, nuwokedwe m’nyanja; ndipo ukadamvera inu.

Luk 17:7 Koma ndani mwa inu ali naye mtumiki wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi udye;

Luk 17:8 Wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe?

Luk 17:9 Kodi ayamika mtumikiyo chifukwa kuti adachita molamulidwa sindinganiza choncho?

Luk 17:10 Chotero inunso m’mene mutachita zonse zimene adakulamulirani, nenani, Ife ndife atumiki wosapindula tangochita zimene tayenera kuzichitazo.

Luk 17:11 Ndipo kudali, popita ku Yerusalemu Iye adalikudutsa pakati pa Samariya ndi Galileya.

Luk 17:12 Ndipo m’mene adalowa Iye m’mudzi wina, adakomana naye amuna khumi akhate, amene adayima kutali;

Luk 17:13 Ndipo iwo adakweza mawu, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire ife chifundo.

Luk 17:14 Ndipo pakuwawona adati kwa iwo, Pitani, kadziwonetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kudali, m’kupita kwawo, adakonzedwa.

Luk 17:15 Ndipo m’modzi wa iwo, pakuwona kuti adachiritsidwa, adabwerera m’mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mawu akulu;

Luk 17:16 Ndipo adagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo adali Msamariya ameneyo.

Luk 17:17 Ndipo Yesu adayankha nati, Kodi sadakonzedwa khumi? Koma ali kuti asanu ndi anayi aja?

Luk 17:18 Sadapezeka wobwera kudzalemekeza Mulungu koma mulendo uyu yekha.

Luk 17:19 Ndipo adati kwa iye, Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.

Luk 17:20 Ndipo pamene Afarisi adamfunsa Iye, kuti Ufumu wa Mulungu ukudza liti; adawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi mawonekedwe;

Luk 17:21 Ndipo sadzanena, Tawonani uwu, kapena uwo! Pakuti, tawonani, Ufumu wa Mulungu uli m’kati mwa inu.

Luk 17:22 Ndipo Iye adati kwa wophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuwona limodzi la masiku a mwana wa munthu, koma simudzaliwona ilo.

Luk 17:23 Ndipo adzanena ndi inu, Tawonani ilo! Tawonani ili! Musachoka kapena kuwatsata.

Luk 17:24 Pakuti monga mphezi ing’anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niwunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa munthu m’tsiku lake.

Luk 17:25 Koma ayenera ayambe wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi m’badwo uno

Luk 17:26 Ndipo monga kudakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu.

Luk 17:27 Anadya adamwa, adakwatira, adakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa adalowa m’chombo, ndipo chinadza chigumula, nichiwawononga onsewo.

Luk 17:28 Monga momwenso kudakhala masiku a Loti; anadya, adamwa, anagula adagulitsa, adadzala, adamanga nyumba;

Luk 17:29 Koma tsiku limene Loti adatuluka m’Sodoma udabyumbwa moto ndi Sulfure zochokera kumwamba, ndipo zidawawononga onsewo.

Luk 17:30 Momwemo kudzakhala tsiku lakubvumbuluka Mwana wa munthu.

Luk 17:31 Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa denga, ndi akatundu ake m’nyumba, asatsike kukatenga; ndipo iye amene ali m’munda chimodzimodzi asabwere ku zake za m’mbuyo.

Luk 17:32 Kumbukirani mkazi wa Loti.

Luk 17:33 Iye ali yense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye ali yense adzautaya, adzausunga.

Luk 17:34 Ndinena ndi inu, usiku womwewo anthu adzakhala awiri pakama m’modzi; m’modzi adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.

Luk 17:35 Padzakhala akazi awiri wopera pamodzi, m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

Luk 17:36 Padzakhala amuna awiri m’munda; m’modzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.

Luk 17:37 Ndipo iwo adayankha nanena kwa Iye, kuti Ambuye? Ndipo adati kwa iwo kumene kulikonse kuli mtembo, pomweponso mbalame za miyimba zidzasonkhana.



18

Luk 18:1 Ndipo adawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafoka mtima;

Luk 18:2 Nanena, mumzinda mwa kuti mudali woweruza wosawopa Mulungu ndi wosasamala munthu.

Luk 18:3 Ndipo m’mumzinda mudali mkazi wa masiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane.

Luk 18:4 Ndipo sadafuna pa nthawiyo; koma bwino bwino adati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusasamala munthu;

Luk 18:5 Koma chifukwa cha kundibvuta ine mkazi wa masiye ameneyu ndidzamuweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kubwerabwera kwake.

Luk 18:6 Ndipo Ambuye adati; Tamverani chonena woweruza wosalungama.

Luk 18:7 Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo wosankhidwa ake akumuyitana usana ndi usiku popeza aleza nawo mtima?

Luk 18:8 Ndinena ndi inu, Adzawachitira chilungamo mwachangu. Koma mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?

Luk 18:9 Ndipo adatinso kwa ena amene adadzikhulupirira mwa iwo wokha kuti adali wolungama, napeputsa onse ena:

Luk 18:10 Anthu awiri adakwera kupita kukachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mzake wamsonkho.

Luk 18:11 Mfarisi adayimilira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena, wopambapamba, wosalungama, achigololo, kapenanso monga wa msonkho uyu.

Luk 18:12 Ndimasala chakudya kawiri Sabata limodzi, ndimapereka limodzi la magawo khumi la zonse ndiri nazo.

Luk 18:13 Koma wamsonkhoyo adayima patali sadafuna kungakhale kukweza maso Kumwamba, komatu adadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu mundichitire chifundo, ine wochimwa.

Luk 18:14 Ndinena ndi inu, Munthu uyu adatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama osati uja ayi: pakuti yense wodzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.

Luk 18:15 Ndipo adadza nawo kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene wophunzira adawona, adawadzudzula.

Luk 18:16 Koma Yesu adawayitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa wotere.

Luk 18:17 Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.

Luk 18:18 Ndipo mkulu wina adamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha?

Luk 18:19 Koma Yesu adati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji, palibe wabwino, koma m’modzi, ndiye Mulungu.

Luk 18:20 Udziwa malamulo Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.

Luk 18:21 Ndipo adati, Izi zonse ndazisunga kuyambira pa ubwana wanga.

Luk 18:22 Tsopano pamene Yesu adamva izi, adati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi; gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma cheni cheni m’Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

Luk 18:23 Koma pamene adamva izi adagwidwa ndi chisoni chambiri; pakuti adali nacho chuma chambiri.

Luk 18:24 Ndipo Yesu pomuwona iye kuti adali ndi chisoni, Iye adati Ha! Nkobvuta kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu!

Luk 18:25 Pakuti nkwapafupi kwa ngamila ipyole pa diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.

Luk 18:26 Koma akumvawo adati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa?

Luk 18:27 Ndipo Iye adati, zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.

Luk 18:28 Pamenepo Petro adati, Tawonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu.

Luk 18:29 Koma adati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum’bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu.

Luk 18:30 Koma adzalandira zobwezedwa koposatu m’nthawi yino; ndipo m’nthawi ili nkudza moyo wosatha.

Luk 18:31 Ndipo adadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Tawonani, tikwera kumka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.

Luk 18:32 Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malobvu.

Luk 18:33 Ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo pa tsiku la chitatu adzawukanso.

Luk 18:34 Ndipo sadadziwitsa kanthu ka izi: ndi mawu awa adawabisikira ndipo sadazindikira zonenedwazo.

Luk 18:35 Ndipo kunali pamene adayandikira ku Yeriko, msawona wina adakhala m’mbali mwa njira, napemphapempha:

Luk 18:36 Ndipo pakumva khamu la anthu alimkupita, adafunsa; Ichi nchiyani?

Luk 18:37 Ndipo adamuwuza iye, Yesu wa ku Nazarete ali kudutsa apa.

Luk 18:38 Ndipo adafuwula, nanena, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo.

Luk 18:39 Ndipo iwo wotsogolera adamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye adafuwulitsa kwambiri, Mwana wa Davide, Mundichitire ine chifundo.

Luk 18:40 Ndipo Yesu adayima, nalamulira kuti abwere naye kwa Iye; ndipo m’mene adafika pafupi, adamfunsa iye,

Luk 18:41 Nanena, ufuna ndikuchitire chiyani? Ndipo iye adati, Ambuye, kuti ndipenyenso.

Luk 18:42 Ndipo Yesu adati kwa iye, penyanso: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.

Luk 18:43 Ndipo pomwepo adapenyanso, namtsata Iye, nalemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuwona, adachitira Mulungu mayamiko.



19

Luk 19:1 Ndipo Yesu adalowa, napyola pa Yeriko.

Luk 19:2 Ndipo tawonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyu; ndipo iye adali mkulu wa amisonkho, adali wachuma.

Luk 19:3 Ndipo adafuna kuwona Yesu ndiye uti, ndipo sadathe, chifukwa cha kupanikizana, pakuti adali wamfupi msinkhu.

Luk 19:4 Ndipo adathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuwona Iye; pakuti adati apita njira yomweyo.

Luk 19:5 Ndipo m’mene anadza pamalopo Yesu adakweza maso nati kwa iye, Zakeyu, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m’nyumba mwako.

Luk 19:6 Ndipo adafulumira, natsika, namlandira Iye wokondwera.

Luk 19:7 Ndipo m’mene adachiwona adang`ung`udza onse, nanena, Adalowa amchereze munthu ali wochimwa.

Luk 19:8 Ndipo Zakeyu adayimilira nati kwa Ambuye, Tawonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndidalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndidzambwezera kanayi.

Luk 19:9 Ndipo Yesu adati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.

Luk 19:10 Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.

Luk 19:11 Ndipo pakumva izi iwo, Iye adawonjeza nanena fanizo, chifukwa adali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo adayesa kuti Ufumu wa Mulungu udzawonekera pomwepo .

Luk 19:12 Pamenepo Iye adati, Munthu wa fuko lomveka adamka ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.

Luk 19:13 Ndipo adayitana atumiki ake khumi, nati kwa iwo, chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.

Luk 19:14 Koma mfulu za pa mudzi pake zidamuda, nizituma akazembe amtsate m’mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyu akhale mfumu yathu.

Luk 19:15 Ndipo kunali pakubwera iye, atalandira ufumuwo, adati ayitanidwe kwa iye atumiki aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo adapindulira pochita malonda.

Luk 19:16 Ndipo adafika woyamba, nanena, Mbuye ndalama yanu idachita niwonjeza ndalama khumi.

Luk 19:17 Ndipo adati kwa iye, Chabwino mtumiki wa bwino iwe; popeza udakhala wokhulupirika m’chaching’ono, khala nawo ulamuliro pa mizinda khumi.

Luk 19:18 Ndipo adadza wachiwiri, nanena, Mbuye ndalama yanu yapindula ndalama zisanu.

Luk 19:19 Ndipo adati kwa iyenso, khala iwenso woweruza mizinda isanu.

Luk 19:20 Ndipo wina adadza, nanena, Mbuye, tawonani, siyi ndalama yanu, ndayisunga m’kasalu:

Luk 19:21 Pakuti ndidakuwopani, popeza inu ndinu munthu wowuma mtima: munyamula chimene simudachiyika pansi, mututa chimene simudachifesa.

Luk 19:22 Ndipo adanena kwa iye, Pakamwa pako ndi kuweruza, mtumiki woyipa iwe, udadziwa kuti ine ndine munthu wowuma mtima, wonyamula chimene sindidachiyimika, ndi wotuta chimene sindidachifesa;

Luk 19:23 Ndipo sudapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadayitenga ndi phindu lake?

Luk 19:24 Ndipo adati kwa iwo akuyimilirapo, Mchotsereni ndalamayo, nimupatse iye wokhala nazo ndalama khumi.

Luk 19:25 Ndipo iwo adati kwa Iye, Ambuye, ali nazo ndalama khumi.

Luk 19:26 Ndinena ndi inu, kuti yense wokhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa.

Luk 19:27 Koma adani anga aja wosafuna kuti ndidzakhale mfumuyawo, bwerani nao kuno nimuwaphe pamaso panga.

Luk 19:28 Ndipo m’mene adanena izi adawatsogolera nakwera kumka ku Yerusalemu.

Luk 19:29 Ndipo kudali, m’mene Iye adayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lotchedwa la Azitona, adatuma awiri a wophunzira ake.

Luk 19:30 Nanena, Pitani ku mudzi uli pandunji panu; m’menemo, polowa, mudzapeza mwana wabulu womangidwa, pamenepo palibe munthu adakwerapo nthawi ili yonse; mum’masule iye nimubwere naye.

Luk 19:31 Ndipo munthu akati kwa inu, mum’masuliranji? Mudzatero naye, Ambuye amfuna iye.

Luk 19:32 Ndipo adachoka wotumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo.

Luk 19:33 Ndipo pamene adamasula mwana wa bulu, eni ake adati kwa iwo, Mum’masuliranji mwana wa bulu?

Luk 19:34 Ndipo iwo adati, Ambuye amfuna iye.

Luk 19:35 Ndipo adadza naye kwa Yesu; ndipo adayalika zobvala zawo pa mwana wabuluyo, nakwezapo Yesu.

Luk 19:36 Ndipo pakupita Iye, adayala zobvala zawo m’njira.

Luk 19:37 Ndipo poyandikira Iye tsono potsetsereka pake pa phiri la Azitona, khamu lonse la wophunzira lidayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mawu akulu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu adaziwona;

Luk 19:38 Nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m’dzina la Ambuye; mtendere m’Mwamba, ndi ulemerero m’Mwambamwamba.

Luk 19:39 Ndipo Afarisi ena a m’khamu la anthu adati kwa Iye, Mphunzitsi, dzudzulani wophunzira anu.

Luk 19:40 Ndipo Iye adayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa akhala chete miyala idzafuwula pomwepo.

Luk 19:41 Ndipo m’mene adayandikira, adawona mzindawo nawulirira.

Luk 19:42 Nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.

Luk 19:43 Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;

Luk 19:44 Ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala umodzi pa umzake; popeza sudazindikira nyengo yakuyenderedwa kwako.

Luk 19:45 Ndipo Iye adalowa m’kachisi, nayamba kutulutsa iwo akugulitsa ndi kugula malonda;

Luk 19:46 Nanena kwa iwo, Kwalembedwa, Nyumba yanga ndi nyumba yakupemphereramo; koma inu mwayiyesa iyo phanga la achifwamba.

Luk 19:47 Ndipo adalikuphunzitsa m’kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe akulu, ndi alembi ndi akulu a anthu adafunafuna njira yomuwonongera Iye;

Luk 19:48 Ndipo sadapeza chimene adzamchitira: pakuti anthu onse adali ndi chidwi pakumva Iye.



20

Luk 20:1 Ndipo kudali lina la masiku awo m’mene Iye adalikuphunzitsa anthu m’kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe akulu ndi alembe adadza kwa Iye.

Luk 20:2 Ndipo iwo adati kwa Iye, nanena, Mutiwuze muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene adakupatsani ulamuliro umenewu?

Luk 20:3 Ndipo Iye adayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani Inenso chinthu chimodzi mundiwuze.

Luk 20:4 Ubatizo wa Yohane udachokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu?

Luk 20:5 Ndipo adakambirana mwa wokha, nanena, Ngati tinena udachokera Kumwamba; adzati, simudamkhulupilira chifukwa ninji?

Luk 20:6 Ndiponso ngati tikanena, Udachokera kwa anthu, anthu onse adzatiponya miyala; pakuti adakopeka mtima, kuti Yohane adali m’neneri.

Luk 20:7 Ndipo iwo adayankha kuti sitikuwuzani kumene udachokera.

Luk 20:8 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Ndingakhale Inenso sindikuwuzani za ulamuliro umene ndichita zinthu izi.

Luk 20:9 Ndipo Iye adayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu wina adalima munda wa mphesa, nawukongoletsa kwa wolima munda, napita kudziko lakutali nagonerako nthawi yayikulu.

Luk 20:10 Ndipo pa nyengo ya zipatso adatumiza mtumiki wake kwa wolima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo: koma wolimawo adampanda, nambweza wopanda kanthu.

Luk 20:11 Ndipo adatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso adampanda, namchitira chipongwe, nambweza, wopanda kanthu.

Luk 20:12 Ndipo adatumizanso wina wa chitatu; ndipo iyenso adamvulaza, namtaya kunja.

Luk 20:13 Ndipo adati mwini mundawo, Ndidzachita chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga amene ndikondana naye; kapena adzamchitira iye ulemu.

Luk 20:14 Koma wolimawo, pamene adamuwona, adawuzana wina ndi mzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba, tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu.

Luk 20:15 Ndipo adamponya kunja kwa mundawo, namupha. Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawachitira chiyani?

Luk 20:16 Iye adzafika nadzawononga wolima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo adamva, adati Mulungu asatero!

Luk 20:17 Koma Iye adawapenyetsetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chidalembedwa, Mwala umene womanga nyumba adawukana, womwewo udakhala mutu wa pangodya.

Luk 20:18 Munthu ali yense wakugwa pa mwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupera ngati ufa.

Luk 20:19 Ndipo alembi ndi ansembe akulu adafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo adawopa anthu; pakuti adazindikira kuti adanenera pa iwo fanizo ili.

Luk 20:20 Ndipo adamyang’anira, natumiza wozonda, amene adadziwonetsera ngati wolungama mtima, kuti akamkole pa mawu ake, kotero kuti akampereke Iye kwa akulu ndi aulamuliro wa kazembe.

Luk 20:21 Ndipo adamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu kowonadi.

Luk 20:22 Kodi mkuloledwa kwa ife kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?

Luk 20:23 Koma Iye adazindikira Chinyengo chawo, nati kwa iwo, chifukwa chiyani mukundiyesa?

Luk 20:24 Tandiwonetsani Ine khobiri. Chithunzithunzi ndi cholemba chake nchayani? Adati iwo, cha Kayisala.

Luk 20:25 Ndipo Iye adati kwa iwo, chifukwa chake perekani kwa Kayisala zake za Kayisala, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.

Luk 20:26 Ndipo sadakhoza kugwira mawuwo pamaso pa anthu; ndipo adazizwa ndi kuyankha kwake, nakhala chete.

Luk 20:27 Ndipo anadza kwa Iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuwuka kwa akufa; ndipo adamfunsa Iye,

Luk 20:28 Nanena, Mphunzitsi, Mose adatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale wake adzakwatira mkaziyo, nadzamuwukitsira mbale wake mbewu.

Luk 20:29 Tsono padali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba adakwatira mkazi , nafa wopanda mwana;

Luk 20:30 Ndipo wachiwiri adamkwatira mkaziyo, nafa, nasiya wopanda mwana,,

Luk 20:31 Ndipo wachitatu adamtenga mkaziyo; ndipo choteronso asanu ndi awiri onse, sadasiya mwana, namwalira.

Luk 20:32 Pomalizira adamwaliranso mkaziyo.

Luk 20:33 Chotero pa kuwuka kwa akufa iye adzakhala mkazi wayani wa iwo? Pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye.

Luk 20:34 Ndipo Yesu adati kwa iwo, Ana adziko lapansi akwatira nakwatiwa:

Luk 20:35 Koma iwo akuyesedwa woyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuwuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa:

Luk 20:36 Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuwuka kwa akufa.

Luk 20:37 Tsopano popeza akufa awuka, adasonyeza ngakhale Mose, pa chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.

Luk 20:38 Pakuti Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.

Luk 20:39 Ndipo alembi ena adayankha nati, Mphunzitsi, mwanena bwino.

Luk 20:40 Pakuti sadalimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu kena.

Luk 20:41 Koma Iye adati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristuyo ndiye Mwana wa Davide?

Luk 20:42 Pakuti Davide yekha anena m’buku la Masalmo, Ambuye adanena kwa Ambuye wanga, khala padzanja langa lamanja.

Luk 20:43 Kufikira Ine ndidzayika adani ako pansi pa mapazi ako.

Luk 20:44 Chotero Davide adamtchula Iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wake bwanji?

Luk 20:45 Ndipo pamene anthu onse adalimkumva Iye, adati kwa wophunzira.

Luk 20:46 Chenjerani nawo alembi, amene afuna kuyendayenda wobvala miyinjiro, nakonda kuyankhulidwa m’misika, ndi mipando ya ulemu m`masunagoge ndi zipinda za ulemu m`maphwando;

Luk 20:47 Amene awononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa.



21

Luk 21:1 Ndipo Yesu adakweza maso, nawona anthu eni chuma alikuyika zopereka zawo mosungiramo ndalama.

Luk 21:2 Ndipo adawona mkazi wina wamasiye waumphawi akuyika momwemo timakobiri tiwiri.

Luk 21:3 Ndipo Iye adati, Zowonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi adayikamo koposa onse;

Luk 21:4 Pakuti onse amenewa adayika mwa unyinji wawo pa zoperekazo; koma Iye mwa kusowa kwake adayikamo za moyo wake, zonse adali nazo.

Luk 21:5 Ndipo pamene ena adalikunena za kachisiyo, kuti adakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, adati Iye,

Luk 21:6 Zinthu izi mukuziwona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala umzake, umene sudzagwetsedwa.

Luk 21:7 Ndipo iwo adamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzawoneka liti? Ndipo chizindikiro chake ndi chiyani pamene izi ziti zidzachitike?

Luk 21:8 Ndipo Iye adati, Yang’anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m’dzina langa, nadzanena, Ndine Khristu ndipo, nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pawo.

Luk 21:9 Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mipanduko, musawopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.

Luk 21:10 Pamenepo Iye adanena kwa iwo, Mtundu wa anthu udzawukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina:

Luk 21:11 Ndipo kudzakhala zibvomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akuti akuti, ndipo kudzakhala zowopsa ndi zizindikiro zazikulu zochokera kumwamba.

Luk 21:12 Koma zisadachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzapita nanu kwa mafumu ndi akazembe chifukwa cha dzina langa.

Luk 21:13 Ndipo kudzakhala kwa inu ngati umboni.

Luk 21:14 Chifukwa chake tsimikizani mumtima mwanu, kuti usadafike mlandu musalingilire chimene mudzayankha.

Luk 21:15 Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.

Luk 21:16 Ndipo mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi afuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani.

Luk 21:17 Ndipo anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa.

Luk 21:18 Ndipo silidzawonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.

Luk 21:19 Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiliro.

Luk 21:20 Koma pamene pali ponse mudzawona, Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a nkhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira.

Luk 21:21 Pamenepo iwo ali m’Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumilaga asalowemo.

Luk 21:22 Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zikwaniritsidwe.

Luk 21:23 Koma tsoka iwo akukhala ndi mwana ndi akuyamwitsa masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.

Luk 21:24 Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kumka ku mitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza kufikira kuti nthawi zawo za anthu akunja zakwanira .

Luk 21:25 Ndipo kudzakhala zizindikiro padzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkokomo wake pa nyanja ndi mafunde ake;

Luk 21:26 Anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirimkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.

Luk 21:27 Ndipo pamenepo adzawona Mwana wa munthu alimkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Luk 21:28 Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.

Luk 21:29 Ndipo adanena nawo fanizo; Onani mtengo wa mkuyu ndi mitengo yonse;

Luk 21:30 Pamene iphuka, muyipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo.

Luk 21:31 Inde, chotero inunso pakuwona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.

Luk 21:32 Indetu ndinena ndi inu, M`bado uno sudzapitirira, kufikira zonse zitakwaniritsidwa.

Luk 21:33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mawu anga sadzapita.

Luk 21:34 Koma mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyayidya ndi kuledzera ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa.

Luk 21:35 Pakuti ngati msampha lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi.

Luk 21:36 Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera nthawi zonse, kuti inu mudzayesedwa woyenera ndi kupulumuka kuzinthu izi zonse zimene zidzachitika, ndi kuyimilira pamaso pa Mwana wa Munthu.

Luk 21:37 Ndipo usana uli wonse Iye adalikuphunzitsa m’kachisi; ndi usiku uli wonse adatuluka, nagona pa phiri lotchedwa la Azitona.

Luk 21:38 Ndipo anthu onse adalawira m`mamawa kudza kwa Iye ku kachisi kudzamvera Iye.



22

Luk 22:1 Tsopano phwando la mikate yopanda chotupitsa lidayandikira, ndilo lotchedwa Paskha.

Luk 22:2 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adafunafuna njira yomuphera Iye chifukwa adawopa anthuwo.

Luk 22:3 Pamenepo Satana adalowa mwa Yudase wonenedwa Isikariyote, amene adawerengedwa m’modzi wa khumi ndi awiriwo.

Luk 22:4 Ndipo iye adachoka nayankhulana ndi ansembe akulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo.

Luk 22:5 Ndipo adakondwera, napangana naye kumpatsa Iye ndalama.

Luk 22:6 Ndipo iye adalonjeza, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.

Luk 22:7 Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa lidafika, limene idayenera kuphedwa nsembe ya paskha.

Luk 22:8 Ndipo Iye adatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitani mutikonzere ife Paskha, kuti tidye.

Luk 22:9 Ndipo iwo adanena naye, Mufuna tikakonzere kuti?

Luk 22:10 Ndipo Iye adati kwa iwo, Onani, mutalowa m’mzinda, adzakomana ndi inu munthu atasenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.

Luk 22:11 Ndipo mukanene kwa mwini nyumba wabwinoyo, Mphunzitsi anena nawe, chipinda cha alendo chiri kuti, m’mene ndikadye Paskha pamodzi ndi wophunzira anga?

Luk 22:12 Ndipo iyeyo adzakuwonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko.

Luk 22:13 Ndipo adapita iwo, napeza monga adatero nawo; ndipo adakonza Paskha.

Luk 22:14 Ndipo itadza nthawi yake, Iye adakhala pachakudya, pansi ndi atumwi khumi ndi awiri pamodzi naye.

Luk 22:15 Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndidalakalaka ndithu kudya paskha uyu pamodzi ndi inu, ndisadayambe kusautsidwa.

Luk 22:16 Pakuti ndinena ndi inu, Sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu.

Luk 22:17 Ndipo adatenga chikho, ndipo pamene adayamika, adati; Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha.

Luk 22:18 Pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.

Luk 22:19 Ndipo adatenga mkate, nayamika, adaunyema, nawapatsa, nanena, ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.

Luk 22:20 Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.

Luk 22:21 Koma onani, dzanja lake la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi ine.

Luk 22:22 Pakuti zowonadi Mwana wa munthu amukatu, monga kudayikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka Iye!

Luk 22:23 Ndipo adayamba kufunsana mwa iwo wokha, ndiye yani mwa iwo amene adzachita ichi.

Luk 22:24 Ndipo kudakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu.

Luk 22:25 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, ochitira zabwino.

Luk 22:26 Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wang’ono; ndi iye ali mfumu, akhale ngati wotumikira.

Luk 22:27 Pakuti wamkulu ndani, iye wakukhala pachakudya kapena wotumikirapo? Si ndiye wakukhala pachakudya kodi? Koma Ine ndiri pakati pa inu monga ngati wotumikira.

Luk 22:28 Koma inu ndinu amene mudakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga.

Luk 22:29 Ndipo Ine ndikuyikirani ufumu, monganso Atate wanga adandiyikira Ine,

Luk 22:30 Kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.

Luk 22:31 Ndipo Ambuye adati, Simoni, Simoni, tawona, Satana adafuna akutenge kuti akupete ngati tirigu:

Luk 22:32 Koma ndidakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ulimbikitse abale ako.

Luk 22:33 Ndipo adati kwa Iye, Ambuye ndiri wokonzeka kupita ndi Inu, kundende ndi kuimfa.

Luk 22:34 Ndipo Iye adati, Ndikuwuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine.

Luk 22:35 Ndipo Iye adati kwa iwo, pamene ndidakutumizani wopanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba ndi nsapato, mudasowa kanthu kodi? Ndipo iwo sadanene kanthu.

Luk 22:36 Ndipo pamenepo adati kwa iwo, Koma tsopano iye amene ali ndi thumba la ndalama alitenge, ndi thumba lakamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga.

Luk 22:37 Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwaniritsidwa mwa Ine, Ndipo adawerengedwa ndi anthu wophwanya lamulo; pakuti izi zakwa Ine ziri nacho chimaliziro.

Luk 22:38 Ndipo iwo adati, Ambuye, tawonani, malupanga awiri awa. Ndipo Iye adati kwa iwo, Chakwanira.

Luk 22:39 Ndipo Iye adatuluka, napita monga adafuchita, ku phiri la Azitona; ndipo wophunzira adamtsata Iye.

Luk 22:40 Ndipo pofika pamalopo, adati kwa iwo, pempherani kuti mungalowe m’kuyesedwa.

Luk 22:41 Ndipo adapatukana nawo kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera.

Luk 22:42 Nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.

Luk 22:43 Ndipo adamuwonekera Iye m’ngelo wa Kumwamba namlimbikitsa Iye.

Luk 22:44 Ndipo pokhala Iye m’chipsinjo mtima adapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake lidakhala ngati madontho akulu a mwazi ali mkugwa pansi.

Luk 22:45 Ndipo pamene adanyamuka pakupemphera anadza kwa wophunzira, nawapeza ali m’tulo ndi chisoni.

Luk 22:46 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mugoneranji? Dzukani, pempherani kuti mungalowe m’kuyesedwa.

Luk 22:47 Pamene Iye adali chiyankhulire, tawonani, khamu la anthu, ndipo iye wotchedwa Yudase, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, adawatsogolera; nayandikira Yesu nampsopsona Iye.

Luk 22:48 Koma Yesu adati kwa iye, Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi chimpsopsono kodi?

Luk 22:49 Ndipo m’mene iwo akumzinga Iye adawona chimene chiti chichitike, adati, Ambuye tikanthe ndi lupanga kodi?

Luk 22:50 Ndipo wina wa iwo adakantha mtumiki wa mkulu wa nsembe, namdula khutu lake lamanja.

Luk 22:51 Koma Yesu adayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo adakhudza khutu lake, namchiritsa.

Luk 22:52 Ndipo pamenepo Yesu adati kwa ansembe akulu ndi akapitawo a kachisi, ndi akulu amene anadza kumgwira Iye, mudatuluka ndi malupanga ndi zibonga kodi monga ngati mugwira wachifwamba?

Luk 22:53 Masiku onse, pamene ndidali ndi inu m’kachisi, simudatansa manja anu kundigwira: koma nyengo yino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa m’dima ndi wanu.

Luk 22:54 Ndipo pamenepo adamtenga Iye, napita naye, nalowa m’nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro adamtsata patali.

Luk 22:55 Ndipo pamene adasonkha moto m’kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro adakhala pakati pawo.

Luk 22:56 Ndipo m’dzakazi wina adamuwona iye alikukhala m’kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso adali naye.

Luk 22:57 Koma iye adakana, nati, mkaziwe, Sindimdziwa Iye.

Luk 22:58 Ndipo popita kamphindi, adamuwona wina, nati, Iwenso uli m’modzi wa iwo. Koma Petro adati, Munthu iwe, sindine.

Luk 22:59 Ndipo patapita ngati ola limodzi, wina adanenetsa, kuti, Zowonadi, munthu uyunso adali naye, pakuti ndiye Mgalileya.

Luk 22:60 Koma Petro adati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chiyankhulire tambala adalira.

Luk 22:61 Ndipo Ambuye adapotoloka, nayang’ana Petro. Ndipo Petro adakumbukira mawu a Ambuye, kuti adati kwa iye, Asadalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.

Luk 22:62 Ndipo Petro adatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.

Luk 22:63 Ndipo amuna amene adalikusunga Yesu adam’nyoza Iye, nampanda.

Luk 22:64 Ndipo adamkulunga Iye m’maso nampanda Iye kumaso namfunsa, nati; Nenera wakupanda Iwe ndani?

Luk 22:65 Ndipo zambiri zina adam’nenera Iye, namchitira mwano.

Luk 22:66 Ndipo pamene kudacha, bungwe la akulu a anthu lidasonkhana, ndiwo ansembe akulu ndi alembi; ndipo adapita naye ku bwalo lawo, nanena,

Luk 22:67 Ngati uli Khristu, utiwuze. Ndipo Iye adati kwa iwo, Ndikakuwuzani, simukhulupirira:

Luk 22:68 Ndipo ndikakufunsani kanthu, simundiyankha ndipo simundilola kupita.

Luk 22:69 Koma kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala pa dzanja la manja la mphamvu ya Mulungu.

Luk 22:70 Pamenepo onse adati, Kodi ukutero uli Mwana wa Mulungu? Ndipo Iye adati kwa iwo, Inde munena kuti ndine amene.

Luk 22:71 Ndipo iwo adati, Tifuniranjinso mboni? Pakuti ife tokha tamva m’kamwa mwa Iye mwini.



23

Luk 23:1 Ndipo khamu lonselo lidanyamuka kupita naye kwa Pilato.

Luk 23:2 Ndipo adayamba kum’nenera Iye, kuti, Tidapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Khristu Mfumu.

Luk 23:3 Ndipo Pilato adamfunsa Iye, nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Iye adamyankha nati, Mwatero.

Luk 23:4 Ndipo Pilato adati kwa ansembe akulu ndi makamu a anthu, ndiribe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.

Luk 23:5 Ndipo iwo adawopseza kwambiri nanena kuti, Amasonkhezera anthuwo, naphunzitsa m’Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.

Luk 23:6 Koma pamene Pilato adamva, adanfunsa ngati munthuyu adali M’galileya.

Luk 23:7 Ndipo m’mene adadziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake wa Herode, adamtumiza Iye kwa Herode, amene adali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa.

Luk 23:8 Ndipo Herode, pamene adawona Yesu, adakondwa ndithu; pakuti adayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa adamva zinthu zambiri za Iye; nayembekeza kuwona chozizwitsa china chochitidwa ndi Iye.

Luk 23:9 Ndipo adamfunsa Iye mawu ambiri; koma Iye sadamyankha kanthu.

Luk 23:10 Ndipo ansembe akulu ndi alembi adayimilira, nam’nenera Iye kolimba.

Luk 23:11 Ndipo Herode ndi asilikari ake ankhondo adampeputsa Iye, nam’nyoza, nambveka Iye chofunda chonyezimila, nambwezera kwa Pilato.

Luk 23:12 Ndipo Herode ndi Pilato adachita chibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana.

Luk 23:13 Ndipo Pilato pamene adayitana ansembe akulu, ndi olamulira ndi anthu, kuti asonkhane,

Luk 23:14 Nati kwa iwo, mudadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wopandutsa anthu; ndipo tawonani, Ine ndidamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindidapeza pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mum’nenera Iye:

Luk 23:15 Inde ngakhale Herode yemwe; pakuti iye adambwezera Iye kwa ife; ndipo tawonani, sadachita Iye kanthu koyenera kufa.

Luk 23:16 Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kum’masula Iye.

Luk 23:17 (Popeza kuti amkawamasulira iwo munthu m’modzi pa phwando)

Luk 23:18 Koma iwo onse pamodzi adafuwula, nati, Chotsani munthu uyu, mutimasulire Baraba.

Luk 23:19 Ndiye munthu amene adaponyedwa m’ndende chifukwa cha mpanduko m’mudzi ndi cha kupha munthu.

Luk 23:20 Ndipo Pilato adayankhulanso nawo, nafuna kumasula Yesu.

Luk 23:21 Koma iwo adafuwula, nanena, Mpachikeni, mpachikeni.

Luk 23:22 Ndipo iye adati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu adachita choyipa chanji? Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kum’masula.

Luk 23:23 Koma adamkakamiza ndi mawu wokweza, napempha kuti Iye apachikidwe. Ndipo ndi mawu awo, mawu akulu a nsembe adalakika.

Luk 23:24 Ndipo Pilato adaweruza kuti chimene adali kufunsa chichitidwe.

Luk 23:25 Ndipo adawamasulira amene adaponyedwa m’ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo, adampempha; koma adapereka Yesu mwa chifuniro chawo.

Luk 23:26 Ndipo popita naye, adagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikuchokera kumidzi, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.

Luk 23:27 Ndipo udamtsata unyinji wa ukulu a anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pachifuwa, namlirira Iye.

Luk 23:28 Koma Yesu adawapotolokera iwo nati, Ana akazi inu aku Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.

Luk 23:29 Chifukwa tawonani masiku alimkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.

Luk 23:30 Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, bisani ife.

Luk 23:31 Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?

Luk 23:32 Ndipo adalinso awiri ena, ndiwo wochita zoyipa, adatengedwa pamodzi ndi Iye kuti aphedwe.

Luk 23:33 Ndipo pamene adafika ku malo dzina lake Kalivari, adampachika Iye pamtanda pomwepo, ndi wochita zoyipa omwe, m’modzi ku dzanja lamanja ndi wina kulamanzere.

Luk 23:34 Ndipo Yesu adanena, Atate muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo adagawana zobvala zake, poyesa mayere.

Luk 23:35 Ndipo anthu amene adayima adalikupenya. Ndi akulunso adamlalatira Iye, nanena, Adapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.

Luk 23:36 Ndipo asilikalinso adamnyoza, nadza kwa Iye nampatsa vinyo wosasa.

Luk 23:37 Nanena, ngati Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha.

Luk 23:38 Ndipo lembo lidalembedwa m`malembedwe a Chigriki, Latini ndi Chi Hebri pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA.

Luk 23:39 Ndipo m’modzi wa wochita zoyipa adapachikidwawo adamchitira Iye mwano nanena , Ngati uli Khristu Iwe: Udzipulumutse wekha ndi ife.

Luk 23:40 Koma winayo adayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suwopa Mulungu, powona uli m’kulangika komweku?

Luk 23:41 Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tirikulandira zoyenera zimene tidazichita: koma munthu uyu sadachita kanthu kolakwa.

Luk 23:42 Ndipo iye adati kwa Yesu, Ambuye, mundikumbukire pamene mukudza mu Ufumu wanu.

Luk 23:43 Ndipo Yesu adanena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m’Paradayiso.

Luk 23:44 Ndipo ola lake pamenepo lidali ngati lachisanu ndi chimodzi: ndipo padali m’dima padziko lonse kufikira ola la chisanu ndi chinayi;

Luk 23:45 Ndipo dzuwa linada, ndipo chinsalu chotchinga cha m’kachisi chadang’ambika pakati.

Luk 23:46 Ndipo pamene Yesu adafuwula ndi mawu akulu, adati, Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo atanena motero, adapereka mzimu wake.

Luk 23:47 Ndipo pamene Kenturiyo adawona chidachitikacho, adalemekeza Mulungu nanena, Zowonadi munthu uyu adali wolungama.

Luk 23:48 Ndipo makamu onse adasonkhana kudzapenya ichi, pamene adawona zidachitikazo, adapita kwawo ndi kudziguguda pachifuwa.

Luk 23:49 Ndipo womdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, adayima kutali, nawona zinthu izi.

Luk 23:50 Ndipo tawonani, padali munthu dzina lake Yosefe, ndiye mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama:

Luk 23:51 (Amene sadabvomereza kuweruza kwawo ndi ntchito yawo) wa ku Arimateya, muzinda wa Ayuda ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu.

Luk 23:52 Iyeyu adapita kwa Pilato napempha mtembo wake wa Yesu.

Luk 23:53 Ndipo adawutsitsa, naukulunga m’salu ya bafuta, nawuyika m’manda wosemedwa m’mwala, m’menemo sadayika munthu ndi kale lonse.

Luk 23:54 Ndipo tsiku limenero lidali lokonzekera, ndipo sabata lidayandikira.

Luk 23:55 Ndipo akazi, amene adachokera naye ku Galileya, adamtsata m’mbuyo, nawona manda, ndi mayikidwe a mtembo wake.

Luk 23:56 Ndipo adapita kwawo, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa sabata adapumula monga mwa lamulo.



24

Luk 24:1 Koma tsiku loyamba la sabata, m’banda kucha, anadza kumanda atatenga zonunkhira zimene adazikonza ndi ena pamodzi nawo.

Luk 24:2 Ndipo adapeza mwala utakunkhunizidwa kuuchotsa pamanda.

Luk 24:3 Ndipo m’mene adalowa sadapezamo mtembo wa Ambuye Yesu.

Luk 24:4 Ndipo kudali, m’mene adathedwa nzeru nacho, tawonani amuna awiri adayimilira pafupi pawo atabvala zonyezimira:

Luk 24:5 Ndipo m’mene adakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zawo, adati kwa iwo, Mufuniranji wa moyo pakati pa akufa?

Luk 24:6 Iye kulibe kuno, koma wawuka Iye, komatu kumbukirani muja adayankhula nanu, pamene adali m’Galileya,

Luk 24:7 Ndi kunena kuti Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m’manja a anthu wochimwa, ndi kupachikidwa, ndi kuwuka tsiku lachitatu.

Luk 24:8 Ndipo adakumbukira mawu ake.

Luk 24:9 Ndipo anabwerera kuchokera kumanda nafotokonzera zonse khumi ndi m’modziyo, ndi wotsala onse.

Luk 24:10 Koma padali Mariya wa Magadala, ndi Jowana, ndi Mariya amake a Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nawo amene adanena izi kwa atumwiwo.

Luk 24:11 Ndipo mawu awo adawoneka pamaso pawo ngati nkhani chabe, ndipo sadawakhulupirire iwo.

Luk 24:12 Koma Petro adanyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama adawona nsalu zoyera pazokha; ndipo adachoka napita kwawo, nazizwa ndi chija chidachitikacho.

Luk 24:13 Ndipo tawonani, awiri a mwa iwo adali kupita tsiku lomwelo ku mudzi dzina lake Emawu, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi.

Luk 24:14 Ndipo adali kukambirana nkhani za izi zonse zidachitika.

Luk 24:15 Ndipo kudali m’kukambirana kwawo ndi kufunsana, Yesu mwini adayandikira natsagana nawo.

Luk 24:16 Koma maso awo adagwidwa kuti asamzindikire Iye.

Luk 24:17 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mawu awa ndi wotani muli kukambirana wina ndi mzake pamene mukuyenda ndi chisoni? Ndipo adayima ndi nkhope zawo zachisoni.

Luk 24:18 Ndipo m’modzi wa iwo, dzina lake Kleopa, adayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m’Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?

Luk 24:19 Ndipo Iye adati kwa iwo, zinthu zanji? Ndipo adati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarete, ndiye munthu m’neneri wamphamvu m’ntchito, ndi m’mawu, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;

Luk 24:20 Ndi kuti ansembe akulu ndi olamulira athu adampereka Iye ku chiweruzo cha imfa ndipo, adampachika Iye.

Luk 24:21 Ndipo tidayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzawombola Israyeli. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi.

Luk 24:22 Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene adalawirira m`mamawa kumanda;

Luk 24:23 Ndipo m’mene sadaupeza mtembo wake, anadza, nanena kuti adawona m’masomphenya angelo, amene adanena kuti ali ndi moyo Iye.

Luk 24:24 Ndipo ena mwa iwo adali nafe adachoka kumka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sadamuwona.

Luk 24:25 Ndipo Iye adati kwa iwo, Opusa inu, ndi wozengereza mtima kusakhulupirira zonse adaziyankhula aneneri!

Luk 24:26 Kodi sadayenera Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake?

Luk 24:27 Ndipo adayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za Iye yekha.

Luk 24:28 Ndipo adayandikira ku mudzi umene adalikupitako; ndipo adachita ngati adafuna kupitirira.

Luk 24:29 Ndipo adamuwumiriza Iye, nati, khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo adalowa kukhala nawo.

Luk 24:30 Ndipo kudali m’mene Iye adakhala nawo pachakudya, adatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo.

Luk 24:31 Ndipo maso awo adatseguka, ndipo adamzindikira Iye; ndipo adawakanganukira iye nawachokera.

Luk 24:32 Ndipo adati wina ndi mzake, mtima wathu sudali wotentha m’kati mwathu nanga m’mene adayankhula nafe m’njira, m’mene adatitsegulira malembo?

Luk 24:33 Ndipo adanyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi m’modziwo, ndi iwo adali nawo atasonkhana pamodzi,

Luk 24:34 Nanena, Ambuye adawuka ndithu, nawonekera kwa Simoni.

Luk 24:35 Ndipo iwo adawafotokozera za m’njira, ndi umo adadziwika nawo m’kunyema kwa mkate.

Luk 24:36 Ndipo pakuyankhula izi iwowa, Yesu mwini yekha adayimirira pakati pawo; nanena nawo, Mtendere ukhale nanu.

Luk 24:37 Koma adawopsedwa ndi kuchita mantha, nayesa kuti adalikuwona mzimu.

Luk 24:38 Ndipo Iye adati kwa iwo, Mukhala bwanji wobvutika? Ndipo mtsutso wanu uwuka bwanji m’mitima mwanu?

Luk 24:39 Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe m’nofu ndi mafupa monga muwona ndiri nazo Ine.

Luk 24:40 Ndipo m’mene adanena ichi, adawawonetsera iwo manja ake ndi mapazi ake.

Luk 24:41 Koma pokhala iwo chikhalire wosakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?

Luk 24:42 Ndipo adampatsa Iye chidutswa cha nsomba yokazinga ndi uchi.

Luk 24:43 Ndipo adachitenga, nachidya pamaso pawo.

Luk 24:44 Ndipo Iye adati kwa iwo, Awa ndi mawuwo ndidayankhula ndi inu pamene ndidali nanu kuti ziyenera kukwaniritsidwa za Ine m’chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.

Luk 24:45 Ndipo Iye adawatsegulira chidziwitso chawo, kuti adziwitse malembo,

Luk 24:46 Ndipo Iye adati kwa iwo, kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nawuke kwa akufa tsiku lachitatu:

Luk 24:47 Ndi kuti kulalikidwe m’dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machismo kwa mitundu yonse, kuyambira kuYerusalemu.

Luk 24:48 Inu ndinu mboni zazinthu izi.

Luk 24:49 Ndipo onani, Ine nditumiza kwa inu lonjezano la Atate wanga: koma khalani inu mumzinda wa Yerusalemu muno kufikira mwabvekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.

Luk 24:50 Ndipo Iye adatuluka nawo kufikira ku Betaniya; nakweza manja ake, nawadalitsa.

Luk 24:51 Ndipo kudali, pakuwadalitsa Iye adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba.

Luk 24:52 Ndipo adamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu:

Luk 24:53 Ndipo adakhala chikhalire m’kachisi kuyamika ndi kudalitsa Mulungu. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE