Jude


1

Jud 1:1 Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo woyitanidwa ndi opatulidwa mwa Mulungu Atate, ndi wosungidwa mwa Yesu Khristu.

Jud 1:2 Chifundo chikhale kwa inu ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni.

Jud 1:3 Wokondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbane motsimikiza chifukwa kuti chikhulupiliro chapatsidwa kamodzi kwa woyera mtima.

Jud 1:4 Pakuti pali anthu ena adakwawira m’seri, ndiwo amene aja adalembedwa mayina awo kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, namkaniza Ambuye Mulungu yekha ndi Ambuye wathu Yesu Khristu.

Jud 1:5 Koma ndifuna kukukumbutsani kuti ngakhale mudadziwa zonse kale, kuti Ambuye atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m’dziko la a Aigupto, adawononganso iwo wosakhulupilira.

Jud 1:6 Angelonso amene sadasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu adasiya pokhala pawo pawo, adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.

Jud 1:7 Monga Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuyizungulira, yotsatana nayoyo, idadzipereka kuchiwerewere, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iyikidwa chitsanzo, yobwezeredwa chilango cha moto wosatha.

Jud 1:8 Momwemonso iwo m’kulota kwawo adetsa matupi awo, napeputsa ufumu nachitira mwano maukulu awulemerero.

Jud 1:9 Koma Mikayeli mkulu wa angelo pakuchita makani ndi mdierekezi adatsutsana za thupi la Mose, sadalimbika mtima kutchulira chifukwa chomchitira mwano, koma adati, Ambuye akudzudzule.

Jud 1:10 Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika nazo eni.

Jud 1:11 Tsoka kwa iwo! Pakuti adayenda m’njira ya Kayini, ndipo adadziwononga m’chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m’chitsutsano cha Kore.

Jud 1:12 Iwo ndiwo wokhala mawanga pa maphwando anu achikondano, pakudya nanu pamodzi, akudzidyetsa wokha mopanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;

Jud 1:13 Mafunde woopsa a nyanja, akuwinduka thobvu la manyazi a iwo wokha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.

Jud 1:14 Ndipo kwa iwo, Enoke, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, adanenera za izi kuti, Tawona, akudza Ambuye ndi woyera ake zikwi makumi,

Jud 1:15 Kudzachitira onse chiweruziro ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zawo zonse zosapembedza, zimene adazichita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene wochimwa osapembedza adayankhula pa Iye.

Jud 1:16 Amenewo ndiwo wodandaula, wodelera, akuyenda monga mwa zilakolako zawo; ndipo pakamwa pawo ayankhula zazikuluzikulu, akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.

Jud 1:17 Koma, wokondedwa, mukumbukire mawu wonenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu.

Jud 1:18 Kuti adanena nanu, panthawi yotsiriza padzakhala wotonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo wokha.

Jud 1:19 Iwo ndiwo wopatukitsa, anthu a makhalidwe achibadwidwe, wosakhala naye Mzimu.

Jud 1:20 Koma inu, wokondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiliro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mwa Mzimu Woyera,

Jud 1:21 Mudzisunge nokha, m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha.

Jud 1:22 Ndipo kwa ena khalani ndi chifundo musiyanitse;

Jud 1:23 Koma ena muwapulumutse ndi mantha kuwakwatula ku moto podana nawonso, malaya wochitidwa mawanga ndi thupi.

Jud 1:24 Tsopano kwa Iye amene akhoza kukusungani kuti mungagwe, ndi kukuyimikani pamaso pa ulemerero wake wopanda chilema ndi chimwemwe chopitirira,

Jud 1:25 Kwa Mulungu wanzeru yekha Mpulumutsi wathu, kukhale ulemerero,ndi ukulu ndi ulamuliro ndi mphamvu, tsopano ndi kufikira nthawi zonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE