James


1

Jas 1:1 Yakobo mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m’chibalaliko: ndikupatsani moni.

Jas 1:2 Abale anga, muchiyese chimwemwe chokha, pamene mukugwa m’mayesero a mitundu mitundu;

Jas 1:3 Pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiliro.

Jas 1:4 Koma chipiliro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi wopanda chilema, osasowa kanthu konse.

Jas 1:5 Ngati wina wa inu inkasowa nzeru, apemphere kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, ndi mosatonza; ndipo adzampatsa iye.

Jas 1:6 Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse. Pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.

Jas 1:7 Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye.

Jas 1:8 Munthu wa mitima iwiri akhala wosakhazikika pa njira zake zonse.

Jas 1:9 Lolani m;bale wokhala modzichepetsa akondwere m’mene iye wakwezedwa.

Jas 1:10 Pamene achuma adzatsitsidwa pansi: pakuti adzapita monga duwa la udzu.

Jas 1:11 Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa mawonekedwe ake awonongeka; koteronso wachuma adzafota m’mayendedwe ake.

Jas 1:12 Wodala munthu wakupilira poyesedwa; pakuti pamene wabvomerezeka, adzalandira Korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.

Jas 1:13 Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu: pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoyipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu:

Jas 1:14 Koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera nichim’nyenga.

Jas 1:15 Pamenepo chilakolakocho chitayima, chibala uchimo: ndipo uchimo utakula msinkhu, ubala imfa.

Jas 1:16 Musanyengedwe, abale anga wokondedwa.

Jas 1:17 Mphatso ili yonse yabwino, ndi chininkho chiri chonse changwiro zichokera kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko amene alibe chisanduliko, kapena m’thunzi wa chitembenukiro.

Jas 1:18 Mwa chifuniro chake mwini adatibala ife ndi mawu a chowonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zake.

Jas 1:19 Mudziwa abale anga wokondedwa, kuti munthu aliyense akhale watcheru, wodekha poyankhula, wodekha pakupsa mtima.

Jas 1:20 Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.

Jas 1:21 Mwa ichi, mutabvula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choyipa, landirani ndi chifatso mawu wowokedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.

Jas 1:22 Koma khalani akuchita mawu, wosati akumva wokha, ndi kudzinyenga nokha.

Jas 1:23 Pakuti ngati munthu ali wa kumva mawu, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake mkalilore:

Jas 1:24 Pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, nayiwala pompaja adali wotani.

Jas 1:25 Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo la ufulu, natero chipenyerere, ameneyo posakhala wakumva wakuyiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.

Jas 1:26 Ngati wina adziyesera kuti ali wopembedza, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthu uyu nkopanda pake.

Jas 1:27 Mapembedzedwe woyera ndi wosadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.



2

Jas 2:1 Abale anga, musakhale nacho chikhulupiliro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero ndi kusamala mawonekedwe a munthu.

Jas 2:2 Pakuti akalowa munsonkhano wanu munthu wobvala mphete yagolide, ndi chobvala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chobvala chalitsiro;

Jas 2:3 Ndipo mukalemekeza iye wobvala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe ima uko, kapena khala pansi pa mpando wa mapazi anga:

Jas 2:4 Kodi simudasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala woweruza woganizira zoyipa?

Jas 2:5 Mverani, abale anga wokondedwa; kodi Mulungu sadasankha osauka a dziko lapansi akhale wolemera m’chikhulupiliro, ndi wolowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?

Jas 2:6 Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwo ku mabwalo a milandu?

Jas 2:7 Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muyitanidwa nalo?

Jas 2:8 Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, uzikonda mzako monga uzikonda wekha, muchita bwino:

Jas 2:9 Koma ngati musamala mawonekedwe a munthu, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga wolakwa.

Jas 2:10 Pakuti aliyense amene asunga malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.

Jas 2:11 Pakuti Iye wakuti, usachite chigololo, adatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

Jas 2:12 Yankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.

Jas 2:13 Pakuti chiweruziro chiribe chifundo kwa iye amene sadachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.

Jas 2:14 Chipindulo chake n’chiyani, abale anga, munthu akanena. Ndiri nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa?

Jas 2:15 Mchimwene kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake.

Jas 2:16 Ndipo wina wa inu akanena nawo, mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake n’chiyani?

Jas 2:17 Momwemonso chikhulupiliro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa m’kati mwakemo.

Jas 2:18 Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiliro, ndipo ine ndiri nazo ntchito; undiwonetse ine chikhulupiliro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuwonetsa iwe chikhulupiliro changa chotuluka m’nchito zanga.

Jas 2:19 Ukhulupilira iwe kuti Mulungu ali m’modzi; uchita bwino: ziwanda zikhulupiliranso, ndipo zinthunthumira.

Jas 2:20 Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiliro chopanda ntchito chiri chakufa?

Jas 2:21 Abrahamu kholo lathu, sadayesedwa wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake isake nsembe pa guwa la nsembe?

Jas 2:22 Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro?

Jas 2:23 Ndipo adakwaniridwa malembo wonenawa, ndipo Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo adatchedwa bwenzi la Mulungu.

Jas 2:24 Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.

Jas 2:25 Ndipo momwemonso sadayesedwa wolungama Rahabi mkazi wadamayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira yina?

Jas 2:26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.



3

Jas 3:1 Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa tidzalandira kutsutsidwa kwakukulu

Jas 3:2 Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

Jas 3:3 Tawonani, tiyikira akavalo zogwirira m’kamwa mwawo kuti atimvere, tipotolozanso thupi lawo lonse.

Jas 3:4 Tawonani, zombonso; zingakhale ndi zazikulu zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigilo laling’ono ndithu kumene kuli konse afuna wogwira tsigilo.

Jas 3:5 Kotero lilimenso monga chiwalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zinthu zazikulu. Tawonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!

Jas 3:6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu layikika lilime, limene lidetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe achibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi gehena.

Jas 3:7 Pakuti mtundu uli wonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa za m’nyanja, zimazolowetsedwa, ndipo zizoloweretsedwa ndi anthu.

Jas 3:8 Koma lilime palibe munthu akhoza kulizolowezetsa; liri choyipa chotaktata, lodzala ndi ululu wakupha.

Jas 3:9 Timayamika nalo Ambuye ndi Atate; timatemberera nalonso anthu, wokhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu.

Jas 3:10 Kuchokera m’kamwa m;modzi momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.

Jas 3:11 Kodi kasupe atulutsira pa una womwewo madzi wokoma ndi owawa?

Jas 3:12 Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sakhoza kutulutsa wokoma.

Jas 3:13 Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Awonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake munzeru yofatsa.

Jas 3:14 Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m’mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho chowonadi.

Jas 3:15 Nzeru iyi sindiyo yotsika Kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda.

Jas 3:16 Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi ntchito ya choyipa chiri chonse.

Jas 3:17 Koma nzeru yochokera Kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomveka bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, ndi yopanda chinyengo.

Jas 3:18 Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mu mtendere kwa iwo akuchita mtendere.



4

Jas 4:1 Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera ku zilakolako zanu zochita nkhondo m’ziwalo zanu?

Jas 4:2 Mulakalaka, ndipo zikusowani: mukupha, ndipo mukhumba simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.

Jas 4:3 Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koyipa, kuti mukachimwaze pochita zilakolako zanu.

Jas 4:4 Inu amuna ndi akazi achigololo, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziyika kukhala mdani wa Mulungu.

Jas 4:5 Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita kaduka?

Jas 4:6 Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza wodzikuza, koma apatsa chisomo wodzichepetsa.

Jas 4:7 Potero mverani Mulungu. Koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Jas 4:8 Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, wochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.

Jas 4:9 Khalani wosautsidwa, lirani, lirani misozi: kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

Jas 4:10 Dzichepetseni nokha pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Jas 4:11 Musamanenerana zoyipa, wina ndi mzake, abale,wonenera zoyipa mbale wake, kapena woweruza m’bale wake, anenera choyipa lamulo naweruza lamulo:koma ngati uweruza lamulo: suli wochita lamulo, komatu woweruza.

Jas 4:12 Woyika lamulo, ndiye m’modzi ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga; koma iwe woweruza mzako ndiwe yani?

Jas 4:13 Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa ku mzinda wakuti wakuti, ndikukhala komweko chaka ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nawo:

Jas 4:14 Inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Uli monga nthunzi, wakuwonekera kanthawi kakang’ono, ndi pamenepo ukanganuka.

Jas 4:15 Mudayenera kunena motere, akalola Ambuye tikakhala ndi moyo, tidzachita ichi kapena icho.

Jas 4:16 Koma tsopano mudzitamandira m’kudzikuza kwanu: kudzitamandira kuli konse kotero nkoyipa.

Jas 4:17 Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.



5

Jas 5:1 Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu.

Jas 5:2 Chuma chanu chawola ndi zobala zanu zijiwa ndi njenjete.

Jas 5:3 Golidi wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku wotsiriza.

Jas 5:4 Tawonani, malipiro a antchitowo adakolola m’minda yanu, wosungidwa ndi inu powanyenga, afuwula; ndipo mafuwulo a wokololawo adalowa makutu a Ambuye wa makamu.

Jas 5:5 Mwadyerera padziko lapansi, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m’tsiku lakupha.

Jas 5:6 Mudatsutsa, ndipo mudapha wolungamayo, Iye sadakaniza inu.

Jas 5:7 Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Tawonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya myundo ndi masika.

Jas 5:8 Lezani mtima inunso, khazikitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.

Jas 5:9 Musayipidwe wina ndi mzake, abale, kuti mungatsutsidwe. Tawonani, woweruza ayima pakhomo.

Jas 5:10 Tengani, abale chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene adayankhula m’dzina la Ambuye.

Jas 5:11 Tawonani, tiwayesera wodala wopilirawo. Mudamva za chipiliro cha Yobu, ndipo mwawona chitsirizo cha Ambuye kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.

Jas 5:12 Koma pamwamba pa zinthu zonse, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula m’mwamba kapena dziko lapansi, kapena lumbiro lina liri lonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iyayi wanu akhale iyayi; kuti mungagwe m’chitsutso.

Jas 5:13 Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Ayimbire masalmo.

Jas 5:14 Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziyitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye:

Jas 5:15 Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ngati adachita machimo, adzakhululukidwa kwa iye.

Jas 5:16 Chifukwa chake mubvomerezane wina ndi mzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mzake kuti muchiritsidwe. Pemphero lokhudza kwambiri la munthu wolungama lichita kwakukulu m’machitidwe ake.

Jas 5:17 Eliya adali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo adapemphera motsimikizira kuti mvula isabvumbwe: ndipo siyidagwa mvula pa dziko lapansi zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.

Jas 5:18 Ndipo adapempheranso, ndipo m'mwamba mudatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake.

Jas 5:19 Abale, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi chowonadi, ndipo ambweza iye mzake;

Jas 5:20 Azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa ku njira yake yosochera adzapulumutsa munthu ku imfa, ndipo adzabvundikira machismo awunyinji.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE