Hebrews


1

Heb 1:1 Kale Mulungu adayankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana,

Heb 1:2 Koma pakutha pake pa masiku ano adayankhula kwa ife mwa Mwana amene adamuyika wolowa nyumba wa zinthu zonse, mwa Iyenso adalenga mayiko ndi am’mwamba omwe.

Heb 1:3 Ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zones ndi mawu a mphamvu yake, m’mene adachita chiyeretso cha machimo athu, adakhala padzanja lamanja ;la Ukulu m’Mwamba;

Heb 1:4 Atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo.

Heb 1:5 Pakuti kwa m’ngelo uti adati nthawi ili yonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala iwe? Ndiponso Ine ndidzakhala kwa Iye Atate? Ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana?

Heb 1:6 Ndiponso pamene atenga wobadwa woyamba kulowa naye m’dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.

Heb 1:7 Ndipo za angelo anenadi, Amene ayesa angelo ake mizimu, ndi womtumikira Iye akhale lawi lamoto.

Heb 1:8 Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi. Ndipo ndodo yachifumu yowongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.

Heb 1:9 Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choyipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerera chenicheni.

Heb 1:10 Ndipo, Inu Ambuye, pachiyambipo mudayika maziko ake a dziko, ndipo miyamba ili ntchito ya manja anu pamwamba pa anzanu:

Heb 1:11 Iyo idzawonongeka; komatu Inu mudzakhalitsa; ndipo iyo yonse idzasuluka monga achitira malaya;

Heb 1:12 Monga chofunda mudapinda, monga malaya, ndipo idzasanduka: koma Inu ndinu yemweyo, ndipo zaka zanu sizidzatha.

Heb 1:13 Koma za m’ngelo uti adati nthawi ili yonse, khala pa dzanja lamanja langa, kufikira ndikayika adani ako chopondapo mapazi ako?

Heb 1:14 Kodi siyili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?



2

Heb 2:1 Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.

Heb 2:2 Pakuti ngati mawu adayankhulidwa ndi angelo adakhala wokhazikika, ndipo cholakwira chiri chonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama.

Heb 2:3 Kodi tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchiyankhula, ndipo iwo adachimva adatitsimikizira ife;

Heb 2:4 Pochitira umboni pamodzi nawo Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa ndi zozizwitsa za mitundu mitundu ndi mphatso za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.

Heb 2:5 Pakuti sadagonjetsera angelo dziko liri mkudza limene tinenali.

Heb 2:6 Koma wina adachita umboni pena nati, “Munthu nchiyani kuti mumkumbukira iye? Kapena mwana wa munthu kuti mucheza naye?

Heb 2:7 Mudamchepsa pang’ono kuposa angelo, mudambveka iye Korona waulemerero ndi ulemu, ndipo mudamuyika iye woyang’anira ntchito za manja anu:

Heb 2:8 Koma inu mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake. Pakutero Iye adayika zinthu zonse pansi pa iye, sadasiye kanthu kosamugonjera iye. Koma tsopano sitiziwona zinthu zonse zomgonjera iye.

Heb 2:9 Koma tiwonaYesu, amene adamchepsa pang’ono ndi angelo, chifukwa cha zowawa za imfa, wobvala Korona wa ulemerero ndi ulemu, ndikuti Iye mwa chisomo cha Mulungu alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.

Heb 2:10 Pakuti kudamuyenera Iye, amene mwa Iye muli zinthu zonse, potenga ana ambiri alowe ulemerero, kupanga mtsogoleri wa chipulumutso chawo wangwiro mwa zowawa.

Heb 2:11 Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa m’modzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale,

Heb 2:12 Ndikunena, ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuyimbirani.

Heb 2:13 Ndiponso ndidzayika chikhulupiliro changa mwa Iye. Ndiponso, tawonani, Ine ndi ana amene Mulungu adandipatsa Ine.

Heb 2:14 Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nawo makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuwononge iye amene adali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;

Heb 2:15 Ndikuwombola iwo onse amene pochita mantha ndi imfa m’moyo wawo wonse adamangidwa ukapolo.

Heb 2:16 Ponena zowona Iye sadatenge pa iye chilengedwe cha angelo; koma iye adatenga pa iye mbewu ya Abrahamu.

Heb 2:17 Potero kudamuyenera iye kufanizidwa ndi abale ake, kuti akakhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kukapanga chiyanjanitso cha anthu chifukwa cha uchimo.

Heb 2:18 Pakuti mwa ichi iye popeza adamva zowawa, poyesedwa mwiniyekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.



3

Heb 3:1 Potero abale woyera mtima, wolandirana nawo mayitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wansembe wa chibvomerezo chathu, Khristu Yesu;

Heb 3:2 Amene adakhala wokhulupirika kwa Iye adamuyikayo, monganso Mose m’nyumba yake yonse.

Heb 3:3 Pakuti munthu ameneyu wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga iye amene amanga nyumba ali ndi ulemu woposa nyumbayo.

Heb 3:4 Pakuti nyumba ili yonse ili naye munthu adayimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.

Heb 3:5 Ndipo Mosetu ndithudi adali wokhulupirika m’nyumba yake yonse, monga m’tumiki, kuchitira umboni wa zinthuzo zimene zidzayankhulidwa mtsogolo;

Heb 3:6 Koma Khristu monga Mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa chitsimikiziro ndi chimwemwe cha chiyembekezo, kuchigwira mpaka kumapeto.

Heb 3:7 Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, lero ngati mudzamva mawu ake,

Heb 3:8 Musaumitse mitima yanu, monga kudawawawa mtima, mtsiku la mayesero m’chipululu:

Heb 3:9 Pamene makolo anu adandiyesa Ine, ndikundibvomereza Ine, ndikuwona ntchito zanga zaka makumi anayi.

Heb 3:10 Momwemo ndidakwiya nawo m’bado uwu, ndipo ndidati, nthawi zonse amalakwa mmitima yawo; ndipo sadazindikire njira zanga.

Heb 3:11 Chotero ndidalumbira mu ukali wanga, Sadzalowa mpumulo wanga.

Heb 3:12 Tapenyani, abale, kuti kapena ungakhale mwa wina wa inu mtima woyipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;

Heb 3:13 Koma dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo.

Heb 3:14 Pakuti takhala ife wolandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsitsa chiyambi cha chitsimikizo chathu kuchigwira mpaka kumapeto;

Heb 3:15 Umo anena, Lero ngati mudzamva mawu ake, musaumitse mitima yanu, monga kuwawidwa mtima.

Heb 3:16 Pakuti ena,pamene adamva, adawawidwa mtima: kodi si onse aja adatuluka mu Aigupto ndi Mose?

Heb 3:17 Koma ndi ayani adakwiya nawo zaka makumi anayi? Kodi siamene adachimwa aja, amene mitembo yawo yidagwa m’chipululu?

Heb 3:18 Ndipo ndi ayani adawalumbirira Iye kuti asalowe mpumulo wake, koma kwa iwo amene sadakhulupirire?

Heb 3:19 Chotero tawona kuti sadakhoza kulowa chifukwa cha kusakhulupirira.



4

Heb 4:1 Chifukwa chake tiwope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angawoneke ngati adaliperewera.

Heb 4:2 Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo: koma iwowa sadapindula nawo mawu wolalikidwawo, popeza sadasanganizika ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.

Heb 4:3 Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga iye adanena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga: zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuchikhazikitso cha maziko a dziko lapansi.

Heb 4:4 Pakuti iye wanena za malo ena a tsiku lachisanu ndi chiwiri, naterodi, Ndipo Mulungu adapumula tsiku la chisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse.

Heb 4:5 Ndipo m’malo awanso, ngati adzalowa mpumulo wanga.

Heb 4:6 Powona pamenepo tsono patsalanso kuti ena alowe mmenemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino udalalikidwa koyamba kwa iwo sadalowamo chifukwa cha kusakhulupirira.

Heb 4:7 Alangizanso tsiku lina, ndi kunena m’Davide, itapita nthawi yayikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale, Lero ngati mudzamva mawu ake, musaumitse mitima yanu.

Heb 4:8 Pakuti ngati Yesu akadawapumitsa iwo, sakadayankhulanso mtsogolomo za tsiku lina.

Heb 4:9 Momwemo utsalira mpumulo kwa anthu a Mulungu.

Heb 4:10 Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini ku ntchito zake, monganso Mulungu ku zake za Iye.

Heb 4:11 Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m’chitsanzo chomwechi cha kusamvera.

Heb 4:12 Pakuti mawu a Mulungu ali a moyo, ndi wochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konse konse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

Heb 4:13 Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala pambalambanda ndi zobvundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.

Heb 4:14 Popeza tsono tiri naye mkulu wansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chibvomerezo chathu.

Heb 4:15 Pakuti sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofoka zathu; koma anayesedwa m’zonse monga ife, koma wopanda uchimo.

Heb 4:16 Potero tiyeni ife tilimbike poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tikalandire chifundo, ndi kupeza chisomo chakuthandiza mnthawi yakusowa.



5

Heb 5:1 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense, wotengedwa mwa anthu, amayikika chifukwa cha anthu m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mphatso, ndiponso nsembe, chifukwa cha machimo:

Heb 5:2 Akhale wokhoza kumva chifundo ndi wosadziwa ndi wolakwa popeza iye yekhanso amagwidwa ndi chifowoko.

Heb 5:3 Ndipo chifukwa chakecho ayenera, monga m’malo a anthuwo, moteronso m’malo a iye yekha, kupereka nsembe chifukwa cha machimo.

Heb 5:4 Ndipo palibe munthu adzitengera mwiniyekha ulemu uwu, komatu iye amene ayitanidwa ndi Mulungu, monga unaliri ndi Aroni.

Heb 5:5 Koteronso Khristu sadadzilemekeza yekha kukhala mkulu wansembe; koma Iye amene adati kwa Iye, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala Iwe.

Heb 5:6 Monga iye adanenanso mmalo ena, Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melikizedeke.

Heb 5:7 Ameneyo m’masiku athupi lake, pamene adapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kolimba ndi misozi kwa Iye amene akhoza kumpulumutsa Iye mu imfa, ndipo adamvedwa chifukwa adawopa;

Heb 5:8 Angakhale adali Mwana, komabe iye adaphunzira kumvera mwa zinthu zimene iye adamva nazo kuwawa;

Heb 5:9 Ndipo popangidwa kukhala wangwiro, adakhala iye woyambitsa chipulumutso chosatha kwa iwo onse amene amvera iye;

Heb 5:10 Wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melikizedeke.

Heb 5:11 Kwa Iye tiri nazo zinthu zambiri zonena, ndizobvuta kuzitanthawuzira, powona inu kuti muli wogontha mmamvedwe.

Heb 5:12 Pakuti ngakhale mwakhala aphunzitsi chifukwa cha nthawiyi, muli nako kusowanso kuti wina akuphunzitseninso zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala wonga wofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.

Heb 5:13 Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mawu achilungamo: pakuti ali khanda.

Heb 5:14 Koma chakudya chotafuna chiri cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo adazoloweretsa zizindikiritso zawo posiyanitsa chabwino ndi choyipa.



6

Heb 6:1 Mwa ichi, posiya mfundo za chiphunzitso cha Khristu, tiyeni ife tipite chitsogolo ku ungwiro; osayikanso maziko akulapa kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi achikhulupiliro cha kwa Mulungu,

Heb 6:2 Achiphunzitso cha ubatizo, ndi a chakuyika manja, ndi a chakuuka kwa akufa, ndi a chachiweruziro chosatha.

Heb 6:3 Ndipo ichi tidzachita, ngati atatilola Mulungu.

Heb 6:4 Pakuti sikutheka kwa iwo amene adaunikidwa panthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala wolandirana naye Mzimu Woyera,

Heb 6:5 Ndipo analawa mawu wokoma a Mulungu, ndi mphamvu za dziko lirimkudza,

Heb 6:6 Ngati akagwa m’chisokero posiya njirayo; kuwakonzanso iwo kuti alapenso; powona iwo alikudzipachikiranso iwowokha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.

Heb 6:7 Pakuti nthaka imene idamwa mvula imene imadza kawiri kawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adayilimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu:

Heb 6:8 Koma ikabala minga ndi mitungwi, ikanidwa, ndipo yatsala pang’ono kutembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.

Heb 6:9 Koma, wokondedwa, takopeka nanu ndi zinthu zabwino, ndizo zinthu zimene zigwirizana pamodzi ndi chipulumutso, chotero titero pakuyankhula kwathu.

Heb 6:10 Pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzayiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachiwonetsera ku dzina lake, muja mudatumikira woyera mtima ndipo mutumikirabe.

Heb 6:11 Koma tikhumba kuti yense wa inu awonetsere nzeru yomweyi kuchidzalo chachitsimikizo cha chiyembekezo mpaka chimariziro:

Heb 6:12 Kuti musakhale aulesi, koma wotsatira a iwo amene mwa chikhulupiriro ndi mopirira adalandira malonjezano.

Heb 6:13 Pakuti pamene Mulungu adapanga malonjezano ndi Abrahamu, chifukwa iye analibe cholumbirira chachikulu,adadzilumbirira mwa Iye yekha.

Heb 6:14 Ndikuti, zowona kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa ndidzachulukitsa iwe.

Heb 6:15 Ndipo chotero, iye atatha ndi chifatso kupirira, adalandira lonjezano.

Heb 6:16 Pakuti anthu ndithudi alumbirira pa wamkulu: ndipo lumbiro lachitsimikizo kwa iwo litsiriza matsutsano onse.

Heb 6:17 Choteronso Mulungu, pofuna kuwonetsa kuchuluka kwa wolowa a lonjezano ku uphungu wake wosasinthika, adatsimikizira izi mwa lumbiro.

Heb 6:18 Kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, mwa zimenezo kudali kobvuta kuti Mulungu aname, tiyenera ife tikakhale nacho chitonthozo cholimba, ife amene tidapulumuka pothawa kuti tikagwiritsitse chiyembekezo choyikika pamaso pathu.

Heb 6:19 Ndicho chiyembekezo chimene tiri nacho monga nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndichimene tilowa nacho m’katikati mwa chophimba.

Heb 6:20 M’mene Yesu wotitsogolera adatsogola kulowa chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.



7

Heb 7:1 Pakuti Melikizedeke uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene adakomana ndi Abrahamu, pobwerera iye atawapha mafumu aja, namdalitsa;

Heb 7:2 Amenenso Abrahamu adamgawira limodzi la magawo khumi la zonse ndiye posandulika poyamba ali Mfumu ya chilungamo, pameneponso Mfumu ya Salemu, ndiyo Mfumu ya mtendere;

Heb 7:3 Wopanda atate ake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu, iyeyu wakhala wansembe kosalekeza.

Heb 7:4 Koma tapenyani ukulu wake wa munthu uyu, amene Abrahamu, kholo lalikulu, adampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo.

Heb 7:5 Ndipo indetu iwowa mwa ana a Levi, akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale awo, angakhale adatuluka m’chiwuno cha Abrahamu;

Heb 7:6 Koma iye amene mawerengedwe achibadwidwe chake sachokera mwa iwo, adatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene adali nawo malonjezano.

Heb 7:7 Ndipo popanda chitsutsano konse wam’ngono adalitsidwa koposa wamkulu.

Heb 7:8 Ndipo pano anthu amene amafa amalandira chakhumi; koma kumeneko iye alandira iwo, kwa amene kudachitiridwa umboni kuti ali ndi moyo.

Heb 7:9 Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzi limodzi la magawo khumi adapereka limodzi lamagawo khumi;

Heb 7:10 Pakuti pajapo adali m’chuuno cha atate wake, pamene Melikizedeke adakomana naye.

Heb 7:11 Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa chilevi, (pakuti momwemo anthu adalandira chilamulo) pakadatsala kusowa kotani kuti awuke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melikizedeke, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?

Heb 7:12 Pakuti pakusintha unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisinthike.

Heb 7:13 Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.

Heb 7:14 Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu adatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sadayankhula kanthu ka ansembe.

Heb 7:15 Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melikizedeke,

Heb 7:16 Amene wakhala si monga mwa lamulo la thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;

Heb 7:17 Pakuti amchitira umboni, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.

Heb 7:18 Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufoka kwake, ndi kusapindulitsa kwake.

Heb 7:19 Pakuti chilamulo sichidachitira kanthu kakhale kopanda chilema, koma kubweretsa kwa chiyembekezo chabwino kudachitadi; mwa chimenecho ife tiyandikira nacho chifupi kwa Mulungu.

Heb 7:20 Monga momwe kudachitika sikopanda lumbiro iye adakhala wansembe:

Heb 7:21 (Chifukwa ansembe ajawa adapangidwa kopanda lumbiro; koma uyu ndi lumbiro mwa iye amene adanena kwa iye, walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.)

Heb 7:22 Momwemonso Yesu wapangidwa kukhala chitsimikizo cha pangano labwino.

Heb 7:23 Ndipo iwo zowonadi ambiri adakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe:

Heb 7:24 Koma munthu uyu, chifukwa kuti akhalabe Iye nthawi yosatha ali nawo unsembe wosasinthika.

Heb 7:25 Chifukwa chake kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.

Heb 7:26 Pakuti mkulu wa ansembe wotere adatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choyipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi wochimwa, wakukhala wopitirira miyamba.

Heb 7:27 Amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyamba chifukwa cha zoyipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoyipa za anthu; pakuti ichi adachita kamodzi kwatha, podzipereka yekha.

Heb 7:28 Pakuti chilamulo chimayika akulu a ansembe anthu, wokhala nacho chifoko; koma mawu a lumbiro, amene adafika chitapita chilamulo, ayika Mwana, woyesedwa wopanda chilema ku nthawi zonse.



8

Heb 8:1 Tsopano mutu wa izi tanenazi ndi uwu; Tiri naye mkuru wansembe wotere, amene adakhala pa dzanja la manja la mpando wachifumu wa Ukulu m’Mwamba;

Heb 8:2 Mtumiki wa malo wopatulika, ndi wa chihema chowona, chimene Ambuye adachimanga, simunthu ayi.

Heb 8:3 Pakuti mkulu wa ansembe ali yense ayikidwa kupereka mphatso, ndiponso nsembe; potero mkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka.

Heb 8:4 Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mphatso monga mwa lamulo.

Heb 8:5 Amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa ndi Mulungu m’mene adafuna kupanga chihema; pakunena kuti, onetsetsa, atero iye kuti, uchite zinthu zonse monga mwa chitsanzocho chawonetsedwa kwa iwe m’phiri.

Heb 8:6 Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka choposa, umonso ali nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano woposa.

Heb 8:7 Pakuti pangano loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo.

Heb 8:8 Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena, Tawonani, akudza masiku, anena Ambuye, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda;

Heb 8:9 Losati longa pangano ndidalichita ndi makolo awo, tsikuli ndidawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m’dziko la Aigupto; kuti iwo sadakhalebe mpangano langa, ndipo Ine sindidawasamalira iwo, anena Ambuye.

Heb 8:10 Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israyeli, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga mnzeru zawo, ndipo pamtima pawo ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu: ndipo adzandikhalira Ine anthu:

Heb 8:11 Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu m’nzake, ndipo yense mbale wake, ndi kuti zindikira Ambuye: pakuti onse adzadziwa Ine kuyambira wam’ng’ono kufikira wamkulu wa iwo.

Heb 8:12 Pakuti ndidzachitira chifundo zosalungama zawo, ndipo machimo ndi zoyipa zawo sindidzazikumbukanso.

Heb 8:13 Pakunena Iye pangano latsopano, adagugitsa loyambali. Tsopano chimene chiri mkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka.



9

Heb 9:1 Ndipo zowonadi kuti chipangano choyambachi chidali nazo zoyikika za kutumikira Umulungu, ndi malo wopatulika a pa dziko lapansi.

Heb 9:2 Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m’menemo mudali choyikapo nyali, ndi gome, ndi mkate wowonekera; amene atchedwa malo wopatulika.

Heb 9:3 Koma m’kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chimene chitchedwa Malo Wopatulikitsa;

Heb 9:4 Wokhala nayo mbale ya zofukiza yagolidi ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golidi, momwemo mudali mbiya yagolidi yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaphukayo; ndi magome a chipangano;

Heb 9:5 Ndi pamwamba pake aKerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano padera padera.

Heb 9:6 Tsopano pamene zinthu izi zidakonzeka kotero, ansembe amalowa m’chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kugwira ntchito ya Mulungu.

Heb 9:7 Koma kulowa m’chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene amapereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu:

Heb 9:8 Mzimu Woyera adatsimikizira ichi, kuti njira yolowa nayo kumalo wopatulikitsa siyidawonetsedwe, pokhala chihema choyamba chiri chiyimire:

Heb 9:9 Ndicho chiphiphiritso cha ku nthawi yomweyi, m’mene mphatso ndi nsembezo zidaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kumuyesa wamgwiro wotumikirayo.

Heb 9:10 Chimene chikhala m’zoyikika za thupi zokha ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe wosiyanasiyana, woyikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.

Heb 9:11 Koma atafika Khristu, Mkulu wansembe wa zabwino ziri mkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi;

Heb 9:12 Kosati mwa mwazi wa mbuzi ndi ana ang’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, adalowa kamodzi kumalo wopatulika, atalandirapo chiwombolo chosatha chifukwa cha ife.

Heb 9:13 Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, ndi makala ang’ombe yamthandi wowazawaza pa iwo wodetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi:

Heb 9:14 Koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene adadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

Heb 9:15 Ndipo mwa ichi Iye ali nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti popeza kudachitika imfa yakuwombola zolakwa za pa chipangano choyamba kuti iwo, woyitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.

Heb 9:16 Pakuti pamene pali pangano pafunika pafike imfa ya mwini panganolo.

Heb 9:17 Pakuti chipangano chikhala ndi mphamvu atafa mwini wake; pakuti sichikhala ndi mphamvu konse pokhala mwini pangano ali ndi moyo;

Heb 9:18 Momwemonso chipangano choyambacho sichidakonzeka chopanda mwazi.

Heb 9:19 Pakuti pamene Mose adayankhulira anthu onse lamulo liri lonse monga mwa chilamulo, adatenga mwazi wa ana a ng’ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiyira ndi hisope, nawaza buku, ndi anthu onse,

Heb 9:20 Nati, Uwu ndi mwazi wa chipangano Mulungu adakulamulirani.

Heb 9:21 Ndiponso chihema ndi zotengera zonse za utumikiro adaziwaza momwemo ndi mwaziwo.

Heb 9:22 Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo popanda kukhetsa mwazi palibe kumasuka.

Heb 9:23 Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za m’Mwamba ziyeretsedwe ndi izi:- koma za m’mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zabwino zoposa izi.

Heb 9:24 Pakuti Khristu sadalowa m’malo wopatulika womangika ndi manja, amene ndi chinthunzinthu-nzi cha enieniwo; komatu m’Mwamba momwe kuwonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife:

Heb 9:25 Kosati kuti adzipereke yekha kawiri kawiri; monga mkulu wa nsembe alowa m’malo wopatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;

Heb 9:26 Chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawiri kawiri kuyambira makhazikitsidwe a maziko a dziko lapansi: koma tsopano kamodzi kokha kumatsiriziro a nthawi wawonekera Iye kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Mwiniyekha.

Heb 9:27 Ndipo monga kwayikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro:

Heb 9:28 Chotero Khristunso adaperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri; adzawonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.



10

Heb 10:1 Pakuti chilamulo, pokhala nacho chithunzithunzi cha zabwino zirimkudza, wosati chifaniziro chenicheni cha zinthunzo, sizikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.

Heb 10:2 Pakutero iwo sakadasiya kupereka nsembe? Chifukwa kuti wopembedzawo atatha kuyeretsadwa kamodzi sakadatha kukhala nacho chikumbumtima cha machimo.

Heb 10:3 Komatu mu nsembe izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka.

Heb 10:4 Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotse machimo.

Heb 10:5 Chotero ichi polowa m’dziko lapansi anena Nsembe ndi chopereka simudazifuna, koma thupi mudandikonzera Ine.

Heb 10:6 Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simudakondwera nazo;

Heb 10:7 Pamenepo ndidati, Tawonani ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu Mulungu.

Heb 10:8 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simudazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),

Heb 10:9 Pamenepo adati Iye, Tawonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu Mulungu. Iye anachotsa choyambacho, kuti akayike chachiwiricho.

Heb 10:10 Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi kwatha.

Heb 10:11 Ndipotu wansembe aliyense amayima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kuchotsa machimo:

Heb 10:12 Koma munthu uyu, m’mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, adakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire.

Heb 10:13 Kuchokera pamenepa adikira kufikira Adani ake ayikidwa akhale chopondapo mapazi ake.

Heb 10:14 Pakuti ndi nsembe imodzi adawayesera angwiro chikhalire iwo woyeretsedwa.

Heb 10:15 Pameneponso Mzimu Woyeranso achita umboni kwa ife: pakuti adatha kunena kale,

Heb 10:16 Iri ndi pangano ndidzapangana nawo, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: ndidzapereka malamulo anga akhale pa mtima pawo; ndipo pa nzeru zawo ndidzawalemba;

Heb 10:17 Ndipo machimo awo ndi zoyipa zawo sindidzakumbukiranso.

Heb 10:18 Tsopano pomwe pali chikhululukiro cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo.

Heb 10:19 Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m’malo wopatulika, ndi mwazi wa Yesu.

Heb 10:20 Panjira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera ife, mwa chotchinga, ndicho thupi lake;

Heb 10:21 Ndipo popeza tiri naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;

Heb 10:22 Tiyeni tiyandikire ndi mtima wowona, m’chitsimikizo chokwana chachikhulupiriro, ndi mitima yathu yowazidwa kuchotsa chikumbumtima choyipa, ndi matupi athu wosambitsidwa ndi madzi woyera.

Heb 10:23 Tiyeni tigwiritse chibvomerezo chosagwedera chachikhulupiriro chathu; (pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika:)

Heb 10:24 Ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.

Heb 10:25 Wosaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandawulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku liri kuyandika.

Heb 10:26 Pakuti tikachimwa ife eni ake mwadala, titatha kulandira chidziwitso cha chowonadi, palibenso nsembe ina yotsalira Chifukwa cha machimo,

Heb 10:27 Koma kulindira kwina kowopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuwononga wotsutsana nawo.

Heb 10:28 Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa wopanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:

Heb 10:29 Ndipo kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene adapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene adayeretsedwa nawo chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo?

Heb 10:30 Pakuti timdziwa Iye amene adati, kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Aterotu Ambuye adzaweruza anthu ake.

Heb 10:31 Kugwa m’manja a Mulungu wamoyo nkowopsa.

Heb 10:32 Koma takumbukirani masiku akale, m’menemo mudaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa:

Heb 10:33 Pena pochitidwa chinthu chowawitsidwa mwa matonzo ndi zisautso; pamene mudalawana nawo iwo wochitidwa zotere.

Heb 10:34 Pakuti mudamva chifundo ndi iwo a m’ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho chuma choposa chachikhalire m’mwamba.

Heb 10:35 Potero musataye kulimbika mtima kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu.

Heb 10:36 Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.

Heb 10:37 Pakuti katsala kanthawi kakang’ono ng’ono, ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa.

Heb 10:38 Tsopano wolungama adzakahla ndi moyo mwa m’chikhulupiriro: ndipo ngati munthu aliyense abwerera m’mbuyo, moyo wanga udzakhala wosa kondwera mwa iye.

Heb 10:39 Koma ife si ndife a iwo a kubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.



11

Heb 11:1 Tsopano chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.

Heb 11:2 Pakuti mwa ichi akulu adalandira umboni wabwino.

Heb 11:3 Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti mayiko ndi a m’mwamba womwe adakonzedwa ndi mawu a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizidapangidwa zochokera mwa zinthu zowonekazo.

Heb 11:4 Ndi chikhulupiriro Abeli adapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kayini, imene adachitidwa umboni nayo kuti adali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mphatso yake; ndipo mwa ichi iye, angakhale adafa ayankhulabe.

Heb 11:5 Ndi chikhulupiriro Enoki adatengeka kuti angawone imfa; ndipo sadapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asadamtenge, adachitidwa umboni kuti adakondweretsa Mulungu.

Heb 11:6 Koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa Iye; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye mwa khama.

Heb 11:7 Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisadapenyeke, ndi pochita mantha, adamanga chombo cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake; kumene adatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chiri monga mwa chikhulupiriro.

Heb 11:8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu poyitanidwa adamvera kutuluka kumka ku malo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo adatuluka wosadziwa kumene ankamukako.

Heb 11:9 Ndi chikhulupiriro adakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhala m’mahema pamodzi ndi Isake ndi Yakobo, wolowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo.

Heb 11:10 Pakuti adayembekezera mzinda wokhala nawo maziko, m’misiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.

Heb 11:11 Ndi chikhulupiriro Saranso adalandira mphamvu yakukhala ndi pakati, pa mbewu ndipo adabereka mwana patapita nthawi yake. Popeza adamuwerengera Iye wokhulupirika amene adalonjeza.

Heb 11:12 Mwa ichinso kudachokera kwa m’modzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji, ngati nyenyezi za m’mwamba, ndi ngati mchenga uli m’mbali mwa nyanja wosawerengeka.

Heb 11:13 Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, wosalandira malonjezano, komatu adawawona ndi kuwayankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi wogonera padziko.

Heb 11:14 Pakuti iwo akunena zinthu zotere awonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lawo.

Heb 11:15 Ndipo zowonadi, ngati iwo akadakhala wosamalira za dziko limene iwo adachokeralo, iwo akadakhala ndi mwayi wokhoza kubwerera.

Heb 11:16 Koma tsopano adakhumba dziko labwino, ndilo la Kumwamba: mwa ichi Mulungu sachita nawo manyazi pomuyitana Mulungu wawo; pakuti adawakonzera mzinda.

Heb 11:17 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, adapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano adapereka mwana wake wayekha;

Heb 11:18 Amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbewu yako idzayitanidwa:

Heb 11:19 Powerengera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, adamlandiranso.

Heb 11:20 Ndi chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau, zokhudzana ndi zinthu ziri nkudza.

Heb 11:21 Ndi chikhulupiriro Yakobo, pamene adalimkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yake.

Heb 11:22 Ndi chikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, adatchula za matulukidwe a ana a srayeli; nalamulira za mafupa ake.

Heb 11:23 Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akumbala, popeza adawona kuti ali mwana woyenera; ndipo sadawopa ulamuliro wa mfumu.

Heb 11:24 Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu adakana kutchulidwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farawo:

Heb 11:25 Nasankhula kuchitidwa zoyipa pamodzi ndi anthu a Mulungu kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoyipa zakanthawi kochepa;

Heb 11:26 Nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa chuma cha Aigupto; pakuti adapenyerera chobwezera cha mphotho.

Heb 11:27 Ndi chikhulupiriro adasiya a Aigupto, wosawopa mkwiyo wa mfumu; pakuti adapirira molimbika, monga ngati kuwona wosawonekayo.

Heb 11:28 Ndi chikhulupiriro adachita Paskha, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuwononga ana woyamba angawakhudze iwo.

Heb 11:29 Ndi chikhulupiriro adawoloka Nyanja Yofiyira kuyenda ngati pamtunda; ndipo a Aigupto poyesanso adamizidwa.

Heb 11:30 Ndi chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.

Heb 11:31 Ndi chikhulupiriro Rahabu wachiwerewere uja sadawonongeka pamodzi ndi wosamverawo, popeza adalandira wozonda ndi mtendere.

Heb 11:32 Ndipo ndinena chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideyoni, Baraki, Samsoni, Yefita; za Davide ndi Samueli ndi aneneri.

Heb 11:33 Amene mwa chikhulupiriro adagonjetsa ma ufumu, adachita chilungamo, adalandira malonjezano adatseka pakamwa mikango.

Heb 11:34 Nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, nalimbikitsidwa pokhala wofoka, adakula mphamvu kunkhondo, adapitikitsa magulu a nkhondo ya chilendo.

Heb 11:35 Akazi adalandira akufa awo mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena adanzunzidwa, wosalola kuwomboledwa, kuti akalandire chiwukitso chabwino.

Heb 11:36 Koma ena adayesedwa ndi matonzo ndi mikwapulo, inde nsinganso, ndi kuwatsekera m’ndende:

Heb 11:37 Adaponyedwa miyala, adachekedwa pakati, adayesedwa, adaphedwa ndi lupanga, adayendayenda wobvala zikopa za nkhosa, ndi zikopa za mbuzi, nakhala wosowa, wosautsidwa, wochitidwa zoyipa.

Heb 11:38 (Amenewo dziko lapansi silidayenera iwo:) wosokerera m’zipululu, ndi m’mapiri, ndi m’mapanga, ndi m’mawuna adziko.

Heb 11:39 Ndipo iwo onse atatha kulandira umboni mwa chikhulupiriro, sadalandira lonjezanolo.

Heb 11:40 Mulungu potikonzera ife zinthu zabwino, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife.



12

Heb 12:1 Chifukwa chake ifenso popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chiri chonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiyikira ife ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,

Heb 12:2 Poyang’ana Yesu amene ali woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu, chifukwa cha chimwemwe choyikidwa pamaso pake, adapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Heb 12:3 Pakuti talingilirani Iye amene adapirira ndi wochimwa ndi wotsutsana naye kotere kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.

Heb 12:4 Simudakana kufikira mwazi pomenyana nalo tchimo.

Heb 12:5 Ndipo mwayiwala dandauliro limene linena nanu monga ana, Mwana usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye:

Heb 12:6 Pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira.

Heb 12:7 Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake samlanga?

Heb 12:8 Koma ngati mukhala wopanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli a m’thengo, si ana ayi.

Heb 12:9 Komanso tidali nawo atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tidawalemekeza: kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

Heb 12:10 Pakutitu iwo adatilanga masiku wowerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nawo pachiyero chake.

Heb 12:11 Chotero chilango chiri chonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa: koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere kwa iwo wozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

Heb 12:12 Mwa ichi limbitsani manja wogowoka, ndi mawondo wolobodoka;

Heb 12:13 Ndipo lambulani misewu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m’njira, koma chichiritsidwe.

Heb 12:14 Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe m’modzi adzawona Ambuye;

Heb 12:15 Ndi kuyang’anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungaphuke muzu wina wakuwawa mtima ungabvute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nawo;

Heb 12:16 Kuti pangakhale wachiwerewere, kapena wam’nyozo, ngati Esau, amene adagulitsa ukulu wake wobadwa nawo ndi mtanda umodzi wachakudya.

Heb 12:17 Pakuti mudziwa kutinso pamene adafuna kulowa dalitsolo, adakanidwa pakuti sadapeza malo wolapa ngakhale adalifunafuna ndi misozi.

Heb 12:18 Pakuti simudayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe.

Heb 12:19 Ndi mawu a lipenga, ndi manenedwe a mawu, manenedwe amene iwo adamvawo adapempha kuti asawonjezerepo mawu:

Heb 12:20 (Pakuti sadakhoza kupirira nacho chimene adalamulidwacho, kuti ngati nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala kapena kulasidwa ndi mibvi:

Heb 12:21 Ndipo mawonekedwewo adali woopsa wotere, kuti Mose adati, Ndiwopatu ndi kunthunthumira:)

Heb 12:22 Komatu mwayandikira ku phiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi unyinji wochuluka wa angelo,

Heb 12:23 Ndi kwa mnsonkhano wa onse ndi mpingo wa wobadwa woyamba wolembedwa m’Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya wolungama woyesedwa angwiro,

Heb 12:24 Ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakuyankhula chokoma choposa mwazi wa Abeli.

Heb 12:25 Penyani kuti musamkane iye woyankhulayo. Pakuti ngati iwowa sadapulumuka, pomkana Iye amene adawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife ngati tipatuka kwa Iye woyankhula kuchokera Kumwamba:

Heb 12:26 Amene mawu ake adagwedeza dziko lapansi; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lapansi lokha, komanso la Kumwamba.

Heb 12:27 Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.

Heb 12:28 Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.

Heb 12:29 Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.



13

Heb 13:1 Chikondi cha pa abale chikhalebe

Heb 13:2 Musayiwale kuchereza alendo: pakuti mwa ichi ena adachereza angelo wosachidziwa.

Heb 13:3 Kumbukirani am’singa, monga am’singa anzawo; wochitidwa zoyipa, monga ngati inunso adatero nanu m’thupi.

Heb 13:4 Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa: pakuti achiwerewere ndi achigololo adzaweruzidwa ndi Mulungu.

Heb 13:5 Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zinthu zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye adati, sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Heb 13:6 Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzawopa chimene munthu adzandichitira.

Heb 13:7 Kumbukirani atsogoleri anu, amene adayankhula nanu Mawu a Mulungu: ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.

Heb 13:8 Yesu Khristu ali yemweyo dzulo ndi lero, ndi ku nthawi zonse.

Heb 13:9 Musatengedwe ndi ziphunzitso za mitundu mitundu, ndi zachilendo: pakuti mkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sadapindula nazo.

Heb 13:10 Tiri nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako.

Heb 13:11 Pakuti matupi anyama zija, mwazi wa izo umatengedwa ndi mkulu wa nsembe kulowa m’malo wopatulika, chifukwa cha zoyipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa.

Heb 13:12 Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva zowawa kunja kwa chipata.

Heb 13:13 Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa msasa wosenza tonzo lake.

Heb 13:14 Pakuti pano tiribe mzinda wokhalitsa, komatu tikufunafuna uli mkudzawo.

Heb 13:15 Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yobvomereza dzina lake.

Heb 13:16 Koma musayiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena: pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.

Heb 13:17 Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere: pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.

Heb 13:18 Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tiri nacho chikumbu mtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino.

Heb 13:19 Koma ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.

Heb 13:20 Tsopano Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wa mkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu.

Heb 13:21 Mukhale inu angwiro muntchito iri yonse yabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa inu zomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Ameni.

Heb 13:22 Ndipo ndikudandaulirani inu, abale, lolani mawu a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu kalata mwachidule.

Heb 13:23 Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga ndidzakuwonani inu.

Heb 13:24 Apatseni moni atsogoleri anu onse, ndi woyera mtima onse. Iwo onsenso a ku Italiya akupereka moni.

Heb 13:25 Chisomo chikhale ndi inu nonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE