Galatians


1

Gal 1:1 Paulo, mtumwi, (wosachokera kwa anthu, kapena kwa munthu koma kwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene adamuwukitsa Iye kwa akufa;)

Gal 1:2 Ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya:

Gal 1:3 Chisomo chikhale kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate ndi wochokera kwa Ambuye wathu Yesu Khristu,

Gal 1:4 Amene adadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m’nyengo yino ya pansi pano yoyipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu:

Gal 1:5 Kwa Iye ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.

Gal 1:6 Ndizizwa kuti msanga motere mulikutunsika kuchoka kwa iye amene adakuyitanani m’chisomo cha Khristu, kutsata ku Uthenga wina:

Gal 1:7 Umene suli wina; koma pali ena akubvuta inu, nafuna kuyipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.

Gal 1:8 Koma ngakhale ife, kapena m’ngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene tidakulalikirani ife akhale wotembereredwa.

Gal 1:9 Monga tidanena kale, kotero ine ndinenanso tsopano, ngati wina akulalikirani uthenga wabwino wosati umene mudawulandira, akhale wotembereredwa.

Gal 1:10 Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala mtumiki wa Khristu.

Gal 1:11 Pakuti ndikudziwitsani inu, abale za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.

Gal 1:12 Pakutitu sindidawulandira kwa munthu, kapena sindidauphunzira, komatu udadza mwa bvumbulutso la Yesu Khristu.

Gal 1:13 Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa chipembedzo cha chiyuda, kuti ndidazunza Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuwupasula:

Gal 1:14 Ndipo ndidakhala wopindulitsa mchipembedzo cha chiyuda kuposa ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndidakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.

Gal 1:15 Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene adandipatula, ndisanabadwe, nandiyitana ine mwa chisomo chake.

Gal 1:16 Ndikuti abvumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndikamlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindidafunsana ndi thupi ndi mwazi;

Gal 1:17 Kapena kukwera kumka ku Yerusalemu sindidamkako kwa iwo amene adakhala atumwi ndisadakhale mtumwi ine, komatu ndidapita ku Arabiya, ndipo ndidabweranso ku Damasiko.

Gal 1:18 Pamenepo patapita zaka zitatu, ndidakwera kumka ku Yerusalemu kukawonana naye Petro, ndipo ndidakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.

Gal 1:19 Koma wina wa atumwi sindidamuwona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

Gal 1:20 Ndipo tsopano zinthu ndikulembera kwa inu, tawonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.

Gal 1:21 Pamenepo ndinadza kumbali za Suriya ndi Kilikiya.

Gal 1:22 Koma ndidali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu:

Gal 1:23 Koma adalimkumva kokha, kuti iye wakutizunza ife kale, tsopano akulalikira chikhulupiriro chimene adachipasula kale.

Gal 1:24 Ndipo iwo adalemekeza Mulungu mwa ine.



2

Gal 2:1 Pamenepo popita zaka khumi ndi zinayi ndidakweranso kumka ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnaba, ndidamtenganso Tito.

Gal 2:2 Koma ndidakwera kumkako mwabvumbulutso; ndipo ndidawawuza iwo Uthenga Wabwino umene ndiulalikira pakati pa amitundu; koma m’seri kwa iwo womveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga chabe.

Gal 2:3 Komatu ngakhale Tito, amene adali ndi ine, ndiye Mhelene, adakakamizidwa kuti adulidwe:

Gal 2:4 Ndicho chifukwa cha abale wonyenga wolowezedwa m’seri amene adalowa m’seri kudzazonda ufulu wathu umene tiri nawo mwa khristu Yesu,kuti tikhale mgoli:

Gal 2:5 Kwa iwo sitidawapatse mpata mowagonjera ngakhale ola limodzi; kuti chowonadi cha Uthenga Wabwino chipitirirebe mwa inu.

Gal 2:6 Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati adali wotani kale, kulibe kanthu kwa) ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu iwo womvekawo sadandiwonjezera ine kanthu.

Gal 2:7 Koma pena, pakuwona kuti adayikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe:

Gal 2:8 (Pakuti Iye wakuchita mwa Petro kumtuma kwa wodulidwa yemweyo adachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu:)

Gal 2:9 Ndipo pakuzindikira chisomocho chidapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa, ndi Yohane amene adayesedwa mizati adapatsa ine ndi Barnaba dzanja lamanja lachiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa a mdulidwe

Gal 2:10 Pokhapo kuti tikumbukire a umphawi; ndicho chomwe ndidafulumira kuchichita.

Gal 2:11 Koma pamene Kefa anadza ku Antiyokeya ndidatsutsana naye pamaso pake, pakuti adatsutsika wolakwa.

Gal 2:12 Pakuti asadafike ena wochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, kuwopa iwo amene adali a ku mdulidwe.

Gal 2:13 Ndipo Ayuda wotsala adapusitsidwa pamodzi naye; kotero kuti Barnabanso adatengedwa ndi chinyengo chawo.

Gal 2:14 Komatu pamene ndidawona kuti sadali kuyenda kowongoka, monga mwa chowonadi cha Uthenga Wabwino, ndidati kwa Petro pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe wa amitundu, ndipo si wa Ayuda, mukangamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe wa Ayuda?

Gal 2:15 Ife amene tiri Ayuda pachibadwidwe ndipo osati wochimwa a kwa amitundu, Gal 2:16 Koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama mwa ntchito za lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tidakhulupirira mwa Yesu Khristu, kuti tikayesedwe wolungama mwa chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si mwa ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama mwa ntchito za lamulo.

Gal 2:17 Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa wolungama mwa Khristu, tipezedwanso tiri wochimwa tokha, kodi Khristu ali mtumiki wa uchimo chifukwa chake? Msatero ayi.

Gal 2:18 Pakuti ngati ndimanganso zinthu zimene ndaziwononga. Ndidzipangitsa ndekha kukhala wolakwa.

Gal 2:19 Pakuti ine mwa lamulo ndafa ku lamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.

Gal 2:20 Ndapachikidwa pamodzi ndi Khristu: sindikhalanso ndi moyo mwa ine ndekha, koma sindinenso koma Khristu akhala mwa ine: Ndipo moyo umene ndiri nawo tsopano m’thupi, ndikhala nawo mwa chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene adandikonda ine, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Gal 2:21 Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chidadza mwa lamulo,pamenepo Khristu adafa chabe.



3

Gal 3:1 Agalatiya wopusa inu adakulodzani ndani, kuti musamvere chowonadi, inu amene Yesu Khristu adawonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?

Gal 3:2 Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, kodi mudalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?

Gal 3:3 Kodi muli wopusa wotere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mwakhalitsidwa angwiro mwa thupi?

Gal 3:4 Kodi mudamva zinthu zowawa zambiri zotere kwachabe? Ngati ndi choncho ndiye kwachabe.

Gal 3:5 Iye amene atumikira kwa inu Mzimu, nachita zozizwitsa pakati pa inu, atero Iye kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva mwa chikhulupiriro?

Gal 3:6 Monga choteronso Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo.

Gal 3:7 Chotero zindikirani kuti iwo a chikhulupiriro omwewo ndiwo ana a Abrahamu.

Gal 3:8 Ndipo malembo pakuwoneratu kuti Mulungu adzayesa wolungama amitundu ndi chikhulupiriro, adayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse;

Gal 3:9 Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.

Gal 3:10 Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa ali yense wosakhala m’zonse zolembedwa m’buku la chilamulo, kuzichita izi.

Gal 3:11 Ndipo chidziwikiratu kuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu, pakuti; Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.

Gal 3:12 Koma chilamulo sindicho chochokera kuchikhulupiriro koma munthu wakuchita adzakhala ndi moyo ndi icho.

Gal 3:13 Khristu watiwombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m’malo mwathu; pakuti kwalembedwa, wotembereredwa ali yense wopachikidwa pamtengo.

Gal 3:14 Kuti dalitso la Abrahamu mwa Yesu Khristu, likadze kwa a mitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimu, mwa chikhulupiriro.

Gal 3:15 Abale ndinena monga mmanenedwe a anthu. Pangano, lingakhale la munthu, litatsimikizika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuwonjezerapo.

Gal 3:16 Ndipo tsopano malonjezano adanenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Sadanena, Ndipo kwa mbewu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, ndipo kwa mbewu yako ndiye Khristu.

Gal 3:17 Ndipo ichi ndinena, pangano limene lidatsirizika kale ndi Mulungu mwa Khristu,lamulo lidadza zitapita zaka silingathe kufafaniza kuti lonjezo likhale lopanda ntchito .

Gal 3:18 Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma Mulungu adampatsa Abrahamu mwa lonjezano.

Gal 3:19 Nanga kutumikira kwa chilamulo tsono? Chidawonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu ya Iye amene adamulonjeza imene adayilonjezera; ndipo chidakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe.

Gal 3:20 Koma nkhoswe siyikhala nkhoswe ya m’modzi; koma Mulungu ali m’modzi.

Gal 3:21 Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nawo malonjezano a Mulungu? Msatero ayi. Pakuti ngati chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kupatsa moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.

Gal 3:22 Komatu lembo lidatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa wokhulupirirawo.

Gal 3:23 Koma chisanadze chikhulupiriro tidasungidwa pomvera lamulo wotsekedwa ku chikhulupiriro chimene ku nthawi yake chidzakhala chibvumbulutsidwa.

Gal 3:24 Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe wolungama ndi chikhulupiriro.

Gal 3:25 Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso womvera namkungwi.

Gal 3:26 Pakuti inu nonse ,muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.

Gal 3:27 Pakuti nonse amene munabatizidwa mwa Khristu mudabvala Khristu.

Gal 3:28 Muno mulibe Myuda kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna kapena mkazi; pakuti muli nonse m’modzi mwa Khristu Yesu.

Gal 3:29 Koma ngati muli a Khristu, muli mbewu ya Abrahamu,ndiwolowa m’nyumba monga mwa lonjezano.



4

Gal 4:1 Tsopano ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali mwana, sasiyana ndi kapolo, angakhale iye ali mwini mbuye wa zonse;

Gal 4:2 Komatu ali wakumvera womsungira, ndi adindo, kufikira nthawi yoyikika kale ndi atate wake.

Gal 4:3 Koteronso ife, pamene tidali ana, tidali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi:

Gal 4:4 Koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu adatuma Mwana wake wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,

Gal 4:5 Kuti akawombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.

Gal 4:6 Ndipo popeza muli ana, Mulungu adatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m’mitima yanu, wofuwula Abba, Atate.

Gal 4:7 Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati ndi mwana,pamenepo wolowa nyumbanso ya Mulungu mwa Khristu.

Gal 4:8 Komatu pajapo posadziwa Mulungu inu, mudachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m’chibadwidwe chawo;

Gal 4:9 Koma tsopano podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofowoka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuyichitira ukapolo.

Gal 4:10 Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka.

Gal 4:11 Ndiwopera inu kuti kapena ndagwira ntchito pa inu pachabe.

Gal 4:12 Abale, ndikupemphani, khalani monga ine pakuti inenso ndiri monga inu. Simudandichitira choyipa ine.

Gal 4:13 Koma mudziwa kuti m’kufowoka kwa thupi ndidakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba.

Gal 4:14 Ndipo yeselo langa la thupi m’thupi inu simudalipeputsa, kapena simulikana, komatu mudandilandira ine monga m’ngelo wa Mulungu, monga khristu Yesu mwini;

Gal 4:15 Pamenepo dalitso lanu liri kuti? Limene mudaliyankhula. Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadakhala kotheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.

Gal 4:16 Kotero kodi ndasanduka m’dani wanu, chifukwa ndikuwuzani zowona?

Gal 4:17 Achita changu pa inu koma sikokoma ayi, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu.

Gal 4:18 Koma nkwabwino kuchita changu m’zabwino nthawi zonse, sipokha pokha pokhala nanu pamodzi ine.

Gal 4:19 Tiyana tanga, amene ndirikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu awumbika mwa inu.

Gal 4:20 Ndikhumba nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mawu anga; chifukwa ndikayikira za inu.

Gal 4:21 Ndiwuzeni, inu akukhumba kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo?

Gal 4:22 Pakuti kwalembedwa, kuti Abrahmu adali nawo ana amuna awiri, m’modzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi m’modzi wobadwa mwa mfulu.

Gal 4:23 Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano.

Gal 4:24 Zinthu izi ndizo zophiphiritsa: pakuti awa ndi mapangano awiri, m’modzi wa ku phiri la Sinayi, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.

Gal 4:25 Koma Hagara ndiye phiri la Sinayi, m’Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake.

Gal 4:26 Koma Yerusalemu wa Kumwamba uli wa ufulu, ndiwo amayi a ife tonse..

Gal 4:27 Pakuti kwalembedwa, Kondwera chumba iwe wosabala; yimba nthungululu, nufuwule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna.

Gal 4:28 Tsopano ife, abale, monga Isake, tiri ana a lonjezano.

Gal 4:29 Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi adazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano.

Gal 4:30 Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.

Gal 4:31 Chifukwa chake, abale, sitiri ana a mdzakazi, komatu a mfulu.



5

Gal 5:1 Khristu adatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu, chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.

Gal 5:2 Tawonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mudulidwa, Khristu simudzapindula naye kanthu.

Gal 5:3 Ndichitanso umboni kwa munthu yense wodulidwa, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse.

Gal 5:4 Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa wolungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.

Gal 5:5 Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera mwa chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo.

Gal 5:6 Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro chakuchita mwa chikondi.

Gal 5:7 Mudathamanga bwino; adakuletsani mdani kuti musamvere chowonadi?

Gal 5:8 Kukopa uku sikuchokera kwa Iye amene adakuyitanani.

Gal 5:9 Chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse.

Gal 5:10 Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nawo mtima wina; koma iye wakubvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chiweruzo chake.

Gal 5:11 Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chokhumudwitsa cha mtanda chidatha.

Gal 5:12 Ndidakakonda iwo ngakhale adakachotsedwa amene abvuta inu.

Gal 5:13 Pakuti adakuyitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nawo ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwa chikondi tumikiranani wina ndi mzake.

Gal 5:14 Pakuti mawu amodzi monga awa akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo: Uzikonda mzako monga udzikonda iwe mwini.

Gal 5:15 Koma ngati mulumana ndi kudyana wina ndi mzake, chenjerani mungamezane.

Gal 5:16 Koma ine ndinena, muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi.

Gal 5:17 Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zinthu zimene muzifuna musazichite.

Gal 5:18 Ngati Mzimu akusogolerani, simuli womvera lamulo.

Gal 5:19 Ndipo ntchito za thupi ziwonekera, ndizo chigololo, chiwerewere, chodetsa, kukhumba zonyansa.

Gal 5:20 Kupembedza mafano, ufiti, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,

Gal 5:21 Njiru, kupha, kuledzera, mchezo ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo monga ndachita, kuti iwo akuchita zinthu zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Gal 5:22 Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro.

Gal 5:23 Chifatso, chiletso; pochita zimenezi palibe lamulo.

Gal 5:24 Koma iwo a Khristu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.

Gal 5:25 Ngati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

Gal 5:26 Tisakhale wokhumba ulemerero wachabe woyambana wina ndi mzake, akuchitirana njiru wina ndi mzake.



6

Gal 6:1 Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu a uzimu mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Gal 6:2 Nyamuliranani zothodwetsa za wina ndi mzake, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.

Gal 6:3 Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.

Gal 6:4 Koma munthu aliyense ayesere ntchito yake, ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.

Gal 6:5 Pakuti munthu aliyense adzasenza katundu wake wa iye mwini.

Gal 6:6 Koma iye amene aphunzira mawu, ayenera agawire wophunzitsayo m’zinthu zonse zabwino.

Gal 6:7 Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso iye adzachituta.

Gal 6:8 Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chibvundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

Gal 6:9 Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufowoka.

Gal 6:10 Chifukwa chake, monga tili ndi mwayi tichitira anthu onse zabwino, makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.

Gal 6:11 Tawonani, malembedwe akuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini.

Gal 6:12 Onse amene akhumba kuwonekera wokoma m’thupi, iwowa akukangamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti akuwopa kuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu.

Gal 6:13 Pakuti angakhale iwo womwe wodulidwa sasunga lamulo; komatu akhumba inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m’thupi lanu.

Gal 6:14 Koma Mulungu akukana kuti ndisadzitamandire ine konse konse, iyayi, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.

Gal 6:15 Pakuti mwa Khristu Yesu, mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.

Gal 6:16 Koma onse amene ayenda monga mwa chilamulo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israyeli wa Mulungu.

Gal 6:17 Kuyambira tsopano palibe munthu andibvute, pakuti ndiri nazo ine m’thupi mwanga zipsera za AmbuyeYesu.

Gal 6:18 Abale mtendere wa Ambuye wathu Yesu Khristu ukhale ndi mzimu wanu. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE