Ephesians


1

Eph 1:1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, kwa woyera mtima amene ali mu Aefeso, ndi kwa iwo wokhulupirika mwa Khristu Yesu:

Eph 1:2 Chisomo chikhale kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi wochokera, kwa Ambuye Yesu Khristu.

Eph 1:3 Wolemekezeka Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m’zakumwamba mwa Khristu:

Eph 1:4 Monga adatisankha ife mwa Iye, asadakhazikike maziko a dziko lapansi, kuti tikhale ife woyera mtima, ndi wopanda chilema pamaso pake m’chikondi.

Eph 1:5 Adatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kudakomera chifuniro chake.

Eph 1:6 Kuti uyamikike ulemerero wa chisomo chake, chimene adatichitira ife kukhala wolandiridwa mwa wokondedwayo

Eph 1:7 Mwa Iye tiri ndi mawomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa chuma cha chisomo chake.

Eph 1:8 Chimene adatichulukitsira ife mu nzeru zonse, ndi chisamaliro.

Eph 1:9 Adatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kudamkomera ndi monga adatsimikiza mtima kale mwa Iye yekha.

Eph 1:10 Kuti pamakonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zinthu zonse mwa Khristu, za Kumwamba ndi za padziko: ngakhale zili mwa Iye:

Eph 1:11 Mwa Iye tidayesedwa cholowa chake, popeza tidakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse mwa uphungu wa chifuniro chake;

Eph 1:12 Kuti ife amene tidakhulupirira mwa Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.

Eph 1:13 Mwa Iyeyo inunso, mutamva mawu a chowonadi; Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, mudasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,

Eph 1:14 Ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti ake ake akawomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.

Eph 1:15 Mwa ichi inenso, m’mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu, ndi chikondi cha kwa oyera mtima onse.

Eph 1:16 Sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m’mapemphero anga;

Eph 1:17 Kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire Iye:

Eph 1:18 Ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuyitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa woyera mtima,

Eph 1:19 Ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife wokhulupira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba.

Eph 1:20 Imene adachititsa mwa Khristu, m’mene adamuwukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m’zakumwamba.

Eph 1:21 Pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lotchedwa, si m’nyengo yino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza:

Eph 1:22 Ndipo adakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu wa zonse ku mpingo.

Eph 1:23 Limene liri thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m’zonse.



2



Eph 2:1 Ndipo inu adakupatsani moyo, pokhala mudali akufa ndi zolakwa ndi zochimwa zanu;

Eph 2:2 Zimene mudayendamo kale, monga mwa mayendedwe adziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wamlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana akusamvera.

Eph 2:3 Amene ife tonsenso tidagonera pakati pawo kale, mzilakolako za thupi lathu, ndi kuchita chifuniro cha thupi, ndi za maganizo, ndipo tidali ana a mkwiyo chibadwire, monganso wotsalawo.

Eph 2:4 Koma Mulungu amene ali wachuma mu chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene adatikonda nacho,

Eph 2:5 Tingakhale tidali akufa m’zolakwa zathu, adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli wopulumutsidwa ndi chisomo;)

Eph 2:6 Ndipo adatiwukitsa pamodzi, natikazikitsa pamodzi m’zakumwamba mwa Khristu Yesu:

Eph 2:7 Kuti akawonetsere m’nyengo ziri mkudza chuma choposa cha chisomo chake, mkukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu.

Eph 2:8 Pakuti muli wopulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu; chiri mphatso ya Mulungu:

Eph 2:9 Chosachokera ku ntchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense.

Eph 2:10 Pakuti ife ndife opangidwa ake, wolengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu adazipangiratu, kuti tikayende m’menemo.

Eph 2:11 Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m’thupi, wotchedwa kusadulidwa ndi iwo wotchedwa a mdulidwe umene udachitika ndi manja;

Eph 2:12 Kuti nthawi ija mudali wopanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, wopanda chiyembekezo, ndi wopanda Mulungu m’dziko lapansi:

Eph 2:13 Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene mudali kutali kale, adakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Khristu.

Eph 2:14 Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene adachita kuti onse awiri akhale m’modzi, nagumula khoma lotchinga pakati pa ife.

Eph 2:15 Atachotsa udani m’thupi lake, ndiwo mawu a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu m’modzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere;

Eph 2:16 Ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m’thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nawo udaniwo:

Eph 2:17 Ndipo adadza, adalalikira mtendere kwa inu amene mudali kutali, ndi kwa iwo amene adali pafupi.

Eph 2:18 Kuti mwa Iye ife tonse awiri tiri nawo malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu m’modzi.

Eph 2:19 Tsopano simulinso alendo ndi wongobwera, komatu muli a mudzi womwewo wa woyera mtima ndi abanja la Mulungu;

Eph 2:20 Ndi womangidwa pa maziko wa atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;

Eph 2:21 Mwa Iye mamangidwe onse akhala wolumikizika pamodzi bwino, akula, akhale kachisi wopatulika mwa Ambuye;

Eph 2:22 Mwa Iye inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.



3

Eph 3:1 Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,

Eph 3:2 Ngatitu mudamva za machitidwe a chisomo cha Mulungu chimene adandipatsa ine cha kwa inu:

Eph 3:3 Ndi umo adandizindikiritsa chinsinsicho mwa bvumbulutso, ( monga ndidalemba kale mwachidule,

Eph 3:4 Chimene mukhoza kuzindikira nacho, pakuchiwerenga, chidziwitso changa m’chinsinsi cha Khristu.)

Eph 3:5 Chimene sadazindikiritsa ana a anthu m’mibado yina, monga adachibvumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake woyera mwa Mzimu:

Eph 3:6 Kuti amitundu ali wolowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zimzathu zathupilo, ndi wolandira nafe pamodzi malonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino;

Eph 3:7 Umene adandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene adandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake.

Eph 3:8 Kwa ine, wochepa ndi wochepetsa wa onse woyera mtima, adandipatsa chisomo ichi, ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;

Eph 3:9 Ndikuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chidabisika kuyambira kale kale mwa Mulungu wolenga zonse mwa Yesu Khristu:

Eph 3:10 Kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m’zakumwamba nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,

Eph 3:11 Monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene adachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu:

Eph 3:12 Amene tiri naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.

Eph 3:13 Mwa ichi ndikhumba kuti musade nkhawa m’zisautso zanga chifukwa cha inu ndiwo ulemerero wanu.

Eph 3:14 Chifukwa cha ichi ndipinda mawondo anga kwa Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,

Eph 3:15 Amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina,

Eph 3:16 Kuti akupatseni inu monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, mwa munthu wamkati mwanu.

Eph 3:17 Kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m’mitima yanu; kuti mukhale wozika mizu ndi wotsendereka m’chikondi,

Eph 3:18 Kuti mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi woyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndikuzama kwake ndi kukwera.

Eph 3:19 Ndikuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.

Eph 3:20 Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Eph 3:21 Kwa Iye kukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu kufikira mibado yonse ya nthawi za nthawi. Ameni.



4

Eph 4:1 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera mayitanidwe amene mudayitanidwa nawo,

Eph 4:2 Ndikuwonetsera kudzichepetsa konse ndi chifatso , ndi kuwonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mzake, mwa chikondi.

Eph 4:3 Ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere

Eph 4:4 Pali thupi limodzi ndi Mzimu m’modzi, monganso adakuyitanani m’chiyembekezo chimodzi cha mayitanidwe anu;

Eph 4:5 Ambuye m’modzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi,

Eph 4:6 Mulungu m’modzi ndi Atate wa onse, amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m’kati mwa inu nonse.

Eph 4:7 Ndipo kwa yense wa ife chapatsidwa chisomo, monga mwa muyeso wamphatso ya Khristu.

Eph 4:8 Chifukwa chake anena, m’mene adakwera Kumwamba adamanga ndende undende, naninkha za mphatso kwa anthu.

Eph 4:9 (Koma ichi, chakuti, adakwera, nchiyani nanga koma kuti Iye adatsikiranso ku madera akunsi kwa dziko?

Eph 4:10 Iye wotsikayo ndiye yemweyonso adakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.)

Eph 4:11 Ndipo Iye adapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa; ndi ena aphunzitsi;

Eph 4:12 Kuti akonzere woyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;

Eph 4:13 Kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, munthu wangwiro, ku muyeso wamsinkhu wachidzalo cha Khristu:

Eph 4:14 Kuti tisakhalenso makanda, wogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi matsenga a anthu, ndi kuchenjera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa.

Eph 4:15 Koma pakuyankhula chowonadi mwa chikondi; tikakule m’zinthu zonse, kufikira Iye; amene ali mutu ndiye Khristu:

Eph 4:16 Kuchokera mwa Iye m’thupi lonse, logwirizana ndi kulumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe athupi, kufikira chimangiriro chake mwa chikondi.

Eph 4:17 Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye kuti simuyendanso inu monganso amitundu ayendera, m’chitsiru cha mtima wawo,

Eph 4:18 Wodetsedwa m’nzeru zawo, woyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chiri mwa iwo, chifukwa cha kuchititsidwa khungu kwa mitima yawo:

Eph 4:19 Amenewo popeza sadazindikiranso kanthu konse, adadzipereka wokha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso pamodzi ndi umbombo.

Eph 4:20 Koma inu simudaphunzira Khristu chotero.

Eph 4:21 Ngatitu mudamva Iye, ndipo mudaphunzitsidwa mwa Iye monga chowonadi chiri mwa Yesu;

Eph 4:22 Kuti mubvule kunena za makhalidwe anu woyamba a munthu, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za chinyengo;

Eph 4:23 Koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu.

Eph 4:24 Ndipo mubvale munthu watsopano, amene adalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha chowonadi.

Eph 4:25 Mwa ichi, mutataya zonama, yankhulani zowona yense ndi mzake: pakuti tiri ziwalo wina ndi mzake.

Eph 4:26 Kwiyani, koma musachimwe: dzuwa lisalowe muli chikwiyire:

Eph 4:27 Ndiponso musampatse malo mdiyerekezi.

Eph 4:28 Wakubayo asabenso: koma makamaka agwiritse ntchito nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.

Eph 4:29 Nkhani yonse yobvunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira, kuti ikatumikire chisomo kwa iwo akumva.

Eph 4:30 Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene mudasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la mawomboledwe.

Eph 4:31 Chiwawo chonse ndi kupsa mtima ndi mkwiyo ndi chiwawa ndi mayakhulidwe oyipa zichotsedwe kwa inu pamodzi ndi zoyipa zonse.

Eph 4:32 Ndipo mukhalirane a chikondi wina ndi mzake amtima wabwino akukhululukirana nokha, monganso Mulungu chifukwa cha Khristu adakhululukira inu.





5

Eph 5:1 Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana wokondedwa;

Eph 5:2 Ndipo yendani m’chikondi monganso Khristu adakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

Eph 5:3 Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiliro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu monga kuyenera woyera mtima.

Eph 5:4 Kapena chinyanso ndi kuyankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.

Eph 5:5 Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosilira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

Eph 5:6 Asakunyengeni inu munthu ndi mawu wopanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

Eph 5:7 Chifukwa chake musakhale wolandirana nawo.

Eph 5:8 Pakuti kale mudali mdima, koma tsopano muli kuwunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuwunika;

Eph 5:9 Pakuti chipatso cha Mzimu tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo ndi chowonadi;)

Eph 5:10 Kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani.

Eph 5:11 Ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu; koma makamakanso muzitsutse.

Eph 5:12 Pakuti zochitidwa nawo m’seri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi

Eph 5:13 Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuwunika, ziwonekera; pakuti chonse chakuwonetsa chiri kuwunika

Eph 5:14 Mwa ichi anena khala maso wogona iwe, nuwuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.

Eph 5:15 Potero penyani bwino umo muyendera, si monga wopanda nzeru, koma monga anzeru.

Eph 5:16 Akuchita mwachangu, popeza masiku ali woyipa.

Eph 5:17 Chifukwa chake musakhale wosadziwa koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani!

Eph 5:18 Ndipo musaledzere naye vinyo, m’mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu;

Eph 5:19 Ndikudziyankhulira nokha ndi masalmo, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba mokometsera Ambuye mumtima mwanu.

Eph 5:20 Ndikupereka mayamiko kwa Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zinthu zonse, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;

Eph 5:21 Ndi kumverana wina ndi mzake m’kuwopa Mulungu.

Eph 5:22 Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye.

Eph 5:23 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo; ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

Eph 5:24 Choncho monga Mpingo umvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna awo m’zinthu zonse.

Eph 5:25 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu adakonda Mpingo, adzipereka yekha m’malo mwake;

Eph 5:26 Kuti akaupatule, atauyeretsa ndi kuusambitsa ndi madzi mwa mawu,

Eph 5:27 Kuti Iye akadziyikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere: komatu kuti ukhale woyera, ndi wopanda chilema.

Eph 5:28 Koteronso amuna azikonda akazi awo a iwo wokha monga ngati matupi a iwo wokha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha.

Eph 5:29 Pakuti munthu sanadane nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Ambuye ndi Mpingo.

Eph 5:30 Pakuti ife tiri ziwalo za thupi lake, za m’nofu wake ndi mafupa ake.

Eph 5:31 Chifukwa cha ichi munthu adzasiya atate ake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.

Eph 5:32 Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo.

Eph 5:33 Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo awonetsetse kuti akulemekeza mwamuna wake.



6

Eph 6:1 Ananu mverani akukubalani mwa Ambuye: pakuti ichi nchabwino.

Eph 6:2 Lemekeza atate wako ndi amako; (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano;)

Eph 6:3 Kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yayikulu padziko.

Eph 6:4 Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu: komatu muwalere iwo ndi chilangizo cha Ambuye.

Eph 6:5 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwawopa ndi kunthunthumira nawo, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwa Khristu;

Eph 6:6 Simonga mwa kutumikira mwachinyengo, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima;

Eph 6:7 Akuchita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye, si anthu ayi.

Eph 6:8 Podziwa kuti chinthu chabwino chiri chonse munthu aliyense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

Eph 6:9 Ndipo ambuye inu, muwachitire zinthu zomwezi iwowa; nimuleke kuwawopsa; podziwa kuti Ambuye wawo ndi wanu ali m’Mwamba ndipo palibe tsankhu kwa Iye.

Eph 6:10 Chotsalira abale, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake.

Eph 6:11 Tabvalani zida zonse za Mulungu; kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdiyerekezi.

Eph 6:12 Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika adziko lapansi a mdima uno, ndi a mizimu yoyipa yamulengalenga.

Eph 6:13 Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuyima chitsutsire pofika tsiku loyipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.

Eph 6:14 Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m’chuwuno mwanu ndi chowonadi mutabvalanso chapachifuwa cha chilungamo;

Eph 6:15 Ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere.

Eph 6:16 Koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoze kuzima nacho mibvi yonse yoyaka moto ya woyipayo.

Eph 6:17 Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mawu a Mulungu.

Eph 6:18 Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo kudikirira m`menemo ndi chipiriro chonse ndi kupembedzera woyera mtima onse.

Eph 6:19 Ndi kwa ine ndemwe kuti andipatse mawu, kuti ndikatsegule pakamwa panga molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino,

Eph 6:20 Chifukwa cha umene ndiri kazembe wa mu unyolo, kuti m’menemo ndikayankhule molimbika, monga ndiyenera kuyankhula.

Eph 6:21 Koma kuti mukadziwe inunso za makhalidwe anga, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tukiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye.

Eph 6:22 Amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu.

Eph 6:23 Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Eph 6:24 Chisomo chikhale ndi iwo onse amene akonda Ambuye wathu Yesu Khristu mowonadi. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE