Colossians


1

Col 1:1 Paulo,mtumwi wa Yesu Khristu mwachifuniro cha Mulungu,ndi Timoteo mbale wathu.

Col 1:2 Kwa woyera mtima ndi abale wokhulupirika,mwa Khristu aku Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu..

Col 1:3 Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi kupempherera inu nthawi zonse,

Col 1:4 Kuyambira pamene tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu,ndi chikondi muli nacho kwa woyera mtima onse,

Col 1:5 Chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu m’Mwamba,chimene mudachimva kale m’mawu a chowonadi cha Uthenga Wabwino;

Col 1:6 Umene udafikira kwa inu;monganso m’dziko lonse lapansi umabala zipatso,numakula monganso mwa inu,kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira Chisomo cha Mulungu m’chowonadi;

Col 1:7 Monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mzathu wokondedwa,ndiye mtumiki wokhulupirika wa Khristu chifukwa cha ife;

Col 1:8 Amenenso adatifotokozera chikondi chanu mwa Mzimu.

Col 1:9 Mwa ichi ifenso,kuyambira tsiku limene tidamva,sitileka kupempherera inu, ndi kukhumba kuti mukadzadzidwe ndichizindikiritso cha chifuniro chake munzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu;

Col 1:10 Kuti mukayende koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo,ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino,ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu;

Col 1:11 Wolimbikitsidwa m’chilimbiko chonse,monga mwa mphamvu ya ulemerero wake,kuchitira chipiliro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe;

Col 1:12 Ndikuyamika Atate,amene adatiyeneretsa ife kulandirana nawo cholowa cha woyera mtima m’kuwunika:

Col 1:13 Amene adatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima,natisunthitsa kutilowetsa m’ufumu wa Mwana wa chikondi chake.

Col 1:14 Amene tiri nawo mawomboledwe mwa mwazi wa m’kukhulukidwa kwa zochimwa zathu:

Col 1:15 Amene ali fanizo la Mulungu wosawonekayo,wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse;

Col 1:16 Pakuti mwa iye ,zidalengedwa zonse za m’mwamba,ndi za padziko zowoneka ndi zosawoneka,kapena mipando ya chifumu, kapena maufumu kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zidalengedwa mwa iye ndi kwa iye.

Col 1:17 Ndipo iye ali woyamba wa zonse;ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.

Col 1:18 Ndipo Iye ali mutu wathupi, Mpingo ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa;kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.

Col 1:19 Pakuti kudamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire;

Col 1:20 Mwa iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye yekha, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu ndinena, kapena pali zinthu za padziko,kapena za m’mwamba.

Col 1:21 Ndipo inu, wokhala alendo akale ndi adani m’chifuwa chanu m’ntchito zoyipazo,koma tsopano adakuyanjanitsani.

Col 1:22 M’thupi lake la imfayo,kukayimika inu woyera,ndi wopanda chilema ndi wosatsutsika pamaso pake;

Col 1:23 Ngatitu mukhalabe m’chikhulupiriro,wochilimika ndi wokhazikika ndi wosasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva,wolalikidwa cholengedwa chonse chapansi pa thambo;umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.

Col 1:24 Amene tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu; ndi kukwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khritsu mthupi langa chifukwa cha thupi lake; ndiwo Mpingo;

Col 1:25 Amene ndidakhala mtumiki wake monga mwa udindo wa Mulungu umene adandipatsa ine wakuchitira inu,wakukwaniritsa mawu aMulungu;

Col 1:26 Ndiwo chinsinsicho chidabisika kuyambira pa nthawizo,ndi kuyambira pa mibadoyo;koma adachiwonetsa tsopano kwa woyera mtima ake;

Col 1:27 Kwa iwo amene Mulungu adafuna kuwazindikiritsa chuma chimene chiri chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu ,ndiye Khritsu mwa inu,chiyembekezo cha ulemerero;

Col 1:28 Amene timlalikira ife,ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyenze mu nzeru zonse, kuti tiwonetsere munthu aliyense wangwiro mwa Khritsu Yesu:

Col 1:29 Kuchita ichi ndidzibvutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.



2

Col 2:1 Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndiri nayo chifukwa cha inu,ndi iwowa a m’Lawodikaya,ndi onse amene sadawone nkhope yanga m’thupi;

Col 2:2 Kuti itonthozeke mitima yawo,nalumikizike pamodzi iwo m’chikondi kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso,kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu ndi cha Atate ndiye Khristu;

Col 2:3 Amene chuma chonse cha nzeru ndi chidziwitso chibisika mwa Iye.

Col 2:4 Ichi ndinena kuti munthu asakusocheletseni inu ndi mawu wokopa kopa.

Col 2:5 Pakuti ndingakhale ndiri kwina m’thupi,komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu,wokondwera pakupenya makonzedwe anu,ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.

Col 2:6 Chifukwa chake monga momwe mudalandira Khristu Yesu Ambuye chotero muyende mwa Iye.

Col 2:7 Wozika mizu ndi womangiririka mwa Iye,ndi wokhazikika m’chikhulupiriro,monga mudaphunzitsidwa,ndi kuchulukitsa chiyamiko.

Col 2:8 Chenjerani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma,mwa kukonda nzeru kwake,ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu,potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu.

Col 2:9 Pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m’thupi.

Col 2:10 Ndipo inu muli angwiro mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;

Col 2:11 Amenenso mumadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m’mabvulidwe a thupi, mu m’dulidwe wa Khristu:

Col 2:12 Popeza mudayikidwa m’manda pamodzi ndi Iye mu ubatizo,momwemonso mudaukitsidwa pamodzi ndi Iye m’chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene adamuwukitsa Iye kwa akufa.

Col 2:13 Ndipo inu, pokhala akufa m’zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, adakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m’mene adakhululukira inu zolakwa zonse;

Col 2:14 Adatha kutifanizira cha pa ifecho cholembedwa m’zoyikikazo,chimene chidali chotsutsana nafe;ndipo adachichotsera pakatipo,ndi kuchikhomera ichi pamtanda wake;

Col 2:15 Atabvula maukulu ndi maulamuliro, adawawonetsera poyera, nawagonjetsera iwo m`menemo.

Col 2:16 Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m’chakudya, kapena m`chakumwa, kapena m’kunena za tsiku la phwando, kapena lokhala mwezi kapena masiku asabata:

Col 2:17 Zimene ndizo mthunzi wa zinthu zilimkudzazo; koma thupi ndi la Khristu.

Col 2:18 Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphoto yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo,ndi kukhalira mu izi zimene sadaziwona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake.

Col 2:19 Wosagwira mutuwo kuchokera kwa Iye amene thupi lonse limodzi lilumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.

Col 2:20 Chiyani nanga ngati mudafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji ku zoyikikazo,monga ngati moyo wanu mukhala nawo m’dziko lapansi.

Col 2:21 (Usayikapo dzanja;usalawa;usakhudza;

Col 2:22 Ndizo zonse zakuwonongedwa pochita nazo)monga mwa malangizo ndi maphunziro wa anthu?

Col 2:23 Zimene ziri nawotu manenedwe anzeru m` chifuniro chakudzipembedza ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma ziribe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.



3

Col 3:1 Chifukwa chake ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu,funani za kumwamba,kumene kuli Khristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.

Col 3:2 Lingalirani zakumwamba osati za padziko lapansi ayi.

Col 3:3 Pakuti mudafa,ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Col 3:4 Pamene Khristu adzawoneka amene ndi moyo wathu, pamenepo inunso mudzawonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero.

Col 3:5 Chifukwa chake fetsani ziwalozo ziri padziko; chiwerewere, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choyipa, ndi chisiliro, chimene chiri kupembedza mafano:

Col 3:6 Chifukwa cha zinthu izi zomwe umadza m’kwiyo wa Mulungu pa ana akusamvera:

Col 3:7 Zimene mudayendamo inunso kale, pamene mudakhala ndi moyo wanu m’menemo.

Col 3:8 Koma tsopano mudataya inunso zonse: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m’kamwa mwanu.

Col 3:9 Musamanamizana wina ndi mzake;popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake;

Col 3:10 Ndipo mudabvala munthu watsopano, amene alikukonzeka m’nzeru mwa chifaniziro cha Iye adamlenga iye:

Col 3:11 Pamene palibe Mhelene ndi Myuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wotchedwa wakunja, Msikuti, kapolo,mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m’zonse.

Col 3:12 Chifukwa chake bvalani monga wosankhika a Mulungu, woyera mtima ndi wokondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso kuleza mtima;

Col 3:13 Kulolerana wina ndi mzake, ndi kukhululukirana eni nokha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mzake; monganso Khristu, adakhululukira inu, teroni inunso.

Col 3:14 Koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima waungwiro wonse.

Col 3:15 Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m’mitima yanu, kulingakonso mudayitanidwa m’thupi limodzi ndipo khalani akuyamika.

Col 3:16 Aloleni Mawu a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndikuphunzitsa ndi kuyambirirana eni nokha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo za uzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi Chisomo mumtima mwanu.

Col 3:17 Ndipo chiri chonse, mukachichita m’mawu kapena muntchito, chitani zones m’dzina la Ambuye Yesu, ndikuyamika Mulungu Atate mwa Iye.

Col 3:18 Akazi inu mverani amuna anu,monga kuyenera mwa Ambuye.

Col 3:19 Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.

Col 3:20 Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.

Col 3:21 Atate inu,musaputa ana anu,kuti angataye mtima.

Col 3:22 Akapolo inu, mverani m’zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga wokondweretsa anthu, komatu amtima umodzi, akuopa Ambuye;

Col 3:23 Chiri chonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, wosati kwa anthu ayi;

Col 3:24 Podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; pakuti mutumikira Ambuye Khristu mwa ukapolo.

Col 3:25 Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama adachitacho; ndipo palibe tsankhu pakati pa anthu.



4

Col 4:1 Ambuye inu chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana, podziwa kuti inunso muli naye Mbuye m’Mwamba.

Col 4:2 Chitani khama m’kupemphera,nimudikire momwemo ndi chiyamiko;

Col 4:3 Ndikutipemphereranso ife pomwepo, kutiMulungu atitsegulire ife pakhomo pa mawu,kuti tiyankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m’ndende;

Col 4:4 Kuti ndichiwonetse ichi monga ndiyenera kuyankhula.

Col 4:5 Muyende mu nzeru ndi iwo akunja, kuchita changu nthawi ingatayike.

Col 4:6 Mawu anu akhale m’chisomo nthawi zonse wokoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Col 4:7 Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tukiko,m’bale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mzanga mwa Ambuye:

Col 4:8 Amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichi chomwe,kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu;

Col 4:9 Pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali m`modzi wa inu zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu zinthu zonse zimene zachitika kuno.

Col 4:10 Aristarko wa m’ndende mzanga akupatsani moni, ndi Marko,msuweni wa Barnaba (amene mudalandira malamulo ngati abwera kwa inu; )

Col 4:11 Ndi Yesu,wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo wokha ndiwo antchito amzanga a mu Ufumu wa Mulungu;ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.

Col 4:12 Akupatsani moni Epafra ndiye m`modzi wa inu, ndiye mtumiki wa Yesu Khristu, wakulimbika chifukwa cha inu m’mapemphero ake masiku onse,kuti mukayime angwiro ndi wodzazidwa m’chifuniro chonse cha Mulungu.

Col 4:13 Pakuti ndimachitira Iye umboni ali ndi changu chachikulu cha kwa inu, ndi iwo a m’Lodikaya, ndi iwo a m’Herapoli.

Col 4:14 Luka sing’anga wokondedwa,ndi Dema,akupatsani moni.

Col 4:15 Patsani moni abale ali m’Lodikaya, ndi Numfa, ndi Mpingowo wa m’nyumba yawo.

Col 4:16 Ndipo pamene muwerenga kalata uyu,amuwerengenso ku Mpingo wa ku Lodikaya, ndi inunso momwemo muwerenge wa ku Lodikaya.

Col 4:17 Ndipo nenani kwa Arkipo, samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye kuti uwukwanitse.

Col 4:18 Moni wa dzanja langa ine Paulo, kumbukirani nsinga zanga. Chisomo chikhale nanu. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE