Acts


1

Act 1:1 Zolemba zoyamba ndidakulembera Teofilo, mawu aja ndidakonza, za zonse Yesu adayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa,

Act 1:2 Kufikira tsiku lija adatengedwa kumka Kumwamba, atatha Iye kuwalamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha.

Act 1:3 Kwa iwonso amene adadziwonetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, nawonekera kwa iwo masiku makumi anayi, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu:

Act 1:4 Ndiponso posonkhana nawo pamodzi, adawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu adikire lonjezano la Atate, limene, adati, mudalimva kwa Ine.

Act 1:5 Pakuti Yohane adabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asadapite masiku ambiri.

Act 1:6 Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, adamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?

Act 1:7 Koma Iye adati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate adaziyika muwulamuliro wake wa Iye yekha.

Act 1:8 Komatu mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake adziko.

Act 1:9 Ndipo m’mene adanena zinthu izi, ali chipenyerere iwo, adanyamulidwa; ndipo mtambo udamlandira Iye kumchotsa pamaso pawo.

Act 1:10 Ndipo pakukhala iwo chipenyerere Kumwamba pomuwona Iye alimkupita kumwamba, tawonani, amuna awiri wobvala zoyera adayimilira pambali pawo;

Act 1:11 Amenenso adati; Amuna inu a ku Galileya, muyimiranji ndi kuyang’ana Kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzabwera momwemo monga mudamuwona ali mkupita Kumwamba.

Act 1:12 Pamenepo iwowa anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri lonenedwa la Azitona, limene kuchokera ku Yerusalemu, ndi ulendo woyendako pa tsiku la sabata.

Act 1:13 Ndipo pamene adalowa, adakwera ku chipinda cha pamwamba, kumene adali kukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andreya, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeyu ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyu, ndi Simoni Zelota ndi Yuda mwana wa Yakobo.

Act 1:14 Iwo onse adali kukangalika ndi mtima umodzi m’kupemphera, ndi kupembedzera pamodzi ndi akazi,ndi Mariya, amake a Yesu, ndi abale ake omwe.

Act 1:15 Ndipo m’masiku awa adayimilira Petro pakati pa wophunzira, nati (nambala ya maina a anthu wosonkhana pamalo pomwepo ndiwo ngati zana limodzi ndi makumi awiri)

Act 1:16 Amuna inu, abale, kudayenera kuti lemba likwaniritsidwe, limene Mzimu Woyera adayamba kunena mwa m’kamwa mwa Davide za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.

Act 1:17 Chifukwa adali wowerengedwa mwa ife, ndipo adalandira gawo lake la utumiki uwu.

Act 1:18 Munthu uyu tsono adadzigulira munda ndi mphotho ya zoipa; ndipo adagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse adakhuthuka;

Act 1:19 Ndipo chidadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti mundawo m’chinenedwe chawo umatchedwa Akeldana, ndiwo munda wa mwazi.

Act 1:20 Pakuti kwalembedwa m’buku la Masalmo, pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wogonapo; ndipo uyang’aniro wake autenge wina.

Act 1:21 Potero kuyenera kuti wina wa amunawo adatsatana nafe nthawi yonseyi imene Ambuye Yesu adalowa ndikutuluka mwa ife,

Act 1:22 Kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija Iye adatengedwa kumka Kumwamba kutisiya ife, m’modzi ayenera kusankhidwa akhale mboni ya kuwuka kwake pamodzi ndi ife.

Act 1:23 Ndipo adayimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba, amene adatchedwanso Yusto, ndi Matiya.

Act 1:24 Ndipo adapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri m’modziyo amene mudamsankha,

Act 1:25 Kuti alowe malo a utumiki uwu ndi Utumwi, kuchokera komwe Yudase adapatuka, kuti apite ku malo a iye yekha.

Act 1:26 Ndipo adayesa mayere pa iwo; ndipo adagwera Matiya; ndipo adawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi m’modzi wa Atumwi.



2

Act 2:1 Ndipo pamene tsiku la Pentekoste lidafika, iwo onse adali amtima umodzi pa malo amodzi.

Act 2:2 Ndipo mwadzidzidzi adamveka mawu wochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene adalikukhalamo.

Act 2:3 Ndipo pamenepo adawonekera kwa iwo malilime wogawanika, wonga a moto; ndipo udakhala pa iwo onse wayekha wayekha.

Act 2:4 Ndipo iwo adadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula ndi malilime ena, monga Mzimu adawayankhulitsa.

Act 2:5 Ndipo adali mu Yerusalemu wokhalako Ayuda, amuna wopembedza, wochokera ku mtundu uli wonse pansi pa thambo.

Act 2:6 Koma pochitika mawu awa, khamu la lidasonkhanalo, lidasokonezeka popeza aliyense wa iwo adamva iwowa alikuyankhula m’chiyankhulidwe chake cha iye yekha.

Act 2:7 Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena wina ndi mzake, Tawonani, awa onse ayankhulawa sali Agalileya kodi?

Act 2:8 Ndipo nanga, ife tikumva bwanji munthu aliyense, m’chiyankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho?

Act 2:9 Aparti ndi Amedi, ndi Ayelami, ndi iwo wokhala m’Mesopotamiya, m’Yudeya ndiponso m’Kapadokiya, m’Ponto, ndi m’Asiya;

Act 2:10 M’Frugiya, ndiponso m’Pamfuliya, m’Aigupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo wochokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso wopinduka,

Act 2:11 Akrete ndi Aarabu tikuwamva iwo alikuyankhula m’malilime athu za ntchito zodabwitsa za Mulungu.

Act 2:12 Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mzake, kodi ichi n’chiyani?

Act 2:13 Koma ena adawaseka, nanena kuti anthu awa Akhuta vinyo wa lero.

Act 2:14 Koma Petro, adayimilira pamodzi ndi khumi ndi m’modziwo, nakweza mawu ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Akuyudeya, ndi inu nonse wokhala m’Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu ku mawu anga.

Act 2:15 Pakuti awa sadaledzere monga muyesa inu; pakuti ndi ola lachitatu lokha la tsiku;

Act 2:16 Komatu ichi ndi chimene chidanenedwa ndi m’neneri Yoweli;

Act 2:17 Ndipo kudzali m’masiku wotsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi liri lonse ndipo ana anu amuna, ndi a akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzawona masomphenya, akulu anu adzalota maloto:

Act 2:18 Ndiponso pa atumiki anga ndi pa adzakazi anga m’masiku awa; ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.

Act 2:19 Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa pansi pa thambo la kumwamba, ndi zizindikiro pansi pa dziko lapansi Mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;

Act 2:20 Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi lowonekera;

Act 2:21 Ndipo kudzali,kuti yense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.

Act 2:22 Amuna inu Aisrayeli, mverani mawu awa; Yesu Mnazarate, mwamuna wobvomerezedwa ndi Mulungu pakati pa inu, mwa zozizwa ndi zizindikiro, zimene Mulungu adazichita mwa Iye pakati pa inu, monga mudziwa nokha.

Act 2:23 Ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woyikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwamtenga ndi kumupha ndi manja a anthu wosayeruzika;

Act 2:24 Yemweyo Mulungu adamuwukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikudali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.

Act 2:25 Pakuti Davide anena za Iye, ndidawona Mbuye pamaso panga nthawi zonse, chifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndisasunthike.

Act 2:26 Mwa ichi udakondwera mtima wanga, ndipo lidasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m’chiyembekezo.

Act 2:27 Pakuti simudzasiya moyo wanga ku Gehena, kapena simudzapereka woyera wanu awone chibvunde.

Act 2:28 Mundidziwitsa ine njira za moyo; mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.

Act 2:29 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posawopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira nayikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.

Act 2:30 Potero pokhala m’neneri iye, ndi kudziwa kuti Mulungu adamulumbirira Iye lumbiro, kuti mwa chipatso cha m’chuwuno mwake, kolingana ndi thupi, adzamuwukitsira Khristu, kuti adzakhale pa mpando wachifumu wake;

Act 2:31 Iye powona ichi kale, adayankhula za kuwuka kwa Khristu, kuti sadasiyidwa m’Gehena, ndipo thupi lake silidawona chibvunde.

Act 2:32 Yesu ameneyo, Mulungu adamuwukitsa za ichi tiri mboni ife tonse.

Act 2:33 Potero, popeza adakwezedwa ndi dzanja la manja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, adatsanulira ichi, chimene inu tsopano mupenya ndi kumva.

Act 2:34 Pakuti Davide sadakwera Kumwamba ayi; koma iye mwiniyekha adati, Ambuye adati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa.

Act 2:35 Kufikira ndikayike adani ako chopondapo mapazi ako.

Act 2:36 Chifukwa chake lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti Mulungu adamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu mudampachika.

Act 2:37 Koma pamene adamva ichi, adalaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?

Act 2:38 Pamenepo Petro adati kwa iwo, lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Act 2:39 Pakuti lonjezano liri kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, ngakhale onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitana.

Act 2:40 Ndipo ndi mawu ena ambiri adachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse nokha kwa m’bado uno wokhotakhota.

Act 2:41 Pamenepo iwo amene adalandira mawu ake mokondwera anabatizidwa; ndipo adawonjezeka tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

Act 2:42 Ndipo iwo adali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi m’chiyanjano, m’kunyema mkate ndi mapemphero .

Act 2:43 Koma padadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zidachitika mwa atumwi.

Act 2:44 Ndipo onse wokhulupirira adali pamodzi, nakhala nazo zinthu zonse zodyerana.

Act 2:45 Ndipo zimene adali nazo, ndi chuma chawo, adazigulitsa nazigawira kwa anthu onse, monga yense adasowera.

Act 2:46 Ndipo tsiku ndi tsiku adali chikhalire ndi mtima umodzi m’kachisi, ndipo adanyema mkate kuchokera nyumba ndi nyumba, nalandira chakudya ndi chisangalalo, ndi mtima umodzi.

Act 2:47 Nalemekeza Mulungu ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye adawawonjezera mumpingo tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.



3

Act 3:1 Tsopano Petro ndi Yohane adalikukwera kupita kukachisi pa ola lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinayi

Act 3:2 Ndipo munthu wina wosayenda chibadwire adanyamulidwa, amene amkamuyika tsiku ndi tsiku pakhomo la kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zachifundo kwa iwo wolowa m’kachisi;

Act 3:3 Ameneyo pakuwona Petro ndi Yohane akuti alowe m’kachisi, adapempha alandire zachifundo.

Act 3:4 Ndipo, Petro pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane adati, Tiyang’ane ife.

Act 3:5 Ndipo iye adabvomereza iwo, nalingilira kuti adzalandira kanthu kuchokera kwa iwo.

Act 3:6 Pamenepo Petro adati, siliva ndi golide ndiribe; koma chimene ndiri nacho, ichi ndikupatsa, M’dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, nyamuka nu yende.

Act 3:7 Ndipo adamgwira iye ku dzanja lake lamanja, nam’nyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zidalimbikitsidwa.

Act 3:8 Ndipo adazunzuka, nayimilira, nayenda; ndipo adalowa pamodzi nawo m’kachisi, nayenda nalumpha, nayamika Mulungu.

Act 3:9 Ndipo anthu onse adamuwona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu;

Act 3:10 Ndipo iwo adamzindikira iye, kuti ndiye wopempha zachifundo amene adakhala pa khomo lokongola la kachisi: ndipo adadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera.

Act 3:11 Koma m’mene munthu wosayenda amene adachiritsidwa uja adagwira Petro ndi Yohane, adawathamangira pamodzi anthu onse kukhumbi lotchedwa la Solomo alikudabwa kwakukulu ndithu.

Act 3:12 Koma m’mene Petro adachiwona, adayankha kwa anthu, Amuna inu a Israyeli, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamuyendetsa iye ndi mphamvu yathu, kapena ndi chiyero ndi chipembedzo chathu?

Act 3:13 Mulungu wa Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu; adalemekeza Mwana wake Yesu; amene inu mudampereka ndi kumkana Iye pamaso pa Pilato, pamene iyeyu adafuna kum’masula.

Act 3:14 Koma inu mudakana Woyera ndi Wolungamayo, ndipo mudapempha munthu wakupha apatsidwe kwa inu.

Act 3:15 Ndipo mudapha Mkulu wa moyo, amene Mulungu adamuwukitsa kwa akufa; za ichi ife ndife mboni.

Act 3:16 Ndipo mudzina lake kupyolera mu chikhulupiliro cha munthu uyu, chamlimbikitsa iye amene mumuwona, nimumdziwa; inde, chikhulupiriro chimene cha mwa Iye chidampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.

Act 3:17 Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti mudachita izi mosadziwa monganso wolamulira anu.

Act 3:18 Koma zinthu zimenezo zimene Mulungu kale adaziwonetseratu m’kamwa mwa aneneri ake onse, kuti Khristu adzamva zowawa, choteroIye adakwaniritsa.

Act 3:19 Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye;

Act 3:20 Ndipo adzatuma Khristu amene poyamba adalalikidwa kwa inu;

Act 3:21 Amene thambo la Kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu adayankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake onse woyera chiyambire cha dziko lapansi.

Act 3:22 Pakuti Mosetu adati kwa makolo, Mbuye Mulungu wanu adzawukitsira inu m’neneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m’zinthu zonse akayankhula nanu.

Act 3:23 Ndipo kudzali, kuti moyo uli wonse wosamvera m’neneri ameneyu, udzasakazidwa kuchotsedwa pakati pa anthu.

Act 3:24 Inde, ngakhale ndi aneneri onse kuyambira Samueli ndi womutsatira, onse amene adayankhula adanenera za masiku awa.

Act 3:25 Inu ndinu ana a aneneri, ndi apanganolo Mulungu adapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, ndipo mu mbewu yako mafuko onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

Act 3:26 kwa inu choyamba, Mulungu, atatha kuwukitsa Mwana wake Yesu, adamutuma Iye kukudalitsani inu, kukubwezani yense wa inu ku zoyipa zanu.



4

Act 4:1 Koma pamene adalikuyankhula ndi anthu, ansembe ndi m’dindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadza kwa iwo,

Act 4:2 Ali wobvutika mtima chifukwa adaphunzitsa anthuwo, nalalikira za Yesu za kuwuka kwa akufa.

Act 4:3 Ndipo adawathira manja, nawayika mundende kufikira m’mawa; pakuti adali madzulo amenewo.

Act 4:4 Koma ambiri a iwo amene adamva mawuwo adakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chidali ngati zikwi zisanu.

Act 4:5 Zitapita izi m’mawa mwake, oweruza awo, ndi akulu, ndi alembi;

Act 4:6 Ndipo Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Alesandro, ndi onse amene adali afuko la mkulu wa ansembe, adasonkhana pamodzi ku Yerusalemu.

Act 4:7 Ndipo m’mene adawayimika pakati, adafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m’dzina lanji, mwachita ichi inu?

Act 4:8 Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera adati kwa iwo, oweruza a anthu inu, ndi akulu a Israyeli,

Act 4:9 Ngati ife lero tiweruzidwa chifukwa cha ntchito yabwino imene yachitika pa munthu wolumalayu, ndi momwe wachiritsidwira iye;

Act 4:10 Chidziwike bwino kwa inu nonse, ndi kwa anthu onse a Israyeli, kuti m’dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu mudampachika, amene Mulungu adamuwukitsa kwa akufa, mwa Iyeyo munthuyu ayimira pamaso panu wamoyo.

Act 4:11 Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu womanga nyumba, umene wakhala mutu wa pangodya.

Act 4:12 Ndipo palibe chipulumuso mwa wina yense: pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la Kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.

Act 4:13 Tsopano pamene adawona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu wosaphunzira ndi wopulukira, adazizwa ndipo adawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.

Act 4:14 Ndipotu pakuwona munthu wochiritsidwayo alikuyimilira pamodzi nawo, analibe kanthu kakunena kotsutsa.

Act 4:15 Koma pamene adawalamulira iwo achoke m’bwalo la akulu, adanena wina ndi mzake.

Act 4:16 Nanena kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chawoneka kwa onse akukhala m’Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.

Act 4:17 Komatu tiwawopseze asayankhulenso m’dzina ili kwa munthu ali yense, kuti chisabukenso kwa anthu.

Act 4:18 Ndipo adawayitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu.

Act 4:19 Koma Petro ndi Yohane adayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu.

Act 4:20 Pakuti sitingathe ife kuleka kuyankhula zinthu zimene tidaziwona ndi kuzimva.

Act 4:21 Koma m’mene adawawopsanso adawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse adalemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.

Act 4:22 Pakuti adali wa zaka zake zoposa makumi anayi munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidawonetsedwa.

Act 4:23 Ndipo m’mene adamasulidwa, anadza kwa anzawo a iwo wokha, nawawuza ziri zonse woweruza ndi akulu adanena nawo.

Act 4:24 Ndipo m’mene adamva, adakweza mawu kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mbuye Inu ndinu Mulungu wolenga Kumwamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja ndi zonse ziri momwemo:

Act 4:25 Amene mwa pakamwa pa Davide mtumiki wanu, mudati,Amitundu asokoseranji ndi anthu alingilira zopanda pake?

Act 4:26 Adadzindandalitsa mafumu adziko ndipo woweruza adasonkhanidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye, ndi Khristu wake.

Act 4:27 Pakuti zowonadi adasonkhana pamodzi Herode, ndi Pontiyo Pilato ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kumchitira choyipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene mudamdzoza,

Act 4:28 Kuti adzachite zimene dzanja lanu ndi uphungu wanu mudazikonzeratu kale kuti zidzachitike.

Act 4:29 Ndipo tsopano Ambuye, penyani kuwopsa kwawo, ndipo patsani kwa atumiki anu kuti ayankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.

Act 4:30 M’mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina laMwana wanu wopatulika Yesu.

Act 4:31 Ndipo m’mene iwo adapemphera, padagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo adadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.

Act 4:32 Ndipo unyinji wa iwo wokhulupilira adali a mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sadanena m’modzi kuti kanthu kachuma adali nacho ndi kakeka iye yekha; koma adali nazo zonse zofanana.

Act 4:33 Ndipo atumwi adachita umboni ndi mphamvu yayikulu za kuwuka kwa Ambuye Yesu; ndipo padali chisomo chachikulu pa iwo onse.

Act 4:34 Pakuti mwa iwo mudalibe wosowa; pakuti onse amene adali nayo minda, kapena nyumba, adazigulitsa nabwera nawo malonda ake a izo adazigulitsa,

Act 4:35 Ndipo adaziyika pa mapazi a atumwi; ndipo adagawira yense monga kusowa kwake.

Act 4:36 Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnaba (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kupro,

Act 4:37 Pokhala nawo munda, adaugulitsa, nabwera nazo ndalama zake, naziyika pamapazi a atumwi.



5

Act 5:1 Koma munthu wina dzina lake Hananiya pamodzi ndi Safira mkazi wake, adagulitsa katundu wawo,

Act 5:2 Napatula pa mtengo wake, mkazi yemwe adadziwa, natenga chotsala, nachiyika pa mapazi a atumwi.

Act 5:3 Koma Petro adati, Hananiya, Satana adadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, kupatula pa mtengo wake wa mundawo?

Act 5:4 Pamene udali nawo sudali wako kodi? Ndipo pamene udawugulitsa sudali m’manja mwako kodi? Bwanji chidalowa ichi mumtima mwako?sudanyenga anthu, komatu Mulungu.

Act 5:5 Ndipo Hananiya pakumva mawu awa adagwa pansi namwalira: ndipo mantha akulu adagwera pa iwo onse amene adamva zinthu izi.

Act 5:6 Ndipo anyamata adanyamuka, namkulunga, nam’nyamula, natuluka naye amuyika.

Act 5:7 Koma atapita monga maola atatu, ndipo mkazi wake, wosadziwa chidachitikacho, adalowa.

Act 5:8 Ndipo Petro adanena naye, Undiwuze, ngati mudagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo adanena, Inde, wakuti.

Act 5:9 Pamenepo Petro adati kwa iye, mudapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Tawona, mapazi awo a iwo amene adayika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.

Act 5:10 Ndipo adagwa pansi pomwepo pamapazi ake, namwalira; ndipo adalowa anyamatawo, nampeza iye atafa, ndipo adam’nyamula kutuluka naye, namuyika iye pambali pa mwamuna wake.

Act 5:11 Ndipo mantha akulu adadza pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumva izi.

Act 5:12 Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zidachitidwa pa anthu; (ndipo adali onse ndi mtima umodzi m’khumbi la Solomo.

Act 5:13 Koma palibe m’modzi wa wotsalawo adalimba mtima kuphatikana nawo: komatu anthu adawakuzitsa.

Act 5:14 Ndipo wokhulupirira adachuluka kuwonjezekabe kwa Ambuye, makamu a amuna ndi akazi).

Act 5:15 Kotero kuti adanyamulanso natuluka nawo wodwala kumakwalala, nawayika pamakama ndi pa mphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chinthunzi chake chigwere wina wa iwo.

Act 5:16 Pamenepo lidadzanso khamu kuchokera kumizinda yozungulira Yerusalemu, litatenga wodwala, ndi wobvutika ndi mizimu yonyansa; ndipo adachiritsidwa onsewa.

Act 5:17 Pamenepo adawuka mkulu wa ansembe ndi onse amene adali naye, ndiwo ampatuko wa Asaduki, ndipo adali wodzazidwa ndi mkwiyo.

Act 5:18 Ndipo adawathira manja atumwi, nawayika m’ndende ya anthu wamba.

Act 5:19 Koma m’ngelo wa Ambuye adatsegula makhomo a ndende usiku, nawatulutsa iwo, nati;

Act 5:20 Pitani, ndipo imilirani, nimuyankhule m’kachisi kwa anthu onse mawu a Moyo umenewu.

Act 5:21 Ndipo pamene adamva ichi, adalowa m’Kachisi m’banda kucha, naphunzitsa. Koma adadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene adali naye, nasonkhanitsa abwalo la akulu, ndi akulu onse a ana a Israyeli, natuma kundende atengedwe ajawo.

Act 5:22 Koma asilikali amene adafikako sadawapeza m’ndende, ndipo pobwera adafotokoza,

Act 5:23 Nanena, Nyumba ya ndende zowonadi tidapeza chitsekere ndi chitetezo chonse ndi alonda ali chiyimilire pakhomo; koma pamene tidatsegula sitidapezamo m’modzi yense.

Act 5:24 Koma m’mene adamva mawu awa m’dindo wa Kachisi ndi ansembe akulu adathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.

Act 5:25 Ndipo pamenepo padadza wina nawafotokozera, kuti Tawonani, amuna aja mudawayika m’ndende ali m’Kachisi, alikuyimilira ndi kuphunzitsa anthu.

Act 5:26 Pamenepo adachoka mdindo pamodzi ndi asilikali; nadza nawo, koma osawagwiritsitsa, pakuti adawopa anthu, kuti angaponyedwe miyala.

Act 5:27 Ndipo m’mene adadza nawo, adawayika pa bwalo la akulu. Ndipo adawafunsa mkulu wa ansembe.

Act 5:28 Nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitse kutchula dzina ili; ndipo tawonani mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.

Act 5:29 Pamenepo Petro ndi atumwi ena adati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.

Act 5:30 Mulungu wa makolo athu adawukitsa Yesu, amene mudamupha inu, ndi kumpachika pa mtengo.

Act 5:31 Ameneyo Mulungu adamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mfumu ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israyeli kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.

Act 5:32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; ndi Mzimu Woyeranso, amene Mulungu adapereka kwa iwo akumvera Iye.

Act 5:33 Koma m’mene adamva ichi, iwo adapsa mtima, nafuna kuwapha.

Act 5:34 Koma adanyamukapo wina pa bwalo la akulu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliyeli, mphuniztsi wa chilamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang’ono.

Act 5:35 Ndipo iye adati kwa iwo, amuna inu a Israyeli, tamachenjerani mwa inunokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.

Act 5:36 Pakuti asadafike masiku ano adawuka Tewuda, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu adaphatikana naye, chiwerengero chawo ngati mazana anayi; ndipo adaphedwa; ndi onse amene adamvera iye adamwazika, napita pachabe.

Act 5:37 Atapita ameneyo, adawuka Yuda wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso adawonongeka, ndi onse amene adamvera iye adabalalitsidwa.

Act 5:38 Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umenewu kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka:

Act 5:39 Koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke wotsutsana ndi Mulungu.

Act 5:40 Ndipo adabvomerezana ndi iye; ndipo m’mene adayitana atumwi, adawakwapula nawalamulira asayankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo adawamasula.

Act 5:41 Ndipo pamenepo iwo adapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti adayesedwa woyenera kunzunzidwa chifukwa cha dzina lake.

Act 5:42 Ndipo masiku onse, m’kachisi ndi m’nyumba sadaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.



6

Act 6:1 Koma masiku awo, pakuchulukitsa wophunzira, kudabuka madandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye awo adayiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.

Act 6:2 Ndipo khumi ndi awiri adayitana khamu la wophunzira, nati, sikuyenera ife kuti tisiye mawu a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.

Act 6:3 Chifukwa chake, abale yang’anani mwa inu amuna asanu ndi awiri ambiri yabwino, wodzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawayike agwire ntchito iyi.

Act 6:4 Koma ife eni tokha tidzapitiriza chilimbikire kupemphera, ndi kutumikira mawu.

Act 6:5 Ndipo mawu amenewa adakonda khamu lonse; ndipo adasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo ndi Prokoro, ndi Nikanora, ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolawo, ndiye wopinduka wa ku Antiyokeya:

Act 6:6 Amenewo adawayika pamaso pa atumwi; ndipo m’mene adapemphera, adayika manja pa iwo.

Act 6:7 Ndipo mawu a Mulungu adakula; ndipo chiwerengero cha wophunzira chidachuluka kwakukulutu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe lidamvera chikhulupirirocho.

Act 6:8 Ndipo Stefano, wodzala ndi chikhu lupiriro ndi mphamvu, adachita zodabwitsa zazikulu ndi zozizwa pakati pa anthu.

Act 6:9 Pamenepo adawuka ena a m’sunagoge wotchedwa wa Alibertino, ndi Akurenayo, ndi wa Alesandreyo, ndi mwa iwo a ku Kilikiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.

Act 6:10 Ndipo sadathe kuyitsutsa nzeru ndi Mzimu amene adayankhula naye.

Act 6:11 Pamenepo iwo adanyengerera anthu amene adati, tidamumva iye alikunenera motsutsana ndi Mose ndi Mulungu mawu amwano.

Act 6:12 Ndipo adawutsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu,

Act 6:13 Nayimika mboni zonama, zonena. Munthu ameneyo saleka kunenera mwano malo ano woyera, ndiponso chilamulo;

Act 6:14 Pakuti tidamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo adzawononga malo ano, nadzasintha miyambo imene Mose adatipatsa.

Act 6:15 Ndipo adampenyetsetsa onse wokhala m’bwalo la akulu, nawona nkhope yake ngati kuti akuwona nkhope ya m’ngelo.



7

Act 7:1 Ndipo mkulu wa nsembe adati, zitero zinthu izi kodi?

Act 7:2 Ndipo iye adati, amuna inu abale, ndi atate, tamverani, Mulungu wa ulemerero adawonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m’Mesopotamiya, asadayambe kukhala m’Harana;

Act 7:3 Ndipo adati kwa iye, Tuluka ku dziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye kudziko limene ndidzakusonyeza iwe.

Act 7:4 Pamenepo iye adatuluka m’dziko la Akaldayo namanga m’Harana; ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Iye adamsuntha alowe m’dziko lino, m’mene mukhalamo tsopano.

Act 7:5 Ndipo sadampatsa cholowa chake m’menemo, ngakhale popondapo phazi lake iyayi; ndipo adamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale cholowa chake, ndi la mbewu yake yomtsatira, angakhale adalibe mwana pamenepo.

Act 7:6 Koma Mulungu adalankhula chotero, kuti mbewu yake idzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choyipa, zaka mazana anayi.

Act 7:7 Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzawuweruza Ine, adatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine pamalo pano.

Act 7:8 Ndipo adampatsa iye pangano la mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isake adabala Yakobo, ndi Yakobo adabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.

Act 7:9 Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, adamgulitsa amuke naye ku Aigupto; ndipo Mulungu adali naye,

Act 7:10 Namlanditsa iye m’zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farawo mfumu ya ku Aigupto; ndipo adamuyika iye kazembe pa nyumba yake yonse.

Act 7:11 Tsopano idadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi chisautso chachikulu; ndipo sadapeza chakudya makolo athu.

Act 7:12 Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu mu Aigupto, adatuma makolo athu ulendo woyamba.

Act 7:13 Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe adazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe lidazindikirika kwa Farawo.

Act 7:14 Ndipo Yosefe adatumiza, nayitana Yakobo atate wake, ndi a pabanja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.

Act 7:15 Ndipo Yakobo adatsikira ku Aigupto; ndipo adamwalira, iye ndi makolo athu;

Act 7:16 Ndipo adawanyamula kupita nawo ku Shekemu, nawayika m’manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Emori m’Shekemu.

Act 7:17 Koma m’mene idayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo adakula nachuluka m’Aigupto,

Act 7:18 Kufikira idawuka mfumu yina ya Aigupto imene siyidamdziwa Yosefe.

Act 7:19 Imeneyo idachenjerera fuko lathu, niwachitira choyipa makolo athu, niwatayitsa tiana tawo, kuti tingakhale ndi moyo.

Act 7:20 Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokongola ndithu; ndipo adamlera miyezi itatu m’nyumba ya atate ake;

Act 7:21 Ndipo pakutayika iye, adamtola mwana wa mkazi wa Farawo, namlera akhale mwana wake.

Act 7:22 Ndipo Mose adaphunzira nzeru zonse za a Aigupto; nakhala wamphamvu m’mawu ake ndi m’ntchito zake.

Act 7:23 Koma pamene zaka zake zidafikira ngati makumi anayi, kudalowa kumtima kwake kuzonda abale ake ana a Israyeli.

Act 7:24 Ndipo powona wina woti alikumchitira choyipa, iye adamchinjiriza, nam’bwezera chilango wozunzayo, nakantha m’Aigupto.

Act 7:25 Ndipo adayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sadazindikira.

Act 7:26 Ndipo m’mawa mwake adawawonekera alikulimbana ndewu, ndipo adafuna kuti, awayanjanitsenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitira choyipa bwanji?

Act 7:27 Koma iye wakumchitira mzake choyipa adamkankha, nati, Wakuyika iwe ndani mkulu ndi wotiweruza?

Act 7:28 Kodi ufuna kundipha ine, monga muja udaphera m’Aigupto dzulo?

Act 7:29 Ndipo Mose adathawa pa mawu awa, nakhala mlendo m’dziko la Midyani; kumeneko adabala ana amuna awiri.

Act 7:30 Ndipo zitatha zaka makumi anayi, adamuwonekera m’ngelo m’chipululu cha Sina, m’lawi la moto wa chitsamba.

Act 7:31 Koma Mose pakuwona adazizwa pachowonekachi; ndipo pakuyandikira iye kukawona, kudadza mawu wa Ambuye.

Act 7:32 Akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isake, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose adanthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako.

Act 7:33 Pamenepo Ambuye adati kwa iye, bvula nsapato zako ku mapazi ako; pakuti pa malo pamene uyimapo mpopatulika.

Act 7:34 Kuwona ndawona kupsinjidwa kwa anthu anga ali m’Aigupto, ndipo ndamva kubuwula kwawo; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano tiye kuno, ndikutume ku Aigupto.

Act 7:35 Mose uyu amene adamkana, ndi kuti, Wakuyika iwe ndani mkulu ndi wotiweruza? Ameneyo Mulungu adamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la m’ngelo womuwonekera pachitsamba.

Act 7:36 Ameneyo adawatsogolera, natuluka nawo atachita zozizwa ndi zizindikiro m’Aigupto, ndi m’nyanja yofiyira, ndi m’chipululu zaka makumi anayi.

Act 7:37 Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israyeli, Mulungu adzakuwukitsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine. Inu mudzamvere ameneyo.

Act 7:38 Uyu ndiye amene adali mu Mpingo m’chipululu pamodzi ndi m’ngelo wakuyankhula naye m’phiri la Sinai, ndi makolo athu; amene adalandira maneno amoyo akutipatsa ife;

Act 7:39 Amene makolo athu sadafuna kumvera iye, koma adamkankha achoke, nabwerera m’mbuyo mumtima mwawo ku Aigupto.

Act 7:40 Nati kwa Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene adatitulutsa m’Aigupto, sitidziwa chomwe chamgwera.

Act 7:41 Ndipo adapanga mwana wa ng’ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja awo.

Act 7:42 Koma pamenepo Mulungu adatembenuka, nawapereka iwo apembedze gulu la Kumwamba; monga kwa lembedwa m’buku la aneneri, kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zake makumi anayi m’chipululu, nyumba ya Israyeli inu?

Act 7:43 Ndipo mudatenga chihema cha Moloki, ndi nyenyezi ya Mulungu wanu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira izo; ndipo ndidzakutengani kumka nanu m’tsogolo mwake mwa Babulo.

Act 7:44 Chihema cha umboni chidali ndi makolo athu m’chipululu, monga adalamula Iye wakuyankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiwona.

Act 7:45 Chimenenso makolo athu akudza m’mbuyo adalowa nacho ndi Yoswa polandira iwo cholowa chawo cha kwa amitundu, amene Mulungu adawayingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;

Act 7:46 Amene adapeza chisomo pamaso pa Mulungu, nakhumba kupeza chihema cha Mulungu wa Yakobo.

Act 7:47 Koma Solomo adam’mangira Iye nyumba.

Act 7:48 Komatu Wam’mwamba-mwambayo sakhala m’kachisi womangidwa ndi manja; monga m’neneri anena,

Act 7:49 Thambo la Kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga; mudzandimangira nyumba yotani? Ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi wotani?

Act 7:50 Kodi silidapanga dzanja langa zinthu izi zonse?

Act 7:51 Owuma makosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga adachita makolo anu, momwemo inu.

Act 7:52 Ndiye yani wa aneneri amene makolo anu sadamzunza? Ndipo adawapha iwo amene adawonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha:

Act 7:53 Inu amene mudalandira chilamulo monga chidayikidwa ndi m’ngelo, ndipo simudachisunga.

Act 7:54 Koma pakumva zinthu izi adapsa mtima, adamkukutira iye mano awo.

Act 7:55 Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, adapenyetsetsa Kumwamba, nawona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuyimilira padzanja lamanja la Mulungu.

Act 7:56 Ndipo adati, Tawonani, ndipenya m’Mwamba motseguka, ndi Mwana wa munthu alikuyimilira pa dzanja la manja la Mulungu.

Act 7:57 Pamenepo iwo adafuwula ndi mawu akulu, natseka m’makutu mwawo, namkhamukira iye ndi mtima umodzi,

Act 7:58 Ndipo adamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zidayika zobvala zawo pa mapazi a m’nyamata dzina lake Saulo.

Act 7:59 Ndipo adamponya miyala Stefano, alikuyitana Mulungu, ndi kunena Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.

Act 7:60 Ndipo m’mene adagwada pansi, adafuwula ndi mawu akulu, Ambuye, musawayikire iwo tchimo ili. Ndipo m’mene adanena ichi, adagona tulo.



8

Act 8:1 Ndipo Saulo adalikubvomerezana nawo pa imfa yake. Ndipo panthawiyo kudayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo udali m’Yerusalemu; ndipo adabalalitsidwa onse m’mayiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ayi.

Act 8:2 Ndipo adamuyika Stefano anthu wopembedza, namlira maliro akulu.

Act 8:3 Ndipo Saulo adapasula Mpingo, nalowa m’nyumba iriyonse, nakokamo amuna ndi akazi, nawayika m’ndende.

Act 8:4 Pamenepo iwo wobalalitsidwawo adapitapita nalalikira mawuwo.

Act 8:5 Ndipo Filipo adatsikira ku mzinda wa ku Samariya nawalalikira Khristu kwa iwo.

Act 8:6 Ndipo anthuwo ndi mtima umodzi adasamalira zinthu zonenedwa ndi Filipo, pamene adamva, napenya zozizwa zimene iye adazichita.

Act 8:7 Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa idatuluka, yofuwula ndi mawu akulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi wopunduka, adachiritsidwa.

Act 8:8 Ndipo padakhala chimwemwe chachikulu m’muzindamo.

Act 8:9 Koma padali munthu wina dzina lake Simoni amene adachita matsenga m’mundzimo kale, nadabwitsa anthu a ku Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye adali munthu wamkulu:

Act 8:10 Ameneyo adamsamalira onsewo, kuyambira wam’ng’ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa yayikulu.

Act 8:11 Ndipo adamsamalira iye, popeza nthawi yayikulu adawadabwitsa iwo ndi matsenga ake.

Act 8:12 Koma pamene adakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, adabatizidwa, amuna ndi akazi.

Act 8:13 Ndipo Simoni mwini wake adakhulupiriranso; ndipo m’mene adabatizidwa, dakhara ndi Filipo; ndipo pakuwona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zirikuchitika, anadabwa.

Act 8:14 Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu adamva kuti Samariya adalandira mawu a Mulungu, adawatumizira Petro ndi Yohane:

Act 8:15 Amenewo, m’mene adatsikirako, adawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera;

Act 8:16 (Pakuti kufikira pamenepo nkuti asadagwe pa wina m’modzi wa iwo; koma adangobatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.)

Act 8:17 Pamenepo adayika manja pa iwo, ndipo adalandira Mzimu Woyera.

Act 8:18 Koma pakuwona Simoni kuti mwa kuyika manja kwa atumwi adapatsidwa Mzimu Woyera, adawatengera ndalama.

Act 8:19 Nanena, Ndipatseni inenso mphamvu yimeneyi, kuti amene aliyense ndikayika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.

Act 8:20 Koma Petro adati kwa iye, Ndalama yako iwonongeke nawe, chifukwa udalingilira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.

Act 8:21 Ulibe gawo kapena cholandira ndi mawu awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.

Act 8:22 Chifukwa chake lapa choyipa chako ichi, pemphera kwa Mulungu, kuti kapena akukhululukire iwe cholingilira cha mtima wako.

Act 8:23 Pakuti ndiwona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama.

Act 8:24 Ndipo Simoni adayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.

Act 8:25 Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kuyankhula mawu a Ambuye, adabwerera kumka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino ku midzi yambiri ya Asamariya.

Act 8:26 Koma m’ngelo wa Ambuye adayankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kumka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.

Act 8:27 Ndipo adanyamuka napita; ndipo tawona munthu wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yayikazi ya a Ethiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene adadza ku Yerusalemu kudzapembedza,

Act 8:28 Ndipo iye adalimkubwerera, nalikukhala pa gareta wake, nawerenga m’neneri Yesaya.

Act 8:29 Pamenepo Mzimu adati kwa Filipo, yandikira, nudziphatike ku gareta uyu.

Act 8:30 Ndipo Filipo adamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya m’neneri, ndipo adati, Kodi muzindikira chimene muwerenga?

Act 8:31 Ndipo iye adati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo adapempha Filipo akwere nakhale naye.

Act 8:32 Koma palembo pamene adalikuwerengapo ndipo, Ngati nkhosa adatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwana wa nkhosa ali du pamaso pa womsenga, kotero sadatsegula pakamwa pake;

Act 8:33 M’kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chidachotsedwa; m’bado wake adzawubukitsa ndani? Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake.

Act 8:34 Ndipo mdindoyo adayankha Filipo, nati, Ndikupemphani m’neneri anena ichi za yani? Za yekha kapena za munthu wina?

Act 8:35 Ndipo Filipo adatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.

Act 8:36 Ndipo monga adapita panjira pawo, adadza kumadzi ena; ndipo mdindoyo adati, Tawonapo pano pali madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?

Act 8:37 Ndipo Filipo adati, ngati ukhulupirira ndi mtima wako wonse; ukhoza kubatizidwa. Ndipo iye adayankha nati, Ndikhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.

Act 8:38 Ndipo adamuwuza kuti ayimitse gareta; ndipo adatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo adam’batiza iye.

Act 8:39 Ndipo pamene adakwera kutuluka m’madzi, Mzimu wa Ambuye adakwatula Filipo; ndipo mdindoyo sadamuwonanso, pakuti adapita njira yake wokondwera.

Act 8:40 Koma Filipo adapezedwa ku Azotu; ndipo popitapita adalalikira Uthenga Wabwino m’mizinda yonse, kufikira adadza iye ku Kayisareya.



9

Act 9:1 Koma Saulo wosaleka kupumira pa akuphunzira wa Ambuye kuwopsa ndi kupha, adamka kwa mkulu a ansembe.

Act 9:2 Napempha kwa iye akalata akumka nawo ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena wotsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nawo womangidwa ku Yerusalemu.

Act 9:3 Ndipo poyenda ulendo wake, kudali kuti iye adayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuwunika kochokera kumwamba:

Act 9:4 Ndipo adagwa pansi, namva mawu akunena naye, Saulo, Saulo, undinzunziranji Ine?

Act 9:5 Koma iye adati, Ndinu yani Ambuye? Ndipo adati, Ndine Yesu amene umnzunza. Ndikobvuta kwa iwe kumenyana ndi zisonga zakuthwa kwambiri.

Act 9:6 Ndipo iye adanthunthumira ndikudabwa nati, Ambuye, kodi mufuna kuti ine ndichite chiyani? Ndipo Ambuye adati kwa iye, Uka, nulowe m’mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.

Act 9:7 Ndipo amunawo akumperekeza iye adayima du, atamvadi mawu, koma osawona munthu.

Act 9:8 Ndipo Saulo adawuka pansi; koma potseguka maso ake, sadapenya munthu aliyense; ndipo adamgwira dzanja, namtenga nalowa naye m’Damasiko.

Act 9:9 Ndipo adakhala masiku atatu wosawona, ndipo sadadya kapena kumwa.

Act 9:10 Koma ku Damasiko kudali wophunzira wina dzina lake Hananiya; ndipo Ambuye adati kwa iye m’masomphenya, Hananiya. Ndipo adati, Ndiri pano, Ambuye.

Act 9:11 Ndipo Ambuye adati kwa iye, Tawuka, pita kukhwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m’nyumba ya Yuda, ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso; pakuti tawona, alikupemphera,

Act 9:12 Ndipo adawonam’masomphenya mwamuna dzina lake Hananiya, alikulowa, nayika manja ake pa iye, kuti apenyenso.

Act 9:13 Ndipo Hananiya adayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti adachitiradi choyipa woyera mtima anu m’Yerusalemu.

Act 9:14 Ndi kuti pano ali nawo ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuyitana pa dzina lanu.

Act 9:15 Koma Ambuye adati kwa iye, Pita, pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa a mitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli.

Act 9:16 Pakuti Ine ndidzamuwonetsa iye zinthu zazikulu zimene ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.

Act 9:17 Ndipo adachoka Hananiya, nalowa m’nyumbayo; ndipo adayika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene adakuwonekera pa njira wadzerayo, wandituma ine, kuti ulandire kuwona kwako ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.

Act 9:18 Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m’maso mwake ngati mamba, ndipo adapenyanso; nipo adawuka nabatizidwa.

Act 9:19 Ndipo adalandira chakudya, nawona nacho mphamvu. Ndipo adakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena.

Act 9:20 Ndipo pomwepo iye adalalikira Khristu m’masunagoge, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.

Act 9:21 Koma onse amene adamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene adawononga m’Yerusalemu onse akuyitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nawo womangidwa kwa ansembe akulu.

Act 9:22 Koma Saulo adakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda wokhala m’Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndiye Khristu.

Act 9:23 Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda adapangana kuti amuphe iye:

Act 9:24 Koma chiwembu chawo chidadziwika ndi Saulo. Ndipo iwo anamdikiriranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe.

Act 9:25 Koma wophunzira adamtenga iye usiku, namtsitsira pakhoma la linga, mumtanga.

Act 9:26 Koma m’mene adafika ku Yerusalemu, adayesa kudziphatika kwa wophunzira; ndipo adamuwopa iye onse, osakhulupirira kuti iye adali wophunzira.

Act 9:27 Koma Barnaba adamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adawonera Ambuye m’njira, ndi kuti adayankhula naye, ndi kuti m’Damasiko adalalikira molimbika mtima m’dzina la Yesu.

Act 9:28 Ndipo iye adali nawo pamodzi iwo nalowa ndikutuluka ku Yerusalemu.

Act 9:29 Ndipo iye adayankhula molimbika mtima m’dzina la Ambuye Yesu; ndipotu adayankhula natsutsana ndi Ahelene; koma adapita nafuna kuti amuphe iye.

Act 9:30 Koma m’mene abale adachidziwa, adapita naye ku Kayisareya, namtumiza achoke kumka ku Tariso.

Act 9:31 Pamenepo mipingo ya m’Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya idapumula nikhala yolimbikitsidwa ndi mtendere, nikhazikika; ndipo idayenda m’kuwopa kwa Ambuye ndi m’chitonthozo cha Mzimu Woyera, nichuluka.

Act 9:32 Koma kudali, pakupita Petro ponseponse, adatsikiranso kwa woyera mtima akukhala ku Luda.

Act 9:33 Ndipo adapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene adagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene adagwidwa manjenje.

Act 9:34 Ndipo Petro adati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo adawuka pomwepo.

Act 9:35 Ndipo adamuwona iye onse akukhala ku Luda ndi ku Sarona, natembenukira kwa Ambuye amenewa.

Act 9:36 Koma m’Yopa mudali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo adadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene adazichita.

Act 9:37 Ndipo kudali m’masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye adamgoneka m’chipinda chapamwamba.

Act 9:38 Ndipo popeza Luda ndi pafupi ndi Yopa, m’mene adamva wophunzirawo kuti Petro adali pomwepo, adamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwe mudze kwa ife.

Act 9:39 Ndipo Petro adanyamuka, napita nawo. M’mene adafikako, adapita naye kuchipinda cha pamwamba; ndipo amasiye onse adayimilirapo pali iye, nalira, namuwonetsa malaya ndi zobvala zimene Dorika adasoka, pamene adali nawo pamodzi.

Act 9:40 Koma Petro adawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo adati, Tabita, uka. Ndipo adatsegula maso ake; ndipo pakuwona Petro, adakhala tsonga.

Act 9:41 Ndipo Petro adamgwira dzanja, nam’nyamutsa; ndipo m’mene adayitana woyera mtima ndi amasiye, adampereka iye wamoyo.

Act 9:42 Ndipo kudadziwika ku Yopa konse; ndipo ambiri adakhulupirira Ambuye.

Act 9:43 Ndipo kudali, kuti adakhala iye m’Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.



10

Act 10:1 Ndipo kudali munthu ku Kayisareya, dzina lake Korneliyo, Kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya.

Act 10:2 Ndiye munthu wopembedza, ndi wakuwopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene adapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kwambiri nthawi zonse.

Act 10:3 Iye adapenya masomphenya poyera, m’ngelo wa Mulungu alimkudza kwa iye, ngati ola lachisanu ndi chinayi la usana, nanena naye, Korneliyo.

Act 10:4 Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuwopa, adati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo adati kwa iye, mapemphero ako ndi zachifundo zako zidakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.

Act 10:5 Ndipo tsopano tumiza amuna ku Yopa, ayitane munthu Simoni, wotchedwanso Petro:

Act 10:6 Iye adacherezedwa ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m’mbali mwa nyanja. Iye adzakuwuza iwe zoyenera kuchita.

Act 10:7 Ndipo m’mene adachoka m’ngelo amene adayankhula ndi Korneliyo, adayitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene adamtumikira kosalekeza;

Act 10:8 Ndipo m’mene adawafotokozera zonse, adawatuma ku Yopa.

Act 10:9 Koma m’mawa mwake, pokhala pa ulendo pawo iwowa, m’mene adayandikira mudzi, Petro adakwera padenga kukapemphera, ngati pa ola lachisanu ndi chimodzi;

Act 10:10 Ndipo adagwidwa njala, nafuna kudya. Koma m’mene adalikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka;

Act 10:11 Ndipo adawona pathambo patatseguka, ndipo chotengera chirimkutsika, chonga ngati nsalu chachikulu, chogwiridwa pangodya zake zinayi, ndi kutsikira padziko la pansi.

Act 10:12 M’menemo mudali nyama za miyendo inayi za mitundu yonse, ndi zokwawa za pa dziko ndi mbalame za m’lengalenga.

Act 10:13 Ndipo adamdzera mawu, Tawuka, Petro; ipha, nudye.

Act 10:14 Koma Petro adati, iyayitu, Mbuye; pakuti sindidadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.

Act 10:15 Ndipo mawu adamdzeranso nthawi yachiwiri, chimene Mulungu adayeretsa, usachiyesa chinthu wamba.

Act 10:16 Ndipo chidachitika katatu ichi; ndipo pomwepo chotengeracho chidatengedwa kumka Kumwamba.

Act 10:17 Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawawona akuti chiyani, tawonani, amuna aja wotumidwa ndi Korneliyo, atafunsira nyumba ya Simoni, adayima pa chipata.

Act 10:18 Ndipo adayitana nafunsa ngati Simoni wotchedwanso Petro, acherezedwako.

Act 10:19 Ndipo m’mene Petro adalingilira za masomphenya, Mzimu adanena naye, Tawona, amuna atatu akufuna iwe.

Act 10:20 Tawuka, nutsike, Ndipo upite nawo, wosakayika kayika; pakuti ndawatuma ndine.

Act 10:21 Pamenepo Petro adatsikira kwa anthuwo amene adatumizidwa kwa iye ndi Korneliyo, nati, Tawonani, ine ndine mumfuna; chifukwa chake mwadzera chiyani?

Act 10:22 Ndipo iwo adati, Korneliyo, munthu wolungama ndi wakuwopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, adachenjezedwa ndi Mulungu mwa m’ngelo woyera kuti atumize nakuyitaneni mumuke ku nyumba yake, ndi kumumvetsa mawu anu.

Act 10:23 Pamenepo adawalowetsa nawachereza. Ndipo m’mawa mwake adanyamuka natuluka nawo, ndi ena wa abale a ku Yopa adamperekeza iye.

Act 10:24 Ndipo m’mawa mwake atatha kulowa m’Kayisareya. Koma Korneliyo adalikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi abwenzi ake eni eni.

Act 10:25 Ndipo padali m’mwawa mwake pakulowa Petro, Korneliyo adakomana naye, nagwa pamapazi ake, namlambira iye.

Act 10:26 Koma Petro adamuwutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu.

Act 10:27 Ndipo pakukamba naye, adalowa napeza ambiri atasonkhana;

Act 10:28 Ndipo iye adati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu adandiwonetsera ine ndisanenere ali yense ali munthu wamba kapena wonyansa.

Act 10:29 Chifukwa chakenso ndidadza wosakana, m’mene mudatuma kundiyitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiyitaniranji?

Act 10:30 Ndipo Korneliyo adati, Atapita masiku anayi ndidali kusala chakudya kufikira ora iri, ndikupemphera m’nyumba yanga pa ola lachisanu ndi chinayi; ndipo tawonani, padayimilira pamaso panga munthu wobvala chobvala chonyezimira.

Act 10:31 Ndipo adati, Korneliyo, lamveka pemphero lako, ndipo zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu.

Act 10:32 Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akayitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m’nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, mbali mwa nyanja, ameneyo akadza adzayankhula ndi iwe.

Act 10:33 Pamenepo ndidatumiza kwa inu wosachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake tawonani tiri tonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zinthu zonse Mulungu adakulamulirani.

Act 10:34 Pamenepo Petro adatsegula pakamwa pake, nati, Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu pakati pa anthu:

Act 10:35 Koma m’mitundu yonse, wakumuwopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.

Act 10:36 Mawu amene adatumiza kwa ana a Israyeli, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)

Act 10:37 Mawuwo muwadziwa inu, adamvekawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane adawulalikira:

Act 10:38 Za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene adapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse wosautsidwa ndi mdiyerekezi, pakuti Mulungu adali pamodzi ndi Iye.

Act 10:39 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zonse adazichita m’dziko la Ayuda ndi m’Yerusalemu; amenenso adamupha, nampachika pamtengo.

Act 10:40 Ameneyo, Mulungu adamuwukitsa tsiku lachitatu, nalola kuti awonetsedwe poyera;

Act 10:41 Si kwa anthu onse ayi, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atawuka iye kwa akufa.

Act 10:42 Ndipo adatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti, uyu ndiye amene ayikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.

Act 10:43 Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti mwa dzina lake yense wokhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ake, mwadzina lakelo.

Act 10:44 Pamene Petro adali chiyankhulire, Mzimu Woyera adagwa pa onse akumva mawuwo.

Act 10:45 Ndipo iwo onse wokhulupirirawo akumdulidwe amene adadza ndi Petro anadadwa, chifukwa pa amitundunso padathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.

Act 10:46 Pakuti adawamva iwo alikuyankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu pamenepo Petro adayankha,

Act 10:47 Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?

Act 10:48 Ndipo adalamulira iwo abatizidwe mdzina la Ambuye. Pamenepo adampempha iye atsotse masiku.



11

Act 11:1 Koma atumwi ndi abale wokhala m’Yudeya adamva kuti amitundunso adalandira mawu a Mulungu.

Act 11:2 Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo akumdulidwe adatsutsana naye,

Act 11:3 Nanena kuti, Mudalowa kwa anthu wosadulidwa, ndi kudya nawo.

Act 11:4 Koma Petro adayamba kuwafotokozera chilongosolere, kuyambira poyambirira pa nkhani nanena,

Act 11:5 Ndidali ine muzinda wa Yopa ndi kupemphera; ndipo mkukomoka ndidawona masomphenya, chotengera chirikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pa ngodya zake zinayi; ndi kutsika kumwamba, ndipo chidadza pa ine:

Act 11:6 Chimenecho ndidachipenyetsetsa ndichilingilira, ndipo ndidawona nyama za miyendo inayi zapadziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za mlengalenga.

Act 11:7 Ndipo ndidamvanso mawu akunena ndi ine, Tawuka Petro; ipha, nudye.

Act 11:8 Koma ndinati, Iyayitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikadalowe m’kamwa mwanga ndi kale lonse.

Act 11:9 Koma mawu adayankha nthawi yachiwiri wotuluka m’mwamba, chimene Mulungu adachiyeretsa, usachiyesa chinthu wamba.

Act 11:10 Ndipo ichi chidachitika katatu; ndipo zidakwezekanso zonse kumwamba.

Act 11:11 Ndipo tawonani, pomwepo amuna atatu adali atayima kale pa khomo la nyumba m’mene mudali ife, adatumidwa kwa ine wochokera ku Kayisareya.

Act 11:12 Ndipo Mzimu adandiwuza ndinke nawo, wosakayika konse. Ndipo abale awa asanu ndi m’modzi adandiperekezanso adamuka nane; ndipo tidalowa m’nyumba ya munthuyo:

Act 11:13 Ndipo adatiwuza ife kuti adawona m’ngelo atayimilira m’nyumba yake, ndikuti, Tumiza anthu ku Yopa, akayitane Simoni, wonenedwanso Petro;

Act 11:14 Amene adzayankhula nawe mawu, amene udzapulumutsidwa nawo iwe ndi apabanja ako onse.

Act 11:15 Ndipo m’mene ndidayamba kuyankhula, Mzimu Woyera adawagwera, monga adatero ndi ife poyamba paja,

Act 11:16 Ndipo pamenepo ndidakumbukira mawu a Ambuye, kuti adanena, Yohane anabatizatu ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.

Act 11:17 Ngati tsono Mulungu adawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tidakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu?

Act 11:18 Ndipo pamene adamva zinthu izi, adakhala du, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, potero Mulungu adapatsa kwa a mitundunso kutembenukira mtima kumoyo.

Act 11:19 Tsopano iwotu, wobalalikawo chifukwa cha chinzunzocho chidadza pa Stefano, adafikira ku Foyinike, ndi Kupro, ndi Antiyokeya, wosayankhula mawu kwa wina yense koma kwa Ayuda wokha wokha.

Act 11:20 Ndipo padali mwa iwo, amuna aku Kupro, ndi Kurena, amenewo, m’mene adafika ku Antiyokeya, adayankhula ndi Ahelene, ndi kulalikira za Ambuye Yesu.

Act 11:21 Ndipo dzanja la Ambuye lidali nawo; ndi chiwerengero chachikulu chidakhulupirira ndi kutembenukira kwa Ambuye.

Act 11:22 Ndipo mbiri ya zinthu izi idamveka m’makutu a Mpingo wakukhala m’Yerusalemu; ndipo adatuma Barnaba apite kufikira ku Antiyokeya.

Act 11:23 Ameneyo m’mene adafika, nawona chisomo cha Mulungu, adakondwera; ndipo adawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kumamatira kwa Ambuye.

Act 11:24 Chifukwa adali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidawonjezeka kwa Ambuye.

Act 11:25 Pamenepo Barnaba adatuluka kumka ku Tariso kukafunafuna Saulo:

Act 11:26 Ndipo m’mene adampeza, adadza naye ku Antiyokeya. Ndipo kudali, kuti chaka chonse adasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo wophunzira adayamba kutchedwa Akhristu ku Antiyokeya.

Act 11:27 Koma masiku awa aneneri adatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiyokeya.

Act 11:28 Ndipo adayimirira m’modzi wa iwo, dzina lake Agabo, nalosera mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yayikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza m’masiku a Klaudiyo Kaisara.

Act 11:29 Pamenepo wophunzira, yense monga adakhoza, adatsimikiza mtima kutumiza thandizo kwa abale wokhala m’Yudeya;

Act 11:30 Ndipo adazichita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnaba ndi Saulo.



12

Act 12:1 Tsopano pa nyengo imeneyo Herode mfumu adathira manja ena a mu Mpingo kuwachitira zoyipa.

Act 12:2 Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane.

Act 12:3 Ndipo pakuwona kuti kudakondweretsa Ayuda, adawonjezapo nagwiranso Petro. (Ndipo awo adali masiku a mkate wopanda chotupitsa).

Act 12:4 Ndipo m’mene adamgwira, adamuyika m’ndende, nampereka kwa magulu anayi wa alonda, lonse anayi anayi, amdikire iye; ndipo adafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha.

Act 12:5 Pamenepo ndipo Petro adasungika m’ndende; koma Mpingo udampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.

Act 12:6 Ndipo pamene Herode adati amtulutse, usiku womwewo Petro adalikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi unyolo uwiri; ndipo alonda wokhala pakhomo adadikira ndende.

Act 12:7 Ndipo tawonani, m’ngelo wa Ambuye adayimilirapo, ndipo kuwunika kudawala mokhalamo iye; ndipo adakhoma Petro m’nthiti, namuwutsa iye, nanena, Tawuka msanga. Ndipo unyolo udagwa kuchoka m’manja mwake.

Act 12:8 Ndipo m’ngelo adati, Dzimangire m’chuwuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo adanena naye, Funda chobvala chako nunditsate ine.

Act 12:9 Ndipo adatuluka namtsata; ndipo sadadziwa kuti mchowona chochitidwa ndi m’ngelo, koma adayesa kuti alikuwona masomphenya.

Act 12:10 Ndipo m’mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, adadza ku chitseko chachitsulo chakuyang’ana kumzinda; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo adatuluka, napitilira khwalala limodzi; ndipo pomwepo m’ngelo adamchokera.

Act 12:11 Ndipo Petro atatsitsimuka adati, Tsopano ndidziwa zowona, kuti Ambuye adatuma m’ngelo wake nandilanditsa ine m’dzanja la Herode, ndi ku chilingiliro chonse cha anthu a chiyuda.

Act 12:12 Ndipo m’mene adalingilirapo, adadza ku nyumba ya Mariya amake a Yohane wonenedwanso Marko; kumene ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo ankapemphera.

Act 12:13 Ndipo pamene Petro adagogoda pa chitseko cha khomo, lidadza kudzabvomera buthu, dzina lake Roda.

Act 12:14 Ndipo pamene adazindikira mawu ake a Petro, chifukwa cha kukondwera sadatsegula pakhomo, koma adathamanga nalowanso, nawawuza kuti Petro alikuyima pakhomo.

Act 12:15 Koma adati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo adalimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo adanena, ndiye m’ngelo wake.

Act 12:16 Koma Petro adapitiriza kugogoda; ndipo m’mene adamtsegulira, adamuwona iye, nadabwa.

Act 12:17 Koma m’mene adawatambasulira dzanja akhale chete, adawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m’ndende. Ndipo adati, Muwawuze Yakobo ndi abale izi. Ndipo adatuluka napita kwina.

Act 12:18 Tsopano kutacha, padali phokoso lalikulu mwa asilikali, Petro wamuka kuti.

Act 12:19 Ndipo pamene Herode adamfunamfuna wosampeza, adafunsitsa wodikira nalamulira aphedwe. Ndipo adatsikira ku Yudeya kumka ku Kayisareya, nakhalabe kumeneko.

Act 12:20 Ndipo Herode adayipidwa nawo a ku Turo ndi Sidoni; ndipo adamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m’mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, adapempha mtendere, popeza dziko lawo lidapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.

Act 12:21 Ndipo tsiku lopangira Herode adabvala zobvala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mawu a pabwalo.

Act 12:22 Ndipo wosonkhanidwawo adafuwula, ndiwo mawu a Mulungu, si a munthu ayi.

Act 12:23 Ndipo pomwepo m’ngelo wa Ambuye adamkantha, chifukwa sadampatsa Mulungu ulemerero; ndipo adadyedwa ndi mphutsi natsirizika.

Act 12:24 Koma mawu a Mulungu adakula, nachuluka.

Act 12:25 Ndipo Barnaba ndi Saulo adabwerera kuchokera ku Yerusalemu m’mene adatsiriza utumiki wawo natenga pamodzi nawo Yohane wonenedwanso Marko.



13

Act 13:1 Ndipo kudali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiyokeya mu mpingo wa komweko, ndiwo Barnaba, ndi Simeoni, wonenedwa Nigeri, ndi Lukiya wa ku Kurene, Manayeni woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo.

Act 13:2 Ndipo pakutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera adati, Mundipatulire Ine Barnaba ndi Saulo ku ntchito imene ndidawayitanira.

Act 13:3 Ndipo pamene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuyika manja pa iwo, adawatumiza amuke.

Act 13:4 Pamenepo iwo, wotumidwa ndi Mzimu Woyera, adatsikira ku Selukeya; ndipo pochokera kumeneko adapita m’chombo ku Kupro.

Act 13:5 Ndipo pamene adakhala ku Salami, adalalikira m’masunagoge a Ayuda; ndipo adali nayenso Yohane monga wakuwathangatira iwo.

Act 13:6 Ndipo m’mene adapitilira chisumbu chonse kufikira Pafo, adapezapo munthu, wamatsenga m’neneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Baryesu:

Act 13:7 Ameneyo adali ndi kazembe Sergiyo Paulo, ndiye munthu wa nzeru. Yemweyo adayitana Barnaba ndi Saulo, nafunitsa kumva mawu a Mulungu.

Act 13:8 Koma Elima watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) adawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe kuchikhulupiriro.

Act 13:9 Koma Saulo, (ndiye Paulo) wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adampenyetsetsa iye,

Act 13:10 Ndipo adati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuyipsa njira zolunjika za Ambuye?

Act 13:11 Ndipo tsopano tawona, dzanja la Ambuye liri pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa ndi nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo adamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.

Act 13:12 Pamenepo kazembe pakuwona chochitikacho adakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.

Act 13:13 Tsopano pamene Paulo ndi gulu lake adamasuka kuchokera ku Pafo, iwo adafika ku Perge wa ku Pamfuliya; koma Yohane adapatukana nawo nabwerera kumka ku Yerusalemu.

Act 13:14 Koma pamene iwowa adachoka ku Perge adafika ku Antiyokeya wa m’Pisidiya; ndipo adalowa m’sunagoge tsiku la sabata, nakhala pansi.

Act 13:15 Ndipo m’mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge adatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nawo mawu akudandawulira anthu, nenani.

Act 13:16 Ndipo Paulo adanyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israyeli, ndi inu akuwopa Mulungu, mverani.

Act 13:17 Mulungu wa anthu awa Israyeli adasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m’dziko la Egupto, ndipo ndi dzanja lokwezeka adawatulutsa iwo m’menemo.

Act 13:18 Ndipo monga nthawi ya zaka, makumi anayi adawalekerera m’chipululu.

Act 13:19 Ndipo m’mene adawononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri m’kanani, adawapatsa dziko cholowa pakuchita mayere.

Act 13:20 Ndipo zitatha izi iye adawapatsa iwo, woweruza kwa zaka mazana anayi kudza makumi asanu, kufikira Samueli m’neneriyo.

Act 13:21 Ndipo kuyambira pamenepo adapempha mfumu; ndipo Mulungu adawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, mpata wa zaka makumi anayi.

Act 13:22 Ndipo m’mene adamchotsa iye, adawawutsira Davide akhale mfumu yawo; amenenso adamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.

Act 13:23 Wochokera mu mbewu yake ya munthu uyu, Mulungu, monga mwa lonjezano, adautsira Israyeli Mpulumutsi, Yesu.

Act 13:24 Pamenepo Yohane adalalikira asadafike Iye, ubatizo wakulapa kwa anthu onse a Israyeli.

Act 13:25 Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, adanena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma tawonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kumasura nsapato za kumapazi ake.

Act 13:26 Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo a mwa inu akuwopa Mulungu, kwa inu atumidwa mawu a chipulumutso ichi.

Act 13:27 Pakuti iwo akukhala m’Yerusalemu, ndi oweruza awo, popeza sadamzindikira Iye, ngakhale mawu a aneneri wowerengedwa masabata onse, adakwaniritsa pakumtsutsa Iye

Act 13:28 Ndipo ngakhale kuti sadapeza chifukwa chakumuphera, adapempha Pilato kuti Iye aphedwe.

Act 13:29 Ndipo atakwaniritsa zonse zolembedwa za Iye, adamtsitsa kumtengo, namuyika m’manda.

Act 13:30 Koma Mulungu adamuwukitsa Iye kwa akufa.

Act 13:31 Ndipo adawonekera masiku ambiri ndi iwo amene adamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.

Act 13:32 Ndipo ife tikulalikirani inu za Uthenga Wabwino wa lonjezano lochitidwa kwa makolo,

Act 13:33 Kuti Mulungu wakwaniritsa ili kwa ana athu pakuwukitsa Yesu; monganso mulembedwa m’Salmo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.

Act 13:34 Ndipo monga ndi kunkhudzana ndikuti Iye adawukitsa Iye kwa akufa, wosabwereranso kuchibvundi, adateronso, ndidzakupatsani inu madalitso woyera ndi wotsimikizika a Davide.

Act 13:35 Chifukwa anenanso m’Salmo lina, simudzapereka Woyera wanu awone chibvundi.

Act 13:36 Pakutitu, Davide, m’mene adautumikira uphungu wa Mulungu mu m’bado mwake mwa iye yekha, adagona tulo, nayikidwa kwa makolo ake, nawona chibvundi:

Act 13:37 Koma Iye amene Mulungu adamuwukitsanso sadawona chibvundi.

Act 13:38 Chotero kudziwike kwa inu amuna ndi abale, kuti mwa munthu uyu, kulalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo:

Act 13:39 Ndipo mwa Iye yense wokhulupira ayesedwa wolungama kumchotsera zimene simudakatha kudzichotsera poyesedwa wolungana ndi chilamulo cha Mose.

Act 13:40 Chifukwa chake chenierani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo;

Act 13:41 Tawonani, inu wopeputsa, ndikuzizwa ndi kuwonongeka; kuti ine ndigwira, ntchito imene m’masiku anu, simudzayikhulupira wina ngakhale munthu wina adzakuwuzani.

Act 13:42 Ndipo pamene Ayuda adatuluka m’sunagoge, amitundu adapempha kuti adzayankhule nawonso mawu awa Sabata likudzalo.

Act 13:43 Ndipo m’mene anthu a m’sunagoge adabalalika, Ayuda ambiri ndi wopinduka wopembedza adatsata Paulo ndi Barnaba; amene poyankhula nawo, adawawumiriza akhale m’chisomo cha Mulungu.

Act 13:44 Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mzinda wonse kudzamva mawu a Mulungu.

Act 13:45 Koma Ayuda, pakuwona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zinthu zoyankhulidwa ndi Paulo, monga zosemphana komanso za mwano.

Act 13:46 Ndipo Paulo ndi Barnaba adalimbika mtima ponena, nati, Kudafunika kuti mawu a Mulungu ayambe ayankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, tawonani, ife titembenukira kwa amitundu.

Act 13:47 Pakuti kotero adatilamulira Ambuye ndi kuti, Ndakuyika iwe kuwunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero adziko lapansi.

Act 13:48 Ndipo pakumva ichi amitundu adakondwera, nalemekeza mawu a Mulungu; ndipo onse amene adayikidwiratu ku moyo wosatha adakhulupirira.

Act 13:49 Ndipo mawu a Ambuye anabukitsidwa m’dziko lonselo.

Act 13:50 Koma Ayuda adautsa akazi wopembedza ndi wolemekezekeka, ndi zika zazikulu za muzindawo, nawawutsira chizunzo Paulo ndi Barnaba, ndipo adawapitikitsa iwo m’malire awo.

Act 13:51 Koma iwo, adawasansira fumbi la kumapazi awo nadza ku Ikoniyo.

Act 13:52 Ndipo akuphunzira adadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.



14

Act 14:1 Ndipo kudali pa Ikoniyo kuti adalowa pamodzi m’sunagoge wa Ayuda, nayankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Ahelene lidakhulupirira.

Act 14:2 Koma ayuda wosakhulupirira adawutsa mitima ya amitundu ndikupangitsa maganizo awo kuti achitire zoipa abale athu.

Act 14:3 Chifukwa chake adakhala nthawi yayikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene adachitira umboni mawu a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja awo.

Act 14:4 Ndipo khamu la mumzinda lidagawikana; ena adali ndi Ayuda koma ena adali ndi atumwi.

Act 14:5 Ndipo pamene padakhala chigumukiro cha amitundu ndi cha ayuda ndi cha oweruza awo, kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala.

Act 14:6 Iwo adamva, nathawira ku mizinda ya Lukawoniya, Lustra ndi Derbe, ndi dziko lozungulirapo.

Act 14:7 Ndipo kumeneko adalalikira Uthenga Wabwino.

Act 14:8 Ndipo pa Lustra padakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m’mapazi mwake, wopunduka chibadwire m’mimba ya amake, amene sadayendepo nthawi zonse:

Act 14:9 Ameneyo adamva Paulo alimkuyankhula; ndipo Paulo pomyang’anitsitsa, ndi kuwona kuti adali ndi chikhulupiriro cholandira nacho machiritso,

Act 14:10 Adati ndi mawu akulu, tayimilira. Ndipo iyeyu adazunzuka nayenda.

Act 14:11 Ndipo pamene anthu adawona chimene adachita Paulo, adakweza mawu awo, nati m’chinenero cha Lukawoniya, Milungu yatsikira kwa ife yokhala monga anthu.

Act 14:12 Ndipo adamutcha Barnaba, Jupitala; ndi Paulo, Merkasi, chifukwa adali wotsogola kunena.

Act 14:13 Pamenepo wansembe wa Jupitala wokhala kumaso kwa mzinda, adadza nazo ng’ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi anthu.

Act 14:14 Pamene adamva atumwi Paulo ndi Barnaba, adang’amba zofunda zawo, nathamangira m’kati mwa anthu nafuwula,

Act 14:15 Nati, Anthunu, bwanji mukuchita zinthu zimenezi? Ifenso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene adalenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse ziri momwemo.

Act 14:16 M’mibadwo yakale Iye adaleka mitundu yonse iyende m’njira zawo.

Act 14:17 Koma sadadzisiyira Iye mwini wopanda mboni, popeza adachita zabwino, natipatsa ife zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yathu ndi chakudya ndi chikondwerero.

Act 14:18 Ndipo pakunena zinthu izi, anthuwo adachita mantha naleka wosapereka nsembe kwa iwo.

Act 14:19 Ndipo adafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiyokeya ndi Ikoniyo; nakopa anthu, ndipo adamponya Paulo miyala, namkokera kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.

Act 14:20 Koma pamene adamzinga akuphunzirawo, adawuka iye, nalowa m’mumzinda; m’mawa mwake adatuluka ndi Barnaba kumka ku Derbe.

Act 14:21 Pamene atatha kulalikira Uthenga Wabwino pamzinda umenewo, ataphunzitsa ambiri, anabweranso ku Lustra ndi Ikoniyo ndi Antiyokeya.

Act 14:22 Nalimbikitsa mitima ya wophunizra, nawadandawulira iwo kuti akhalebe m’chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

Act 14:23 Ndipo pamene adawayikira akulu mosankha pa Mpingo uliwonse atatha kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, adayikiza iwo kwa Ambuye amene adamkhulupirirayo.

Act 14:24 Ndipo adapitilira pa Pisidiya, nafika ku Pamfuliya.

Act 14:25 Ndipo atalalikira mawu m’Perge, adatsikira ku Ataliya:

Act 14:26 Komweko adachoka m’chombo kumka ku Antiyokeya, kumene adayikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adayimalizayo.

Act 14:27 Pamene adafika nasonkhanitsa Mpingo adabwerezanso zomwe Mulungu adachita nawo, kuti adatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.

Act 14:28 Ndipo adakhala komweko ndi wophunzira nthawi yayitali.



15

Act 15:1 Ndipo adadza ena wotsikira ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwa mwambo wa Mose, simungathe kupulumutsidwa.

Act 15:2 Ndipo pamene Paulo ndi Barnaba adachitana nawo makani ndi mafunsano, abale adapatula Paulo ndi Barnaba, ndi ena a iwo, kuti akwere kumka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.

Act 15:3 Ndipo iwo adaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Foyinika ndi Samariya, nawafotokozera za kutembenuka mtima kwa amitundu; anakondweretsa kwambiri abale onse.

Act 15:4 Pamene adafika ku Yerusalemu, adalandiridwa ndi mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo adawafotokozeranso zonse zimene Mulungu adachita nawo.

Act 15:5 Koma adawuka ena a mpatuko wa Afarisi wokhulupirira, nati, kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwawuza kuti asunge chilamulo cha Mose.

Act 15:6 Ndipo adasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo.

Act 15:7 Ndipo pamene padali mafunsano ambiri, Petro adayimilira, nati, kwa iwo, amuna inu, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu adasankha mwa inu, kuti m’kamwa mwanga amitundu amve mawu a Uthenga Wabwino nakhulupirire.

Act 15:8 Ndipo Mulungu amene adziwa mitima, adawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga adatipatsa ife;

Act 15:9 Ndipo sadalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yawo m’chikhulupiriro.

Act 15:10 Nanga bwanji tsopano muli kumuyesa Mulungu, kuti muyike pa khosi la wophunzira goli, limene sadatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

Act 15:11 Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, monga iwo omwe.

Act 15:12 Ndipo khamu lonse lidatonthola; ndipo adamvera Barnaba ndi Paulo akuwafotokozeranso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu adachita nawo pa amitundu.

Act 15:13 Ndipo pamene iwo adatonthola Yakobo adayankha, nati, Abale, Mverani ine:

Act 15:14 Simoni wafotokoza kuti poyamba Mulungu adayang’anira a mitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.

Act 15:15 Ndipo zinthu izi zigwirizana ndi mawu a aneneri; monga kudalembedwa.

Act 15:16 Zikadzatha izi, ndidzabwera, ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chidagwa; ndidzamanganso zopasula zake, ndipo ndidzachiyimikanso:

Act 15:17 Kuti anthu wotsalira afunefune Ambuye, ndi amitundu onse amene dzina langa lidatchulidwa pa iwo, ati Ambuye amene achita zinthu zonse.

Act 15:18 Chodziwika kwa Mulungu ndi ntchito zake zonse kuyambira pa chiyambi cha dziko lapansi.

Act 15:19 Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisabvute a mwa amitundu amene adatembenukira kwa Mulungu:

Act 15:20 Koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi chiwerewere, ndi zopotola, ndi mwazi.

Act 15:21 Pakuti Mose, kuyambira nthawi yakale ali nawo m’mizinda yonse iwo amene amlalikira iye, akuwerenga mawu ake m’masunagoge masabata onse.

Act 15:22 Pamenepo chidakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse yense kusankha anthu a m’gulu lawo, ndi kuwatumiza ku Antiyokeya ndi Paulo ndi Barnaba; ndiwo Yuda wotchedwa Barnaba, ndi Sila, akulu a mwa abale;

Act 15:23 Ndipo iwo adalemba makalata natumiza kwa iwo mmalembedwe wotere, Atumwi ndi akulu ndi abale atumiza moni kwa abale a mwa amitundu a mu Antiyokeya, ndi Suriya, ndi Kilikiya.

Act 15:24 Popeza tamva kuti ena amene adatuluka mwa ife adakubvutani ndi mawu, nasocheretsa mitima yanu; amene adanena nanu kuti muyenera kuti mudulidwe ndi kusunga chilamulo, amenewo ife sitinawatume:

Act 15:25 Chidatikomera ife ndi mtima umodzi, kusankha anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi wokondedwa athu Barnaba ndi Paulo.

Act 15:26 Amuna amene adapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu.

Act 15:27 Tatumiza tsono Yuda ndi Sila, omwenso adzakuwuzani ndi mawu zinthu zomwezo.

Act 15:28 Pakuti chidakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi;

Act 15:29 Kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi chiwerewere; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.

Act 15:30 Tsono pamene iwo adamuka adatsikira ku Antiyokeya; ndipo adasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.

Act 15:31 Imene pamene adayiwerenga, adakondwera chifukwa cha kusangalatsa chake.

Act 15:32 Ndipo Yuda ndi Sila, wokhala eni wokha aneneri, anadandaulira abale ndi mawu ambiri, nawalimbikitsa iwo.

Act 15:33 Ndipo pamene iwo adakhala nthawi, abale adalawirana nawo ndi mtendere amuke kwa iwo amene adawatumiza.

Act 15:34 Komabe zidasangalatsa Sila kuti akhalebe komweko.

Act 15:35 Koma Paulo ndi Barnaba adakhalabe m’Antiyokeya, akuphunzitsa, ndi kulalikira mawu a Ambuye pamodzi ndi ena ambirinso.

Act 15:36 Patapita masiku, Paulo adati kwa Barnaba, Tibwererenso, tizonde abale m’mizinda yonse m’mene tidalalikiramo mawu a Ambuye, tiwone mkhalidwe wawo.

Act 15:37 Ndipo Barnaba adafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko.

Act 15:38 Koma sikudamkomera Paulo kumtenga iye amene adawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nawo ku ntchito.

Act 15:39 Ndipo padali kupsetsana mtima, kotero kuti adalekana wina ndi mzake; ndipo Barnaba adatenga Marko nalowa m’chombo, namka ku Kupro.

Act 15:40 Koma Paulo adasankha Sila namuka, woyamikiridwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye.

Act 15:41 Ndipo iye adapita kupyola pa Suriya ndi Kilikiya, natsimikizira Mipingo.



16

Act 16:1 Ndipo adafikanso ku Derbe ndi Lustra: ndipo tawonani, padali wophunzira wina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mhelene:

Act 16:2 Ameneyo adamchitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.

Act 16:3 Iyeyo Paulo adafuna kuti amuke naye, ndipo adamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene adakhala m’mayikomo; pakuti onse adadziwa kuti atate wake adali Mhelene.

Act 16:4 Pamene adapita kupyola pamizinda, adapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene adalamulira atumwi ndi akulu wokhala mu Yerusalemu.

Act 16:5 Kotero mipingoyo idakhazikika m’chikhulupiriro, ndipo inachuluka m’chiwerengero chake tsiku ndi tsiku.

Act 16:6 Ndipo pamene iwo adapita kupyola pa dziko la Frugiya ndi dera la Galatiya, pamenepo adaletsedwa ndi Mzimu Woyera kuti asalalikire mawu m’Asiya;

Act 16:7 Adayesa atafika ku Musiya, kumka ku Bituniya; koma Mzimu sadawaloleze.

Act 16:8 Ndipo iwo podutsa pa Musiya, adatsikira ku Trowa.

Act 16:9 Ndipo masomphenya adawonekera kwa Paulo usiku; padali munthu wa ku Makedoniya alimkuyimilira, namdandaulira kuti, muwolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithandize ife.

Act 16:10 Ndipo atawona masomphenya, pomwepo adayesa kutulukira kumka ku Makedoniya, potsimikizira kuti Mulungu adayitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.

Act 16:11 Chotero tidachokera ku Trowa m’chombo, m’mene tidalunjikitsa ku Samotrake, ndipo m’mawa mwake ku Neapoli;

Act 16:12 Pochokera kumeneko tidafika ku Filipi, mzinda wa ku Makedoniya, waukulu wa m’dzikomo, wa milaga ya Aroma; ndipo tidakhala mumzindawo masiku ena.

Act 16:13 Ndipo pa tsiku la sabata tidatuluka kumzinda kumka ku mbali ya mtsinje, kumene tidaganizira kuti amapempherako; ndipo tidakhala pansi ndi kuyankhula ndi akazi amene adasonkhana.

Act 16:14 Ndipo adatimva mkazi wina dzina lake Lidiya, wogulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiyatira, amene adapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye adatsegula, kuti amvere zimene adazinena Paulo.

Act 16:15 Ndipo pamene adabatizidwa iye ndi a pabanja pake adatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m’nyumba yanga, mugone m’menemo. Ndipo adatiwumiliza ife.

Act 16:16 Ndipo panali, pamene tidalikupita kukapemphera, adakomana ndi ife namwali wina amene adali ndi mzimu wambwembwe, amene adapindulira ambuye ake zambiri pa kubwebweta pake.

Act 16:17 Ameneyo adatsata Paulo ndi ife, nafuwula, kuti, Anthu awa ndi atumiki a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.

Act 16:18 Ndipo adachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo adabvutika mtima ndithu, nachewuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m’dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo udatuluka nthawi yomweyo:

Act 16:19 Koma pamene Ambuye ake adawona kuti kulingalira kwa kupindula kwawo kwatha, adagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kumalo a msika kubwalo la woweluza.

Act 16:20 Ndipo adamka nawo kwa woweruza, nati; Anthu awa wokhala Ayuda abvutitsa kwambiri mzinda wathu,

Act 16:21 Ndipo aphunzitsa miyambo imene siyiloleka ife kuyilandira, kapena kuyichita, chifukwa ndife Aroma.

Act 16:22 Ndipo lidagumukira iwo khamulo; ndipo woweruza adawang’ambira malaya awo; nalamulira kuti awakwapule.

Act 16:23 Ndipo pamene adawawonetsa mikwingwirima yambiri, adawayika m’ndende, nawuza mdindo kuti awasunge bwino.

Act 16:24 Pakumva iye kulamulira kotero adawayika m’chipinda cha m’kati, namangitsa mapazi awo m’zigologolo.

Act 16:25 Ndipo pakati pa usiku, Paulo ndi Sila adalimkupemphera, nayimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m’ndendemo adalimkuwamva.

Act 16:26 Ndipo mwadzidzidzi padali chibvomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende adagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse padatseguka; ndi unyolo wonse udamasuka.

Act 16:27 Ndipo pamene adadzuka kutulo mdindoyo, adawona kuti pa makomo a ndende padatseguka, ndipo adasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am’ndende adathawa.

Act 16:28 Koma Paulo adafuwula ndi mawu akulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tiri muno.

Act 16:29 Ndipo mdindo adayitanitsa nyali, natumphira mkati, alimkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Sila,

Act 16:30 Ndipo adawatulutsa iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?

Act 16:31 Ndipo iwo adati; khulupirira pa Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi apabanja ako.

Act 16:32 Ndipo adayankhula naye mawu a Ambuye, pamodzi ndi onse a mnyumba mwake.

Act 16:33 Ndipo adawatenga ola lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yawo; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a mnyumba mwake.

Act 16:34 Ndipo pamene iye adawatenga iwo kulowa nawo kunyumba kwake, anawakhazikira chakudya,anasangalala kwambiri, pamodzi ndi a panyumba yake yonse pokhulupirira Mulungu.

Act 16:35 Ndipo pamene kudacha, woweruza adatumiza asilikali, kuti Mukamasule anthu aja adzipita.

Act 16:36 Ndipo mdindo wa ndende adawafotokozera mawuwo kwa Paulo, nati, Woweruza atumiza mawu kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.

Act 16:37 Koma Paulo adati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tiri Aroma, natiyika m’ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m’seri? Iyayi, ndithu; koma adze wokha atitulutse.

Act 16:38 Ndipo asilikaliwo adafotokozera mawuwo kwa woweruza; ndipo iwowo adawopa, pakumva kuti adali Aroma.

Act 16:39 Ndipo adadza nawapembedza; ndipo pamene adawatulutsa, adawapempha kuti achoke muzinda wawo.

Act 16:40 Ndipo adatuluka m’ndendemo, nalowa m’nyumba ya Lidiya: ndipo pamene adawona abale, adawatonthoza iwo ndipo adachoka.



17

Act 17:1 Tsopano pamene adapitilira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, adafika ku Tesalonika, kumene kudali sunagoge wa Ayuda.

Act 17:2 Ndipo Paulo, monga amachita, adalowa kwa iwo; ndipo masabata atatu adanena ndi iwo za m’malembo, natanthauzira,

Act 17:3 Natsimikiza, kuti kudayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuwuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.

Act 17:4 Ndipo ena a iwo adakhulupirira, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akulu osati wowerengeka.

Act 17:5 Koma Ayuda amene sadakhulupirire anadukidwa mtima, natenga anthu ena woyipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso mzinda wonse; ndipo adagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.

Act 17:6 Ndipo pamene sadawapeza adakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa oweruza a muzinda, nafuwula kuti, omwe aja amene anatembenuza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;

Act 17:7 Amene Yasoni wawalandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo a Kayisala; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu.

Act 17:8 Ndipo iwo adabvuta anthu, ndi oweruza a muzinda, pamene adamva zinthu zimenezi.

Act 17:9 Ndipo pamene adalandira chikole kwa Yasoni ndi enawo adawamasula.

Act 17:10 Pomwepo abale adatumiza Paulo ndi Sila usiku kumka ku Bereya; pamene iwo adafika komweko adalowa m’sunagoge wa Ayuda.

Act 17:11 Amenewa adali mfulu koposa a m’Tesalonika, popeza adalandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zidali zotero.

Act 17:12 Ndipo ambiri a iwo adakhulupirira; ndi akazi a chihelene wolemekezeka ndi amuna, osati wowerengeka.

Act 17:13 Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika adazindikira kuti mawu a Mulungu adalalikidwa ndi Paulo ku Bereyanso, adadza komwekonso, nawutsa, kubvuta anthu.

Act 17:14 Pomwepo abale adatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Sila ndi Timoteo adakhalabe komweko.

Act 17:15 Koma iwo amene adaperekeza Paulo adadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Sila ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, adachoka.

Act 17:16 Tsopano pamene Paulo adalindira iwo pa Atene, adabvutidwa mtima pamene adawona mudzi wonse wadzala ndi mafano.

Act 17:17 Chotero tsono adatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m’sunagoge, ndi m’bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene adakomana nawo.

Act 17:18 Ndipo akukonda nzeru ena a Epikureya ndi a Stoyiki adatengana naye. Ena adati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa adalalikira Yesu ndi kuwuka kwa akufa.

Act 17:19 Ndipo adamgwira, namka naye ku Arewopagi, nati, kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi cha tsopano uchinena iwe?

Act 17:20 Pakuti ufika nazo ku makutu athu zinthu za chilendo; tifuna tsono kudziwa, zinthu izi ndizotani?

Act 17:21 (Pakuti Aatene onse ndi alendo akukhalamo amataya nthawi yawo, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva zinthu zatsopano.)

Act 17:22 Ndipo Paulo adayimilira pakati pa phiri la Masi nati, Amuna inu a Atene, mzinthu zonse ndiwona kuti muli wopembedzetsa.

Act 17:23 Pakuti popita, ndi kuwona zinthu zimene muzipemphedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa motere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA.chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.

Act 17:24 Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja.

Act 17:25 Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;

Act 17:26 Ndipo ndiye m’modzi adalenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo.

Act 17:27 Kuti afunefune Ambuye, kapena akamfufuze ndi kumpeza Iye,ngakhale kuti Iye sakhala patali ndi yense wa ife;

Act 17:28 Pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a kuyimba anu ati, pakuti ifenso tiri mbadwa zake.

Act 17:29 Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu sitiyenera kulingalira kuti Umulungu uli wofanafana ndi golidi, kapena Siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.

Act 17:30 Ndipo nthawi za kusadziwako tsono Mulungu adalekerera; koma tsopanotu alimkulamulira anthu onse ponse ponse alape.

Act 17:31 Chifukwa adapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene adamuyikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene adamuwukitsa Iye kwa akufa.

Act 17:32 Ndipo pamene adamva za kuwuka kwa akufa ena adaseka pwepwete; koma ena adati, Tidzakumvanso iwe za nkhani iyi.

Act 17:33 Choncho Paulo adachoka pakati pawo.

Act 17:34 Koma ena adadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso mudali Diyonisiyo M-arewopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nawo.



18

Act 18:1 Zitapita zinthu izi, Paulo adachoka ku atene, nadza ku Korinto;

Act 18:2 Ndipo adapeza Myuda wina dzina lake Akula, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Priskila, (chifukwa cha Klaudiyo adalamulira Ayuda onse achoke m’Roma;) ndipo Paulo adadza kwa iwo;

Act 18:3 Ndipo popeza adali wa ntchito imodzimodzi, adakhala nawo, ndipo iwowa adagwira ntchito; pakuti ntchito yawo idali yosoka mahema.

Act 18:4 Ndipo adafotokozera m’sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.

Act 18:5 Koma pamene Sila ndi Timoteo adadza potsika ku Makedoniya, Paulo adapsinjidwa mu mzimu, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.

Act 18:6 Koma pamene iwo adamkana, nachita mwano, adakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndiribe nanu chifukwa; kuyambira tsopano ndimka kwa amitundu.

Act 18:7 Ndipo adachoka kumeneko, nalowa m’nyumba ya munthu wina, dzina lake Tito Yustro, amene adapembedza Mulungu, nyumba yake idayandikizana ndi sunagoge.

Act 18:8 Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, adakhulupirira pa Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri adamva, nakhulupirira, nabatizidwa.

Act 18:9 Ndipo Ambuye adati kwa Paulo usiku m’masomphenya, Usawope, koma yankhula, usakhale chete:

Act 18:10 Chifukwa Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuyipse; chifukwa ndiri ndi anthu ambiri muzinda uno.

Act 18:11 Ndipo adakhala komweko chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mawu a Mulungu mwa iwo.

Act 18:12 Tsono pamene Galiyo adali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi adamuwukira Paulo, namka naye ku mpando wachiweruziro.

Act 18:13 Nanena, uyu akopa anthu apembedze Mulungu mosemphana ndi chilamulo.

Act 18:14 Koma Paulo pamene adati atsegule pakamwa pake, Galiyo adati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa chosalungama, kapena dumbo loyipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;

Act 18:15 Koma akakhala mafunso a mawu ndi mayina ndi chilamulo chanu; muyang’ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.

Act 18:16 Ndipo adawapitikitsa pa mpando wa chiweruziro.

Act 18:17 Ndipo ahelene onse adagwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda iye kumpando wa chiweruziro. Ndipo Galiyo sadasamalira zimenezi.

Act 18:18 Ndipo Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, adatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m’chombo ku Suriya, pamodzi naye Priskila ndi Akula; popeza adameta mutu wake m’Kokreya; pakuti adawinda.

Act 18:19 Ndipo iye adafika ku Aefeso, ndipo iye adalekana nawo pamenepo: koma iye yekha adalowa m’sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.

Act 18:20 Ndipo pamene iwo adamfunsa iye kuti akhale nthawi yina yowonjezerapo sadawabvomereza;

Act 18:21 Ndipo adawatsazika, nati, ndiyenera ine mwanjira iriyonse kusunga mphwando iri limene likudza ku Yerusalemu: koma ndidzabweranso kwa inu ngati akalola Mulungu. Ndipo adayenda pamadzi kuchoka ku Aefeso.

Act 18:22 Ndipo pamene adakocheza pa Kayisareya, adakwera nalankhula ndi mpingo, natsikira ku Antiyokeya.

Act 18:23 Ndipo atakhala kumeneko nthawi, adachoka, napita pa dziko lonse la Galatiya ndi Frugiya ndicholinga, cholimbikitsa akuphunzitsa onse.

Act 18:24 Ndipo adafika ku Aefeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Alesandreya, munthu woyankhula mwanzeru; ndipo adali wamphamvu m’malembo.

Act 18:25 Munthu ameneyu adalangizidwa m’njira ya Ambuye; pokhala nawo mzimu wachangu, adanena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Ambuye, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha.

Act 18:26 Ndipo iye adayamba kuyankhula molimba mtima m’sunagoge, koma pamene adamumva iye Priskila ndi Akula, adamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.

Act 18:27 Ndipo pamene iye adafuna kuwoloka kumka ku Akaya, abale adamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa akuphunzira kuti amlandire: ndipo pamene adafika, iye adathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo;

Act 18:28 Pakuti ndi mphamvu adakopa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu.



19

Act 19:1 Ndipo patapita nthawi, pamene Apolo adali ku Korinto, Paulo anadutsa kupyola magombe amumtunda nafika ku Aefeso: ndipo adapeza wophunzira ena;

Act 19:2 Iye adati kwa iwo, kodi mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira? Ndipo iwo adati iyayi, sitidamva konse kuti kudzakhalanso Mzimu Woyera.

Act 19:3 Ndipo iye adati, Nanga munabatizidwa ndi chiyani? Ndipo adati, Mu ubatizo wa Yohane.

Act 19:4 Pamenepo adati Paulo, Yohane indetu anabatiza ndi ubatizo wa kulapa, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Khristu Yesu.

Act 19:5 Ndipo pamene adamva ichi, adabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu.

Act 19:6 Ndipo pamene Paulo adayika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera adadza pa iwo; ndipo adayankhula ndi malilime ndi kunenera.

Act 19:7 Ndipo amuna onse adalipo ngati khumi ndi awiri.

Act 19:8 Ndipo iye adalowa m’sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu.

Act 19:9 Koma pamene ena adawumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoyipa Njirayo pamaso pa khamu, adawachokera, napatutsa akuphunzira, nafotokozera masiku onse m’sukulu ya Turano.

Act 19:10 Ndipo adachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse wokhala m’Asiya adamva mawu a Ambuye Yesu, Ayuda ndi Ahelene onse.

Act 19:11 Ndipo Mulungu adachita zozizwitsa zapaderadera ndi manja a Paulo:

Act 19:12 Kotero kuti adamuka nazo kwa wodwala msalu zopukutira ndi za pa ntchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zidawachokera, ndi mizimu yoyipa idatuluka.

Act 19:13 Koma Ayuda enanso woyendayenda, wotulutsa ziwanda, adadziyesera wokha kutchula pa iwo amene adali ndi mizimu yoyipa dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.

Act 19:14 Ndipo padali ana a amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkulu wa ansembe amene adachita chotero.

Act 19:15 Ndipo udayankha mzimu woyipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu yani?

Act 19:16 Ndipo munthu, mwa iye amene mudali mzimu woyipa, adawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti adathawa m’nyumba amaliseche ndiwobvulazidwa.

Act 19:17 Ndipo zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene adakhala ku Aefeso; ndipo mantha adagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu lidakuzika.

Act 19:18 Ndipo ambiri a iwo wokhulupirirawo adadza, nabvomereza, nawonetsa ntchito zawo.

Act 19:19 Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga adasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa anthu onse; ndipo adawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.

Act 19:20 Chotero mawu a Ambuye adakula mwamphamvu nalakika.

Act 19:21 Ndipo zitatha zinthu izi, Paulo adatsimikiza mu mzimu wake, atapita kupyola pa Makedoniya ndi Akaya, kumka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuwonanso ku Roma.

Act 19:22 Pamenepo adatuma ku Makedoniya awiri a iwo adamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini adakhalabe nthawi m’Asiya.

Act 19:23 Nthawi yomweyo kudali phokoso lambiri lakunena za Njirayo.

Act 19:24 Pakuti munthu wina dzina lake Demetriyo wosula siliva, amene adapanga tiakachisi tasiliva ta Diyana, adawonetsera amisili phindu lambiri;

Act 19:25 Amenewo iye adawasonkhanitsa pamodzi ndi amisili a ntchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife timapeza chuma chathu.

Act 19:26 Ndipo muwona ndi kumva, kuti si pa Aefeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, aulo uyu akopa ndi kutembenuza anthu ambiri, ndi kuti, Sindiyo milungu iyi imene ipangidwa ndi manja;

Act 19:27 Sikuti ndi ntchito yathu yokhayi imene iri pachiwopsezo ndi kunyonyosoka; komanso kuti kachisi wa mulungu wathu wamkazi Diyana adzayamba kunyozedwa; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a m’Asiya onse, ndi onse a m’dziko lokhalamo anthu, ampembedza.

Act 19:28 Ndipo pamene adamva zonenazi, adadzala ndi mkwiyo, nafuwula, nati, Wamkulu ndi Diyana wa ku Aefeso.

Act 19:29 Ndipo muzinda monse mudadzaza ndi chisokonezeko, ndipo adagwira Gayondi Arstarko, amuna Akumakedoniya, anzake a Paulo woyenda nawo, nathamanga iwo onse ndi mtima umodzi kunka kubwalo la masewera.

Act 19:30 Ndipo pamene Paulo adafuna kulowa kwa anthu, akuphunzira ake sadamloleza.

Act 19:31 Ndipo akulu ena a m’Asiyanso, popeza adali abwenzi ake, adatumiza mawu kwa iye, namupempha kuti asadziponye yekha ku bwalo lamasewera.

Act 19:32 Ndipo ena adafuwula za chinthu china, ndi enanso chinthu china; ndikuti mnsonkhano wonse udasokonezeka; ndipo unyinji sudadziwa chifukwa chake cha chimene adasonkhanira.

Act 19:33 Ndipo adatuluka Alesandro m’khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro adatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.

Act 19:34 Koma pozindikira kuti ali Myuda, kudali mawu amodzi a kwa onse akufuwula monga maola awiri, Wamkulu ndi Diyana wa Aefeso.

Act 19:35 Ndipo pamene mlembi wa mzinda adatontholetsa anthuwo, adati, Amuna a Aefeso inu, munthu uyu ndindani wosadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wopembedza Mulungu wamkazi wamkulu Diyana, ndi fano limene lidagwa pansi kuchokera ku Jupita?

Act 19:36 Powona pamenepo kuti zinthu izi. Sizingalankhulidwe mozitsutsa, muyenera inu kukhala chete, ndi kusachita kanthu mothamanga.

Act 19:37 Pakuti mwatenga anthu awa, wosakhala wolanda za m’kachisi, kapena wochitira Mulungu wanu wamkazi mwano.

Act 19:38 Ngati tsono Demetriyo ndi amisili wokhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; asiyeni adandaulirane wina ndi mzake.

Act 19:39 Koma ngati mufuna kanthu kazinthu zina, kadzaganiziridwa pa m’sonkhano wina wolamulidwa.

Act 19:40 Pakuti mpotiwopsa kuti tachita chipolowe lero; popanda chifukwa chake chachipolowechi.

Act 19:41 Ndipo pamene adanena izi, anabalalitsa msonkhanowo.



20

Act 20:1 Ndipo litaleka phokoso, Paulo adayitana wophunzirawo, ndipo m’mene adawakupatira, adalawirana nawo, natuluka kumka ku Makedoniya.

Act 20:2 Ndipo m’mene adapitapita m’mbali zijazo, nawadandaulira, adadza ku Girisi.

Act 20:3 Ndipo adakhalako miyezi itatu, ndipo kumeneko Ayuda adapangira chiwembu, pomudikirira pamene iye ankati apite mchombo ku Suriya, naganizira zobwerera kudzera ku Makedoniya.

Act 20:4 Ndipo adamperekeza kufikira ku Asiya Sopatro mwana wa Puro, wa ku Bereya; ndi Atesalonika, Aristarko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Derbe, ndi Timoteo; ndi aku Asiya, Tukiko ndi Trofimo.

Act 20:5 Koma iwowa anatitsogolera, natiyembekezera ife pa Trowa.

Act 20:6 Ndipo tidapita m’chombo kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tidawapeza ku Trowa; pamenepo tidatsotsa masiku asanu ndi awiri.

Act 20:7 Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana akuphunzira kunyema mkate, Paulo adalalikira kwa iwo, popeza adati achoka m’mawa mwake; ndipo adanena chinenere kufikira pakati pa usiku.

Act 20:8 Ndipo mudali nyali zambiri m’chipinda cha pamwamba m’mene adasonkhanamo pamodzi.

Act 20:9 Ndipo pamenepo pazenera padali m’nyamata wina dzina lake Utiko adakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo iyeyu, adagwa posanja pachiwiri, ndipo adamtola wakufa.

Act 20:10 Ndipo potsikirako Paulo, adamgwera iye namfungatira, nati Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo.

Act 20:11 Ndipo m’mene adakweranso, nanyema mkate, nadya, nakamba nawo nthawi, kufikira kucha, adachoka.

Act 20:12 Ndipo adadza naye m’nyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu.

Act 20:13 Ndipo ife tidatsogolera kumka ku mchombo, ndipo tidapita ku Aso, pamenepo tidati timtenge Paulo; pakuti adatipangira chomwecho, koma adati ayenda pamtunda yekha.

Act 20:14 Ndipo pamene adakomana ndi ife ku Aso, tidamtenga, ndipo tidafika ku Mitilene.

Act 20:15 Ndipo m’mene tidachokerapo, m’mawa mwake tidafika pandunji pa Kiyo; ndipo m’mawa mwake tidafika ku Samo, ndipo tidakhala pa Trogiliamu; ndi m’mawa mwake tidafika ku Mileto.

Act 20:16 Pakuti Paulo adatsimikiza mtima kudzera ku Aefeso, chifukwa sadafune kuti ataye nthawi m’Asiya; chifukwa adafulumira iye, kuti ngati mkotheka, akakhale ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste.

Act 20:17 Ndipo pokhala ku Mileto adatuma ku Aefeso, nayitana akulu a Mpingo.

Act 20:18 Ndipo pamene adafika kuli iye, adati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndidafika ku Asiya, ndi makhalidwe wotani amene ndinakhala pamodzi ndi inu nthawi zonse,

Act 20:19 Wotumikira Ambuye ndi mtima wodzichepetsa ndi misozi, ndi mayesero adandigwera ndi ziwembu za Ayuda.

Act 20:20 Kuti sindidakubisirani zinthu zopindulitsa kwa inu, koma ndakuwonetserani, ndi kuphunzitsa inu pabwalo, ndi kuchokera nyumba ndi nyumba,

Act 20:21 Kuchitira umboni pamodzi kwa Ayuda ndi Ahelene wakulapa kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro chakulinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Act 20:22 Ndipo tsopano, tawonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zinthu zimene zidzandigwera ine kumeneko.

Act 20:23 Koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m’mizinda yonse, ndi kunena kuti msinga ndi zisautso zindilindira.

Act 20:24 Komatu palibe chimodzi cha zinthu izi chingathe kundisuntha ine, sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi chimwemwe, ndi utumiki umene ndidaulandira kwa Ambuye Yesu, kukachitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.

Act 20:25 Ndipo tsopano, tawonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndidapitapita mwa inu kulalikira za ufumuwo, wa Mulungu simudzawonanso nkhope yanga.

Act 20:26 Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndiribe chifukwa ndi mwazi wa munthu aliyense.

Act 20:27 Pakuti sindidakubisirani pa kukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.

Act 20:28 Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera adakuyikani woyang’anira, kuti mudyetse Mpingo wa Mulungu, umene adaugula ndi mwazi wa Iye yekha.

Act 20:29 Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, idzalowa mimbulu yolusa, yosalekerera gululo.

Act 20:30 Ndipo mwa inu nokha adzawuka anthu, woyankhula zokhotakhota, kupatutsa wophunzira awatsate.

Act 20:31 Chifukwa chake chenjerani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindidaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.

Act 20:32 Ndipo tsopano, abale, ndikuyikizani kwa Mulungu, ndi kwa mawu a chisomo chake, chimene chiri ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse woyeretsedwa.

Act 20:33 Sindidasilira siliva, kapena golidi, kapena chobvala cha munthu ali yense.

Act 20:34 Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa adatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine.

Act 20:35 M’zinthu zonse ndidakupatsani chitsanzo, chakuti pogwira ntchito, kotero muyenera kuthandiza wofowoka ndi kukumbukira mawu wa Ambuye Yesu, kuti adati yekha, kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

Act 20:36 Ndipo m’mene adanena izi, iye adagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.

Act 20:37 Ndipo onsewa adalira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona.

Act 20:38 Nalira makamaka chifukwa cha mawu adanenawa, kuti sadzawonanso nkhope yake. Ndipo adamperekeza iye kuchombo.



21

Act 21:1 Ndipo kudali, titalekana nawo ndi kukankha chombo, tinadza molunjika ku Kowo, ndi m’mawa mwake ku Rode, ndipo pochokera ku Patara:

Act 21:2 Ndipo m’mene tidapeza chombo chakuwoloka kumka ku Foyinike, tidalowamo, ndi kupita nacho.

Act 21:3 Tsopano pamene tidafika popenyana ndi Kupro, tidamsiya kudzanja lamanzere, ndipo tidapita ku Suriya; ndipo tidakocheza ku Turo; pakuti pamenepo chombo chidafuna kutula akatundu wake.

Act 21:4 Ndipo m’mene tidapeza wophunzira, tidakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa adanena ndi Paulo mwa Mzimu kuti asakwera kunka ku Yerusalemu.

Act 21:5 Ndipo kudali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kumka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, adatiperekeza kufikira kutuluka mumzinda; ndipo pogwadwa pa m’chenga wa kunyanja, tidapemphera.

Act 21:6 Ndipo pamene tidalawirana wina ndi mzake tidalowa m’chombo, koma iwo adabwerera kwawo.

Act 21:7 Ndipo pamene tidatsiriza ulendo wathu wochokera ku Turo, tidafika ku Ptolemayi; ndipo m’mene tidayankhula abale, tidakhala nawo tsiku limodzi.

Act 21:8 Ndipo m’mawa mwake ife amene tidali amgulu lake la Paulo, tidachoka, ndipo tidafika ku Kayisareya, ndipo m’mene tidalowa m’nyumba ya Filipo mlaliki, m’modzi wa asanu ndi awiri aja, tidakhala naye.

Act 21:9 Ndipo munthuyu adali nawo ana akazi anayi, anamwali, amene adanenera.

Act 21:10 Ndipo pokhalapo masiku ambiri, adatsika ku Yudeya m’neneri dzina lake Agabo.

Act 21:11 Ndipo adadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, munthu mwini lamba ili, adzam’manga kotero Ayuda a m’Yerusalemu, nadzampereka m’manja a amitundu.

Act 21:12 Koma pamene tidamva zinthu izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko kuti asakwere iye kumka ku Yeursalemu.

Act 21:13 Pamenepo Paulo adayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine sikumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.

Act 21:14 Ndipo pokana iye kukopeka, tidamleka, ndi kumalizira kunena kuti, kufuna kwa Ambuye kuchitidwe.

Act 21:15 Ndipo atapita masiku awa tidakonza akatundu athu, ndikukwera ku Yerusalemu.

Act 21:16 Ndipo adamuka nafenso ena a wophunzira a ku Kayisareya, natenganso wina Nasoni wa ku Kupro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.

Act 21:17 Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale adatilandira mokondwera.

Act 21:18 Ndipo m’mawa mwake Paulo adalowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse adali pomwepo.

Act 21:19 Ndipo atawayankhula iwo, adawafotokozera chimodzi chimodzi zinthu zimene Mulungu adachita kwa amitundu mwa utumiki wake.

Act 21:20 Ndipo pamene adazimva, izi adalemekeza Mulungu; nati, kwa iye, Uwona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirire; ndipo ali nacho changu onsewa cha pa chilamulo:

Act 21:21 Ndipo iwo adamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana awo, kapena asayende monga mwa miyambo.

Act 21:22 Chingachitike ndi chiyani tsono? Khamu lidzafuna kudza pamodzi: pakuti Adzamva kuti iwe wafika.

Act 21:23 Chifukwa chake uchite ichi tikuwuza iwe; tiri nawo amuna anayi amene adachita chowinda;

Act 21:24 Amenewa uwatenge nudziyeretse nawo pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, ndipo usunga chilamulo.

Act 21:25 Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tidalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi chiwerewere.

Act 21:26 Pamenepo Paulo adatenga anthuwo, ndipo m’mawa mwake m’mene adadziyeretsa nawo pamodzi, adalowa m’Kachisi, kukatsimikizira za chimarizidwe cha masiku a kuyeretsedwa, kufikira kuti nsembe yiperekedwe ya aliyense wa iwo.

Act 21:27 Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri adati amarizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuwona iye m’kachisi, adawutsa anthu, namgwira,

Act 21:28 Nafuwula, Amuna a Israyeli, tithandizeni, ameneyu ndi munthu uja adaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso adatenga Ahelene nalowa nawo m’Kachisi, nadetsa malo ano woyera.

Act 21:29 (Pakuti adawona Trofimo wa ku Aefeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo adayesa kuti Paulo adamtenga nalowa naye m’Kachisi).

Act 21:30 Ndipo mzinda wonse udasokonezeka, ndipo anthu adathamanga pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa m’Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo padatsekedwa.

Act 21:31 Ndipo m’mene adafuna kumupha iye, wina adamuwuza kapitawo wamkulu wa gululo kuti m’Yerusalemu monse muli chisokonezo.

Act 21:32 Ndipo pamenepo iye adatenga asilikali ndi a Kenturiyonso, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuwona kapitawo wamkulu ndi asilikali, adaleka kumpanda Paulo.

Act 21:33 Pamenepo poyandikira kapitawo wamkulu adamgwira iye, nalamulira am’mange ndi unyolo uwiri; ndipo adamfunsa kuti ndi yani uyu ndipo wachita chiyani?

Act 21:34 Koma wina adafuwula chinthu china, wina china, m’khamulo; ndipo m’mene sadathe kudziwa zowona chifukwa cha phokoso adalamulira amuke naye kulinga.

Act 21:35 Ndipo pamene adafika pamakwerero, kudatero kuti adamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa anthu.

Act 21:36 Pakuti khamu la anthu lidatsata, ndikufuwula, Mchotseni iye.

Act 21:37 Ndipo poti alowe naye m’linga, Paulo adanena kwa kapitawo wamkulu, mundilole ndi kuwuzeni kanthu? Ndipo adati, kodi udziwa chihelene?

Act 21:38 Si ndiwe Mu Aigupto uja kodi, udachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinayi kuchipululu?

Act 21:39 Koma Paulo adati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa mzinda wa Kilikiya, mfulu ya mzinda womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndiyankhule ndi anthu.

Act 21:40 Ndipo m’mene adamlola, Paulo adayimilira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, adayankhula nawo m’chinenedwe cha Chihebri, nanena,



22

Act 22:1 Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu.

Act 22:2 (Ndipo pakumva kuti adayankhula nawo m’chinenedwe cha Chihebri, adaposa kukhala chete; ndipo adati,)

Act 22:3 Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m’Tariso mzinda wa Kilikiya, koma ndaleredwa mu mzinda muno, pa mapazi a Gamaliyeli; wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndidali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero.

Act 22:4 Ndipo ndidanzunza Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.

Act 22:5 Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu: kwa iwo amenenso ndidalandira akalata kumka nawo kwa abale, ndipo ndidapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nawo womangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.

Act 22:6 Ndipo kudali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kudandiwalira pondizungulira ine kuwunika kwakukulu kuchokera kumwamba.

Act 22:7 Ndipo ndidagwa pansi, ndipo ndidamva mawu akunena nane, Saulo, Saulo, undinzunziranji Ine?

Act 22:8 Ndipo ndidayankha, Ndinu yani Ambuye? Ndipo adati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete amene umzunza.

Act 22:9 Ndipo iwo wokhala nane adawonadi kuwunika, ndipo adachita mantha; koma sadamva mawu akuyankhula nane.

Act 22:10 Ndipo ndidati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye adati kwa ine, Tawuka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zinthu zonse zoyikika kwa iwe uzichite.

Act 22:11 Ndipo popeza sindidapenya, chifukwa cha ulemerero wa kuwunikako, adandigwira dzanja iwo amene adali ndi ine, ndipo ndidafika ku Damasiko.

Act 22:12 Ndipo munthu dzina lake Hananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene am’chitira umboni wabwino Ayuda onse akukhala kumeneko.

Act 22:13 Adadza kwa ine, ndipo poyimilirapo adati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ola lomwelo ndidapenya.

Act 22:14 Ndipo adati, Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake, nuwone Wolungamayo, numve mawu wotuluka m’kamwa mwake.

Act 22:15 Ndipo udzakhara mboni yake kwa anthu onse, za zimene udaziwona ndi kuzimva.

Act 22:16 Ndipo tsopano uchedweranji? Tawuka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuyitane pa dzina la Ambuye.

Act 22:17 Ndipo kudali, nditabwera ku Yerusalemu ndidalikupemphera m’kachisi, ndidachita ngati kukomoka;

Act 22:18 Ndipo ndidamuwona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga m’Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wonena za Ine.

Act 22:19 Ndipo ndidati ine, Ambuye, adziwa iwo wokha kuti ndidali kuyika m’ndende ndi kuwapanda m’masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu:

Act 22:20 Ndipo pamene adakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndine ndidalikuyimirirako, ndi kubvomerezana nawo, ndi kusunga zobvala za iwo amene adamupha iye.

Act 22:21 Ndipo adati kwa ine,nyamuka; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kumka kutali kwa amitundu.

Act 22:22 Ndipo adamumva kufikira mawu awa; ndipo adakweza mawu awo nanena, Achoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

Act 22:23 Ndipo pofuwula iwo, ndi kutaya zobvala zawo, ndi kuwaza fumbi mumlengalenga,

Act 22:24 Kapitawo wamkulu adalamulira kulowa naye kunyumba ya kulinga; nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake chiyani kuti amfuwulira chomwecho.

Act 22:25 Ndipo m’mene adam’manga iye ndi msingazo, Paulo adati kwa Kenturiyo wakuyimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, wosalakwa?

Act 22:26 Ndipo pamene adamva ichi Kenturiyo, adamka kwa kapitawo wamkulu, namuwuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyu ndi Mroma.

Act 22:27 Ndipo kapitawo wa mkuluyo adadza, nati kwa iye, ndiwuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo adati, Inde.

Act 22:28 Ndipo kapitawo wa mkulu adayankha, Ine ndalandira ufulu ndi mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo adati; ine ndinabadwa Mroma.

Act 22:29 Pamenepo iwo amene adati amfunsefunse, adamsiya: ndipo kapitawo wamkulunso adawopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adam’manga iye.

Act 22:30 Koma m’mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti adam’nenera Ayuda, adam’masula iye, nalamulira asonkhane ansembe akulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo adatsika naye Paulo, namuyika pamso pawo.



23

Act 23:1 Ndipo Paulo popenyetsetsa a m’bwalo la akulu adati, Amuna, abale ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbu mtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.

Act 23:2 Ndipo mkulu wa ansembe Hananiya adalamulira akuyimirirako ampande pakamwa pake.

Act 23:3 Pamenepo Paulo adati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe: ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza ine monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine mosemphana ndi chilamulo?

Act 23:4 Ndipo iwo akuyimirirako adati, ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?

Act 23:5 Ndipo Paulo adati, sindidadziwa, abale, kuti ndiye mkulu wansembe; pakuti kwalembedwa, usamnenera choyipa oweruza wa anthu ako.

Act 23:6 Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena, Afarisi, adafuwula m’bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuwuka kwa akufa.

Act 23:7 Ndipo pamene adatero, kudakhala malekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo khamulo lidagawikana.

Act 23:8 Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuwuka kwa akufa, kapena m’ngelo, kapena mzimu; koma Afarisi abvomereza zonse ziwiri.

Act 23:9 Ndipo chidawuka chipolowe chachikulu; ndipo alembi ena a kwa Afarisi adayimilira, natsutsana, nanena, sitipeza choyipa chiri chonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena m’ngelo wayankhula naye; sitiyenera kulimbana ndi Mulungu.

Act 23:10 Ndipo pamene padawuka chipolowe chachikulu, kapitawo wamkulu adawopa kuti angamkhadzule Paulo, ndipo adalamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pawo, nadze naye kulowa naye mnyumba ya m’linga.

Act 23:11 Ndipo usiku wake Ambuye adayimirira pa iye, nati, khala wokondwa; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.

Act 23:12 Ndipo kutacha, Ayuda adapangana za chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo.

Act 23:13 Ndipo iwo amene adachita chilumbiro ichi adali woposa makumi anayi.

Act 23:14 Ndipo iwo adadza kwa ansembe akulu ndi kwa akulu nati tadzimanga tokha ndi temberero lalikulu kuti sitidzadya kapena kumwa kanthu kufikira titamupha Paulo.

Act 23:15 Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu muzindikiritse kapitawo wamkulu kuti atsike naye kwa inu, mawa monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asadayandikire iye.

Act 23:16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo adamva za chiwembu chawo, ndipo anadza nalowa m’linga, namfotokozera Paulo.

Act 23:17 Ndipo Paulo adadziyitanira Kenturiyo wina, nati, Pita naye m’nyamata uyu kwa kapitawo wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokonzera iye.

Act 23:18 Pamenepo adamtenga, napita naye kwa kapitawo wamkulu, nati, Wamsinga Paulo adandiyitana, nandipempha ndidze naye m’nyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakuyankhula ndi inu.

Act 23:19 Ndipo kapitawo wamkulu adamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m’seri, chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?

Act 23:20 Ndipo adati, Ayuda adapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa ku bwalo la milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.

Act 23:21 Koma musakopedwe nawo: pakuti amlalira iye woposa makumi anayi a iwo amene adadzitemberera wokha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekera tsopano nayang’anira lonjezano lanu.

Act 23:22 Pamenepo kapitawo wamkulu adamuwuza m’nyamatayo apite, namlamulira kuti asawuze munthu ali yense kuti wandizindikiritsa zinthu izi.

Act 23:23 Ndipo adayitana a Kenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira ku Kayisareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ola lachitatu la usiku.

Act 23:24 Ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felike kazembeyo.

Act 23:25 Ndipo adalembera kalata m’malembedwe wotere:

Act 23:26 Klawudiya Lusiya kwa kazembe womveketsa Felike, ndikuyankhulani.

Act 23:27 Munthu uyu adagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndidafikako ine ndi asilikali, ndipo ndidamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.

Act 23:28 Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa cha kuti adamnenera iye, ndidatsikira naye ku bwalo la akulu awo:

Act 23:29 Ndipo ndidapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chawo; koma adalibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena kumangigwa.

Act 23:30 Ndipo m’mene adandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndidamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera amnenere kwa inu.Tsalani bwino.

Act 23:31 Ndipo pamenepo asilikali, monga adawalamulira, adatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri.

Act 23:32 Koma m’mawa mwake adasiya apakavalo amperekeze, nabwera kunyumba ya kulinga:

Act 23:33 Iwowo, m’mene adafika ku Kayisareya, adapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.

Act 23:34 Ndipo m’mene adawerenga adafunsa achokera m’dera liti; ndipo pozindikira kuti adali wa ku Kilikiya;

Act 23:35 Ndidzamva mlandu wake adatero, pamene akukunenera afika. Ndipo adalamulira kuti amdikire iye m’nyumba yoweruzira mlandu ya Herode.



24

Act 24:1 Ndipo atapita masiku asanu adatsika mkulu wa ansembe Hananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo adafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.

Act 24:2 Ndipo pamene adamuyitana, Tertulo adayamba kumnenera ndi kunena, popeza tiri nawo mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muwukonzera mtundu wathu zabwino.

Act 24:3 Tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felike womveka inu.

Act 24:4 Koma kuti ndingawonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu.

Act 24:5 Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woyambitsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mapanduko wa Anazarene:

Act 24:6 Amenenso adayesa kuyipsa kachisi; amene tamgwira ndipo ayenera kuweruzidwa molingana ndi chilamulo chathu.

Act 24:7 Koma kapitawo wamkulu Lusiya adafika kwa ife ndipo ndi chisokonezo chachikulu adamtenga iye m’manja athu.

Act 24:8 Nalamulira womnenera ake kuti adze kwa inu; kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za zinthu izi zonse timnenerazi.

Act 24:9 Ndipo Ayudanso adabvomerezana naye, natsimikiza kuti zinthu izi zidali chomwecho.

Act 24:10 Ndipo pamene kazembe adamkodola kuti anene, Paulo adayankha, podziwa inu kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera:

Act 24:11 Popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri wokha chikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira.

Act 24:12 Ndipo sadandipeza m’kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuwutsa khamu la anthu, kapena m’sunagoge kapena mu mzinda:

Act 24:13 Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano.

Act 24:14 Koma ichi ndibvomera kwa inu kuti monga mwa njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse ziri monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri:

Act 24:15 kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo wokhanso achilandira, kuti kudzakhala kuwuka kwa wolungama ndi wosalungama.

Act 24:16 M’menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.

Act 24:17 Ndipo zitapita zaka zambiri ndidadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka.

Act 24:18 Popeza izi adandipeza woyeretsedwa m’kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; koma padali Ayuda ena a ku Asiya.

Act 24:19 Ndipo kukadakhala bwino atakhala pano pamaso panu ndi kunenera ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.

Act 24:20 Kapena iwo amene ali kunowa anene ngati adapeza chosalungama chirichonse, poyimirira ine pamaso pa bwalo la akulu,

Act 24:21 Koma mawu awa amodzi wokha, amene ndidafuwula poyimilira pakati pawo, kunena za kuwuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.

Act 24:22 Ndipo pamene Felike adamva zinthu izi, pokhala nacho chidziwitso chonse cha Njirayo, iye adawachedwetsa nati, pamene Lusiya kapitawo wamkulu akadzatsika ndidzazindikira momveka za nkhani yanu.

Act 24:23 Ndipo adalamulira Kenturiyo ansunge Paulo, ndipo akhale nawo ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.

Act 24:24 Koma atapita masiku ena, adadza Felike ndi Drusila mkazi wake, ndiye Myuda, nayitana Paulo, ndipo adamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu.

Act 24:25 Ndipo m’mene adamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chirimkudza, Felike adagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikawona nthawi, ndidzakuyitana iwe.

Act 24:26 Adayembekezanso kuti Paulo adzampatsa iye ndalama kuti mwina amasule iye; chifukwa chakenso adamuyitana iye kawiri kawiri, nakamba naye.

Act 24:27 Koma zitapita zaka ziwiri Porkiyo Festo adalowa m’malo a Felike; ndipo Felike pofuna kuti Ayuda amkonde adamsiya Paulo mndende,



25

Act 25:1 Tsopano pamene Festasi adalowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, adakwera kumka ku Yerusalemu kuchokera ku Kayisareya.

Act 25:2 Pamenepo wamkulu wa ansembe ndi wakulu wa Ayuda, adamuuza iye za Paulo ndikumpempha iye,

Act 25:3 Nampempha kukonderedwa kuti amtumize iye adze ku Yerusalemu; iwo atamchitira chifwamba kuti amuphe panjira.

Act 25:4 Koma Festasi adayankha, kuti Paulo asungike ku Kayisareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posachedwa.

Act 25:5 Chifukwa chake, anati kwa iwo kuti, amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo kuti ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo am’nenera iye.

Act 25:6 Ndipo m’mene adatsotsa kwa iwo masiku woposera khumi wokha adatsikira ku Kayisareya; ndipo m’mawa mwake adakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti amtenge Paulo.

Act 25:7 Ndipo m’mene adafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu adayimilira pomzinga iye, nam’nenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sadakhoza kuzitsimikizira.

Act 25:8 Koma Paulo podzikanira adanena, Sindidachimwa kanthu kapena kamchilamulo, kapena kamkachisi, kapena Kayisala.

Act 25:9 Koma Festasi pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, adayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kumka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine komweko kunena za zinthu izi.

Act 25:10 Koma Paulo adati, Ndiri kuyimirira pa mpando wa chiweruziro cha Kayisala, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindiwachitira kanthu koyipa, monga nokha mudziwa bwino.

Act 25:11 Pamenepo ngati ndiri wochita zoyipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zachabe, palibe m’modzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kayisala.

Act 25:12 Pamenepo Festasi atakamba ndi aphungu ake, adayankha, Wanena, nditulukira kwa Kayisala; kwa Kayisala udzapita.

Act 25:13 Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Bernike adafika kuKayisareya, kudzamuyankhula Festasi.

Act 25:14 Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Festasi adafotokozera mfumuyo mlandu wake wa Paulo, nanena, pali munthu adamsiya m’ndende Felike:

Act 25:15 Amene ansembe akulu ndi akulu wa Ayuda adamnenera kwa ine, ndiri ku Yerusalemu, nandipempha kuti ndiyipse mlandu wake.

Act 25:16 Koma ndidawayankha, kuti machitidwe wa Aroma satero, kupereka munthu asadayambe woneneredwayo kupenyana nawo womnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho.

Act 25:17 Potero pamene adasonkhana pano, sindidachedwa, koma m’mawa mwake ndidakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndidalamulira adze naye munthuyo.

Act 25:18 Ndipo pamene adayimirira womneneza, sadamtchulira konse chifukwa cha zoyipa zonga ndizilingilira ine:

Act 25:19 Koma adali nawo mafunso ena wotsutsana naye a chipembedzo cha iwo wokha, ndi mafunso a za wina Yesu, amene adafa, za amene Paulo adati kuti ali ndi moyo.

Act 25:20 Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndidamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za nkhani iyi.

Act 25:21 Koma Paulo pakunena kuti asungidwe, akatulukire kwa Augusto, ndidaweruza kuti asungidwe iye kufikira ndidzamtumiza kwa Kayisala.

Act 25:22 Ndipo Agripa adati kwa Festasi, Ndifuna nanenso ndimve ndekha munthuyo. Adati, Mawa mudzamva iye.

Act 25:23 M’mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Bernike ndi chimwambo chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitawo akulu, ndi amuna womveka a mudziwo, ndipo pakulamulira Festasi, adadza naye Paulo.

Act 25:24 Ndipo Festasi adati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muwona munthu uyu amene unyinji wonse wa Ayuda adandiwuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuwula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo.

Act 25:25 Koma ndidapeza ine kuti sadachita kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha adati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.

Act 25:26 Koma ndiribe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti ndikatha kumfunsafunsa ndikhale nako kanthu kolemba.

Act 25:27 Pakuti chiwoneka kwa ine chopanda nzeru, potumiza wamsinga, posatchulanso zifukwa za mlandu wake.



26

Act 26:1 Ndipo Agripa adati kwa Paulo, kwaloledwa udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, adatambasula dzanja nadzikanira:

Act 26:2 Ndidziyesera wamwayi, mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo:

Act 26:3 Makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.

Act 26:4 Mayendedwe amoyo wanga tsono, kuyambira pa chibwana changa, amene adakhala chiyambire mwa mtundu wanga m’Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse;

Act 26:5 Andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndidakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzo chathu.

Act 26:6 Ndipo tsopano ndiyimilira pano ndiweruzidwe pa chiyembekezo cha lonjezano limene Mulungu adalichita kwa makolo athu:

Act 26:7 Mwalonjezano limene mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, adayembekezera chiyembekezo chimene chikudza, ndipo Chifukwa cha chiyembekezo chimenecho, Mfumu, Agripa, ndi zomwe nditsutsidwa ndi Ayuda.

Act 26:8 Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu awukitsa akufa?

Act 26:9 Indetu, ndi ine ndekha, kuti ndikhala ngati kuti ndichita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu m’nazarayo.

Act 26:10 Chimenenso ndidachita m’Yerusalemu: ndipo ndidatsekera ine woyera mtima ambiri m’ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndidabvomerezapo.

Act 26:11 Ndipo ndidawalanga kawirikawiri m’masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndikuwanzunza ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku mizinda yakunja.

Act 26:12 M’menenso popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe akulu kuli masana.

Act 26:13 Ndidawona panjira, Mfumu, kuwunika kuchokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa,kudawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.

Act 26:14 Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndidamva mawu akunena kwa ine m’chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undinzunziranji Ine? Mkobvuta kwa iwe kumenyana ndi zisonga zakuthwa kwambiri.

Act 26:15 Ndipo ndidati, ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye adati, Ine ndine Yesu amene iwe umnzunza.

Act 26:16 Komatu uka, yimilira pamapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndidawonekera iwe, kukuyika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya zinthu izi zidzakuwonekera iwe;ndi zinthu zina zimene ndidzakuwonetsa iwe.

Act 26:17 Ndi kukulanditsa iwe kwa anthu, ndi kwa a mitundu, amene ndikutuma kwa iwo.

Act 26:18 Kukawatsegulira maso awo, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuwunika, ndi kuchokera ku ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo a kuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.

Act 26:19 Potero, Mfumu Agripa, sindidakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba.

Act 26:20 Komatu kuyambira kwa iwo a m’Damasiko, ndi a m’Yerusalemu, ndi m’dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndidalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.

Act 26:21 Chifukwa cha izi Ayuda adandigwira m’Kachisi, nayesa kundipha.

Act 26:22 Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiyimilira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang’ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzafika:

Act 26:23 Kuti Khristu amve zowawa, kuti Iye, akhale woyamba wa akuwuka kwa akufa, awonetsere kuwunika kwa anthu ndi kwa amitundu.

Act 26:24 Koma pakudzikanira mwiniyekha momwemo, Festasi adati ndi mawu akulu, Uli ndi misala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.

Act 26:25 Koma Paulo adati, Ndiribe misala, Festasi womvekatu; koma nditulutsa mawu achowonadi ndi umunthu weni weni..

Act 26:26 Pakuti mfumuyo idziwa zinthu izi, kwa iye amene ndiyankhula nayenso mosawopa; pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadam’bisikira; pakuti ichi sichidachitika m’seri.

Act 26:27 Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? Ndidziwa mumawakhulupirira.

Act 26:28 Ndipo Agripa adati kwa Paulo, Iwetu uli pafupi kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.

Act 26:29 Ndipo Paulo adati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang’ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero wonga ndiri ine kupatulapo kumangidwaku..

Act 26:30 Ndipo pamene iye adanena izi, mfumu ndi kazembe ndi Bernike, ndi iwo akukhala nawo adanyamuka:

Act 26:31 Ndipo atapita padera adayankhula wina ndi mzake, nanena, Munthu uyu sadachita kanthu koyenera imfa, kapena kumangidwa.

Act 26:32 Pamenepo Agripa adati kwa Festasi, Tikadakhoza kumasula munthuyu, akadapanda kunena, Ndikatulukire kwa Kayisala.



27

Act 27:1 Ndipo pamene padatsimikiza kuti tipite m’chombo kumka ku Italiya, adapereka Paulo ndi andende ena kwa Kenturiyo dzina lake Yuliyo, wa gulu la Augusto.

Act 27:2 Ndipo m’mene tidalowa m’chombo cha ku Adramatiyo chikati chipite kumka ku malo a ku mbali ya Asiya, tidayenda, ndipo Aristarko M’makedoniya wa ku Tesalonika, adali nafe.

Act 27:3 Ndipo m’mawa mwake tidangokocheza ku Sidoni; ndipo Yuliyo adachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze.

Act 27:4 Ndipo pochokanso pamenepo, tidapita kutseri kwa Kupro, popeza mphepo idawomba mokomana nafe.

Act 27:5 Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwake kwa Kilikiya ndi Pamfuliya, tidafika ku Mura mzinda wa Lukiya.

Act 27:6 Ndipo pamenepo Kenturiyo adapezako chombo cha ku Alesandriya, chilikupita ku Italiya, ndipo tidakweramo.

Act 27:7 Ndipo m’mene tidapita pang’onopang’ono masiku ambiri,ndi kufika mobvutika pandunji pa Knido, ndipo popeza siyidatilolanso mphepo, tidapita mtseri mwa Krete, pandunji pa Salimone.

Act 27:8 Ndipo popazapaza mobvutika, tidafika ku malo ena dzina lake Pokocheza Pokoma; pafupi pamenepo padali mzinda wa Laseya.

Act 27:9 Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo udayamba kukhala wowopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo adawachenjeza iwo.

Act 27:10 Nanena kwa iwo, Amuna inu, ndiwona ine kuti ulendo udzatitengera kuwonongeka ndi kutayika kwambiri, sikwa akatundu wokha kapena chombo chokha, komatunso kwa miyoyo yathu.

Act 27:11 Koma Kenturiyo adakhulupirira wa chiwongolero ndi mwini chombo makamaka, wosasamala mawu a Paulo.

Act 27:12 Ndipo popeza dowoko silidakoma kugonapo nyengo yachisanu, unyinji udachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Foyinika, ndi kugonako, ndilo dowoko la ku Krete, loloza kumpoto ndikumwera.

Act 27:13 Ndipo powomba pang’ono mwera, poyesa kuti adachita chifuniro, adakoka nangula, napita m’mbali mwa Krete.

Act 27:14 Koma patapita pang’ono idawombetsa kuchokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Eurokulo.

Act 27:15 Ndipo pogwidwa nacho chombo, chosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tidangotengedwa.

Act 27:16 Ndipo popita kuseri kwa chisumbu chaching’ono dzina lake Kauda, tidali ndi ntchito yambiri kuti tibwere kuchombo koma mobvutika:

Act 27:17 Ndipo m’mene adawukweza, adachita nazo zothandizira, nakulunga chombo; ndipo pakuwopa kuti angatayike pa Surti, adatsitsa. mathanga, natengedwa motero.

Act 27:18 Ndipo mobvutika kwakukulu ndi namondweyo, m’mawa mwake adayamba kutaya akatundu;

Act 27:19 Ndipo tsiku lachitatu adataya ndi manja awo a iwo eni zipangizo za mchombo.

Act 27:20 Ndipo m’mene dzuwa kapena nyenyezi sizidatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng’ono adatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuka chidatichokera pomwepo.

Act 27:21 Ndipo pamene atakhala nthawi yayikulu wosadya kanthu, Paulo adayimilira pakati pawo, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, sitikadadzitengera kuwonongeka ndi kutayika kotereku.

Act 27:22 Koma tsopano ndikuchenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo m’modzi mwa inu, koma chombo ndicho.

Act 27:23 Pakuti adayimilira kwa ine usiku walero m’ngelo wa Mulungu amene ndiri wake, amenenso ndimtumikira.

Act 27:24 Nanena, Usawope Paulo; ukayimilira pamaso pa Kayisala, ndipo tawona, Mulungu adakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi.

Act 27:25 Chifukwa chake, amuna inu, limbikani mtima; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe adanena ndi ine.

Act 27:26 Koma tiyenera kuponyedwa pa chisumbu china chake.

Act 27:27 Koma pofika usiku wakhumi ndi chinayi, potengedwa ife kwina ndi kwina m’nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amalinyero adazindikira kuti adalikuyandikira pafupi ndi dziko lina:

Act 27:28 Ndipo adayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri, ndipo katapita kanthawi , adayesanso napeza mikwamba khumi ndi isanu.

Act 27:29 Ndipo pakuwopa tingatayike pamiyala, adaponya anangula anayi kumakhaliro, nakhumba kuti kuche.

Act 27:30 Ndipo m’mene amalinyero adafuna kuthawa m’chombo, natsitsira bwato m’nyanja, monga ngati adati aponye anangula kulikulu,

Act 27:31 Paulo adati kwa Kenturiyo ndi kwa asilikali, ngati awa sakhala m’chombo inu simukhoza kupulumuka.

Act 27:32 Pamenepo asilikali adadula zingwe za bwato, nalisiya kuti ligwe.

Act 27:33 Ndipo popeza kudalikucha, Paulo adawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinayi limene mudalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu.

Act 27:34 Chomwecho ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; kuti mukhale ndi thanzi: pakuti sadzatayika m’modzi wa inu.

Act 27:35 Ndipo atanena izi, adatenga mkate, nayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m’mene adaunyema adayamba kudya.

Act 27:36 Ndipo adakhala wolimba mtima onse, ndipo sadatenga chakudya china .

Act 27:37 Ndipo ife tonse tiri m’chombo ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi m’modzi.

Act 27:38 Ndipo m’mene adakhuta, adapepuza chombo, nataya tirigu m’nyanja.

Act 27:39 Ndipo kutacha sadazindikira dzikolo; koma adawona pali bondo la m’chenga; kumeneko adafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako chombo.

Act 27:40 Ndipo m’mene adataya anangula adawasiya m’nyanja, namasulanso zingwe zomanga chiwongolero; ndipo pokweza thanga la kumutu, pamenepo analunjikitsa kum’chenga.

Act 27:41 Koma adakwama pamalo pamene padakumana nyanja ziwiri, ndipo chombo chidatsamitsidwapo ndipo kulikulu kwa chombo, kudakhala kosasunthika, koma kumakhaliro kudasweka ndi mphamvu ya mafunde.

Act 27:42 Ndipo uphungu wa asilikali udati awaphe andende, angasambire, ndi kuthawa.

Act 27:43 Koma Kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, adawaletsa angachite cha uphungu wawo; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m’nyanja, nafike pamtunda;

Act 27:44 Ndipo wotsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m’chombo. Ndipo kudatero kuti onse adapulumukira pamtunda.



27

Act 28:1 Ndipo atapulumuka, pamenepo adadziwa kuti chisumbucho chidatchedwa Melita.

Act 28:2 Ndipo akunja adatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti adasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula idalimkugwa, ndi chifukwa cha kuzizira.

Act 28:3 Koma pamene Paulo adawola chisakata cha nkhumi, nachiyika pa moto, idatulukamo njoka, chifukwa cha kutentha, idaluma dzanja lake.

Act 28:4 Koma pamene akunjawo adawona chirombocho chiri lende pa dzanja lake, adanena wina ndi mzake, zowona munthuyu ndiye wambanda, angakhale adapulumuka m’nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.

Act 28:5 Koma adakutumulira chirombocho kumoto, wosamva kupweteka.

Act 28:6 Koma adayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa pansi ndi kufa pomwepo; koma m’mene adalindira nthawitu, nawona kuti sadampweteke, adasintha maganizo awo, nati, iye adali Mulungu.

Act 28:7 Koma pafupi pamenepo padali minda, mwini wake ndiye mkulu wa chisumbucho, dzina lake Popliyo; amene adatilandira ife, natichereza mokoma masiku atatu.

Act 28:8 Ndipo kudatero kuti atate wake wa Popliyo adagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo adalowa, napemphera, nayika manja pa iye, namchiritsa.

Act 28:9 Ndipo patachitika ichi, enanso a m’chisumbu, wokhala nazo nthenda, adadza nachiritsidwa:

Act 28:10 Amenenso adatichitira ulemu wambiri; ndipo pochoka ife adatiyikira zotisowa.

Act 28:11 Ndipo itapita miyezi itatu tidayenda m’chombo cha ku Alesandriya,chidagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chizindikiro chake, chidali kuti, Ana –a – mapasa.

Act 28:12 Ndipo pamene tidakocheza ku Surakusa, tidatsotsako masiku atatu.

Act 28:13 Ndipo pochokapo tidapaza ntifika ku Regiyo; ndipo lidapita tsiku limodzi adayamba mwera, ndipo m’mawa mwake tidafika ku Potiyolo:

Act 28:14 Pamenepo tidakomana ndi abale, amene adatiwumilira tikhale nawo masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tidafika ku Roma.

Act 28:15 Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, adadza kukomana nafe kubwalo la Apiyo, ndi ku nyumba za Alendo zitatu; ndipo pamene Paulo adawawona adayamika Mulungu, nalimbika mtima.

Act 28:16 Ndipo pamene tidafika ku m’Roma, Kertuliyo adapereka amndende kwa woyang’anira wamkulu. Koma Paulo sadaperekedwe koma adakhala pa yekha ndi msilikali womdikira iye

Act 28:17 Ndipo kudali atapita masiku atatu, Paulo,adayitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, adanena nawo, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindidachita kanthu kakuyipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, adandipereka wam’singa kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma.

Act 28:18 Ndipo atandifunsafunsa ine adafuna kundimasula, popeza padalibe chifukwa cha kundiphera.

Act 28:19 Koma pakukanapo Ayuda, ndidafulumidwa mtima kutulukira kwa Kayisala: sikunena kuti ndidali nako kanthu kakunenera mtundu wanga.

Act 28:20 Chifukwa cha ichi tsono ndikupemphani inu mundiwone ndi kuyankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israyeli ndamangidwa ndi unyolo uwu.

Act 28:21 Ndipo adati kwa iye, Ife sitidalandira akalata wonena za inu wochokera ku Yudeya, kapena sadadza kuno wina wa abale ndi kutiwuza kapena kuyankhula kanthu koyipa ka inu.

Act 28:22 Koma tifuna kumva mutiwuze muganiza chiyani; pakuti za gulu la mpatuko uwu, tidziwa kuti awunenera mutsutsana nawo ponseponse.

Act 28:23 Ndipo pamene adampangira tsiku, adadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo adawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m’chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.

Act 28:24 Ndipo ena adakhulupirira zonenedwazo, koma ena sadakhulupirira.

Act 28:25 Koma popeza sadabvomerezana, adachoka atanena Paulo mawu amodzi, kuti, Mzimu Woyera adayankhula kokoma mwa Yesaya M’neneri kwa makolo anu.

Act 28:26 Ndikuti, Pita kwa anthu awa, nuti, Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; ndipo pakupenya mudzapenya, koma wosawona konse;

Act 28:27 Pakuti ndi mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m’makutu mwawo m’molema kumva, ndipo maso awo adawatseka; kuti angawone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse iwo.

Act 28:28 Potero dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzachimva.

Act 28:29 Ndipo pamene adanena mawu awa, Ayuda adachokapo, ndipo adakambirana mwa iwo wokha.

Act 28:30 Ndipo Paulo adakhala zaka ziwiri za mphumphu m’nyumba yake yolipira nalandira onse akufika kwa iye.

Act 28:31 Ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za zinthu zokhudzana ndi Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE