3 John


1

3Jn 1:1 Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m’chowonadi.

3Jn 1:2 Wokondedwa, ndikhumba kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino monga mzimu wako ulemera.

3Jn 1:3 Pakuti ndidakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za chowonadi chako, monga umayenda m’chowonadi.

3Jn 1:4 Ndiribe chimwemwe choposa ichi chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’chowonadi.

3Jn 1:5 Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chiri chonse, uwachitira abale ndi alendo womwe;

3Jn 1:6 Amene adachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wawo koyenera Mulungu, udzachita bwino;

3Jn 1:7 Pakuti chifukwa cha dzinali adatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu.

3Jn 1:8 Chifukwa chake ife tiyenera kulandira wotere, kuti tikakhale wothandizana nacho chowonadi.

3Jn 1:9 Ndalemba kwa Mpingo; komatu Diyotrofe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, sanatilandira ife.

3Jn 1:10 Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mawu woyipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo wofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo.

3Jn 1:11 Wokondedwa, usatsatire chimene chiri choyipa komatu chimene chiri chabwino.

3Jn 1:12 Demetriyo ali ndi mbiri yabwino kwa anthu onse, ndichowonadi chomwe; inde, ndipo ife tichita umboni; ndipo mudziwa kuti umboni wathu uli wowona.

3Jn 1:13 Ndinali nazo zambiri za kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndicholembera cha kapezi.

3Jn 1:14 Koma ndiyembekezera kukuwona iwe msanga, ndipo tidzayankhulana maso ndi maso. Mtendere ukhale ndi iwe, akukupatsa moni abwenzi athu. Undiperekere moni mowatchula mayina awo.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE