2 Timothy


1

2Ti 1:1 Paulo mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa mwa Khristu Yesu.

2Ti 1:2 Kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu.

2Ti 1:3 Ndiyamika Mulungu amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m’mapemphero anga usiku ndi usana;

2Ti 1:4 Kukhumba kwakukulu kofuna kuwona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndikadzadzidwe nacho chimwemwe;

2Ti 1:5 Pamene ndikumbukira chikhulupiriro chako chosafowoka chiri mwa iwe, chimene chidayamba kukhala mwa ambuyako Loisi, ndi mwa mayi wako Yunisi; ndipo ndakopeka mtima, mwa iwenso.

2Ti 1:6 Chifukwa chake, ndikukumbutsa iwe kuti uyitakase mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe ya mwa kuyika kwa manja anga.

2Ti 1:7 Pakuti Mulungu sadatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi woganiza bwino.

2Ti 1:8 Potero usachita manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wa ndende wake; komatu ukhale olandirana nawo masautso a Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;

2Ti 1:9 Amene adatipulumutsa ife, natiyitana ife ndi mayitanidwe woyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu zisadayambe nthawi zosayamba.

2Ti 1:10 Koma chawonetsedwa tsopano mwa kuwonekera kwa Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, amene wagonjetsa imfa, nawonetsera poyera moyo ndi chosabvunda mwa Uthenga Wabwino:

2Ti 1:11 Umene ndayikikapo ine mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wake.

2Ti 1:12 Chifukwa cha ichinso ndimva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndidziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndakopeka kuti lye ndiwokwanitsa kusunga chimene ndadzipereka nacho kwa lye kufikira tsiku lijalo.

2Ti 1:13 Gwira chitsanzo cha mawu omveka bwino, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chiri mwa Khristu Yesu.

2Ti 1:14 Kuti chinthu chabwino chidaperekedwa kwa iwe, uchisunge mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.

2Ti 1:15 Ichi uchidziwa, kuti onse a mu Asiya abwerere kusiyana nane; a iwo ali Fugelo ndi Hermogene.

2Ti 1:16 Ambuye achitire banja la Onesiforo chifundo; pakuti adatsitsimutsa ine kawiri kawiri, ndipo sadachita manyazi ndi unyolo wanga:

2Ti 1:17 Koma pamene ndidali ku Roma ine, iye adandifunafuna ine ndi khama, nandipeza.

2Ti 1:18 Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye mtsiku lijalo: ndi muja danditumikira m’zinthu zambiri mu Aefeso, uzindikira iwe bwino.



2

2Ti 2:1 Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m’chisomo cha mwa Khristu Yesu.

2Ti 2:2 Ndipo zinthu zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uyikize kwa amuna wokhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.

2Ti 2:3 Umve zowawa pamodzi nane monga m’silikali wabwino wa Yesu Khristu.

2Ti 2:4 Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akamkondweretse iye amene adamlemba usilikali.

2Ti 2:5 Koma ngatinso wina ayesana nawo m’makani a masewero, sabvekedwa korona ngati sadayesana monga adapangana.

2Ti 2:6 Wam’munda wogwiritsitsa ntchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo.

2Ti 2:7 Lingilira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziwitso m’zinthu zonse.

2Ti 2:8 Kumbukira kuti Yesu Khistu,wochokera mu mbewu ya Davide, adawukitsidwa kwa akufa monga mwa Uthenga wanga Wabwino.

2Ti 2:9 M’mene ine ndimva mabvuto a zowawa, monga wochita zoyipa; ngakhale mpaka kumangidwa, koma mawu a Mulungu samangidwa.

2Ti 2:10 Mwa ichi ndipilira mzinthu zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutso cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.

2Ti 2:11 Wokhulupirika mawuwa: pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhalanso ndi moyo mwa Iye:

2Ti 2:12 Ngati tipilira tidzachitanso ufumu ndi Iye; ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife.

2Ti 2:13 Ngati tikhala wosakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sakhoza kudzikana yekha.

2Ti 2:14 Uwakumbutse zinthu izi, ndi kuwachitira umboni pa maso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mawu wosapindulitsa kanthu, koma wogwetsa iwo akumva.

2Ti 2:15 Phunzira kuti udziwonetsere wekha kwa Mulungu wobvomerezeka, mwamuna wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wogawa molunjika nawo bwino mawu a chowonadi.

2Ti 2:16 Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzachulukirabe kutsata chisapembedzo.

2Ti 2:17 Ndipo mawu awo adzanyeka chironda; a iwo ali Humenayo ndi Fileto.

2Ti 2:18 Ndiwo amene adasokera kunena za chowonadi, ponena kuti kuwuka kwa akufa kwachitika kale napasula chikhulupiriro cha ena.

2Ti 2:19 Komatu maziko a Mulungu ayimikidwa mokhazikika, wokhala ndi chosindikizira ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo adzipatule kuchoyipa aliyeyense wakutchula dzina la Khristu.

2Ti 2:20 Koma m’nyumba yayikulu simuli zotengera za golide ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndi zina za ulemu, koma zina zopanda ulemu.

2Ti 2:21 Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa zinthu izi, adzakhala chotengera cha ulemu, chopatulika, choyenera kuchigwiritsa ntchito Ambuye, chokonzekeretsedwa kuntchito yonse yabwino.

2Ti 2:22 Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuyitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.

2Ti 2:23 Koma mafunso wopusa ndi wosaphunzirapo kanthu upewe, podziwa kuti abala ndewu.

2Ti 2:24 Ndipo kapolo wa Ambuye asalimbane; koma akhale waulere pa anthu onse wodziwa kuphunzitsa, woleza,

2Ti 2:25 Wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenukiro, kukazindikira chowonadi;

2Ti 2:26 Ndikuti akadzipulumutse ku msampha wa mdierekezi, amene adagwidwa naye, ukapolo kukachita chifuniro chake.



3

2Ti 3:1 Koma zindikira ichi, kuti masiku wotsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.

2Ti 3:2 Pakuti anthu adzakhala wodzikonda wokha, wokonda ndalama, wodzitamandira, wodzikuza, amwano, wosamvera, akuwabala, wosayamika, wosayera mtima

2Ti 3:3 Wopanda chikondi chachibadwidwe, wosayanjanitsika, akudierekeza, wosakhoza kudziletsa, awukali, wosakonda abwino.

2Ti 3:4 Achiwembu, aliwuma, wolimbirira, wotukumuka mtima, wokonda zokondweretsa munthu, wosati wokonda Mulungu;

2Ti 3:5 Akukhala nawo mawonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adayikana; kwa iwonso udzipatule.

2Ti 3:6 Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m’nyumba nagwira akazi wopusa, wosenza akatundu a zoyipa zawo, wotengedwa nazo zilakolako za mitundu mitundu,

2Ti 3:7 Wophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufika ku chizindikiritso cha chowonadi.

2Ti 3:8 Ndipo monga momwe Yane ndi Yambre adatsutsana naye Mose, kotero iwonso adzatsutsana nacho chowonadi: ndiwo anthu wobvunditsitsa mtima, wosatsimikizidwa pachikhulupiriro.

2Ti 3:9 Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwawo kudzawonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.

2Ti 3:10 Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiliro.

2Ti 3:11 Mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga adandichitira mu Antiyokeya, mu Ikoniya, mu Lustro, mazunzo wotere wonga ndawamva; ndipo m’zonsezi Ambuye adandilanditsa.

2Ti 3:12 Ndipo onse akufuna kukhala wopembedza m’moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.

2Ti 3:13 Koma anthu woyipa ndi wonyenga, adzayipa chiyipile, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.

2Ti 3:14 Koma ukhalebe iwe mu zinthu zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa.

2Ti 3:15 Ndi kuti kuyambira umwana wako wadziwa malembo wopatulika, wokhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

2Ti 3:16 Lemba liri lonse adaliwuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo;

2Ti 3:17 Kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito ili yonse yabwino.



3





AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE