2Thessalonians


1

2Th 1:1 Paulo, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu: [2Th 1:2 Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu. [2Th 1:3 Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera, pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mzake mochuluka. [2Th 1:4 Kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m’mipingo ya Mulungu chifukwa cha chipiliro chanu ndi chikhulupiriro chanu, m’mazunzo anu onse ndi zisautsozo zimene mupirira nazo; [2Th 1:5 Ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu, kuti mukawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu umenenso mudamva nawo zowawa; [2Th 1:6 Powona kuti ndicho chilungamo kwa Mulungu kuti abwezere chinzunzo kwa iwo akukuchitirani inu chisautso. [2Th 1:7 Ndi kwa inu amene munzunzidwa pumulani pamodzi ndi ife, ndipo pamene Ambuye Yesu adzabvumbuluka kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu,. [2Th 1:8 M’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osadziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu Khristu. [2Th 1:9 Amene adzalangidwa ndicho chiwonongeko chosatha chochokera ku nkhope ya Ambuye ndi ku ulemerero wa mphamvu yake. [2Th 1:10 Pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake ndi kukhala woyamikiridwa ndi onse wokhulupirira (pakuti mudakhulupirira umboni wathu tidauchita kwa inu) m’tsiku lija. [2Th 1:11 Chomwechonso tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kumayitanidwe awa, ndikukwaniritsa chokoma chonse cha ubwino wake ndi ntchito yachikhulupiriro ndi mphamvu; [2Th 1:12 Kuti dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu. [ [

2

2Th 2:1 Ndipo tikupemphani abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye. [2Th 2:2 Kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mawu, kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika. [2Th 2:3 Munthu asakunyengeni kwina kulikonse, kuti tsikulo silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho nabvumbulutsike munthu wawuchimoyo mwana wa chionongeko. [2Th 2:4 Amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zochedwa Mulungu, kapena zopembezeka, kotero kuti iye monga Mulungu wakhala pansi ku kachisi wa Mulungu nadziwonetsera yekha kuti ali Mulungu. [2Th 2:5 Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani zinthu izi. [2Th 2:6 Ndipo tsopano chomletsa muchidziwa, kuti akabvumbulutsidwe iye m’nyengo yake ya iye yekha. [2Th 2:7 Pakuti chinsinsi cha kusayeruzika chayambadi kuchita, chokhachi pa womletsa tsopano, kufikira a kam’chotsa pamenepo. [2Th 2:8 Ndipo pamene adzabvumbulutsidwa wosayeruzikayo amene Ambuye Yesu adzamuwononga ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuwononga ndi mawonekedwe a kudza kwake. [2Th 2:9 Ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozwizwa zonama, [2Th 2:10 Ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo. [2Th 2:11 Ndipo chifukwa cha ichi Mulungu adzatumiza kwa iwo molimba machitidwe akusocheretsa, kuti akhulupirire bodza, [2Th 2:12 Kuti onse awonongeke amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama. [2Th 2:13 Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi. [2Th 2:14 Kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu. [2Th 2:15 Chifukwa chake tsono, abale, chirimikani, gwiritsitsani miyambo imene tinakuphunzitsani kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu. [2Th 2:16 Tsopano Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyekha, ndi Mulungu amene ndi Atate wathu amene adatikonda ife natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo, [2Th 2:17 Atonthoze mitima yanu nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mawu onse abwino. [ [

3

2Th 3:1 Chotsalira, abale mutipempherere kuti mawu a Ambuye afalikire nalemekezedwe, monganso kwanu, [2Th 3:2 Ndi kuti tilanditsidwe m’manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si anthu onse amene ali ndi chikhulupiriro. [2Th 3:3 Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu nadzakusungani kuletsa woyipayo. [2Th 3:4 Koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani. [2Th 3:5 Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m’chikondi cha Mulungu ndi m’chipiriro poyembekezera Khristu. [2Th 3:6 Tsopano tikulamulirani, abale m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu kuti, musiye kuyenda pamodzi ndi m’bale aliyense woyenda mosalongosoka, wosatsata mwambo umene adaulandira iye kwa ife. [2Th 3:7 Pakuti mudziwa inu nokha momwe muyenera kutitsatira ife: pakuti sitidakhala ife pakati pa inu mosalongosoka; [2Th 3:8 Kapena sitinadya mkate chabe pa dzanja la munthu ali yense komatu ndi chibvuto ndi chipsinjo tidagwira ntchito usiku ndi usana kuti tingalemetse wina wa inu: [2Th 3:9 Si chifukwa kuti tiribe ulamuliro, komatu tidadziyika tokha, tikhale chitsanzo kwa inu, kuti mukatsatire ife. [2Th 3:10 Pakutinso pamene tidali nanu tidakulamulirani ichi kuti, ngati munthu safuna kugwira ntchito asadyenso. [2Th 3:11 Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti akuyenda mosalongosoka osafuna kugwira ntchito konse koma ali ochita mwina ndi mwina. [2Th 3:12 Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo wokha. [2Th 3:13 Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino. [2Th 3:14 Koma ngati wina samvera mawu athu m’kalata uyu, m’dziweni bwino bwino ameneyo. Kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi: [2Th 3:15 Koma musamuyese m’dani, koma mumuyambirire ngati m’bale. [2Th 3:16 Ndipo Ambuye wa mtendere yekha akupatseni inu mtendere nthawi zonse, omwemo Ambuye akhale ndi inu nonse. [2Th 3:17 Moni wa Paulo ndipo ndi dzanja langa mwini, chimene ndi chizindikiro m’kalata aliyense ndiko kulemba kwanga. [2Th 3:18 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE