2 Peter


1

2Pe 1:1 Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m’chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu:

2Pe 1:2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m’chidziwitso cha Mulungu, ndi cha Yesu Ambuye wathu.

2Pe 1:3 Popeza mphamvu ya Umulungu wake idatipatsa ife zinthu zonse za moyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiyitana ife ku ulemerero ndi ukoma.

2Pe 1:4 Mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi ukulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale wogawana nawo Umulungu wake, mudapulumuka ku chibvundi chiri pa dziko lapansi m’chilakolako.

2Pe 1:5 Ndipo mwa ichi, pakutengeraponso changu chonse, muwonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi pa ukoma chizindikiritso.

2Pe 1:6 Ndi pa Chizindikiritso chodziletsa; ndi chodziletsa chipiliro; ndi pachipiliro chipembedzo;

2Pe 1:7 Ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; chikondi, cha pa abale chikondi.

2Pe 1:8 Pakuti ngati zinthu izi zikhala mwa inu, ndipo zikachuluka, zidzapanga kuti musakhale wosabala inu zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Khristu.

2Pe 1:9 Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, ndipo sangathe kuwona patali ndipo wayiwala matsukidwe ake potaya zoyipa zake zakale.

2Pe 1:10 Momwemo abale wonjezani kuchita changu kukhazikitsa mayitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita zinthu izi simudzagwa nthawi zonse:

2Pe 1:11 Chotero polowerera padzakhala matumikiridwe akwa inu, khomo lolowera ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.

2Pe 1:12 Mwa ichi, sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za zinthu izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m’chowonadi chiri ndi inu.

2Pe 1:13 Inde, ndichiyesa chokoma, pokhala ine mu msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;

2Pe 1:14 Podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu adandiwonetsa ine.

2Pe 1:15 Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira zinthu izi.

2Pe 1:16 Pakuti sitidatsata miyambi yachabe, pamene tidakudziwitsani mphamvu ndi mabweredwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tidali mboni zopenya ndi maso ukulu wake.

2Pe 1:17 Pakuti adalandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mawu wotere wochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene mwa Iye ndikondwera naye.

2Pe 1:18 Ndipo mawu awa wochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.

2Pe 1:19 Ndipo tiri nawo mawu a chinenero wokhazikika koposa: amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikawuka nyenyezi yanthanda pa mtima wanu:

2Pe 1:20 Ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha.

2Pe 1:21 Pakuti kale lonse chinenero sichidadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu woyera a Mulungu adayakhulidwa pamene adagwidwa ndi Mzimu Woyera.



2

2Pe 2:1 Koma pakadakhalanso pakati pa anthuwo aneneri wonama, monganso padzakhala aphunzitsi wonama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m’seri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo wokha chitayiko chakudza msanga.

2Pe 2:2 Ndipo ambiri adzatsata njira yawo ya zonyansa; chifukwa cha iwo njira ya chowonadi idzanenedwa za mwano.

2Pe 2:3 Ndipo m’chisiliro adzakuyesani malonda ndi mawu wonyenga; amene chiweruzo chawo sichidachedwa ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chawo sichiwodzera.

2Pe 2:4 Pakuti ngati Mulungu sadalekerera angelo adachimwawo, koma adawaponya kundende nawayika ku mayenje amdima, asungike kufikira chiweruziro;

2Pe 2:5 Ndipo sadalekerera dziko lapansi lakale, koma adasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi amzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko lapansi lawosapembedza chigumula;

2Pe 2:6 Ndipo pakuyisandutsa makala mizinda ya Sodoma ndi Gomora adayitsutsa poyigwetsa, atayiyika chitsanzo cha iwo akukhala wosapembedza;

2Pe 2:7 Ndipo adapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe wonyansa a woyipa aja.

2Pe 2:8 (Pakuti wolungamayo pokhala pakati pawo ndi kuwona ndi kumva zawo, adadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zawo zosayeruzika)

2Pe 2:9 Ambuye adziwa kupulumutsa wopembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga wosalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe:

2Pe 2:10 Koma makamaka iwo akutsata zathupi, m’chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osawopa kanthu, wotsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemu wawo.

2Pe 2:11 Popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano.

2Pe 2:12 Koma iwo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuwonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu wosazidziwa, adzawonongeka m’kuwononga kwawo;

2Pe 2:13 Ndipo adzalandira mphoto ya chosalungama; amene akondwera mkudyerera zowononga ndiwo amawanga ndi zilema, akudyerera m’madyerero anu achinyengo pamene akudyerera nanu;

2Pe 2:14 Wokhala nawo maso wodzala ndi chigololo, wosakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; wokhala nawo mtima wozolowera kusilira; ana a temberero.

2Pe 2:15 Posiya njira yolunjika adasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene adakonda malipiro a chosalungama;

2Pe 2:16 Koma adadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mawu, woyankhula ndi mawu a munthu, adaletsa misala ya m’neneriyo.

2Pe 2:17 Iwo ndiwo akasupe wopanda madzi, mitambo yotengedwa, ndi mphepo yamkuntho amene mdima wakuda bii uwasungikira kosatha.

2Pe 2:18 Pakuti poyankhula mawu wotukumuka wopanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe wolakwawo.

2Pe 2:19 Ndikuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo eni wokha ali atumiki achibvundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wake.

2Pe 2:20 Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akodwanso nazo m`menemo, nagonjetsedwa, zotsiriza zawo zidzayipa koposa zoyambazo.

2Pe 2:21 Pakuti pakadakhala chinthu chabwino kwa iwo akadapanda kudziwa njira ya chilungamo, ndi poyizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.

2Pe 2:22 Chidawayenera iwo cha mwambi wowona, Galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulika m’thope.



3

2Pe 3:1 Wokondedwa, uyu ndiye kalata wachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu wowona ndi kukukumbutsani:

2Pe 3:2 Kuti mukumbukire mawu wonenedwa kale ndi aneneri woyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa ife atumwi anu:

2Pe 3:3 Ndi kuyamba ku chizindikira ichi kuti masiku wotsiriza adzafika wonyoza ndi kuchita zonyoza, woyenda monga mwa zilakolako za iwo eni.

2Pe 3:4 Ndi kunena,liri kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.

2Pe 3:5 Pakuti ichi ayiwala dala, kuti miyamba idakhala kale lomwe, ndi dziko lidawungika ndi madzi ndi mwa madzi, mawu a Mulungu:

2Pe 3:6 Mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka:

2Pe 3:7 Koma miyamba ndi dziko lapansi la masiku ano, ndi mawu womwewo zayikika, zosungikira kumoto kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu wosapembedza.

2Pe 3:8 Koma ichi chimodzi musayiwale, wokondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.

2Pe 3:9 Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

2Pe 3:10 Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala usiku; m’mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi za m’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko lapansi ndi ntchito ziri momwemo zidzatenthedwa.

2Pe 3:11 Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu wotani nanga, m’mayendedwe wopatulika ndi m’chipembedzo.

2Pe 3:12 Akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m’menemo miyamba potentha moto idzakanganuka ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.

2Pe 3:13 Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.

2Pe 3:14 Momwemo, wokondedwa, popeza muyembekezera izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, wopanda banga ndi wopanda chilema.

2Pe 3:15 Ndipo dziwerengereni kuti kupirira kwa Ambuye wathu ndicho chipulumutso; monganso m’bale wathu wokondedwa Paulo kolingana ndi nzeru zopatsidwa kwa iye wakulemberani;

2Pe 3:16 Monganso mu akalata ake onse pokamba momwemo za zinthu izi, m’menemo muli zinthu zina zobvuta kuzizindikira, zimene anthu wosaphunzira ndi wosakhazikika apotoza, monganso atero nawo malembo ena, ndi kudziwononga nawo eni okha.

2Pe 3:17 Inu, tsono, wokondedwa, pozizindikira zinthu izi, chenjerani kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo wosayeruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.

2Pe 3:18 Koma kulani mu chisomo ndi m`chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE