2 John


1

2Jn 1:1 Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikonda m’chowonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira chowonadi;

2Jn 1:2 Chifukwa cha chowonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife kunthawi yosatha.

2Jn 1:3 Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m’chowonadi ndi m’chikondi.

2Jn 1:4 Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena wa ana anu alikuyenda m’chowonadi, monga ndidalandira lamulo lochokera kwa Atate.

2Jn 1:5 Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tidali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mzake.

2Jn 1:6 Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulo monga mudalimva kuyambira pachiyambi kuti mukayende momwemo.

2Jn 1:7 Pakuti wonyenga ambiri adatuluka, kulowa m’dziko lapansi, ndiwo amene sabvomereza kuti Yesu Khristu adadza m’thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.

2Jn 1:8 Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.

2Jn 1:9 Aliyense wochimwa ndi, wosakhala m’chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m’chiphunzitso, iyeyo ali nawo Atate ndi Mwana.

2Jn 1:10 Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamulandire iye kunyumba kwanu, ndipo musamuyankhule.

2Jn 1:11 Pakuti iye wakumuyankhula ayanjana nazo ntchito zake zoyipa.

2Jn 1:12 Pokhala ndiri nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kuyankhula nanu maso ndi maso, kuti chimwemwe chanu chikwaniritsidwe.

2Jn 1:13 Ana a mlongo wanu wosankhika, akupereka moni. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE