2 Corinthians


1

2Co 1:1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu ndi Timoteo m’bale wathu, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi woyera mtima onse amene ali mu Akaya lonse:

2Co 1:2 Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

2Co 1:3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse;

2Co 1:4 Wotitonthoza ife mu msautso yathu yonse , kuti tikathe ife kutonthoza iwo wokhala mu msautso uli yonse, mwa chotonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

2Co 1:5 Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.

2Co 1:6 Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupilira kwa masautso womwewo amene ifenso timva kuti ngati titonthozedwa ndi chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu.

2Co 1:7 Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli woyanjana ndi masautsowo, koteronso chitonthozo.

2Co 1:8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale wosadziwa za chisautso chathu tidakomana nacho mu Asiya, kuti tidathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu:

2Co 1:9 Koma tokha tidakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuwukitsa akufa:

2Co 1:10 Amene adatilanditsa mu imfa yayikulu yotere, nadzatilanditsa ife; Amene timyembekezera kuti adzatilanditsanso;

2Co 1:11 Pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.

2Co 1:12 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m’chiyero ndi kuwona mtima kwa Umulungu, si mu nzeru ya thupi, koma m’chisomo cha Mulungu tidadzisunga m’dziko lapansi, koma koposa kwa inu.

2Co 1:13 Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga kapenanso mubvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti kuzindikira kufikira chimaliziro;

2Co 1:14 Monganso mudatizindikira ife pena, kuti ife ndife chimwemwe chanu, monga momwe inunso muli chimwemwe chathu m’tsiku la Ambuye Yesu.

2Co 1:15 Ndipo m’kulimbika kumene ndidafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nalo phindu lachiwiri;

2Co 1:16 Ndipo popyola kwanu kupita ku Makedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kuchokera ku Makedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.

2Co 1:17 Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndidachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, inde, inde ndi ayi, ayi?

2Co 1:18 Koma monga Mulungu ali wowona, kuti mawu athu kwa inu sakhala inde ndi ayi.

2Co 1:19 Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene adalalikidwa mwa inu ndi ife ine ndi Silivano ndi Timoteo, sadakhala inde ndi ayi, koma adakhala inde mwa Iye.

2Co 1:20 Pakuti monga mwa mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye inde; chifukwa chakenso ali mwa Iye Ameni, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

2Co 1:21 Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu mwa Khristu, natidzodza ife, ndiye Mulungu;

2Co 1:22 Amenenso adatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

2Co 1:23 Komanso ine ndiyitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti ndidalekerera inu kuti ndisafikenso ku Korinto.

2Co 1:24 Sikuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala wothandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muyimadi.



2

2Co 2:1 Koma ndidatsimikiza mtima mwa ine ndekha ndisadzenso kwa inu ndi chisoni.

2Co 2:2 Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndam’mvetsa chisoni?

2Co 2:3 Ndipo ndidalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chimwemwe cha inu nonse.

2Co 2:4 Pakuti m’chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndidalembera inu ndi misozi yambiri; sikuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndiri nacho koposa.

2Co 2:5 Koma ngati wina wachititsa chisoni, sadachititsa chisoni ine, koma pena kuti ndisasenzetse inu nonse.

2Co 2:6 Chilango ichi ndi chokwanira kwa munthu wotere .Chimene chidakhudza ambiri.

2Co 2:7 Kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo angamizidwe ndi chisoni chocholuka.

2Co 2:8 Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.

2Co 2:9 Pakuti chifukwa cha mathero ano ndalemba, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli womvera m’zonse.

2Co 2:10 Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu mu umunthu wa Khristu.

2Co 2:11 Kuti asatichenjerere Satata; pakuti sitikhala wosadziwa machenjerero ake.

2Co 2:12 Kuwonjezera apa ndinadza ku Trowa kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamenepo padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye.

2Co 2:13 Ndidalibe mpumulo mu mzimu wanga; posapeza ine Tito Mbale wanga; koma polawirana nawo ndidamka ku Makedoniya.

2Co 2:14 Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m’chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo lachidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.

2Co 2:15 Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu mwa iwo kupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuwonongeka;

2Co 2:16 Koma kwa ena fungo la imfa ku imfa; ndi kwa ena fungo lamoyo ku moyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

2Co 2:17 Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuwononga mawu a Mulungu; koma monga mwa chowona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tiyankhula mwa Khristu.



3

2Co 3:1 Kodi tirikuyambanso kudzibvomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, akalata wotibvomerezetsa kwa inu, kapena wochokera kwa inu?

2Co 3:2 Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse:

2Co 3:3 Popeza mwawonetsedwa kuti muli kalata wa Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi inki, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome a miyala koma m’magome a mitima yathupi.

2Co 3:4 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Khristu.

2Co 3:5 Sikuti tiri wokwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu.

2Co 3:6 Amenenso adatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo,komala mzimu pakuti chilembo chipha, koma mzimu apatsa moyo.

2Co 3:7 Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m’miyala, udakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sadathe kuyang’anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene udalikuchotsedwa:

2Co 3:8 Nanga utumiki wa Mzimu udzakhala ndi ulemerero wotani?

2Co 3:9 Pakuti ngati utumiki wa chitsutso udali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira mu ulemerero kwambiri.

2Co 3:10 Pakuti chimene chidachitidwa cha ulemerero sichidachitidwa cha ulemerero m’menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo.

2Co 3:11 Pakuti ngati chimene chirikuchotsedwa chidakhala mu ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chiri mu ulemerero.

2Co 3:12 Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tiyankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu;

2Co 3:13 Ndipo si monga Mose, amene adayika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israyeli asayang’anitse pa chimaliziro cha chimene chidalikuchotsedwa:

2Co 3:14 Koma mitima yawo idachititsidwa khungu; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosabvundukuka, chimene chirikuchotsedwa mwa Khristu.

2Co 3:15 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pa mtima pawo.

2Co 3:16 Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, chophimbacho chichotsedwa.

2Co 3:17 Koma Ambuye ndiye Mzimuyo: ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

2Co 3:18 Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirore ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera ku ulemerero kumka ku ulemerero, monga mwa mzimu wa Ambuye .



4

2Co 4:1 Chifukwa chake popeza tiri nawo utumiki umenewu, monga talandira chifundo, sitifowoka;

2Co 4:2 Koma takaniza zobisika za manyazi, wosayendayenda mochenjerera kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga; koma ndi mawonekedwe a chowonadi tidzibvomerezetsa tokha ku chikumbu mtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.

2Co 4:3 Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika;

2Co 4:4 Mwa amene Mulungu wa nthawi yino yapansi pano udachititsa khungu maganizo awo a wosakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.

2Co 4:5 Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Khristu Yesu Ambuye ndi ife tokha atumiki anu, chifukwa cha Yesu.

2Co 4:6 Pakuti Mulungu amene adalamulira kuwala kutuluke mumdima, ndiye amene adawala m’mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope ya Yesu Khristu.

2Co 4:7 Koma tiri nacho chuma ichi m’zotengera za dothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.

2Co 4:8 Ndife wosautsika monsemo, koma wosapsinjika; wosinkhasinkha koma wosakhala kakasi;

2Co 4:9 Wozunzidwa, koma wosatayika; wogwetsedwa, koma wosawonongeka;

2Co 4:10 Nthawi zonse tiri kusenzasenza m’thupi kufa kwake kwa Ambuye Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi mwathu.

2Co 4:11 Pakuti ife amene tiri ndi moyo tiperekeka ku imfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uwoneke m’thupi lathu lakufa.

2Co 4:12 Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu.

2Co 4:13 Koma pokhala nawo mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndidakhulupirira, chifukwa chake ndidayankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tiyankhula;

2Co 4:14 Podziwa kuti Iye amene adawukitsa Ambuye Yesu adzawukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiwonetsa pamodzi ndi inu.

2Co 4:15 Pakuti zinthu zonsezi n`chifukwa cha kwa inu, kuti chisomo, chochulukitsa mwa unyinjiwo, chochulukitsidwa mwakudzera m`mayamiko ambiri akasefukire ku ulemerero wa Mulungu.

2Co 4:16 Chifukwa chake sitifowoka; koma ungakhale umunthu wathu wa kunja ubvunda, munthu wa m’kati mwathu akonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

2Co 4:17 Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;

2Co 4:18 Popeza sitipenyerera zinthu zowoneka, koma zinthu zosawoneka; pakuti zinthu zowoneka ziri za nthawi, koma zinthu zosawoneka ziri zosatha.



5

2Co 5:1 Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu yipasuka, tiri nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha m’Mwamba.

2Co 5:2 Pakuti m’menemo tibuwula, ndi kukhumbitsa kubvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera kumwamba.

2Co 5:3 Ngatitu pobvekedwa sitipezedwa amaliseche.

2Co 5:4 Pakutinso ife wokhala mu msasawu tibuwula pothodwa; sikunena kuti tifuna kubvulidwa, koma kubvekedwa, kuti cha imfacho chimezedwe ndi moyo.

2Co 5:5 Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu amene adatipatsa ife chikole cha Mzimu

2Co 5:6 Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tiri kwathu m’thupi, sitiri kwa Ambuye.

2Co 5:7 (Pakuti tiyendayenda chikhulupiriro si mwa mwamawonekedwe:)

2Co 5:8 Koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m’thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.

2Co 5:9 Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye.

2Co 5:10 Pakuti ife tonse tiyenera kuwonetsedwa ku mpando wa kuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m’thupi; monga momwe adachita, kapena chabwino kapena choyipa.

2Co 5:11 Podziwa tsono kuwopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tiwonetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndikhulupirira kuti tiwonetsedwa m’zikumbu mtima zanu.

2Co 5:12 Sitidzibvomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nawo iwo akudzitamandira powoneka pokha, wosati mumtima.

2Co 5:13 Pakuti ngati tiri woyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tiri anzeru zathu, titero kwa inu.

2Co 5:14 Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti m’modzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;

2Co 5:15 Ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo wokha, koma kwa Iye amene adawafera iwo nawuka.

2Co 5:16 Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi koma tsopano sitimzindikiranso chotero.

2Co 5:17 Chifukwa chake ngati munthu ali yense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, tawonani, zakhala zatsopano.

2Co 5:18 Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene adatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Yesu Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso.

2Co 5:19 Ndiko kunena kuti Mulungu adali mwa Khristu, alimkuyanjanitsa dziko lapansi kwa iye yekha, wosawawerengera zolakwa zawo; ndipo adayikiza kwa ife mawu a chiyanjanitso.

2Co 5:20 Chifukwa chake tiri atumiki m’malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu ali kudandaulira mwa ife; tiwumiriza inu m’malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

2Co 5:21 Ameneyo sadadziwa uchimo adamyesera uchimo m’malo mwathu: kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.



6

2Co 6:1 Ife pamenepo monga antchito pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu.

2Co 6:2 (Pakuti anena, M’nyengo yolandiridwa ndidamva iwe, ndipo m’tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza; tawonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, tawonani, tsopano ndilo tsiku lachipulumutso.)

2Co 6:3 Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chiri chonse, kuti utumikiwo usanenezedwe:

2Co 6:4 Koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu; m’kupilira kwambiri, m’zisautso, m’zikakamizo, m’zopsinja,

2Co 6:5 M’mikwingwirima, m’ndende, m’mapokoso, m’mabvutitso, m’madikiriro, m’masalo a chakudya;

2Co 6:6 M’mayeredwe, m’chidziwitso, m’chilekerero, m’kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m’chikondi chosanyenga,

2Co 6:7 M’Mawu a chowonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa chamuna cha chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,

2Co 6:8 Mwa ulemerero, ndi mwa m’nyozo, mwa mbiri yoyipa ndi mbiri yabwino; monga wosocheretsa, ngakhale ali wowona;

2Co 6:9 Monga wosadziwika, ngakhale adziwika bwino; monga ali kufa, ndipo tawonani tiri ndi moyo; monga wolangika, ndipo wosaphedwa;

2Co 6:10 Monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga a umphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga wokhala wopanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

2Co 6:11 M’kamwa mwathu m’motseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.

2Co 6:12 Simupsinjika mwa ife, koma mupsinjika mumtima mwanu.

2Co 6:13 Ndipo kukhala chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.

2Co 6:14 Musakhale womangidwa m’goli ndi wosakhulupirira wosiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuwunika kuyanjana bwanji ndi m’dima?

2Co 6:15 Ndipo Khristu abvomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

2Co 6:16 Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti inu ndinu kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu adati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndi iwo adzakhala anthu anga.

2Co 6:17 Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudze kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,

2Co 6:18 Ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana amuna ndi akazi, anena Ambuye Wamphamvu yonse.



7

2Co 7:1 Pokhala nawo tsono malonjezano amenewa, wokondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.

2Co 7:2 Tipatseni malo; sitidamchitira munthu chosalungama, sitidayipsa munthu, sitidachenjerera munthu.

2Co 7:3 Sindinena ichi kuti ndikutsutseni; pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.

2Co 7:4 Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m’chisautso chathu chonse.

2Co 7:5 Pakutinso pakudza ife m’Makedoniya thupi lathu lidalibe mpumulo, koma tidasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, mkatimo mantha.

2Co 7:6 Komabe Mulungu amene atonthoza wodzichepetsa, ndiye Mulungu, adatitonthoza ife pa kufika kwake kwa Tito;

2Co 7:7 Koma si ndi kufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene adatonthozedwa nacho mwa inu, pamene adatiwuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, changu chanu cha kwa ine; kotero kuti ndidakondwera koposa.

2Co 7:8 Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata uja, sindilapa; ndingakhale ndidalapa; pakuti ndiwona kuti kalata uja adakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yochepa.

2Co 7:9 Tsopano ndikondwera si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni cha kukulapa; pakuti mwamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m’kanthu kali konse.

2Co 7:10 Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuziramtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni, koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.

2Co 7:11 Pakuti, tawonani, ichi chomwe chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, inde chodzikonza, inde mkwiyo, inde mantha, inde kukhumbitsa inde changu, inde kubwezera chilango! M’zonse mudatsimikizira nokha kuti muli woyera mtima m’menemo.

2Co 7:12 Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindidachita chifukwa cha iye amene adachita choyipa, kapena chifukwa cha iye amene adachitidwa choyipa, koma kuti khama lanu la kwa ife liwonetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.

2Co 7:13 Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m’chitonthozo chanu,inde tidakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake udatsitsimutsidwa ndi inu nonse.

2Co 7:14 Pakuti ngati ndazitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindidamvetsedwa manyazi; koma monga tidayankhula zonse ndi inu m’chowonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene ndidapanga pamaso pa Tito, kudakhala chowonadi.

2Co 7:15 Ndipo chikondi chenicheni chake chichulukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti mudamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.

2Co 7:16 Ndikondwera kuti mzinthu zonse ndilimbika mtima za inu.



8

2Co 8:1 Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwa Mipingo ya ku Makedoniya;

2Co 8:2 Kuti m’chitsimikizo chachikulu cha chisawutso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chawo, ndi kusawuka kwawo kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuwolowa mtima wawo.

2Co 8:3 Pakuti monga mwa mphamvu yawo, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yawo;

2Co 8:4 Adachita eni ake natiwumiriza ndi kutidandawulira za mphatsozo, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa woyera mtima.

2Co 8:5 Ndipo izi adachita, si monga tidayembekeza; koma adayamba kudzipereka wokha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.

2Co 8:6 Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga adayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.

2Co 8:7 Koma monga muchulukira m’zonse m’chikhulupiriro ndi m’mawu, ndi m’chidziwitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m’chisomo ichi.

2Co 8:8 Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena chowonadi cha chikondi chanunso.

2Co 8:9 Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu kuti, chifukwa cha inu adakhala wosawuka, angakhale adali wachuma, kuti inu ndi kusawuka kwake mukakhale wachuma.

2Co 8:10 Ndipo m’menemo ndipereka malangizo anga : pakuti chimene chipindulira inu, amene mudayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.

2Co 8:11 Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kudali chibvomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m’chimene muli nacho.

2Co 8:12 Pakuti ngati chibvomerezocho chiri pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.

2Co 8:13 Pakuti sinditero kuti anthu ena akamasuke, ndi inu mulemetsedwe.

2Co 8:14 Koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwawo nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwawo kukwanire kusowa kwanu: kuti pakhale chilingano:

2Co 8:15 Monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichidamtsalira; ndi iye wosonkhetsa pang’ono sichidamsowa.

2Co 8:16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.

2Co 8:17 Pakutitu adalandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, adatulukira kumka kwa inu mwini wake.

2Co 8:18 Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake mu Uthenga Wabwino kuli m’Mipingo yonse;

2Co 8:19 Ndipo si ichi chokha, komanso adasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m’chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuwonetsa chibvomerezo chathu;

2Co 8:20 Ndi kupewa ichi kuti munthu asatidandaule za kuchulukira kumene tikutumikira.

2Co 8:21 Pakuti tikonzeretu zinthu zokoma, si pa maso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

2Co 8:22 Ndipo tidatumiza mbale wathu awaperekeze iwo amene tamtsimikizira kawiri kawiri ali wakhama m’zinthu zambiri; koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ndiri nako kwa inu.

2Co 8:23 Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali aumiki a Mipingo, ndi ulemerero wa Khristu.

2Co 8:24 Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.



9

2Co 9:1 Pakuti za utumiki wa kwa woyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;

2Co 9:2 Pakuti ndidziwa chibvomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amakedoniya, kuti Akaya adakonzekeratu chitapita chaka ndi changu chanu chidautsa wochulukawo.

2Co 9:3 Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m’menemo; kuti monga ndidanena, mukakhale wokonzeratu:

2Co 9:4 Kuti kapena akandiperekeze aku Makedoniya nadzakupezani inu wosakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m’kulimbika kumeneku.

2Co 9:5 Chifukwa chake tidayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati m’dalitso, ndipo si monga mwa kuwumiriza.

2Co 9:6 Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mowuma manja, mowuma manjanso adzatula. Ndipo iye wakufesa mowolowa manja, mowolowa manjanso adzatula.

2Co 9:7 Munthu aliyense achite monga adatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza: pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

2Co 9:8 Ndipo Mulungu akonza kuchulukitsa chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m’zinthu zonse, mukachulukire ku ntchito yonse yabwino;

2Co 9:9 (Monga kwalembedwa; Anabalalitsa, adapatsa kwa wosawuka: chilungamo chake chikhala ku nthawi yonse.

2Co 9:10 Ndipo iye wopatsa mbewu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbewu yanu yofesa, nadzawonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu:)

2Co 9:11 Polemeretsedwa inu m’zonse ku kuwolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.

2Co 9:12 Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za woyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri.

2Co 9:13 Popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chibvomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuwolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;

2Co 9:14 Ndipo iwo, mwa pempherero lawo la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu.

2Co 9:15 Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yosatheka kuneneka.



10

2Co 10:1 Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu:

2Co 10:2 Koma ndipempha ine kuti pokhala ndiri pomwepo ndisalimbike mtima ndi kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tirikuyendayenda monga mwa thupi.

2Co 10:3 Pakuti pakuyendayenda m’thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi.

2Co 10:4 (Pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi; koma zamphamvu mwa Mulungu za kupasula malinga;)

2Co 10:5 Ndikugwetsa malingaliro, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera Khristu;

2Co 10:6 Ndikukhala wokonzeka kubwezera chilango kusamvera konse kudzakwaniridwa.

2Co 10:7 Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati munthu wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, muloleni iye mwa iye yekha aganizirenso ichi, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife tiri a Khristu.

2Co 10:8 Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene adatipatsa Ambuye ku kumangilira, ndipo si ku kugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa:

2Co 10:9 Kuti ndisawoneke monga ngati kukuwopsani mwa akalatawo.

2Co 10:10 Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo wolemera, ndi amphamvu; koma mawonekedwe athupi lake ngofowoka, ndi mawu ake ngachabe.

2Co 10:11 Wotereyo ayese ichi kuti monga tiri ife ndi mawu mwa akalata, pokhala palibe ife, tiri woterenso m’machitidwe pokhala tiri pomwepo.

2Co 10:12 Pakuti sitilimba mtima kudziwerengera, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzibvomerezetsa wokha; koma iwowa, podziyesera wokha mwa iwo wokha, ndi kudzifananitsa iwo wokha pakati pa iwo wokha ndipo sazindikira.

2Co 10:13 Koma ife sitidzazitamandira popitilira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu adatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.

2Co 10:14 Pakuti sititambalitsiradi moposa muyeso tokha, monga ngati sitidafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mwa kulalikira Uthenga Wabwino wa Khristu:

2Co 10:15 Wosadzitamandira popitilira muyeso mwa machititso wa ena; koma tiri nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira,

2Co 10:16 Kukalalikira Uthenga Wabwino kupyola m’mayiko a mtsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale.

2Co 10:17 Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye.

2Co 10:18 Pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wobvomerezeka.



11

2Co 11:1 Mwenzi kwa Mulungu mutandilola pang’ono ndi chopusacho; komanso mundilole.

2Co 11:2 Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Umulungu; pakuti ndidakupalitsani ubwenzi kwa mwamuna m’modzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.

2Co 11:3 Koma ndiwopa, kuti pena, monga njoka idanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angayipsidwe kusiyana nako kuwona mtima ndi kuyera mtima ziri mwa Khristu.

2Co 11:4 Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitidalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simudalandira, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simudalandira, mulolana naye bwino lomwe.

2Co 11:5 Pakuti ndiyesa kuti sindidaperewera konse ndi atumwi woposatu.

2Co 11:6 Ndipo ndingakhale ndiri wosadziwa manenedwe abwino, koma sinditero m’chidziwitso, koma mzinthu zonse taziwonetsa bwino pakati panu

2Co 11:7 Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndidalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwa ufulu?

2Co 11:8 Ndidalanda za Mipingo yina, ndikulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu.

2Co 11:9 Ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindidalemetse munthu ali yense; pakuti chimenechidandisowa kwa ine abale akuchokera ku Makedoniya, adakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo mzinthu zonse ndidachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.

2Co 11:10 Pakuti chowonadi cha Khristu chiri mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya.

2Co 11:11 Chifukwa chiyani? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.

2Co 11:12 Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m’mene adzitamandiramo, apezedwe monga ife.

2Co 11:13 Pakuti wotere ali atumwi wonyenga, wochita mochenjerera, wodziwonetsa ngati atumwi a Khristu.

2Co 11:14 Ndipo kulibe kudabwa; pakuti satana yemwe adziwonetsa ngati m’ngelo wa kuwunika.

2Co 11:15 Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumwi ake adziwonetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo.

2Co 11:16 Ndinenanso, munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang’ono.

2Co 11:17 Chimene ndiyankhula sindiyankhula monga mwa Ambuye koma monga wopanda nzeru, m’kulimbika kumene kwa kudzitamandira.

2Co 11:18 Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.

2Co 11:19 Pakuti mulolana nawo wopanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru nokha.

2Co 11:20 Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu,ngati wina adzikweza yekha, ngati wina akupandani pankhope.

2Co 11:21 Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tidakhala wofowoka, koma m’mene wina alimbika mtimamo, (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.

2Co 11:22 Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali a Israyeli? Inenso. Kodi ali mbewu ya Abrahamu? Inenso.

2Co 11:23 Kodi ali atumiki a Khristu? (ndiyankhula monga moyaluka), makamaka ine; m’zibvutitso mochulukira, m’ndende mochulukira, m’mikwingwirima mosawerengeka, mu imfa kawiri kawiri.

2Co 11:24 Kwa Ayuda ndidalandira kasanu mikwingwirima makumi anayi kuperewera umodzi.

2Co 11:25 Katatu ndidamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndidaponyedwa miyala, katatu ndidatayika posweka chombo, ndidakhala m’kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;

2Co 11:26 M’maulendo kawiri kawiri, mowopsa mmadzi,mowopsa mwake mwa wolanda, mowopsa modzera kwa mtundu wanga, mowopsa modzera kwa amitundu, mowopsa mumzinda,mowopsa mchipululu, mowopsa m’nyanja, mowopsa mwa abale wonyenga;

2Co 11:27 Mzolemetsa ndi mzowawa, m’madikiro kawirikawiri, m’njala ndi ludzu, m’masalo a chakudya kawiri kawiri, mkuzizidwa ndi umaliseche.

2Co 11:28 Popanda zakunjazo chimene chimadza kwa ine chondisindikiza tsiku ndi tsiku chilabadiro cha Mipingo yonse.

2Co 11:29 Afoka ndani wosafowoka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?

2Co 11:30 Ngati ndiyenera kudzitamandira ndidzazitamandira mu zinthu zokhudzana ndi kufowoka kwanga.

2Co 11:31 Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathuYesu Khristu, Iye amene alemekezeka ku nthawi yonse, adziwa kuti sindinama.

2Co 11:32 M’damasiko kazembe wa mfumu Areta adalindizitsa mudzi wa Adamasiko kuti andigwire ine;

2Co 11:33 Ndipo mwazenera, mumtanga, adanditsitsa pakhoma, ndipo ndidapulumuka m’manja mwake.



12

2Co 12:1 Ndiyenera kudzitamandira kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumansomphenya ndi mabvumbulutso a Ambuye.

2Co 12:2 Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m’thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kumka naye Kumwamba kwachitatu.

2Co 12:3 Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m’thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu:)

2Co 12:4 Kuti anakwatulidwa kumka ku paradiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.

2Co 12:5 Chifukwa cha wotereyo ndidzadzitamandira; koma chifukwa cha ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m’zofoka zanga.

2Co 12:6 Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru, pakuti ndidzanena choonadi, koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.

2Co 12:7 Ndipo kuti ndingakwezeke koposa mwa mabvumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa

2Co 12:8 Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine.

2Co 12:9 Ndipo ananena kwa ine, chisomo changa chikukwanira pakuti mphamvu yanga ikonzedwa m’ufoka chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondwera m’maufoko anga kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

2Co 12:10 Chifukwa chake ndisangalala m’mmaufoko, m’ziwawa, m’zikakamizo, m’manzunzo, m’zipsinjo, chifukwa cha Khristu, pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndiri wa mphamvu.

2Co 12:11 Ndakhala wopusa mwakuzitamandira; pakuti inu mwandikakamiza; Pakuti muyenera kundibvomereza ine; pakuti sindiperewera ndi atumwi oposatu m’kanthu konse ndingakhale ndiri chabe.

2Co 12:12 Indetu zizindikiro za mtumwi zinachitika pakati pa inu m’chipiriro chonse; ndi zizindikiro ndi zozizwa, machitidwe amphamvu.

2Co 12:13 Pakuti kuli chiani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala yina; ngati si ichi kuti ine ndekha sindidakulemetsani inu? Ndikhululukireni pa choipa ichi.

2Co 12:14 Taonani nthawi yachitatu iyi ndakonzeka ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakulemetsani pakuti sindifuna za inu koma inu: pakuti ana sayenera kuwunjikira makolo, koma makolo kuwunjikira ana.

2Co 12:15 Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngakhale ndikonda inu kwambiri koma ine ndidzakondedwa pang`ono.

2Co 12:16 Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wochenjera ine, ndinakugwirani ndi chinyengo.

2Co 12:17 Ndinapindula kwa inu mwa wina aliyense amene ndidamtuma kwa inu.

2Co 12:18 Ndidakhumba Tito ndipo pamodzi ndi iye ndidatumiza m`mbale. Kodi Tito adakuchenjererani. Sitidayendayenda naye mzimu yemweyo kodi? Kodi sitidayenda m`mapazi womwewo.

2Co 12:19 Mumayesa tsopanolino kuti tirikuwiringula kwa inu. Tiyankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Tiyankhula pamso pa Mulungu mwa Khristu, Koma tichita zinthu zonse okondedwa chifukwa chakumangirira kwanu.

2Co 12:20 Pakuti ndi zaopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuma; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikudza, mapokoso;

2Co 12:21 Kuti pakudzanso ine Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalilire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chiwerewere, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.



13

2Co 13:1 Nthawi yachitatu iyi ndiri nkudza kwa inu mkamwa mwa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.

2Co 13:2 Ndinanena kale, ndipo ndidanena ndisanafikeko, monga pamene ndidali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe ndidalembera, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti ngati ndidzanso sindidzawaleka;

2Co 13:3 Popeza mufuna chitsimikizo cha Khristu, wakuyankhula mwa ine; amene safoka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;

2Co 13:4 Pakuti ngakhale Iye adapachikidwa m’ufoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tiri ofoka mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.

2Co 13:5 Dziyeseni nokha ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizireni nokha kapena simudazindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu, mukhala opanda kudzitsimikizira.?

2Co 13:6 Koma ndiyembekeza kuti mudzazindikira kuti sitiri osatsimikizidwa.

2Co 13:7 Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koyipa; sikuti ife tikaoneke obvomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.

2Co 13:8 Pakuti sitikhoza kuchita kanthu pokana choonadi, koma kwa chowonadi.

2Co 13:9 Pakuti tikondwera pamene ife tifoka ndi inu muli amphamvu; ndi ichinso tikhumba, ndicho ungwiro wanu.

2Co 13:10 Chifukwa cha ichi ndakulembera zinthu izi pokhala palibe, Kuti pokhala ndiri pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye adandipatsa ine, wakumangilira, ndipo siwakuwononga.

2Co 13:11 Chotsalira, abale, tsalani bwino. Khalani angwiro, mutonthozedwe; khalani amtima umodzi khalani mumtendere; ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.

2Co 13:12 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsompsono chopatulika.

2Co 13:13 Oyera mtima onse akupatsani moni inu.

2Co 13:14 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE