1 Timothy


1

1Ti 1:1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamulo cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, chiyembekezo chathu:

1Ti 1:2 Kwa Timoteo mwana wanga weniweni m’chikhulupiriro: chisomo, chifundo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

1Ti 1:3 Monga ndidakulamulira iwe kuti ukhalebe ku Aefeso, popita ine ku Makedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse chiphunzitso china.

1Ti 1:4 Kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, amene atumikira mafunso, koposatu kumangirira kwa Umulungu kumene kuli m’chikhulupiriro:

1Ti 1:5 Tsopano chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi, chochokera mu mtima woyera ndi m’chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga:

1Ti 1:6 Zimenezo, ena pozilambalala adapatukira kutsata mawu wopanda pake:

1Ti 1:7 Pofuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena kapena azilimbikirazi.

1Ti 1:8 Koma tidziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu achita nalo monga mwa lamulo;

1Ti 1:9 Koma podziwa ichi, kuti lamulo siliyikika kwa munthu wolungama, koma kwa osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi am’nyozo, akupha atate ndi akupha amayi, akupha amzawo.

1Ti 1:10 Achigololo, akuchita zoyipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, wolumbira zonama, ndipo ngati kuli kanthu kena kamene ndikosemphana ndi chiphunzitso cholamitsa;

1Ti 1:11 Monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene udaperekedwa mkukhulupirika kwanga.

1Ti 1:12 Ndiyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu Ambuye wathu, kuti adandiyesa wokhulupirika, nandiyika kuutumiki;

1Ti 1:13 Amene kale ndidali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu adandichitira chifundo, popeza ndidazichita wosazindikira, wosakhulupirira.

1Ti 1:14 Koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chiri mwa Khristu Yesu.

1Ti 1:15 Mawuwa ali wokhulupirika ndi woyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa wochimwa wa iwowa ine ndine woposa.

1Ti 1:16 Komatu mwa ichi adandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akawonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m’tsogolo kufikira moyo wosatha.

1Ti 1:17 Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosabvunda, yosawoneka, Mulungu wa nzeru yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.

1Ti 1:18 Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino.

1Ti 1:19 Ndikukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chawo chidatayika:

1Ti 1:20 A iwo amene ali Humenayo ndi Alesandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusayankhula zamwano.



2

1Ti 2:1 Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;

1Ti 2:2 Chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikakhale wodekha mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekezeka monsemo.

1Ti 2:3 Pakuti ichi n’chokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;

1Ti 2:4 Amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.

1Ti 2:5 Pakuti pali Mulungu m’modzi ndi Mtetezi m’modzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu;

1Ti 2:6 Amene adadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse; kuti akachitidwe umboni m’nyengo zake.

1Ti 2:7 Umene adandiyika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zowona mwa Khristu, wosanama ine;) mphunzitsi wa a mitundu m’chikhulupiriro ndi chowonadi.

1Ti 2:8 Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja woyera, wopanda mkwiyo ndi makani:

1Ti 2:9 Momwemonso, akazi adzibveke wokha ndi chobvala choyenera, ndi manyazi, ndi chiletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;

1Ti 2:10 Komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu) mwa ntchito zabwino.

1Ti 2:11 Mkazi aphunzire akhale wachete m’kumvera konse.

1Ti 2:12 Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.

1Ti 2:13 Pakuti Adamu adayamba kulengedwa, pamenepo Heva.

1Ti 2:14 Pakuti Adamu sadanyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa adalowa m’kulakwa.

1Ti 2:15 Koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.



3

1Ti 3:1 Mawuwa ali wokhulupirika, ngati mwamuna akhumba udindo wa woyang’anira, ayifuna ntchito yabwino.

1Ti 3:2 Ndipo kuyenera woyang’anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi m’modzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

1Ti 3:3 Wosati woledzera, kapena womenyana ndewu; komatu wofatsa, wopanda ndewu, wosakhumba chuma;

1Ti 3:4 Woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nawo ana ake womvera iye ndi kulemekeza konse;

1Ti 3:5 (Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba yake ya iye yekha, adzasamalira bwanji Mpingo wa Mulungu?)

1Ti 3:6 Asakhale amene watembenuka mtima kumene, kuti podzitukumula ndi kunyada, ngagwe ndi kutsutsa kwa mdierekezi.

1Ti 3:7 Kuyeneranso kuti iwo a kunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.

1Ti 3:8 Momwemonso atumiki akhale wolemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati achisiliro chonyansa;

1Ti 3:9 Wokhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m’chikumbumtima chowona.

1Ti 3:10 Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala wopanda chifukwa.

1Ti 3:11 Momwemo akazi awonso akhale wolemekezeka, wosadierekeza, wodzisunga, wokhulupirika m’zonse.

1Ti 3:12 Atumiki akhale mwamuna wa mkazi m’modzi woweruza bwino ana awo, ndi iwo a m’nyumba yawo ya iwo wokha.

1Ti 3:13 Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera wokha mbiri yabwino ndi kulimbika kwakukulu m’chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

1Ti 3:14 Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa,

1Ti 3:15 Koma ngati ndichedwa kuti udziwe momwe: uyenera kukhalira m’nyumba ya Mulungu, umene uli Mpingo wa Mulungu wamoyo, m’zati ndi maziko a m’chilikizo wa chowonadi.

1Ti 3:16 Ndipo pobvomereza chinsinsi chakuchitira Umulungu ulemu n’chachikulu: Mulungu amene adawonekera m’thupi, adayesedwa wolungama mumzimu, adapenyeka ndi angelo, adalalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m’dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.



4

1Ti 4:1 Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda;

1Ti 4:2 M’mawonekedwe wonyenga a iwo onena mabodza, wosindikizidwa m’chikumbumtima mwawo monga ndi chitsulo chamoto;

1Ti 4:3 Akuletsa ukwati; wosiyitsa zakudya zina, zimene Mulungu adazilenga kuti achikhulupiriro ndi wozindikira chowonadi azilandire ndi chiyamiko.

1Ti 4:4 Pakuti cholengedwa chiri chonse cha Mulungu n’chabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kukanidwa ngati kalandiridwa ndi chiyamiko:

1Ti 4:5 Pakuti kayeretsedwa ndi Mawu a Mulungu ndi pemphero:

1Ti 4:6 Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Yesu Khristu, woleledwa bwino m’mawu achikhulupiriro, ndi chiphunzitso chabwino chimene iwe wachitsata.

1Ti 4:7 Koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba uzikane. Ndipo udzizolowetse kuchita chipembedzo.

1Ti 4:8 Pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la moyo uno, ndi la moyo uli mkudza.

1Ti 4:9 Wokhulupirika mawuwa ndi woyenera kulandiridwa ndi onse.

1Ti 4:10 Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tiri nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa wokhulupirira.

1Ti 4:11 Lamulira izi, nuziphunzitse.

1Ti 4:12 Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo wokhulupirira, m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, mu mzimu, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.

1Ti 4:13 Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga kuchenjeza, ndi kuphunzitsa.

1Ti 4:14 Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuyika kwa manja a akulu.

1Ti 4:15 Uzilingalire zinthu izi; mu izi ukhale; kuti phindu lako liwonekere kwa onse.

1Ti 4:16 Udziyang’anire iwemwini ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.



5

1Ti 5:1 Wamkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;

1Ti 5:2 Akazi akulu ngati amayi; akazi ang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.

1Ti 5:3 Chitira ulemu amasiye amene ali a masiye ndithu.

1Ti 5:4 Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi n’cholandirika pamaso pa Mulungu.

1Ti 5:5 Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m’mapembedzero usiku ndi usana.

1Ti 5:6 Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo.

1Ti 5:7 Ndipo zinthu izi ulamulire kuti akhale iwo wopanda chilema.

1Ti 5:8 Koma ngati wina sadziwa kugawira mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo akhala woyipa kuposa wosakhulupirira.

1Ti 5:9 Asawerengedwe wamasiye ngati sadafike zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wamwamuna m’modzi.

1Ti 5:10 Wambiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsapo mapazi wa woyera mtima, ngati adathandizapo wosautsidwa , ngati adatsatadi ntchito zonse zabwino.

1Ti 5:11 Koma amasiye ang’ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa;

1Ti 5:12 Pokhala nacho chitsutso, popeza adataya chikhulupiriro chawo choyamba.

1Ti 5:13 Ndipo aphunziranso kuchita ulesi, aderuderu; koma wosati ulesi wokha, komatunso ayankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, woyankhula zosayenera.

1Ti 5:14 Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye a ang’ono, nabale ana, nawatsogolere mnyumba, osapatsa chifukwa kwa m’daniyo chakulalatira.

1Ti 5:15 Pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.

1Ti 5:16 Ngati pali mwamuna kapena mkazi ali nawo amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.

1Ti 5:17 Akulu akuweruza bwino awerengedwe woyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.

1Ti 5:18 Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng’ombe yophuntha tirigu. Ndipo wogwira ntchito ayenera kulandira malipiro ake.

1Ti 5:19 Pamkulu usalandire chom’nenezera koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.

1Ti 5:20 Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti wotsalawo ena achite mantha.

1Ti 5:21 Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Ambuye Yesu Khristu, ndi angelo wosankhidwa, kuti usunge zinthu izi kopanda kusiyanitsa, wosachita kanthu monga mwa tsankhu.

1Ti 5:22 Usafulumira kuyika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoyipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.

1Ti 5:23 Usakhalenso wakumwa madzi wokha, koma ugwiritse ntchito vinyo pang’ono, chifukwa cha m’mimba mwako ndi zofowoka zako zobwera kawiri kawiri.

1Ti 5:24 Zochimwa za anthu ena ziri zowoneka kale, zitsogola kumka kumlandu; koma enanso ziwatsata.

1Ti 5:25 Momwemonso pali ntchito zabwino zidawonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizikhoza kubisika.



6

1Ti 6:1 Onse amene ali akapolo am’goli, ayesere ambuye a iwo wokha woyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano.

1Ti 6:2 Ndipo iwo akukhala nawo ambuye akukhulupira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali wokhulupira ndi wokondedwa, ndi woyanjana nawo pa chokomacho. Izi uziphunzitse, nuchenjeze.

1Ti 6:3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosabvomerezana nawo mawu a moyo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitso chiri monga mwa chipembedzo;

1Ti 6:4 Iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mawu, kumene zichokerako njiru, ndewu, zamwano, mayerekezo woyipa,

1Ti 6:5 Makani wopanda pake a anthu woyipsika nzeru ndi wochotseka chowonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa: kwa iwo udzipatule.

1Ti 6:6 Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu.

1Ti 6:7 Pakuti sitidatenga kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano.

1Ti 6:8 Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.

1Ti 6:9 Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi mu msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko.

1Ti 6:10 Pakuti muzu wa zoyipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, adasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.

1Ti 6:11 Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu izi: nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiliro, chifatso.

1Ti 6:12 Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuyitanira, ndipo wabvomereza chibvomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

1Ti 6:13 Ndikulamulira pa maso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene adachitira umboni chibvomerezo chabwino kwa Pontiyo Pilato;

1Ti 6:14 Kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira mawonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu.

1Ti 6:15 Limene adzaliwonetsa m’nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye;

1Ti 6:16 Amene Iye yekha ali nawo moyo wosatha, wakukhala m’kuwunika kosakhoza kufikako; amene munthu sadamuwona, kapena sadakhoza kumuwona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Ameni.

1Ti 6:17 Lamulira iwo a chuma m’nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, komatu Mulungu, amene atipatsa ife chuma cha zinthu zonse kochuluka, kuti tikondwere nazo;

1Ti 6:18 Kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakonzekere kugawira ena, ndikuyanjana;

1Ti 6:19 Ndikudziyikira wokha maziko abwino kunyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo wosatha.

1Ti 6:20 Timoteo iwe; sunga, chimene chayikizidwa kuchikhulupiriro chako, nupewe zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama:

1Ti 6:21 Chimene ena pochibvomereza, adalakwa m’chikhulupiriro. Chisomo chikhale nanu. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE