1 Thessalonians


1

1Th 1:1 Paulo, Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu: chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

1Th 1:2 Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kukumbukira inu m’mapemphero athu;

1Th 1:3 Ndikukumbukira kosalezeka ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu ndi Atate wathu;

1Th 1:4 Podziwa, abale wokondedwa chisankhidwe chanu cha kwa Mulungu.

1Th 1:5 Pakuti Uthenga Wabwino wathu sudadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’zitsimikizo zazikulu; monga mudziwa tidakhala wonga wotani mwa inu chifukwa cha inu.

1Th 1:6 Ndipo mudayamba kukhala akutsanza athu, ndi wa Ambuye, m’mene mudalandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera:

1Th 1:7 Kotero kuti mudayamba kukhala inu chitsanzo kwa onse akukhulupirira m’Makedoniya ndi m’Akaya.

1Th 1:8 Pakuti kuchokera kwa inu kudamveka mawu wa Ambuye, osati m’Makedoniya ndi Akaya mokha, komatu m’malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidafalikira; kotero kuti sikufunika kwa ife kuyankhula kanthu.

1Th 1:9 Pakuti iwo wokha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu adali wotani; ndi momwe mudatembenukira kwa Mulungu posiyana nawo mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo;

1Th 1:10 Ndikulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene adamuukitsa kwa akufa, ndiye Yesu wotipulumutsa ife ku mkwiyo ulimkudza.



2

1Th 2:1 Pakuti abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sadakhala wopanda pake;

1Th 2:2 Koma ngakhale tidamva zowawa kale, ndipo adatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Afilipi, tidalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kuyankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.

1Th 2:3 Pakuti kudandaulira kwathu sikuchokera kukusochera kapena kuchidetso, kapena m’chinyengo:

1Th 2:4 Komatu monga Mulungu adatibvomereza kutiyikiza Uthenga Wabwino, kotero tiyankhula; osati monga wokondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.

1Th 2:5 Pakuti sitidagwiritsa ntchito nawo mawu wosyasyalika nthawi ili yonse, monga mudziwa, kapena kusilira, mboni ndi Mulungu;

1Th 2:6 Kapena sitidafuna kukhala wofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa ena, tingakhale tidali nayo mphamvu yakukulemetsani monga atumwi a Khristu.

1Th 2:7 Komatu tidakhala wofatsa pakati pa inu, monga m’mene mlezi afukata ana ake a iye yekha:

1Th 2:8 Potero pokhara wokhudzidwa ndichikhumbo cha kwa inu tidabvomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala wokondedwa kwa ife.

1Th 2:9 Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chibvuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tidalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.

1Th 2:10 Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tidakhala woyera mtima ndi wolungama ndi wosalakwa kwa inu akukhulupirira:

1Th 2:11 Monga mudziwa momwe tidalimbikitsidwira ndi kutonthozedwa ndi kulamulira wina aliyense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,

1Th 2:12 Kuti muyende koyenera Mulungu, amene adakuyitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha ndi ulemerero.

1Th 2:13 Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza chifukwa, pamene mudalandira mawu a Mulungu, amene mudawamva kwa ife, simudawalandire monga mawu a anthu, komatu monga ali chowonadi ndithu, mawu a Mulungu amenenso agwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira.

1Th 2:14 Pakuti inu, abale, mudayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m’Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zonsezi inu mudazimva kuwawa ndi anthu a mdziko lanu la inu nokha, monganso iwo adachitira a Ayuda.

1Th 2:15 Amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri awo, natinzunza ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nawo anthu onse;

1Th 2:16 Natiletsa ife kuti tisayankhule ndi amitundu kuti apulumutsidwe; kudzazitsa machimo awo nthawi zonse: chifukwa mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.

1Th 2:17 Koma ife, abale, angakhale adatichotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ayi, tidayesetsa koposa kuwona nkhope yanu ndi chikhumbo chachikulu.

1Th 2:18 Chifukwa tidafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana adatiletsa.

1Th 2:19 Pakuti chiyembekezo chathu, mchiyani kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye n’chiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu Khristu pakufika kwake?

1Th 2:20 Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.



3

1Th 3:1 Chifukwa chake, posakhoza kulekereranso, tidabvomereza mtima atisiye tokha ku Atene;

1Th 3:2 Ndipo tidatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m’Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu:

1Th 3:3 Kuti asasunthike munthu aliyense ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiyika ife tichite izi.

1Th 3:4 Pakutinso, pamene tidali ndi inu tidakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudachitika, monganso mudziwa.

1Th 3:5 Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndidatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo ntchito yathu yikadakhala yopanda pake.

1Th 3:6 Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiwona ife, monganso ife kukuwonani inu:

1Th 3:7 Chifukwa cha ichi, abale, tatonthozedwa pa inu m’kupsinjika kwathu konse ndi chisautso chathu chonse, mwa chikhulupiriro chanu:

1Th 3:8 Pakuti tsopano tiri ndi moyo ngati inu muchilimika mwa Ambuye.

1Th 3:9 Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;

1Th 3:10 Ndikuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikawone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewerera pa chikhulupiriro chanu?

1Th 3:11 Koma tsopano Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu atitsogolere m’njira yakufika kwa inu.

1Th 3:12 Koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m’chikondano wina kwa mzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu:

1Th 3:13 Kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m’chiyero pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu Khristu pamodzi ndi woyera mtima ake onse.



4

1Th 4:1 Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga mudalandira kwa ife mayendedwe wokoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.

1Th 4:2 Pakuti mudziwa malangizo amene tidakupatsani mwa Ambuye Yesu.

1Th 4:3 Pakuti ichi ndichifuniro cha Mulungu ndicho chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kuchiwerewere:

1Th 4:4 Aliyense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu;

1Th 4:5 Kosati m’chisiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu:

1Th 4:6 Asapitilireko munthu, nanyenge mbale wake m’menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tidakuchenjezani, ndipo tidachitapo umboni.

1Th 4:7 Pakuti Mulungu sadayitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso.

1Th 4:8 Chifukwa chake iye wonyoza ichi, sanyoza munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa ife.

1Th 4:9 Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani inu ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mzake;

1Th 4:10 Ndipo zowonadi, mudawachitira ichi abale onse a m’Makedoniya lonse. Koma tikupemphani, abale, kuti muchuluke ndi kuchuluka koposa;

1Th 4:11 Ndikuti muphunzire, kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tidakulamulirani;

1Th 4:12 Kuti mukayende mowona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.

1Th 4:13 Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona, kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.

1Th 4:14 Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.

1Th 4:15 Pakuti ichi tinena kwa inu m’mawu wa Ambuye, kuti ife wokhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera wogonawo.

1Th 4:16 Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuwu, ndi mawu a m’ngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu: ndipo akufa mwa Khristu adzawuka choyamba.

1Th 4:17 Pamenepo ife wokhala ndi moyo wotsalafe tidzakwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.

1Th 4:18 Chomwecho, tonthozanani wina ndi mzake ndi mawu awa.



5

1Th 5:1 Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale sikufunika kuti ndikulembereni.

1Th 5:2 Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.

1Th 5:3 Pamenepo adzangonena, Mtendere ndi chitetezo, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera iwo, monga zowawa za mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.

1Th 5:4 Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala.

1Th 5:5 Pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; simuri a usiku, kapena amdima;

1Th 5:6 Chifukwa chake tsono tisagone monga achitira enawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.

1Th 5:7 Pakuti iwo akugona, agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.

1Th 5:8 Koma ife popeza tiri a usana tisaledzere, titabvala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi, ndi chisoti chimene ndi chiyembekezo cha chipulumutso.

1Th 5:9 Pakuti Mulungu sadatiyika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu,

1Th 5:10 Amene adafa m’malo mwathu, kuti, pamene tidzuka kapena kugona, tikhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.

1Th 5:11 Mwa ichi tonthozanani, ndipo mangiliranani wina ndi mzake, monganso mumachita.

1Th 5:12 Koma abale, tikupemphani, adziweni iwo amene amagwira ntchito mwa inu, nakhala akulu akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu;

1Th 5:13 Ndipo muwachitire ulemu wapamwambatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo, ndipo khalani ndimtendere mwa inu nokha.

1Th 5:14 Ndipo tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, tonthozani amantha mtima, chilikizani wofoka, mukhale woleza mtima pa anthu onse.

1Th 5:15 Penyani kuti wina asabwezere choyipa womchitira choyipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa anthu onse.

1Th 5:16 Kondwerani nthawi zonse.

1Th 5:17 Pempherani kosalekeza.

1Th 5:18 Mzinthu m’zonse yamikani: pakuti ichi ndichifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.

1Th 5:19 Musazime Mzimuyo.

1Th 5:20 Musanyoze manenero.

1Th 5:21 Yesani zinthu zonse; sungani chokomacho.

1Th 5:22 Mupewe mawonekedwe onse a choyipa.

1Th 5:23 Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konse konse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

1Th 5:24 Wakuyitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita.

1Th 5:25 Abale, tipempherereni ife.

1Th 5:26 Patsani moni abale onse ndi chipsompsono chopatulika.

1Th 5:27 Ndikulamurirani mwa Ambuye kuti kalatayu awerengedwe kwa abale onse woyera mtima.

1Th 5:28 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE