1 Peter


1

1Pe 1:1 Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa wosankhidwa akukhala alendo achibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya.

1Pe 1:2 Wosankhidwa mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m’chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.

1Pe 1:3 Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chochuluka, adatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu,

1Pe 1:4 Kuti tilandire cholowa chosabvunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’Mwamba inu,

1Pe 1:5 Amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiliro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza:

1Pe 1:6 M’menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu:

1Pe 1:7 Kuti mayesedwe a chikhulupiliro chanu, ndiwo amtengo wake woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe wochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa kuwonekera kwa Yesu Khristu:

1Pe 1:8 Amene mungakhale simudamuwona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, mukhulupirira inde, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:

1Pe 1:9 Ndikulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu.

1Pe 1:10 Mwa chipulumutso ichi chimene aneneri adachifunafuna, nafufuza mosamalitsa amene adanenera mwa chisomocho chimene chidzadza pa inu.

1Pe 1:11 Ndikufufuza nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo adalozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nawo.

1Pe 1:12 Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sadadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene adakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba: zinthu izi angelo adakhumba kusuzumiramo.

1Pe 1:13 Mwa ichi, podzimanga m’chuuno, kunena za mtima wanu; mukhale wodzisunga, nimuyembekeze konse konse chisomo chiri kutengedwa kudza nacho kwa inu m’bvumbulutso la Yesu Khristu;

1Pe 1:14 Monga ana womvera wosadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala wosadziwa inu:

1Pe 1:15 Komatu monga Iye wakuyitana inu ali woyera mtima, khalani inunso woyera mtima m’makhalidwe anu onse:

1Pe 1:16 Popeza kwalembedwa, mudzikhala woyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima:

1Pe 1:17 Ndipo mukamuyitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho pakati pa anthu, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu:

1Pe 1:18 Podziwa kuti simudawomboledwa ndi zobvunda, golidi ndi siliva, kusiyana nawo makhalidwe anu achabe wochokera kwa makolo anu;

1Pe 1:19 Koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:

1Pe 1:20 Amene adazindikirikatu asadakhazikike maziko a dziko lapansi, koma adawonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi.

1Pe 1:21 Chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiliro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.

1Pe 1:22 Powona mwayeretsa moyo wanu pomvera chowonadi mwa Mzimu mu chikondi choyera cha pa abale, mukondane kwenikweni wina ndi mzake ndi mtima wa ngwiro:

1Pe 1:23 Wokhala wobadwanso, osati ndi mbewu yofeka, komatu yosawola, mwa mawu a Mulungu a moyo ndi wokhalitsa.

1Pe 1:24 Popeza, anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wawo wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa:

1Pe 1:25 Koma Mawu wa Ambuye akhala chikhalire. Ndiwo mawu a Uthenga Wabwino wolalikidwa kwa inu.



2

1Pe 2:1 Momwemo pakutaya choyipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi mawonekedwe wonyenga, ndi kaduka ndi mayankhulidwe aliwonse woyipa.,

1Pe 2:2 Monga makanda obadwa lero khumbani mkaka wa mawu kuti mukakule nawo:

1Pe 2:3 Monga mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima.

1Pe 2:4 Amene pakudza kwa Iye, monga mwala wa moyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu.

1Pe 2:5 Inunso ngati miyala ya moyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe woyera mtima, akupereka nsembe za uzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

1Pe 2:6 Chifukwa chake kwalembedwa m’lembo, tawonani, ndiyika m’ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.

1Pe 2:7 Kwa inu tsono akukhulupirira, ali wa mtengo wake; koma kwa iwo wosamvera mwala umene womangawo adaukana, womwewo udayesedwa mutu wa pa ngodya,

1Pe 2:8 Ndipo mwala wakukhumudwa nawo, ndi thanthwe lopunthwitsa; kwa iwo akukhumudwa ndi mawu, pokhala wosamvera, kumenekonso adayikidwako.

1Pe 2:9 Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu amwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene adakuyitanani mutuluke mumdima, mulowe kuwunika kwake kodabwitsa;

1Pe 2:10 Inu amene mu nthawi yakale simudali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simudalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.

1Pe 2:11 Wokondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi wogonera, mudzikanize ku zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;

1Pe 2:12 Ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale wokoma, kuti, m’mene akamba za inu ngati wochita zoyipa, akalemekeze Mulungu pakuwona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.

1Pe 2:13 Tadzigonjani kwa zoyikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye: ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;

1Pe 2:14 Kapena kwa akazembe, monga wotumidwa ndi iye kukalanga wochita zoyipa, koma kuyamikira wochita zabwino.

1Pe 2:15 Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti, ndikuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu wopusa:

1Pe 2:16 Monga mfulu, koma wosakhala nawo ufulu monga chobisira choyipa, koma ngati atumiki a Mulungu.

1Pe 2:17 Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Wopani Mulungu. Chitirani mfumu ulemu.

1Pe 2:18 Akapolo inu, gonjerani ambuye anu ndi kuwopa konse, osati abwino ndi aulere wokha, komanso aukali.

1Pe 2:19 Pakuti ichi ndi choyamikirika ngati munthu, chifukwa cha chikumbu mtima pa Mulungu apirira mu zophweteka pakumva zowawa wosaziyenera.

1Pe 2:20 Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapilira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapilira, ichi ndi chobvomerezeka pa maso paMulungu.

1Pe 2:21 Pakuti mwa ichi mudayitanidwa: pakutinso Khristu adamva zowawa m’malo mwathu, natisiyirani chitsanzo kuti tikalondore mapazi ake.

1Pe 2:22 Ngakhale sadachita tchimo, ndipo m’kamwa mwake sichidapezedwa chinyengo:

1Pe 2:23 Amene pochitidwa chipongwe, sadabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sadawopsa, koma adapereka mlandu kwa Iye woweruza molungama:

1Pe 2:24 Amene adasenza machimo athu mwini yekha m’thupi mwake pamtengo, kuti ife, akufa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo: ameneyo mikwingwirima yake mudachiritsidwa nayo.

1Pe 2:25 Pakuti mudali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwatembenukira kwa M’busa ndi Woyang’anira wa moyo wanu.



3

1Pe 3:1 Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti ngatinso ena samvera mawu, akakodwe wopanda mawu mwa mayendedwe a akazi;

1Pe 3:2 Pakuwona mayendedwe anu woyera ndi kuwopa kwanu:

1Pe 3:3 Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kwa kubvala chobvala;

1Pe 3:4 Koma kukhale munthu wobisika wa mtima, m’chobvala chosawola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.

1Pe 3:5 Pakuti koteronso kale akazi woyera mtima, amene adakhulupirira mwa Mulungu, adadzikometsera wokha, pokhala womvera amuna awo a iwo wokha:

1Pe 3:6 Monganso Sara adamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake a akazi ngati muchita bwino osawopa chowopsa chiri chonse.

1Pe 3:7 Momwemonso amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chofowoka, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.

1Pe 3:8 Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, wochitirana chifundo wina ndi mzake, wokondana ndi abale, achisoni, wodzichepetsa:

1Pe 3:9 Osabwezera choyipa ndi choyipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzachita ichi mwayitanidwa, kuti mulandire dalitso.

1Pe 3:10 Pakuti iye wofuna kukonda moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choyipa, ndi milomo yake isayankhule chinyengo:

1Pe 3:11 Ndipo apatuke pa choyipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuwulondola.

1Pe 3:12 Pakuti maso, a Ambuye ali pa wolungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye itsutsana ndi iye wochita zoyipa.

1Pe 3:13 Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choyipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino?

1Pe 3:14 Komatu ngatinso mukamva zowawa chifukwa cha chilungamo, wodala inu; ndipo musawope pakuwopsa kwawo, kapena musadere nkhawa;

1Pe 3:15 Koma mumpatulikitse kwa Ambuye Mulungu mitima yanu; wokonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.

1Pe 3:16 Ndikukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani inu zoyipa monga wochita zoyipa kuti akachite manyazi ndi mayendedwe anu abwino mwa Khristu.

1Pe 3:17 Pakuti, kumva zowawa kwanu chifukwa cha kuchita zabwino, ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoyipa, nkwabwino kumva zowawa chifukwa chakuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu.

1Pe 3:18 Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, wolungama m’malo mwa wosalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mu mzimu:

1Pe 3:19 M’menemonso adapita, nalalikira mizimu idali m’ndende;

1Pe 3:20 Imene m’nthawi yakale idakhala yosamvera, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kudalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka kwa chombo, m’menemo wowerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, adapulumutsidwa mwa madzi:

1Pe 3:21 Chimenenso chiri chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, (kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu,) mwa kuuka kwa Yesu Khristu:

1Pe 3:22 Amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu; atalowa m’Mwamba; pali angelo, ndi ma ulamuliro, ndi zimphamvu, zopangidwa zikhale zomgonjera Iye.



4

1Pe 4:1 Popeza Khristu adamva zowawa m’thupi chifukwa cha ife, mudzikonzere inunso mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m’thupi walekana nalo tchimo;

1Pe 4:2 Kuti nthawi yotsalira asakhalenso Iye ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma kuchifuniro cha Mulungu.

1Pe 4:3 Pakuti m’nthawi yakale idatifikira ife kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda ife m’kukhumba zonyansa, mzilakolako, kuledzera, madyerero, mamwayimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka:

1Pe 4:4 M’menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nawo kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, akuyankhula zoyipa pa inu:

1Pe 4:5 Amenewo adzadziwerengera wokha kwa Iye amene ndi wokonzeka kuweruza a moyo ndi akufa.

1Pe 4:6 Chifukwa cha ichi ndi chifukwa chake udalalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m’thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.

1Pe 4:7 Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chiri pafupi: chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m’mapemphero:

1Pe 4:8 Koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chidzakwiriritsa unyinji wa machimo.

1Pe 4:9 Mucherezane wina ndi mzake, opanda udani.

1Pe 4:10 Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo wina ndi mzake, ngati adindo wokoma a chisomo cha mitundu mitundu cha Mulungu.

1Pe 4:11 Akayankhula wina, ayankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nawo ulemerero ndi mphamvu ku nthawi za nthawi. Ameni.

1Pe 4:12 Wokondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu cha chilendo chakuchitikirani inu:

1Pe 4:13 Koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa bvumbulutso la ulemerero wake mukasangalale ndikukondwera kwakukulukulu.

1Pe 4:14 Ngati munyozedwa pa dzina la Khristu, wodala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi wa Mulungu apuma pa inu: kumbali yawo amuyankhulira Iye zoyipa, koma kumbali yanu Iye alemekezedwa.

1Pe 4:15 Koma asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena ngati mbala, kapena ngati wochita zoyipa, kapena ngati wodudukira nkhani za anthu ena.

1Pe 4:16 Koma ngati munthu wina akumva zowawa chifukwa choti ndi Mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina ili.

1Pe 4:17 Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba pa ife, chitsiriziro cha iwo wosamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chotani?

1Pe 4:18 Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndikuyesetsa kokha kokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzawoneka kuti?

1Pe 4:19 Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu ayike moyo wawo kwa Iye ndi kuchita zokoma monga kwa Wolenga wokhulupirika.



5

1Pe 5:1 Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nawo ulemerero umene udzabvumbulutsidwawo:

1Pe 5:2 Dyetsani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokangamiza; koma mwa ufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu.

1Pe 5:3 Osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma wokhala zitsanzo za gululo.

1Pe 5:4 Ndipo pakuwonekera M’busa wamkulu, mudzalandira Korona wa ulemerero, wosafota.

1Pe 5:5 Momwemonso anyamata inu, mverani akulu.Koma nonsenu mubvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza wodzikudza, koma apatsa chisomo kwa wodzichepetsa.

1Pe 5:6 Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni:

1Pe 5:7 Ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

1Pe 5:8 Khalani wodzisunga, dikirani chifukwa mdani wanu mdierekezi, monga ngati mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina kuti akam’meze:

1Pe 5:9 Ameneyo mumkanize pokhazikika m’chikhulupiliro, podziwa kuti zowawa zomwezo ziri mkukwaniritsidwa pa abale anu ali m’dziko lapansi.

1Pe 5:10 Ndipo Mulungu wa chisomo chonse amene adakuyitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu Yesu, mutamva zowawa kanthawi, adzapanga inu angwiro,adzakhazikitsa,adzalimbikitsa,adza chirikiza inu.

1Pe 5:11 Kwa Iye kukhale ulemerero ndi ulamuliro ku nthawi za nthawi. Ameni.

1Pe 5:12 Mwa Silvano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwa chidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo chowona cha Mulungu ndi ichi mwa chimenechi muyimemo.

1Pe 5:13 Mpingo wa ku Babulo wosankhidwa pamodzi nanu ukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga.

1Pe 5:14 Patsanani moni wina ndi mzake ndi chipsopsono cha chikondi: mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu Yesu. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE