1 John


1

1Jn 1:1 Chimene chidaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiwona m’maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mawu a moyo.

1Jn 1:2 (Ndipo moyowo udawonekera, ndipo tidawona ndipo tichita umboni, ndipo tikukuwonetsani moyo wosathawo, umene udali kwa Atate nuwonekera kwa ife)

1Jn 1:3 Chimene tidachiwona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife: ndipo ndithu chiyanjano chathu chirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu.

1Jn 1:4 Ndipo zinthu izi tilemba ife, kwa inu kuti chimwemwe chanu chikwaniritsidwe.

1Jn 1:5 Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.

1Jn 1:6 Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita chowonadi:

1Jn 1:7 Koma ngati tiyenda m’kuwunika, monga Iye ali m’kuwunika, tiyanjana wina ndi mzake, ndipo mwazi wa Yesu Khristu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

1Jn 1:8 Tikati kuti tiribe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe chowonadi.

1Jn 1:9 Ngati tibvomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chiri chonse.

1Jn 1:10 Ngati tinena kuti sitidachimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mawu ake sakhala mwa ife.



2

1Jn 2:1 Tiana tanga, zinthu izi ndalembera inu, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama:

1Jn 2:2 Ndipo Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu: koma osati athu wokha, komanso machimo adziko lonse lapansi.

1Jn 2:3 Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake.

1Jn 2:4 Iye wonena kuti, Ndimdziwa Iye, koma sasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe chowonadi.

1Jn 2:5 Koma iye amene asunga mawu ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chikhala changwiro. M’menemo tizindikira kuti tiri mwa Iye.

1Jn 2:6 Iye wonena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga adayenda Iyeyo.

1Jn 2:7 Wokondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene mudali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo lakalelo ndilo mawu amene mudawamva kuyambira pachiyambi.

1Jn 2:8 Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chiri chowona mwa Iye ndi mwa inu: kuti mdima wapita, ndi kuwunika kowona kwayamba kuwala.

1Jn 2:9 Iye amene anena kuti ali m’kuwunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino.

1Jn 2:10 Iye amene akonda mbale wake akhala m’kuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.

1Jn 2:11 Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.

1Jn 2:12 Ndikulemberani, tiana, popeza machimo anu adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake.

1Jn 2:13 Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pa chiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamlaka woyipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

1Jn 2:14 Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi Mawu a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woyipayo.

1Jn 2:15 Musakonde dziko lapansi, kapena zinthu za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye.

1Jn 2:16 Pakuti chiri chonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.

1Jn 2:17 Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake: koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.

1Jn 2:18 Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi: ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo wokana Khristu ambiri.M’menemo muzindikira kuti ndi nthawi yotsiriza iyi.

1Jn 2:19 Adatuluka mwa ife, komatu sadali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma adatuluka kuti awonekere kuti sadali onse a ife.

1Jn 2:20 Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.

1Jn 2:21 Sindidakulemberani chifukwa simudziwa chowonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera ku chowonadi.

1Jn 2:22 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu sali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana.

1Jn 2:23 Yense wokana Mwana, alibe Atate: (koma) iye wobvomereza Mwana ali ndi Atatenso.

1Jn 2:24 Koma inu, chimene mudachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala chimene mudachimva kuyambira pa chiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana ndi mwa Atate.

1Jn 2:25 Ndipo ili ndi lonjezano Iye adatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha.

1Jn 2:26 Zinthu izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.

1Jn 2:27 Ndipo inu kudzoza kumene mudalandira kuchokera kwa Iye, kukhala kwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli kowona, sikuli bodza ayi, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.

1Jn 2:28 Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akadzawonekera Iye tidzakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake.

1Jn 2:29 Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti ali yensenso wochita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.



3

1Jn 3:1 Tawonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife wotere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silidamzindikire Iye.

1Jn 3:2 Wokondedwa, tsopano tiri ana a Mulungu, ndipo sichidawoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuwoneka Iye, tidzakhala wofanana ndi Iye, pakuti tidzamuwona Iye monga ali.

1Jn 3:3 Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.

1Jn 3:4 Yense wakuchita tchimo achimwira lamulo: ndipo tchimo ndilo kuswa lamulo.

1Jn 3:5 Ndipo mudziwa kuti Iyeyu adawonekera kudzachotsa machimo athu; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.

1Jn 3:6 Yense wokhala mwa Iye sachimwa: yense wakuchimwa sadamuwona Iye, ndipo sadamdziwa Iye.

1Jn 3:7 Tiana, munthu asakusokeretseni inu: iye wochita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama.

1Jn 3:8 Iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi adachimwa kuyambira pachiyambi. Chifukwa cha ichi Mwana wa Mulungu adawonekera, ndiko kuti akawononge ntchito za mdierekezi.

1Jn 3:9 Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbewu yake ikhala mwa iye: ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.

1Jn 3:10 M’menemo awoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo sali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.

1Jn 3:11 Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mzake.

1Jn 3:12 Osati monga Kayini adali wochokera mwa woyipayo, namupha mbale wake. Ndipo adamupha iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zidali zoyipa, ndi za mbale wake zolungama.

1Jn 3:13 Musazizwe, abale, likadana nanu dziko lapansi.

1Jn 3:14 Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka mu imfa kulowa m’moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda m’bale wake akhala mu imfa.

1Jn 3:15 Yense wodana ndi mbale wake ali wakupha munthu: ndipo mudziwa kuti wakupha munthu ali yense alibe moyo wosatha wakukhala mwa lye.

1Jn 3:16 Umo tizindikira chikondi cha Mulungu, popeza Iyeyu adapereka moyo wake chifukwa chaife: ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.

1Jn 3:17 Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, nawona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pom’mana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?

1Jn 3:18 Tiana, tanga, tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’chowonadi.

1Jn 3:19 Umo tidzazindikira kuti tiri wochokera m’chowonadi, ndipo tidzakhazikitsa mitima yathu pamaso pake.

1Jn 3:20 M’mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zinthu zonse.

1Jn 3:21 Wokondedwa mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu.

1Jn 3:22 Ndipo chimene chiri chonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zinthu zomkondweretsa pamaso pake.

1Jn 3:23 Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mzake, monga Iye adatipatsa lamulo.

1Jn 3:24 Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m’menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene adatipatsa ife.



4

1Jn 4:1 Wokondedwa, musamakhulupirira mzimu uli wonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri wonyenga ambiri adatuluka kulowa m’dziko lapansi.

1Jn 4:2 M’menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uli wonse umene ubvomereza kuti Yesu Khristu adadza m’thupi, uchokera mwa Mulungu;

1Jn 4:3 Ndipo mzimu uliwonse umene subvomereza kutiYesu Khristu adadza mthupi, suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m’dziko lapansi tsopano lomwe.

1Jn 4:4 Inu ndinu wochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo mudayilaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu ali wamkulu kuposa iye wakukhala m’dziko lapansi

1Jn 4:5 Iwo ndiwo wochokera m’dziko lapansi: mwa ichi ayankhula monga wochokera m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera.

1Jn 4:6 Ife ndife wochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife. Momwemo tizindikira mzimu wa chowonadi, ndi mzimu wachisokeretso.

1Jn 4:7 Wokondedwa tikondane wina ndi mzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, nazindikira Mulungu.

1Jn 4:8 Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi:

1Jn 4:9 Umo chidawoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu adatuma Mwana wake wobadwa yekha alowe m’dziko lapansi kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.

1Jn 4:10 Umo muli chikondi, sikuti ife tidakonda Mulungu, koma kuti Iye adatikonda ife, ndipo adatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.

1Jn 4:11 Wokondedwa, ngati Mulungu adatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mzake.

1Jn 4:12 Palibe munthu adamuwona Mulungu nthawi ili yonse. Ngati tikondana wina ndi mzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife.

1Jn 4:13 M’menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye ndi Iye mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake.

1Jn 4:14 Ndipo ife tawona, ndipo tichita umboni kuti Atate adatuma Mwana kuti akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.

1Jn 4:15 Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.

1Jn 4:16 Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu, ndi Mulungu akhala mwa iye.

1Jn 4:17 M’menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m’tsiku la chiweruziro: chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tiri ife m’dziko lino lapansi.

1Jn 4:18 Mulibe mantha m’chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango. Ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m’chikondi.

1Jn 4:19 Tikonda Iye, chifukwa adayamba Iye kutikonda.

1Jn 4:20 Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye m’bale wake, ali wabodza; pakuti iye wosakonda m’bale wake amene wamuwona, akonda Mulungu bwanji amene sadamuwona?

1Jn 4:21 Ndipo lamulo iri tiri nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso m’bale wake.



5

1Jn 5:1 Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu: ndipo yense wakukonda Iye amene adabala akondanso iye amene adabadwa wochokera mwa Iye.

1Jn 5:2 Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kusunga malamulo ake.

1Jn 5:3 Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sakhala wolemetsa.

1Jn 5:4 Pakuti chirichonse chimene chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi: ndipo ichi ndi chigonjetso tigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu.

1Jn 5:5 Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi; koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu.

1Jn 5:6 Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi wokha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye chowonadi.

1Jn 5:7 Pakuti pali atatu akuchita umboni, M’mwamba, Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyera: ndipo iwo atatu ali m’modzi.

1Jn 5:8 Ndipo pali atatu, akuchita umboni m’dziko lapansi, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi: ndipo awa atatu agwirizana mu m’modzi.

1Jn 5:9 Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti adachita umboni za Mwana wake.

1Jn 5:10 Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboni mwa iye yekha: iye wosakhulupirira Mulungu adamuyesa Iye wonama; chifukwa sadakhulupirira umboni wa Mulungu adauchita wa Mwana wake.

1Jn 5:11 Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu adatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake.

1Jn 5:12 Iye wakukhala ndi Mwana ali nawo moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.

1Jn 5:13 Zinthu izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.Kuti mukhulupirire padzina la mwana wa Mulungu.

1Jn 5:14 Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake atimvera ife:

1Jn 5:15 Ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chiri chonse tichipempha, tidziwa kuti tiri nazo zinthu izi tazikhumba kwa Iye.

1Jn 5:16 Ngati wina akawona m’bale wake alikuchimwa tchimo losati la ku imfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo wosati a ku imfa. Pali tchimo la ku imfa: za ilo sindinena kuti mupemphere.

1Jn 5:17 Chosalungama chiri chonse chiri uchimo: ndipo pali tchimo losati la ku imfa.

1Jn 5:18 Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woyipayo samkhudza.

1Jn 5:19 Ndipo tidziwa kuti tiri ife wochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woyipayo.

1Jn 5:20 Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Wowonayo, ndipo tiri mwa Wowonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Uyu ndiye Mulungu wowona ndi moyo wosatha.

1Jn 5:21 Ana, dzisungeni eni nokha kupewa mafano. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE