1 Corinthians


1

1Co 1:1 Paulo, woyitanidwa akhale mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sositene m’bale wathu,

1Co 1:2 Kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m’Korinto, ndiwo woyeretsedwa mwa Khristu Yesu, woyitanidwa akhale woyera mtima, pamodzi ndi onse akuyitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m’malo monse, ndiye wawo, ndi wathu:

1Co 1:3 Chisomo chikhale kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

1Co 1:4 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu;

1Co 1:5 Kuti m’zonse muli achuma mwa Iye, m’mawu onse, ndi chidziwitso chonse;

1Co 1:6 Monga momwe umboni wa Khristu udakhazikika mwa inu:

1Co 1:7 Kotero kuti siyikusowani inu; mphatso pakulindira inu kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu:

1Co 1:8 Amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale wopanda chilema m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.

1Co 1:9 Mulungu ali wokhulupirika amene mudayitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu.

1Co 1:10 Koma ndikudandawulirani inu, abale mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzi modzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mwangwiro mu m`mtima umodzi womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.

1Co 1:11 Pakuti zidamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu.

1Co 1:12 Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu.

1Co 1:13 Kodi Khristu wagawika? Kodi Paulo adapachikidwa chifukwa cha inu? Kapena kodi mudabatizidwa m’dzina la Paulo?

1Co 1:14 Ndiyamika Mulungu kuti sindidabatiza m’modzi yense wa inu, koma Krispo ndi Gayo;

1Co 1:15 Kuti anganene m’modzi kuti mwabatizidwa m’dzina langa.

1Co 1:16 Koma ndidabatizanso a pa banja la Stefana; za ena, sindidziwa ngati ndidabatiza wina yense.

1Co 1:17 Pakuti Khristu sadandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mawu, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.

1Co 1:18 Pakuti kulalikira kwa mtanda kuli ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tiri kupulumutsidwa ndi mphamvu ya Mulungu.

1Co 1:19 Pakuti kwalembedwa, Ndidzawononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa wochenjera ndidzakutha.

1Co 1:20 Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sadayipusitsa nzeru ya dziko lapansi?

1Co 1:21 Pakuti popeza m’nzeru ya Mulungu dziko la pansi, mwa nzeru yake, silidadziwa Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa wokhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.

1Co 1:22 Ndipo popeza Ayuda afuna zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru:

1Co 1:23 Koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa a helene chinthu chopusa:

1Co 1:24 Koma kwa iwo woyitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Ahelene, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu.

1Co 1:25 Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zawo; ndipo chofowoka cha Mulungu chiposa anthu mphamvu zawo.

1Co 1:26 Pakuti penyani mayitanidwe anu, abale, kuti sayitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, ayi:

1Co 1:27 Koma Mulungu adasankhula zopusa za dziko lapansi kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo Mulungu adazisankhula zinthu zofowoka za dziko la pansi kuti akachititse manyazi zamphamvu;

1Co 1:28 Ndipo zinthu zopanda pake za dziko lapansi, ndi zinthu zonyozeka, adazisankhula Mulungu, inde ndi zinthu zoti kulibe kuti zikathere zinthu zoti ziliko.

1Co 1:29 Kuti thupi liri lonse lisadzitamande pamaso pake.

1Co 1:30 Koma kwa iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene adayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiwombolo:

1Co 1:31 Kuti monga kwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamandire mwa Ambuye.



2

1Co 2:1 Ndipo ine, abale, m’mene ndidadza kwa inu, sindidadza ndi kuposa kwa mawu, kapena kwa nzeru, poyankhula kwa inu umboni wa Mulungu.

1Co 2:2 Pakuti ndidatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu pakati pa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa.

1Co 2:3 Ndipo ine ndidakhala nanu mu ufowoko ndi m’mantha, ndi monthunthumira mwambiri.

1Co 2:4 Ndipo mawu anga ndi kulalikira kwanga sikudakhala ndi mawu wokopa anzeru, koma m’chiwonetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;

1Co 2:5 Kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m’nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.

1Co 2:6 Koma tiyankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu anthawi yino ya pansi pano, amene alimkuthedwa:

1Co 2:7 Koma tiyankhula nzeru ya Mulungu m’chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu adayikiratu, pasadakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu:

1Co 2:8 Imene sadayidziwa m’modzi wa akulu anthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero.

1Co 2:9 Koma monga kwalembedwa, zimene diso silidaziwona, ndi khutu silidazimva, nisizidalowa mu mtima wa munthu, zimene zili zonse Mulungu adakonzereratu iwo akumkonda Iye.

1Co 2:10 Koma kwa ife Mulungu wabvumbulutsa adatiwonetsera izo kwa ife mwa Mzimu wake; pakuti Mzimu asanthula zinthu zonse, inde zinthu zakuya za Mulungu.

1Co 2:11 Pakuti ndani wa anthu adziwa zinthu za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwenso zinthu za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.

1Co 2:12 Koma sitidalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zinthu zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwa ulere.

1Co 2:13 Zinthu zimenenso tiyankhula, si ndi mawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma wophunzitsidwa ndi Mzimu; kulinganiza zinthu za mzimu ndi za mzimu.

1Co 2:14 Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwa uzimu.

1Co 2:15 Koma iye amene ali wa uzimu ayesa zinthu zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi munthu.

1Co 2:16 Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tiri nawo mtima wa Khrstu.



3

1Co 3:1 Ndipo ine, abale sindidakhoza kuyankhula ndi inu monga ndi a uzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu.

1Co 3:2 Ndidadyetsa inu mkaka, sichakudya cholimba ayi; pakuti simudachikhoza; ngakhale tsopano lino simuchikhoza; pakuti muli athupi.

1Co 3:3 Pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndewu ndi mpatuko pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

1Co 3:4 Pakuti wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mzake, ndine wa Apolo; simuli athupi kodi?

1Co 3:5 Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene mudakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye adampatsa.

1Co 3:6 Ndidadzala ine, adathilira Apolo; koma Mulungu adakulitsa.

1Co 3:7 Chotero sali kanthu iye wobzala kanthu kalikonse kapena wothilirayo; koma Mulungu amene akulitsa.

1Co 3:8 Tsopano Iye wobzalayo ndi iye wothilirayo ali amodzi; ndipo munthu aliyense adzalandira mphotho yake ya iye yekha monga mwa ntchito yake ya iye.

1Co 3:9 Pakuti ife ndife antchito pamodzi ndi Mulungu; olima a Mulungu, nyumba ya Mulungu ndi inu.

1Co 3:10 Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndidayika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang’anire umo amangira pamenepo.

1Co 3:11 Pakuti palibe munthu wina akhoza kuyika maziko ena, koma amene ayikidwako, ndiwo Yesu Khristu.

1Co 3:12 Tsopano ngati munthu wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu.

1Co 3:13 Ntchito ya munthu aliyense idzawonetsedwa; pakuti tsikulo lidzayisonyeza, chifukwa kuti idzabvumbuluka mmoto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya munthu ali yense idzakhala yotani.

1Co 3:14 Ngati ntchito ya munthu ali yense ikhala imene adayimangako pamenepo, adzalandira mphotho.

1Co 3:15 Ngati ntchito ya munthu wina idzatenthedwa, zidzawonongeka zake zonse; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.

1Co 3:16 Kodi simudziwa kuti muli kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu akhala mwa inu?

1Co 3:17 Ngati munthu aliyense awononga kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuwononga; pakuti kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

1Co 3:18 Munthu aliyense asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu dziko lino la pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.

1Co 3:19 Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m’chenjerero lawo.

1Co 3:20 Ndiponso Ambuye azindikira zolingalira za anzeru, kuti ziri zopanda pake.

1Co 3:21 Chifukwa chake palibe munthu m’modzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse mzanu.

1Co 3:22 Ngakhale Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena ziri mkudza; zonse ndi zanu;

1Co 3:23 Koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu.



4

1Co 4:1 Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu.

1Co 4:2 Komatu pano pakufunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

1Co 4:3 Koma kwa ine kuli kanthu kakang’ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu, kuweruzidwa ndi munthu: inde sindidziweruza ndekha.

1Co 4:4 Pakuti sindidziwa kanthu mwa ine ndekha chotero sindiri pano monga wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.

1Co 4:5 Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzawonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nawo uyamiko wake wa kwa Mulungu.

1Co 4:6 Koma izi abale ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitilira zimene zilembedwa; kuti pasakhale m’modzi wodzitukumulira wina ndi mzake.

1Co 4:7 Pakuti akusiyanitsa iwe ndani ndi wina? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sudachilandira?

1Co 4:8 Tsopano mwakhuta, tsopano mwalemerera kale, mwalamulira monga mafumu wopanda ife; ndipo ndidakakonda kwa Mulungu kuti inu mulamulire kuti ifenso tikalamulire limodzi ndi inu.

1Co 4:9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu adakhazikitsa ife atumwi wotsiriza, monga kudayikidwa ku imfa monga tili ife; pakuti takhala ife chowonetsedwa ku dziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.

1Co 4:10 Tiri wopusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli wanzeru inu mwa Khristu; tiri ife wofowoka, koma inu amphamvu; inu ndinu wolemekezeka, koma ife ndife wonyozeka.

1Co 4:11 Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tiri amaliseche, tikhomedwa, tiribe malo okhala;

1Co 4:12 Ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipilira;

1Co 4:13 Ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa zadziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.

1Co 4:14 Sindilembera zinthu izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga wokondedwa.

1Co 4:15 Pakuti mungakhale muli nawo aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndabala inu mwa Uthenga Wabwino.

1Co 4:16 Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine.

1Co 4:17 Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo m’Mipingo yonse.

1Co 4:18 Koma ena adzitukumula, monga ngati sindidalimkudza kwa inu.

1Co 4:19 Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mawu a iwo wodzitukumula, koma mphamvuyi.

1Co 4:20 Pakuti ufumu wa Mulungu siuli m’mawu, koma mumphamvu.

1Co 4:21 Mufuna chiyani? Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa?



5

1Co 5:1 Kwamveka ndithu kuti kuli chiwerewere pakati pa inu, ndipo chiwerewere chotere chonga sichimveka mwa a mitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.

1Co 5:2 Ndipo mukhala wodzitukumula, osati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene adachita ntchito iyi.

1Co 5:3 Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndidaliko, zokhudzana ndi iye adachita ntchito iyi,

1Co 5:4 M’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu.

1Co 5:5 Kumpereka iye wochita chotere kwa satana, kuti liwonongeke thupi, kuti mzimu, upulumutsidwe m’tsiku la Ambuye Yesu.

1Co 5:6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse?

1Co 5:7 Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli wosatupa. Pakuti Khristu Pasakha wathu waperekedwa chifukwa cha ife:

1Co 5:8 Chifukwa cake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuyipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuwona mtima, ndi chowonadi:

1Co 5:9 Ndidalembera inu, m’kalata uja, kuti musayanjana ndi achiwerewere;

1Co 5:10 Si konse konse ndi a chiwerewere a dziko lino lapansi, kapena osirira, ndi wolanda kapena ndi wopembedza mafano; pakuti mkutero mukatuluke m’dziko lapansi.

1Co 5:11 Koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachiwerewere, kapena wosilira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, ayi:

1Co 5:12 Pakuti nditani nawo akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m’katimo simuwaweruza ndi inu?

1Co 5:13 Koma iwo akunja awaweruza Mulungu? Chotsani munthu woyipayo pakati pa inu nokha.



6

1Co 6:1 Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nawo mlandu pa mzake, kupita kukaweruzidwa kwa wosalungama, osati kwa woyera mtima?

1Co 6:2 Kapena kodi simudziwa kuti woyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi lidzaweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa?

1Co 6:3 Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?

1Co 6:4 Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe mu Mpingo.

1Co 6:5 Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe m’modzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale?

1Co 6:6 Koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa wosakhulupirira.

1Co 6:7 Koma pamenepo pali chosowa konse konse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuyipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?

1Co 6:8 Koma muyipsa, nimunyenga, ndipo mutero nawo abale anu.

1Co 6:9 Kapena simudziwa kuti wosalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; achiwerewere, kapena wopembedza mafano, kapena achigololo, kapena akudzipsa okha ndi manthanyula.

1Co 6:10 Kapena mbala, kapena wosilira, kapena woledzera, kapena wolalatira, kapena wolanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

1Co 6:11 Ndipo ena a inu mudali wotere: koma mudasambitsidwa, koma mudayeretsedwa, koma mudayesedwa wolungama, m’dzina la Ambuye Yesu ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

1Co 6:12 Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.

1Co 6:13 Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzawononga iyi ndi izi. Koma thupi siliri la chiwerewere, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi.

1Co 6:14 Koma Mulungu adawukitsa Ambuye, ndiponso adzawukitsa ife mwa mphamvu yake.

1Co 6:15 Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero ayi.

1Co 6:16 Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.

1Co 6:17 Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.

1Co 6:18 Thawani chiwerewere. Tchimo liri lonse munthu akalichita liri kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.

1Co 6:19 M`chiyani kodi? simudziwa kuti thupi lanu liri kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu ndipo simukhala a inu nokha?

1Co 6:20 Pakuti mudagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu, ndi mu mzimu wanu, zimene ziri zake za Mulungu.



7

1Co 7:1 Koma za izi mudandilembera inezi: kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.

1Co 7:2 Komabe poletsa chiwerewere munthu aliyense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

1Co 7:3 Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; chimodzimodzinso mkazi kwa mwamuna.

1Co 7:4 Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; ndipo momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mkazi ndiye.

1Co 7:5 Musamakanizana wina ndi mzake koma kubvomerezana kwanu, ndiko kwa nthawi, kuti mukadzipereke kukasala ndi kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.

1Co 7:6 Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa lamulo.

1Co 7:7 Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndiri ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti.

1Co 7:8 Koma ndinena kwa wosakwatira ndi kwa akazi a masiye, kuti kuli bwino iwo ngati akhala monganso ine.

1Co 7:9 Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha thupi.

1Co 7:10 Koma wokwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ayi, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna:

1Co 7:11 Komanso ngati amsiya akhale wosakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.

1Co 7:12 Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye: ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.

1Co 7:13 Ndipo mkazi ngati ali naye mwamuna wosakhulupira, nabvomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo

1Co 7:14 Pakuti mwamuna wosakhulupirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mwamunayo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala woyera.

1Co 7:15 Koma ngati wosakhulupirayo achoka, achoke, m’milandu yotere samangidwa ukapolo mwamunayo, kapena mkaziyo: koma Mulungu watiyitana ife mumtendere.

1Co 7:16 Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?

1Co 7:17 Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu ayitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiyika m’Mipingo yonse.

1Co 7:18 Kodi wayitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi wayitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe.

1Co 7:19 Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusungu kwa malamulo a Mulungu.

1Co 7:20 Munthu ali yense akhale m’mayitanidwe m’mene adayitanidwamo.

1Co 7:21 Kodi udayitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko.

1Co 7:22 Pakuti iye amene adayitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woyitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu.

1Co 7:23 Mudagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu.

1Co 7:24 Abale, munthu aliyense akhale m’mene adayitanidwamo momwemo akhale ndi Mulungu.

1Co 7:25 Koma kunena za anamwali, ndiribe lamulo la Ambuye; koma ndipereka kuweruza kwanga, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika.

1Co 7:26 Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chibvuto cha nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.

1Co 7:27 Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.

1Co 7:28 Koma ungakhale ukwatira, sudachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sadachimwa. Koma wotere adzakhala nacho chibvuto m’thupi, ndipo ndikulekani.

1Co 7:29 Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe;

1Co 7:30 Ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu.

1Co 7:31 Ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti mawonekedwe adziko ili apita.

1Co 7:32 Koma ndifuna kuti mukhale wosalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye.

1Co 7:33 Koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake.

1Co 7:34 Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo.

1Co 7:35 Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, wopanda chochewukitsa.

1Co 7:36 Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wa mkazi chosamuyenera, ngati pali kupitilira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe.

1Co 7:37 Koma iye amene ayima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nawo ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wa mkazi unamwali wake, adzachita bwino.

1Co 7:38 Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita bwino koposa.

1Co 7:39 Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, pokhapokha mwa Ambuye.

1Co 7:40 Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuweruza kwanga; ndipo ndiganiza kuti inenso ndiri naye Mzimu wa Mulungu.



8

1Co 8:1 Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: tidziwa kuti tiri nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chidzitukumula, koma chikondi chimangilira.

1Co 8:2 Ngati munthu aliyense ayesa kuti adziwa kanthu sadayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.

1Co 8:3 Koma ngati munthu aliyense akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.

1Co 8:4 Tsono kunena za kudya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano siliri kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma m’modzi.

1Co 8:5 Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m’mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri.

1Co 8:6 Koma kwa ife kuli Mulungu m’modzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye m’modzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse ziri mwa Iye, ndi ife mwa Iye.

1Co 8:7 Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, wozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbumtima chawo, popeza nchofowoka, chidetsedwa.

1Co 8:8 Koma chakudya sichitibvomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tiribe kupindulako.

1Co 8:9 Koma yang’anirani kuti ufulu wanu umene ungakhale chokhumudwitsa wofowokawo.

1Co 8:10 Pakuti ngati munthu aliyense akawona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya m’kachisi wa fano, kodi chikumbumtima chake, popeza ali wofowoka, sichidzalimbikitsidwa kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano?

1Co 8:11 Pakuti mwa chidziwitso chako wofowokayo atayika, ndiye mbale amene Khristu adamfera.

1Co 8:12 Koma pakuchimwira abale, ndi kubvulaza chikumbumtima chawo chofowoka, muchimwira kotero Khristu.

1Co 8:13 Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama ku nthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse m`bale wanga.



9

1Co 9:1 Kodi sindine mtumwi? Kodi sindine mfulu? Kodi sindidawona Yesu Khristu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?

1Co 9:2 Ngati sindiri mtumwi kwa ena, komatu ndiri kwa inu: pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.

1Co 9:3 Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi,

1Co 9:4 Kodi tiribe ulamuliro wa kudya ndi kumwa?

1Co 9:5 Kodi tiribe ulamuliro wakuyendayenda naye mulongo mkazi, monganso atumwi ena, ndi abale wa Ambuye ndi Kefa?

1Co 9:6 Kapena kodi ife tokha, Barnaba ndi ine, tiribe ulamuliro wakusagwira ntchito?

1Co 9:7 Msilikari ndani achita nkhondo, nthawi ili yonse nadzifunira zake yekha? Awoka mpesa ndani, wosadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, wosadya mkaka wake wa gululo?

1Co 9:8 Kodi ndiyankhula izi monga mwa anthu? ndinena zinthu izi monga munthu? Kapena chilamulo sichinenanso zomwezo?

1Co 9:9 Pakuti m’chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamiza ng’ombe pakupuntha iyo tirigu. Kodi Mulungu asamalira ng’ombe?

1Co 9:10 Kapena achinena ichi konse konse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nawo.

1Co 9:11 Ngati takufeserani inu zinthu za uzimu, ndi chithu chachikulu ngati ife tituta za thupi lanu?

1Co 9:12 Ngati ena ali nawo ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitidachita nawo ulamuliro umene; koma timalola tonse, kuti tingachite chotchinga Uthenga Wabwino wa Khristu.

1Co 9:13 Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za kachisi amadya za m’kachisi, ndi iwo akuyimilira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

1Co 9:14 Chomwechonso Ambuye adalamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

1Co 9:15 Koma ine sindidachita nako kanthu ka zinthu izi: ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti, kundikomera ine kufa, koma wina asayesa kwachabe kudzitamanda kwanga.

1Co 9:16 Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndiribe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; inde tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.

1Co 9:17 Pakuti ngati ndichita ichi chibvomerere, mphotho ndiri nayo; koma ngati si chibvomerere, adandikhulupirira ine mu udindo wa uthenga wabwino umene udaperekedwa kwa ine.

1Co 9:18 Mphotho yanga nchiyani tsono? Indetu kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale wa ulere, kuti ndisayipse ulamuliro wanga mu Uthenga Wabwino.

1Co 9:19 Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa anthu onse, ndidadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule wochuluka.

1Co 9:20 Ndipo kwa Ayuda ndidakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo womvera lamulo monga womvera lamulo kuti ndipindule iwo womvera malamulo;

1Co 9:21 Kwa iwo wopanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo wopanda lamulo.

1Co 9:22 Kwa wofowola ndidakhala ngati wofowoka, kuti ndipindule iwo wofowoka. Ndakhala zinthu zonse kwa anthu onse, kuti pali ponse ndikapulumutse ena.

1Co 9:23 Koma ndichita izi zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale wogawana naye..

1Co 9:24 Kodi simudziwa kuti iwo akuchita mpikisano wa liwiro, athamangadi onse, koma m’modzi alandira mphotho? Motero thamangani, kuti mukalandire.

1Co 9:25 Koma munthu ali yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wobvunda koma ife wosabvunda.

1Co 9:26 Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati modzi womenyana wopanda kanthu.;

1Co 9:27 Koma ndisunga thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wosayenera ndekha kulandira mphoto.



10

1Co 10:1 Pakuti sindifuna, kuti mukhale wosadziwa, abale, kuti makolo athu onse adali pansi pa mtambo, nawoloka nyanja onse;

1Co 10:2 Nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m’nyanja,

1Co 10:3 Ndipo nadya onse chakudya cha uzimu chimodzimodzi;

1Co 10:4 Ndipo namwa onse chakumwa cha uzimu chimodzimodzi; pakuti adamwa mwa thandwe la uzimu lakuwatsata; koma thandwelo ndiye Khristu.

1Co 10:5 Koma wochuluka a iwo Mulungu sadakondwera nawo; pakuti adawataya m’chipululu.

1Co 10:6 Koma zinthu izi ndi chitsanzo chathu ndi cholinga kuti tisalakalake zoyipa ife, monganso iwowo adalakalaka.

1Co 10:7 Kapena musakhale wopembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu adakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.

1Co 10:8 Kapena tisachite dama monga ena a iwo adachita chiwerewere, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.

1Co 10:9 Kapena tisayese Khristu monga ena a iwo adayesa, nawonongeka ndi njoka zija.

1Co 10:10 Kapena musadandaule, monga ena a iwo anadandaula, nawonongeka ndi wowonongayo.

1Co 10:11 Koma izi zidachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zidalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.

1Co 10:12 Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chiliri, ayang’anire kuti angagwe.

1Co 10:13 Sichidakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzayikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupilirako.

1Co 10:14 Chifukwa chake, wokondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

1Co 10:15 Ndinena monga kwa anthu anzeru; lingilirani inu chimene ndinena ndi ziwanda.

1Co 10:16 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa sichiri chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?

1Co 10:17 Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse tigawana ku mkate umodzi.

1Co 10:18 Tapenyani Israyeli monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe kugawana ndi guwa la nsembe?

1Co 10:19 Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chiri kanthu? Kapena kuti fano liri kanthu kodi?

1Co 10:20 Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda;ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

1Co 10:21 Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye ndi ku gome la ziwanda.

1Co 10:22 Kodi kapena tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?

1Co 10:23 Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse, zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

1Co 10:24 Munthu asafune zake za iye yekha koma za mzake.

1Co 10:25 Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima.

1Co 10:26 Pakuti dziko lapansi liri la Ambuye, ndi kudzala kwake.

1Co 10:27 Ngati wina wa wosakhulupirira akuyitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiyikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbumtima.

1Co 10:28 Koma ngati wina akati kw ainu, yoperekedwa nsembe kwa mafano iyi, musadye, chifukwa cha iye wakuwuzayo, ndi chifukwa cha chikumbumtima; pakuti dziko lapansi liri la Ambuye ndi zonse za mkati mwake.

1Co 10:29 Ndinena chikumbumtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbumtima cha wina?

1Co 10:30 Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji zoipa chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo?

1Co 10:31 Chifukwa chake, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

1Co 10:32 Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Ahelene, kapena Mpingo wa Mulungu.

1Co 10:33 Monga inenso ndikondweretsa onse m’zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha ambiri, kuti apulumutsidwe.



11

1Co 11:1 Khalani wonditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu.

1Co 11:2 Ndipo ndikutamandani inu abale kuti m’zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndidapereka kwa inu.

1Co 11:3 Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa mwamuna aliyense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.

1Co 11:4 Mwamuna aliyense wobveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake.

1Co 11:5 Koma mkazi aliyense popemphera kapena kunenera wobvula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.

1Co 11:6 Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.

1Co 11:7 Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.

1Co 11:8 Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna.

1Co 11:9 Pakutinso mwamuna sadalengedwa chifukwa cha mkazi; koma mkazi chifukwa cha mwamuna.

1Co 11:10 Chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nawo ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.

1Co 11:11 Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi mwa Ambuye.

1Co 11:12 Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse ziri za kwa Mulungu.

1Co 11:13 Lingilirani mwa inu nokha; kodi nkuyenera kuti mkazi apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu?

1Co 11:14 Kodi chibadwidwe sichitiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chimnyozetsa iye?

1Co 11:15 Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba.

1Co 11:16 Koma akawoneka munthu wina achita ngati motetana, tiribe makhalidwe wotere, kapena ife, kapena mipingo ya Mulungu.

1Co 11:17 Tsopano pakulengeza ichi mwa inu sindikutamani inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choyipa.

1Co 11:18 Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndibvomereza penapo.

1Co 11:19 Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo wobvomerezedwa awonetsedwe pakati pa inu.

1Co 11:20 Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi simusonkhanira kudya mgonero wa Ambuye.

1Co 11:21 Pakuti pakudyaku aliyense ayambe watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

1Co 11:22 Chiyani? mulibe nyumba zodyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m’menemo? Sindikutamani.

1Co 11:23 Pakuti ine ndidalandira kwa Ambuye, chimenenso ndidapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja adaperekedwa, adatenga mkate.

1Co 11:24 Ndipo m’mene adayamika, adawunyema, ndipo adati, Tengani, idyani, ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.

1Co 11:25 Koteronso chikho chitatha chakudya, ndi kuti, chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse; mukamwa chikhale chikumbukiro changa.

1Co 11:26 Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.

1Co 11:27 Chifukwa chake, yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

1Co 11:28 Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate umenewo, ndi kumwera chikho chimenecho.

1Co 11:29 Pakuti iye wakudya ndi kumwa kosayenera, akadya ndi kumwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupi la Ambuyelo.

1Co 11:30 Chifukwa chake ambiri mwa inu afowoka, nadwala, ndipo ambiri agona.

1Co 11:31 Koma ngati tikadakaziweruza tokha sitikadaweruzidwa.

1Co 11:32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

1Co 11:33 Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.

1Co 11:34 Ngati wina ali ndi njala adye kwawo; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.



12

1Co 12:1 Koma zamphatso za uzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa.

1Co 12:2 Mudziwa kuti pamene mudali amitundu, mudatengedwa kumka kwa mafano aja wosayankhula, monga mudatsogozedwa.

1Co 12:3 Chifukwa chake, ndikuwuzani inu, kuti palibe munthu wakuyankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.

1Co 12:4 Ndipo pali mphatso zosiyana koma Mzimu yemweyo.

1Co 12:5 Ndipo pali utumiki wosiyana, koma Ambuye yemweyo.

1Co 12:6 Ndipo pali machitidwe wosiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse.

1Co 12:7 Koma kwa onse kwapatsidwa mawonekedwe a Mzimu kuti apindule nawo,

1Co 12:8 Pakuti kwa m’modzi kwapatsidwa mwa Mzimu mawu a nzeru; koma kwa mzake mawu a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo.

1Co 12:9 Ndi kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu m’modziyo;

1Co 12:10 Ndi kwa wina zozizwitsa za mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime;

1Co 12:11 Koma zonse za izi achita Mzimu m’modzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afunira.

1Co 12:12 Pakuti monga thupi liri limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonse zathupi limodzilo zili thupi limodzi momwemonso Khristu.

1Co 12:13 Pakutinso mwa Mzimu m’modzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m’thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tidmwetsedwa Mzimu m’modzi.

1Co 12:14 Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi , koma zambiri.

1Co 12:15 Ngati phazi likati, popeza sindiri dzanja, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi chifukwa cha ichi?

1Co 12:16 Ndipo ngati khutu likati, popeza sindiri wa diso, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi chifukwa cha ichi?

1Co 12:17 Ngati thupi lonse likadakhala diso kukadakhala kuti kumvera. Ngati thupi lonse lidakakhala khutu kukada khala kuti kununkhiza?

1Co 12:18 Koma tsopano, Mulungu adayika ziwalo zonsezo m’thupi, monga kudamkondweretsa.

1Co 12:19 Koma ngati zonse zikadakhala chiwalo chimodzi; likadakhala kuti thupi?

1Co 12:20 Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi.

1Co 12:21 Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, sindikufunani inu.

1Co 12:22 Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofowoka m’thupi, zifunika kwambiri:

1Co 12:23 Ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m’thupi, pa izi tiyika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa.

1Co 12:24 Koma zokoma zathu ziribe kusowa; koma Mulungu adalumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho; kuti kusakhale chisiyano m’thupi.

1Co 12:25 Kuti pasakhale kugawanika m`thupi koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chimzake.

1Co 12:26 Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva zowawa ziwalo zina zimva kuwawa pamodzi nacho, chingakhale chiwalo chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.

1Co 12:27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

1Co 12:28 Ndipotu Mulungu adayika ena mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, kulongosola ntchito, malilime a mitundu mitundu.

1Co 12:29 Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali onse aphunzitsi kodi? Ali wonse wochita zozizwa?

1Co 12:30 Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse ayankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira?

1Co 12:31 Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuwonetsani njira yokoma yoposatu.



13

1Co 13:1 Ndingakhale ndiyankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe chikondi, ndikhala mkuwa wowomba, kapena nguli yolira.

1Co 13:2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe chikondi ndiri chabe.

1Co 13:3 Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa wosawuka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndiribe chikondi, sindipindula kanthu ayi.

1Co 13:4 Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikudza,

1Co 13:5 Sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima msanga, sichilingilira zoyipa;

1Co 13:6 Sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi chowonadi;

1Co 13:7 Chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipilira zinthu zonse.

1Co 13:8 Chikondi sichimalephera, koma kapena zonenera zidzalephera, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzatha

1Co 13:9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.

1Co 13:10 Koma pamene changwiro chafika, tsono cha mderamdera chidzamalizika.

1Co 13:11 Pamene ndidali mwana ndidayankhula monga mwana, ndidamvetsa monga mwana, ndidanganiza monga mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa zinthu chabe za chibwana.

1Co 13:12 Pakuti tsopano tipenya m’kalilore, ngati m`chilape; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.

1Co 13:13 Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi:



14

1Co 14:1 Tsatani chikondi, koma funitsitsani mphatso za uzimu, koma koposa kuti mukanenere.

1Co 14:2 Pakuti iye wakuyankhula lilime sayankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu ayankhula zinsinsi.

1Co 14:3 Koma iye wakunenera ayankhula ndi anthu chomangilira ndi cholimbikitsa, ndi chotothoza.

1Co 14:4 Iye wakuyankhula lilime, adzimangilira yekha, koma iye wakunenera amangilira Mpingo.

1Co 14:5 Ndipo ndifuna inu nonse muyankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakuyankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangilira.

1Co 14:6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kuyankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindiyankhula ndi inu kapena m’bvumbulutso, kapena m’chidziwitso, kapena m’chinenero, kapena m’chiphunzitso.

1Co 14:7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mawu, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa malilidwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiwombedwa kapena kuyimbidwa?

1Co 14:8 Pakuti ngati lipenga lipereka mawu wosazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?

1Co 14:9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mawu womveka bwino, chidzazindikirika bwanji chimene chiyankhulidwa? Pakuti mudzayankhula mosapindulitsa.

1Co 14:10 Iripo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mawu pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa tanthawuzo

1Co 14:11 Chifukwa chake, ngati sindidziwa tanthawuzo la mawuwo ndidzakhala kwa iye woyankhulayo wakunja, ndipo woyankhulayo adzakhala wakunja kwa ine.

1Co 14:12 Momwemo inunso, popeza muli wofunitsitsa mphatso za uzimu, funani kuti mukachuluke kukumangilira kwa Mpingo.

1Co 14:13 Chifukwa chake iye woyankhula lilime, apemphere kuti iye amasulire.

1Co 14:14 Pakuti ngati ndipemphera m’lilime mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.

1Co 14:15 Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzayimba ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi chidziwitso.

1Co 14:16 Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala nawe m`chipinda wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?

1Co 14:17 Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiliridwa.

1Co 14:18 Ndiyamika Mulungu kuti ndiyankhula malilime koposa inu nonse;

1Co 14:19 Koma mu mpingo ndifuna kuyankhula mawu asanu ndi chidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kuyankhula mawu zikwi khumi m’malilime.

1Co 14:20 Abale, musakhale ana m’chidziwitso, koma m’choyipa khalani makanda, koma m’chidziwitso akulu misinkhu.

1Co 14:21 Kwalembedwa m’chilamulo, ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzayankhula nawo anthu awa: ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

1Co 14:22 Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo wosakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.

1Co 14:23 Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akayankhule malilime, ndipo akalowemo anthu wosaphunzira, kapena wosakhulupira, kodi sadzanena kuti mwachita misala?

1Co 14:24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, akhutitsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

1Co 14:25 Chotero zobisika za mtima wake zidzawonetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.

1Co 14:26 Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangilira.

1Co 14:27 Ngati munthu wina ayankhula malilime, achite ndi awiri, koma woposa atatu ayi, ndipo motsatana; ndipo m’modzi amasulire.

1Co 14:28 Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma ayankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.

1Co 14:29 Ndipo aneneri ayankhule awiri kapena atatu, ndi ena aweruze.

1Co 14:30 Koma ngati kanthu kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo.

1Co 14:31 Pakuti mukhoza nonse kunenera m’modzi m’modzi, kuti onse aphunzire, ndi onse aatonthozedwe.

1Co 14:32 Ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;

1Co 14:33 Pakuti Mulungu sali woyambitsa chisokonezo koma wa mtendere, monga mwa Mipingo yonse ya woyera mtima.

1Co 14:34 Akazi anu akhale chete m’Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kuyankhula. Koma akhale womvera, monganso chilamulo chinena.

1Co 14:35 Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna awo a iwo wokha kwawo: pakuti kunyanzitsa mkazi kuyankhula mu Mpingo.

1Co 14:36 Chiyani? Mawu a Mulungu adatuluka kwa inu? Kapena adafika kwa inu nokha?

1Co 14:37 Ngati wina ayesa kuti ali m’neneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye.

1Co 14:38 Koma ngati wina akhala wosadziwa, akhale wosadziwa.

1Co 14:39 Chifukwa chake, abale anga funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kuyankhula malilime.

1Co 14:40 Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.



15

1Co 15:1 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani inu, umenenso mudalandira, umenenso muyimamo.

1Co 15:2 Umenenso mupulumutsidwa nawo ngati muwusunga monga momwe ndidalalikira kwa inu; ngati simudakhulupira chabe.

1Co 15:3 Pakuti ndidapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndidalandira, kuti Khristu adafera zoyipa zathu, monga mwa malembo;

1Co 15:4 Ndi kuti adayikidwa; ndi kuti adawukitsidwa tsiku la chitatu, monga mwa malembo;

1Co 15:5 Ndi kuti adawonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;

1Co 15:6 Pomwepo adawoneka pa nthawi imodzi kwa abale woposa mazana asanu, amene wochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena adagona.

1Co 15:7 Pomwepo adawonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse.

1Co 15:8 Ndipo potsiriza pake pa onse, adawoneka kwa inenso monga mtayo.

1Co 15:9 Pakuti ine ndiri wam’ng’ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndidazunza mpingo wa Mulungu.

1Co 15:10 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndiri ine amene ndiri; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichidakhala chopanda pake, koma ndidagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.

1Co 15:11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero mudakhulupira.

1Co 15:12 Koma ngati Khristu alalikidwa kuti wawukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuwuka kwa akufa?

1Co 15:13 Koma ngati kulibe kuwuka kwa akufa, Khristunso sadawukitsidwa;

1Co 15:14 Ndipo ngati Khristu sadawukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chiri chabe.

1Co 15:15 Inde ndipo ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tidachita umboni kunena za Mulungu kuti adawukitsa Khristu; amene sawukitsidwa, ngati kuli tero kuti akufa sadawukitsidwa:

1Co 15:16 Pakuti ngati akufa sadawukitsidwa, Khristunso sadawukitsidwa

1Co 15:17 Ndipo ngati Khristu sawukitsidwa, chikhulupiriro chanu chiri chopanda pake; muli chikhalire m’machimo anu.

1Co 15:18 Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu adatayika.

1Co 15:19 Ngati tiyembekezera Khristu m’moyo uno wokha, tiri ife aumphawi woposa wa anthu onse.

1Co 15:20 Koma tsopano Khristu wawukitsidwa kwa akufa, chipatso chowundukura cha iwo akugona.

1Co 15:21 Pakuti monga imfa idadza mwa munthu kuwuka kwa akufa kudadzanso mwa munthu.

1Co 15:22 Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, chotero mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.

1Co 15:23 Koma munthu aliyense m’dongosolo lake la iye yekha, Khristu chipatso choyamba pambuyo pake iwo a Khristu; pomwepo iwo a Khristu pakubwera kwake.

1Co 15:24 Pomwepo padzafika chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, pamene adzathetsa ulamuliro wonse,ndi mphamvuzonse.

1Co 15:25 Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira atayika adani onse pansi pa mapazi ake.

1Co 15:26 Mdani wotsiriza amene adzawonongedwa ndiye imfa.

1Co 15:27 Pakuti Iye adagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene adagonjetsa zonsezo kwa Iye.

1Co 15:28 Ndipo pamene zonsezi zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene adamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.

1Co 15:29 Ngati sikutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa sawukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha akufa?

1Co 15:30 Nanga ifenso tiri m’mowopsa bwanji nthawi zonse?

1Co 15:31 Nditsutsa chifukwa cha chimwemwe chanu chimene ndiri nacho mwa Khristu Yesu Ambuye wathu, ndifa tsiku ndi tsiku.

1Co 15:32 Ngati mwa khalidwe la wathu ndidalimbana ndi zirombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa sawukitsidwa tidye, timwe pakuti mawa timwalira.

1Co 15:33 Musanyengedwe; chiyanjano choyipa chiyipsa makhalidwe wokoma.

1Co 15:34 Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu: ndiyankhula kunyazitsa inu.

1Co 15:35 Koma munthu wina adzati, Akufa awukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?

1Co 15:36 Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa:

1Co 15:37 Ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbewu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina:

1Co 15:38 Koma Mulungu ayipatsa thupi longa afuna; ndi kwa mbewu yonse thupi lake lake.

1Co 15:39 Nyama yonse siyili imodzimodzi; koma yina ndi ya anthu, ndi yina ndiyo nyama ya zoweta, ndi yina ndiyo nyama ya mbalame, ndi yina ya nsomba.

1Co 15:40 Palinso matupi a m’mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa la m’mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.

1Co 15:41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi ina mu ulemerero.

1Co 15:42 Chomwechonso kudzakhala kuwuka kwa akufa. Lifesedwa m’chibvundi, liwukitsidwa m’chisabvundi:

1Co 15:43 Lifesedwa mu m’nyozo, liwukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m’chifowoko, liwukitsidwa mumphamvu.

1Co 15:44 Lifesedwa thupi la chibadwidwe, liwukutsidwa thupi la uzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.

1Co 15:45 Koteronso kwalembedwa, munthu woyamba Adamu, adakhala mzimu wamoyo; Adamu wotsiriza adakhala mzimu wakupatsa moyo.

1Co 15:46 Koma cha uzimu sichiri choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo cha uzimu.

1Co 15:47 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka; munthu wachiwiri ndiye Ambuye wakumwamba.

1Co 15:48 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.

1Co 15:49 Ndipo monga tabvala fanizo la wanthakayo, tidzabvalanso fanizo la wakumwambayo.

1Co 15:50 Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chibvundi sichilowa chisabvundi.

1Co 15:51 Tawonani ndikuwuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,

1Co 15:52 M’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzawukitsidwa wosabvunda, ndipo ife tidzasandulika.

1Co 15:53 Pakuti chobvunda ichi chiyenera kubvala chisabvundi, ndi cha imfa ichi kubvala chosafa.

1Co 15:54 Ndipo pamene chobvunda ichi chikadzabvala chisabvundi ndi cha imfa ichi chikadzabvala chosafa, pamenepo padzachitika mawu wolembedwa, Imfayo yamezedwa mchigonjetso.

1Co 15:55 Haa imfa ululu wako uli kuti?Haa imfa,manda ako ali kuti? chigonjetso chako chiri kuti?

1Co 15:56 Koma ululu wa imfa ndiwo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndicho chilamulo.

1Co 15:57 Koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khris

1Co 15:58 Chifukwa chake, abale anga wokondedwa, khalani wokhazikika, wosasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.



16

1Co 16:1 Tsopano kunena za chopereka cha kwa woyera mtima, monga ndidalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.

1Co 16:2 Pa tsiku loyamba la sabata aliyense wa inu asunge yekha, monga momwe adapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.

1Co 16:3 Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa woyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.

1Co 16:4 Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.

1Co 16:5 Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Makedoniya; pakuti ndidzapyola Makedoniya.

1Co 16:6 Ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yozizira kuti mukandiperekeze ine kumene kuli konse ndipitako.

1Co 16:7 Pakuti sindifuna kukuwonani tsopano popitilira: pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.

1Co 16:8 Koma ndidzakhala ku Aefeso kufikira Pentekoste.

1Co 16:9 Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo woletsana nafe ndi ambiri.

1Co 16:10 Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha: pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine.

1Co 16:11 Chifukwa chake munthu aliyense asampeputse: koma mumperekeze mumtendere kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera ine pamodzi ndi abale.

1Co 16:12 Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuwumiliza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichidali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene awona nthawi.

1Co 16:13 Dikirani, chirimikani m’chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.

1Co 16:14 Zinthu zanu zonse zichitike m’chikondi.

1Co 16:15 Koma ndikupemphani inu, abale (mudziwa banja la Stefana, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti adadziyika wokha kutumikira woyera mtima.)

1Co 16:16 Kuti inunso mubvomere wotere, ndi yense wakuchita nawo, ndi kugwiritsa ntchito.

1Co 16:17 Koma ndikondwera pa kudza kwawo kwa Stefana, ndi Fortunato, ndi Akayiko; chifukwa iwo adandikwaniritsa chotsalira chanu.

1Co 16:18 Pakuti adatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muwazindikire wotere.

1Co 16:19 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni inu. Akupatsani ndithu moni mwa Ambuye, Akula ndi Priska, pamodzi ndi mpingo wa m’nyumba yawo.

1Co 16:20 Abale onse akupatsani moni Patsanani moni ndi kupsopsonana kopatulika.

1Co 16:21 Moni wa ine Paulo ndi dzanja langa.

1Co 16:22 Ngati munthu wina sakonda Ambuye Yesu Khristu, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.

1Co 16:23 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu.

1Co 16:24 Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Ameni.



AMAZING GRACE BIBLE INSTITUTE